Text
stringlengths
292
6.6k
labels
int64
0
19
Ndinkacheza ndi mchimwene wake Akuti amapitapita kunyumba kwa namwali potengera chinzake chomwe chidalipo pakati pa iye ndi mchimwene wa namwaliyo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Adagwiriziza kale unkhoswe: Emmanuel ndi Hawa Emmanuel Katiko akuti nthawi zonse amasowa tulo kulingalira za Hawa Mulele koma amalephera kumasuka powopa kuononga chinzake. Tinkakhala limodzi ku Chiwembe mumzinda wa Blantyre ndipo mchimwene wake adali mnzanga koma ine maso adali pa mchemwali wakeyo adatero Emmanuel. Iye adati mchaka cha 2009 ndipo adalimba mtima nkufunsira msungwanayo ndipo zidatheka mpaka madongosolo kuyambika. Pa 7 November 2011 chinkhoswe chidachitika ku Chiwembe komweko ndipo akuti akuyembekezera ukwati woyera. Iye adati adasangalatsidwa ndi Hawa chifukwa cha khalidwe lake lofatsa ndi lodzichepetsa komanso kudzilemekeza. Hawa adati kwa iye kukwatiwa ndi Emmanuel ndi chinthu chapamwamba chomwe amalakalaka chitamuchitikira. Zidayenda momwe ndinkafunira. Timakondana ndiposo ndi mwamuna wabwino woopa mulungu ndi wachikondi, adatero Hawa. Awiriwa akuti akufuna Mulungu awatsogolere muulendo wawo wa banja kuti adzakhale limodzi mpaka kale popanda chosokoneza.
15
Akayidi 60 Omwe Anatulutsidwa Abweleranso Mmanja mwa Apolisi Akayidi oposa 60 mwa omwe anatulutsidwa ku ndende za mdziko muno masabata apitawa alinso mmanja mwa apolisi atapezeka akuchita za umbava ndi umbanda atangotulutsidwa. Mwapasa: Tinakhwimitsa chitetezo kwambiri Sabata zapitazo, boma linatulutsa akayidi oposa 1000 mu ndende za dziko lino ati pofuna kuchepetsa chiwerengero cha akayidiwa mu ndende-zi pofuna kuwatetedza ku mliri wa COVID-19. Mkulu wa apolisi mdziko muno a Duncan Mwapasa, ati potsatira kutulutsidwa kwa akayidiwa apolisi anakhwimitsa chitetezo poyika njira zina za ukadaulo zotetezera anthu ndi katundu wawo Nthawi iliyonse ku prison kukatuluka anthu pa pardon amakhalapo anthu 143 omwe atulutsidwa pa pardon nde umbanda umakwera kwambiri ndipo ife apolisi ngakhale tilipo ochepa tinaika ndondomeko zabwino zoti tikwaniritse kutumikira madera onse ndipo padakali pano anthu oposa 60 ndi omwe agwidwa tsopano, anatero a Mwapasa.
7
Makuponi otsiriza afika mzigawo Mabanja ovutikitsitsa tsopano akhoza kumwetulira kutsatira kaamba ka kubwera kwa makuponi otsiriza a zipangizo zaulimi zotsika mtengo. Boma lati lalandira makuponi omaliza, zomwe zipangitse kuti alimi ovutikitsitsa 812 100 apeze zipangizozi mzigawo za pakati ndi kumpoto. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Makuponiwa abwera panthawi yomwe aphungu a ku Nyumba ya Malamulo komanso atsogoleri a mabungwe omwe si aboma akhala akudzudzula boma chifukwa cha kuchedwetsa pogawa makuponi komanso ganizo loyamba kugawa makuponi mchigawo cha kummwera. Wachiwiri kwa mkulu woyendetsa ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo muunduna wa zamalimidwe, Osborne Tsoka, adatsimikiza za kufika kwa makuponiwa ndipo adaonjezera kuti boma lamaliza kusankha anthu omwe alandire makuponiwa mmaboma 27 ndipo boma la Dowa lokha ndiko ntchitoyi ikupitirira. Tsoka adafotokoza: Tikudziwa kuti tikuthamangitsana ndi nthawi. Ichi ndi chifukwa chake tamwanza anthu kuti akhale akupereka makuponiwa kwa alimi mzigawo ziwiri zomwe zinali zisanalandire. Padakalipano, makuponi anyamulidwa kupita mmaboma omwe anthu adali asanalandire. Tikakamba za maboma, boma la Dowa ndilo latsala kuti timalize ntchito yosankha anthu omwe alandire makuponiwa. Ndikukhulupirira kuti pofika kumapeto a sabatayi ntchitoyi ikhala itatha. Poyankhula mwapadera, nduna ya zaulimi ndi chitukuko cha madzi Dr Allan Chiyembekeza adati sadatekeseke ndi chikayiko cha mabungwe omwe si aboma chakuti ndondomekoyi chaka chino ikumana ndi zokhoma. Sabata yatha, boma lidalandira makuponi oyamba ofikira anthu 687 900 mchigawo cha kumwera. Koma potsirapo ndemanga pa anthu ovitikitsitsa omwe alandire makuponiwa chaka chino, mafumu ena, maka mchigawo cha kumpoto adandaula kuti kusankha maina sikunayende bwino chaka chino chifukwa ena omwe asankhidwa kuti alandire nawo si anthu ovutikitsitsa, koma opeza bwino chifukwa ali mzintchito zolipidwa pamwezi. Ku Rumphi, nyakwawa ina ya mdera la Gulupu Chikulamasinda kwa Themba la Mathemba (Paramount Chief) Chikulamayembe, idati ndi yokhumudwa chifukwa mwa anthu 9 omwe alandire makuponiwa mmudzi mwake asanu ndi oti sali pamudzipo koma mzintchito monga ku Blantyre, ku Lilongwe ndi ku Mzuzu komanso wina ndi mphunzitsi ku Kasungu. Inde ndi a mmudzi mwanga, koma si ovutikitsita. Ine mwini wakene ndimagwira ntchito ku Blantyre koma dzina langa latuluka pamndandanda wa omwe apindule ndi makuponiwa kusiya anthu ovutikitsitsa mmudzi mwanga. Sindidziwa kuti amasankha bwanji mainawa chifukwa akadatifunsa mafumufe kuti woyenera ndani kulandira makuponi tikadawapatsa maina a anthuwo, osati kusankha okha. Okhala ndi anthu ndan, iwowo kapena ife mafumu? idafunsa mfumuyo, yomwe sidafune kuti itchulidwe poopera mawa.
4
Papa Apempha Akhristu Akule Mchikhulupiliro Wolemba: Thokozani Chapola ds/2019/08/francis.jpg 308w" sizes="(max-width: 542px) 100vw, 542px" />Papa Francisko Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Fransisco walimbikitsa akhristu kuti adzionetsa kukula muchikhristu pakukhala ndi chikhulupiliro ngati a Malitiri osiyanasiyana. Papa walankhula izi ku likulu la mpingowu ku Vatican kwa anthu omwe anasonkhana pa bwalo la St. Peters Square mu mzindawo. Mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu wati, moyo wokula mu chikhristu komanso mu chikhulupiliro ndi wofunikira kwambiri potengeraso ndi mmene zinthu ziliri masiku ano. Pamenepa Papa analimbikitsa akhristu kuti adzikonda kuwerenga baibulo komanso kumva mau a Mulungu pafupipafupi.
13
Papa Alimbikitsa Sukulu za Ukachenjede za Katolika Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco walimbikitsa sukulu za ukachenjede za mpingo-wu kuti zidzithandiza bwino ophunzira kuti akamaliza azikathandiza bwino pa ntchito zotukula madera awo. Papa Francisko Papa amalankhula izi kwa mamembala a bungwe la sukulu za ukachenjede za mpingowu pa dziko lonse la International Federation of Catholic Universities, komwe mwazina wakumbutsanso ntchito za mamembala a bungwe-li kuti adzidzipereka pa ntchito zokweza maphunziro a msukulu-zi. Bungwe-li likhala likuchita mkumano wake mu mzinda wa Rome mdziko la Italy.
3
ECM Ipempha Anthu Alemekeze Lamulo Podikira Chigamulo Alemba chikalatacho-Ena mwa maepiskopi a katolika ku Malawi Bungwe la ma episkopi a mpingo wa katolika mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM) lapempha anthu mdziko muno kuti alemekeze lamulo pamene akuyembekezera chigamulo cha bwalo la milandu pa nkhani yokhudza chisankho cha president. Ma episkopiwa anena izi kudzera mu chikalata chomwe atulutsa lero chomwe achilemba ndi mawu otsogolera akuti Ambuye Mundipange Kukhala Chida Chodzetsa Mtendere omwe ndi mawu omwe ananena Francis wa ku Assis woyera. Iwo ati padakali pano pamene akhristu ayamba nyengo ya Advent, ndi kofunika kuti anthu apitirize kukhala a bata zomwe zikugwirizana ndi uthenga omwe anatulutsa mwezi wa June chaka chino. Ma episkopiwa alangiza anthu mdziko muno kuti chigamulochi chikadzabwera ndipo ngati sichidzawakomera, azavomereze kapena kutsutsana nacho mwamtendere komanso motsata malamulo a dziko lino. Iwo apempha anthu kuti apewe kuchitira ena nkhanza pofuna kuwawopseza komanso apewe kufalitsa nkhani zabodza zokhudza nkhani yomwe ili ku bwalo la milandu maka kudzera pa masamba a mchezo pa makina a internet zomwe zingadzetse mpungwepungwe ndi kusokoneza mtendere mdziko muno. Pamenepa ma episkopiwa apempha nthambi zonse za mpingowu komanso nyumba zofalitsa nkhani za mpingowu kuti zibwere ndi njira zowakonzekeretsa anthu kuzavomereza chigamulo cha bwalo la milandu pofuna kupititsa patsogolo mtendere komanso mgwirizano mdziko muno. Ma episkopiwa ati apitilira kupemphelera chilungamo, mtendere, kukhululukirana komanso mgwirizano mdziko muno ndipo apempha akhristu a mpingowu kuti achite chimodzimodzi.
7
Nthula: Abambo ofooka kuchipinda achangamuke Akuti abambo ena amafooka pamene akucheza ndi akazi awo chifukwa cha zina zomwe zimasowekera pamene machezawa ali mkati. Ichi nchifukwa chake makolo akale amakhulupirira kuti pakhale nthula kapena kuti mthunduwere zomwe zimachangamutsa amuna oterewa. Ibra Monjeza wa mmudzi mwa Sauka kwa T/A Malemia mboma la Zomba ndiye akufotokoza izi kwa BOBBY KABANGO. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Monjeza kufotokozera anthu za kufunikira kwa nthunduwere Tidziwane bwinobwino. Ine ndi Monjeza, ndine mlimi komanso anthu amandidziwa bwino ndi ulangizi wanga. Ulangizi wokhudza mabanja komanso ulimi. Ndi ulangizi wanji omwe mutipatse lero? Ndikupatsani ulangizo omwe ndimawafotokozera anthu pafupifupi tsiku lililonse. Uwu ndi ulangizi kwa amayi zomwe ayenera kuchita kuti bambo asamafooke pamene akucheza nawo. Ndiye amayenera atani? Nkhani ndi nthula basi. Kugwiritsa ntchito nthula molondola ndiye kuti zako zayera, bambo abwekera nthawi zonse ndipo sangafooke. Nthula nchiyani? Ndi zibalobalo za kamtengo kakangono kamene kamakhala ndi minga. Ena amati nthunduwere ndipo mbuzi zimadyanso. Mwati zimathandiza chiyani? Dziwani kuti macheza pakati pa bambo ndi mayi amakhalabwino ngati aliyense akusangalala. Bambo amakhala nthawi yaitali pamene akucheza ndi mayi ngati mayiyo wapanga zomusangalatsa. Apa ndi pamene tikuti nthula zimagwira ntchito kuti machezawa akhale a nthawi. Nthula ndiye zimapanga chiyani? Zimakometsera machezawo. Kuti athe nthawi pakufunika nthula kuti nonse awiri akhutitsidwe. Mumazitani nthulazo kuti zifike pamenepa? Umafunika uthyole nthulayo koma usankhe yoti ikupita koola, imakhala yoti ili biii! kuda. Dziwani kuti amayi ndiwo amagwiritsira ntchito nthulayi osati amuna. Imangopangitsa kuti mwamuna asangalale pamene akucheza. Ndiye munthu wa mayiyo atani akatenga nthulayo? Amayingamba pakati ndi kumagwiritsira ntchito. Pakutha pa sabata mayiyo amakhala wasinthiratu, akati acheze ndi mwamuna zimakhala zabwino chifukwa mwamuna amasangalala ndithu. Amazigwiritsa bwanji ntchito ndipo chimathekacho nchiyani? Akangoyicheka pakati nthulayo, basi apite kwa mayi aliyense amene ndi wamkulu mdera lawo ndipo akamuuza bwino momwe angaigwiritsire ntchitomo. Akaigwiritsa ntchito bwino, amakhala mkazi woti mwamuna amasangalala naye pamene akuchita macheza ndipo ngakhale amuna ofooka amalimbikitsidwa. Tafotokozani bwino. Sindinena. Dziwani kuti kale mtundu ulionse umadziwika ndi zochita zake. Angoni, Achewa ndi ena timawadziwa momwe akuchitira kuchipinda koma masiku ano aliyense amatsata njira zomwe akufuna kuti asangalatse amuna ake. Kale Alhomwe timawadziwa ndi mikanda, koma lero upezanso ena omwe ndi Alhomwe alibe mikanda. Izitu zikusonyeza kuti chikhalidwe chidasokonekera ndipo aliyense akupanga chomwe akufuna. Izi ndikunenazi ndi zachikhalidwe ndiye sindinganene wamba. Osati mukungotinamiza apa? Kodi inu mudakwatira? Kapena mudayambapo mwacheza ndi mayi ndipo mudasiyanitsapo? Chifukwa ngati mudachitapo izi, bwezi mutandimvetsa. Sindikunama, izi ndi zoona. Inuyo mudasiyanitsapo? [Akuseka.] ndikudziwa chomwe ndikunena.
15
Kupitakufa? Mbiri yakale imeneyo! Matenda a HIV/Edzi asokoneza miyambo ina monga mwambo wa kupitakufa, womwe umapereka mphamvu kwa fisi kuti akakonze maliro pocheza ndi namfedwa kwa sabata ziwiri ndipo machezawo amachitika katatu patsiku. Chifukwa cha matendawa, kwabwera njira ya nanawa yomwe yazilalitsa mwambo wa kupitakufawu. BOBBY KABANGO adali mboma la Nsanje komwe adacheza ndi mlembi wa nyakwawa Masanzo kwa T/A Mlolo. Mkaka: Mwambo wa nanawa timangomwa mankhwala othamangitsa imfa Tidziwane, achimwene Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndine Joseph Mkaka. Kodi amfumu tawapeza? Ayi, iwowa adzukirira kudimba. Akuyembekezereka kubwerako madzulo chifukwa ntchito yakula kumeneko. Tidalire kuti inu mutithandiza pa vuto lathu? Musakaikenso, ndine mlembi wa amfumuwo ndiye palibe chomwe sindikuchidziwa chokhudza mudzi uno ndi miyambo yomwe timatsata. Kodi mwambo wa kupitakufa ukuchitikabe kuno? Zikuchitika koma mobisa chifukwa momwe matenda a Edzi aopseramu sungayerekeze kumachitabe mwambowu. Amabungwe akhala akufika kumemeza anthu kuti miyambo yoipa, monga umenewu, itheretu ndipo zipatso zake zikuonekadi pano. Ndiye mukutani kuti imfa ithawe pakhomo? Timagwiritsa mankhwala a nanawa amene amathamangitsa imfa pakhomo. Kuno anthu ambiri tikutsata zimenezi. Nanawa nchiyani? Ndi mankhwala amene singanga amachita pakhomo pamene pagwa maliro. Anthu, maka achibale, amamwa mankhwalawo molandirana ndipo pakhomopo pamakhala bwino. Zimachitika nthawi yanji? Maliro akachitika monga lero, mawa timakaika ndiye timasweretsa tsiku limodzi pamene timasonkhana kudzasesa. Nthawi yosesa mpamene mwambo wa nanawa umachitika. Mungathe kuchita mwambowu nthawi iliyonse kaya ndi masana kapena madzulo. Kodi mankhwalawa mumatemera kapena mumadya? Mankhwalawa ali pawiri. Ena amakhala a madzi. Amawaika mkapu ndiye aliyense wachibale amalandirana mankhwalawo kumamwa pangono mpaka nonse achibale akukwaneni. Pamene mankhwala ena amawaika kudenga kwa nyumba yomwe mumagona malemuwo. Mumawasomeka kudenga mbali yomwe kuli khomo kuti anthu akamalowa mnyumbamo azigwira mankhwalawo. Mukutanthauza wachibale aliyense amayenera amwe mankhwalawo? Zimatero kumene. Nonse mumalandirana, kumwa pangono basi, aliyense kamodzi komanso momapatsirana. Nanga achibale amene sadafike pamwambowo mumawatani? Achibale amene nthawi ya malirowo kapena tsiku la kusesalo palibepo, timawasungira mankhwalawo. Mankhwala ake ndi amene tawasomeka kudenga aja. Tsiku lomwe akonza zodzafika pakhomopo, timawalandira ndi kuwatengera kunyumba yomwe kudachitika malirowo. Ndiye pamene tikulowa mnyumbayo, timawapatsa mankhwala aja kuti agwire. Akangotero basi amabwezeretsa mankhwalawo kudengako. Amachitanso china chiti? Palibe, ngati agwira mankhwalawo ndiye kuti nawonso akonzedwa ku imfa yomwe idakangogwa pakhomopo. Nthawi yomwe munkatsata mwambo wa kupitakufa zinkakhala bwanji? Maliro akachitika chonchi, timapeza fisi kuti apite kunyumba yomwe kwachitika malirowo akacheze ndi namfedwayo. Katatu patsiku kapena zikavuta atha kumacheza nawo kawiri patsiku kwa sabata ziwiri. Fisiyu ntchito yake idali yoti achotse mzimu wa imfa womwe wakuta pakhomopo. Mpaka katatu? Ndiye zidalikolikotu Hahaha! Eeh, amasangalala kwambiri koma pano zimenezi zidatha.
1
PAC iunguza za boma la chifedulo Nthumwi zomwe zimakumana mumzinda wa Blantyre kukambirana za nkhani yakuti zigawo za dziko lino zizikhala ndi mtsogoleri wakewake pansi pa mtsogoleri wa dziko zati nkhaniyi kuti iyende bwino mpofunika kusintha malamulo ena. Mfundoyi ikugwirizana ndi zomwe adanena mphunzitsi wa za ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Blessings Chinsinga, kuti popanda kuunika malamulo, nkhaniyi ikhoza kudzetsa chisokonezo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Senior Chief Chikumbu ya ku Mulanje kufuna kutsitsa mfundo pamsonkhanowo Choyamba tiunike kuti malamulo athu akutinji chifukwa mukhoza kukhala ndi zigawo zodziyimira pazokha zomwe zingamakolanenso chifukwa cha malamulo omwe mukutsata, adatero Chinsinga. Msonkhanowo udakonzedwa ndi bungwe la mipingo la Public Affairs Committee (PAC) ndipo cholinga chake chidali kuunika chomwe chidayambitsa nkhaniyi ndi kukambirana momwe ingayendere. Malinga ndi wapampando wa bungwe la PAC, Mbusa Felix Chingota, nthumwi za kumsonkhanowo zidapeza kuti nkhaniyo idachokera pakusamvetsetsana pa momwe zinthu zina zikuyendera. Nthumwi zidapeza kuti nkhani monga kusankhana kochokera, kukondera pakasankhidwe ka maudindo, kusiyanitsa pakagawidwe ka zinthu ndi kupondereza zitukuko zomwe atsogoleri ena adayamba ndi zina mwa zinthu zomwe anthu akuona kuti ndi bwino aziyendetsa okha zinthu, adatero Chingota. Mlangizi wa mtsogoleri wa dziko lino pankhani za mgwirizano wa mdziko muno, Vuwa Kaunda, adati ndi cholinga cha mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti anthu azipereka maganizo awo kuti zinthu ziziyenda bwino. Kaunda adati Mutharika adalumbira kuti adzalemekeza malamulo a dziko lino omwe amapereka mwayi kwa Amalawi wolankhula zakukhosi kwawo. Mafumu nawo ayamikira zomwe lidachita bungwe la PAC pokonza msonkhanowo ndi zomwe nthumwi zidagwirizanazo. Paramount Chief Chikulamayembe wa ku Rumphi adati nzopatsa chidwi kuti boma ndi mabungwe akugwirizana pankhani yofuna kudzetsa umodzi ndi mtendere pomanga mfundo zoyendetsera nkhani zikuluzikulu monga imeneyi. Apa ndiye kuti zinthu ziyenda kusiyana nkuti anthu azingopanga phokoso lopanda tsogolo lake. Tionera kwa akuluakuluwo kuti akonza zotani, adatero Chikulamayembe. Koma malinga ndi Chinsinga, nkhaniyi ingaphweke Amalawi atalangizidwa bwino momwe ulamuliro wotere ungayendere. Iye adati nzomvetsa chisoni ndi kuchititsa mantha kuti Amalawi ena akungotsatira maganizo a anzawo chifukwa chosamvetsetsa. Iyitu si nkhani yaingono koma pakuoneka kuti anthu ambiri sakumvetsetsa mutuwu mmalo mwake angotsatirapo poti walankhulayo amamukhulupirira. Mpofunikanso kumasulira bwinobwino tanthauzo la nkhaniyi nkuphunzitsa Amalawi kuti azipereka maganizo awo enieni, adatero Chinsinga. Iye adati ulamuliro wotere ndi njira yoyendetsera boma yomwe dziko limagawidwa mmagawo omwe amayendetsa okha ntchito za chitukuko koma ali pansi pa ulamuliro wa mtsogoleri mmodzi. Iye adati kutengera pamgongo nkhani yotereyi kukhoza kubweretsa kusamvana ndi chisokonezo pazinthu zingonongono. Muganizire apa. Dzikoli ndi lalingono kwambiri komanso njira zobweretsa ndalama nzochepa. Pofuna kugawa, mpofunika kuunika bwinobwino mmene malire akhalire komanso kuti chigawo chanji chitenga chiyani, adatero Chinsinga. Mkulu wa bungwe la PAC, Robert Phiri, adati msonkhano womwe bungweli lidakonza udakambirana zina mwa nkhani zoterezi. Msonkhanowo udachitika Lolemba ndi Lachiwiri mumzinda wa Blantyre ndipo udabweretsa pamodzi akuluakulu a mnthambi za boma, mabungwe oyima paokha ndi otsata mbiri ya dziko lino. Phiri adati zomwe adakambirana akuluakuluwo azitulutsa ndi kuzipereka kuboma ndi mabungwe kuti zipereke chithunzithunzi cha mmene angagwirire ntchito ndi anthu pankhaniyi. Mmbuyomu, kafukufuku yemwe nyuzipepala ya The Nation idachita adasonyeza kuti aphungu 61 mwa 100 alionse adati nkhaniyi itapita ku Nyumba ya Malamulo akhoza kuikana. Nyuzipepalayi itafunsa aphungu 122 mwa 193, 75 adati angakane mfundoyi, aphungu 17 adali asanaganize ngati angaivomereze kapena ayi pomwe aphungu 30 adati angavomereze za mfundoyi. Mchaka cha 2006, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adanena kuti boma la mtunduwu likhoza kuthandiza pachitukuko cha dziko lino. Uku kudali msonkhano wounikira malamulo a dziko lino. Koma masiku ano, Mutharika amatsutsana ndi maganizowa ati kugawa dziko. Pamsonkhanowo padali a zipani zosiyanasiyana, mafumu, azipembedzo, mabungwe omwe si aboma ndipo amayendetsa zokambiranazo ndi sipikala wakale wa Nyumba ya Malamulo Henry Chimunthu Banda ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wakale wa dziko lino Justin Malewezi.
11
Kanema ya Papa ndi Yabodza-Bishop Tambala Episkopi wa diocese ya Zomba, Ambuye George Desmond Tambala wachenjeza akhristu a mpingo wa katolika kuti asakhulupilire mawu omwe ali mu mu kanema yomwe ikuyenda pa makina a Internet yotanthauzira molakwika zomwe Papa Francisco adayankhula mu chaka cha 2014. Tambala: Akungofuna kunyozetsa mpingo wathu Ambuye Tambala awuza Radio Maria Malawi kuti uthenga womwe adayankhula Papa Francisko udali wa mu chiyankhulo chachi Taliana ndipo udali ofunira mafuno abwino anthu a mpingo wa katolika ku America. Iwo ati anthu omwe atanthauzira kanemayu ali ndi cholinga chofuna kunyozetsa mpingo wakatolika ndi utsogoleri wake ndi cholinganso choti akhristu a mpingo-wu apandukire mbusa wawoyu. Ambuye Tambala ati anthuwa ndi osafunira zabwino mpingo wa katolika ndipo ali ndi cholinga choti akhristu a mpingo wa katolika adane ndi mtsogoleri wawo.
14
Green Light Foundation Idzala Mitengo Mndende Wolemba: Thokozani Chapola 2019/11/zomba-prison.jpg 336w" sizes="(max-width: 817px) 100vw, 817px" />Ndende ya Zomba: Amodzi mwa malo omwe kudzalidwe mitengoyi Bungwe la Green Light Foundation lati lidzala mitengo mu ndende zina za dziko lino pofuna kubwezeretsa chilengedwe. Mkulu wa bungweli mayi Carol Kachilika auza Radio maria Malawi kuti ntchitoyi iyamba mu nyengo ya mvula yomwe ikudzayi. Mayi Phiri ati awona kuti chilengedwe chikuwonongeka kwambiri mdziko muno ndipo mkoyenera kuti achitepo kanthu. Iwo ati achitanso izi pofuna kuphunzitsa akayidi moyo wodzala mitengo komanso kusamalira chilengedwe kuti akadzatuluka adzikachita. Zina mwa ndende zomwe mugwiridwe ntchitoyi ndi za Mikuyu, Zomba, Mzuzu, Rumphi komanso Kasungu.
18
Kaneneni akakuchitikirani nkhanza, apolisi auza ana Pamene dziko lino limakumbukira masiku 16 othana ndi nkhanza za mbanja, apolisi amema atsikana kuti azikanena akachitidwa nkhanza kwa makolo awo kapena kupolisi. Mkulu woyanganira zapolisi ya mmudzi mdziko muno, Yunus Lambat, adanena izi pokumbukira maikuwa, amene adayambira pa 25 November mpaka pa 10 December kusukulu ya Blantyre Girls. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Patsikulo, apolisi komanso akuluakulu a makampani osiyana adapita kukapereka uphungu komanso kuthokoza atsikana amene adakhoza bwino mkalasi. Tadala: Nkhanza zisatilepheretse Mtsikana amene adasangalatsa anthu patsikuli ndi Tadala Kadzakalowa wa zaka 11 amene adakhala nambala wani musitandede 8. Tadala, yemwe akukhumbira atadzagwira ntchito ya udotolo, adaponderera ophunzira 140 mkalasi mwawo. Polankhula za tsikuli, Tadala adati iye ndi wokondwa kuti akuluakulu adapeza chabwino kuwafotokozera ufulu wawo komanso zomwe angachite ngati ufulu wawo waphwanyidwa. Ndimafuna kudzakhala dotolo, izi sizingatheke ngati wina akupondereza ufulu wanga. Ndadziwa ufulu wanga, komanso zomwe ndingachite ngati wina atandiphwanyira ufuluwo, adatero iye. Iye adalangiza atsikana anzake kuti asiye kumwa mowa ponena kuti izi zingasokoneze tsogolo lawo.
7
Sungani mbatata mmunda, Mnkhuti kuti isaonongeke Alfred Mumba wa mboma la Dowa amalima mbatata pa malo okwana maekala 5. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Iye amapeza matumba osachepera 250 a mbatata pachaka kuchokera pa malowa koma chomvetsa chisoni nchoti amangokwanitsa kugulitsa theka lokha la zokolola zake. Mbatata imasungika nthawi yaitali mukaisamala bwino Ndikanyamula matumba 10 kupita nawo ku msika, 5 okha ndiomwe ndimagulitsa pa mtengo wabwinoko ndipo osalawo, ndimagulitsa mongotaya kapena kungozisiya ku msika komweko. Izi zimakhala chomwechi chifukwa ogulawo amatiphwathulitsa matumba ndikusankhamo zomwe akufuna ndipo zotsalazo amazisiya ndikupita kwa ogulitsa wina, iye adatero. Katswiri wa mbewu za mtunduwu kwa Bvumbwe Miswell Chitete adati zokolola za mbewuyi za pakati pa 30 ndi 50 pa 100 zilizonse zimaonongeka mdziko muno. Iye adati ngakhale mbatata sizichedwa kuonongeka, zimakhala osaonongeka mosachepera miyezi itatu zikasiyidwa mmunda momwemo osazikumba kapena miyezi 9 zikasungidwa mnkhuti. Malinga ndi Chitete, njirazi ndizothandiza kuti mlimi azitha kugulitsa mbewuyi pangonopangono kapena nthawi yomwe yayamba kusowa choncho akhoza kupindula nayo. Mbatata ikakhwima sizikutanthauza kuti mlimi akolole yonse ndikupita nayo ku msika chifukwa akagulitsa yochepa chabe ndipo yambiri izangoonongeka kapena agulitsa mongotaya, iye adatero. Iye adafotokoza kuti mlimi akhoza kuilekerera mmunda momwemo ndikuzayamba kukumba pamene waona kuti mbatata yachepa pa msika kuti apindule nayo kwambiri. Katswiriyu adati vuto lomwe mlimi akhoza kukumana nalo posunga mmunda ndi la kufumbwa kwa mbatata kaamba ka anankafumbwe. Chitete adati vutoli silalikulu kwenikweni chifukwa akhoza kuthana nalo pokwirira mingalu kuti anankafumbwewa azisowa polowera. Mlimi akhoza kusankha kusunga mbatata yake mu nkhuti ndikuzaigwiritsa ntchito mtsogolo kapena kumatengamo pangonopangono kufikira izathe, iye adatero. Katswiriyu adati nkhuti ndi dzenje losungiramo mbatata ndipo mlimi amakumba molingana ndi kuchuluka kwa zokolola zake za mbewuyi. Akamaliza kukumba, Chitete adati mlimi amayenera kusanja mbatata yake mzigawo. Iye adafotokoza kuti pamwamba pa chigawo chilichonse amayenera kuwazapo phulutsa kapena mchenga ndipo dzenje lija likadzadza, alikwirire. Akachoka apo, katswiriyu adafotokoza kuti mlimi amayenera aziyifukula mwezi uliwonse ncholinga choti akapeza kuti ikumera, azichotsa mphukirazo ndipo potero imasungika kwa nthawi yaitali. Njira ina yotetezera mbatata kuti isaonongeke ndikuipala makaka. Makakawa akauma mlimi akhoza kupanga ufa ndikumaphikira phalala, thobwa ndi zina zambiri, iye adatero. Katswiri wa mbewu za masamba ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Eric Chilembwe adati alimi akhoza kuchulukitsa phindu ku mbewuyi pogulitsa yophika kale kapena yootcha. Mulu umodzi wa mbatata umagulitsidwa motsika mtengo pamene kuyiphika kapena kuyiotcha ndikumagulitsa ndalama yake imakhala yooneka, iye adatero. Jean Pakuku ndi mmodzi mwa anthu a bizinesi omwe akupititsa patsogolo miyoyo ya alimi mdziko muno powagula mbatata yofiyira mkati ndikumapangira zinthu monga buledi ndi masikono.
4
Akupitilira Kukumana Ndi Zokhoma Kamba ka Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi Anthu a mdera la mfumu yaikulu Mwambo mboma la Zomba ati akupitilirabe kukumana ndi zokhoma kutsatira ngozi yadzidzidzi yomwe inagwa mderalo chaka chatha. Mmodzi mwa mzika za derali a Peter Taibu anena izi lachitatu pa mkumano omwe bungwe lowona za chitukuko mu mpingo wa katolika la Catholic Development Commission in Malawi (CADECOM) linakonza pakati pa anthuwa ndi akuluakulu a khonsolo ya boma la Zomba komwe amakambirana njira zomwe angayike pofuna kuthana ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi mderalo. Ngozi ngati izi zinadzetsa mavuto ochuluka Anthuwa apempha boma kuti liwamangire malo oti adzithawirako pamene madzi asefukira ndi cholinga choti asamasokoneze maphunziro kaamba koti ati pa nthawiyi amakabisala msukulu. Anthu azikathawira ku nyumba zomwe zimangidwe zija ndiye kuti ana azipitabe ku sukulu. Komanso pali misewu yovuta kuwoloka komwe tikufuna ma bridge, anatero a Taibu. Koma poyankhapo pa nkhaniyi mmodzi mwa akuluakulu a khonsolo ya boma la Zomba a Chriss Nawata anati khonsoloyo ikudziwa za mavuto omwe anthu akukumana ndipo anati ali mkati mokonza dongosolo lolimbikitsa kuti anthu adzichita mabizinesi osawononga zachilengedwe komanso ulimi wothilira pofuna kuti anthu adzitha kupedza zosoweka pa miyoyo yawo. Koma bungwe lowona zachitukuko mu mpingo wa katolika la Catholic Development Commission in Malawi (CADECOM) lomwe linakonza mkumanowu lati likufunitsitsa kuwona kuti miyoyo ya anthu akumudzi ndi yotetezeka ku mavuto a kusintha kwa nyengo. Ndipo mmodzi mwa akuluakulu a bungweli mdziko muno a Aerone Kandiwo-Ntaya ati bungwe lawo likhala likutsatira bwino pa zomwe khonsolo ya boma la Zomba yalonjeza kuti ichita mderali. Bungwe la CADECOM likugwira ntchitoyi mmaboma a Zomba, Balaka ndi Machinga ndi thandizo lochokera ku boma la Scotland kudzera ku mabungwe a Trocaire ndi Scalf.
18
Kudali kumapemphero a achinyamata Munthu aliyense ngakhale atakhala wachisodzera imakwana nthawi yomwe amayenera kusiya kusereula ndi kuchita zinthu zogwira mtima. Sam Sambo, ngakhale adali wachisodzera, adakhala adalimba mtima pamene adakumana ndi Emelia Chaula pofuna kumuuza za kumtima kwake. Watengeratu basi: Sam ndi Emelia patsiku la ukwati wawo Emelia ndi mphunzitsi wa kupulaimale pomwe Sam akugwira ntchito ndi bungwe la God Cares Orphan komanso amachita zisudzo ndipo ndi wapampando wa bungwe la Theatre Association Northern Chapter. Sam atamuona Emelia sadaugwire mtima koma tsiku lomwelo adamuuza za kugunda kwa mtima wake podziwa kuti bobobo samuthandiza ndipo akachedwetsa ena angamulande njoleyo. Sam adati iye adamuthira diso koyamba Emelia kumapemphero a achinyamata ndipo naye msungwana sadachedwe kugonekera khosi Sam atamuuza mawu achikondi. Mnyamatayu adalonjeza kuti iye wake ndi Emelia ndipo akazi ena adalibe nawonso ntchito ndipo kuchokera pomwepo Sam sadayanganenso akazi ena kufikira tsiku la ukwati wawo. Awiriwa adamanga woyera kumpingo wa St Andrews CCAP ku Mzuzu ndipo madyerero adachitikira pa Victory Temple ku Mzuzu komweko pa 11 July chaka chino. Sam adaululira Msangulutso kuti iye adagwa mchikondi ndi Emelia kaamba ka mtima wake wolimbikira ndi wodzipereka pantchito ya Mulungu. Emelia amachokera mmudzi mwa Kawazamawe, Themba la Mathemba (Paramount Chief) Chikulamayembe mboma la Rumphi ndipo ndi woyamba kubadwa mbanja la ana asanu. Sam ndi wa mmudzi mwa Yobe Sambo Inkosi Mtwalo mboma la Mzimba ndipo ndi wachiwiri kubadwa mbanja la ana asanunso. Banja latsopanoli lati silikufuna banja losalimba ngati mabanja ambiri amasiku ano ndipo iwo anenetsa kuti nthawi zonse aonetsetsa kuti akuika Mulungu patsogolo. Iwo ati nthawi zonse akakhala ndi vuto amayangana kwa Mulungu osati kupita kwa anthu omwe akhoza kukulitsa kavuto kakangono.
15
Akuganizira mwana kupha bambo ake Kudalembedwa mBaibulo kuti masiku otsiriza mitundu idzaukirana ndipo ana nawo adzaukira makolo awo koma osati momwe zafikira Mponda T/A Nyoka mboma la Mchinji. Mwana wina kumeneko akumusunga mchitokosi pomuganizira kuti adapha bambo ake pankhani ya malo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mneneri wapolisi mbomalo, Moses Nyirenda, watsimikiza kuti apolisi akusunga Christopher Chirwa wa zaka 56 pomuganizira kuti adapha bambo ake Pataleo Chirwa wa zaka 90, powanyonga pakhosi malingana nzotsatira za kuchipatala. Ndi mmene nkhani yonse ilili, tikukaikira mwana wa malemuyu pa zifukwa zingapo. Choyamba, adali limodzi tsiku lomwe malemuyo adakapezeka atafa. Chachiwiri, malemuyo adapezeka ali ndi chingwe mkhosi koma pamalo oti munthu sangadzimangilire ndipo chomaliza, achipatala adatsimikiza kuti malemuyo adafa kaamba kokhinyika, adatero Nyirenda. Nthawi zambiri, anthu omwalira kaamba kodzimangilira, amapezeka akulendewera, kutanthauza kuti sikelo ya thupi lonse imathera pakhosi pomwe padina chingwe chodzimangiliriracho. Chomwe chidazizwitsa anthu pa imfa ya bamboyu nchakuti adapezeka atakoledwa chingwe mkhosi ngati adadzimangirira koma thupi lonse lili pansi ngati wakhala tsonga ndipo nthambi yomwe idagwira chingweyo ili yowetezeka. Patsikulo, lomwe ndi pa 16 July, 2016 mmawa, Nyirenda adati mwanayo adauza bambo ake kuti apite kudimbako akaunikirane za malire koma bamboyo sadabwerere mpaka pomwe adapezeka atafa mmunda wina wa mphepete mwa njira. Nyirenda adati apolisi atafika pamalopo adatenga mtembo wa bamboyo nkupita nawo kuchipatala kuti akaupime pomwe mwanayo adapita naye kupolisi kuti afufuze nkhani yonse mwaufulu.
7
A maufulu ayamikira MCP Akatswiri andale kudzanso mabungwe oimira ufulu wa anthu mdziko muno ayamikila chipani chachikulu chotsutsa boma cha Malawi Congress Party (MCP) powonetsa chitsanzo chabwino kwambiri potsata ndale za demokalase posankha anthu mmaudindo kupyolera mnjira yovomelezeka ya chisankho. Chakwera (wachiwiri kuchokera ku manja) limodzi ndi mkazi wake Monica komanso akuluakulu ena kumsonkhanowo Mmiyezi iwiri yotsana ya July kudzanso August chaka chino, MCP yachititsa zisankho mu zigawo za kumwera ndi pakati. Ndipo mmenemo chaika anthu atsopano mmipando yosiyasiyana oyendetsa chipanichi mzigawozo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Katswiri wa ndale ku sukulu ya ukachenjede ya University of Malawi chigawo cha Chancellor College a Mustapha Husseni, ati zomwe ikuchita MCP ndiye zoyenera komanso zofunika kwambiri pa ulamuliro wa demokalase mchipani. Chipanichi mpofunika kuchiyamikira pazomwe chikuchitazi. Chikuchita ndale zololerana za-intraparty democracy, ndipo ife tingoti asaleke zimenezi chifukwa kumeneku ndiye kulimbitsa chipani mnjira yoyenera, atero a Husseni. Malinga ndi mneneli wa MCP a Jessie Kabwira, chipanichi chichititsanso chisankho chonga chomwechi ku chigawo cha kumpoto. Iwo ati akuchita zimenezi kuti chipanichi chikhale cholimba, ndicholinga chakuti pomadzafika nthawi ya chisankho chachikuru chosankha prezidenti wadziko, aphungu, kudzanso makhansala mu 2019, chidzakhale cha mphamvu kwambiri mmadera onse adziko lino. Mkulu wa Centre for the Deveopment of People (Cedep) , a Gift Trapence, sadabise mau kukhosi ponena kuti zimenezi sizachilendo ai, kaamba kakuti ndikofunikiradi kutero, maka poyanganila kuti eni ake a zipani za ndale ndi anthu wamba omwe ndiwochuruka. Zotsatira zake nzakuti zinthu zikamayenda motero, anthu ambiri amakhala nacho chikhulupiliro chipani choterocho. Iwo amadziwa kuti pakutero icho chikutsatsa njira zabwino za democracy. Ndiponso izi sizifunika mchipani mokhamo ai, komanso ngakhale dziko lonse, adatero a Trapence. Nawonso a Timothy Mtambo, a Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), potsilira ndemanga afotokoza kuti MCP yawonetsa kukhwima nzeru mu ndale za demokalase poika anthu mmaudindo mchipanichi kudzera mnjira yovomelezeka yachisankho. Zoonadi iyi ndi njira yabwino kwambiri, kusiyana ndikungoloza ndi chala kapena kumangosankhana ndi pakamwa pokha. Kuwonjezera pamenepa, ife tikupempha kuti zisathere pa maudindo angonoangono okhawa ai, komanso ngakhale wa pulezident ndi ena otere, zidzikhalanso chimodzimodzi. Pamenepa sitikunena MCP yokha ai, komanso zipani zonse za ndale mdziko muno, atero a Mtambo. A Mtambo anatinso ndizodabwitsa kuti MCP yomwe inkakanitsitsa kubweretsa ndale za demokalse mu ulamuliro wake wa chipani chimodzi, lero lino ikuposa zipani zina, pokhala patsogolo kuwonetsa chitsanzo chabwino pa ndale za zipani zambiri mdziko muno. A Mtambo anadzudzulanso mchitidwe omwe akuti zikuchita zipani zina mdziko muno, posankha mwana kaya mchimwene wake wa pulezident wa chipanicho kukhala mulowa malo, pomwe mtsogoleriyo akutula pansi udindo. Ngakhale kuti mdziko muno muli ufulu wakuti wina aliyense akhoza kupikisana nawo pa udindo wina uliwonse, komabe, mchitidwe okhala ngati waufumu, osiilana udindo muzipani za ndale ukukhumudwitsa anthu, komanso kuwopseza chitetezo cha ndale za democray. Zoterezi sizabwino nkamodzi komwe. Ndipo zitheretu. Apatu sitikunena muchipani cha ndale chokha ai, komanso ngakhale dziko lonse la Malawi. Tisawumilize anthu kuchita zomwe mwina iwo sakufuna. Alekeni otsatila chipani asankhe okha munthu yemwe akumufuna kuwatsogolera mchipanimo. Ndiye tikawonetsetsa, komanso kunena mwa chilungamo poyelekeza ndi zipani zina, zimenezo sitinaziwone pakali pano mu MCP. Pachifukwachi ndithu tikuwayamikira komanso kuwalimbikitsa kuti zimenezi apitilize, adatero Mtambo.
11
Anthu 7 afa pa ngozi mboma la Ntcheu Wolemba: Thokozani Chapola 0823-WA0070.jpg 584w" sizes="(max-width: 209px) 100vw, 209px" /> Anthu asanu ndi awiri (7) afa ndipo ena atatu avulala modetsa nkhawa galimoto yomwe anakwera itawombana ndi galimoto ina mboma la Ntcheu. Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub Inspector Hestings Chigalu watsimikiza za ngoziyi yomwe yachitikira pa Kanyimbo mbomalo. Iye wati mwa anthu amene afa pa ngoziyi amuna alipo anayi ndi akazi atatu. Lorry yomwe ndi frightliner imachoka ku Ntcheu kupita ku Dedza, driver amathamanga kwambiri ndipo atafika pa malopa anaphonya nsewu ndi kupita mbali ina ya nsewu komwe anakaomba magalimoto ena atatu, anatero Chigalu. Malinga ndi Chigalu, truck yi ati inanyamula ma belo afodya ndipo imodzi mwa galimoto zowombedwazo ndi minibus yomwe munakwera anthu ochulukirapo. Mwa anthu 7 amene afa pa ngoziyi anthu 6 ndi omwe anali mu minibus yo ndipo mmodzi ndi dalaivala wa galimoto ina yomwenso yawombedwa pa malopa.
14
Ophuzira Msukulu za Ukachenjede Apempha Boma Litsegule Sukulu Ophunzira msukulu za ukachenjede mdziko muno alembera kalata boma ndi cholinga choti litsekule sukuluzi zomwe zinatsekedwa kaamba ka mliri wa Coronavirus. Sukulu ngati izi zinatsekedwa Mlembi wa bungwe la ophunzira msukulu wa ukachenjede zonse za mdziko muno Gospel Sulebati wauza Radio Maria Malawi kuti ophunzirawa abwera ndi ganizoli powona kuti sukulu ndi zotseka pamene anthu a ndale mdziko muno akuchita misonkhano yokopa anthu pokonzekera chisankho chomwe chikudzachi komwenso akumasonkhanitsa anthu ambiri malo amodzi. Pamenepa iye wati mu chikalatachi ayikamo ndondomeko zomwe akuti azikatsatira ngati boma lingavomere kutsekuladi sukuluzi. Nkhani yaikulu ndi yoti tikufuna boma litsegule sukulu kamba ka zomwe tikuona kuti misonkhano ya ndale ikuchitika ndiponso ma border ndi otsegula, anatero Sulebati. Iye wati malinga ndi kalata yomwe alembera bomali ati ndi okonzeka kutsatira njira zopewera matenda a COVID-19 sukuluzi zikatsegulidwa. Padakalipano unduna wa zamaphunziro sunayankhulepo kanthu pa nkhaniyi.
3
Khrisimasi ya maluzi Kwangotsala masiku anayi kuti chisangalalo cha Khrisimasi chifike pachimake koma ochita bizinesi zosiyanasiyana akudandaula kuti sizikudziwika kuti nyengoyi yafikadi malingana ndi momwe akuvutiramalonda. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ochita malonda mmisika ikuluikulu ya mmizinda ya Mzuzu, Lilongwe ndi Blantyre ati pomafika nthawi ngati zino mzaka zammbuyomu, bizinesi zawo zimayenda kwambiri moti ena amapikula katundu kawiri kapena katatu pasabata, koma chaka chino akuti zimenezo kulibeko. Ngakhale msitolo zikuluzikulu monga za Shopright malonda sakuyenda kwenikweni Anthu ena omwe adapikulira katundu mwezi wa November mpaka lero akadagulitsa yemweyo, malonda akuvuta. Zoti ndi December malonda amayenda ayi ndithu, osadziwika nkomwe, adatero Mlembi wa ochita malonda mumsika wa mzinda wa Mzuzu Justin Hara pocheza ndi Tamvani Lachitatu. Iye adati momwe zikuonekera, anthu alibe ndalama kapena ndalama ali nazo koma akuopa kuti akazisakaza adzavutika, malingana ndi momwe chuma chikuyendera. Tikuganiza kuti ambiri akulingalira za mafizi akwerawa komanso akuti akaona momwe chuma chikuyendera akuda nkhawa kuti akadya ndalama adzakhala pamavuto aakulu. Magulitsidwe ake akungokhala ngati talowa kale January, adatero Hara. Wa pampando wa msika waukulu mumzinda wa Lilongwe, George Banda, adati zikuoneka kuti chaka chino mumsika nzamalodza zomwe sizidachitikepo nkale lonse. Malonda asanduka ngati muja amachitira a minibasi kuchita kuthamangira munthu kunjira kumukokera pamalonda, kutanthauza kuti bizinesi yafika povuta. Zikumatheka ena mpaka kuweruka momwe adabwerera ndithu, adatero Banda. Mkuluyu adapereka tsatanetsatane wa momwe ochita malondawa amatcherera bizinesi zawo polinganiza katundu yemwe amakonda anthu akumudzi ndi apantchito zomwe adati sizikutheka chaka chino. Timatchera kuti mwezi wa November timapikula zomwe amakonda anthu akumudzi ndipo timayembekezera kuti tikalowa December katundu ameneyu amakhala atatha chifukwa anthu ambiri akumudzi amadzaguliratu zinthu kuti azikagwira ntchito zina. Tikamalowerera mkati mwa December, timakapikula za anthu apantchito mtawuni, koma pano ambiri tikadali ndi katundu woyambirirayo, adatero Banda. Kaphidigoliyu sadasiye anthu a kummwera komwe akuti nako zinthu sizikuyenda momwe zimakhalira mmbuyomu. Wapampando wa ochita malonda mumsika waukulu ku Blantyre, Himon Amanu, adati nyengo ngati ino mumsinkawu mumakhala gulu la mundipondera mwana, koma chaka chino anthu akuyenda mosacheukacheuka. Zinthu zatembenukiratu, palibe chikuyenda. Anthu afumbata ndalama zawo ndipo sakufuna kuononga, ayi, adatero Amanu. Zonsezi nchifukwa cha kuchepa mphamvu kwa ndalama ya kwacha. Chaka chino chokha kuchoka mu March ndalama ya kwacha yagwa kuchoka pa K435 posinthanitsa ndi ndalama ya Amerika ya dollar kufika pa K612 mwezi uno wa December. Kuchepa mphamvu kwa ndalamayi kwadza chifukwa chakuti dziko lino silikugulitsa malonda kumaiko akunja mokwanira. Kupatula fodya, shuga, tiyi, thonje ndi mbewu zina, palibe malonda omwe dziko lino likudalira kuti akhazikitse kwacha pansi. Malingana ndi odziwa za chuma, mphamvu ya ndalama imakhazikika ngati dziko likupanga katundu wabwino yemwe maiko ena akumukhumba. Dziko la Malawi limadalira mabungwe ndi maiko akunja omwe amapereka thandizo la ndalama, zomwe zimapangita kuti ndalama ya kwacha isakhale pendapenda. Ndiye pomwe mabungwewa adati asiya kuthandiza dziko lino kaamba ka kusolola ndalama mboma, mavuto akhala aakulu mdziko muno. Chinanso chomwe chikupangitsa kuti ndalama ya kwacha iguge ndi chakuti dziko la Amerika chuma chake chikuyenda bwino kwambiri, zomwe zapangitsa kuti ndalama ya dollar ikhale yamphamvu kuposa ndalama zina monga ndalama ya pound. Izi zapangitsa kuti maiko ambiri osauka akhale pachiopsezo chifukwa chuma chawo sichikuyenda bwino. Bungwe la International Monetary Fund (IMF) lomwe ndi limodzi la mabungwe omwe amathandiza dziko lino ndi ndalama, msabatayi lati dziko la Malawi liyenera kukhwimitsa ndondomeko ya zachuma chake kuti anthu osolola ndalama asiye. Bungwelo latinso boma lichepetse kusakaza ndalama pazinthu za zii zopanda mutu, kuonjezera kuti boma likuyenera kuchitapo kanthu kuti zinthu zitsike mtengo poonetsetsa kuti pali mfundo zabwino zoongolera chuma. Koma bungwe la amipingo la Public Affairs Committee (PAC) lati anthu asaiwale cholinga cha chikondwererochi poganizira zosakaza ndalama. Wapampando wa bungweli, mbusa Felix Chingota, wati nyengoyi ndi yokumbukira kubadwa kwa mpulumutsi Yesu Khrisitu osati kungolingalira zonjoya basi. Inde, ndi nyengo yachisangalalo anthu akuyenera kusangalala, koma asaiwale cholinga cha chisangalalocho chifukwa ena amapezeka kuti chisangalalo chomwecho avulala nacho mwinanso kutaya nacho moyo mmalo mopata moyo mwa Yesu Khrisitu, adatero Chingota.
2
African Airlines Yataya 400 Million Dollars Kaamba ka Coronavirus Bungwe lowona za maulendo a pa ndege kuno ku Africa la African Airlines lati lawononga ndalama zokwana 4 Hundred Million za ku America chiyambireni mliri wa kachilombo ka Coronavirus mdziko la China kuyambira mwezi wa February chaka chino. Malipoti awailesi ya BBC ati izi zadza kutsatira kutsekedwa kwa mabwalo andege mmaiko akuno ku Africa ngati njira imodzi yofuna kupewa kufala kwa kachilomboka kaamba koti maiko ambiri amachita malonda ndi dziko la china. Ngakhale izi ziri chomwechi komwe kumafikira ndege zonse kuno ku Africa mdziko la Ethiopia adakagwirabe ntchito zawo ponyamula anthu mdzikolo kupita komanso kubwera mdziko la China mmizinda yonse isanu ya mdzikolo. Polankhulapo mkulu wa bungwe la International Air Transport Association (IATA) Raphael Kuuchi wati ntchito za malonda zomwe zimayenda bwino zayima kaamba ka kuletsedwa kwa maulendo apandege mmaiko akuno ku Africa kupita kapena kubwera mdziko la China. Mayiko omwe aletsa maulendo a pa ndenge ndi dziko la China ndi monga South Africa, Tanzania, Mauritus, Morocco, Rwanda komanso Kenya. Padakali pano nthendayi yafikira mmaiko a Egypt, Tunisia, Morocco, Algeria, Nigeria komanso Senegal kuno ku Africa.
2
Anthu Atentha Nyumba ya Mfumu Yawo ku Dedza Apolisi mboma la Dedza akusakasaka anthu ena omwe achita zaupandu potentha nyumba za mfumu Kapesi ya mdera la mfumu yayikulu Kachere mbomalo, ati pokwiya ndi zimene achita powagulitsira malo a makolo awo ku khonsolo ya bomalo. Wachiwiri kwa ofalisa nkhani za apolisi mbomalo Sergeant Cassim Manda watsimikiza za nkhaniyi. Iye wati anthu aupanduwo poyamba anakumana ndi bwanamkubwa wa mbomalo ndi kuwadandaulira za nkhaniyi, koma kuti sanamvane bwino. Anthuwo pambuyo pake anagoganiza zokachitira zamtopola onse omwe amakhudzidwa ndi nkhaniyi kuphatikizapo mfumuyi, anatero Manda. Padakalipano onse omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi omwe ndi a Rodrick Kapesi a mmudziwo, kudzanso a Daveston Mandalawe omwenso ndi Group Village Headman Memezeya, ndinso Dalison Magwaza omwe ndi mlangizi wa amfumu ayamba kukhala mwamathantha ati powopa kuti mwina anthu a zamtopolawo atha kuwachita chiwembu.
14
Bwalo lilanga mphunzitsi wochimwitsa mwana Bwalo la milandu la majisitireti la Mzuzu lapeza mphunzitsi wina wolakwa pamlandu wochimwitsa mtsikana wosakwana zaka 16, komanso kupereka mankhwala ochotsera pathupi pomwe adampatsa. Bwaloli likuyembekezeka kupereka chilango chake mawa pa 22 February. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Lachinayi sabata yatha bwaloli lidamva kuti Mtendere Phiri, wa zaka 31, yemwe kwawo ndi ku Bembeke, T/A Kachindamoto, mboma la Dedza, adayamba kugonana ndi mwanayu mwezi wa April chaka chatha. Bwaloli lidamva kuti Phiri, yemwe amaphunzitsa pasukulu ina yapulaimare ku Ekwendeni mboma la Mzimba, adanyengerera mtsikanayu kuti akakana chibwenzi, asiya kuphunzitsa pasukulupo ndipo apita kwina. Izi zidamukhudza mtsikanayu ndipo posafuna kuti mphunzitsiyo achoke, adamulola ndipo ankapita kunyumba kwake mkazi wake akapita ku Mzuzu kwa mayi ake, adawerenga majisitireti Agness Gondwe. Apatu nkuti Phiri yemwe adavala malaya ofiira, ali wera mchitokosi cha bwalo la milandu, naye mkazi wake ali poteropo kumvetsera majisitiretiyu. Ndipo iye adapitiriza kuti malinga ndi umboni womwe udaperekedwa mbwalolo masiku apitawo, awiriwa ankachita zadamazi kuchipinda kwa mphunzitsiyu. Gondwe adati mtsikanayu adauzanso bwalolo poperekera umboni wake kuti zadamazi zidachitika kosawerengeka ndipo Phiri adamuuza kuti akadzadutsitsa mwezi osasamba adzamudziwitse msanga. Iye adati mwezi wa July msikanayu adaima ndipo atamudziwitsa mphunzitsiyu, sadachedwe koma kumupatsa mapilitsi awiri a Brufen komanso a Bactrim zomwe sizidaphule kanthu chifukwa pathupipo sipadachoke. Majisitiretiyu adati apa mtsikanayu adapita kutchuthi mumzinda wa Mzuzu komwe pobwerera mmwezi wa September mayi ake adamuzindikira kuti adali ndi pathupi. Iye adati mayi a mtsikanayu adamuuzitsa kuti asachotse mimbayo, koma izi sizidathandize chifukwa atakumananso ndi mphunzitsiyo adamuuza kuti ngati atasunge pathupipo zake zida. Malinga ndi umboni womwe udaperekedwa mbwalo lino, Phiri adamuuza mtsikanayo kuti apite naye kuchipatala cha Banja La Mtsogolo (BLM) akamuchotse, koma atakana adakagula mankhwala asanu ndi anayi kuchipatalachi, adatero Gondwe. Mtsikanayu atamwa, pathupipo padachokadi pakati pa usiku ndipo adakataya zomwe zidatulukazo mchimbudzi. Koma madzi adachita katondo pomwe mtsikanayu adayamba kugudubuzika ndi ululu wa mmimba ndipo adaulula kwa mayi ake kuti mphunzitsiyo ndiye adali mwini nkhaniyi. Apa adathamangira naye pachipatala chachingono cha mderali komwe adamutumiza kuchipatala chachikulu cha Mzuzu Central komwe adamuchotsa zotsalira. Ndipo mayi a mwanayu molimbikitsidwa ndi a mabungwe adakamangala kupolisi komwe adamutsekera Phiri pa September 23 chaka chatha. Christon Ghambi, yemwe akuimira mphunzitsiyu, adaseketsa bwaloli pomwe adalipempha kuti limuganizire phiri posampatsa chilango chokhwima poti adapereka mankhwala ochotsera pathupiwo kuti tsogolo la mwanayu lisaonongeke.
7
Khansala Adandaula ndi Mchitidwe Otumiza Ana ku Jubeki Wolemba: Sylvester Kasitomu Anthu a mboma la Mangochi awapempha kuti apewe mchitidwe ololera ana awo kuti azitengedwa ndikupita nawo kunja kwa dziko lino ndi cholinga chofuna kukawapezera ntchito kamba koti mchitidwe-wu ndi umene ukuyika pa pachiopsezo miyoyo ya ana ambiri mdziko muno. Khansala wa dera la Nthundu mdera la pakati mboma la Mangochi khansala Coster Bwanali ndi amene wanena izi polankhula ndi mtolankhani wathu. Iye wati ndi zomvetsa chisoni kuti ana ambiri akapita mmayiko ena kukagwira ntchito akumakagwilitsidwa ntchito zoposa usinkhu wawo ndi zina zosayenera, kotero makolo akuyenera kumaonetsetsa kuti akutetedza bwino ana awo ku mchitidwe-wu. Ife anthu akumangochi kuno timakonda kutumiza ana athu ku jubeki koma tisakudziwa komwe akukafikira kapena munthu amene akumutenga izi tidziwe kuti ndi zolakwika ndipo tikuyenera kusiya khalidwe limeneli, anatero Bwanali. Mwazina iwo apempha makolo omwe atumiza ana awo mmaiko akunja kuti akagwire ntchito zosiyanasiyana kuti achenjere maka popewa kupasira anawa anthu oti sakuwadziwa bwino bwino kaamba koti ena mwa iwo amakhala ndi zolinga zolakwika. Boma la Mangochi ndi limodzi mwa maboma amene ali ndi anthu ambiri omwe akugwira ntchito komanso kukhala ku maiko akunja zomwe zikuchititsa kuti milandu yozembetsa anthu ikule mbomali.
14
Chipalamba ku Malawi Dziko la Malawi likusanduka chipalamba. Kafukufuku wathu wapeza kuti mafumu ndi apolisi ena ndiwo akuthandizira kusambula dzikoli pamene akuthandizira kudula mitengo mosasamala ndi kuotcha makala. Lidali dziko la nkhalango zowirira. Koma lero, madera ambiri ali mbee! Ukaona mitengo, ndiye kuti ndi pamanda. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Makala kudikira kuti awatengere kumalonda Malinga ndi unduna woona zachilengedwe, dziko lino lili pamwamba pa maiko a mu Sadc posakaza mitengo ndipo padziko lonse lapansi, lili pa nambala 4. Mtolankhani wathu sabata yatha adalowa geni ya makala mboma la Ntcheu. Uku ndi kumalire a Neno ndi Mwanza. Iye adapeza anthu ochuluka akuchita bizinesi yootcha ndi kugula makala. Mitengo yambiri yatsala kuderali ndipo amene amapanga makala mmaboma a Mwanza ndi Neno asamukira kumeneko. Mtunda woposa makilomita 90 umene udali ndi mitengo yambiri yachilengedwe lero ndi mpala. Mitengo yatha ndipo mitengoyi ikugwetsedwa mmalire a Malawi ndi Mozambique. Mtolankhaniyu atafika, adauzidwa kuti akakumane ndi nyakwawa Kabwayibwayi ya mboma la Ntcheu yomwe imupatse malo woti agwetse mitengo. Mfumuyo idatsimikiza kuti mitengo ilipo ndipo kuti mtolankhaniyu aotche makala, akuti amayenera kulipira cha nkhalango. Cha nkhalango ndi K2 000, idatero mfumuyo. Mtolankhani adauza mfumuyi kuti akufuna apange uvuni zisanu zotalika mamita 20. Koditu kuli golide [mitengo], ndi zotheka, idatero mfumuyo. Mita imodzi ndi K2 000, ngati mulibe ndalama ndiye mukaphula makalawo mudzapereka matumba atatu [olemera makilogalamu 50 lililonse], adaonjeza. Poona kuti zitenga masiku ambiri, mtolankhaniyu adaganiza zogula makala kwa ogulitsa ena kumeneko. Thumba lililonse limagulidwa K2 000. Kuti thumba lifike ku Blantyre kokagulitsira, umayenera ulipe K2 500 kwa mwini galimoto. Kupatula izi, adatinso ndipereke K300 pa thumba lililonse yomwe imakhala ya apolisi. Masiku ambiri timakumana ndi apolisi amene amatilipiritsa. Ndiye timakonzeratu kunoko kuti tisavutike mayendedwe, amene amathandiza mtolankhaniyo kupanga makalawa, Happy adatero. Mtolankhaniyo atafunsa Happy kuti pa roadblock ya polisi ya Zalewa akalipira chiyani, iye adayankha kuti malowo ngosavuta. Harry adaoda matumba 70. Mungomupatsa dalaivala K2 500 ndi K300, ndalamayi imathandiza zonsezi ndipo matumba anu akakupezani ku Blantyre, adatero. Anthu onse amene adali ndi makala adapereka ndalama zawo kwa woyanganira kampuyo pamene iwo adanyamuka ulendo ku Blantyre. Lachisanu onse amene adakwezetsa makala awo adachoka kumaloko. Sitiyenda limodzi ndi galimotoyi, adzangotiuza kuti makala afika, tiyeni tibakadikirira ku Blantyre, adatero Happy. Sipadatenge nthawi, Loweruka mma 3 koloko mmawa, mtolankhaniyu adalandira foni kuti galimotoyo yomwe idanyamula matumba 250 yafika msika wa Khama ku Machinjiri. Onse amene adakweza makalawo adali pamalopo kugulitsa makalawo. Patsikulo bizinesi simayenda bwino chifukwa thumba lomwe poyamba limagulidwa K9 000, limapita pa K5 000 mpakanso kumafika pa K3 500. Malinga ndi unduna woona zachilengedwe, pafupifupi mahekitala 3.4 miliyoni aonongeka pootcha makala. Mu June chaka chino, komiti yoona zachilengedwe ku Nyumba ya Malamulo idapempha undunawu kuti uletse kuotcha komanso kugulitsa makala mdziko muno. Wachiwiri kwa mkulu wa za nkhalango Ted Kamoto akuti dera la Neno, Ntcheu ndi Mwanza ndi lomwe likutulutsa makala ambiri pakadalipano. Kumeneko mitengo ikugwetsedwa kwambiri pamene akupanga makala, adatero. Malinga ndi Kamoto vuto la kuotcha makala lakulanso kwambiri chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi komanso kuchepa kwa chiwerengero cha Amalawi amene amagwiritsa ntchito magetsi pophika. Amalawi 85 mwa 100 alionse amagwiritsa ntchito makala ndi nkhuni pophika. Izi zili choncho, 15 mwa 100 ndiwo amagwiritsa ntchito magetsi. Izi zafika pena chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi, adatero iye. Koma mneneri wa polisi James Kadadzera akuti anthu akuyenera akanene kupolisi ngati wapolisi wina akufuna ziphuphu kuti adutsitse makala. Ngatinso akuti akumapereka ndalama ku 997, atiuze nambala ya galimotoyo. Komanso atiuze wapolisi amene walandirayo, adatero iye.
18
Anatchereza Mkazi wanga koma mkonono Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Langa ndi dandaulo pa mkazi wanga wokondeka. Iyetu mwano alibe ndiponso ntchito amagwira molimbika. Abale anga amawalemekeza ndipo ana athu akuloledwa bwino. Koma chimodzi, mkazi wanga mkonono. Ndichite chiyani? YH, Zomba. YH, Zoonadi mkonono nthawi zina umasokoneza anthu ena. Komatu ichi si chifukwa choti nkudana nawo. Muziwalimbikitsa akazi anuwo kuti azigona chambali kapena kuti champeni, osati chagada. Mudziwe kuti nthawi zina mkonono umadza chifukwa munthu ndi wonenepa kwambiri. Choncho alimbikitseni akazi anuwo azichita masewera olimbitsa thupi kuti mwina thupi nkuchepako komanso kusamala zimene amadya kuti zisakhale zonenepetsa kwambiri. Nthawi zinanso, kumwa mowa kwambiri ngakhalenso kusuta kumakuza mkonono. Kusiya izi kukhonza kuthandiza. Koma ngati zikupitirira, mukhonza kumatchinga makutu anu ndi zinthu zina monga thonje. Ngati nyumba yanu ndi ya zipinda zingapo, mukhonza kumakagona chipinda china. Machitidwe a mbanja muziona nokha. Mwamuna wanga ulesi Zikomo Anatchereza, Ndidakwatirana ndi mwamuna wanga chaka chatha koma ndiwaulesi osati masewera. Ndimagwira ntchito masiku ochuluka ndine ndipo ndikabwera amayembekezera kuti ndiphike ndine komanso kukonza mnyumba. Nthawi zonse ndimakhala otopa moti sabata iliyonse ndimapita kwa makolo anga kuti ndikapumeko. Ndichite naye chiyani? AB, Lilongwe. AB, Nzomvetsa chisoni kuti amuna ena akadali ndi moyo woti ntchito zonse azigwira ndi amayi. Kukakhala kumudzi, mupeza amayi ndi abambo apita limodzi kumunda kukalima. Pobwera uko, amayi asenza nkhuni kumbuyo atabereka mwana. Kufika pakhomo, amayiwo amapita kumadzi, kenako kuphika nsima ndi ndiwo. Chonsecho abambo akusewera bawo. Khalidwe ili ndi lachikale. Zoti ntchito zonse zapakhomo azigwira ndi mayi zidapita. Mukuyenera kulankhula naye mwamuna wanuyo chifukwa izi sizikuthandizani. Komanso mopempha, zothawira kwa makolo anu sizikuthandizani. Kumeneko sikuthana ndi vuto koma kungolikankhira kaye pambali. Adakwatiwa ndi ndale? Anatchereza, Ndimanyadira ndi malangizo anu. Kale, ndinkaona ngati sindingakhale ndi vuto mpaka kukuuzani. Koma izi zandikulira. Mkazi wanga koma ndale. Chingasinthe chipani cholamula, iye amapezeka nsalu ya chipanicho ali nacho. Ndipo kukangoti kuli msonkhano, timayembekezera kuti tidya mochedwa. Ndikamufunsa, amayankha kuti akukonza kapansi, tilemera chifukwa anzake ena apita patsogolo poimbira ndi kuvinira andale. Ndimusiye? Dennis M, Zomba. Bambo Dennis, Kuimbira andale kumayenera kutha kalekale. Nzomvetsa chisoni kuti amayi, asungwana komanso abambo ndi achinyamata ena akusiya ntchito zawo kukaimbira andale. Ili si vuto la amayi okha, mwaonapo inu achinyamata akudzipenta makaka a chipani. Sindikudziwa kuti amapindula chiyani. Koma chomwe ndikudziwa uku nkutaya nthawi.
12
Akhumudwa ndi kutsika kwa nandolo Alimi a nandolo ena mboma la Mulanje, ati ali ndi nkhawa ndi kutsika mtengo kwa nandolo modzidzimutsa pamsika zomwe zikukayikitsa alimiwo ngati apindule naye chaka chino. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mmodzi mwa alimiwo, Henry Kapalasa, wa mmudzi mwa Chabwera kwa T/A Mabuka mbomalo, adati nandolo watsika mtengo kwambiri padakalipano zomwe alimi sadayembekezere kuti zingatero popeza malonda adayamba bwino mmadera ambiri. Pamene ena akolola nandolo, wina akadali mmunda kuti aume bwino Kapalasa, yemwe ndi gogo wa zilumika zoposa 90, adati chiyembekezo chake pa mbewuyo chayamba kumira mmadzi popeza lingaliro loti apeza makwacha a nkhaninkhani pakutha pamsikawo, ayamba kukayikitsa. Kuno alimi ambiri tapeza nandolo wochuluka koma tsopano tagwira njakata ndi momwe zilili pamsika popeza miyezi yapitayi nandolo tinkagulitsa pa mtengo wa K600 pa kilogalamu koma tsopano lero wafika pa K300 pa kilo. Kutsika kotereku sikunachitikepo nkale lonse, adatero Kapalasa. Iye akuganiza kuti mchitidwewu nkubera alimi omwe amadalira ulimi wokhawo pa chaka kuti apeze makwacha otukulira banja lake. Chaka chino chimanga sichinachite bwino kudera lino moti anthu ambiri tayamba kale kukumana ndi mavuto adzaoneni ndi kukwera kwa mtengo wa chimanga popeza thumba la chimanga cholemera makilogalamu 50 lafika kale pa K12 000. Maso athu adali nganganga pa nandolo kuti mwina tikagulitsa tipeza ndalama zogulira chimanga, koma pamenepa tasowa pogwira, anadandaula iye. Kapalasa akufunitsitsa boma likadalowererapo msanga ncholinga choti alimi apeze phindu lokwanira pa ulimiwo. Gogoyo akuganiza kuti kupanga magulu zingathandize alimiwo kupeza phindu lamnanu pa ulimiwo. Alimi ambiri mboma la Mulanje adakolola nandolo wochuluka ndiponso wina adakali mminda kulindira kuti awume moyenera. Masiku apitawo mkulu wa bungwe la alimi a nandolo la Nandolo Association of Malawi Susan Chimbayo adapempha alimi kuti asagulitse msanga nandolo wawo, komanso kuti akonze magulu kuti azikagulitsa ku makampani kumene mtengo umakhalako bwino.
13
Okhudzidwa ndi Nsewu wa Chingale Sanalandirebe Chipukuta Msonzi Anthu omwe akhudzidwa ndi ntchito yokonza nsewu wa Lirangwe-Chingale-Machinga mu gawo loyamba la ntchitoyi apempha boma kuti lichite changu kuwapatsa chipukuta misonzi kuti apeze malo okhala. Malinga ndi mfumu Kalalichi 2 ya mmdera la mfumu yaikulu Mlumbe mboma la Zomba, iyo ndi yokhudzidwa kwambiri kamba koti chiyambire cha ntchitoyi yomwe tsopano yadutsa masiku ake omalizira pa gawo loyamba palibe amene walandira chipukuta misonzi. Anthu sanalandirebe nde tikusowa kuti akatsiriza ntchitoyi tizakafunsa kuti za ndalama zathu, inatero mfumu Kalalichi. Wati anthuwo athandizidwa-Kajanga Poyankhapo za nkhaniyi mneneri kubungwe loona za misewu la Roads Authority a Portia Kajanga ati zolembalemba zonse zokhudza chipepeso zili mmanja mwa bungwe loona zamalo ndipo akamaliza awapatsa chipukuta misonzi ngakhale boma silikuyenera kutero kamba ka malamulo. A Kajanga ati anthuwa ndalamazi apatsidwa kaamba kongomveredwa chisoni kaamba koti malamulo amaletsa kupepesa anthu omwe amanga kapena kulima mu gawo limodzi la nsewu.
17
Ndale pamaliro nchitonzo Katswiri pa zachikhalidwe, Emily Mkamanga wati zomwe zakhala zikuchitika pa miyambo ya maliro mdziko muno ndi belu lozindikiritsa kuti andale si ofunika kuwapatsa mpata wolankhula pa miyamboyi. Mkamanga adanena izi pamene mpungwepungwe udabuka pamaliro a mayi a Senior Chief Lukwa ku Kasungu pomwe phungu wa deralo wa chipani cha MCP Amon Nkhata adalandidwa chimkuzamawu ndi gavanala wa DPP Osward Chirwa pomwe mmodzi mwa akuluakulu a DPP Hetherwick Ntaba adathothedwa pamaliropo. Izi zachititsa mfumu yaikulu ya Achewa ku Zambia, Malawi ndi Mozambique Kalonga Gawa Undi alembere mafumu a kuno kuti afotokoze chimene chidatsitsa dzaye kuti mpungwepungwewo ugwe. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mmbuyomu, Paramount Lundu idawoozedwa pamaliro a mfumu Kabudula pomwe adanena kuti chipani cha MCP sichingalamulirenso dziko lino. Ndipo kudalinso mpungwepungwe ku zovuta za anthu amene adamira panyanja ku Jalawe mboma la Rumphi pomwe achipani cha DPP adakhambitsana ndi a Livinstonia Synod ya CCAP. Mkamanga adati nthawi ya maliro, anamfedwa amakhala mchisoni ndipo khamu la anthu omwe limasonkhana limadzakuta ndi kukhuza malirowo osati kudzamvera kampeni kapena mfundo za ndale. Sindidziwa kuti amaganiza bwanji. Nthawi yoti mnzako akulira, iwe sungasandutse guwa lochitirapo kampeni. Kuli bwino andalewo asamapatsidwe mpata nkomwe woti alankhule pamaliro, adatero iye. Iye adati zimamvetsanso chisoni kuti anthu ena amaveka maliro dzina la chipani pomati maliro awa ndi achipani chakuti pomwe pachilungamo chake, chipani chilibe maliro, maliro amakhala a banja. Chilowereni chaka chino chokha, malilo angapo makamaka a anthu akuluakulu kapena odziwika akhala akusokonekera chifukwa cha zolankhula za andale.
11
Tsiku lokumbukira usodzi Chaka chino zangokumanizana ndendende kuti lero, pa 21 November, ndi tsiku loganizira nsomba ndi ntchito za usodzi padziko la pansi (World Fisheries Day). Bungwe la United Nations lidakhazikitsa tsikuli pokhudzidwa ndi kuchepa kwa nsomba komanso kusakazika kwa zachilengedwe zammadzi padziko lonse. Patsikuli, asodzi padziko lonse amakonza zochitika zosiyanasiyana zozindikiritsa anthu kufunika kwa nsomba pamiyoyo ndi chitukuko cha maiko awo, dziko lapansi komanso kusamalira zachilengedwe zammphepete mwa nyanja. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kwathu kuno, tsikuli lidakumbukiridwa koyamba chaka chathachi pamwambo umene udachitikira mboma la Nkhata Bay. Mwambowo udakonzedwa ndi bungwe la Ripple Africa. Miyoyo ya anthu oposa 400 000 amene amadalira usodzi paumoyo wawo ili pa chiopsezo, kaamba kochepa kwa nsomba mnyanja ndi mmitsinje ya dziko lino. Chimene chikuchitika pakalipano nchakuti pamene mitundu ya nsomba zofunika kwambiri monga chambo, kampango ndi utaka zikusowa, mpamene bonya akuchulukirachulukirabe. Mtsogolo muno tidzafotokozera chifukwa chiyani zinthu zikubwerera chammbuyo chonchi, koma pakalipano nkofunika kulimbikitsa njira zimene zikutsatidwa poteteza nsomba kuti anthu ambiri asadzasowe pogwira zisanatheretu. Usakhale udindo wa boma lokha komanso mafumu, asodzi eni ake, anthu wamba, mabungwe monga a Ripple Africa, USAID Pact, World Fish Centre ndi sukulu zaukachenjede kugwirana manja ndi kumaimba nyimbo imodzi poteteza nsomba. Nyanja zonse za mdziko muno zimayerekezedwa kuti zimatulutsa nsomba zoposera 50 000 tonnes pachaka, zomwe nzochepa kwambiri kukwanitsa kudyetsera mtundu wa Amalawi. Motero sizodabwitsa kuti nsomba zina zimalowa mdziko muno kuchokera kumaiko ena. Kaamba ka kuchepa kwa nsomba, munthu mmodzi akumuyerekeza kuti akumadya makilogalamu anayi okha mmalo mwa makilogalamu 14 a nsomba pachaka. Izi zikupereka chithunzithunzi kuti ndi nsomba zochepa zimene zikumaphedwa mnyanja ndi mmitsinje ya dziko lino, motero nkofunika kulimbikitsa njira zobwezeretsanso chiwerengero cha nsomba monga kutseka kwa nyanja komanso kuyambitsa ulimi woweta nsomba mmaiwe.
15
Anatchezera Ndazunguzika Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 18 ndipo ndinazunguzika mutu chaka chatha pomwe ndinapezeka ndi kachilombo ka HIVkoma sindinagonepo ndi munthu ngakhale ndinali nacho chibwenzi. Amayi anga ali ndi HIV koma abambo anga alibe. Banja la makolo anga lidatha ndili ndi chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri. Ndine woyamba kubadwa koma ana onse obadwa kwa amayi anga amabadwa ndi kachilombo. Amayi anga akuti adatenganso pathupi ine ndili ndi miyezi 9 koma abambo anga amakana kuti mwanayo adali wawo. Ndiye ine zinandizunguza mutu kuti kodi zidayenda bwanji. Abambo anga ndi amayi anga ondipeza amandinena kuti ndinatenga kachilomboka kwa chibwenzi chomwe ndinali nacho. Mankhwala ndinayamba kumwa sabata yomwe anandipeza ndi kachilomboka popeza chitetezo chinali chotsika kwambiri, koma sindinadwale, ndidangopita ndekhala kukayezetsa ndipo ndinalibe nkhawa iliyonse. Koma pano ndikusowa mtendere. Ndithandizeni, chonde, nditani? RM, Mzuzu Zikomo mwana wanga RM, Nkhani yako ndaimva bwino lomwe ndipo ndakunyadira chifukwa ndiwe mtsikana wolimba mtima. Si ambiri amene amalimba mtima kukayezetsa magazi ngakhale sakudwala kuti adziwe momwe chitetezo chilili mthupi mwawo, ambiri amaopera kutalitalisafuna kudziwa nkomwe ngati ali ndi kachilombo kapena ayi. Wanena kuti udapezeka ndi kachilombo ka HIV chaka chatha koma wanenetsa kuti sudagonanepo ndi munthu wina aliyense ndiye zidatheka bwanji kupezeka ndi kachilomboka? Iyidi ndi nkhani yozunguza chifukwa ngakhale pali njira zambiri zotengera kachilomboka, njira yodziwika kwambiri ndi yogonana mosadziteteza ndi munthu amene ali ndi kachilomboko. Koma zimatheka ndithu kutenga kachilomboka mwatsoka ndithu ndipo imodzi mwa njira zotere ndi kutengera kachilomboka pobadwa kuchokera kwa mayi amene ali nako. Ndikhulupirira iweyo udatenga kachilomboka panthawi yobadwa chifukwa wanena kuti ana onse obadwa mwa mayi ako akumapezeka ndi kachilombo ka HIV. Chomwe ndingakulangize nchoti pitiriza kumwa mankhwala otalikitsa moyo ndipo udzisunge monga wadzisungira nthawi yonseyi ndipo udzakhala ndi moyo wautali, wosadwaladwala. Uziyesetsa kuti usamakhale ndi nkhawa chifukwa izi zikhoza kubweretsa mavuto ena pamoyo wako. Uzilandira uphungu woyenera kwa akatswiri odziwa za kachilombo ka HIV kuti ukhalebe ndi moyo wathanzi ndi wansangala, osati kudzimvera chisoni. Kupezeka ndi kachilombo sikutanthauza kuti ufa nthawi iliyonse, ayi, utha kukhala zakazaka mpaka kukalamba monga ine, bola kudzisamalira. Amadikira ndimuimbire Anatchereza, Ndine mtsikana wa zaka 15 ndipo ndili ndi chibwenzi koma anapita ku Nkhotakota. Poyamba timaimbirana foni koma panopa adaleka, amadikira ine ndiimbe. Kodi pamenepa ndimudikire? Agogo, ndithandizeni.
12
Phwitiko: Kutambasula za maphunziro Unduna wa zamaphunziro udalonjeza zotukula maphunziro mdziko muno. Poyesetsa kukwaniritsa izi, undunawu uli ndi mapologalamu osiyanasiyana. Mmiyezi yapitayi undunawu udakonza zokweza fizi kuti uzitolera ndalama zokwanira zotukulira maphunziro. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mneneri wa undunawu Rebecca Phwitiko: Phwitiko: Ndimalumikiza unduna ndi atolankhani Tafotokoza mbiri yako. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine Rebecca Phwitiko, ndidabadwira ndi kukulira mumzinda wa Blantyre koma ndimachokera mmudzi mwa Danda, T/A Kalumbu mboma la Lilongwe. Nanga mbiri ya maphunziro ako ndiyotani? Ndidaphunzira kusekondale ya Our Lady of Wisdom ku Blantyre mzaka za 1999 mpaka 2002 kenako nkukapanga maphunziro a ukachenjede ku Chancellor College. Panopa ndikuonjezera maphunzirowa kuti ndikhale ndi Masters Degree. Udindo wako weniweni ku Unduna wa zamaphunziro ndi wotani? Kwenikweni ntchito yanga ndi yokhudzana ndi zofalitsa nkhani za undunawu. Ntchito yokonza zokhudza uthenga wopita kwa anthu, kulumikiza unduna ndi nyumba zofalitsa ndi kusindikiza nkhani, kukonza zochitika za unduna ndi kusanthula zomwe olemba ndi kufalitsa nkhani alemba ndi kulandira madandaulo ochokera kunthambi zosiyanasiyana ndi zina mwa ntchito zanga. Usadalandire udindo umenewu unkagwira ntchito yanji? Ndinkagwira ntchito kuwayilesi ya boma ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC) ngati mkonzi wa mapologalamu, muulutsi ndi mtolankhani. Umagwiritsa bwanji ntchito nthawi yako yapadera? Ndikakhala ndi mpata ndimakonda kuwerenga mabuku okamba za Africa. Ndimakondanso kumvera nyimbo ndi kuyenda kuona malo osiyanasiyana. Unduna wa zamaphunziro umanena kuti cholinga chake choyamba nkutukula maphunziro. Kodi mukuchitaponji pofuna kukwaniritsa zimenezi? Choyamba unduna wa zamaphunziro uli ndi udindo waukulu kuphunzitsa mtundu wa Amalawi. Udindo umenewu timagwirira ophunzira, aphunzitsi, makolo ndi ofalitsa komanso kusindikiza nkhani. Pofuna kukwaniritsa izi, tili ndi mapologalamu ambiri koma kuti onsewa atheke, mpofunika mgwirizano waukulu pakati pa ife ndi magulu onse omwe ndatchulawa ndipo mzati wake nkulumikizana pafupipafupi komanso moyenerera.
3
Boma lisavomereze kuchotsa pathupi Potsatira zomwe ndinalemba sabata yatha, mmodzi wa awerengi watumiza maganizo ake motere: Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Rabecca, Ndine mmodzi mwa amene ndimatsatira zimene umalemba patsamba ili ndipo sindinagwirizane ndi maganizo omwe udalemba sabata yatha kuti ndi bwino malamulo a dziko lino alole amayi omwe akufuna kuti azitha kuchotsa pakati mzipatala. Ndikudziwa pali mavuto omwe akudza kaamba koti anthu akuchotsa pakati pogwiritsa ntchito njira zoopsa zomwe zikumavulaza kapena kupha amayi ndi atsikana, komabe yankho la mavutowa si kuvomereza kuti anthu azingotaya pakati mwachisawawa. Ine ndimakhulupirira kuti moyo ndi mphatso ya mtengo wapatali yomwe Namalenga amapereka kwa munthu. Malembo amanenetsa kuti tisanabadwe kapena kuti munthu asanapangidwe nkomwe mmimba mwa mayi wake, Mulungu amakhala atamudziwa kale. Kwa ine, izi zikusonyeza kuti pathupi paliponse pamapangidwa ndi Mulungu amene amapereka moyo, posaona kuti wotenga pathupiyo akadali pasukulu, wagwiririridwa kaya sadalowe mbanja. Ndiye ngati Mulungu walola kuti woterewa akhale woyembekezera ndiye kuti amakhala ndi cholinga ndi moyo wa mwana akuyembekezeredwayo, choncho ncholakwika kuti mayiyo aloledwe kuti azichotsa moyowo. Ngati chamukomera Mulungu kuti pakhale moyo, Mulunguyo amadziwa kuti mwana wobadwayo asamalidwa bwanji. Timaona anthu amisala akubereka ana nkumakula mmatauni ndi mmizindamu. Ngati munthu wamisala akutha kulera mwana, kuli bwanji anthu alungalunga? Mwina simunaonepo, koma ine ndikudziwa za ana ena omwe adabadwa makolo awo ali pasukulu kapena sadalowe mbanja, ndipo ndikamba pano anawa ndi anthu ofunikira omwe amapindulira dziko liko komanso kuthandiza makolo awo. Izi zomati anthu azichotsa mimbazi zimangoyangana mavuto alero osaunikira kutsogolo komanso cholinga cha Mulungu pokulola kuti ukhale ndi pathupi. Ndikudziwa kuti kutenga pathupi uli pasukulu kapena usanapeze banja zimaoneka ngati zolakwika, koma izi zisapangitse kuchotsa pathupi kukhala ngati ndi chithu cholungama. Ndine mayi Banda, Blantyre.
11
Achita phwando ndi kuimitsidwa kwa Kuluunda Lero kuli madyerero mmudzi mwa Senior Chief Bibi Kuluunda mboma la Salima kusangalalira kuti mfumuyi yaimitsidwa kugwira ntchito yake mbomali. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anthu a mmudzimu kuphatikizaponso mafumu ena akhala akubindikira kuofesi ya DC wa bomali pofuna kukakamiza boma kuti ichotse mfumuyi poiganizira kuti ndi yaziphuphu. Anthuwa adayamba mbindikirowo pa 11 April wapiyatu. Lachitatu lapitali mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adasayina kalata yoimitsa Kuluunda amene wakhala paufumuwu kwa zaka 20, kupereka chimwemwe kwa anthuwa. Mtsogoleri wa anthuwa, Muhammad Chingomanje, adati chimwemwe ndi chosayamba. Wayamba waimitsidwa ufumu: Kuluunda Lero [Lachinayi pa 5 May] lidzakhala tsiku lachimwemwe pamoyo wanga. Lero lidzakhala tsiku lapaderadera mmbiri ya dziko la Malawi, maka kwa ife anthu a ku Salima. Titagona panja pa ofesi ya DC kwa masiku 24, lero yankho labwera. Aliyense ndi wokondwa komanso wachimwemwe ndi zomwe zachitika lero, adatero Chingomanje. Kulankhula ndi Chingomanje pafoni kudali kovutirapo chifukwa cha nyimbo zomwe anthu amaimba komanso phokoso lachimwemwe lomwe limamveka. Nyakwawa Chilaboto ya mwa Gulupu Kawanga mdera la Kuluunda, idati iye komanso mafumu onse 31 amene amachita nawo mbindikirowo ndi okondwa ndi ganizo la Mutharika. Mtendere wadza mmudzi mwanga limodzi ndi anthu anga 1 800 amene ndimawalamulira. Takhala tikulira ndi mfumuyi kwa zaka koma maso athu adali kuboma kuti atiyankhe. Lero ndi chimwemwe paliponse, idatero mfumuyi uko akuimba nyimbo yachimwemwe. Mfumuyi idati lero kukhala phwando chifukwa yankho labwera. Tikupha ngombe komanso mbuzi, tikhala ndi tsiku lalikulu Lamulunguli chifukwa zomwe timapempha zayankhidwa. Aliyense abweretsa zakudya kusangalala kuti tsiku lomwe timaliyembekeza lakwana, adatero Chilaboto. Iye adati monga mfumu, nkhani ya kuimitsidwa kwa Kuluunda ithandiza ntchito yake chifukwa kwa nthawi ndakhala ndikulimbana ndi amfumuwa pankhani zoti nanunso simungazimvetsetse. Nthawi yoti tipume yakwana tsopano. Titaimbira foni Kuluunda kuti timve maganizo ake, adangoti: Ndili mminibasi ndiye sitingamvane. Mundiimbirenso. Titaimbanso mfumuyi sidayankhe foni. Malinga ndi nduna ya maboma aangono Kondwani Nankhumwa, Mutharika waganiza zoimitsa Kuluunda malinga ndi nkhani za katangale zomwe mfumuyi ikukhudzidwa nazo monga zoti idalandira K30 miliyoni ya Green Belt Initiative zoti igawire anthu okhudzidwa ndi polojekitiyi, koma sidalongosole komwe idapita K15 miliyoni.
8
Chipatala cha khansa chitheka September Odwala khansa ayembekezere kupuma umoyo wina. Chipatala chachikulu chothana ndi matendawa chitsegulidwa September chaka chino mumzinda wa Lilongwe. Nduna ya zaumoyo Atupele Muluzi yatsimikiza za nkhaniyi ndipo yati chifukwa cha ichi, boma lichepetsa kapena kusiyiratu kutumiza odwala ena kunja kukalandira thandizoli. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Peter Mutharika kukhazikitsa ntchito yomanga chipatala cha khansa Odwala khansa timawatumiza kunja kukalandira thandizo, kumangidwa kwa chipatalachi kwatonthoza ambiri chifukwa mmalo mopita kunja, azithandizidwa mdziko momwemuno, adatero Muluzi. Malinga ndi nthambi yowona zaumoyo padziko lonse ya World Health Organisation (WHO), matenda a khansa amapulula anthu pafupifupi 9 miliyoni pa chaka. WHO ikutinso anthu pafupifupi 8 mwa 10 alionse amene akupululuka ndi khansa ndi ochokera mmaiko osauka makamaka mu Africa momwe muli dziko la Malawi. Mdziko muno, khansa yomwe yafala ndi yokhudza chiberekero, pakhosi komanso mmagazi yomwe anthu akulephera kuphupha. Chifukwa chachikulu nkuchedwa kupita kuchipatala komanso maiko 30 mwa maiko 100 alionse osauka ali ndi zipatala zoyenera zothandiza khansa, adatero Leslie Mgalula woimilira WHO mdziko muno. Lachitatu msabatayi, Tamvani itayendera chipatalachi idapeza ntchito yokhoma malata ili mkati, kupereka chiyembekezo kwa Amalawi amene akhala akulira kwa zakazaka. Mmodzi mwa anthu amene adapulumuka ku khansa, Janet Bonwel wa mmudzi mwa Ndindi mboma la Salima, kumangidwa kwa chipatalako ndi chokoma kwa odwala matendawa. Ndidapezeka ndi khansa ya pamwendo mu 2001. Mzipatala amangondipatsa panado basi, ululu sumatha, adatero pamene adati adavutika ndi matendawa kwa zaka 6. Iye wati boma lionetsetse kuti chipatalachi chithandize aliyense osati kusala osauka. Mkulu wa bungwe loyanganira za anthu ovutika ndi khansa la Cancer Association of Malawi, Regina Njirima, wati khansa imafunika chipatala chakechake ngati momwe zakhaliramu. Izi zimachitika chifukwa anthu a vuto la khansa amafunika kuonedwa pafupipafupi, adatero. Njirima adati boma likuyenera kuchilimika kufalitsa uthenga momwe anthu angapezere thandizo kuchipatalachi ponena kuti aliyense akuyenera adziwe za thandizo lomwe chipatalachi chidzipereka.
6
Papa Wati Ufulu Wolankhula Zakukhosi ndi Ofunika Mtsogoleri wa Mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati ufulu woyankhula za kukhosi ndi ofunika pa moyo wa munthu. Papa Francisko walankhula izi lachisanu kulikulu la Mpingowu ku Vatican pamene amatsegulira likulu la bungwe lomwe limaona za maphunziro mmaiko lotchedwa Scholas Occurrentes. Polankhula pa mwambowo, Papa Francisko wati bungweli ndi lothandiza anthu maka achinyamata kutulutsa maganizo awo zomwe zingawathandize kuti akule muzochitika zao komanso kumanga tsogolo lawo. Patsikuli, Papa analandiridwa ndi achinyamata ochokera mmaiko osiyanasiyana monga Japan Argentina, United States of America, Mozambique, Haiti, Mexico, Spain komanso Italy. Pamwambowo panali akazi a atsogoleri a maiko asanu. Bungwe la Scholar Occurrentes ndi limodzi mwa mabungwe a utumiki wa a papa ndipo likupezeka mmaiko 190 pa dziko lonse lapansi.
14
Dziko la Tanzania Layamikira Amalawi Posunga Bata pa Nthawi Yosintha Ulamuliro Dziko la Tanzania layamikira dziko lino posunga bata komanso mtendere pa nthawi ya kusintha kwa ulamuliro wa dziko lino. Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko la Tanzania mayi Samia Suluhu Hassan wauza atolankhani lolemba ku Lilongwe pambuyo pa zokambirana ndi mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera kuti zomwe mzika za dziko lino zawonetsa mu nthawiyi ndi chitsimikizo chakuti ndi zotheka kulemekeza ufulu wa demokalase. Wayamikira dziko la Malawi-Suluhu Zokambiranazi zinachitika pambuyo pa mwambo opereka lupanga la utsogoleri komanso ukulu wa gulu la asilikali a nkhondo a dziko lino kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera, pomwenso mayi Hassan ndi nthumwi zina zochokera mayiko a kunja anali nawo. Apa mayi Hassan atsimikizira dziko lino kuti dziko lawo lipitiriza kuthandizana ndi dziko lino pa ntchito monga za malonda pofuna kukweza chuma cha maiko awiriwa. Polankhula atalandira lupanga la nkhondo, Chakwera walonjeza kuti awonetsetsa kuti wathetsa katangale, wacheptsa mphamvu za mtsogoleri wa dziko komanso kulimbikitsa umodzi pakati pa anthu. Chakwera wapempha mzika za dziko lino kuti zikhale zolimbika pa ntchito ponena kuti nthawi yofupa anthu osakhetsera thukuta yatha.
11
Mwangonde: Khansala wachinyamata Akamati achinyamata ndi atsogoleri a mawa, ambiri amaganiza kuti izi ndi nkhambakamwa chabe. Koma achinyamata ena, monga Lusubilo Mwangonde, akukwaniritsa akupherezetsa mawuwa osati pongolota kuti adzakhala, koma kutsogolera kumene chifukwa nthawi yawo yakwana. DAILES BANDA adacheza ndi Mwangonde, khansala wachinyama, yemwe akuimira Jumbo Ward mumzinda wa Mzuzu, motere: Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ali ndi masomphenya: Mwangonde Tikudziweni Ndine Lusubilo Mwangonde, ndili ndi zaka 27 zakubadwa. Ndinabadwa mbanja la ana asanu ndipo ndine wachinayi kubadwa. Ndimachokera mmudzi mwa Mwamalopa, kwa Paramount Chief Kyungu mboma la Karonga. Sindili pabanja pakadalipano. Mbiri ya maphunziro anu ndi yotani? Maphunziro anga a pulaimale ndidachitira kusukula yapulaiveti ya Viphya mumzinda wa Mzuzu ndipo asekondale ndidachitira pa Phwezi Boys mboma la Rumphi. Ndili ndi diploma ya Accounting ndipo pakadalipano ndikupanga digiri komanso Chartered Accounting kusukulu ya Malawi College of Accountancy (MCA). Mudayamba bwanji zandale? Kuyambira ndili wachichepere, zaka 12, ndakhala ndikukhala mumaudindo a utgogoleri. Ichi ndi china mwa zinthu zomwe zidandilimbikitsa kuti ndikhoza kudzapambana pazisankho. Koma chachikulu chomwe chidandichititsa kuti ndilowe ukhansala chidali chifukwa chakuti ndinkafuna kupereka mpata kwa anthu kuti azitha kuyankhula zakukhosi kwawo polimbikitsa demokalase ndi chitukuko. Ntchito mukugwira ndi zomwe munkayembekezera? Eya, ndiponso ndinkayembekezera zambiri. Masomphenya anu ndi otani pandale? Ine ndine munthu wokhulupirira Mulungu ndipo ndili ndi chikhulupiriro choti Iye ndi amene adzandionetsere zomwe ndikuyera kuchita ndi tsogolo langa. Zinthu zina zomwe mumachita ndi chiyani pambali pa ukhansala? Ndikakhala sindikugwira ntchito yaukhansala ndimakhala ndikuchita bizinesi, nthawi zina ndimakhala ndili kusukulu komwe ndikuchita maphuro anga a digiri. Kuonjezera pamenepo ndili ndi bungwe lomwe ndidayambitsa ndi anzanga ena la Centre for Participatory Democracy lomwe limalimbikitsa demokalase. Zomwe mwakwanitsa ndi zotani? Ndathandiza kuti ntchito yopala misewu ya kudera la Moyale itheke. Misewuyi yakhala nthawi yaitali osapalidwa. Ndidathandiziranso kuti ochita malonda ayambe kumanga mashopu anjerwa ndi kusiya kumangira matabwa kapena zigwagwa. Ndidakwanitsanso kukaimirira khonsolo ya Mzuzu ku Nyumba ya Malamulo. Ndaonanso kuti ntchitoyi yandithandiza kusintha momwe ndimaonera zinthu komanso ndimakumana ndi anthu osiyanasiyana omwe amandiphunzitsa zinthu zambiri.
11
Bungwe la CCJP mu Dayosizi ya Dedza Laphunzitsa Mwapadera anthu Ake Oyanganira Chisankho Dayosizi ya mpingo wa katolika ya Dedza yati iwonetsetsakuti chisankho chomwe chichitike mawa lino chiyende mokomera mfundo za democracy. Wapampando wa nthambi yoyanganira za chitukuko cha anthu mu dayosiziyo bambo Paul Kumkumbira ndi omwe anena izi pa maphunziro omwe bungwe la CCJP mu dayosiziyo limaphunzitsa anthu ake omwe aziyanganira nawo chisankhochi. Iwo ati awonetsetsa kuti chisankhochi chikhale chokomera mzika zonse za dziko lino, pofuna kupewa mavuto ena omwe angadze ngati chisankhochi sichiyenda bwino. Monga mukudziwa mmawa kuli chisankho, ife ngati dayosizi ya Dedza tinakonza msonkhano kuti tiphunzitse nthumwi zathu za bungwe limeneli la CCJP zimene zikutenga nawo mbali ngati oyanganira kuti awonetsetse kuti chisankhochi chayenda mokomera ulamuliro wa democracy, anatero bambo Kunkumbira. Iwo ati zina mwa mfundo zomwe amawaphunzitsa ndi kuona monga mmene mfundo zoyendetsera chisankho zayendera monga kusegulidwa kwa malo oponyera voti, komaso anthu amaulumali athandizidwa bwanji komanso mmene abungwe loyendetsera chisankho agwirira ntchito. Mmodzi mwa anthu omwe anachita nawo maphunzirowa a Aida Madinga ati aphunzira zambiri maka pa nkhani yowonetsetsa kuti pasakakhale chinyengo.
11
Koma malonjezo enawa! Kaya zidali zoona, kaya zabodza, zimamveka kuti nthawi imene Bakili Muluzi ankafuna mpando wa upulezidenti adalonjeza zinthu zingapo. Iye adalonjeza kuti aliyense adzakhala ndi nsapato. Onenawo nkumatinso Muluziyo adalonjeza kuti adzapereka fetereza wa ulele. Komatu atatenga mpando, Muluzi, Atcheya, adanenetsa kuti sadalonjeze nsapato. Nanga ndingadziwe kuti munthu wa ku Chitipa amavala sayizi yanji? adazizwa. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndipo pa nkhani ya feteleza, iye adati: Sindinati ndidzabweretsa fetereza wa ulele ayi. Ndidati fetereza wa uleya. Izitu ndakumbukira chifukwa cha zimene andale agundika kulonjeza pano. Zimandichititsa chidwi zimene andale amalankhula akafuna mpando. Ndikumbuka bwino lomwe Joyce Banda nthawi yomwe amafuna kuti amusankhe pachisankho cha 2014. Amati akafika ku Nkhata Bay, amanena kuti ine kwathu ndi kuno. Akafika ku Zomba, chimodzimodzi. Kulikonse kumene iye wafika amati ndi kwawo. Si kuti zayamba lero. Ngakhale Dr Hastings Kamuzu Banda ankanena kuti akufuna anthu ake azigona nyumba zosathonya kukamagwa mvula, azivala bwino komanso asamagone ndi njala. Mmawwu ake, iye amanena kuti dzikoli walifikitsa patali zedi, pomwe palibenso angalifikitse. Pofuna utsogoleri, andale amalonjeza zambiri. Mawu a Richard Nixon, mtsogoleri wa dziko la America pa 20 July 1969 amapherezera izi. Iye adati atsogoleri ambiri amalonjeza anthu kuti adzawapatsa mwezi, koma osawapatsa. Iye adati ndi iye yekha amene adapereka mwezi umene adalonjeza. Izi adanena Neil Armstrong komanso Edward Aldrin atakhala anthu oyamba padziko la pansi kuyenda ku mwezi. Izi zidadza chifukwa Nixon adaika ndalama zochuluka ku kafukufuku wa za mlengalenga. Komatu tonse tikudziwa bwino kuti Nixon adatula pansi udindo mu 1972 kaamba ka nkhani ya Watergate, inde komwe tidabera dzina la Cashgate. Tsono nchifukwa chiyani ndikunena zonsezi? Ndakhala ndikutsatira bwino zimene amalankhula Saulos Chilima pa misonkhano yokopa anthu kuti adzamuvotere. Kungobenthula chabe, poyamba adanena kuti chipani chake cha UTM chidzalipirira aliyense amene adzaimire chipanicho ukhansala komanso uphungu. Lonjezo ilo. Iye akutinso adzabweretsa sitima yothamanga zedi, yoyendera magetsi! Pamene njanji zathu zidamera mitengo, tizingodikira. Zimandipatsa chidwi kuti amalankhula zogwirizana ndi dera limene ali. Malonjezo amakhala ochuluka. Ku Nkhotakota adalokambapo zolimbikitsa ulimi wa chamba osati chosuta. Ku Mwanza adalonjeza kulimbikitsa ulimi wa zipatso mpaka mafakitale. Malonjezo awa, si bwino kudzatitsamwa. Izi zili apo, palinso atsogoleri ena amene amafuna kutionetsa kuti adabadwa nawo utsogoleri.
11
Boma Lipempha Anthu Asamalire Zitukuko Wolemba: Sylvester Kasitomu Boma lapempha anthu kuti azisamalira zitukuko zomwe zikumangidwa mmadera osiyanasiyana a mdziko muno. Nduna ya zofalitsa nkhani ndi kuphunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana a Mark Botoman ndi omwe anena izi pambuyo poyendera chipatala chomwe changomangidwa kumene cha Makina mdera a Zomba Chisi. Botomani yemwenso ndi phungu wa derali, wati kumangidwa kwachipatalachi kuthandiza kuchepetsa mtunda umene anthu a mderali amayenda akafuna thandizo la chipatala. Anthu ambiri mdera lino amayenda mtunda wautali kufuna thandizo lachipatakla ena amapita kuphalombe ena amathandizidwa pa chipatala cha mission konkuno koma kubwera kwa chipatala ichi kuchepetsa ena mwa maqvuto pankhani zaumoyo omwe anthu amakumana nawo mdera lino, anatero Botoman. ndipo Polankhulapo mkulu wa zaumoyo mboma la Zomba, Dr. Raphael Piringu wati anthu oposa 21 000 ndi omwe akuyembekezeka kupindulira ndi chipatalachi chikatsekuliridwa. Chipatalachi achimanga bwino ndipo ntchito yatsala pangono kutha panopa chatsala ndikumanga chipinda choti azimayi azichiriramo komanso kupanga register mukaundula wazipatala za mboma lino la Zomba, anatero Dr. Piringu. Chipatalachi ati achitsekulira posachedwapa ntchito yonse ikatha kaamba koti pali zina zomwe zatsala kuti zikonzedwe chipatalachi chisanayambe kugwira ntchito.
2
Bambo wa Mboma la Dowa Wapha Mwana Wake Apolisi mboma la Dowa akusunga bambo wina yemwe ndi Langani Malizani wa zaka 68 kamba komuganizira kuti wapha mwana wake wa zaka 27 pomubaya ndi mpeni aria-describedby="caption-attachment-11075" class="size-full wp-image-11075" src="https://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2020/04/Gladson-Mbumpha.jpg" alt="" width="194" height="259" />Watsimikiza za nkhaniyo-Mbumpha Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub-Inspector Gladson Mbumpha watsimikidza zankhaniyi. Iye wati malemuyu Brave Malizani, pa 19 April chaka chino adalezera ndipo atafika kunyumba adayamba kumenya bambo ake, koma pofuna kuziteteza bamboyo anatenga mpeni ndi kubaya mwanayo pachifuwa. Ife apolisi mboma la Dowa tamanga bamboyu yemwe wapha mwanawake kamba koti analedzera kodetsa nkhawa ndipo amavutitsa pa nyumbapo, anatero Mbumpha. Mbumpha wati bamboyo akuyembekzereka ku kawonekera kubwalo la milandu kuti akayankhe mulandu wakupha.
14
Kwaterera kwa ntenje Mwanunkha mmudzi mwa Ntenje kwa T/A Machinjiri mboma la Blantyre komwe osungitsa chitetezo mmidzi (community police) adatibulidwa nkumangiriridwa pamtengo kumanda komwekonso adawakumbitsa manda. Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Kuonjezera apo, apolisi omwe amati akasungitse bata kumeneko adabwerako akulikumba la mtondo wadooka, kuthawa anthu okwiya, malinga ndi Gulupu Ntenje wa deralo. Mmene timalemba nkhaniyi nkuti achitetezo a mmudzimu akubisala mtchire pamene ena akulandira chithandizo pachipatala cha Limbe. Akulephera kukhala chifukwa chovulazidwa mmatako: Story Ntenje, yemwe nkhaniyi idachitika mmudzi mwake, adati izi zidachitika pamene anthuwo amaganizira kuti achitetezowo adapha munthu. Gulupuyu akuti lidali Lachinayi pa 1 October pamene mmudzimo anthu ankathamangitsa mnyamata wina amene amamuganizira kuti waba thumba la chimanga kwa agogo ake. Anthu adamugwira ndipo adayamba kumumenya. Achitetezo cha mmudzi ndiwo adamulanditsa kuti asavulazidwe. Adakamutsekera muofesi ndipo adaimbira apolisi ya Bangwe kuti adzamutenge, adatero Ntenje. Iye adati pamene nthawi imakwana 4 koloko madzulo, apolisi adali asadafikebe. Adatiuza kuti alibe mafuta. Kenaka poti tikamuone munthuyo tidapeza kuti wamwalira, adatero Ntenje. Lamulungu pa 4 October, mwambo wa maliro udayamba, koma khamu la anthu ammudzimo akuti lidayamba kunena kuti a achitetezo a mmudzi ndiwo adapha malemuyo. Mmodzi mwa achitetezowo, Davie Story, adati anthuwo adafika kunyumba kwake namugwira cha mma 8 koloko mmawa. Adandigwira kuphatikizaponso anzanga ena awiri amene timagwira nawo ntchito ya chitetezo cha mmudzi. Adatitengera kwa wapampando wathu, koma tidakapeza atcheyawo atathawa. Ndiye adatenga mkazi wawo. Adatitengera kumanda komwe adatikumbitsa manda. Titamaliza adayamba kutikwapula nkutimangirira pamtengo, adatero Story. Ntenje adati panthawiyo, iye adaimbira apolisi kuti abwere. Apolisiwo akuti adalipo anayi ndipo atafika kumandako anthu okwiyawo adayamba kunola zikwanje kuti athane nawo. Zinthu zidavuta, ndipo adaitana apolisi ena. Atafika enawo, tidayesera kukamba ndi anthu okwiyawo kuti awamasule pamtengo achitetezowo, zomwe zidatheka, adatero Ntenje. Koma akutsitsira mmanda bokosi la maliro, mphekesera idamveka kuti anthuwo amafuna kuti achitetezowo awaponyere mdzenjemo nkuwakwiriria limodzi ndi chitandacho. Story, amene akukanika kukhala pansi chifukwa cha kuvulazidwa mmatako, adafotokoza malodzawo motere: Adati tonse anthu 5 tigone limodzi ndi malemuwo. Amati atiponyera mdzenjemo. Zitavuta, apolisi adayamba kutithawitsira komwe adaimika galimoto yawo. Ntenje adati apolisi adathira utsi wokhetsa misozi komabe sizidaphule kanthu ndipo adatha phazi kusiya mmudzimo muli chipwirikiti. Apa mpamene anthuwa adapita kukagwetsa ofesi ya achitetezowo komanso kukayatsa nyumba ya wapampando wawo kuphatikizapo nyumba ya Story. Wapampandoyo, Damiano Dindi, amene adalankhula pafoni ndi Msangulutso kuchokera ku Nsanje, komwe amati akubisala, adati palibe chomwe wapulumutsa mnyumba mwake. Akazi anga ali mmanja mwa apolisi komwe akutetezedwa; mwana wanga wapita kwa achibale; ineyo ndili mtchire pansi pa mtengo wa bulugama mboma la Nsanje. Sindikudziwanso kuti ndi mmudzi mwa ndani, adatero Dindi. Kolowera kwandisowa. Mutu wanga sukugwira chifukwa mnyumbamo mudali K280 000 ya bizinesi komaso katundu wanga yense wapita. Mneneri wa polisi ya Limbe, Pedzisai Zembeneko, adatsimikizira Msangulutso za nkhaniyi ndipo adati womwalirayo dzina lake adali Nyadani Dankeni. Koma Zembeneko adati kafukufuku pankhaniyi adali mkati ndipo adzalankhula zambiri akamaliza zofufuza zawo. Pakalipano palibe amene wamangidwa kaamba ka kumwalira mwadzidzidzi kwa Dankeni kapena, adatero mneneri wa polisiyu.
15
Ma MP olowa PP akonzekere nkhondo Mphunzitsi wa zandale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College (Chanco), komanso anthu ena ati chipani cholamula cha Peoples (PP) chikuyenera kusamala malamulo potolera anthu oti athandize chipanichi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kulankhulaku kwadza pomwe aphungu ena adauza nyuzipeplala ya The Nation Lachisanu sabata yatha kuti mtsogoleri wadziko lino Joyce Banda adawafunsa kui ayambe atuluka zipani zawo asadalowe chake cha PP. Aphunguwa adati Banda adanena izi kunyumba ya boma ya Mtunthama mumzinda wa Lilongwe pomwe iwo adapita kumuyamikira pokhala mtsogoleri wa dziko lino komanso kumutsimikizira kuti agwira naye ntchito limodzi. Apa katswiri wa zandaleyu, Blessings Chinsinga, wati nkuswa malamulo kuchoka chipani chomwe udayimira kuti ukhale phungu ndikukalowa chipani china koma popanda masankho. Izi Chinsinga wati nzoyenera kuti omwe adasankha phunguwo akhale ndi mwayi wosankhanso potsatira kusintha kwa phunguyo. Izi iye wati izi nzoikika mu Gawo 65 la Malamulo Oyendetsera dziko. Gawoli limati: Sipikala alamule kuti mpando ulibe munthu ngati membala amene pachisankho anali wachipani chandale choti chili ndi mpando mnyumbayo kupatula phungu yekhayo ndipo mwachifuniro chake wasiya kukhala membala wachipanicho ndikulowa mchipani china chomwe chili nthumwi mNyumba ya Malamulo. Gawoli limapitirizanso kutsindika kuti Sipikala akhoza kulamula kuti mpandowo ulibe munthu ngatinso phungu wochokayo alowa chipani chandale, kapena bungwe ngakhalenso mgwirizano womwe ntchito zake nzonkera kundale. Apa Chinsinga wati phungu yemwe akufuna kulowa chipani cha PP akonzekere kukachita masankho achibwereza chifukwa akufuna kusintha chipani chomwe adaimira. Koma wachiwiri kwa mneneri wa chipani cha PP, Ken Msonda, wati ganizo ngati limenelo silidatulukepo ku msonkhanowo. Iye wati phungu wofuna kuthandiza boma ali womasuka kutero ngakhale ali kuchipani chomwe chidamulowetsa ku Nyumba ya Malamulo. Iye adati chofunika nkudziwitsa chipani chakalecho komanso Sipikala wa Nyumba ya Malamulo za komwe akupita. Msonda adati pali mphekesera yaikulu kuti mamulumuzana a zipani zina akufuna kulowa PP pofuna kukasokoneza. Phungu wa chipani cha DPP kuchigawo cha kummawa kwa boma la Kasungu, Otria Jere adati wakumanapo ndi Banda kangapo koma za nkhaniyi sadauzidwe. Phunguyu yemwenso ndi wachiwiri wa nduna ya zamaphunziro, adati ngati zitakhala zoona ndiye kuti akuyenera akamve maganizo a anthu omwe adamusankha komanso mafumu kudera lake. Jere adati chomwe mbalizo zikamuuze iye adzamvera. Waluza wati naye ali wokonzeka kumvera ganizo la omwe adamusankha. Iye wati pali zinthu zambiri zomwe zimafunika kuti phungu agwire ntchito ndi boma. Tikati kugwira ntchito ndi boma zimatanthauza zambiri monga kudutsitsa mabilu mNyumba ya Malamulo; apa timatsutsa zoipira Amalawi komanso kuvomereza zomwe zingawathandize, adatero Waluza. Koma Msonda wati aphungu komanso nduna zili ndi phuma pomwe zikufuna kuchoka kuzipani zawo ndikulowa chipani cha PP. Iye adati mwa aphungu komanso nduna 10 alionse, 9 agogoda kale ku PP kufuna kulowa. Msonda wati koma PP siyidatenge aliyense pofuna kuyendetsa kaye mwambo wa maliro a mtsogoleri wakale wa dziko lino, malemu Bingu wa Mutharika. Sitingawatchule maina awo pofuna kuwapatsa ulemu, adatero Msonda. Iye adatinso chipani cha PP chichenjera ndi anthuwa chifukwa ngati dakwanitsa kuthawa Mutharika asadaikidwe mmanda nkosavuta kudzathawanso chipanichi pamavuto. Mlimi wa mmudzi mwa Kachepa kwa T/A Likoswe mboma la Chiradzulu, Limbani Kaombe, wati Banda asapupulume kutenga aphungu omwe ali ku zipani zina chifukwa anthu ali mbali yake. Kale amabungwe adathandiza boma la Mutharika kudutsitsa ndondomeko yachuma pomwe a zipani zotsutsa amakana chifukwa boma la Mutharika panthawiyo limachita zomwe anthu amafuna. Zomwe anthufe timafuna Banda wayamba kuchita monga kukonza ubale ndi maiko ena ndiye ngati ku Nyumba ya Malamulo zikavute ife tidzathandiza, adatero Kaombe. Angapo mwa aphungu a DPP adakana kulankhula pankhaniyi ndipo amadula lamya yawo. Wachiwiri muofesi ya pulezidenti ndi nduna yemwenso ndi phungu wachipani cha DPP mboma la Mwanza, Nicholas Dausi adati alibe chokamba chifukwa akukhuza maliro ndipo anadula lamya yake. Nduna ya zamaphunziro, George Chaponda idati tilankhule ndi mlembi wachipani cha DPP. Titaifunsa ndunayi za ganizo lake ngati phungu iyo inadula lamya yake. Nduna ya zamasewero ndi chitukuko cha achinyamata, Symon Vuwa Kaunda adati ali pamaliro ndiye sangathe kulankhula za ganizo lake. Chipani cha PP sichili mnyumba ya Malamulo ngakhale aphungu ena adalowa chipanichi atathamangitsidwa ndi ena kuchoka kuchipani cha DPP. Mnyumba ya malamulo, chipani cha MCP chili ndi aphungu 30, DPP ili ndi aphungu 140, UDF ili ndi aphungu 18, Mafunde ili ndi phungu mmodzi, Maravi phungu mmodzi, ndi Aford aphungu awiri pomwe ena ndi oima paokha. Kuchigawo chapakati ku Mzimba sikudachitikbe masankho achibwereza kutsatira kumwalira kwa phungu wa DPP, Dontoni Mkandawire.
11
Apolisi akuthetsa milandu ku Nthalire Apolisi ena ku Nthalire mboma la Chitipa akuweruza ndi kuthetsa milandu osaipititsa kubwalo la milandu. Izi zidadziwika sabata yapitayi pomwe bungwe la National Initiative for civic Education (Nice) lidachititsa msokhano mderalo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Aka si koyamba kuti nkhani zotere ziphulike papolisipo. Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) mbomalo, John Moyo, atalandira malipotiwo adaitanitsa mkulu wapolisiyo mwezi wa June chaka chatha. Tidawaitanitsa kumsonkhano umene onse okhudzidwa akadakhalako koma poyamba adati ndiwotangwanika. Tidakonza tsiku lina ndipo tidachita kukawatenga. Adavomera kuti zimalakwika ndipo adati izi zitha, adatero Moyo. Koma mkulu wa polisi ya Nthalire Ben Mwaliwa adati pamsonkhano watsopanowu iyeyo padalibepo. Ine ndikudziwa za msonkhano wa chaka chatha omwe lidakonza ndi bungwe la CCJP. Pamsonkhanowu tidalonjeza kuthetsa mchitidwewu. Mbuyomu madandaulo amenewo adalipo koma zoti pano kukumalandiridwa ndalama ndinamapo, adatero Mwaliwa. Atafunsidwa ngati akumatumiza milandu ku bwalo la milandu, iye adavomera kuti polisi ya Nthalire ikumatumiza milandu kubwalo la milanduyi. Malinga ndi ofisala wa bungweli mboma la Chitipa, Amos Ngoma, akomiti za chitukuko komanso anthu okhudzidwa adatambasula pamsonkhano wapadera sabata yatha kuti milandu ikumathera kupolisi komwe apolisiwa akumapatsidwa ndalama potengera ndi kukula kwa mlandu. Apa tidapempha oweruza milandu mderali kuti azipita kupolisi tsiku ndi tsiku kukatenga malipoti a anthu otsekeredwa mchitokosicho kuti aziunika omwe angapatsidwe belo pasanathe maola 48, adatero Ngoma. Kutulutsidwa kwa anthu asanatengeredwe kukhoti kwachititsa kuti bwalo la majisitileti ku Nthalire lisamalandire milandu zomwe zikupereka mafunso kwa ena mwa anthu ogwira ntchito pabwalopo chifukwa Nthalire ndi tauni yaikulundithu, imenenso ili mmalire a dziko lino ndi la Zambia ndipo kupalamula nkwakukulu. Malinga ndi ena mwa ogwira ntchito pabwalopo omwe sadafune kutchulidwa maina poopa kuchitidwa chipongwe, bwaloli limayembekezera kumazenga milandu itatu kapena inayi pa tsiku. Koma padakalipano palibe ngakhale mlandu ndi umodzi omwe ukutumizidwa kubwaloli. Tikakafufuza kupolisi timapeza kuti anthu ali mchitokosi ndithu; koma milanduyi ikumathera konko, adatero anthuwo. Pomwe CCJP adachititsa msonkhano mu June, mfumu Chipuwe idati mwana wake wamwamuna adauzidwa kuti apereke K60 000 kuti akatenge njinga yake yomwe idali mmanja mwa apolisi kaamba koti adachita nayo ngozi. Ndipo nawo a bwalo la milandu pa nthawiyo adanenetsa kuti iwo adadziwa kuti china chake si chili bwino kupolisi chifukwa samalandira milandu ngati momwe zilili pano. Mneneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto, Peter Kalaya, adati ngakhale ofesi ya polisi ya Chitipa ikumamvera za nkhaniyi mmisonkhano ndipo palibe wapitako kukawadandaulira za nkhaniyi. Pena pake tikudziwa kuti anthuwa amaopa chifukwa nkhani za katangale zimakhudza anthu awiri. Nawonso amaopa kuti ziwakhudza, adatero Kalaya.
7
Boma Lichenjeza Anthu Oba Zinthu za Mbiri ya Makedzana Wolemba: Thokozani Chapola aria.mw/wp-content/uploads/2019/09/archive.jpg" alt="" width="463" height="367" />Zina mwa zinthu zopezeka ku National Archives Boma lapempha anthu kuti aleke mchitidwe wakuba zinthu zomwe zimapezeka ku malo osungirako zinthu za mbiri ya makedzana (National Archives). Nduna yoona za masewero ndi chikhalidwe a Francis Phiso anena izi ku Zomba pamene anakayendera ma ofesi omwe amasunga mbiri ya makedzana mdziko muno (National Archives). Iwo ati malowa ndi ofunika kuwasamalira ndipo alonjeza kuti boma limanga malo atsopano ndi cholinga choti mbiriyi isamalike kaamba koti ma ofesi a nthambiyi padakalipano ndi aangono. A Phiso(pakati) kulankhula ndid a Lihoma (kumanja) Anthu ena amaba kapenanso kuwononga katundu wopezeka kuno mwina chifukwa kulibe chitetezo chokwanira. Ndiye timanga nyumba yabwino yotetezeka kuti zinthu zimenezi zisamalike, anatero aPhiso. Pamenepa a Phiso ati boma likulingalira zowonjezera mtengo wa ndalama yomwe anthu okawona zinthuzi amalipira kuchoka pa 2000-kwacha pa chaka kupita patsogolo. Polankhulapo mkulu wa National Archives mdziko muno Dr. Paul Lihoma ati ofesi yawo ikusungira mbiri ya dziko lino yolembedwa kuyambira mzaka za mma 1861. Tikusungirazinthu zochuluka kwambiri koma vuto ndi la kasungidwe chifukwa zambiri timazisunga mmapepala ngati mmene amakhalira ma nyuzipepala zomwe sizimachedwa kuwonongeka, anatero a Lihoma. Iwo apempha boma kuti lilingalire zomanga nyumba yabwino yosungirako zinthu za mbiri ya makedzana ndi cholinga choti zisamalilike.
7
Olowa mdziko mozemba aonjeza mavuto mndende Mavuto a mndende za mdziko muno ngosakamba koma kafukufuku wa Tamvani wasonyeza kuti ena mwa mavutowa akudza kaamba ka anthu osamangidwa koma ongosungidwa mndende chifukwa cholowa mdziko muno popanda chilolezo. Malingana ndi wachiwiri wa mneneri wa nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka mdziko muno, Wellington Chiponde, chiwerengero cha anthu oterewa chimasinthasintha kaamba koti yemwe wakonzeka amatuluka nkumanka kwawo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ena mwa olowa mdziko muno popanda chilolezo atawagwira ku Nkhata Bay Aliyense mwa anthuwa amadzionera yekha chochita kuti abwerere kwawo, chifukwa boma siliperekapo chilichonse kupatula kuwadyetsa ndi kuwasunga pamalo okhazikika, omwe nkundendeko, adatero Chiponde. Iye adati anthuwa sakhala kundendeko ngati akayidi koma ngati njira yowathandizira malo okhala ndi chakudya poyembekezera kuti azipita kwawo akakonzeka polingalira kuti dziko lino lilibe malo osungirako nzika za maiko ena zolowa mdziko muno popanda chilolezo. Chiponde adati malamulo amalola anthu oterewa kusungidwa mndende kwa sabata ziwiri zokha ndipo ikakwana nthawiyi amafunsidwa ngati apeza njira yopitira kwawo, koma ngati njirayo sidapezeke, amawapatsanso masiku ena kufikira pomwe adzakonzeke kubwerera kwawo. Si nkhanza, ayi, koma malamulo a dziko amatero kuti nzika ya dziko lina si yoyenera kukhala mdziko muno popanda chilolezo pazifukwa zingapo. Mudziwa kuti boma limayenera kupanga ndondomeko ya zinthu zambiri monga chitetezo, mankhwala, chakudya ndi zina. Kuti ndondomeko imeneyi iyende bwino, boma limayenera kudziwa chiwerengero cha anthu omwe ali mdziko nchifukwa chake othawa nkhondo kapena odzausa mwandondomeko amakhala ndi zowayenereza ndipo amakhala ndi malo awoawo, adatero Chiponde. Iye adati malamulo oterewa ali mdziko lililonse ndipo maiko ena ali ndi malo akeake osungirako anthu oterewa koma poti dziko lino likadalibe malowa, limasunga anthuwa mndende. Potsirapo ndemanga pankhaniyi, mneneri wa zandende mdziko muno, Smart Maliro, adati ichi nchipsinjo chachikulu kwa akuluakulu oyanganira za ndende polingalira kuti iwo amayenera kuti azidyetsa ndi kuyanganira anthuwa kufikira pomwe adzatuluke. Naye adati chiwerengero cha anthuwa chimasinthasintha kutengera ndi momwe akulowera komanso kutuluka koma zonse zimatengera kuti a nthambi yoona za anthu olowa nkutuluka anenanji. Ife timangolandira nkusunga anthuwa koma zonse amayendetsa ndi anthambi yoona za anthu olowa nkutuluka mdziko chifukwa sikuti anthuwa ndi omangidwa, ayi. Nkhawa yathu imangokhala pachisamaliro chifukwa zonse zimagwera ife. Mwachitsanzo timayenera kupeza malo oti akhalepo, chakudya komanso poti chiwerengero cha anthu mndende chimakwera, zinthu monga madzi ndi zina zimagwira ntchito kwambiri ndiye mabilu nawo amakwera, adatero Maliro. Nawo oyanganira za maufulu a anthu ati zomwe amaona anthu olowa mdziko mwachinyengowa nzopweteka komanso zowaphwanyira ufulu kaamba koti amasungidwa mmalo oyenera omangidwa. Mkulu wa bungwe la Centre for Human Right and Rehabilitation (CHRR), Timothy Mtambo, adati ndende za mdziko muno zili ndi mbiri zosakhala bwino, makamaka pankhani yothithikana, zaumoyo ndi kuvuta kwa chakudya. Mkuluyu adaona kuti kusunga anthuwa mmalo ngati amenewa nkuwalakwira kwambiri potengera malamulo a zaufulu wa anthu padziko lonse. Kumeneko nkulakwa chifukwa anthuwa sadamangidwe, ayi, akungoyenera kutumizidwa kwawo basi osati mpaka kumasungidwa mndende ngati kuti azengedwa mlandu nkumangidwa, adatero Mtambo. Iye adati njira yabwino nkumanga malo osungirako anthu oterewa poyembekeza kuti azinka kwawo monga momwe zilili mmaiko ena. Nduna ya zamdziko, Jappie Mhango, adati ganizo lomanga malo osungilako anthuwa ndi labwino, makamaka pankhani yachitetezo, koma adati pakalipano palibe mapulani otere polingalira mavuto a zachuma omwe ali mdziko muno. Ndi maganizo abwino kwambiri chifukwa anthuwa amachokera kosiyanasiyana ndiye sitinganeneretu kuti moyo wawo ndi wotani. Mwina ena adali zigawenga zikuluzikulu kwawo, akhoza kuphunzitsa anthu anthu omwe ali mndende, adatero Mhango. Iye adati mtsogolo muno zinthu zikadzayamba kuyenda bwino, boma lidzaganizirapo kuti mwina lidzamange malo osungirako anthuwa kuti azikakhala kwaokha.
11
Abambo aku Mthawira Alandira Maphunziro a Banki Mkhonde Kwa nthawi yoyamba chikhazikitsireni bungwe la umodzi wa Abambo lomwe ndi la Catholic Men organisation ku Mthawira Parish mu arkidayosizi ya Blantyre mchaka cha 2013, loweruka pa 30th November 2019, linakonza maphunziro akayendetsedwe, kusungisa, komanso kubwereketsa ndalama kuzera ku ma banki am`mudzi. Maphunziro amenewa anachitikira ku tchalitchi la Maria mfumukazi ya mtendere kwa Chikapa yomwe ndi mthambi ya parishi ya Mthawira. Maphunzirowa anasamira pa zolinga zikuluzikulu monga kufuna kupereka ukadaulo wa kayendetsedwe kabwino ka dongosolo losungitsa ndi kubwereketsa ndalama kudzera ku banki nkhonde komanso kukhazikitsa njira zabwino zopewera mavuto ena amene magulu oterewa akhala akukumana nawo monga kulandana katundu ngati wina walephera kubweza ndalama yomwe anabwereka. Ena mwa abambo aku Nthawira parish pambuyo pa maphunziro a banki mkhonde Mau ake, wapampando wa bungweli ku parish ya Mthawira a Martin Chiwaya anati ngakhale kuti cholinga chachikulu cha bungweli ndi kulimbikisa umoyo wa uzimu wa abambo mu mpingo wakalolika, ndikofunikanso kuwunikilanso moyo wawo wa thupi makamaka kumbali ya chuma pozindikira kuti munthu ndi thupi ndi mzimu pamodzi. Abambo akuyenela kukulanso moyo wawo wakuthupi makamaka pa chuma chifukwa iwo ndi amene amayenela kutsogolera mawanja awo pachuma, anatero a Chiwaya. Maphuzirowa omwe anali a tsiku limodzi anakwanisa kubweretsa pamodzi abambo ambiri a mparishiyi. Maphuzirowa ndi ofunika kwa abambo posayanganira njira yomwe amachita kuti apeze ndalama monga kugwira ntchito kapena kuchita bizinezi, anawonjedzera motero a Chiwaya. Pothilirapo ndemanga wachiwiri wa pampando wa tchalitchi la Chikapa a Lovewell Vikho anati maphuzirowa ndi ofunika kwambiri chifukwa athandiza abambowa kuti akwanitse udindo wawo wosamalira mabanja awo makamaka pachuma. Ndizofunika kwambiri kuti abambo azikhalira pamodzi ndikumakhalira limodzi kukambilana mfundo zabwino zoyendetsera ndi kuzipezera chuma, anatero a Vikho. Mwa zina maphunziro oterewa akhalenso akuchitika ku parish zina zopezeka mu arkdayosizi ya Blantyre ndi cholinga chofikira abambo ochuluka opezeka mu arkidayosiziyi.
2
Alendo alanda maudindo mu PP Kusankhidwa kwa alendo ochoka mzipani zina kukhala mmaudindo onona kuchipani cholamula cha Peoples (PP) kungakolezere mavuto kuchipaniko, maka pandawala yolowera kuchisankho cha 2014. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Katswiri wa ndale kusukulu ya Chancellor College, Blessings Chinsinga, mfumu ndi anthu atero msabatayi pounikira zotsatira za chisankho cha akuluakulu oyendetsa chipani cha PP. Chipanichi chidali ndi msonkhano waukulu kuyambira Lolemba mpaka Lachiwiri komwe amkhalakale angapo adagwa chagada, maudindo kupita kwa ena omwe sadathe mvula zingapo kumeneko. Koma wachiwiri kwa mneneri wachipanichi, yemwenso adasankhindwa paudindowu popanda opikisana naye, Ken Msonda, wati Amalawi asade nkhawa chifukwa kusankhidwa kwa andalewo kulimbitsa chipanichi. Ku chisankhocho, mpando wa mtsogoleri udapita kwa yemwe ndi Pulezidenti wa dziko lino, yemwenso ali mwini chipanichi, Joyce Banda, popanda opikisana naye. Wachiwiri wakenso, yemwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko, Khumbo Kachali adangodutsa popanda omugwedeza. Koma kukhetserana thukuta kudakula posankha wachiwiri kwa wachiwiri kwa pulezidenti kuchigawo cha pakati ndi kumwera. Kuchigawo cha pakati, Cassim Chilumpha, yemwe adasomphoka ku UDF mu Epulo kutangodziwika kuti amusankha kukhala nduna, adasankhidwa ndi mavoti 1,253. Iye adagwetsa Clement Stambuli yemwe adapeza 478, Uladi Mussa 277, Chaima Banda 35 ndi William Nkhono yemwe adapeza voti imodzi. Kuchigawo cha kumwera, Sidik Mia yemwenso adasomphoka kuchipani cha DPP ndiye adasankhidwa ndi mavoti 1,711, kugwetsa mkhalalakale Brown Mpinganjira yemwe adapata mavoti 276. Apa Chinsinga wati anthu asangosangalala ndikupambanako komanso adziwe kuti zotere zingayambitse mabala mchipanimo. Iye wati izi zingachitike chifukwa omwe agwa pamasankhowo ndiwo akhala ndi chipanichicho pomwe sichidali mboma. Chinsinga wati kaamba ka zimenezo, zingatheke olirawo kuyamba kaduka kwa anzawo omwe achita bwino pamasankhowo. Iye adatinso nkutheka kuti mwina masankhowo pena sadayende bwino, zomwe zingakwiitse ena omwe adagonja. Mwachitsanzo, Banda pamwambowo adayamikira Mia kuti ndiye adakonza dongosolo lonse kuti msonkhanowo utheke, zomwe Chinsinga adakaikira kuti zingathandizire pa kusankhidwa kwake. Izi nkutheka kuti nzimene zidamupambanitsa; zotere ena sangakondwere nazo. Mpungupungwe mchipani umayambika mmalo otere ndiye chipanichi chisamale, adaunikira Chinsinga. Koma Msonda adati akuluakulu omwe asankhidwe pamutu pa mkhalakale ndi akadaulonso pandale kotero sizingatheke kuti kukwera kwawo kudzetse chisokonezo. Iye adatinso anthuwo adasankhidwa ndi anthu, kusonyeza kuwakhulupirira kuti agwira bwino ntchito yolimbitsa chipani komanso kutukula dziko lino. Koma T/A Nthache ya mboma la Mwanza yati idadzidzimuka nkusankhidwa kwa andale ena omwe adabulika kuzipani zawo. Iyo idati boma la DPP lidazunza anthu mu ulamuliro wake kotero si bwino kutenganso anthu ochokera kumeneko. Ndidaganiza kuti kukhala anthu atsopano. Komabe ndifunire zabwino zonse Pulezidenti ndi achiwiri ake, adatero Nthache. Angell Banda wa mmudzi mwa Jali kwa T/A Mwambo mboma la Zomba wati akukhulupirira kuti kutenga mipando kwa alendo kugwetsa chipani cha PP. Iye wati Mpinganjira ndi mkhalakale kuchipaniko kotero kugwa kwake sangakondwe chifukwa iye wakhala mchipanimo pomwe chisali mboma. Apa zavuta, kutha kwachipani kumeneko, alendowa sibwezi atawalola kuti ayime nawo chifukwa ntchito zawo tikuzidziwa pomwe adali kuzipani zawo. Andale athu akungofuna ndalama osatinso kutitumikira, mapeto ake mudzapeza UDF kapena DPP yonse ili ku PP, awa ndi anthu omwe sitikuwafuna. Joyce Banda achenjere, adatero Angell. Pius Amidu wa mmudzi mwa Sosola kwa T/A Msamala mboma la Balaka wati akuganiza kuti alendowa amanga chipani chifukwa ntchito zawo kuchipani komwe adali zidali zabwino. Amanga chipani amenewo anthu asawaderere, adatero Amidu.
11
Khama ndiye yankho poweta ngombe zamkaka Kuchionetsero cha zaulimi cha National Agriculture Fair ku Trade Fair Grounds mumzinda wa Blantyre, Peacewell Edward Mlanga, wochokera kwa Senior Chief Somba mboma la Blantyre adachita mphumi ndi kupeza chikho atapambana alimi anzake onse omwe adabwera kuchionetserochi. Ulimi wake udapatsa chidwi ngakhale mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika yemwe adatsegulira chionetserochi. Kodi chinsinsi cha mlimiyu nchotani? Esmie Komwa adacheza naye motere: Chidakopa anthu paulimi wanu kuchionetserochi nchiyani? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Choyambirira ngombe yomwe ndidapita nayo kuchionetseroku imaoneka ya thanzi komanso ndi yoti imatulutsa mkaka wochuluka ndipo anthu adadzionera okha. Ngombe za Mlanga zakwana 16 tsopano Ngombe zanu zimatulutsa mkaka wochuluka bwanji? Imodzi imatulutsa mkaka wosachepera malita 35 pa tsiku. Chinsinsi chanu kuti muzipeza mkaka wochuluka chagona pati? Zakudya zokwanira komanso za kasakaniza ndi madzi wokwanira tsiku lililonse. Mumadyetsera zakudya zanji? Kuonjezera pa udzu omwe ndimadyetsera nthawi zonse, mzaka za mmbuyomu ndimadyetsera chakudya chogula cha ngombe chotchedwa dairy marsh koma nditaona kuti chakwera mtengo kwambiri, ndidasiya mmalo mwake ndidayamba kugula zotsalira popanga mowa ku kampani ya Carlsberg, zotchedwa spent green. Ndichotsikirapo mtengo kusiyana ndi chakudya cha kusitolo chifukwa pamwezi ndimagula cha K135 000 pomwe chogulacho kuti chikwane pamafunika ndalama yosachepera K200 000. Kuonjezera apa, ndimadyetseranso madeya a nandolo ndi a chimanga. Mutasiya kugwiritsa ntchito dairy marsh, mkaka sunatsike? Ayi ndithu udakali chimodzimodzi. Mumazipatsa chakudya chochuluka bwanji pa tsiku? Alangizi adatiuza kuti ngombe iliyonse tiziyipatsa chakudya chokwana makilogalamu 200 koma mukudziwanso kuti sizocheza kuti munthu ufike pamenepa kotero nthawi zambiri ndimabwerera pa makilogalamu 170 pa ngombe iliyonse. Nanga madzi amakhala wochuluka bwanji? Madzi ndiye sindinganene, ndimaonetsetsa kuti azikhalamo nthawi zonse. Adandilumikizira mapaipi a madzi ku makola kotero momwera muli mipopi yomwe ndimangotsegula ndikaona kuti atsika. Munayamba liti kuweta ngombe za mkaka? Ndidayamba mu 2000 ndi ngombe imodzi kenako mchaka chotsatiracho ndidagulanso ina basi kuchokera pamenepo zinadzichulukitsa zokha chifukwa nthawi zina zimaswa mapasa. Mmaweta ngombe za mtundu wanji? Zija zimadziwika ndi dzina loti Friesian. Pano zilipo zingati? Zilipo 16 koma zomwe tikukama 7. Bwenzi zitapotsera pamenepa chifukwa zina zimatha kuswa mapasa koma ndimapatitsakonso ena. Muli ndi za mphongonso? Ayi, kuti zitenge bere timaitana alangizi kuti adzadzipatsire umuna wa mtundu wa ngombezi kuti tisasakanize mtundu. Chidakupangitsani kuti muyambe ulimiwu nchiyani? Mayi anga adadwala ndipo kuchipatala adawauza kuti azimwa mkaka tsiku lililonse kotero ndidailowa ntchito yogula mkaka wa mmapaketi. Kenako ndidaganiza zongogula ngombe ya mkaka kuti ndizingokama nkumawapatsa ndipo tsiku lomwelo ndidayamba kukama. Ngombeyi imatulutsa mkaka wodzadza ndowa pa tsiku ndipo umandichulukira choncho wina ndinkangogawa kwa anthu ena a mmudzimu. Posakhalitsa mnzanga wina adanditsina khutu kuti anthu akupanga ndalama pogulitsa ku kampani ya Lilongwe Dairy yomwe imabwera ku Blantyre konkuno nkumagula kotero ndidayamba kuperekera kumeneko ndipo chaka chachiwiri ndidaonjezera ina. Phindu lomwe ndimapeza lidandipangitsa kuti ndilimbikire kwambiri mpomweno ndidakhazikika. Ndi phindu lanji lomwe mwakhala mukupeza kuchokera ku mkaka? Ndidagula malo ndikumangapo nyumba ziwiri zopangitsa lendi, ndagula malo ena wokwana nyumba zitatu zomwe malata ake ndagula kale komanso ndikuphunzitsa ana anga awiri ku poly. Ndidagawirakonso abale anga ena ngombezi omwenso akuthandizikira mu njira zosiyanasiyana mmakomo mwawo, kunena pakhomo panga ndiye sitisowa kanthu. Mumakagulitsa kuti mkaka wanu? Kuyambira Lamulungu mpaka Lachisanu ndimakagulitsa kwa amwenye mtauni pa mtengo wa K180 pa lita wotsalawo ndimakagulitsa ku bulking group pamtengo wa K160 pa lita ndipo Loweruka, ndimakagulitsa kwa mzungu wina wake ku Nyambadwe pa mtengo wa K400 pa lita.
4
Mbali ina ya mnzinda wa Blantyre Kunena zoona, mzinda wa Blantyre ukusintha. Kuona momwe mzindawu akuukongoletsera, ukhoza kuyamika. Maluwa akubzalidwa ponseponse, misewu ndi misika ikukhala yosesedwa ngakhale mwina ndi mwina zinyalala zikutsalira. Posachedwa, taonanso akunena kuti nyumba zonse zosaoneka bwino zigumulidwe. Ndipo kunena za ku Limbe, msewu wa Highway nawo ukupatsa chikoka. Koma ukafika kumalo okwerera basi zosiyanasiyana kufupi ndi msika wa Limbe, kumene ambiri amati kokwerera galimoto za kwa Manje, umakhala ngati wafikanso tauni ina, osati Blantyre. Zisakasa izi ndi malo odyera. Ofika kumene mtauni, amalonda, ogwira ntchito ena ngakhalenso ana asukulu akati akaone kadaunda madzi amalowa mmenemo. Kudya si kudya nanga?
15
Ku Machinga akonzekera ulimi wa fodya Alimi a mmakalabu 7 ati chaka chino akonzeka kulima fodya wochuluka ncholinga chosintha mabanja awo pachuma popeza iwo amakhulupirira kuti fodya ndi mbewu yomwe imabweretsa chuma chochuluka pakhomo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nkhaniyi idadziwika pamene Kampani ya Japanese Tobacco International (JTI) sabata yatha idapereka feteleza pangongole kwa alimi ochokera mdera la mfumu Ngokwe mboma la Machinga pamwambo womwe udachitikira pamsika wa Ngokwe ndipo alimiwo adatsindika kudzipereka paulimiwu chaka chino kuti Malawi asimbe lokoma ndi ndalama zakunja zomwe zimathandizira kuyendetsa ntchito za chitukuko mdziko. JTI idaganiza zochita machawi pofuna kuwagwira mkono alimiwo kuti akwaniritse masomphenya awo. Kampaniyo idakongoza alimiwo matumba a feteleza okulitsa a Super D Compound kwa onse omwe adapanga makalabu a zaulimi kuti iwo alime fodya wochuluka ndi kumusamala bwino. Mmodzi mwa alimiwo, Sitola Banda, adati JTI ikuthandiza alimi a mbomalo kukwaniritsa malingaliro awo kuti chaka chamawa boma lipeze fodya wochuluka. Talandira ngongole ya matumba a feteleza wokulitsa ndipo tikukhulupirira kuti tigwiritsa ntchito thandizoli moyenera. Makalabu omwe ndi aakuluakulu adakongozedwa feteleza matumba 200 pofuna kuti achilimike ndi ntchito za kuminda yawo. Si bwino mlimi kusiya ntchito za kumunda nkumapita uku ndi uku koyangana feteleza mnyengo yoti ulimi wafika kale pampondachimera, Banda adatero. Iye adati dera la Ngokwe makedzana lidali ndi minda ya fodya yochuluka ndipo alimi ankatumiza fodya wambiri kumisika ya fodya mdziko muno. Choncho iye adapempha alimiwo kuti adzipereke kotheratu kaamba koti nalonso boma limaika chidwi pafodya kuti chuma chiyende bwino. Tiyeni titukule dziko lathu potenga nawo mbali paulimiwu. Mlimi wochenjera adafesa kale fodya wake kunazare ndipo pakadalipano maso ali tcheru kuyembekeza kumwamba kuti mvula igwa liti, adaonjezera Banda. Mlimiyu, yemwe amachokera mkalabu ya Kondwerani mmudzi mwa Muwawa, T/A Ngokwe, adathokoza kampani ya JTI kaamba kowapatsa poyambira, zomwe zakhazikitsa pansi mitima ya alimi mderalo. Tikuthokoza JTI popereka ngongole yochuluka chotere, apatu sitijejemajejema mvula ikayamba kugwa. Talandira matumba a feteleza okulitsa motengera muyezo wa fodya yemwe tidasayinirana kudzagulitsa kukampaniyo ndipo tikuyembekezanso kulandira matumba ena a feteleza wobereketsa posachedwapa, adatero Banda. Tingopempha Chauta kutipatsa mvula yokwanira chaka chino kuti tikwaniritse khumbo lathu potukula mabanja ndi dziko lathu. Tikuyamikiranso kampaniyi popeza ikutilimbikitsa kubzala mitengo yambiri mmalo momwe tadulamo mitengo yogwiritsira ntchito paulimiwu kuti tichepetse kuononga chilengedwe kuderali, adaonjezera motero Banda. Palinso mabungwe ena monga Mardef, omwe akuthandiza alimi kuderalo powapatsa ngongole ya zipangizo za ulimi kuti asasowe pogwira pamene ntchito ya kumunda yayambika. makedzana lidali ndi minda ya fodya yochuluka ndipo alimi ankatumiza fodya wambiri kumisika ya fodya mdziko muno. Choncho iye adapempha alimiwo kuti adzipereke kotheratu kaamba koti nalonso boma limaika chidwi pafodya kuti chuma chiyende bwino .Tiyeni titukule dziko lathu potenga nawo mbali paulimiwu, adaonjezera Banda. Mlimiyu, yemwe amachokera mkalabu ya Kondwerani mmudzi mwa Muwawa, T/A Ngokwe, adathokoza kampani ya JTI kaamba kowapatsa poyambira, zomwe zakhazikitsa pansi mitima ya alimi mderalo. Tikuthokoza JTI popereka ngongole yochuluka chotere, apatu sitijejemajejema mvula ikayamba kugwa. Talandira matumba a feteleza okulitsa motengera muyezo wa fodya yemwe tidasayinirana kudzagulitsa kukampaniyo ndipo tikuyembekezanso kulandira matumba ena a feteleza wobereketsa posachedwapa, adatero Banda.
4
Apempha mafumu kuunika miyambo Boma komanso nthambi ya mgwirizano wamaiko wa European Union (EU) atsindika kufunika koti mafumu aunikenso miyambo ina yomwe ikadatsatidwa mzigawo zosiyanasiyana mdziko muno. Mfundo iyi ndiyo idatenga gawo lalikulu la msonkhano wa masiku awiri msabata yangothayi wa mafumu akuluakulu ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lukwa: Miyambo ina isinthe Cholinga cha msonkhanowo chidali chofuna kupereka mpata kwa mafumuwa kukambirana za malamulo omwe mafumu amatsata poyendetsa zinthu mmadera mwawo koma kudaoneka kuti milandu yambiri yomwe imafuna malamulowa imakhudzana ndi miyambo. Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa abambo, amayi, anyamata ndi asungwana Jean Kalirani adanena motsindika kuti amai ndi ana ambiri amachitiridwa nkhanza zikuluzikulu kaamba kofuna kukwaniritsa miyambo ina. Nzoona kuti mpaka pano tizikhala tikukamba za miyambo monga kulowakufa, kuchotsa fumbi, phwando la nkhandwe ndi fisi? Zonsezi zikuchitika mmadera momwe mafumu amakhala ndipo ali ndi mphamvu zosintha zinthu, adatero Kalirani. Iye adati Malawi ngati dziko limodzi lomwe lidalowa nawo mumgwirizano wa maiko, ali ndi udindo oonetsetsa kuti zomwe maikowo adagwirizana zikutsatidwa ndipo chimodzi mwa mapanganowo nkuonetsetsa kuti nkhanza kwa amai ndi ana zatha. Woimira bungwe la United Nations (UN) Ama Sande adati iye ndi nthumwi zina za kunthambi ya amayi mu mgwirizano maiko a dziko la pansiwu adagwidwa ndi chisoni atayendera madera ena nkupeza asungwana achichepere omwe adawafotokozera za momwe amakakamiziridwa kugonana ndi akuluakulu. Iye adati adakhudzidwa kwambiri akuluakulu ena omwe adacheza nawo atawayankha poyerayera kuti mwana ndi wa zaka 8 koma akafika zaka 12 ndiye kuti wakula. Chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti zambiri mwa nkhanza zomwe asungwana adafotokoza zimachitika kaamba ka miyambo yomwe imatsatidwa mmadera awo, adatero Sande. Senior Chief Lukwa ya ku Kasungu idati zomwe adanena akuluakuluwa nzoona ndipo adalonjeza kuti pamsonkhanowo mafumu akambirana za mfundo zokhwima zotetezera amayi ndi ana chifukwa chamiyambo. Iye adati kuti izi zitheke nkofunika kuganizira mafumu pankhani yamayendedwe komanso ndalama zogwirira ntchito yawo mosavuta chifukwa nthawi zambiri amalephera kufikira anthu omwe akuzunzika kaamba kosowa pogwira. Woyanganira zakayendetsedwe ka ntchito kuunduna wa maboma angonoangono Norman Mwambakulu adalimbikitsa mafumuwo kuti ali ndi mphamvu zopanga malamulo omwe Nyumba ya Malamulo ikhoza kungovomereza.
1
Zomba Diocese Yalimbikitsa Atumiki Ake Kupulumutsa Miyoyo Ya Akhristu Ku COVID-19 Episkopi wa dayosizi ya Zomba, Ambuye George Desmond Tambala, ati atumiki a mpingo ali ndi udindo waukulu wopulumutsa miyoyo ya anthu omwe akuwatumikira ku nthenda ya COVID-19. Tambala: Atumiki ali ndi udindo wothandiza anthu pa kapewedwe ka nthendayi Episkopi-yu wayankhula izi lachiwiri ku Thondwe Pastoral Centre pomwe anatsogolera gulu la ansembe, asisiteri, ndi abulazala amu dayosizi-yi pa maphunziro a tsiku limodzi omwe anakonzedwa ndi cholinga chofuna kumvetsa bwino nkhani zokhudza nthenda-yi. Ambuye Tambala ati anaona kuti ndi kofunika kuti atumiki alandire uthenga woyenera wokhudza nthendayi kuti nawonso athe kutsatira njira zoyenera zopewera matendawa komanso kuti akathe kuthandiza anthu omwe akuwatumikira mmadera awo. Ansembe, asisteri komanso abulazala amakhala pafupi ndi anthu nthawi zambiri. Choncho iwowa ali ndi udindo waukulu wowathandiza anthuwo pa kapewedwe ka nthendayi yomwe yabwera movuta kwambiri. Tinakonza maphunzirowa kuti iwo amvetse kaye bwino za nthendayi kenako akathandize anthu mmadera momwe akukhala, anatero Ambuye Tambala. Masiku apitawa Ambuye Tambala anapemphanso akhristu a mpingo wa katolika mdziko muno kuti asataye mtima koma apemphere zolimba kuti papezeke anthu amene akwanitse kupeza mankhwala ochizira nthendayi.
6
Aphungu aku nyumba ya Malamulo apitilira kupempha zitukuko ByRichard Makombe content/uploads/2019/07/parl3-300x168.jpg" alt="" width="712" height="399" /> Aphungu a nyumba ya malamulo ya Malawi Aphungu a kunyumba ya malamulo lachitatu sabata ino anapitilira kupempha zitukuko zosiyanasiyana zomwe akufuna kuti boma liwachitire ku madera awo. Ambiri mwa aphunguwa apempha boma kuti liganizire zomanga misewu, zipatala komanso sukulu pofuna kuthandiza kuti anthu adzipeza thandizo losiyanasiyana mosavuta. Mmodzi mwa aphungu yemwe akuyimira dela la Dowa Ngala a Arthur Sungitsa, apempha boma kupyolera ku unduna wa zaumoyo kuti limange chipatala ku derali, pofuna kuthandiza anthu kuti adzipeza thandizo la zaumoyo mosavuta. Ku dera komwe ndikuimira kwakhala kulibe chipatala cha boma kwa nthawi yaitali, zomwe zimaika pachiwopsezo miyoyo ya anthu ambiri anatero a Sungitsa. A Sungitsa ati anthu aku derali akuvutika kulipira ndalama zambiri kuchitala chomwe sichaboma choncho ali ndi chiyembekezo kuti boma limanga chipatala pofuna kuthetsa vutoli. Mavuto akula kwambiri chifukwa anthu ena amwalira kuchapatala cholipilitsacho eni ake amakaniza kumasula mtembo,zomwe zili zosakhala bwino,nchifukwa chake ndikuyesetsa kuchitapo kanthu kuti boma limange chipatalaanatero a Sungitsa. Poyankhulapo phungu wa dera la Mangochi Malombe Misolo Mussa Kapichira ati akufuna kuti boma likonze zipatala ku dera kwawo komwe padakali pano zinthu sizili bwino. Mmawu awo a Mussa adandaula ndi kusowa chidwi kwa nduna zina za boma, zomwe ati sizimamvetsera bwino zomwe aphunguwa amafotokoza zokhudza madera awo. A Kapichira, anapitilira kudandaula ndi khalidwe la nduna zina zomwe zimango-yenda-yenda pomwe aphungu amayankhula mnyumbayi, zomwe akuti zimapereka nkhawa pa zatsogolo la zomwe aphunguwa akupempha.
2
Kapito adzudzula kukweza mitengo Patangotha sabata bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) litakweza mitengo ya magetsi ndi mafuta agalimoto, madera ena maka kumidzi zinthu akuti zayamba kale kukwera mtengo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mmaderawa, monga ku Chikhwawa, mitengo yogayitsira komanso maulendo a galimoto akuti yakwera kwambiri. Kukwera mitengo kwa zinthuku kukutsutsana ndi zomwe bungwe la Mera, lomwe limayanganira za magetsi ndi mafuta, lidanena kuti kukwera kwa mafuta ndi magetsi sikuchititsa kuti zinthu zikwere mtengo. Bungweli lidakweza mitengo yogulira mafuta ndi magetsi Lachinayi sabata yathayi. Bungweli lidati kuyambira Lachisanu pa 9 Novembala, petulo azigulitsidwa pa K606.30 kuchoka pa K539.00 pa lita. Dizilo adati azigulitsidwa pa K509.90 kuchoka pa K434.30 pa lita. Lidatinso mtengo wogulira magetsi wakwera kuchoka pa K16.05 kilowatt hour kufika pa K22.78 kilowatt hour. Apa anthu ati boma litsitse mtengo wa mafuta ndi magetsi kapena lipeze njira zoti katundu yemwe wayamba kale kukwera mtengo atsike. Anthuwa omwe ena ndi abizinesi ati ngakhale akuchita bizinesi komabe malinga ndi kukwera mtengo kwa zinthu kukhala kovuta kuti azipeza phindu pa zomwe akuchita. Macleod Banda wa mmudzi mwa Maide kwa T/A Maseya mboma la Chikhwawa ndipo ndi mlimi wa mpendadzuwa akuti kumeneko zigayo ndi maulendo zakwera. Thini la malita 15 timagayitsa K120 koma pano lili pa K150. Izi ndi zigayo zoyendera magetsi. Tikafuna kulowa mtawuni kuno timakwera lole ndipo timalipira K900 koma mafuta atangokweramu akweza kufika pa K1 200 ena K1 300. Kuno anthu amalima mpunga ndipo amapita nawo ku Limbe, thumba la makilogalamu 50 amatilipitsa K300 koma pano tikulipira K500, adatero Banda, yemwe adatinso boma lichitepo kanthu. Abdul Sapala, yemwe amameta ku Mbayani mumzinda wa Blantyre wati iye pamwezi amapeza K11 000. Nyumba yomwe akumeteramo akuti amalipira K5 000, nyumba yomwe amakhalanso amalipira K6 000. Apa ndiye kuti ndalama yanga yatha komanso ndikuyenera kusamala banja. Enanso kumudzi akuyangana ine. Pobwera kuntchito ndimalipira K150. Ndalama yomwe ndimapeza siikuphula kanthu, adatero Sapala yemwe amatchajanso mafoni molipitsa. Chipinda chometerachi akuti akukweza mtengo chifukwa cha magetsi, nyumbanso akweza, komanso minibasi akweza zomwe zikuvuta kuti tsono titani? Ndalama yomwe ndimagwiritsira ntchito ndiyomwe ndimapeza ndikatchaja mafoni yomwe siimakwananso K5000 pamwezi, adawonjezera Sapala. Iye adati ngakhale atakweza mtengo wometera kuchoka pa K100 anthu sangabwerenso ndipo wati boma lichitepo kanthu. Amadu Kawonga yemwe amagulitsa makala kwa Chemusa mumzindawu wati kukwera mtengo kwa magetsi ndi mafuta agalimoto kukutanthauza mavuto kwa anthu. Kajumbo kakangono ka makala timagulitsa K40, koma ndikakweza mtengo anthu sangamagule. Phindu sindikulipeza chifukwa komwe timakapikula makalawa nakonso akweza mtengo. Ndalama zomwe ndikupeza pamwezi siimakwana K10 000 koma ndikuyenera ndisamale banja, kumudzinso akudikira ine, pamwezi ndilipire nyumba, madzi magetsi omwe akweranso mtengo. Boma lidakatsitsako mtengo wa magetsi ndi mafuta agalimoto kuti zinthu zikhale zotchipa kwa ife, adatero mkuluyu. Mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama), John Kapito wati ndi zomvetsa chisoni kuti zinthu zikumka ziyipirayipirabe. Iye wati izi zikuchitika chifukwa boma lataya anthu ake pomwe akumva ululu kaamba ka kukwera mtengo kwa zinthu. Kapito watinso anthu akuyenera adziwe ufulu wawo kuti atha kuchita ziwonetsero zosonyeza kukhumudwa ndi kusayenda bwino kwa zinthu. Tikhala tikufotokozera anthu kuti atha kuchita ziwonetsero zokhumudwa ndi kukwera mtengo kwa zinthu, adatero Kapito. Nduna yofalitsa nkhani, Moses Kunkuyu, wati nzoona kuti zinthu mmadera ena zaipa koma anthu asade nkhawa chifukwa chuma chikangoyamba kuyenda bwino mavuto onse atha. Pa miyezi 18 yomwe tidanena pali chiyembekezo kuti zinthu ziyamba kuyenda bwino, adatero Kunkuyu, yemwenso ndi mneneri wa boma.
10
Chipani cha DPP Chayimitsa Membala Wake Wamkulu Chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP), chayimitsa mmodzi mwa mamembala ake a Mike Chitenje ati kaamba kosowa mwambo. Wayimitsidwa Mchipani-Chitenje (wavala chipewa ndi malaya a mizere) Malinga ndi chikalata chomwe Radio Maria Malawi yawona, chomwe chasayinidwa ndi mlembi wamkulu wa chipanichi mayi Grezelder Jeffrey lachisanu pa 24 April, Chitenje yemwenso amadziwika ndi dzina loti Bangwe 1, waonetsa khalidwe loyipa lomwe litha kuwononga mbiri ya chipanichi pomwe iye amadzudzula monyoza mkulu wa chitetezo cha pulezidenti wa dziko lino a Norman Chisale. Chikalatachi, chachenjeza mkuluyu kuti asayankhe chikalatachi mu njira iliyonse ndipo komiti yosungitsa mwambo mchipanichi imuyitanitsa posachedwapa ndipo akanyalanyaza achotsedwa mchipani kuti akalowe chipani chilichonse chomwe akufuna. Posachedwapa Bangwe 1 amene ndi mmodzi mwa achinyamata a chipani cha DPP mchigawo cha kummwera, wakhala akudzudzula mkulu wa chitetezo cha pulezidenti Mutharika a Norman Chisale kudzera mmasamba a mchezo a intaneti, ponena kuti akutsekereza mamembala ena a DPP kupeza thandizo kuchokera kwa pulezidenti, zomwe sizinasangalatse chipanichi.
11
Mkulu Wa Zaumoyo Ku Dedza Wavulala Pa Ngozi Mkulu wa zaumoyo mboma la Dedza, Dr. Regina Chimenya wavulala atawombedwa ndi njinga yamoto mmbali mwa nsewu wochoka ku Lilongwe kupita ku Dedza mbomalo. Malingana ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sergeant Cassim Manda, ngoziyi yachitika dzulo pomwe mayiwa anayimika galimoto yawo mmbali mwa nsewu-wu pa msika wa Bembeke kuti agule ndiwo za masamba. Njingayi yomwe imathamanga kwambiri akuti inawawomba pomwe amaika masambawo kumbuyo kwa galimoto yawo. Dalaivala wa njingayi Alufeyo Chalusa akawonekera kwa bwalo la milandu kuti akayankhe mlandu wovulaza munthu kaamba koyendetsa njinga mosasamala.
14
Mayi Wakupha Mwana Wanjatidwa Apolisi mboma la Ntcheu amanga mayi wa zaka 24 zakubadwa kamba komuganizira kuti anataya mwana mchimbudzi atangochira kumene. Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub Inspector Hastings Chigalu mayi-yu ndi Tina Golozera ndipo anapalamula mlanduwu usiku wa pa 24 March 2020. Chigalu: Mchitidwe umenewu ukuchulukira Sub Inpector Chigalu anati mayiyu anatenga pathupi ndipo posakondwa ndi izi anaganiza zochotsa pathupo ponena kuti sanali okonzeka kulera mwanayu poti alinso ndi mwana wina wangono. Usiku wa patsikuli mayiyu anamwa makhwala oti achotse pathupipo ndipo anabadwitsa mwana wamoyo yemwe anakamuponya mu chimbudzi adakali ndi moyo. Mayiyu ataona kuti anthu ammudzimu amudzindikira kuti wabadwitsa mwana anathawa mmudzimo ndipo pa 28 mwezi uno anakazipereka yekha ku polisi komwe anamutsekera kuti ayankhe mlandu wakupha mwana wake zomwe zikutsutsana ndi gawo 210 loyendetsera malamulo a dziko lino. Mayiyu Tina Golozera amachokera mdera la mfumu yaikulu Njolomole, mboma lomweli la Ntcheu.
7
GIZ Yapereka Wailesi 400 ku Boma la Mangochi Bungwe la GIZ lapereka thandizo la wailesi zoyendera mphamvu ya dzuwa mboma la Mangochi ndi cholinga choti zithandizire kupereka mauthenga a kapewedwe ka mliri wa Coronavirus. Chimphepo: Thandizoli ndi lofunika kwambiri Polankhula pa mwambo wolandira katunduyi bwanamkubwa wa boma la Mangochi mbusa Moses Chimphepo wayamikira bungweli kamba ka thandizolo. Thandizo limeneli ndi lofunika kwambiri chifukwa monga mukudziwira padakalipano pakufunika kufalitsa mauthenga a nthenda imeneyi ya COVID-19 za mmene anthu angapewere ndi zina. Choncho wailesi zimenezi zitithandiza pa ntchito yofalitsa mauthenga kuti aziwafikira anthu akumudzi mboma lathu lino la Mangochi, anatero a Chimphepo. Polankhulanso mkulu wa bungweli mdziko muno Allan Wosku anati bungweli lili mkati mothandiza dziko la Malawi ndi zipangizo zothandizira pa kapewedwe ka nthendayi mdziko muno. Thandizoli lomwe ndi la wailesi zoposa 400 ndi la ndalama zokwanira 11 Million Kwacha.
14
Chakwera chenjeraAPM Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika Lachinayi adachenjeza mtsogoleri wa chipani cha MCP Lazarus Chakwera ponena kuti akukolezera zipolowe za ndale. Koma Chakwera, polankhula ndi mtolankhani wathu Mutharika atangotha kulankhulako, adati Mutharika ayenera kutulutsa umboni pa zoti akudzetsa mpungwepungwe. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Polankhula ku mtundu wa Amalawi potsatira mpungwepungwe umene wabuka pamene otsatira MCP akhala akuchita zionetsero mmizinda ya Lilongwe ndi Blantyre komanso maboma Kasungu, Dowa ndi Nkhotakota, Mutharika adati Chakwera achenjere chifukwa kulekerera otsatira MCP kuchita zionetsero kukhonza kuchititsa kuti mwazi ukhetsedwe. Zomwe ndinene pano zikhoza kumanga kapena kuphwasula mtundu, Mutharika adayamba motero. Ndamvetsedwa kuti Chakwera sakufuna kutsatira za chisankho komanso mfundo za demokalase pobweretsa chisawawa. Akufuna Amalawi atenge boma kupyolera muziwawa. Izi sizitheka. Mawu a Mutharika adadza tsiku limene apolisi adaponya utsi wokhetsa misonzi ku maofesi a MCP pomwe Chakwera amakambirana ndi Kazembe wa dziko la America Virginia Palmer amene akumaliza ntchito yake mdziko lino ndipo wakhala akukumana ndi atsogoleri osiyanasiyana. Izi zidachitikanso pomwe apolisi adamanga otsatira MCP 19, kuphatikizapo phungu wachipanicho mumzinda wa Lilongwe Alfred Jiya. Mutharika adadzudzula Chakwera ponena kuti akuchita izi pomwe adakatulanso nkhani yotsutsana ndi chisankho kubwalo la milandu. Padakalipano, khoti lapadera lakhazikitsidwa pomwe oweruza milandu asanu akuyembekezeka kugamula ngati zotsatira za chisankho cha pa 21 May zingavomerezedwe kapena ayi. Mmawu ake, Chakwera adati ayankhapo pa nkhaniyi bwinobwino, koma pakufunika umboni kuti akusokoneza ndiye. Abwere ndi umboni. Sindinena zambiri pano mpaka nditakonzeka, adatero iye. Chisokonezo chidayamba pomwe bungwe la MEC lidalengeza kuti Mutharika ndiye adapambana chisankhocho, motsatana ndi Chakwera kenako mtsogoleri wa UTM Party Saulos Chilima. Msabatayi, otsatira MCP adachita zionetsero makamaka ku Lilongwe komwe mwa zina adathamangitsa ogwira ntchito mboma kulikulu la boma ku Capital Hill mumzindawo. Iwo adachita izi ngakhale bwalo la milandu lidaluzanitsa milandu ya MCP ndi UTM Party ponena kuti ndi yofanana. Aneneri a zipani ziwirizo, Maurice Munthali ndi Joseph Chidanti-Malunga adati ndi wokonzeka kuyendetsa limodzi milanduyo. Katswiri pa za malamulo Edge Kanyongolo adagwirizana ndi zipani ziwirizo pokamangala kukhoti chifukwa malamulo amalola zipani kutero ngati sakukhutira ndi momwe chisankho chayendera. Iye adatinso otsatira MCP ali ndi ufulu wochita zionetsero ngati akutsatira ndondomeko. Pali nkhani zina zomwe oweruza akaziona kuti nzofunika bwalo lapadera, amazitumiza kwa mkulu wa makhoti yemwe amaziunikanso payekha ndipo akakhutira, amakhazikitsa khoti la oweruza osachepera atatu omwe amaweruza nkhaniyo, watero Kanyongolo. Wachiwiri woyanganira za kampeni mu MCP George Zulu yemwenso ndi phungu wa chipanicho kumwera cha kummawa kwa mzinda wa Lilongwe adati gululo lidzachoka ku Capital Hill Mutharika akadzatula pansi udindo. Akhoti ali ndi njira zawo zomwe amatsata pankhani zoterezi, alekeni azigwira ntchito yawo. Nafenso kuno tikutsata njira yathu ndipo tizibwera kuno tsiku lililonse la ntchito kuti kusapezeke munthu ogwira ntchito mmaofesi a boma, adatero Zulu. Kanyongolo adatsimikiza kuti nkhani yomwe ili mukhoti ndi zomwe akuchita otsatira chipani cha MCP ndi anzawo sizikukhudzana. Ndi nkhani ziwiri zosiyana, a khoti azipitiriza kuyendetsa nkhani yomwe ili mmanja mwawo. Awanso ndi ufulu wawo potengera malamulo kupanga chionetsero motsatira ndondomeko, adatero Kanyongolo. Koma mkulu woyanganira zofalitsa nkhani ku unduna wa zofalitsa nkhani Gedion Munthali adati ufulu onena zakukhosi sukukhudzana ndi kutseketsa maofesi a boma chifukwa izi zikutanthauza kuimitsa boma, kusokoneza anthu osalakwa ndi kuononga katundu wa boma. Kuimitsa ntchito za boma, kuzunza anthu osalakwa, kugenda galimoto ndi kuphwanya katundu wa mmaofesi sizikukhudzana ndi kunena za kukhosi. Uwu ndi uchigandanga, adatero Munthali. Padakalipano landuwo uweruzidwa ndi Healey Potani, Michael Tembo, Ivy Kamanga, Dingiswayo Madise komanso Redson Kapindu. Aliyense akhala ndi chigamulo chake koma onse adzabwera pamodzi ndi kukhala ndi chigamulo chimodzi.
11
Akufuna boma likweze malipiro Bungwe loona za ufulu wa anthu ogwira ntchito la Malawi Congress of Trade Union (MCTU) lapempha boma kuti likweze mlingo wa ndalama zotsikitsitsa zomwe munthu angalandire, komanso kuti anthu amene amalandira ndalama zochepera K50 000 pamwezi asamakhome msonkho. Polankhula pamwambo wokumbukira tsiku la ogwira ntchito Lolemba ku Lilongwe, mkulu wa bungwelo Luther Mambala adapempha boma kuti lionjezere ndalama za ogwira ntchito zotsikitsitsa zichoke pa K25 000 kufika pa K45 000. Ndipo adati okhoma msonkho azikhala olandira K50 000 kupita mtsogolo osati K25 000 monga zilili pano. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mambala: Zinthu zakwera Mambala adati akufunitsitsa boma litengere nkhaniyi ku Nyumba ya Malamulo kuti aphungu akaikaimbirane. Nyumba ya Malamulo imayembekezeka kutsegulidwa dzulo ndipo aphungu akambirana ndondomeko ya chuma. Chiyembekezo chathu nchoti nkhaniyi ifike kwa aphungu amene angatithandize, adatero Mambala. Bungweli lidapemphanso boma kuti lipeze njira zothetsera kuzimazima kwa magetsi zomwe ati zakhudza makampani kuti azipeza phindu lokwanira zomwe zikupangitsa kuti ena awachotse ntchito. Mneneri wa boma Nicholas Dausi adalangiza bungwelo kuti lipereke madandaulo awo ku unduna wa zachuma omwe ungatengere nkhaniyi ku Nyumba ya Malamulo. Sindinganene zomwe boma lichite koma kungowalangiza kuti nkhaniyi aitengere ku unduna wa zachuma womwe ungatsatize bwino nkhaniyi, adatero Dausi.
2
Amayi adandaulira boma ndi za HIV, Edzi Bungwe la mgwirizano wa achipembedzo, zipani zandale komanso mabungwe omwe siaboma la Public Affairs Committee (PAC), layamba kuunikanso momwe Gawo 65 la malamulo oyendetsera dziko lino lingagwirire ntchito. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Msonkhanowu womwe udayamba Lachiwiri mpaka Lachitatu msabatayi udachitikira ku hotelo ya Sunbird Mount Soche mumzinda wa Blantyre. Malinga ndi Bishop Montfort Stima yemwe adatsegulira msonkhanowo adati cholinga cha msonkhanowo ndi kupeza momwe lamuloli lingagwirira ntchito muulamuliro wa demokalase. Gawoli limapereka mphamvu kwa sipikala wa Nyumba ya Malamulo kuchotsa phungu yemwe walowa chipani china ndipo kudera lake kumayenera kuchitikenso chisankho. Gawoli lakhala vuto mdziko muno pomwe aphungu akhala akulowa zipani zina koma osachotsedwa uphungu. Zotere zikachitika ndipo mbali ina ikapempha sipikala kuti achotse phunguyo, ena akhala akukatenga chiletso kubwalo lamilandu kuletsa sipukalayo kuti asamuchotse pampando. Pomwe mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bingu wa Mutharika adatuluka mchipani cha UDF ndikukayambitsa DPP mu 2005, aphungu ambiri adachoka ku UDF ndipo nkhani ya gawoli ndiyo idatenga malo koma palibe phungu yemwe adakhudziwa. Atamwalira Mutharika, aphungu ambiri adachoka ku DPP ndikukalowa chipani cha mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda cha PP. Apa malinga ndi Stima, nchifukwa pali msonkhanowu kuti akambirane ndikupeza yankho pa gawoli.
6
Kusakaza kudaimitsa zinthu Kalinde: Kusokonekerako kudadzetsa umphawi Bungwe loyanganira zaufulu wa anthu la Malawi Human Rights Commission (MHRC) lati kusokonekera kwa kayendetsedwe ka chuma cha boma kudapangitsa kuti chitetezo chilowe pansi mdziko muno. Mkulu wa bungweli, Sophie Kalinde, wati kusokonekeraku kudadzetsa umphawi kwa anthu ambiri zomwe zidapangitsa kuti mchitidwe wa umbava ndi umbanda ukule ndipo apolisi ntchito iwachulukire. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iye wati chifukwa chotaya chikhulupiliro mwa apolisi anthu adayamba kulanga okha akagwira munthu oganiziridwa mlandu komanso kugenda ndi kuphwanya maofesi a polisi. Anthu amaukirira ndi kumaphwanya maofesi apolisi mpakana awiri adaferapo. Ndiponso chiwerengero cha anthu omwe adaphedwa poganiziridwa kuti ndi akuba kusonyeza kuti anthu samakhulupirira polisi, adatero Kalinde. Iye adati zonsezi zidayamba chifukwa anthu amasowa pogwira chifukwa ndalama zimasowa zitabedwa ndi anthu ogwira ntchito mboma. Magulu osiyanasiyana ati kuperewera kwa chitetezoku kudapangitsa kuti ntchito zina ndi zina za chitukuko zibwerere mmbuyo. Zina mwa ntchito zomwe akuti zidasokonekera ndi zamalonda zomwe akuti eni malonda amamangika akafuna kutsegula makampani ndi mafakitale opanga katundu osiyanasiyana poopa kuberedwa ndi kuvulazidwa. Oimira a malonda ochokera ku China, Peng Zhou Bing, wati mu 2013 mtunduwu udamenyedwa ndi kulandidwa ndalama ndi katundu wankhaninkhani zomwe adakonzekera kutsegulira ndi kutukulira makampani awo koma adalephera kutero. Pali anzathu ambiri omwe amafuna kubwela kudzakhazikitsa ntchito za malonda zosiyanasiyana koma amagwa ulesi akamamva momwe zinthu zilili kuno pa chitetezo, adatero Bing. Bing wati imodzi mwa ntchito zamalonda zomwe zidasokonekera chifukwa cha umbava ndi umbandawu ndi yomanga fakitale yopanga mapepala ku Lilongwe yomwe mwini wake ndi a Zhao. Iye wati fakitaleyi imayenera kukhala ndi makina atatu opangira mapepala koma achiwembu adaba mabokosi omwe mudali zitsulo za makina awiri ndipo pano makina amodzi okha ndiwo akugwira ntchito. Anthu ena saganiza bwino chifukwa makina enawo akadakhala kuti akugwiranso ntchito bwenzi kampaniyi italemba ntchito anthu ambiri omwe akungokhala. Mchaka chimenechi, katundu ndi ndalama zathu zankhaninkhani zabedwa komanso anzathu ena adakhapidwa, adatero Bing. Mmodzi mwa ochita malonda a zovala za kaunjika mumsika wa Lilongwe John Melekiyasi wati ngakhale apolisi adayesetsa kukhwimitsa chitetezo, nkhanza zidalipo makamaka akanyulana ndi mavenda. Iye wati nthawi zambiri apolisi amakhala ndi chithunzithunzi cholakwika cha mavenda ndiye kulakwitsa kulikonse amakutenga ngati mlandu wawukulu pomwe pali zoyipa zambiri zomwe akungowonerera. Sikuti amalakwitsa kuchepetsa chipwirikiti mtauni koma khani imavuta ndi nkhanza chifukwa nkhani ingonongono umapeza kuti ayamba kumenya kapena kuphulitsa utsi okhetsa misozi komwe kuli kulakwira anthu chabe, adatero Melekiyasi. Apolisi ati chitetezo chidayenda bwino mdziko muno mchaka cha 2013 koma anthu amangokhala ndi mantha chifukwa cha mbiri yakale ya polisi ndi ziwembu zina ndi zina zomwe zimamveka. Mkulu oyendetsa ntchito za kafukufuku ndikuonetsetsa kuti ntchito za polisi zikuyenda bwino, George Kayinga, wati chitetezo chidakwera mmizinda ya mdziko muno chifukwa cha mgwirizano omwe udalipo pakati pa anthu ndi apolisi. Chitetezo chidayenda bwino kwambiri mchaka chimenechi chifukwa tikayerekeza ndi mmene zidalili mmbuyomu tikuona kusitha kwakukulu koma kuti anthu adakali ndi mantha mmaganizo awo koma akhulupilire kuti chitetezo chili bwino ndipo chipitilira kuyenda bwino, watelo Kayinga. Iye wati maso a anthu ali pakagwiridwe ntchito ka polisi ndiye pakakhala vuto lalingono anthu amangowona ngati polisi ikulephela pomwe ikuchita bwino mu zinthu zambiri.
2
DODMA Yakhazikitsa Ndondomeko Zatsopano ku Dedza Ofesi yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi mboma la Dedza yati ichilimika pa ntchito yokhazikitsa ndondomeko zofuna kuchepetsa ngozi za mtunduwu mbomalo. Kusintha kwa nyengo kukubweretsa mavuto ngati awa Mmodzi mwa akuluakulu ku ofesiyi a Blessings Kamtema anena izi pa maphunziro a atolankhani a mboma la Dedza, pomwenso amafotokozera za ndondomeko ya momwe ofesi yawo imagwilira ntchito pa nthawi ya ngozi zogwa mwadzidzidzi. Mwazina iwo ati pakufunika mgwirizano wabwino pakati pa ofesi yawo ndi atolonkhani pofuna kupewa kulemba nkhani zosokoneza anthu pamene kwachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi. Ndi bwino kuti tichite zitukuko zimene zingachepetse mavuto omwe amabwera Kamba ka mavuto ogwa mwa dzidzidzi komanso tiyike njira zina zomwe zingateteze kuti ngozi zimenezi zisachitike, anatero a Kamtema. Polankhulapo mmodzi mwa atolankhani omwe anatenga nawo gawo pa maphunzirowa George mponda wati maphunzirowa amuthandiza kudziwa momwe angalembere nkhani zokhudza ngozi zogwa mwadzidzidzi.
18
Moi Walowa Mmanda Mwambo woyika mmanda thupi la mtsogoleri wakale wa dziko la Kenya Daniel Arap Moi wachitika pa bwalo la sukulu ya ukachenjede ya Kabarak mdera la Nakuru mdzikolo. Walamulira dziko la Kenya kwa zaka 27-Moi Malipoti a wailesi ya BBC ati president wa dzikolo Uhuru Kenyatta komanso wachiwiri wake William Ruto anali nawo pa mwambowo omwe unatsogoleredwa ndi mpingo wa African Inland (AIC) komwe mtsogoleriyu amkapemphera pamene adali moyo. Moi anababwa pa 2 September mchaka cha 1924 ndipo wamwalira pa 4 February 2020. Iye anakhalapo wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikolo kuyambira mchaka cha 1967 mpaka 1978 ndipo anadzakhala president kutsatira imfa ya yemwe anali mtsogoleri wa dzikolo Jomo Kenyata mchaka cha 1978. Moi yemwe wamwalira sabata yatha ali ndi zaka 95, ndi mtsogoleri wachiwiri wa dziko la Kenya komanso mtsogoleri amene walamulira kwambiri dziko la Kenya kuyambira mchaka cha 1978 mpaka 2002. Pamene Anthu ena akuti adzamkumbukira Moyi ngati tate weniweni wokonda dziko lake, ena akuti ulamuliro wake unali opondereza, wa tsankho komanso katangale.
14
Chilima Alangiza Ogwira Ntchito Mboma Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulos Chilima yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM wati anthu ogwira ntchito mboma ayenera kumagwira ntchito zawo mokomera anthu osati kukwanilitsa zofuna zawo zokha. Wadzudzula ogwira ku MEC, MBC-Chilima Dr. Chilima amalankhula izi pa msonkhano wa atolankhani womwe anachititsa lachitatu ku likulu la chipanichi mu mzinda wa Lilongwe kutsatira chigamulo cha bwalo la milandu kuti chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chichitikenso ponena kuti chinali ndi zolakwika zambiri. Iye wati izi zili chomwechi kamba koti bungwe la MEC lidachita zinthu mofuna kukondweletsa anthu owerengeka osati nzika zochuluka za dziko lino choncho onse ogwira ntchito mboma ayenera kutengerapo phunziro. Pamenepa Dr. Chilima wati wapampando wa bungwe la MEC, Dr. Jane Ansah komanso makomishonala onse a MEC atule pansi ma udindo awo ndipo kuti anthu ena alowe mmalo kuti adzayendetse chisankho chomwe chikubwerachi.
14
Pemphererani dziko lino, ipempha ECM Mpingo wa katolika wapempha Amalawi kuti apempherere dziko la Malawi ndi utsogoleri wadziko lino panyengo ya Lenti. Muuthenga wake wanyengoyi, mkulu wa mabishopu mgulu la Episcopal Conference of Malawi (ECM) Joseph Zuza wati padakali pano, Amalawi akudutsa mumazunzo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Zuza adati: Atsogoleri athu ali ndi udindo waukulu woti moyo uzikhala ofewa wa ife tonse. Monga okhulupirira tiyenera kudziwa kuti Mulungu sangatitaye. Zuza adati zina mwa zomwe Amalawi ayenera kupempherera kuti zichepe ndi katangale ndi ziphuphu, kukondera ochokera kudera kwanu, kusankhana mitundu, zilakolako zakuthupi, ufiti, nkhanza kwa ana, uchidakwa ndi kupembedza Satana. Zuza adapempha akatolika kuti aziyesetsa kukhala Akhristu achitsanzo, ndikutsatira malamulo a Mulungu. Aliyense ayenera kuonetsetsa kuti akukhala okhulupirika pamaso pa Mulungu, adatero Zuza. Ndipo muuthenga wake mnyengoyi, Papa Benedict wachikhumi ndi chisanu nchimodzi adati masiku 40 amene Akatolika akhale akupunguza ayenera kulingalira za mawu opezeka pa Ahebri 10 ndime 24. Tiyenera kukhudzidwa ndi mavuto a ena; kukhala okondana kumanso kugwira ntchito zabwino, adatero Papayo. Kwa masiku 40, Akatolika amakhala akupunguza ndipo zimayamba ndi tsiku la phulusa, lomwe lidali Lachitatu. Panthawiyo, iwo amakhala akupemphera, kugawana, kulingalira molimba, kusala komanso kuchita zachifundo mpaka nthawi ya Pasaka mu Epulo.
13
Aphungu, Makhansala Akana Lipoti la Nthambi ya Ulimi Komiti ya makhansala ndi aphungu a ku nyumba ya malamulo ya mboma la Zomba yakana kuvomeredza lipoti la kuofesi yoona za malimidwe pa nkumano womwe unachitika lachisanu chifukwa lipotili linali ndi zolakwika zambiri. Poyankhula litabwedzedwa lipotilo phungu wa mdera la Zomba Chisi a Mark Botomani wati nyumbayi yabwedza lipotilo chifukwa komiti yomwe imawona zamalimidwe sidafotokodze momwe Anthu akhudzidwira ndi ngozi za kusefukira kwa madzi ndinso kuonongeka kwa mbewu zawo. A Botomani omwenso ndi nduna yodzofalitsa nkhani ati boma la Zomba lakhudzidwa kwambiri ndi madzi osefukira choncho amafuna kuti lipotilo lifotokodze momwe anthu akhudzidwira ndi njala. Poyankhulapo wapampando wa khonsolo ya bomalo la Khansala Wilson Likhusa naye anati akugwilizana ndi kubwezedwa kwa kwa lipotili.
4
Chisankho chopanda mudyo? Kodi azitaya? Chisankho cha 2019 ena sakuchionetsa dovu pamene zipani 12 zimene zidatulutsa atsogoleri mu 2014, zinayi zokha pakadalipano ndi zimene zaonetsa chidwi chotulutsa atsogoleri. Izi zikuchitika pamene kwangotsala miyezi 7 yokha kuti dziko lino lichititse chisankho chapatatu chomwe chichitike mu May chaka chikudzachi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chibambo: Cheteyu ndiye kuti sitiyimira Zipani zinayizo ndi Democratic Progressive Party (DPP), Peoples Party (PP), Malawi Congress Party (MCP) ndi cha United Democratic Front (UDF). Komanso kuli gulu la United Transformation Movement (UTM) lomwe langobwera kumene limenenso likuonetsa chidwi chodzapikisana nawo. Mdziko muno muli zipani zoposa 50 zomwe zidalembetsedwa ndipo zina mwa zipanizo sizipikisana nawo pampando wa mtsogoleri wa dziko. Pocheza ndi Tamvani, zipani zisanu zatsimikiza kuti sizidzapikisananawo mu 2019 malinga ndi kusadabuzika komwe adakuona pachisankho cha 2014. Mwa zipanizi ndi cha Malawi Forum for Unity and Development (Mafunde), Peoples Progressive Movement (PPM), National Salvation Front (Nasaf), United Independence Party (UIP) ndi New Labour Party (NLP). Chipani cha Pfuko (CCP) chomwe mtsogoleri wake anali Davies Katsonga sichipikisana nawo chifukwa chipanicho chidagawana zida pamene mtsogoleri wake Davis Katsonga adasamuka kukalowa ku DPP. Mtsogoleri wa Mafunde, George Mnensa adati alibe chilakolako chopikisananawo ngati mtsogoleri wa dziko lino chifukwa chaka chatha kudali atsogoleri 12 zomwe adaziona kuti ndizokwanira ku fuko la Malawi. Ndibwino kuti tingothandizira kuti mwina pakhale oimira ochepa zomwe zimapangitsa anthu kuti asankhe molondola, adatero Mnensa. Iye adati pali chiyembekezo kuti chipani chake chipanga ubale ndi zipani zina kuti akhale ndi mtsogoleri mmodzi. Pamene mtsogoleri wa Peoples Transformation Party (Petra), Kamuzu Chibambo adati chete amene waoneka kuchipani kwawo ndi umboni kuti alibe khumbo loimira. Achikhala ndikuimira bwezi mutamva zochitika zambirimbiri kuti tiwadziwitse anthu, koma zii amene ndi umboni kuti sitikuyimira. Komanso kugwira ntchito limodzi monga zipani ndi chabwino ku mtundu wa Malawi, adatero Chibambo. Kupatula kugwa mochititsa manyazi komwe adakuona mu 2014, zipanizi zidati zinthu zinanso monga kusagwira ntchito kwa lamulo lokhudza zipani (Political Parties Act) lomwe lidavomerezedwa chaka chatha kwathandiziranso. Iwo akuti sakufuna kudzangodzidzimutsidwa nthawi yothaitha atachititsa kale kampeni. Kadaulo pa ndale, Ernest Thindwa adati sizodabwitsa kuti zipani zikulakatika pamene tikupita kuchisankho cha 2019 chifukwa cha ndondomeko ya chisankho imene dziko lino limatsatira. Iye adati mdziko muno muli ndondomeko yoti amene wapeza mavoti ambiriyo ndi amene wapambana posayangana anthu amene sadamuvotere. Izi zimapangitsa kuti anthu ambiri agwe mphwayi kuti akapikisane nawo ndiye sizachilendo kumva kuti ena azitaya, adatero Thindwa. Iye adati achikhala dziko lino limagwiritsira ntchito ndondomeko ya 50+1, anthu ambiri bwezi ataonetsa chidwi chopikisana nawo.
11
Papa Wati Utumiki ndi Chuma Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati mphatso ya utumiki mu mpingo ndi chuma chachikulu. Papa pa umodzi mwa maulendo ake a utumiki Papa Francisko walankhula izi la mulungu pa bwalo la Saint Peters Square ku Vatican pa tsiku limene mpingowu umachita chaka cha utumiki pakati pa ansembe, asisiteri ndi abulazala ndi ena mu mpingo-wu. Iye wati Maria, Yosefe, Anna ndi Simeon ndi zitsanzo zenizeni za utumiki wa mphamvu komanso wopezeka nthawi zonse. Papa Francisko wati dziko lapansi likusowa atumiki eni-eni amene ali okonzeka kutumikira ndi kulalika za ufumu wa mulungu kudzera mmawu a mulungu komanso zitsanzo zao zabwino. Chaka chilichonse mpingo wa katolika umachita chaka cha atumiki ake mu mpingo.
14
PMS Ipereka Mafuno Abwino a Mwezi wa Kolona Wolemba: Thokozani Chapola ntent/uploads/2019/10/mwakhwawa.jpg" alt="" width="455" height="308" />Mwakhwawa: Mwezi uno ndi opambana kwambiri Ofesi yoona za mabungwe a utumiki wa a Papa ya Pontifical Mission Societies (PMS) yafunira zabwino akhristu a mpingo wakatolika mdziko muno pomwe lero ayamba mwezi wa mapemphero a kolona. Mkulu wa ku ofesi-yi bambo VINCENT MWAKHWAWA auza RADIO MARIA kuti mweziwu wagwilizananso ndi mwezi wapadera wotsekera chaka chapadera cha chibalalitso mu mpingo. Iwo ati mwezi-wu ndi wopambana kwambiri kotero akhristu akuyenera kuugwilitsa bwino ntchito. Mweziwu ndi wapadera chifukwa a Papa komanso mpingo watipempha kukondwelera zaka 100 za kalata yomwe analemba Papa Yohane Paulo wachiwiri komanso chibalalitso cha mpingo kuphatikizapo kolona, anatero bambo Mwakhwawa. Iwo ati akuyembekeza kuti mu mwezi umenewu mmitima ya akhristu muyaka moto wa utumiki popereka molowa manja komanso kupemphera mosalekeza. Polankhulaponso mwapadera mkulu wa bungwe lolimbikitsa mapemphero a KOLONA mdziko a GRACIANO MUKUNUWA akumbutsa akhristu a mpingo wakatolika za ubwino wopemphera kolona maka mu mwezi wa October omwe ndi mwezi wa KOLONA mu mpingowu. Iwo apempha akhristu mdziko muno kuti alemekeze mwezi wu popemphera kolona kosalekeza.
13
Makhonsolo a Zomba, Mangochi Ayamba Kukonzekera COVID-19 Makhonsolo a boma la Zomba komanso Mangochi ayambapo kale zokonzekera pofuna kuteteza anthu ku nthenda ya COVID-19 ngakhale sinafikebe mdziko muno. Pofuna kukonzekera kulimbana ndi matendawa makhonsolo-wa anayitanitsa msonkhano koma mosiyana, komwe kunafika anthu omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana mboma-li. Mwazina pa msonkhano-wu mboma la Zomba, akhazikitsa komiti yomwe muli achitetezo, ocita malonda komabnso ogwira ntchito zosiyanasiyana, ndi cholinga choti akhale akuyendetsa ntchito-zi. Nalo boma la Mangochi lati liwonetsetsa kuti anthu ake ndi otetezeka ku kachilombo ka Coronavirus komwe kakuyambitsa nthenda ya COVID 19. Bwanamkubwa wa bomalo mbusa Moses Chimphepo wati khonsoloyo yayika ndondomeko zabwino zofuna kuwonetsetsa kuti anthu ochokera mmayiko ena monga South Africa komanso dziko la Mozambique lomwe lachita malire ndi bomali, sakulowa mbomalo mwachisawawa.
6
Zomba Cathedral Iyamikira Gulu la Tingathe Wolemba: Thokozani Chapola Gulu la tingathe kumanga nawo Holo mparish ya Sacread aliyamikira kamba kakudzipereka kwake potenga nawo mbali pomanga holo. Mmodzi mwa akuluakulu omwe akuyanganira ntchito yomanga holoyi a Vito Sandifolo ayamikira gululi lamulungu pomwe linakonza fundraising yogulitsa zakudya zosiyanasiyana pa tchalitchi la Zomba Cathedral. Iwo anati gululi lakhala likuthandiza pa ntchitoyi mnjira zosiyanasiyana ndipo apempha akhristu mparishyi kugwirana manja pothandiza ntchitoyi yomwe padakali pano ikusoweka ndalama zosachepera 50 million kwacha. Ntchito imene akugwira ikutithandiza kwambiri. Apitirize kuti thandiza ndipo asatope nafe mmene akuwonekera kuti ndi okonzeka kutero. Kubwera kwawo kwachititsa kuti ntchito yomanga holo isativute kwambiri, anatero a Sandifolo. Iwo ati akhristu atha kupereka chilichonse chomwe angakwanitse kuti chingathandizire pa ntchitoyi osati ndalama zokha. Mmawu ake mmodzi mwa mamembala a gulu la tingathe kumanag nawo holo a lucia mphande ati gulu lawo limadziwa kuti mpingo pawokha sungakwanitse chilichonse. Mpingo wathu wa katolika ukulimbikitsa kumanga mpingo wodzidalira ndipo ife tikutsatira zimenezi. Mwinanso kutsogoloku amne tizayigwiritse ntchito kwambiri ndifeyo achinyamata ndipo ndi chifukwa chake tinawona kuti ndi bwino kuti titengepo gawo, anatero mayi Mphande. Gulu la Tingathe lili ndi mamembala asnu ndi awiri (7) pomwe atsikana alipo asanu ndipo anyamata alipo awiri. Padakalipano gululi lakwanitsa kuthandiza ndi moiyala ya kwale komanso njerwa pa ntchitoyi. Ntchito yomanga holo ya Sacred heart parish ikusoweka ndalama zokwana 150 million kwacha.
14
Akuti akukumana Ndi womwalira Maloza! Mtembo wa mtsikana uli mnyumba, manda atakumbidwa, anthu ena amakumana naye akungozungulirazungulira pamsika komanso mmunda mwa makolo ake. Anthu a mmudzi mwa Mponda mdera la mfumu Mduwa ku Mchinji komwe kwachitika nkhaniyi akuganiza kuti mtsikanayo, Violet Lubani, wa zaka 19 adachita kuphedwa mmasenga. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Katundu wambiri wa banjalo waotchedwa Violet amadandaula kuti diso likumupweteka ndipo adapita naye ku Kamuzu Central Hospital ku Lilongwe komwe adamuchita opareshoni, koma adamwalirira patangopita masiku ochepa. Nyakwawa ndi mafumu adauzidwa komanso anthu adafika mwaunyinji wawo kudzakhudza malirowo. Gulupu Mponda ikuti maloza adayamba kuoneka mtembo wa mtsikanayo utayamba kutuluka thovu mkamwa, mmakutu ndi mphuno. Nkhope ndi nkhungu lake zimasintha. Nkhope yake imaoneka ngati ya mzimayi wachikulire kwambiri, pakapita nthawi imaoneka ngati ya mwamuna. Nkhungu lake limayera pambuyo pake kuda kwambiri, idafotokoza motero gulupuyo. Anthu akudabwa ndi malozazo amayi omwe adapita kukathyola ndiwo zamasamba mmunda mwa makolo amtsikanayo adatulukamo chothawa. Adatifotokozera kuti akumana ndi malemuyo mmundamo. Anthu adathamangira ku mundako, koma sadakampezemo. Tonse tinadabwa, komanso kugwidwa mantha. Mwambo wa maliro udapitirira ngakhale anthu ambiri sadakondwe ndi zomwe zimachitikazo, adatero Mponda. Chipwirikiti chidayamba anthu ena atabweranso ndi uthenga woti akumana ndi mtsikanayo kumsika. Titaona kuti adzukulu ndi anthu ena okwiya ndipo akukambirana zochitira mtopola makolowo powaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya mtsikanayo, tidazembetsa anamalirawo kuopa kuti anthu awachita chipongwe. Mafumu adaitanitsa apolisi kaamba koti zinthu zidafika poyipa, adatero Mponda. Anthu okwiya adagwetsa nyumba ndi kuotcha katundu wa banjalo moti mmene apolisi amafika zinthu zambiri zidali zitaonongeka kale. Mneneri wapolisi wa mboma la Mchinji, Rubrino Kaitano, adati adapeza ziwawa zili mkati moti sakadachoka mpaka kuonerera kuika mtembo wa Violet mmanda. Violet adamwalira pa April 12 ndipo adaikidwa pa April 13. Padakali pano apolisi atsekera mchitokosi anthu oposa 13 kaamba kogumula nyumba zitatu ndi kuotcha katundu wa banjalo. Mponda adati chiikireni malirowo mmanda anthu ambiri akukumanabe ndi mtsikanayo mmalo osiyanasiyana.
19
Idali nthawi ya buleki Sukulu iliyonse imakhala ndi nthawi yopumira kapena kuti nthawi ya buleki. Ena amakangosewerako, ena amakadya, koma Paul Chidale ndi Dolica Mchenga adasinthana Chichewa. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Paul Chidale ndi katswiri wosewera golf komanso akugwira ntchito ku Gestetner ngati ICT Engineer. Dolica ndi wabizinesi. Kukumana kwawo sikukugwirizananso ndi ntchito yawo chifukwa adakumana onsewa ali pasukulu ku Bangwe Private School mumzinda wa Blantyre. Paul akuti panthawiyo adali fomu 3 pamene Dolica adali fomu 1. Iwowa adakhala akuponyerana maso, koma zonse zidakathera kubuleki. Paul kusayinira kuti watengadi Dolica patsiku lodalitsa ukwati wawo Timaponyerana maso mosonyeza kuti timafunana. Tidapezera mwayi nthawi ya buleki pamene tidakumana ndi kucheza, adatero Dolica. Adati akundifuna, koma ndidavutavuta ngakhale pansi pa mtima nanenso ndimamufuna Paul. Kungoti Paul amandisangalatsa machezedwe ake ndi anthu komanso malankhulidwe ake opatsa chikoka, adaonjezera. Paul akuti padatenga kanthawi kuti amumasule Dolica ndi mawu akukhosi chifukwa amafuna aone ngati namwaliyu adali ndi makhalalidwe abwino. Zooneka bwinozo ndiye musakambe, namwaliyu ali bwino komanso ndimafuna kuonetsetsa makhalalidwe ake. Nditakhutira, ndidaganiza zomupezera nthawi ndipo kudali kubuleki komwe ndidakamuuza mawu anga, adatero Paul. Izitu ati zimachitika mwezi wa April mu 2007. Ukwati ndiye adamanga pa 4 October 2015, ku Feed the Children ku Nyambadwe mumzindawu. Amene sadakwatire afatse kaye chifukwa ukwati weniweni umachitika kamodzi pamoyo wa munthu mpaka Mulungu adzakulekanitseni. Ndiye akuyenera atsimikizedi za yemwe akufuna amukwatire kapena kuwakwatira, adatero Paul wa mmudzi mwa Luwanje kwa T/A Chikumbu mboma la Mulanje, polangiza omwe akulingalira za banja.
15
Zionetsero ponseponse Nyimbo imene idavuta pa Wenela tsiku limenelo idali ya Lucius Banda, Jennifer. Mundiuzire Jennifer Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ayeayeyeye Mundiuzire afatse Ayeayeyeye Kokafuna maunitsi akatengako Edzi. Abale anzanga ndiye kudali kuvina ngati tili ku Crossroads Hotel kuyembekezera kudzaonera ukwati woyera pa 20 December pano. Atabwera Abiti Patuma, adati akudzangonditsanzika chifukwa unali ulendo wautali amati auyambewo. Pa Wenela pandilaka. Lero lino ndikupita ku Chitipa, kumene kuli Amalawi enieni a mtima monga Chilembwe. Pamene wapondedwa si bwino kunena kuti akulu mungathe kuchotsako phanzi lanu chifukwa langa lalowa pansi pa phanzi lanulo, adatero Abiti Patuma. Palibe chimene ndidatolapo. Kumenekotu anthu sakuyesa, akwiya chifukwa kuchipatala akupereka chakudya kamodzi patsiku ngati kundende. Tsono munthu angachire bwanji pamene sakudya? Sakukambatu za kusowa kwa mankhwala, adatero Abiti Patuma. Abale anzanga, ndikamati Abiti Patuma amandisokoneza ndimanena chifukwa cha zinthu ngati izi. Adandiyanganitsitsa. Nchifukwa chake Billy Wayaya akamapita yekha pamsewu kusonyeza mkwiyo palibe amamumvetsa. Umbuli ndi nthenda yoopsa zedi. Pajanso kuli za anamwino kuyenda pamsewu. Za ana asukulu otsekeredwa chifukwa cha zionetsero ndiye sitinganene, adapitiriza. Apa ndipo ndidayamba kuzitolera. Paja zionetsero ndiye zangoti mbweee! Zisandikhudze. Zidzandikhudza mukadzakonza chionetsero chonena kuti mukufuna Adona Hilida abwerera kuno ku Wenela. Oipa athawa yekha ndi amodzi mwa mawu omwe adandisiyira atate anga, ndidatero. Za Adona Hilida usachite kukamba. Iwotu ali ngati asirikali akuluakulu a ku Germany amene adazunza Ayuda zaka zapitazo. Nkhondoyo itangotha, asirikaliwo adali kuthawa mdzikolo, ena kukagwidwa ku Brazil mpaka, adatero Abiti Patuma. Ukutanthauza kuti akusiyana ndi Nelson Mandela yemwe adayamba kukhala moyo wothathawa kunja asanakhale paulemerero? Inetu sindikudabwa, chifukwa amabwera ndi zinthu zodabwitsa. Pajatu ndiwo adationetsa kuti nzotheka otsutsa kubera chisankho! Adationetsanso kuti kusolola mwakathithi nkotheka ngakhale wina aomberedwepo, ndidatero. Mmaso mwanga ndimaona mayi wina pompano pa Wenela amene ankakonda kupachika litaka la nsalu paphewa, ati mudzi wonse udziwa palibe ali ndi zitenje zochuluka kuposa iye pano pa Wenela. Abale anzanga dziko laipa ili, kunjaku kwaopsa zedi. Zoona Moya Pete alemba ntchito munthu wosamudziwa polingalira kuti palibenso amadziwa ntchito kuposa iye? Akuluwa phindu lawo ndimalephera kulimvetsa. Pajatu masiku ano kuti upeze ntchito yapamwamba uyenera kudziwana ndi akuluakulu. Palibe cha mahala, adatero Gervazzio ngati wadzuka kutulo. Koma imene amayambitsayo akadaikwanitsa? Ndiye ndangomva kuti ayamba akana kumulemba ntchitoyo? Koma apa pakuonekanso kuti pavuta. Kapena pakufunika kachionetsero kapadera? adabwekera Abiti Patuma.
11
Chipani Cha Poverelle Chadandaula Ndi Kuchepa Kwa Asisteri Wolemba: Sylvester Kasitomu -content/uploads/2019/09/poverelle.jpg 365w" sizes="(max-width: 770px) 100vw, 770px" />Ena mwa asisteri a chipani cha Poverelle Chipani cha asistere cha Poverelle loweruka lapitali chapempha makolo a mpingo wakatolika mdziko muno kuti alimbikitse ana awo moyo wamapemphero kuti akhale atumiki ochuluka komanso odalilika mu mpingowu. Sister BABLA BIMA omwe ndi mkulu wachipanichi mdziko muno anena izi unachitikira Ku parish ya St. Francis Mikoke mu dayosizi ya Dedza pamwambo olandira sister Eurita Kapolo kuchipanichi. Sister Bima (kumanzere) ndi Sister Eurita kapolo yemwe walowa kumene mchipanichi Iwo ati ndi okondwa kaamba koti chipani chawo chawonjezera mtumiki mmodzi patsikuli zomwe ndizonyaditsa kwambiri maka pano pamene chipanichi chiri ndi asisitere ochepa. Ife ndife okodwa kuti lero tawonjezera mtumiki muchipani chathu tipemphe makolo kuti alimbikitse ana awo kuti nkhani za chiitanidwe cha mumpingo ngati ichi, anatero Sister Bima. Mwambowu womwe unasonkhanitsa atumiki komanso akhristu eni ake mu mpingowu unayamba ndi nsembe ya misa yomwe anatsogolera ndi Bambo Philip Mughogho omwe amatumikira mu dayosiziyi.
13
CSC Ipempha Boma Lipereke Chipukuta Misonzi Kwa Okhudzidwa Ndi Nsewu Bungwe La Centre For Social Concern Lapempha Boma Kuti Lichite Changu Kupereka Chipukuta Misonzi Kwa Anthu Omwe Anakhudzidwa Ndi Gawo Loyamba Lomanga Nsewu Wa Machinga Chingale Lirangwe Kamba Koti Izi Zikupereka Mavuto Osiyanasiyana Pamoyo Wawo A Bernard Mphepo Omwe Ndi Mlangizi Ku Bungweli Mu Ndondomeko Ya Economic Governance Ndiyemwe Wanena Izi Atayendera Ndikuwona Ntchitoyi Mmene Ikuyendera Masiku Apitawa. Imodzi mwa nyumba zokhudzidwa ndi nsewu wa Chingale Ndife Okhudzidwa Kwambiri Kuti Boma Silikutengepo Gawo Pankhani Yopereka Chipukuta Misonzi Mpaka Pano. Anthuwa Ufulu Wao Ukuphwanyidwa Munjira Zosiyanasiyana, Tingopempha Boma Kuti Lichite Changu Liwathandize Pozindikira Kuti Nyengo Ino Ndiyamvula . Anatero A Mphepo. Mai Mphatso Charles Ndi Mmodzi Mwa Anthu Omwe Akhudzidwa Ndipo Ati Izi Zikupereka Chiopsyezo Pamoyo Wao Watsiku Ndi Tsiku. Msewuwu Wadutsa Mphepete Mwa Nyumba Kwambiri Ndipo Zikupereka Chiopsyezo Kwa Ana, Komanso Pakhomo Panga Anakumba Ngalande Ndipo Dothilo Anayika Pakhomo Panga Lomwe Likupangitsa Kuti Madzi Adzisefukira Mpaka Kulowa Mnyumba. Anadandaula Motero Mayi Charles. A Masauko Mgwaluko Omwe Ndi Mneneri Ku Bungwe Loona Nkhani Yopereka Chipukuta Misonzi La Roads Fund Administration Wapepesa Chifukwa Chochedwa Kupereka Ndalamazi Zomwe Wati Zimachitika Kamba Kosowa Ndalama Zokwanira Ndipo Walonjeza Kuti Ntchitoyi Ichitika Posachedwapa. Kumbuyoku Tinali Ndimavuto Okhudza Ndalama, Tinali Nazo Zochepa Zomwe Sizikanakwanira Kuti Tilipire Onse Okhudzidwa, Zinakakhala Zokhumudwitsa Kwa Ena Otsalawo, Koma Ndilonjeze Kuti Tsopanso Ndalamazi Zapezeka Ndipo Tili Ndi Chiyembekezo Kuti Tipereka Kwa Onse Okhudzidwa Omwe Analembedwa Mkaundula Sabata Yoyamba Yamwezi Wa January Chaka Chammawachi. Tipepese Chifukwa Chakuchedwaku. Anatero A Mgwaluko Msewuwu Wa Machinga Chingale Lirangwe Uli Mchigawo Choyamba Cha Ntchitoyi Yomwe Ndiyamakilomita Makumi Awiri (20) Yomwe Ikuyambira Ku Lirangwe Kulekeza Ku Chipini.
14
Anthu Akulowelera Malo a Khonsolo ya Ntcheu Khonsolo ya boma la Ntcheu yadandaula ndi anthu ena omwe akuti akulowelera malo a khonsoloyi mmisika ya bomalo. Wapampando wa nthambi yowona zachuma ku khonsoloyi Ezara Mike wauza Radio Maria Malawi kuti zimenezi zikusokoneza ntchito yotolera ndalama za misonkho zomwenso zikuchititsa kuti ogwira ntchito ena ku khonsoloyo akhale nthawi yaitali osalandira malipiro awo. Ina mwa misika ya mboma la Ntcheu Mike wati khonsoloyo imayenera kutolera ndalama zosachepera 180-million-kwacha pa chaka koma padakalipano akukwanitsa kutolera 97 million kwacha yokha. Mmbuyomu anthu akhala akuvutika kuti alandire ndalama zawo penanso kumatha mwina miyezi 12 asanalandire koma tsopano padakalipano tayamba kuzikonza zinthuzo ndipo miyezi yapitayi anthu alandira bwinobwino ndlaama zawo, anatero a Mike. Poplankhulapo wapampando wa msika wa Pengapenga mbomalo a Lenard Zamimba ati mafumu komanso anthu ena ndi omwe akuyambitsa vutoli kaamba koti akumafuna kusonyeza umwini wa malo omwe ndi a boma.
14
ANATCHEZERA Mkazi wanga asabwere? Anatchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndili ndi zaka 25 ndipo ndili pantchito yokhalira pomwepo. Ndine wokwatira ndipo ndili mwana mmodzi. Abwana anga aakazi ndi achikulire kwambiri ndithu koma ndikati ndiwapemphe kuti ndiitanitse mkazi wanga kuti tizidzakhala limodzi amakana. Ndichite bwanji pamenepa? Chonde, thandizeni maganizo. I.J. Mzuzu Zikomo IJ, Ndathokoza chifukwa cha kundilembera kuti ndikuthandizeni maganizo pankhani ya banja lanu. Kodi mudayamba mwawafunsa abwana anuwo kuti nchifukwa chiyani safuna kuti mkazi wanu abwere kuti muzikhala naye pantchitopo? Ndithu payenera kukhala chifukwa. Kodi abwana anuwo ali ndi amuna awo kapena ali okha? Ndafunsa dala mafunsowa chifukwa mwina akhoza kukuthandizani nokha kudziwa chifukwa chomwe safunira kuti mkazi wanu abwere pakhomopo. Mukandiyankha mafunsowa mwina ndidzatha kukuthandizani bwino pa chomwe mungachite chifukwa pano ndinama poti gwero lake lenileni lomwe amakanira kuti mkazi wanu abwere sindikulidziwa nkomwe. Ndisapupulume kupereka chigamulo pomwe nkhani yonse sindikuidziwa bwino lomwe. Natchereza Sakundifunanso Gogo wanga, Ndidakwatiwa chaka chathachi pambuyo popanga chinkhoswe. Tidakhala mbanja mwezi wathuthunthu osandiuza kuti amamwa ma ARV koma tsiku lina ndidatulira nditapeza mankhwalawo mmabotolo. Nditamufunsa mwamuna wangayu adayankha kuti: Pepa mkazi wanga, ndimaopa kuti ndikakuuza ukana kuti tikwatirane. Koma usadandaule chifukwa ndisamala ana ako pamodzi ndi iweyo moyo wanga wonse. Timakhalabe ngati banja, koma nditadwala ndidapita kuchipatala komwe adandiuza magazi koma amati zotsatira zake samaziona bwino. Nditapitanso adandiuza kuti ndilibe kachilombo ka HIV ndipo nditamuuza mwamuna wanga adati sakundifunanso banja ati chifukwa ndilibe kachilombo. Nditani? Chonde ndithandizeni. Zina zikamachitika kumangothokoza Mulungu! Mwati mwamuna wanu akuti basi sakukufunaninso banja chifukwa mulibe kachilombo? Zoona? Cholinga chake kuchokera pachiyambi chidali chiyani? Kunena zoona, iyeyu adali ndi kampeni kakuthwa kumphasaamadziwa bwino lomwe kuti ali ndi kachilombo ka HIV ndipo ndikhoza kunena pano popanda mantha kuti cholinga chake chidali kufalitsa dala kachilomboko. Moyo woipa zedi umenewo. Kufalitsa dala kachilombo ka HIV kapena matenda ena alionse ndi mlandu waukulu ngati sindikulakwa ndipo munthu wotero ayenera kulangidwa. Ndiye inu mwati mwakayezetsa kawiri konse koma sadakupzeni ndi kachilombo, thokozani Chauta! Tsono ngati akuti sakukufunaninso ukwati, inu vuto lanu nchiyani? Alibe chikondi ameneyo, musiyeni mudakali moyo. Koma osangomusiyasiya ameneyo, mukamusumire kumabungwe kapena kukhoti kuti chilungamo chioneke mwina ena angatengerepo phunziro.
12
Ndisathandize mwana wanga? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndi mkazi wanga tidalekana titakhala pabanja zaka ziwiri. Mkaziyu ndidakukwatira titachimwitsana pasukulu ine ndili Fomu 4 pamene iye adali Fomu 2. Ndidali kuchikamwini. Koma zinthu mbanja zidasintha mosadziwika bwino. Mkazi wanga adayamba makani ndipo ndikamabwera kuchokera kuntchito ndimapeza nsima yosaphika, madzi osamba palibe ndipo izi zitachitika kwa sabata mpamene ndidakawatulira nkhaniyi achimwene ake monga ankhoswe a banja lathu koma padalibe chosintha. Chidatsitsa dzaye ndi ichi: ndidamuuza kuti ngati sanena chimene chikupangitsa kuti azichita mwano sagona mnyumbamo ndipo adatulikadi kukawauza achimwene ake. Atabwera achiwene akewo adangofikira kunena kuti ndatopa nawe, uzipita kwanu, siwenso mkamwini pano. Akakhala mchemwaliyu ndimpezera mwamuna, amukwatira. Ndipo adakatenga makiyi kudzakhoma nyumba yanga nthawi ili chamma 11 koloko usiku, mkazi wanga akungoyangana osanenapo kanthu. Ndinanyamuka usiku womwewo ulendo wa kwathu ku Nkhula. ndipo mpaka pano palibe kulumikizana. Ndikati ndikamuone mwana wanga wa zaka ziwiri, Prince, mayi a mkazi wangayo amati adapita ndi mayi ake ku Zomba kwa malume ake koma nditafufuza ndidamvetsedwa kuti mkaziyo adayambanso sukulu yogonera konko papasekondale ya Namikase ku Mdeka komwe akubwereza Fomu 2. Ndiye nditani pamenepa? Kodi banja likatha ndiye kutinso mwana wako usamuthandize? Nanga kutula nkhani kwa ankhoswe nkulakwa? Chonde ndithandizeni. BM Blantyre Okondeka BM, Choyamba ndikuthokozeni chifukwa choyala nkhani yanuyi bwinobwino kuti ndiimvetsetse ncholinga choti ndikuthandizeni. Ndi mmene mwafotokozeramu zikuoneka kuti ankhoswe a banja lanu sadakuthandizeni chifukwa mmalo molimbikitsa banja lanu iwo ndi amene adali patsogolo kulithetsa. Koma banja lenileni silimatha monga banja lanu lidathera; lanu lidatha mwachibwana zedi, kusonyeza kuti ndondomeko zoyenera zokhudza mmene banja limayambira kapena kutha sizidatsatidwe. Choyamba ndikuona kuti banja lanu lidali lokakamiza chifukwa mudachita kuchimwitsana muli pasukulu ndipo pano mwana wakula. Apa nchachidziwikire kuti makolo a mkazi wanu, achimwene ake omwe mukuti ndi ankhonswe a banja lanu, komanso mkazi wanu iye mwini akufuna kuti apitirize sukulu. Uku, mmene ndikuonera, sikulakwa, komabe adayenera kuzindikira kuti kuthetsa banja la zaka ziwiri mwanjira yotere ndi kulakwa. Masiku ano kuli mwawi woti mayi atha kupitiriza sukulu kuchokera kubanja, bola kugwirizana ndi mwamuna wake. Zimatheka ndithu. Padalibe chifukwa choyambira kuchita mwano kapena kuonetsa mkhalidwe woipa ngati mkazi wanu amafuna sukulu, koma kukhala pansi ndi kukambirana za tsogolo lanu ngati banja. Mkaziyo akadatha kukuuzani za maganizo ake ofuna kupitiriza sukulu ndipo ndikhulupirira mukadatha kugwirizana kuti muchita bwanji, osati mmene zidakhaliramo. Mwachidule, pofuna kukuthandizani chochita, ndikuti ngati mumamukondabe mkazi wanu, muwauze ankhose onse-akuchikazi ndi akuchimuna-za cholinga chanu ndipo ngati ali anzeru akhala pansi nkukambirana kuti banja lanu, ngati lidalidi lovomerezeka, lipitirirebe ngakhale mkazi wanu ali kusukulu. Mwana wanu, Prince, asavutike inu mulipo, muthandizeni ndithu mnjira iliyonse chifukwa ndi wanu basi, osati wa wina ayi.
15
Mswati akhale chitsanzo kwa achinyamata Pulezidenti Joyce Banda wati mfumu yachingoni yomwe angoidzoza kumene, Mswati Kanjedza Gomani yachisanu ikhale chitsanzo kwa achinyamata. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Banda amalankhula izi Lamulungu pa 5 Ogasiti pomwe adali mlendo wolemekezeka ku mwabowo ku Lizulu mboma la Ntcheu. Mwazina Banda adapempha anthu andale kuti asasokoneze mfumuyi, yomwe ndi ya zaka 17. Tithandize mfumu yathu kuti igwire bwino ntchito. Fumu ikhale yachilungamo, yodziwa kuweruza milandu; amati milandu sagula ndi chipanda cha mowa. Komanso, ngati boma, ndife osangalala kukhala ndi mfumu yachinyamata ngati imeneyi chifukwa ikhala chitsanzo chabwino kwa achinyamata. Zomwe izichita mfumuyi achinyamata adzitengera iyo, adatero Banda. Mswati Gomani walowa ufumuwo kutsatira imfa ya bambo ake, Willard Kanjedza Gomani yachinayi yomwe idamwalira mwezi wa Sepitembala mu 2009. Pamwambowo, kudabwera akuluakulu andale komanso amabungwe. Nayo mfumu yaikulu ya angoni mdziko la Mozambique, T/A Zimtambira, idali nawo pamwambowo.
11
Mugabe Alowa Mmanda Lamulungu Wolemba: Thokozani Chapola gabe.jpg 624w" sizes="(max-width: 488px) 100vw, 488px" /> Thupi la yemwe anali mtsogoleri wopuma wa dziko la Zimbabwe a Robert Mugabe, liyikidwa mmanda la Mulungu likudzali, pomwe lafika mdzikolo lachitatu masana kuchokera mdziko la Singapore komwe amalandira thandizo la kuchipatala. A Mugabe omwe anali mtsogoleri oyamba dzikolo litalandira ufulu odzilamulira mchaka cha 1980, anamwalira sabata yatha ali ndi zaka 95 zakubadwa. Iwo akhala akutsogolera dzikolo kwa zaka pafupifupi makumi anai, kufikira pomwe anachotsedwa mokakamiza ndi asilikali mchaka cha 2017. Pali chiyembekezo choti thupi la a Mugabe,aliika mmanda la Mulungu likudzali kumalo omwe kumaikidwa anthu omwe anadzipereka pomenyelera tsogolo la dzikolo, pomwenso zikumveka kuti achibale a Mugabe amafuna kuti aikidwe kwawo. Malipoti a wailesi ya BBC akusonyeza kuti anthu mazanamazana anasonkhana pa bwalo la ndege mu mzinda wa Harare dzulo kukalandira thupi la malemu a Robert Gabriel Mugabe.
14
Anatchezera Sitinakumanepo Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi mkazi amene ndidamufunsira pafoni koma sitinaonanepo. Timangoimbirana foni basi koma amandiuza kuti amandikonda kwambiri. Ndimukhululupirire? Zikomo, Nzovuta kukuthandizani chifukwa simunanene kuti zidayamba bwanji kuti mumufunsire mkaziyo pafoni. Kodi nambala yake mudaitenga kuti? Adakupatsani ndi mbale wanu kapena mbale wamkaziyo? Mnzanu? Mnzake? Mwa njira iliyonse, nanunso mukuonetsa kuti mukhoza kukhala ndi kamtima ka chisembwere kapena mwalifunitsitsa banja ndiye mukufuna kupeza mkazi basi. Dekhani. Komanso ine pokhala wa mvula zakale zambiri zikumandidutsa komabe adzukulu ena amandiuza kuti kunjaku kwadza njira zamakono zochezera pafoni monga Whatsapp, Facebook ndi zina zotere. Sindikudziwa ngati nkotheka kuti mudapatsana manambala kupyolera mnjira zimenezi. Choti mudziwe nchakuti njira zopezera mwamuna zimakhala zosiyanasiyana koma chachikulu chimakhala chakuti munthu amene ukumanga naye banja ayenera kukhala yekhayo ukumudziwa bwino. Pali banja apa? Zikomo gogo, Tidamangitsa ukwati ndi mkazi mu 2010. Tili ndi mwana mmodzi. Ali ndi mimba, iye ankakana kukhalira malo amodzi ati poopa kuti mimba ichoka. Nkhaniyo ndidaitengera kwa ankhoswe omwe adatithandiza kuti ziyambenso kuyenda monga banja. Koma mwanayo atabadwa, iye adayambanso kukana zokhalira malo amodzi ati chifukwa azikhala wotopa. Nditayitengera nkhaniyo kwa ankhoswe, adayikanika. Kuntchito adandisamutsira ku Mzuzu koma iye adakana kupita nawo. Ndidapitiriza kumulipirira lendi koma patatha miyezi ingapo adachoka ndipo adapita kwa mayi ake ku Blantyre. Ndidapita komweko koma ukunso adakana zoti tikhalire malo amodzi. Ndichitenji? NJ, Zomba. NJ, Ndikudziwa kuti kukhalira pamodzi si ngodya yokhayo yomangira banja koma iyi ndi njira yosonyezera chikondi pa mwamuna ndi makzi wake choncho ngati wina apezeka kuti akulanga mnzake mnjira yotere, zimasonyeza kuti penapake zinthu si zili bwino. Zifukwa zimene mkazi wanuyo akupereka ndi zopanda pake, kusonyeza kuti pali china chimene akubisa. Msinkhu wangawu, sindidamvepo kuti mimba yachoka chifukwa mwamuna ndi mkazi amagonana mkaziyo ali woyembekezera ndiye izi akuzitenga kuti? Komanso mudziwe kuti mkazi wanuyo akudziwa kuti apa banja lathapo basi. Poyamba, kukukanizaniko. Kachiwiri, nchifukwa chiyani adakana kukutsatirani kuntchito? Ndipo pomaliza nchifukwa chiyani wabwerera pakhomo la amake? Zonsezo ndi zizindikiro kuti apa paipa. Chofunika nchakuti mupite kwa ankhoswe mukatule nkhaniyi. Adasintha Gogo, Ndili ndi mkazi yemwe ndili naye mwana wa zaka zitatu. Malinga ndi mavuto a zachuma, ndidachoka ku Blantyre kudzagwira ntchito ku Lilongwe. Patatha miyezi ingapo adanditsatira. Koma chongobwera kuno, iye adasintha ndipo amakonda kucheza ndi amayi oyendayenda. Ndichitenji? M, Lilongwe. M, Poyamba simunandiuze ngati ukwati wanu uli wa kwa ankhoswe kapena mudangotengana. Ngati ndi wa ankhoswe, kawakambireni. Ngati ayi, poyamba muyenera kumufunsa mkazi wanu chifukwa chimene akuyendera ndi amayi oyendayendawo. Mumuuze kuti ayenera kusintha ndipo ngati sasintha, chochita mukuchidziwa kale. Kunjaku kwaopsa adzakubweretserani matenda.
12
Archdayosizi Ya Blantyre Iyamikira Sister Nsona Wolemba: Glory Kondowe MG-20190916-WA0033.jpg 720w" sizes="(max-width: 357px) 100vw, 357px" /> Komiti yomwe imayendetsa miyambo ikuluikulu mu archdiyosizi ya Blantyre Lamulungu yayamikira ntchito yabwino yomwe Sister Meria Nsona agwira pamene anali membala wa komitiyi. Izi zadza pa mwambo wotsanzikana nawo ndi kulandira sister Hortensia Njala omwe alowa mmalo mwao mwambo womwe unachitikira ku nyumba ya archbishop wa arkidayosiziyo ku CI. Mmawu awo bambo Alfred Chaima omwe ndi mkulu woona za utumiki mu arkidayosiziyo ati sister Nsona anali munthu amene sanabise mphatso zawo potumikira mpingo ngati membala wa komiti yoyendetsa miyambo ikuluikulu yomwe muchingerezi imachedwa kuti Events Committee. Sister Nsona anali munthu wachangu, wosatopa ndi wosawinya potumikira pa nkhani yachipembezo, anatero bambo Chaima. Koma polankhulapo Sister Nsona ati ndi olemera kuthupi komanso uzimu chifukwa cha mphatso zosiyanasiyana zomwe aphunzira ndipo kupambana zonse akuthokoza mulungu chifukwa cha nzosezi nditchito yomwe ansembe agwira. Ndikuthokozanso amayi omwe andiphunzitsa luso losoka la desgning zomwe ndikaphunzitsenso amayi amu dayosizi ya Chikwawa komwe ndikupita, anatero Sister Nsona. Polankhulapo Sister Hortensia Njala omwe alowa mmalo wa sister Nsona ati ndi okondwa kuti akuluakulu a chipani chawo cha Atumiki a Maria Virgo Wodala [Servants of the Blessed Virgin Mary SBVM] powakhulupilira kuwaika mu komitiyi. Siter Meria Nsona atumidwa ndi akuluakulu awo achipani kuti akatumikire mu dayosizi ya Chikwawa kuchoka ku Our Lady of Wisdom mu arkdayosizi ya Blantyre komwe amatumikira.
14
DPP ikutolera Nambala zovotera Ziyangoyango pa chisankho! Anthu ena achipani cha DPP akuti akutolera nambala za ziphaso za unzika, komanso zovotera kwa anthu amene adalembetsa. Izi zikuchitika ku Phalombe, Mulanje, Balaka, Ntcheu, Kasungu, Mchinji ndi Rumphi. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anthu ena akulemba nambala za ziphaso ngati izi Ngakhale mlembi wa DPP, Greselder Jeffery ndi mneneri wake Nicholas Dausi adakana kuikapo mlomo pa nkhaniyi, mdindo wina mchipanicho wauza Tamvani Lachitatu kuti iyi ndi njira yomwe akhazikitsa kuti apeza mavoti ambiri pachisankho chikudzachi. Lolemba Enelesi Nyandula wa mmudzi mwa Bamba mdera la mfumu yaikulu Phambala ku Ntcheu adauza mtolankhaniyu kuti achipani cha DPP adabwera mmudzi mwawo kudzatolera nambalazo. Akufuna nambala za ziphaso zathu, kodi tiwapatse? adafunsira nzeru Nyandula. Akuti nzokhudzana ndi zisankho zikudzazi, ena apereka kale nambala zawo. Iye adati ali ndi mantha kuti mwina sadzapeza mwayi wodzavota poganizira kuti mwina voti yake yaponyedwa kale. Gavanala wa DPP mchigawo cha kummwera mbomalo, Jeremiah Lilani, adavomera kuti akutolera nambalazo popeza wauzidwa ndi akulikulu kwa chipani chawo. Lilani adati DPP ikutolera nambala za anthu omwe akonzekera kudzavotera chipanicho pa May 21. Tikufuna tidziwe amene adzativotere. Tikatolera nambalazo tikumawaika mmaeliya momwe akuyenera kukhala, iye adatero. Titamufunsa kuti adzadziwa bwanji kuti munthuyo wavotera chipanicho, gavanalayo adati ali ndi chikhulupiriro choti anthuwo sadzawaputsitsa podzavota. Kungotolera nambala kokhako aliyense azidziwiratu kuti chipani chovotera ndi cha DPP ndipo tikukhulupirira sadzatipusitsa, adatero Lilani. Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) ladzudzula mchitidwewu. Mmodzi mwa akuluakulu a MEC, Jean Mathanga Lachitatu adati ofesi yake yamva zoti anthu ena akutolera manambala za anthu, koma palibe amene wadandaula ku bungwelo. Iye adati kutenga nambala ya chiphaso cha munthu wina ndi mlandu malingana ndi gawo 24 ndime 3, 4 ndi 5 ya malamulo oyendetsera zisankho a dziko lino ndipo wopezeka wolakwa ayenera kukaseweza zaka 7 mndende. Koma palibe mlandu kungotenga nambala ya chiphaso. Komabe funso ndi loti kodi akufuna akatani nazo? Ukuku ndi kungosokoneza mitu anthu odzavota ndipo tikuyenera kuchitapo kanthu msanga, adatero Mathanga. Iye adati aliyense amene nambala yake yatengedwa, chiphaso chake chidataika kapena kupsa, asadandaule chifukwa adzavotabe. Uthenga umveke kuti nonse amene ziphaso zanu adakutengerani, zidasowa kapena nambala yanu atenga, muli ndi mwayi wodzavota ndipo patsikulo dzapiteni mukavote, iye adatero. Mathanga adati aliyense amene watenga chiphaso kapena nambala ya mnzake sangathe kuigwiritsa ntchito povota. Vutoli lafalikira paliponse Sibongile Machinjiri wa mmudzi mwa Lunguzi mdera la mfumu yaikulu Lundu ku Blantyre adati adauzidwa kuti apereke nambala yake ya unzika, koma sadamufotokozere chifukwa chake. Adatenga nambala ya chitupa changa ndipo poyambapo amati atipatsa chakudya, koma mpaka lero palibe chomwe chachitika, adatero Machinjiri. Enock Mangola, wa zaka 70 wa mmudzi mwa Mishoni, mdera la mfumu yaikulu Mabuka ku Mulanje adati nambala za anthu ena zatengedwa kale mderalo. Sitikudziwa chomwe akufuna apange nazo, koma zayamba kutiopsa, adatero Mangola. Mkulu wa zophunzitsa anthu mbungwe la Nice mchigawo cha kummwera Enoch Chinkhuntha adati bungwe lawo lamva za nkhaniyo ndipo akufufuza. Tikudziwa kuti anthu ena akuchita izi pongofuna kuzunguza ovota. Akufuna kuti aziona ngati wina akatenga nambala yawo ndiye kuti adzadziwa momwe wavotera. Ayi voti ndi ya chinsinsi, adatero Chinkhuntha. Iye adati mwa ena amene akhala akutolera nambalazo ndi mafumu. Uwu ndi mlandu ndipo sitikugona, tikufufuza izi, iye adanenetsa. Malinga ndi Moir Walita Mkandawire yemwe amatsogolera bungwe loima palokha ku Rumphi, izi zikuchitika ku Mlowe, Chiweta, Zunga ndi Old Salawe. Iye adati nkhaniyo itamveka adakadziwitsa bungwe la Nice, koma mpaka lero palibe chachitika. Mkulu wa Nice mboma la Rumphi, Mollen Zgambo, adati akufufuza umboni kuti ayitengere pena nkhaniyi. Gulupu Zinkambani ya ku Nkhamenya mboma la Kasungu idati mchitidwewu adayamba kalekale mderalo. Iye adati mafumu adakumana nkukambirana za mchitidwewu ndipo adagwirizana zothana ndi wina aliyense wopezeka akutolera nambala za anthu. Mariko Zinenani wa mdera la mfumu Kalumo ku Ntchisi adati izi zikuchitika, koma sakudziwa chipani anthu omwe akuchita izi. Anthuwo amati tipereke nambalazo ponena kuti akufuna atilembe kuti tilandire zipangizo zotsika mtengo, koma mpaka lero sitidaone yankho lake, adatero Zinenani. Bungwe la MEC lidalemba anthu 6.8 miliyoni kuti ndiwo akaponye voti.
11
Maliro akapeza ukwati Pamoyo wa munthu, mavuto kapena mtendere zimabwera mosayembekezera. Nthawi zina zovuta zimagwa pamene pali zilinganizo zina zachimwemwe monga ukwati. GIFT CHIMULU adacheza ndi gogochalo Pemba a mboma la Salima kuti amve zambiri maliro akapeza ukwati pa mudzi zimatani? Adacheza motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Gogo zimatani kudera kwanu kuno maliro akagwa pabanja lomwe lakonza chilinganizo cha ukwati? Choyamba ndinene kuti ngati zikafika potero, mafumu ndi mikoko yogona imaima mitu chifukwa cha nkhani imeneyi. Koma ndinene kuti zimatengera kwambiri kuti kodi ubale wa amene wapitayo ndi amene akupanga ukwati ndi wotani? Pemba kufotokozera Chimulu momwe zimakhalira Tiunikireni tsopano zikatero ngati gogochalo, gawo lanu limakhala lotani? Monga mudziwa mafumu amakhala ndi mbali yaikulu panthawi ya ukwati angakhalenso maliro, koma zotero zikagwa timayenerabe kukumana ndi a kubanja pa ganizo lawo, koma nditsindike kuti nthawi zambiri timatsekera kaye zovutazo ndi cholinga choti mwambo waukwati udutsepo. Koma zikatero ena sanganene kuti mwapeputsa maliro? Maganizo otere atha kukhalapo koma choti ndikuuzeni nchoti kukonzekera ukwati sikwatsiku limodzi ayi, pamene maliro amangodza mwadzidzidzi. Komanso timakhulupirira kuti pamene wina wamwalira zake zimakhala kuti zatha, choncho amoyo sangaimike zichitochito zawo kaamba ka zovuta. Inu gogo pa nthawi yanu ngati mfumu zinakugweraponi zoterezi? Pa nthawi yanga ayi! sizidandionekerepo koma ndaziona zikuchika ndili wamngono maliro adayamba atsekeredwa kaye kudikira ukwati udutsepo. Zonse zidayenda bwinobwino popanda milandu potsatira chilinganizo chotero. Koma miyambo ngati imeneyi ana a masiku ano sakuyidziwatu sadzatitukwana tsiku lina tikadzatsekera maliro kaamba ka ukwati? Nkhawa yanu ndi yoona ndipo zikufunikiradi dongosolo kuti ana ongobadwa kumenewa azidziwa miyambo ya makolo komanso momwe angathanirane ndi mavuto okhudza miyambo komanso zikhalidwe zawo. Ndipo gawo lalikulu lili mmanja mwa makolo awo kuti aziwaunikira ana awo. Pomaliza gogo mzimu wa wotisiyayo mukuona ngati amaganiza zotani pomwe tasiya mwambo woika mmanda thupi kaamba ka ukwati? Mukuganiza kwambiri koma monga ndafotokozera muja zoterezi zimachitika mosapanganika, ndipo ngati mzimu wake wakwiya mapemphero amachotsa zonsezo. Ndimalize ndi kunena kuti ngakhale izi zili choncho nthawi zones maliro timawapatsa ulemu wofunikira, timatha kuimika zina zonse kaamba ka zina ndi zina koma paukwati pokhapo ziyenera kutero basi. Mwatero gogo? Eya anthu akavine kenako kulira komanso mwambo wonse wa maliro pambuyo.
15
Anthu Ataya Chikhulupiliro Ndi MEC-CCJP Bungwe la chilungamo ndi mtendere mu dayosizi ya Dedza lati lapeza kuti mzika za dziko lino zilibe chikhulupiriro ndi anthu omwe akuyendetsa chisankho mdziko muno. Anthu sakuwakhulupiliranso Mkulu wa bungweli a Lawrence Puliti alankhula izi pamene bungwe lawo likumemeza anthu kuti akalembetse mkaundula wa mavoti pa chisankho chomwe chichitike mdziko muno pa 2 July chaka chino. A Puliti ati mmadera onse omwe bungweli layenda, anthu ali ndi mkwiyo ndi mmene chisankho choyamba chinayendera ndipo akuona kuti sipakhala kusintha kulikonse ngati amene ayendetse chisankho cha tsopanochi ndi omwewo amene anayendetsa chisankho cha mu 2019.
11
Bajeti iganizire mavuto a anthu Ndondomeko ya chuma ndiyo chiyembekezo chachikulu tsopano chomwe chingachepetse mavuto omwe anthu akukumana nawo kaamba ka kukwera mitengo ya zinthu mdziko muno. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda dzulo watsegulira msonkhano wa aphungu a Nyumba ya Malamulo omwe akuyembekezeka kukakambirana za ndondomeko ya chuma choyendetsera dziko lino (Bajeti) kuyambira chaka chino mpaka 2014. Maganizo a amabungwe, mafumu komanso anthu ena amene takamba nawo asonyeza kuti pokhapokhapo boma liganizire anthu ake popanga ndondomekoyi, ndiye kuti mavuto omwe adza kaamba ka kugwa kwa mphamvu ya kwacha akhoza kunyanyira. Pofotokozera Tamvani, mkulu wa bungwe loona za ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito, mafumu ndi anthu ena ati mavuto, makamaka okhudza nkhani ya mitengo ya zinthu poyerekeza ndi mmene anthu amapezera, akula kwambiri. Ndemangazi zadzudzula kwambiri zina mwa mfundo zomwe ndondomeko ya chuma ya 2012 mpaka 2013 idatsata ponena kuti mmalo mochepetsa mavuto a anthu, zidaonjezera zowawa, makamaka kwa anthu akumudzi omwe kapezedwe ka ndalama nkovuta. Malinga ndi Kapito, zina zomwe zidavuta mu Bajeti ya 2012/2013 ndi zoti pambali poti ndondomeko yomwe ikungothayi ikadayesetsa kuyangana mbali zina, iyo sidaganizire anthu akumudzi chifukwa mbali zambiri zomwe ndondomekoyi idakonza sizidawakhudze. Iye akuti boma lidachotsa misonkho panyuzipepala, kaunjika ndi buledi, mwa zina zomwe amagula kwambiri ndi anthu okhala mmadera a mmizinda ndi mmatauni momwe njira zopezera ndalama zimapezekako kusiyana ndi kumudzi. Bola popanga ndondomeko ya 2013/2014 aganizirepo kwambiri mmene anthu akumidzi angawathandizire kuti azitha kupeza ndalama zogulira katundu wofunika kwambiri pamoyo wa tsiku ndi tsiku. Mndondomeko yomwe ikupita kumapetoyi mbali imeneyi sadayiganizire mokwanira nchifukwa chake anthu akhala akuvutika kwambiri mitengo ya zinthu itayamba kukwera. Ena mpakana anasiya kukwera mabasi chifukwa choopa mtengo ndipo ena adaimika galimoto zawo chifukwa cholephera kugula mafuta. Ndikanakhala wosangalala kwambiri ngati potulutsa ndondomeko ya chaka tikuchiyambachi aganizirepo zinthu ngati zimenezi, adatero Kapito. Itangotuluka Bajeti ya 2012/2013, mneneri wa za chuma mchipani cha Malawi Congress Party (MCP) Joseph Njobvuyalema adati ndondomekoyo idangoganizira anthu okhala kutauni osati kumudzi monga mmene aphungu ambiri ankayembekezera. Kutukula anthu Njobvuyalema adati boma limafunika kuonetsetsa kuti Bajeti ikupatsa anthu akumudzi mwayi wogwira ntchito zingonozingono kuti azitha kupeza kangachepe koti azithandizikira poyerekeza ndi kuti ndalama ya kwacha inachepa mphamvu kwambiri. Nthawi zambiri akumudzi omwe amapezako ndalama amaipeza pakamodzi makamaka akagulitsa mbewu zawo ndiye ndalama ikagwa iwo atagulitsa kale, ndalama yawoyo simalimba choncho amakhala mmavuto pafupipafupi, adatero Njobvuyalema. T/A Njewa ya ku Lilongwe yati popanga ndondomekoyi boma liganizireponso bwino ndalama zopita kuthumba logulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo poganizira kuti chiwerengero cha anthu ofuna kupindula nawo chikunka chikwererakwerera. Njewa adati poganizira mbaliyi boma lionetsetsenso kuti ndondomekoyo ili ndi njira zabwino zoyendetsera kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo poopa kuti alimi angaone zomwe zidaoneka chaka chatha pogula fetereza ndi mbewu zotsika mtengo. Pakufunika kutinso akamakonza ndondomekoyo aganizirepo zokhazikitsa mfundo za kayendetsedwe ka ndalama zogulira zipangizo zotsika mtengo kuti pasamakhale chinyengo cha mtundu uliwonse. Chaka chatha alimi ambiri makamaka kuno kwathu anapezeka kuti agula mbewu yomwe idakanika kumera mpaka anakakamizidwa kugulanso mbewu ina, ndiye ndi mavuto omwe ali mmidzimu pankhani ya zachuma pamenepa, mpofunika patakonzedwa, adatero Njewa. Anthu akutipo chiyani? Foster Ngondo yemwe amakonza galimoto mumzinda wa Lilongwe, akuti pomwe aphungu akukakambirana ndondomekoyi, ndi mwayi kuti athe kukonza zomwe zidavuta kwambiri mchaka chomwe chikuthachi. Akuti masitalaka osiyanasiyana omwe akhala akuchitika okhudza malipiro mchakachi ndi umboni wokwanira kuti anthu adakumana ndi mavuto ambiri omwe akufunika kukonzedwa. Tiyembekezera zakupsa kuchoka kumeneku [ku Nyumba ya Malamulo] osati tizidzatinso pakadakhala chonchi, ayi. Momwe munali mavuto akuluakulu tamuwona ndipo akuluakuluwonso aonamo, choncho akuyenera kuti mmalo ngati amenewo akonzemo, adatero Ngondo. Naye Loveness Botomani, yemwe amagulitsa msitolo yogulitsa ziwiya, wati boma lisalimbe mtima kwambiri ndi ndalama zomwe likuyembekezera kuchokera kufodya chifukwa ndondomeko ya chaka chino ifunika kuonjeramo ndalama zambiri. Tisataye nthawi ndi kuwona ngati tili ndi ndalama zambiri zomwe zachokera kufodya. Tikuyenera kuganiza kuti mu Bajeti ya chaka chino muli zosowa zambiri. Osaiwala kuti pakatipa malipiro akwezedwakwezedwa komanso zina ndi zina zasintha choncho pafunika ndalama zambiri zowonjezera mundondomekoyi, adatero Botomani. Boma likutinji? Koma mneneri wa boma Moses Kunkuyu wati ndondomeko ya chuma ya 2012/2013 yayesetsa kutukula miyoyo ya anthu akumidzi koma kuti sizidawonekere chifukwa nthawi zambiri anthu amathamangira kuloza pomwe pakuperewera. Si zoona kuti ndondomekoyi inasiyiratu kunja anthu akumidzi chifukwa pali zambiri zomwe zinali mndondomekoyi zomwe cholinga chake chinali kutukula miyoyo ya anthu akumidzi ndipo zambiri mwa izo zinakwaniritsidwa. Mndondomekoyi ndalama zina zinagwiritsidwa ntchito ya chitukuko cha kumidzi ya Social Cash Transfer yomwe yapindulirapo anthu ambiri a mmadera a kumidzi komanso munali pologalamu ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo yomwe alimi ambiri akumidzi adapindula nayo, kungotchulapo zochepa chabe, adatero Kunkuyu. Iye adati pokonzekera ndondomeko ya chuma cha 2013/2014 boma linapanga kale kafukufuku wa mnthambi zosiyanasiyana zofunika kulandira ndalama kuphatikizapo madera a kumidzi ndipo lakonzekera bwinobwino. Bajeti ya 2012/2013 idali ya ndalama zokwana K406 biliyoni ndipo mwa ndalamazi, zambiri zinapita ku unduna wa maphunziro womwe udalandira K74 biliyoni ndi unduna wa zaulimi womwe udalandira K68 biliyoni yomwe K40 biliyoni idali ya pologalamu ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo.
2
Boma liganizire bwino pa sabuside Adzavutika: Nkhalamba ndi ana amasiye Mkonzi, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndalemba kalatayi kutsatira zomwe nduna yoona zaulimi a Allan Chiyembekeza adanena masiku apitawa. Mukunena kwawo, a Chiyembekeza adati boma likufuna kuti anthu omwe angalandire mbewu ndi fetereza zotsika mtengo chaka chino asalandirenso chaka chinacho. Iwo akuti izi zithandiza kuthetsa mchitidwe wa chinyengo komanso kuchepetsa mchitidwe woti anthu amodzimodzi ndi amene azipindula mundondomekoyi. Adzavutika: Nkhalamba ndi ana amasiye Ngakhale maganizo amenewa akuoneka ngati abwino, ine ndikuona kuti mfundoyi ipweteketsa magulu ena a anthu. Ndikunena izi chifukwa boma silidatiuze ndondomeko zomwe liike pofuna kuonetsetsa kuti okalamba ndi ana amasiye omwe amalerana okhaokha omwe sangathe kudzigulira feteleza ndi mbewu pamsika liziwathandiza bwanji. Palinso anzathu omwe ali ndi mavuto osiyanasiyana monga kulumala omwe akhala akudalira feteleza ndi mbewu zotsika mtengo kuti apeze kachakudya kokwanira timisiku tingapo kudzera mu ulimi. Awa ndi ena chabe mwa magulu a anthu omwe sangathe kudzigulira mchere wamnthaka ndi mbewu pamsika pomwe thumba limodzi la feteleza panopo ndi cha pakati pa K22 000 ndi K23 000. Choncho, ndikufuna ndifunse boma kudzera kwa a Chiyembekeza kuti litiuze ndondomeko yomwe lakonza poonetsetsa kuti anthu akuthandizika pamene boma likugwiritsa mfundo yoti munthu yemwe wapindula chaka chino asadzapindulenso chaka chinacho.
2
Mafumu ayamikira kuyamba kwa ziphaso Mafumu mdziko muno ati kuyamba kwa ntchito yopanga ndi kupereka ziphaso zosonyeza unzika, ndi chiyambi chopititsa patsogolo ntchito za chitukuko zosiyanasiyana kaamba koti ndi njira imodzi yotsekera manga a katangale. Dzana Lachinayi, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adatsegulira ntchitoyi mumzinda wa Lilongwe ndipo pomva maganizo a mafumu, Tamvani idapeza kuti ntchitoyi ikomera mtundu wa Amalawi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kachindamoto: Tikuyamika Mwa zina, mafumu adati zitupazi zithandiza kuti mchitidwe woba mankhwala mzipatala, kutulutsa ndi kulowetsa katundu mwachinyengo, kuthithikana mmisika ndi maukwati osalongosoka zichepe. Timadandaula usana ndi usiku, chaka ndi chaka kuti mankhwala samalimba mchipatala cha Dedza. Si kuchipatala kokha, ayi, komanso ku Admarc kokagula chimanga ndi kuthithikana mmisika chifukwa chosazindikirana. Ambiri mwa anthu omwe amapindula ndi ochoka kunja kaamba koti pozindikira kuti akuchita zachinyengo, amalawirira nkukakhala oyambirira kulandira thandizo. Amalawi akamabwera amapeza mankhwala atha, malo mumsika atha ngakhalenso chimanga chimene ku Admarc chatha, idatero mfumu yayikulu Kachindamoto ya mboma la Dedza Lachinayi. Mfumu yaikulu Mlauli ya ku Neno, komwe ndi kufupi ndi malire a Malawi ndi Mozambique kudzera ku Mwanza, idati mafumu kumeneko adali pachipsinjo chachikulu pankhani yokhudza milandu ya malo kaamba kamaukwati osadziwika bwino. Anthu amangochoka uko nkudzafunsira mkazi kuno ndiye poti padalibe zitupa, kumakhala kovuta kuwazindikira bola akangodziwako midzi ingapo nkumanamizira kuti amachokera kumeneko. Mapeto pake banja likavuta zimavuta kuweruza kwake ndipo akudza amapezeka kuti alanda malo, adatero Mlauli. Inkosi Khosolo, ya mboma la Mzimba, idati chitupa nchitetezo choyamba kwa munthu kaamba poti kulikonse angapite, anthu amatha kumuzindikira. Timachitira pangozi kapena munthu ukasowa kumene, ukakhala ndi chitupa, anthu amakuzindikira msanga nkukuthandiza, adatero Khosolo.
8
Mangochi Defiler Gets 14 Years IHL By Thokozani Chapola 022.jpg 413w" sizes="(max-width: 518px) 100vw, 518px" /> Senior Resident Magistrate court sitting in Mangochi has convicted and sentenced Asedi Makoloni to 14 years imprisonment with hard labour for defiling a girl under the age of 16 years contrary to section 138(1) of the penal code. State Prosecutor Sub Inspector Emmanuel Kambwiri told the court that from April to June, 2019, at Nombo village, in Traditional Authority Jalasi in Mangochi district, the convict who is a neighbour to the mother of the girl defiled her several times in her bedroom during night time when her mother leaves the house to attend night prayers or funeral ceremony. It came to light when the mother discovered that her daughter has missed menstruation. Upon quizzed, the girl narrated the ordeal, said Kambwiri. The convict pleaded not guilty to the charge levelled against him. The state paraded three witnesses who testified against him beyond any reasonable doubt that made the court to find him quilty. In Mitigation, Makoloni asked for courts leniency because he believed that the girl was above 16 years but in submission, the state prayed for a stiff punishment, citing that as neighbours, the convict choose to defile the girl instead of taking a fatherly role of prorecting her. When passing the sentence, Senior Resident Magistrate Joshua Nkhono concurred with the state, hence, he slapped Makoloni to 14 years imprisonment with hard labour in order to deter would be offenders. Makoloni, 46, hails from Nombo village, Traditional Authority Jalasi in Mangochi district.
7
Nyaude: Tidadabwa ndi zochitika zake Akamaimba nyimbo ya Musalolere Mulungu Ephraim Zonda amaimba ndi mtima wonse polingalira kuti akulowa mbanja mwezi ukubwerawu ndipo Mulungu asalolere kuti adani alepheretse zimenezi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Atupele ndi Ephraim kukonzekera kudzakhala thupi limodzi Ngati kumaloto, Ephraim akamakumbukira tsiku lomwe adaonana ndi Atupele Chikaya. Akuti sadadziwe kuti iwo akhoza kudzakumananso. Ndidamuona koyamba Atupele ku tchalichi cha Zambezi ku Kawale komwe tinkakaimba. Panthawiyo sitidayankhulane koma mwachisomo cha Mulungu tidakumananso ku Chefa komwe tidakaimbanso, adatero Ephraim. Mnyamatayu ndi wachiwiri kubadwa mbanja la ana asanu ndi awiri. Ali ndi luso lopeka nyimbo komanso ali ndi mawu anthetemya moti amaimba mukwaya ya Great Angels. Si zokhazo, amachitanso bizinesi yogula ndi kugulitsa katundu wochokera ku China kuphatikizapo galimoto. Atupele ndi wachiwiri kubadwa mbanja la ana anayi ndipo amagwira ntchito ku Road Traffic ku Zomba. Awiriwa adayamba kucheza muchaka cha 2009 pomwe adakumana ndipo patatha chaka akucheza chomwecho Ephraim adamufunsira Atupele ataona kuti ndi mkazi wabwino. Atupele ndi mkazi amene ali ndi zomuyenereza zomwe mwamuna aliyense amafuna pa mkazi. Atu ndi mkazi wakhalidwe, woopa Mulungu, wanzeru komanso womvetsetsa, adatero Ephraim akunyadira bwezi lakelo. Patatha zaka zisanu ndi chimodzi chikumaniraneni, awiriwa adaganiza zomanga ukwati kuti anthu atsimikize za chikondi chawo. Ukwati wawo uliko pa 12 September chaka chino ndipo akadalitsira ku mpingo wa CCAP ku Area 23 mumzinda wa Lilongwe ndipo madyerero akakhala ku Capital Hotel. Ephraim adanenetsa kuti chomwe chidzawalekanitse iwo ndi imfa basi. Iye adati nthawi yawathandiza kudziwana, zomwe iye akuti zidzawathandiza mbanja mwawo.
15
Madzi siosewera nawo, maka nthawi yamvula Madzi ndi moyo, chifukwa amatithandiza mzambiri. Koma kupanda kusamala, madzi omwewo amadzetsa imfa. Imfa zina za ngozi zamadzi zikhoza kupewedwa. Mayi ali apayu adayenera kusamala chifukwa malo akuchapawo ndiwoopsa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Uwutu ndi mtsinje wa Maperera ku Chikhwawa ndipo kuopsa kwake sikuti kungadze pamene mvula yayamba kugwa pafupi ndi mayiyo. Mvulatu ikhoza kugwa yambiri kumtunda kwa mtsinjewu, mayiyo osadziwa, kenako kumukokolola limodzi ndi mwanayo. Kusamala nkofunika.
18
DPP yaima njiii! pa gawo 64, 65 Chipani cholamula cha DPP chagwirizana ndi zipani zotsutsa boma za MCP ndi PP kuti nkoyenera kutsata Gawo 65 la malamulo oyendetsera dziko lino limene limapereka mphamvu kwa sipikala kuchotsa phungu amene achoka chipani chimene adaimira kuti apambane pachisankho ndikulowa chipani china. Mlembi wamkulu wa chipanicho, Dr Jean Kalirani, adati chipanicho sichikuopa chilichonse kuti lamuloli ligwiritsidwe ntchito poti chikufuna kuti malamulo a dziko lino azitsatidwa mosayangana nkhope. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC DPP yakonzeka kuonetsa chitsanzo chabwino pokwaniritsa malamulo oyendetsera dziko lino. Ku Nyumba ya Malamulo, chipani chathu chikaonetsetsa kuti lamuloli ligwire ntchito. Tikufuna aphungu azikhala mzipani zimene zidawanyamula paphewa kuti akalowe kunyumbayo; sitikufuna khalidwe lomwe lakhalapo kwa nthawi yaitali lomwe aphungu amangosintha zipani momwe afunira, adatero Kalirani. Iye adati akuyembekeza kuti chipani chake, chimene padakali pano chili ndi aphungu 49 mwa 191 a kunyumbayo amene adalumbira pamipando yawo sabata ikuthayi. Chisankho chichitikanso mboma la Thyolo komwe Peter Mutharika, yemwe adapambana pa upulezidenti komanso ku Blantyre kumene yemwe amapikisana nawo adamwalira chisankho chisanachitike. Izi zikusonyeza kuti ngati sichingapeze aphungu ena, chipanichi chikhoza kukazunzika ku Nyumba ya Malamulo kuti zimene chikufuna kuti zidutse chifukwa pamafunika kuti aphungu 129 avomereze kuti zidutse. Mmbuyomu, aphungu ena a zipani zotsutsa boma akhala akukhamukira kuchipani cholamula. Ngakhale sipikala ali ndi mphamvu zochotsa aphungu otere, izi zakhala zikukanika malinga ndi ziletso zimene aphunguwo amatenga kukhoti. Zipani zolamula nazo zakhala zikuchita njomba pagawoli. Zipani za UDF, DPP komanso PP zidalephera kulondoloza za lamuloli. Ndipo Kalilani watinso chipanichi chikufuna kubwezeretsa Gawo 64 la malamulo oyendetsera dziko lino lomwe aphungu adalichotsa mchaka cha 1995. Gawoli, limanena kuti ngati anthu oposa theka la anthu amene adavota nawo pachisankho cha phungu asainira chikalata chimene mmodzi mwa ovotawo apempha bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) kuchotsa phunguyo, sipikala wa nyumbayo apatsidwe mphamvu zochotsa phunguyo potsatira ndondomeko za ku Nyumba ya Malamulo. Koma Kalirani adati chipanichi chitulutsa chitulutsa chikalata cha ndondomeko zomwe chitsate kuti mabilo asakavute kudutsa ku Nyumba ya Malamulo. Tsatanetsatane wa momwe tikwaniritsire izi titulutsa posachedwapa. Padakalipano Amalawi adziwe kuti izi ndi zomwe tikufuna koma momwe tichitire izi, iwo ayembekezere ndondomeko yomwe chipani cha DPP chitulutse, adatero Kalirani. Iye adatinso akuyembekezera kuti aphungu adzaika zofuna za ovota patsogolo kotero ngati kugwiritsa ntchito malamulo awiriwa zili zomwe ovotawo akufuna, aphungu akuyenera kudzakhala patsogolo kukwaniritsa izi posayangana chipani chomwe akuchokera. Katsiwiri pandale Dr Mustafa Hussein wa kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College ku Zomba adati ngati chipani cha DPP chingachitedi zomwe chalonjezazi, demokalase ya dziko lino ipita patsogolo poti khalidwe la aphungu losintha zipani ngati zovala litha. Ngati Gawo 65 la malamulo a dziko linoli lingatsatidwe, iyi ikhala nkhani yabwino kwambiri pankhani ya demokalase. Lamuloli lichititsa kuti phungu aliyense azikhala mchipani chomwe chidamutengera mNyumba ya Malamulo, adatero Hussein. Katswiri pandaleyu adatinso lamuloli lichititsa kuti ovota akhale okhutira nyumbayo chifukwa phungu wawo azikhala kumbali yomwe iwo adamutumiza. Pankhani ya Gawo 64, Hussein adati lamuloli lidzafumbatitsa mphamvu anthu ovota chifukwa azidzatha kuchotsa phungu yemwe sakuchita zomwe anthuwo adamuikira pampando. Ngati lamuloli lithekedi kubwereranso nkuyamba kugwiritsidwa ntchito zidzathandiza anthu ovota kukhala ndi mphamvu zomwe padakalipano alibe. Kwa nthawi yayitali anthu ovota akhala akugwiritsidwa fuwa lamoto pomwe phungu yemwe adamuvotera amawakhumudwitsa koma iwo samatha kumuchotsa kuti asankhe wina. Ovotawo amadikira kuti mpaka pathe zaka zisanu kuti adzakhalenso ndi chisankho, adatero Hussein. Koma Hussein adati Amalawi akuyenera kuchenjera ndi osamala pomwe akubweretsanso Gawo 64 poti likhoza kubweretsa mpungwepungwe pa ndale. Iye adati anthu ena akhoza kumatengerapo mwayi pa lamuloli nkuyamba kuipitsa kagwiridwe ka ntchito ka phungu ndi cholinga chakuti achotsedwe chonsecho mumtima mwawo akufunanso mpandowo. Ku Nyumba ya Malamulo, aphungu oima pawokha ndiwo ali ambiri. Iwo alipo 52 pomwe chipani cha DPP chili ndi aphungu 49. Chipani cha Malawi Congress (MCP) chidapeza aphungu 48 pomwe chipani cha Peoples (PP) chili ndi aphungu 26. Chipani cha United Democratic Front chidapeza aphungu 14. Kawirikawiri aphungu oyima pawokha ndiwo amakhala patsogolo kulowa zipani zina makamaka chipani cholamula.
11
Zidayambira mmalingaliro Mwina tinganene kuti kulimbikira ntchito ndiko kudapangitsa kuti malingaliro omwe Steve Chimenya wa ku Zomba adali nawo asanduke zenizeni ndi kubweretsa chimwemwe mmoyo mwake. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mnyamatayu akuti amati akakhala payekha, mmutu mwake munkabwera chithunzithunzi cha msungwana yemwe adali asadamuoneko nkale lonse kufikira mchaka cha 2014 pomwe tsiku lina kuofesi yake kudatulukira msungwana wofanana ndi wa mmalingaliro akewo. Chimenya ndi nthiti yake patsiku laukwati wawo Rachel Jeremiah Sato wa ku Ntcheu yemwe akuti amagwira ntchito kunyumba ya boma adatumidwa kukagwira ntchito komwe Steve ankagwira ntchito ndipo uku nkomwe zonse zidayambira. Nditamuona, ndidadzimenya mmutumu kuganiza kuti kapena malingaliro aja andipezanso nthawi ya ntchito. Kenako ndidamuona akulowa muofesi yanga ndipo ndidakhulupirira kuti sadali malingaliro chabe. Ndidamupatsa moni, iye nkuyankha, adatero Steve. Iye akuti tsikulo adaweruka mosiyana ndi masiku onse moti olo anthu okumana naye tsikulo ankadabwa ndi nkhope yowala yomwe adali nayo. Iye akuti chiyambi cha chikondi chawo chidali chomwecho mpaka pa 26 September 2015 adachita chinkhoswe kumudzi kwawo kwa Rachel ku Ntcheu ndipo pa 14 November 2015 lidali tsiku la ukwati woyera womwe madyerero ake adachitikira ku Capital Hotel ku Lilongwe. Rachel akuti iye atangomuona Steve chinthu chidamugunda mumtima ndipo patapita masiku angapo pomwe Steve ankamuuza za chikondi, mumtima mwake adali atamukonda kale ngakhale kuti panthawi yomwe ankangocheza iye sankaonetsera.
10
Anthu 6 Atsopano Apezeka ndi Coronavirus, Mmodzi Wamwalira Nambala ya anthu omwe apezeka ndi kachilombo ka Coronavirus akuti yafika 23 potsatira kupezekanso kwa anthu ena asanu ndi mmodzi (6) ndi kachilomboka mdziko muno. Walengeza za nkhaniyi-Namarika Mlembi wa mkulu mu unduna wa za umoyo Dr. Dan Namarika watsimikiza za nkhaniyi pa msokhano wa atolankhani mu mdzinda wa Blantyre ndipo wati awiri mwa anthu-wa afika kumene mdziko muno, kuchokera maiko akunja. Padakalipano undunawu walengezanso kuti mmodzi mwa anthu atsopano omwe anapezeka ndi nthendayi mu mzinda wa Lilongwe wamwalira. Undunawu wati malemuyu analinso ndi mavuto ena a zaumoyo. Zimenezi zikutanthauza kuti chiwerengero cha anthu amene apezeka ndi kachilomboka mdziko muno tsopano chakwera kuchoka ka 17 ndi kufika pa 23, pomwe atatu mwa iwo amwalira, ndipo atatu enanso anachira.
6
Olephera asatuluke DPPMutharika EMMANUEL MUWAMBAYemwe anali mtsogoleri wogwirizira mpando wa pulezidenti wa chipani cha DPP, Peter Mutharika, Lachinayi adalangiza omwe amapikisana nawo pofuna mipando yosiyanasiyana kuti akalephera si bwino kuchoka mchipanicho. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Patsikulo, chipanicho chidali ndi msonkhano waukulu ku Comesa Hall mumzinda wa Blantyre ndipo anthu oposa 80 amalimbirana mipando yosiyanasiyana, kuphatikizapo wa pulezidenti, umene Mutharika amapikisana ndi sipikala wa Nyumba ya Malamulo Henry Chimunthu Banda. Malinga ndi Mutharika, pampikisano ulionse pamakhala wopambana komanso wolephera choncho adapempha olephera kuti asachoke mchipanicho ndi kuchithandiza kuti chidzapambane pachisankho cha chaka chamawa. Musatuluke mchipani. Tiyeni tigwire ntchito limodzi kuti tilowenso mboma, adatero Mutharika. Mutharika adakhala akugwirizira mpandowu kuchokera pomwe mkulu wake Bingu, yemwenso anali mtsogoleri wa dziko lino, adatisiya pa 5 April chaka chatha. Mutharika adati msonkhano waukuluwo udali mwayi kuchipanicho kuti chipite patsogolo. Ndi anzanga ku DPP, takonzeka kuti tilowenso mboma. Chachikulu ndi umodzi, adatero Mutharika. Uwu unali msonkhano woyamba wa chipanichi, chimene adachikhazikitsa mu 2005, Bingu atatuluka mchipani chomwe adaimira pachisankho cha 2004 cha UDF. Mmbuyomu, chipanichi chimangosankha atsogoleri. Malinga ndi wapampando wa msonkhanowo, Nicholas Dausi, pakutha pa msonkhanowo sipakuyenera kudza kugawanikana.
11
Tikulumirabe ana chakudya? Masiku ano pomwe matenda a Edzi afala mwa nkhani nkhani pakufunika kuonetsetsa komanso kusintha zinthu zina zomwe anthu timachita makamaka mokhudzana ndi ana. Mwachitsanzo, anthu tili ndi chizolowezi chosendera nzimbe ana. Akakhala ana oti mano akungoyamba kumera, tikasenda nzimbe inja timailumalumanso kuti isamuvute kutafuna. Kuonjezera apo, timakondanso kuwalumira ana chakudya china ngati mango, magwafa ndi zina zotero. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi sitimangochitira ana athu komanso a abale, anzathu ndi enanso oti tangokumana nawo. Zikuchitika izi tsiku ndi tsiku. Koma tikamachita izi ambiri sitilingalirapo kuti kodi mthupi mwathu muli bwanji pa nkhani ya matenda omwe tingathe kufalitsa kwa anawa kudzera mumate komanso magazi omwe nthawi zina amatha kutsalira pa chakudya chomwe mwana wapatsidwa. Ambiri timangoti bola tamuthandiza mwana olilira chakudyayo. Ngakhale matenda a Edzi amafalikira kwambiri mnjira yogonana, nthawi zina anthu timayiwala kuti mkamwa mukhonzanso kudzera matendawa makamaka ngati anthu ogawana chakudyachi ali ndi zilonda mkwamwa. Nzimbe ndi chimodzi mwa chakudya chomwe nthawi zina chimachekacheka mkamwa choncho nkosavuta kuti mabalawa atulutse magazi omwe akhonza kukumana ndi magazi a mkamwa mwa mwana ngati mwanayonso atadzicheka kapenanso ngati ali ndi bala nkamwa. Pambali pa matenda a Edzi, palinso matenda ena ngati chiseyeye omwe munthu ungathe kumpatsira mwana kupyolera mchankudya chomwe wamulumira. Anawa a msinkhu ogairidwa chakudya motere kapena kusenderedwa nzimbe sadziwa kuti kunja kuno kuli matenda amtunduwu. Sangadziwe kuopsa kwa matendawa kapena kuti angawapewe bwanji. Choncho nkoyenera kuti ife amene tikudziwa za izi titengepo gawo lalikulu poteteza miyoyo ya anayi posaiika pachiopsezo chotenga kachirombo ka Edzi munjira zogairana chakudya poyesetsa kuti tigwiritse ntchito zida ngati mpeni mmalo mwa mano. Ngakhale mauthenga ali ponseponse kuti tikayezetse magazi, si tonse tidayezetsa nkudziwa kuti tili ndi kachilombo kapena ayi. Choncho ndi bwino kungokhala wanthumazi ndi osamalitsa makamaka poonetsetsa kuti moyo wa ana osazindikira zinthu ukutetezedwa ku nthenda zomwe zingathe kupeweka potsata njira zabwino zogawirana chakudya.
10