Text
stringlengths
292
6.6k
labels
int64
0
19
Akhristu 100 Alandira Ulimbitso ku Parish ya Mpiri Wolemba: Sylvester Kasitomu Akhristu amene alandira sacrament la ulimbitso mparish ya St. Marys mu dinale ya Mpiri mu Dayosizi ya Mangochi awapempha kuti agwilitse bwino ntchito mphatso zimene Mulungu mzimu woyera amapereka. Mkulu wa kuofesi yoona za utumiki mu dayosiziyi bambo Medrick Mlava alankhula izi pambuyo popereka sacrament la Ulimbitso kwa akhristu a mparishiyi. Iwo ati akhristu omwe alandira sacramenti-li akuyenera kumalimbikitsa ntchito zabwino kamba koti ndi zimene zikakondweletsa Mulungu. Pamene alandila sacrament la ulimbitso amakhala ngati alandira mangolomera komanso mphatso za mzimu woyera ndiye akuyenera kugwiritsa ntchito mphatsozi mu mpingowu pokhala ansembe asisiteri komanso akhristu eni ake olimbika, anatero bambo Mlava. Akhristu omwe alandira sacrament la ulimbitso patsikuli anali okwana 100.
13
Parishi ya Chirimba Ikufuna Kukhala ya Chitsanzo Wolemba: Thokozani Chapola Akhristu a mparish ya St. Martin Chirimba mu arch-diocese ya Blantyre ati ali ndi maso mphenya ati kutsogoloku akhale imodzi mwa parish ya chitsanzo pa nkhani ya umodzi pa ntchito za chitukuko. Wapampando wa parishi-yi Peter Mzolima ndi yemwe wanena izi lamulungu polankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre. Iye wati pempho lomwe mpingo unapereka kwa akhristu pa nkhani za chitukuko, lathandiza akhristu a mparishi-yi kumvetsa bwino za udindo osamalira atumiki awo komanso akhristu anzawo. Pa ntchito za chitukuko za pano oyambiira kupatsidwa ndi akhristu athu omwe akudziwa bwino za ntchito imeneyo. Timakhulupilira kuti mkhristu wathu tikamuthandiza pomupatsa chochita, athandizika ku banja kwake komanso abwera athandiza popereka mtulo wake komanso chopereka cha lamulungu lililonse, anatero a Mzolima. Iwo ati zimenezi zikuthandiza kuti ntchito zogwiridwa pa parishiyi zikukhala zamakono zomwenso zikuthandiza mpingo kupita patsogolo. ansembe athu akugwira ntchito yotamandika posamalira akhristu ndipo ifenso tikufuna kuwathandiza.
13
Papa Wati Wafetsa Mbeu Ya Mtendere Ku Africa Wolemba: Sylvester Kasitomu .mw/wp-content/uploads/2019/09/pp.jpg" alt="" width="605" height="342" />Papa pa ulendo wake wa mu Africa Mtsogoleri wa Mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati ulendo wake wodzacheza mmaiko a ku Africa unali wodzafetsa mbeu ya mtendere komanso chiyembekezo kwa anthu ammaikowa. Papa amayankhula izi kwa anthu omwe anasonkhana pa bwalo la Saint Peters Square kulikulu la Mpingowu ku VATICAN. Iye wati ulendo wodzacheza mmaiko a mu Africa walimbikitsa umodzi pakati pa atsogoleri a mpingowu komanso a dziko. Pamenepa papa anati ulendowu wapinduliranso achinyamata kaamba koti iwo ndi amene ali ndi kuthekera kothandizapo pantchito yotukula maiko awo komanso mpingo maka pokhala ndi mtima otumikira Mulungu kwathunthu. Mwazina paa anapempha akhristu mmaiko a Mozambique, Madagascar ndi Mauritius kuti mbeu imene wabyzala ibereke zipatso zokomera anthu a mmaikowa komanso mpingo wonse.
14
Aphungu avuta Tsikulo pa Wenela padali ziii! Moti ojiya, osolola ndi osenza onse adali khumakhuma. Ndalamatu, ndalama zalowa ku silent ndiye anthu sakuyenda. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Basi ya Lilongwe imatenga tsiku lonse kuti idzadze. Ambirinso amachita kunenerera. Nchifukwa chake ndidangoganiza zolowera malo aja timakonda pa Wenela. Ndidakapeza Abiti Patuma ndi Gervazzio akumvera nyimbo ya Lucius. Poti sitima, imaphweka akamayendetsa wina. Sindikudziwa kuti nyimboyo adaika chifukwa chiyani! Abiti Patuma adali bize pafoni yake. Koma abale, phungu uyunso ndiye amangokhalira pa Facebook. Taonani lero akuti iye sakufuna kukwezeredwa ndalama. Ndidakuuzani kale kuti uyu wokonda kuvina kanindoyu amangofuna kuti anthu azimumvera. Mwaiwala zija ankanena zolodza azungu osakaza la Mulanje phiri; mwamuiwala kuti ngwanthabwala basi? adatero Abiti Patuma. Zoona. Chomwe ndikudabwa nchakuti kodi bwanji phunguyu akutokota pa Facebook mmalo mwa pagulu la aphungu anzake? Ndikuona ngati nzeru zikumuchepera kapena Chingerezi ndiye vuto kwa regisrator (sic) ameneyu, adayankhira Gervazzio. Abale anzanga, kunena zoona wamisala adaona nkhondo. Vuto limakhala lakuti iye sadathawe, adakhala limodzi ndi anthu ena mmudzimo. Iyetu adafera limodzi ndi ena onse. Kodi iyeyo ngakhale akulankhula pa Facebook kuti anthu amutamandire, malipiro atakwezedwa iyeyo angakane? Chiphimbammaso ichi basi, ndidailowerera. Koma zonse zili apo, aphunguwa akutionjeza pano pa Wenela. Ndalamatu zalowa ku silent ndiye wina azifuna mamiliyoni pamwamba pa mamiliyoni anzake. Ndiye ndinamva wina akunena kuti amalandira zosaposa K250 000. Bodza inu! Momwe anthu awa amayendera, kumalandira maalawansi ochuluka aziti akulandira zochepa? Anthu awa Mulungu adzachititse nthaka iwameze tsiku lina, adatero Abiti Patuma. Usiku wa tsikulo ndidalota maloto odabwitsa. Ndidalota nditapita ku Nyumba ya Malamulo ngati mlendo wa phungu wathu pa Wenela, Mr Water Bouncer, mzungu wathu. Kutuloko ndidaona kuti nyumbayo idapita patsogolo kwambiri. Adali kulankhula ndi phungu wina amene adakhalapo msirikali woimba mabatcha. Indetu ndinena ndi inu aphungu anzanga. Dziko lafika pena. Tatukuka. Onani tili ndi ma tablet, ma laptop, mafoni a touch ndi zida zina koma tikulephera kuzigwiritsa bwino ntchito. Kulibe Wi-fi, adali kutero mkulu wathupi lakeyo. Musandifunse kuti Wi-fi nchiyani chifukwa sindingakuuzeni. Nanga ndichite kukuuzani kuti ndi njira imene anthu angalumikizire makina ndi mafoni awo ku Internet popanda chingwe? Ndimayesatu tsitsi la mbuu ndi mgodi wa nzeru, koma apa zikuoneka ndi zina. Mukalandira ndalama zankhaninkhani tsono mukufunanso Internet yaulere? Mmalo moti mumenyere ufulu kuti Internet ikhale yaulere kwa ana asukulu! Mubwereratu koimba mabatcha kuusirikali, adamuyankha phungu wina. Ndidadzidzimuka.
11
Mtambo Wati MEC Ikhazikitse Ndondomeko Zabwino Mtsogoleri wa gulu la ndale la Citizens for Transformation (CFT), Timothy Mtambo wati pakuyenera kukhala ndondomeko zabwino pa chisankho chomwe chikhudzachi kuti onse omwe akutenga nawo gawo adzakhutire ndi zotsatira zake. Iye amalankhula izi pa msonkhano wa atolankhani lachiwiri ku Lilongwe pomwe anatsindika pa zakufunika kwa chisankho chomwe chikudzachi. Mtambo: Mkulu wa NRB atule pansi udindo Mtambo wati mwachitsanzo, ndondomeko zina zomwe bungwe loyendetsa chisankho la MEC lidagwiritsa ntchito poponya chisankho cha chaka chatha zikuyenera kusinthidwa kuti pakhale njira zatsopano zomwe ati zitha kuthandiza kuti pasakhale zokayikitsa. Pamenepa a Mtambo ati ndizokhumudwitsa kuti pakhala pali mphekesera zoti ana achichepere akulembetsedwa mu kaundula wa bungwe la NRB ndi cholinga chofuna kubera chisankhochi ndipo wati mkulu wabungweli a Mackford Somanje atule pansi udindo wawo. Mkulu wa NRB atule pansi udindo chifukwa cholinga chawo ndi chosokoneza chisankho osati kuthandiza a Malawi ndipo tikupempha kuti njira zomwe zakhazikitsidwa zikonzedwenso, anatero Mtambo. Iye anawonjezera ponena kuti chisankho chomwe chikudzachi sicheyenda bwino pokhapokha makomishonala a bungwe la MEC atule pansi maudindo awo.
11
Aphungu apane boma posakaza chuma Pamene aphungu a ku Nyumba ya Malamulo ayambe kukumana pa 8, mkulu wa bungwe loona zachilungamo pachuma la Malawi Economics Justice Network (Mejn), mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Cunsumers Association of Malawi (Cama) komanso andale ena ati aphungu akuyenera akapane boma potsotsomola misonkho ya Amalawi mmiyezi isanu yokha. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iwo ati Amalawi akufuna amvetsere mwachidwi momwe boma lakombezera misonkhoyo pomwe eni ake ali pamoto ndikukwera mitengo kwa zinthu komwe kudadza ndikugwa kwa ndalama ya kwacha komanso mfundo zina za boma. Mawuwa akudza pomwe kwadziwika kuti mmaunduna ambiri agugudiza kale ndalama zomwe adapatsidwa mndondomeko ya zachuma ya 2012/2013 yomwe idzathe pa 30 Juni chaka chino. Boma lakhala likunena kuti zinthu zina zasokonekera chifukwa cha kugwa mphamvu kwa ndalama ya kwacha. Komanso akhala akunena kuti izi zikafotokozeredwa ku Nyumba ya Malamulo pomwe aphungu akumane. Koma mbali zounikirazi, mkulu wa Mejn, Dalitso Kubalasa, yemwe adali nduna yazachuma mboma la UDF, Friday Jumbe ndi mneneri wa komiti ya zachuma mchipani cha MCP ku Nyumba ya Malamulo, Joseph Njobvuyalema ati boma lisatenge kugwa kwa kwacha ngati chophererera chifukwa bomali ndilo lidagwetsa kwacha kusonyeza kuti bwezi atapeza moponda. Kubalasa wati bungwe lake likuchitanso kafukufuku wa momwe bomali lagwiritsira misonkho ya anthu mnthawi imeneyi. Iye wati malipoti omwe akhala akumveka momwe bomali lagwiritsira misonkho ya anthu zikusonyeza kuti ndondomekoyi boma lasakaza kagwiritsiridwe ka ndalama. Zomwe tikupeza nkuti bomali laonjeza kagwiritsidwe ntchito ka misonkho ya Amalawi. Malipoti okhudza kulira kwa anthu, ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo, mavuto kuchipatala ndi momwe ndalama zikuyendera kubomako zikusonyeza kuti mwambiri mwaipa. Mnkhumano umenewu ukuyenera kupereka chiyembekezo kwa anthu chifukwa ikuchitika pomwe anthu akulira ndikukwera mtengo kwa zinthu. Aphungu apane boma pakusagwiritsira ntchito bwino ndalama mmaunduna, adatero Kubalasa. Mkulu wa bungwe la Cama, John Kapito wati kunyumbako kusakangokhala kupana bomali komanso kukhazikitsa malamulo oti boma likasakaza misonkho padzikhala chilango. Iye adati boma likuyenera kukhala loona mtima pofotokozera Amalawi momwe lagwiritsira ndalama za mndondomeko yazachumayi. Zinthu zayipa, kuchipatala sikuli bwino, misawu yakumbika ngati mosewerera bawo, kusukulunso kwavuta pomwe ndalama zagwira ntchito. Pakuyenera kukhala chilango chokhwima ku boma ngati lachita motere ndipo izi zingakonzedwe ndi aphunguwa, adatero Kapito yemwe adati bungwe lawo likuyembekeza momwe ku Nyumbayo zikakhalire. Jumbe yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha New Labour wati lamulo la Nyumba ya Malamulo ndikuunikira momwe ndondomekoyi yayendera ndiye aphungu akayemebekezere kuti boma lifotokoze bwino. Nduna zokhudzidwa zikuyenera kukafotokoza chomwe chachitika kuti zifike pamenepa, adatero Jumbe. Njobvuyalema adati chipani cha MCP chakonzeka kukapana boma. Iye adati afunsa lipoti ku Unduna wa Zachuma momwe zinthu zayendera. Tikumva kuti pafupifupi unduna uliwonse wagwiritsira ntchito ndalama mosakaza, izi tikafunsa, adatero Njobvuyalema. Mwachitsanzo, ku nyumba ya chifumu kudalowa K1.8 biliyoni kuti agwiritsire ntchito koma pofika Disembala chaka chatha nkuti ndalama zoposa K2.6 biliyoni zitaphwasulidwa kale. Mmaulendo a mtsogoleri wa dziko lino komanso omuyandikira, kudaperekedwa K1.24 biliyoni koma ndalamayo idatha ndipo pakutha pa miyezi isanu nkuti ndalama zoposa K2.3 biliyoni zitagwiritsidwa ntchito. Padakali pano sukulu zina za ukachenjede zaboma zikutseka zipata zake ndi zina zili pachiopsezo chotsatira chifukwa choti boma likuuma manja kupereka thandizo lokwanira. Ndalama zomwe zidatumizidwa msukulumo zatha ndipo kuli ngongole ya K1.6 biliyoni. Sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University (Mzuni) yatumiza kumudzi ophunzira onse. Nayo sukulu ya madotolo ya College of Medicine idatseka zipata zake. Ku Chancellor College (Chanco) kudatumizidwa K4.808 biliyoni mndondomeko yazachuma koma kufika lero ndalamayo idatha ndipo kuli ngongole ya K879 miliyoni. Ku Kamuzu Collage of Nursing kudapita K1.6 biliyoni koma kufika pano ndalamayo yatha kale ndipo kuli ngongole ya K191.3 miliyoni. Kuchipatala nako kuli moto. K4.5 biliyoni ndiyo idapita kuti agulire mankhwala koma pano mzipatala mulibe mankhwala ndipo anthu ali pamoto. Kufika lero K2.1 biliyoni yatha. Ku ndondomeko yazipangizo zotsika mtengo nayo yakungana ndi mavuto chifukwa alimi ambiri akudandaula kuti sadagule feteleza wotsika mtengo. Undunawo udalandira K40.6 biliyoni kuti igulire matani 150 000 afetelezayo. Izi zidapereka chiyembekezo kwa alimi chifukwa nambala ya opindula idakwera kuchoka pa 1.4 kufika pa 1.5 miliyoni koma kulira sikukutha. Tidayesetsa kulankhula ndi nduna ya zachuma, Ken Lipenga yemwe samayankha foni yake. Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda pomwe amagwetsa mphamvu ya kwacha adauza Amalawi kuti timange malamba ponena kuti mavuto afika pamwana wakana phala. Msonkhano wa aphunguwu ndiwokaunguza momwe ndondomeko ya zachuma ya 2012/2013 yayendera.
11
Kulimbana ndi alaliki Ndidakhala pa Wenela tsikulo kubwira mpweya, uku ndikuitanira basi. Ndirande iyi! Machinjiri iyo! Ntcheu-Balaka cha uko!!! ndidali kutero. Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Pajatu masiku ena ndikati ndilowe three engine, kuitanira basi zitatu nthawi imodzi zimatheka. Ya Ntcheu-Balaka ija itadzaza, ndidapita ndikatenge zanga. Kaya ikafika ku Balaka ndilibe nazo ntchito. Ngakhale itapezeka kuti pofika pa Mdeka mwangotsala anthu atatu, zingandikhudze? Nditafika uko ndidapeza munthu wa Mulungu akulalikira, keupempherera apaulendo kuti ayende bwino. Ndikunena pano ziwanda za pamsewu zakonzeka kukulikhani. Ziwanda za pa Linthipe zakonzeka kumwa magazi anu ngati simutetezedwa. Inde ziwanda zochoka pansi pa madzi zikusautsani ngati simulapa, adali kutero mlaliki. Abale anzanga, ulaliki wamtundu wanji uwu wokhala ngati amalankhula nazo ziwanda? Kodi mlaliki ameneyu atati wakatumikira kuchipatala, sanganene kuti: Inu ochimwa inu! Lapani lero lino nditi lapana. Ngati simutero, zifuwa zanuzo zikutengerani kugahena. Kuchita kusaweruzika kwanuko, wa kumoto basi. Ndi mwayi omwe kuti utumiki wa kuchipatala udamusempha. Kodi sindinganene kuti akuopa kuti kuchipatalako sakatulukako ndi loboola ilo amapeza pano pa Wenela? Nkhani ya alaliki ili mkamwamkamwa ndi ya mlaliki Makala Funeral. Mumudziwa bwino woimba uja ankakamba za mfumu Betisezala ndi zolembalemba pakhoma. Tikumva kuti zinavutatu uko ku Mangalande. Mwachidule, zikumveka kuti mlaliki adacheza ndi mnzake wa Abiti Patuma wina pangongole ndiye lero nkhani yonse ili pa mbalambanda. Akungomulakwira mlaliki. Tikudziwa ankamwa, kusuta mpaka kugona mchimbudzi kalelo koma anali asanalape. Lero taonani nkhani zikuphulikazi! adatero Abiti Patuma titakhala malo aja timakonda pa Wenela madzulo a tsikulo. Apa nkuti akundionetsa zithunzi ndi mavidiyo pafoni yake akuonetsa chikondi cha mlaliki ndi uyu msangwana wa kwa Msamati. Nkhanizi zikumavuta kuyankhira. Kukhala ngati chiwanda choipa chalowa pamudzi pano. Taonani mudabweretsa za uyu wojambula mizimu, wopalasa mlengalenga, naye uyu wa matama ndi galimoto zake! Tsono mukutinso bwanji za mlaliki wathu wa ku Chilomoni? adafunsa Gervazzio. Musandifunse kuti nkhaniyi imayenda bwanji chifukwa nanenso sindikudziwa. Chomwe ndikudziwiratu nchakuti awa ndi masiku otsiriza ndipo kuyalutsa anthu a Mulungu ana a njoka ena akuchitenga cha fasho.
13
Achita zionetsero za kuthimathima kwa magetsi Anthu okhudzidwa a mu mzinda wa Lilongwe adachita ziwonetsero zosonyeza kukwiya kwawo ndi kuthimathima kwa magetsi mdziko muno. Cholinga cha ziwonetserozo chidali kukakamiza kampani yogulitsa magetsi Escom kuti ifotokoze, komanso kuthana ndi vuto la magetsi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Vuto la magetsi lafika posauzana moti anthu ena akukhala tsiku lathunthu opanda magetsi. Anthuwo, omwe adatsogoleredwa ndi mkulu wodziwika bwino pa nkhani yomenyera ufulu wa anthu Billy Mayaya, adakapereka chikalata kwa mkulu wa Escom wa mchigawo chapakati McVitty Chiphwanya. Anthuwo adanyamula zikwangwani zodzudzula mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti walephera kuthana ndi vuto la magetsi. Padakali pano mkulu wa kampani yopanga magetsi ya Egenco, William Liabunya, wati boma lagula ma generator kuchokera ku India omwe achepetse vuto la kuthimathima kwa magetsi mdziko muno. Ma generatorwo aikidwa ku Blantyre, Mulanje, Mangochi ndi ku Mzuzu ndipo akuyembekezereka kuyamba kufika mdziko muno kuyambira sabata ya mawa.
2
Akhristu ku Namitembo Awayamikira Kaamba Kothandiza Mpingo Wolemba: Sylvester Kasitomu Akhristu a mparish ya Namitembo mu Dayosizi ya Zomba awayamikira kaamba komvetsa bwino za udindo umene ali nawo pothandiza mpingo-wu modzidalira. Bambo mfumu a parish-yi bambo Henry Chiwaya ndi omwe anena izi polankhula ndi mntolankhani wathu. Iwo ati ndi momwe zinthu zikyendera mu parishi-yo zayamba kuonetsa kuti pano ntchito zotukula mpingo-wu zikuyenda bwino. Mwazina iwo ati monga parish yawo mbuyomu imatumikiridwa ndi ansembe achizungu zomwe zimapangitsa kuti akhristu ozungulira parishiyi kuphatikizapo malimana azikhla ndi ulesi othandiza mpingo maka popereka molowa manja zithu zothandizira parishiyi. Kale kunali kovuta kuti akhristu azitengapo mbali pa nkhani yothandiza mpingo kaamba koti parishi yathu imayendetsedwa ndi thandizo lochokera kwa ansembe achizungu koma pano mmene tawaphunzitsa njira za momwe angathandizire mpingo tikuona kuti akhristu akunvetsa bwino ndipo akuthandza monga kuperekela mphatso za ku nsembe ndi zina, anatero bambo Chiwaya. Parishiyi ili ndi malimana osaposera 75 ndipo kufika pano bambowa akwanitsa kuyendera limana lililonse paokhapokha kupereka maphunzirowa.
13
Kalonga: Waluso lothetsa makhalu Kunja kuno oimba ndiye mbwee koma luso lawo limakhala losiyanasiyana. Ena ali ndi mawu anthetemya, ena amaimba zipangiso monga zingwenyengwenye, saxophone, ngoma pomwe enanso luso lawo ndi kuthyola sitepe. Koma Innocent Kalonga amathetsa anthu mankhalu ndi luso lake-iye amatha kuimba chida chilichonse mbandi popanda vuto, komanso ndi katswiri pojambula nyimbo. CHIMWEMWE SEFASI adafatsa naye motere: Amatha kuyimba chida chilichonse: karonga Ndikudziwe Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina langa ndine Innocent Kalonga ndimakhala ku Chileka mumzinda wa Blantyre. Kodi Innocent Kalonga amatani pa Malawi pano? Inetu ndine katswiri wojambula nyimbo zamtundu wina uliwonse kumbali yojambula mawu komanso zithuzi za kanema ndipo ndimapezeka ku Chileka kuno ku Green Arts Studio komwe ndimakhala ndikujambula nyimbo. Zoti uli ndi luso lojambula udazindikira liti? Ndili ndi zaka 14. Nthawi yatchuthi ndinkakhala ndi chidwi chofuna kudziwa kuti nyimbo amajambula bwanji ndinso kwambiri ndinkakonda kumayesera pakompyuta. Apa mpamene ndidaona kuti zayamba kutheka ndipo padakalipano ndimatha kuimba chida chilichonse chogwiritsidwa ntchito ndi bandi. Kodi luso la zamaimbidwe pa Malawi likupita patsogolo? Kunena zoona mayimbidwe akupita patsogolo kwambiri moti panopa munthu sungakambe za luso osatchula magulu oimba nyimbo moti masiku ano tikuyenera kuvomereza kuti ku Malawi zoimbaimba zapita ndithu. Ndi magulu ati omwe wajambulirako nyimbo? Ndajambulako nyimbo za anthu monga Toza Matafale, Wailing Brothers, Limbani Banda ndi anthu ena ambiri, komanso nyimbo zonse zomwe ndidajambula ine palibe anadandaulako. Kupatula kuimba ndi kupeka nyimbo umapangaso chiyani? Ndimakonda kumvera nyimbo ndipo ndimasangalala kuti takhalapo kalambula bwalo wa oimba amene ndimawakonda.
0
Aphungu adzuma ndi kagawidwe ka makuponi Ganizo la boma loyamba kugawa makuponi ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo mupologalamu ya sabuside lalandilidwa ndi maganizo osiyanasiyana pakati pa aphungu a ku Nyumba ya Malamulo, mafumu ndi Amalawi ena. Kauniuni wa Tamvani wapeza kuti pomwe boma lili ndi maganizo oyamba kugawa makuponiwa mchigawo cha kummwera, anthu ali ndi maganizo ena makamaka polingalira kuti mvula ili pakhomo mzigawo zonse. Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Lachinayi lapitali mudali chisokonezo mNyumba ya Malamulo ku Lilongwe pomwe aphungu amafuna kuti boma lilongosole momveka bwino cholinga choyamba kugawa makuponi kummwera. Nkhani inakula mNyumba ya Malamulo ndi ya makuponi Phungu wa kumadzulo kwa boma la Mzimba Harry Mkandawire ndiye adatokosa nkhaniyi ponena kuti anthu a mboma lake akufunika makuponi ogulira zipangizo zaulimi msanga chifukwa mvula idagwa kale ndipo anthu akudikira kudzala. Nchifukwa chiyani mwasankha kuyambira kummwera pomwe mvula yayamba kale mmaboma ambiri mzigawo zonse? Pamenepa pali mafunso ambiri ofunika mulongosole bwino,adatero Mkandawire. adakhazikike, aphungu ambiri adaimirira pofuna kuonetsa kusakhutira kwawo ndi ganizoli mpaka nduna ya zachuma Goodall Gondwe, yemwe amayankha mmalo mwa nduna ya zamalimidwe, Allan Chiyembekeza, adavomereza kuti ndondomeko ya sabuside idalakwika. Gondwe adati ganizo loyamba kugawa makuponi ku mmwera lidadza polingalira kuti nthawi zambiri mvula imayambira mchigawochi pakudza. Si kuti pali mangawa alionse, ayi, koma monga tikudziwa, chaka ndi chaka mvula imayambira kummwera ikamabwera nchifukwa tidaganiza zoyambira kumeneko, adatero Gondwe. Yankholi silidagwire mtima aphunguwo ndipo adadzudzula boma chifukwa cholephera kukonzekera mokwanira mupologalamuyi. Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe omwe amakhudzidwa ndi nkhani za ulimi wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Tamani Nkhono-Mvula adati ngakhale kuti nchizolowezi kuyambira kummwera kugawa makuponi, chaka chino chokha ndondomeko ikadasintha. Iye adati boma lachedwa pachilichonse mundondomekoyi ndiye sipakufunika kutsatira za mmbuyo koma kupeza njira zomwe zingagwirizane ndi momwe zinthu zilili. Chiyambireni, boma silidakonzekere bwino ndondomekoyi. Pena pake tikhoza kuwamvetsetsa kuti pali mavuto a zachuma koma adadziwa kalekale zimenezi ndipo pano amayenera kukhala ndi njira, adatero Mvula. Iye adati chomwe boma likadachita nkuthamangitsa chilichonse kuti makuponi afikire mmadera onse kuti mvula ikamayamba alimi asadzazingwe nthawi yothaitha. Akuganiza bwanji poti nthawi yatha kale? Mavuto a zachuma ali apo, akadapanga zoti makuponi apezeke msanga ndipo anthu alandire mzigawo zonse msanga. Kunjaku kuli kale njala ndipo ngati sitisamala, chaka cha mawa kukhoza kudzakhala zovuta zenizeni chifukwa alimi ambiri amadalira sabuside ndipo mmadera momwe anthu amalima kwambiri, mvula idagwa kale koma sali ku mmwera, adatero Mvula. Paramount Chief Lundu wa mboma la Chikwawa adati mmadera ambiri mchigawo cha pakati mvula idagwa kale ndipo anthu akungoyembekeza kubzala. Iye adati kuchedwetsa makuponi kupangitsa kuti anthu adzalandire mochedwa zomwe zingachititse kuti mbewu zawo zidzasemphane ndi mvula monga momwe zidalili chaka chatha. Akadangoti tochepa tomweto agawe dziko lonse kuti mzigawo zonse anthu ena abzaleko osati mchigawo chimodzi chokha chifukwa sitikudziwanso kuti makuponi enawo afika liti ndipo adzafika angati, adatero Lundu. Paramount Chief Kyungu wa ku Karonga adati kwa iye nkhani yaikulu padakalipano ndi chakudya osati makuponi monga momwe anthu ena akunenera. Iye adati mvula sidanunkhire mmaboma ambiri mchigawochi ndiye palibe kanthu komwe angayambire chachikulu anthu apeze chakudya basi, adatero Kyungu. T/A Mkanda wa ku Mulanje adati iye ndi wokondwa kuti makuponi afika tsopano mdera lake ndipo akudikira kuti mvula ikagwa anthu akabzale mbewu mminda mwawo.
4
Chigamulo Chiperekedwa pa 3 February Bwalo la zamalamulo lalengeza kuti lipereka chigamulo chake pa nkhani yokhudza chisankho cha president, lolemba likudzali pa 3 February 2020. Malinga ndi chikalata chomwe chasainidwa ndi wachiwiri kwa Registrar wa mabwalo a milandu mdziko muno, chigamulochi chidzaperekedwa ku bwalo lalikulu la milandu la mu mzinda wa Lilongwe nthawi ya 9 koloko mmawa. Malipoti akusonyeza kuti bwaloli lidzapereka mpata woti mbali yomwe siyidzakhutitsidwa ndi chigamulochi idzakadandaule ku bwalo la Supreme. Mtsogoleri wa chipani cha UTM, Saulosi Chilima ndi mzake wa MCP, Lazarus Chakwera anakamangala ku bwalo la milandu ati potsutsana ndi zotsatira za chisankho cha president zomwe bungwe la MEC linalengeza kuti Peter Mutharika wa chipani cha DPP ndi amene anapambana.
11
Dziko la Scotland Layamikira Ubale Wake ndi Malawi Wolemba: Sylvester Kasitomu Mmodzi mwa akuluakulu oyanganira zitukuko za dziko lino mmaiko ena a Nicole Cogan lachinayi wayamikira ubale wabwino omwe ulipo pakati pa dziko la Scotland ndi dziko la Malawi. A Nicole Cogan amalankhula izi Lilongwe pa msonkhano wa pachaka wa bungwe la Malawi-Scotland Partnership MASP. Iye wati kudzera ku bungweli maiko awiriwa akupindula kwambiri pa zitukuko zomwe zikufikira anthu ochuluka komanso kulimbikirtsa ubale wabwino pakati pa maikowa. Polankhulapo modzi mwa akuluakulu kuunduna owona zachuma a Peter Simbani omwenso anali mlendo olemekezeka pa mwambowu anati boma ndi lokhutira ndi ntchito yabwino yomwe boma la Scotland likugwira mdziko muno maka pothandiza dziko lino kudzera mu bungwe la MASP. Kwa iwo amene akulandila ndalama kuchokera mdziko la scotiland akuyenera kukhala okhulupirika podziwa komanso kunena kuchuluka kwa ndalama zomwe zabwera kuno ku Malawi, antero Simbani. Mmawu ake mkulu wa board ya MASP mdziko muno Dr Annie Phoya anati ayaetsetsa kumagwiritsa bwino ntchito ndalama zomwe dziko lino likulandila kuchokera mdziko la Scotland pofuna kuti pasakhale kukaikiridwa kulikonse komanso kupitsa ubalewu patsogolo. Anthu amene alandila ndalalma kuchokera ku scotiland kuti agwirire ntchitoyi akuyigwira mwaukadaulo komanso mooneka kuti pasakhale katangale, anatero Dr. Phoya. Ubale wa maiko a Scotland ndi malawi wakhala ukulimbikitsidwa kuchokera pomwe Dr. David Livingstone anafika mdziko muno zaka 150 zapitazo.
14
Bambo Chikweya Alimbikitsa Bungwe la Abambo mu Mpingo Bambo Focus Chikweya, omwe ndi bambo mfumu a Parish ya mpingo wa katolika ya Mendulo mu arch-diocese ya Blantyre alangiza abambo mu mpingo wa katolika kuti agwirane manja potukula mpingo ndi luso lawo. Iwo amayankhula izi pa mwambo okhadzikitsa bungwe la abambo ku parishi-yo. Nthumwi za bungwe la Umodzi wa abambo zochokera mu arch-diocese ya Blantyre motsogozedwa ndi wapampando ogwirizira bungwe-li a Martin Chiwaya mogwirizana ndi abambo a ku Parish ya Nthawira ndi January, ndi omwe anakakhazikitsa bungwe-li . Poyankhulapo, wapampando wa Parish ya Mendulo a Freeson Tuwaga ati akukhulupilira kuti kubadwa kwa bungwe-li kupititsa patsogolo chitukuko cha parish yawo.
13
Malungo atheretuUnduna Pamene dziko limakumbukira ntchito yothana ndi malungo Lachiwiri, boma la Malawi lati likuyesetsa kuti malungo mdziko muno atheretu. Bungwe la zaumoyo pa dziko lonse la World Health Organisation (WHO) lidapatula 25 April chaka chilichonse kukhala tsiku lokumbukira nthendayi, imene imatengera kuli chete anthu ambiri, makamaka amayi oyembekezera ndi ana a mu Africa.aria Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndipo pamene mutu wa chaka chino Kuthetseratu Malungo ukukhudza dziko la Malawi kwambiri, WHO idalengeza kuti dziko lino, limodzi ndi Kenya komanso Ghana, akhala maiko oyamba padziko lapansi kulandira katemera wa malungo kuyambira chaka cha mawa. Woimira WHO pankhani yolimbana ndi malungo mdziko muno, Wilfred Dodoli adati ndondomeko ya katemerayu ndi yongoyesera chabe koma wati ali ndi chikhulupiliro kuti ndi wothandiza makamaka kwa ana. Uku nkubowoleza chinsinsi chothana ndi malungo. Tikuyembekezera kuti ana 120 000 a pakati pa miyezi isanu ndi 25 mmadera osankhidwa alandira katemerayu, adatero iye. Unduna wa zaumoyo wati katemerayu athandiza kuchepetsanso imfa zodza ndi malungo ndi pafupifupi 40 pa imfa 100 zomwe zimagwa pakati pa ana ndi chiyembekezo choti mtsogolo muno vutoli lidzatheratu. Undunawu watinso wakhazikitsa kafukufuku wofuna kupeza momwe vuto la malungo lilili mdziko muno pofuna kuonjezera mapologalamu ena oyenera kuti dziko la Malawi likwanitse cholinga cha mutu wa chaka chinowo. Mkulu woyanganira ntchito zaumoyo muunduna wa zaumoyo Dr Charles Mwansambo wati kafukufukuyu achitika mmadera osankhidwa ndipo achitidwa ndi madotolo omwe adaphunzitsidwa bwino ntchito ya zaumoyo makamaka zokhudzana ndi malungo. Kafukufukuyu akhudza kuunika kagwiritsidwe ntchito ka masikito otetezedwa, kaperekedwe ka thandizo la mankhwala a malungo, kuyeza malungo ndi kuchuluka kwa magazi mmatupi mwa ana omwe atenge nawo gawo mu kafukufukuyu, adatero Mwansambo. Mu uthenga wa tsiku lokumbukira matenda a malungo, unduna wa zaumoyo udati mzaka zisanu zapitazi, imfa zodza ndi malungo zachepa ndi 60 pa imfa 100 zomwe zinkachitika ndipo undunawu wati ichi nchifukwa cha kuyenda bwino kwa mapologalamuwa. Chifukwa cha mapologalamu monga kugawa masikito onyikidwa mmankhwala, kupopera mankhwala mmakomo ndi kulimbikitsa amayi oyembekezera kuyezetsa malungo ndi kulandira thandizo nthawi yabwino, imfa zodza ndi malungo zatsika, chidatero chikalatacho. Mkulu wa bungwe la zaumoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) George Jobe wati ndondomeko zomwe unduna wa zaumoyo uli nazo ndi zabwino. Iye adati njuga yagona pa momwe ndondomekozi zikuyendetsedwera ndi maphunziro a zaumoyo omwe anthu akulandira kuti azitha kutsatira bwino ndondomekozi kuti zipindule. Ndondomekozi nzabwino koma mpofunika kuunika kuti anthu akuphunzitsidwa mokwanira? Ndikunena izi polingalira zomwe zikuchitika mmaderamu kuti ena akugwiritsa ntchito masikito omwe amalandira powedzera nsomba ndi kupangira madimba, adatero Jobe. Senior Chief Mwadzama ya ku Nkhotakota idavomereza kuti pakadali vuto lalikulu pakati pa anthu kutsatira malangizo makamaka pakagwiritsidwe ntchito ka masikito a udzudzu ngakhale kuti pangonopangono anthu ayamba kumvetsetsa. Poyamba kudali zikhulupiliro zoti mankhwala a masikitowa amafowola anthu koma pano ambiri akumvetsetsa kufunika kogona mmasikito. Tidakhazikitsanso malamulo kuti opezeka akugwiritsa ntchito masikito powedzera nsomba kapena kupangira dimba, tizimulambalala pakabwera mapologalamu ena ndiye anthu akuwopa, adatero Mwadzama. Padakali pano, nduna ya zaumoyo Peter Kumpalume yati dziko lino lasayina pangano ndi dziko la China kuti akatswiri a ku China abwere kudzathandiza pakafukufuku wa mankhwala a zitsamba ochiza malungo. Mankhwalawo alipo ndipo timawagwiritsa ntchito, koma tikufuna kupeza kuti mankhwala omwe angagonjetse malungo ndi ati ndipo tingawakonze bwanji mmafakitale kuti akhale osavuta kugwiritsa ntchito, adatero Kumpalume Dziko la China lidagonjetsa kale malungo ndipo wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo ndi kulera mdzikolo Wang Guogiang adati izi zidatheka pogwiritsa ntchito mankhwala a zitsamba.
6
Za ukamberembere mu Fisp akuti zichepe chaka chino Ntchito yotumiza zipangizo zaulimi zotsika mtengo mupologalamu ya Farm Input Subsidy Programme (Fisp) ili mkati koma nyengo ngati iyi atambwali ofuna kulemera mnjira zachinyengo amachuluka. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Atambwali oterewa akuti amalowerera msika wa zipangizozi ndi njira zosiyanasiyana ndipo pamapeto pake zipangizozi zimakathera mmanja mwa anthu ochita bwino kale mmalo mwa anthu ovutika omwe ndi eni pologalamuyi. Apolisi, unduna wa malimidwe ndi bungwe la mgwirizano wa alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) ati chaka chino salekerera zachinye za mtundu uliwonse mupologalamuyi kuti anthu oyenerera okha ndiwo apindule. Alimi ena mchigawo cha kumwera monga awa ayamba kale kugula zipangizo zotsika mtengo Kumbali yathu, tilimbikitsa chitetezo potumiza apolisi ambiri mmadera ndi mmisika yomwe pologalamuyi ikuchitikira. Tigwira ntchitoyi kudzera mu nthambi yathu ya chitetezo cha mmudzi ndipo ndikunena pano takonzeka kale, adatero wachiwiri kwa wamkulu wa polisi mdziko muno Rodney Jose. Iye adati mmene pologalamuyi imayamba, boma lidapereka mphamvu zoyanganira chitetezo cha zipangizo zotsika mtengozi mmanja mwa apolisi ndipo amaigwira mogwirizana ndi unduna wa zamalimidwe ndi bungwe la alimi la FUM. Chiyambireni pologalamu iyi, tagwirapo akamberembere ambiri. Milandu yambiri imakhala yokhudzana ndi anthu kupezeka ndi makuponi achinyengo, ziphuphu ndi kuzembetsa zipangizozi ndi cholinga chokagulitsa kumaiko akunja, adatero Jose. Mlembi wamkulu muunduna wa zamalimidwe Erica Maganga adati ndi udindo wa mafumu ndi anthu awo kutsina khutu akuluakulu akaona mchitidwe wokayikitsa pakagawidwe, kagulitsidwe ndi kapezedwe ka zipangizozi. Maganga adati boma limaononga ndalama zambiri mupologalamu ya sabuside ncholinga chotukula alimi ovutika ndipo ngati zipangizozi sizikuwafikira ndiye kuti zolinga za boma sizikukwaniritsidwa. Anthu ndiwo amaona zomwe zimachitika mmadera mwawo ndiye iwo ndi amene angakhale oyambirira kukanena kuti akamberemberewo agwidwe ndipo zipangizo zawo zaulimi zipulumuke, adatero Maganga.
4
Nyanja ya Chilwa Ikuyika Pachiopsezo Boma la Zomba ku Coronavirus Boma la Zomba lili pa chiopsezo chokhudzidwa kwambiri ndi nthenda ya Covid-19 kaamba ka kusayezedwa kwa anthu omwe akulowa mdziko muno kudzera pa nyanja ya Chilwa mbomalo. Anthu akumadzera pa nyanjayi osayezedwa Izi zadziwika pamene nduna ya zamalamulo a Bright Msaka amayendera malo omwe boma la Zomba lakonza kuti lidzisungirako anthu omwe angapezeke ndi kachirombo ka Coronavirus komwe kamayambitsa nthendayi. Ndipo poyankhapo pankhaniyi, ndunayi yati boma likuyesetsa kuyeza anthu omwe akumalowa kudzera mzipata zonse za dziko lino ndipo ati boma lichitapo kanthu kuti anthu omwe akumadutsira pa njanjayi adziyezedwanso ngati ali ndi kachilomboka. Pozindikira kuti kuno ku eastern region kuli ma border omwe tikumayeza anthu onse olowa mdziko muno, koma kuno ku Chilwa kulibe malo oyezerawa ndipo anthuwa akulowa popanda chovuta, anatero a Msaka.
6
Khansala wa DPP Wapambana ku Liwawadzi Anthu okhala mdera la Liwawadzi dera la kumpoto kwa boma la Balaka msabatayi anaponya voti pofuna kusankha khansala wa deralo kutsatira imfa ya Thomson titani bwanali yemwe anali khansala wa deralo atasankhidwa pa chisankho cha pa 21 May 2019. Iye anamwalira mwezi wa October 2019. Potsatira izi bungwe la MEC lalengeza zotsatira za chisankho pomwe lati Pharaoh Kambiri yemwe amayimira chipani cha DPP ndi yemwe wapambana. Bungweli lati Liwawadzi Ward inali ndi anthu asanu ndi mmodzi omwe amapakisana ndipo anthu omwe analembetsa kuti adzapnya voti analipo 20,629 koma omwe anakaponyadi voti ndi okwana 4, 608 zomwe zikuyimira 22.34%. Mavoti osavomerezeka analipo 30 kuyimira 0.65%. A Precious Khwiyao Chimtengo, oyima pawokha anapeza mavoti 665, a Pharaoh Kambiri oyimira chipani cha Democratic Progressive (DPP) anapeza mavoti okwana 2,615. A Mervin Makwinja omwe amayimira chipani cha Freedom (FP) anapeza mavoti 101, a Haris Mhere omwe amayimira chipani cha Mbakuwaku Movement for Development (MMD) anapeza mavoti 28, a Ronald Pias Mphepo, omwe amayimira chipani cha Peoples (PP) anapeza mavoti okwana 537 ndipo a Obedi PETERomwe anali oyima pawokha anapeza mavoti 632.
11
Otsatira Tonse Alliance ku Zomba Achita Chikondwelero Atapambana Pa Chisankho Otsatira mgwirizano wa zipani za ndale wa Tonse mu mzinda wa Zomba, dzulo anachita chikondwelero kutsatira kupambana kwawo pa chisankho cha President. Chikondwelerochi chinayambira ku Chinamwali, kuzungulira mu mzinda wa Zomba ndi kukathera pa bwalo la zamasewero la Gymkhana. Poyankhula ndi atolankhani pambuyo pa chisangalarochi, mlembi wa amayi mchipani cha UTM, mayi Mwiza Malweni apempha achinyamata kuti akonde dziko lawo pothandidza pa ntchito za chitukuko zosiyanasiyana. Victory parade yathu ndi chisangalaro chosonyeza kuti tatenga boma tawina ndipo langizo langa ndi lakuti achinyamata tizitenga gawo pothandiza chitukuko cha mdziko osati kuwononga zinthu, anatero mayi Mwalweni. Mmawu ake mlembi wa chipani cha Malawi Congress (MCP) mchigawo chaku mmawa, a Geoffrey Banda anati uthenga omwe amapereka pa tsikuli ndi wa chisangalalo ndipo athokoza Mulungu ponena kuti zomwe amafuna zakwaniritsidwa. Ngati mgwirizano wa Tonse, chaka chino chakhala cha chisangalalo kuyambira pamene bwalo la milandu linagamula kuti kukhale chisankho ndipo chisankhocho chasonyeza kuti mavoti anaberedwadi ndipo lero tikusangalala chifukwa choti tawina, anatero a Banda.
11
Joyce Banda Wamema Anthu Aku Zomba Adzavotere Dr. Chakwera Mtsogoleri wakale wa dziko lino Dr. Joyce Banda wapempha anthu mdziko muno kuti akavotere mtsogoleri wa mgwirizano wa Tonse, Dr. Lazarus Chakwera pa chisankho chomwe chikudzachi. Mayi Banda anena izi lero pa msonkhano omwe anachititsa pa bwalo la zamasewero la Naisi mboma la Zomba. Banda: Tizapitiriza kumangira nyumba anthu ovutika Iwo ati mgwirizanowu uli ndi mfundo zabwino monga kulemba ntchito achinyamata ochuluka, kumangira nyumba anthu ovutikisitsa komanso kuthetsa njala, mwazina. Atsogoleri awiri onsewa agwirizana ndi nkhani imene ndimayikonda ine nkhani yomangira nyumba anthu ovutika, tizalembanso ntchito achinyamata oposa 1 million, anatero Dr. Banda. Ndipo polankhulapo pa msonkhano omwewu wachiwiri kwa president wa chipani cha UTM, Dr. Micheal Usi wapempha atsogoleri a zipani zina za ndale kuti aleke kugwiritsa ntchito zipembedzo pofuna kukopa anthu kuti awavotere. Chisankho ichi sitikukavotera a shehe kapena angaliba. Izi tikukasankha a tsogoleri oti ayendetse dziko lino osati zomwe ena akuganizazo, anatero Dr. Usi. Enanso mwa atsogoleri a Tonse Alliance omwe analankhula pa mwambowu ndi wachiwiri kwa president wa chipani cha Malawi Congress (MCP) Sidik Mia komanso mtsogoleri wag ulu la ndale la Citizens for Transformation (CFT) Timothy Mtambo omwenso anapempha anthu mdizko muno kuti adzavotere mgwirizano wa Tonse pa chisankho chomwe chikudzachi.
11
Cama ikuti zionetsero pa 17 Pamene nkhani yochita zionetsero pokwiya ndi utsogoleri wa Pulezidenti Joyce Banda mmene akuyendetsera dziko lino, ena mwa Amalawi otumikiridwa ati sakuona kuti kuyenda pamsewu kungakhale yankho la mavuto awo kotero ati sachita nawo ziwonetserozo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iwo apempha omwe akukonza ziwonetserowa kuti alole kukambirana ndi boma asadabwere ndi ganizo lochita zionetserozo. Koma mneneri wa gulu lomwe likukonza zionetserozo, Kingsley Mabalani, wati ngati boma linene kuti akambirane pamfundo zisanu ndi ziwiri (7) zomwe akuchitira zionetsero iwo sazengereza. Mabalani wati gulu lawo lalembera kale boma pamfundozo ndipo pofika Lachitatu lapitali nkuti boma lisadayankhe. Mfundo zomwe gululi likuchitira zionetsero ndi: kugwa kwa mphamvu ya kwacha; kuyendayenda kwa Mayi Banda; kuchuluka kwa nduna mmaunduna monga unduna wa zamaphunziro womwe ati uli ndi nduna zinayi; kufotokoza za katundu wake; ndi kulankhula kwa Pulezidenti komwe akuti kukugawanitsa anthu; ndi kuti boma lichepetse katangale. Zinthu zikungokwera mtengo chifukwa cha kugwa kwa ndalama ya kwacha, ndiye tikufuna kuti boma lichitepo kanthu. Talilembera kalata boma pamfundozi ndiye kaya ayankhe olo asayankhe ife zionetsero tichita, Amalawi amvetse mfundo zomwe tikufotokozazi, adatero Mabalani. Koma anthuwa ati akukayika ngati kumeneko anthu sadzaphedwa ponena kuti ziwonetsero zomwe zidachitika pa 20 Julaye mu 2010 anthu 20 adaphedwa. Koma malinga ndi Mabalani, apolisiwo awatsimikizira zodzapereka chitetezo chokwanira patsikulo. Alfred Banda wa mmudzi mwa Ngongonda kwa T/A Njewa ku Lilongwe wati ngakhale anthu ali ndi ufulu wolankhula, amabungwe asatenge anthu ngati zishango. Si kale tidali ndi zionetsero pomwe anthu 20 adaphedwa ndiye panonso akuti tichite zionetsero. Adziwe kuti sitidaiwale, tiyeni tipemphe boma kuti pakhale kukambirana osati zionetsero, adatero Banda. Limbani Kaombe wa mmudzi mwa Kachepa kwa T/A Likoswe mboma la Chiradzulu wati omwe akukonza zionetserowo adziwe kuti njovu zikamamenyana umavutika ndi udzu ndiye zionetsero zisachitike. Inde zinthu sizili bwino, katundu wakwera mtengo koma kutiuza kuti tikayende pamsewu ndiye si zoona. Afuna aphetse anthu osalakwa, ngati akufuna ayende okha koma asavutike ndi kuwamema anthu kuti achite zionetsero, adatero Kaombe. Shemaiah Chavula wa ku Mzuzu wati pakhale kaye zokambirana, ngati zavuta ndiye atha kuchita zionetsero. Koma Charles Kabaghe wa mmudzi mwa Mkombanyama kwa T/A Mwaulambia mboma la Chitipa wati anthu ayende pamsewu ndipo asaope kuphedwa. Inde zionetsero zijazi [za pa 20 July 2010] anthu adaphedwa ndipo Kumpoto kuno ndiko kudaphedwa anthu ambiri, koma apa tisawope. Kuphedwako tazolowera, tiyende pamsewu basi chifukwa zinthu sizili bwino, adatero Kabaghe. Mayi Banda posakhalitsapa pomwe amalankhula ndi Amalawi kudzera pawailesi ya Zodiak Broadcasting Station (ZBS), adati sakuletsa munthu kuti achite ziontserozo ndipo ngakhale pali mfundo yochita zionetsero, iye saali pampanipani. Banda adatinso ngakhale anthu ena akukonzekera zochita ziwonetsero koma iye sagwetsanso mphamvu ya kwacha ponena kuti Amalawi akuyenera kupirira kwa kanthawi kuti zonse zikhale mchimake. Iye adati sakuletsa munthu kuchita ziwonetsero chifukwa malamulo adziko lino amalola kuchita ziwonetsero.
11
St. Marys CDSS Yatsekedwa Maphunziro pa sukulu ya mpingo wa katolika ya St. Marys Community Day Secondary mboma la Machinga, ayimitsidwa kutsatira zionetsero zomwe anthu achipembedzo cha chisilamu amafuna kuchita lero ati pofuna kukakamiza akuluakulu oyendetsa sukuluyi kuti azivomereza atsikana kuvala ma Hijab nthawi ya maphunziro. Malinga mtolankhani wathu yemwe anafika ku sukuluyi, masiku apitawa makolo ndi aphunzitsi pa sukuluyi anagwirizana kuti atsikana achisilamu asamavale ma Hijab zomwe akuti sizinasangalatse atsogoleri a chipembedzo cha chisilamu mderali. Mmawa wa lero ndi pomwe atsogoleriwa pamodzi ndi anthu ena anapita ku sukuluyi kuti akakumane ndi mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi ndi kukamukakamiza kuti avomere atsikana ovala ma Hijab kuchita nawo maphunziro. Anthuwa akuti anakonza dongosolo lakuti achite ziwonetsero pa sukulupa koma izi sizinatheka kamba koti apolisi anafika pa sukulupa mwansanga anthuwo asanasonkhane. Koma polankhulapo mkulu wa nthambi zosiyanasiyana mu dayosizi ya Mangochi, bambo Ted Chigamba ati mawa (lachisanu) akuyembekezeka kukachita zokambirana ndi magulu okhudzidwa ku sukuluyi kuphatikizapo ku sukulu ya pulaimale ya Mpiri mboma lomwelo la Machinga yomwenso inatsekedwa masiku apitawa. Mawa Tikhala tili komweko kukachita nawo zokambirana kuti tiwone kuti mtsogolo muno titsata dongosolo lanji ndipo tikafikanso ku Mpiri komwe maphunziro kumeneko anayamba ayimitsidwa kaamba ka nkhaninso za ngati zomwezi, anatero bambo Chigamba.
14
Zitukuko pa Wenela Nyengo yasintha abale anzanga. Chikuchitika nchiyani? Pano pa Wenela, usiku winawo kudatentha zedi moti usiku onse ndimangokhalira kudzikanda. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kutembenuka ndiye kudali kosayamba, thukuta lili kamukamu! Koma kungocha, mphepo idali kuomba moopsa, mosasula madenga. Ndipo tsiku linalo kudazizira ngati wafikanso mwezi wa June! Chikuchitika nchiyani? Lero kumva kuti kwina mphepo ya mkuntho yasasula madenga, kenako kumvanso kuti kwina mphenzi yapha anthu. Chavuta nchiyani. Tidakhala pa Wenela tsiku limenelo kudikira Moya Pete ankati adzatsegulire chitukuko china. Tonse tidakonzeka, kuitanitsa gologolo, amayi a chisamba aja lero asintha makaka kuchoka ku Polisi Palibe kupita ku Dizilo Petulo Palibe. Eyatu, zaka 51 za kuvina! Gogo ujatu adatipeza tikuvina ndiye mungaletse ndani kuvinira Moya Pete? Iye walakwanji kuti tisamuvinire? Adafika Moya Pete ndi mdipiti wa galimoto zochuluka. Adabwera ndi anzake ambiri, pajatu ali ndi abwenzi ochuluka. Adati tilowoloke njanji, nkumalowera kanjira kachidule kopita ku Mbayani. Tikuyenda chomwecho, tidapeza liboni lomwe amaika kusonyeza kuti pakutsegulidwa chitukuko. Ndayamika kwambiri, abale anzanga, lero lino tikutsegulira msewu umenewu kwambiri. Gogo uja palibe chimene adapanga pano pa Wenela kwambiri, adatero Moya Pete. Abale anzanga, kodi nkhani zotsegula mipita imeneyi nkuchita kutulutsa munthu wamkulu kuchoka kunyumba yachifumu ija adamanga gogo uja. Ndikuuzeni kwambiri. Male Chauvinist Pigs siyidzatiuza zochita pano pa Wenela. Mbamba ndikunenetsa kwambiri. Ndipo posachedwapa, ndikatsegulira gawo la msewu wa ku Amwenye ku Limbe, adaonjezera chomwecho. Abale anzanga, sindikudziwa za inu koma ndisaname, zimandivuta kumvetsetsa zinthuzi. Zili ngati Adona Hilida kunena kuti akulephera kubwerera pano pa Wenela chifukwa palibe wawapatsa nyumba. Kodi zaka zonse ankagawa abakha ankagona mumtengo? Nchifukwa chake nanenso ndidavomereza mawu a Moya Pete kuti momwe zinthu zikukhalira pano pa Wenela, ndithu ana obwera mtsogolo adzatitemberera. Pano pa Wenela pakufunika anthu a maganizo ngati Che Guevera, Nelson Mandela ngakhalenso Fidel Castro. Kupanda apo, tipitiriza kuchemerera otsogolera kusolola akatchula dzina la Mama Tuge, adatero Abiti Patuma titafika malo aja timakonda pa Wenela.
15
T/A Bwananyambi Alowa Mmanda Wolemba: Thokozani Chapola 9/10/bwananyambi.jpg" alt="" width="733" height="412" />Amalimbikitsa maphunziro a atsikana-T/A Bwananyambi Mfumu yaikulu BWANANYAMBI ya mboma la MANGOCHI yomwe yamwalira ku chipatala cha QUEEN ELIZABETH CENTRAL mu mdzinda wa BLANTYRE yalowa mmanda. Mlembi wa bungwe la mafumu a mboma la MANGOCHI, T/A CHOWE anati imfayi yadza kaamba ka nthenda yothamanga magazi. T/A CHOWE auza RADIO MARIA MALAWI kuti boma la MANGOCHI lataya munthu wofunikira kwambiri kumbali yokweza maphunziro aatsikana. Mdera lake lonse ana aakazi samalekera sukulu panjira ndipo amathetsa maukwati a ana achichepere. Timakapemphako mzeru choncho tisowa mzeru zawo, anatero T/A Chowe. T/A Bwananyambi yemwe anali mfumu yokhayo yaikazi mboma la MANGOCHI ayikidwa mmanda ku likulu lawo ku NDUMUNDU ku NAMWERA mboma la MANGOCHI. Polankhulapo mfumu yaikulu ya mtundu wa chiyao Paramount Chief KAWINGA yati mtundu wachiyao wataya munthu ofunikira kwambiri pa chitukuko cha deralo ponena kuti mfumuyi inalinso patsogolo kulimbikitsa ntchito zakusasiyana pakati pa amayi ndi abambo mbomalo. Anali munthu amene amagwiritsa ntchito umayi wake polimbikitsa kuti amayi akhale mmaudindo osiyanasiyana chitsanzo chabwino ndi a MP mayi Lilian Patel. Iwo amalimbikitsanso maphunziro a atsikana mdera mwawo komanso boma lonse la Mangochi, anatero Paramount Chief Kawinga. Mfumuyi yapempha achibale kuti achite bata komanso pambuyo pake asankhe munthu wa makhalidwe abwino monga inalili mfumu yamwalirayi yomwe dzina lawo lenileni linali Atinga Sande. Imfa ya mfumu yaikulu Bwananyambi ikudza patangotha mwezi umodzi, mfumu yaikulu AMIDU ya mboma la Balaka yomwenso ndi ya mtundu wa chiyao itamwalira.
14
JB asabisalire kwa amphawi za kuyenda Pambali poyenda kunja, Banda akukhaliranso kugawa ngombe, nyumba ndi kukweza mafumu Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda wamenyetsa nkhwangwa pamwala ponena kuti, zivute zitani, sangasiye kuyendera anthu mmidzimu ndipo wati zikafika povutitsitsa atha kukwera kabaza. Koma ena mwa anthu omwe athirapo ndemanga pa mawu a mtsogoleriyu, kuphatikizapo akuluakulu ena odziwa za mmene chuma cha boma chukuyendera, apempha mtsogoleriyu kuti asinthe maganizo. Loweruka lapita Banda adauza anthu pabwalo la Kalambo mumzinda wa Lilongwe kuti sasiya kuyendayenda chifukwa ndiyo njira yomwe akuthandizira anthu akumudzi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Iye adati ngati pathine azikwera kabaza (njinga ya hayala) kuti afikire abale ake ovutika. Izi zikutsutsana ndi zomwe boma lake, kudzera mwa nduna ya zachuma Maxwell Mkwezalamba, lidalengeza kuti layamba laimitsa kaye maulendo a nduna, akukuakulu ogwira ntchito mboma, kuphatikizapo Pulezidenti, kuti mwina chuma cha boma chingabwerere mchimake. Bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) sabata yatha lidadandaula ndi maulendo a mtsogoleriyu ponena kuti ndi njira imodzi yowonongera chuma cha dziko lino. Bungweli lidati pamene Pulezidentiyu wayenda mdziko mommuno akumaononga K10 miliyoni patsiku. Koma mneneri wa boma, Brown Mpinganjira, akuti sakudziwa ndalama zomwe zikuwonongeka koma adati atiuzabe pambuyo pa kukumana ndi akuluakulu a zachuma. Ngatidi ndi zoona kuti ulendo wa Pulezidenti woyendera anthu ake mdziko mommuno umadya ndalama zokwana K10 miliyoni patsiku, atati azigwiritse ntchito ina, ikhoza kuthandiza pachitukuko chomwe chingapindulire anthu ochuluka. Mwachitsanzo, mndondomeko ya zachuma cha boma ya 2013/2014, boma lidapatula K7 miliyoni nkuika mthumba la Local Development Fund (LDF) zothandizira pantchito ya chitukuko cha mmidzi mdera la phungu mmodzi pachaka. Mwezi wa October wokha, pali umboni woti mtsogoleriyu adachititsa misonkhano yosachepera 17 mdziko muno. Nduna ikaperekeza mtsogoleriyu imalandira K45 000 patsiku ngati alawansi; wachiwiri kwa nduna amalandira K39 600; wothandizira nduna K15 000; madalaivala ndi achitetezo amapindira mthumba K6 000, malinga ndi malipiro amamulumuzanawa amene adaunikidwanso mu November 2012. Malipirowa amagunda papakulu ngati zochitikazo zikuchitikira kunja kwa Lilongwe. Lachiwiri lapitali, anthu a mmidzi ya Chamba, Msanganiza, Khunju, Kamtukule, Jiya, ndi ina kwa Senior Chief Somba mboma la Blantyre adauza Tamvani kuti iwo ali pamoto chifukwa cha kusowa kwa chimanga, feteleza wa makuponi komanso mankhwala mzipatala. Anthu ena amene adalankhula ndi Tamvani tidawapeza atagona pa Admarc ya Mbame, pomwe ankadikirira chimanga ndi feteleza. Mmodzi mwa anthuwo, Ephraim Kabichi, wa mmudzi mwa Kamtukule, adati: Anthu atha kusangalala pamene mtsogoleriyu wayenda koma amene akuthandizika ndi ochepa. Ndalama zikugwiritsidwa ntchitozo ndi zambiri zomwe zikadapindulira anthu ambiri. Sabata ino ndi yachitatu sindidagule feteleza, feteleza adangobwera kamodzi kokha. Kuchipatala kulibe mankhwala komanso chimanga chidasowa kalekale kuno. Ndalamayo itha kuthandiza anthu tonse kuno. Mkulu wa bungwe loona momwe nkhani zachuma zikuyendera la Malawi Economic Justice Network (Mejn), Dalitso Kubalasa, wati Pulezidenti Banda akungobisala pachipande. Ndalamazo zithanso kuposa K10 miliyoni pamene wayenda. Koma ndalama zimenezi zikuthandiza anthu angati? Ngati dziko tione zimenezi. Tili ndi mavuto ambiri monga kusowa mankhwala mzipatala komanso momwe chuma chathu chilili, adatero Kubalasa, nkuonjezera kuti izi zikuchitika pamene chaka chamawa dziko lino lili ndi chisankho ndiye nzosakaikitsa kuti cholinga cha maulendowo ndi ndale zokopa anthu kuti adzavotere mtsogoleriyu ndi chipani chake cha PP, osati kuti anthu akumudzi ndiwo akupindula nawo. Katakwe pandale Blessings Chinsinga akuti Nyumba ya Malamulo ndiyo ingathane ndi kuyendayenda kwa Banda. Kodi ndalama zimenezi akuzitenga kuti? Kuti mufunse yankho likhala loti zikuchokera mndondomeko yomwe idavomerezedwanso ndi Nyumba ya Malamulo. Ndiye tikuyenera kuona bwino ndalama zomwe zikupita kuthumba lomwe mtsogoleri azigwiritsira ntchito, adatero Chinsinga. Sabata yatha, bungwe la CCJP lidauza atolankhani kuti lakwiya ndi maulendo a Banda ogawa ngombe ndi kukweza mafumu chifukwa akumaononga zambiri kwa anthu ochepa. Ndi zosamveka kuti boma liziononga K10 miliyoni pokagawa ngombe ziwiri za ndalama pafupifupi K400 000. Mtsogoleri asiyire ntchitoyi kwa akuluakulu a kuunduna wa zamalimidwe, adatero mlembi wa bungweli Peter Chinoko. Banda adati maulendowa azichitikabe chifukwa panganolo likuloleza maulendo ofunika okha.
11
Anthu 37 Aphedwa ku Kampani ya Migodi Mdziko la Burkina Faso Anthu pafupifupi 37 aphedwa ndipo ena 60 avulala ku kampani ina ya za migodi mdziko la Burkina Faso. Malipoti a BBC ati anthuwa achitidwa chiwembuchi ndi gulu lina la za uchifwamba lotchedwa Jihadist lachitatu mu mzinda wa Bongu mdzikolo. Padakali pano asilikali a dzikolo, alengeza kuti ayika chitetezo cholimba mu zipata zonse za dzikolo makamaka zomwe zachita malire ndi dziko la Mali. Mu Mwezi wa September chaka chino guluri linaphanso anthu oposera 20 ku company ina yoona za migodi ku mpoto kwa dzikolo. Malinga ndi bungwe loona za anthu othawa kwawo pa dziko lonse, anthu oposera 500 sauzande adathamangitsidwa mnyumba zawo ndipo akusowa pokhala.
14
Uhule wanyanya Lero pa 1 Disembala ndi tsiku limene maiko onse padziko lapansi amakumbukira za nkhondo yolimbana ndi matenda a Edzi. Koma ngati zimene zikuchitika ku Mponela mboma la Dowa zingapitirire, nkhondo yothana ndi matendawa ivutirapo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kumeneko, asungwana achichepere a zaka za pakati pa 10 ndi 14 akuti alusa kwambiri ndi mchitidwe woyendayenda mmalo omwera mowa momwe akumachita zachisembwere ndi abambo akuluakulu kuti apeze ndalama. Polankhula pamsonkhano wothana ndi kukwatiritsa ana msanga umene adakonza a bungwe la Everychild sabata yatha, T/A Dzoole yambomalo yati asungwanawa amachokera mmidzi yozungulira pa Mponela omwe amathawa umphawi kwawo ndipo mfumuyo yapempha apolisi kuti achitepo kanthu pa mchitidwewu. Iye wati asungwana osakwanitsa zaka 15 akumapezeka mmalo omwera mowa ndi ogona alendo kufunafuna abambo oti azichita nawo zachiwerewere posinthanitsa ndi ndalama kapena zinthu zina. Ndakumanapo kangapo ndi ana achichepere makamaka asungwana azaka za pakati pa 10 ndi 14 omwe amagulitsa matupi awo kwa abambo akuluakulu. Mchitidwewu wafika ponyanya kwambiri moti pakufunika njira youthetsera msangamsanga, idatero mfumuyo. Iye adati apolisi akadayesetsa kuchitapo kanthu chifukwa izi zikupangitsa kuti matenda a Edzi asathe komanso zikuchulukitsa chiwerengero cha ana osowa chithandizo cha makolo chifukwa asungwana oterewa akatenga pathupi amangobereka mwana nkumuthawa, adatero Dzoole. Chiwelewele chomwe chimakhudzana kwa mbiri ndi mchitidwe wa uhule ndi njira ayayikulu yomwe imafalitsa matenda a Edzi omwe dziko lonse lapansi likukumbukira lelo. Chikalata chomwe adatulutsa a bungwe la World Health Organisation mu 2011chimasonyeza kuti anthu oposa 34.2 million dziko lonse ali ndi kachilombo ka HIV. Wachiwiri kwa mkulu wa polisi ya Mponela George Ntetemela adatsimikiza za kukula kwa mchitidwe wa uhule mderalo ndipo adati apolisi ali kale pa kalikiliki kusaka njira zochotsera asungwana achichepere mmalo omwera mowa. Cholinga chathu sikumanga munthu koma tikufuna tiwagwire asungwana oterewa kenako tiitane makolo awo kuti tikambirane nawo, adatero Ntetemela. Oimira bungwe la Everychild, Tissie Msonkho, adati asungwana ambiri mdziko muno akumalowa mbanja zaka zoyenerera zisanakwane zomwe zimapangitsa kuti azizunzika. Msonkho anati maukwati ambiri aana achichepele amapangidwa chifukwa cha umphawi, miyambo komanso nkhanza zomwe ana maka asungwana amakumana nazo mmanyumba momwe amakhala.
15
Mgodi wa Kanyika waika anthu pamoto Anthu okhala ku Kanyika mboma la Mzimba ali pachiopsezo chachikulu cha umphawi komanso njala ataletsedwa ndi boma komanso kampani ya Globe Metals and Mining kupanga chitukuko komaso kulima kuderali zaka zitatu zapitazo pofuna kupereka mpata woti kampaniyi iyambe kukumba miyala ya mtengo wapatali kumeneko. Mabanja 248 ndiwo akukhudzidwa ndi nkhaniyi ndipo sadapatsidwebe chipukuta misozi kapena malo ena oti azikakhalako ngakhale kuti iwo adalonjezedwa kuti apatsidwa ndalama ndi malowo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zadzetsa mavuto kuderali kaamba koti nyumba zidayamba kugwa chifukwa choti sizikusamalidwa chifukwa padali chiyembekezo choti iwo achoka. Nyumba 45 zidagweratu moti anthu akukhala muzisakasa, makhitchini, zotsalira za nyumba komanso ena adapita kwa achibale. Bungwe la Chikatolika loona za maufulu a anthu la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) masiku apitawa lidakonza ulendo wa atolankhani kuti akadzionere okha mavuto omwe anthu agwamo. Mavuto omwe anthu akukumana nawo, komanso chetechete wa boma ndi kampaniyi, zapangitsa mafumu ndi anthu a kuderali kuti ngati sachitapo kanthu pa za chipukuta misozi pofika pa 31 March, apanga zoti kampaniyi ichoke basi. Mavutowa afikaso popsesa mtima Inkosi ya Makhosi Mmbelwa yemwe akuti ngati kampaniyi ndi boma sali okonzeka kuyamba ntchito ya mgodi ndi bwino kuti awasiye anthu azikhala mmene akhalira mmbuyomo. Mkulu woyongana za miyala ndi nthaka wa ku Globe Metals and Mining, Chris Ngwena, adati kampani yawo singalankhulepo pankhaniyi kaamba koti pali zokambirana ndi boma. Koma mlembi wamkulu kuunduna wa zachilengwe ndi migodi, Ben Botolo, adati anthu adekhe chifuKwa kampani ya Globe ikuyangana makampani ena oti ithe kugwira nawo ntchito.
6
Anthu Mazanamazana Akusowa Pokhala Ku Bahamas Wolemba: Sylvester Kasitomu Anthu okhala pa chilumba cha pa Nyanja ya Caribean cha Bahamas akusowa pokhala nyumba zawo zitagwa kaamba ka mpempo ya mphanvu ya mafunde yomwe ikuomba panyanjayi. Malipoti akusonyeza kuti mphepiyi imene ikuombayi ndi ya mphanvu kwambiri yomwe ikuyenda pamtunda wa 250 Kilometer pa Ora. Mwazina malipoti kaamba ka mphepoyi kulumikizana kudzera pa makina a internet kukuvutnso kutsatira kuonongeka kwa zida zotumizira mauthenga. Boma la dziko la Bahamas lamanga misasa yodikiliramo anthu omwe akusowa pokhala yokwana 14, ena mwa anthuwa akukhala mmasukulu ndi mmatchalitchi. Aka ndi kachisanu kuchokera mu chaka cha 2016 kuti chilumbachi chikhudzidwe ndi mphepoyi ndipo padakali pano muthu mmodzi wa zaka zisanu ndi zitatu 8 ndi yemwe wafa pa ngpoziyi.
14
Papa Athunzitsa Mitima ya Ovutika Wolemba: Thokozani Chapola Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wathunzitsa mitima anthu omwe akukomana ndi mavuto osiyanasiyana kuti asataye chikhulupiliro koma kudziwa kuti Mulungu amawakonda ndikumva mapemphero awo. Papa kucheza ndi anthu osiyanasiyana Papa Francisco walankhula izi mu uthenga umene watumizira akhristu a mpingo-wu omwe ali mkati kuchita mbindikiro wawo ku tchalichi ku malo oyera a Louds mdziko la France. Bungwe lina lomwe limalimbikitsa moyo wa uzimu pakati pa akhristu a mpingowu mdzikomo ndi lomwe lakonza mbindikiro-wu ngati njira imodzi yokonzekera bwino tsiku loganizira za osauka pa dziko lonse (World Day of the Poor) lomwe ndi lamulungu likudzali pa 17 November 2019.
14
Akukambirana zolola ana a chi Rasta msukulu Unduna wa za maphunziro wati ukukambirana ndi ma Rasta komanso unduna wa za malamulo pa za ana 26 amene ma Rasta adapempha kuti aziloledwa kuphunzira msukulu za boma ali ndi tsitsi la mizeremadiredi. Anawa, amene padakali pano sakupita kusukulu, akuimira ana ena onse a ma Rasta amene amaletsedwa kusunga tsitsi lopotana msukulu za boma za mdziko muno. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mwanamanga: Tinkakambirana ndi Bingu Kalata yomwe unduna wa za malamulo udalembera unduna wa za maphunziro pa 27 January, 2017, idaunikira kuti undunawo ukuyenera kulandira mwana aliyense, kuphatikizapo ana amene akusunga tsitsi lopotana, malinga ndi chipembedzo chawo. Potengera ndi kulemekeza mphamvu ya malamulo a dziko lino, pa magawo 20, 25 ndi 33, ndi ufulu wa mMalawi, aliyense kusasalidwa ndipo munthu aliyense ali ndi ufulu wolandira maphunziro komanso otsatira chipembedzo chomwe akufuna. Kotero, potengera kusintha lamulo lokhudza maonekedwe ndi za kavalidwe pakati pa ophunzira, lomwe limaletsa kusunga tsitsi pasukulu, mukuyenera kulola ana omwe ali ndi tsitsi lopotana potengera chipembedzo cha chi Rasta msukulu za boma, idatero kalatayo. Mneneri wa unduna wa za maphunziro Lindiwe Chide adati undunawu ukudziwa za kalata yochokera ku unduna wa za malamuloyo ndipo adati undunawo ukukambirana ndi mbali zonse zokhudzidwa pa momwe izi zingatsatidwire. Tikukambirana ndi mbali zosiyanasiyana zokhudzidwa za momwe tingayendetsere pulogalamuyi ndipo zikatheka mumva sizidzasowa, adatero Chide. Sukulu za boma za pulaimale ndi sekondale mdziko muno zimathamangitsa ana omwe ali ndi tsitsi lopotana potsatira chipembedzo cha u Rasta ndipo nkhaniyi siyikondweretsa mpangono pomwe eni chipembedzochi. Kwa zaka zoposa 20 tsopano, otsatira chipembedzochi akhala akumenyerera kuti unduna wa zamaphunziro usinthe maganizo nkuyamba kulola anawa msukuluzi kuti nawonso azidyerera ufulu wawo wamaphunziro. Mtsogoleri wachipembedzochi mdziko muno mgawo la Nyabinghi, Ras Mikah Chiserah wati zomwe zikuchitikazi zikutanthauza kuti dziko la Malawi silivomereza chipembedzo cha chi Rasta monga momwe malamulo amanenera. Apatu zikutanthauza kuti ife ma Rasta tikufera chipembedzo chonsecho malamulo amati munthu aliyense ali ndi ufulu otsata chipembedzo chomwe akufuna pambali pa ufulu wa maphunziro, adatero Ras Chiserah. Iye adati pomwe ufulu wa zipembedzo unkabwera kumayambiliro a ulamuliro wa zipani zambiri, iwo ankaona ngati kuponderezedwa kwa owutsatira kwatha koma akudabwa kuti boma likulephera kutsatira malamulo opanga lokha. Kadaulo pa zamalamulo yemwenso ndi mphunzitsi ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College ku thambi ya zamalamulo, Edge Kanyongolo adati ufulu uli ndi mlingo wake koma akaunika nkhani ya ma Rastayi, saonapo vuto. Mmalamulo a dziko lino muli maufulu osiyanasiyana ndipo umodzi mwa maufuluwa nkukondedwa mofanana. Chifukwa chokhacho chomwe ufulu ungapatsidwe mlingo, mpomwe ukuphwanya ufulu wa anthu ena ndipo sindikuona kukhala ndi tsitsi lopotana kukuphwanya ufulu wa munthu wina, adatero Kanyongolo. Malingana ndi mneneri wa Nyabinghi, Ras Fred Mwanamanga, kusunga tsitsi lopotana ndi umodzi mwa mizati ya chipembedzo cha chi Rasta ndipo kuti ngati Amalawi, otsatira chipembedzochi amayenera kuloledwa kupanga chilichonse chomwe otsatira zipembedzo zina amaloledwa kupanga. Pomenyerera ufulu wa maphunziro omwe Mwanamanga adati otsatira chipembedzochi amamanidwa, ma Rasta adakumana ndi mtsogoleri wakale Bingu wa Mutharika yemwe adawalonjeza kuti zonse zikhala bwino. Mwanamanga adati mwatsoka, zisadakhale bwino monga momwe amayembekezeramo, Mutharika adamwalira ndipo izi zidachititsa kuti ma Rastawa ayambirenso nkhondo yomenyerera ufulu wawo. Titangomva za imfa ya a Mutharika, tidasweka mitima chifukwa tidadziwa kuti ntchito ikadalipo. Mu 2013, tidayenda ndawala yokapereka kalata ya madandaulo kulikulu la dziko lino ku Lilongwe komwe tidayankhidwa kuti madandaulo athu apita kwa a Pulezidenti, watero Mwanamanga. Iye wati pakhala pakuchitika zokambirana pankhaniyi pakati pa ma Rasta, unduna wa zamaphunziro, unduna wa za malamulo ndi magulu a zamaufulu ndipo potsatira zokambiranazi, unduna wa za malamulo udalangiza unduna wa za maphunziro kuti uyambe kupereka mpata kwa ophunzira a chipembedzo cha chi Rasta.
3
Mabungwe Adzudzula Mutharika pa Makomishonala Atsopano a MEC Mabungwe osiyanasiyana adzudzula mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika pa momwe wasankhira makomishonala a bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC). Wapampando watsopano wa bungwe la MEC-Kachale Mtsogoleri wa dziko linoyu wasankha anthu atsopano kuti akhale akuluakulu a bungweli, pomwe wasankha Justice Dr. Chifundo Kachale kuti akhale wapampando wa bungweli, kulowa mmalo mwa Justice Dr. Jane Ansah omwe anatula pansi udindowu sabata zapitazo. Makomishonala atsopano omwe asankhidwa ndi a Arthur Nathuru, a Steve Duwa, Dr. Anthony Mukumbwa komanso mayi Olivia Liwewe. Amubwezeretsa mu komishoniyo-Kunje Mutharika wabwezeretsanso mu komishoniyi Dr. Jean Mathanga komanso mayi Linda Kunje. Awiriwa ndi omwe anali kale mu gulu la makomishona a bungweli, omwe anayendetsa nawo chisankho cha chaka chatha, chomwe bwalo la milandu linalamula kuti chichitikenso kaamba koti sichinayende bwino ponena kuti chinali ndi zolakwika zambiri. Mabungwe monga a Public Affairs Comittee (PAC) komanso la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) alankhula mosakondwa ndi zomwe zachitikazi. Polankhula mwapadera kwa atolankhani lamulungu mu mzinda wa Lilongwe, akuluakulu a bungwe la HRDC ati achita zionetsero lachitatu likudzali pofuna kukakamoza aphungu a nyumba ya malamulo kuti akambirane momveka bwino pa za tsiku lomwe chisankho chichitike mdziko muno komanso kuvomereza ma bilu onse okhudza chisankho. Sitingayembekeze kunenas kuti tidikire akambirane zomwe analankhula a President chifukwa analankhula zosathandiza ndi zobwezeresa mmbuyo, anatero Sembereka yemwe ndi mmodzi mwa akuluakulu a bungweli.
11
Sukulu ya Mpiri Yatsekedwanso Maphunziro pa sukulu ya pulaimale ya mpingo wa katolika ya Mpiri mboma la Machinga ayimitsidwa kutsatira ziwawa zomwe zinachitika pa sukuluyo pakati pa asilamu komanso akhristu. Mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi a Cornelius Mua atsimikiza za nkhaniyi polankhula ndi Radio Maria Malawi ndipo ati izi zachitika pamene anthu otsatira chipembedzo cha chisilamu amafuna kukakamiza atsogoleri a sukuluyo kuti azilora ana awo achitsikana kuchita maphunziro pa sukuluyi atavala chovala chotedwa Hijab kumutu kwawo. Maphunziro asokonekera Tinagwirizana mmene sukuluyi imayambiranso pa 17 February paja kuti aliyense wophunzira pano akuyenera kutsatira malamulo omwe mpingo unakhazikitsa chifukwa sukuluyi ndi ya mpingo. Maphunziro sabata imeneyi anayenda bwino kufikira lolemba pa 24 February. Anabwera mashehe atatu omwe amatsogolera gulu lina lomwe linazayambitsa zamtopola pa sukulupa. Anayamba kumenya a school committee komanso akuluakulu ena, anatero a Mua. A Mua ati lachinayi likudzali kukhala msonkhano wa mafumu komanso mbali zonse zokhudzidwa kuti akambirane ndi kuwunika njira zomwe ayenera kutsata ngati sukuluyi ingatsekulidwenso. Aka ndi kachiwiri kuti sukuluyi itsekedwe mchaka chino chokha kutsatira kutsekedwa koyamba mu mwezi wa January ndipo inatsekulidwanso pa 17 February.
14
Lipoti la imfa ya Bingu latekesa boma, DPP Pomwe Malawi waona utsi wokhetsa misozi chifukwa cha kumangidwa kwa mamulumuzana a DPP komanso amaudindo ena mboma, akadaulo pazandale komanso mkulu wa kafukufuku mchipanichi, George Chaponda, ati kunjatidwa kwa akamunawa kugwedeza boma la Peoples (PP) komanso kutekesa DPP. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Akadaulowa, Joseph Chunga, yemwe ndi mphunzitsi pasukulu ya ukachenjede ya Chancellor College ku Zomba, komanso Justine Dzonzi mkulu wa bungwe la Justice Link ati ngakhale mbalizi zingatekeseke komabe izi zingapereke nyonga ku DPP ngati atsogoleri ake sangapezeke ndi kakuda. Ndemangazi zikudza malinga ndi kutoledwa kwa atsogoleri angapo a DPP omwe atchulidwa mlipoti la momwe mtsogoleri wa dziko lino wa kale, Bingu wa Mutharika adamwalirira komanso zochitikachitika zakudza kaamba ka imfayo. Mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda pa 11 June 2012 adasankha komiti yofufuza za nkhaniyo motsogozedwa Jaji wopuma Elton Singini. Iwo adapereka zotsatira za kafukufuku wawo sabata yathayi kwa Pulezidenti Banda. Kutsatira lipotilo, Lolemba pa 11 apolisi adanjata atsogoleri a DPP monga mtsogoleri wa chipani Peter Mutharika; yemwe adaali mneneri wa boma Patricia Kaliati; mneneri wa chipani cha DPP Nicholas Dausi; yemwe adaali nduna ya za umoyo Jean Kalirani; yemwe adaali nduna ya maboma aangono Henry Mussa; yemwe adaali wachiwiri kwa nduna ya zofalitsa nkhani Kondwani Nankhumwa; ndi yemwe adaali nduna ya zamasewero Symon Vuwa Kaunda. Anamandwa ena onjatidwa ndi nduna yoona mapulani a kayendetsedwe ka chuma Goodwell Gondwe; mlembi wamkulu mboma Bright Msaka; ndi wachiwiri wake Necton Mhura. Enanso ndi wachitetezo wa malemu Bingu Duncan Mwapasa. Pofika Lachinayi nkuti zitatsimikizika kuti yemwe adaali mlangizi wa malemu Bingu, Allan Ntata, ali ndi mlandu woyankha. Iye adachoka mdziko muno. Kutoledwa kwa akamunawo kudadzetsa zipolowe mmizinda ya Blantyre, Lilongwe komanso maboma a Phalombe ndi Zomba ndipo apolisi adabalalitsa otsatira DPP omwe amaimba kuti atsogoleriwo awatulutse. Lachitatu, omangidwawa kupatula Kalirani ndi Gondwe, omwe amalandira thandizo kuchipatala chifukwa cha kuthamanga magazi, adakawonekera kubwalo lamilandu la Lilongwe majesitireti komwe adawapeza ndi milandu isanu ndi umodzi (6). Koma Mwapasa adatulutsidwa pabelo ya apolisi ponena kuti mlandu wake udali wochepa kusiyana ndi enawo. Mwa milanduyo ndi monga kuukira boma ndi kulimbikitsa kuukira. Mlanduwu wachiwiriwu akuti adaupalamula pa 5 April pomwe akuti adalimbikitsa mkulu wa asirikali mdziko muno General Henry Odillo kuti atenge boma ndipo adalembanso kalata yokhudza nkhaniyi. Milanduyi imawerengedwa ndi woweruza mlandu kubwalolo, Ruth Chinangwa. Mlanduwo udasamutsidwira kubwalo lalikulu lomwe limazenga milandu ikuluikulu monga kuukira boma. Poona milanduyi yomwe mwa ina zilango zake ndi kukakhala kundende moyo wonse kapena kunyongedwa kumene ngati atapezeka olakwa, akadaulo pazandale akunenetsa kuti izi zili ndi nthenya pandale komanso ntchito za boma. Chaponda, polankhula Lachitatu, adati msonkhano waukulu wa chipani chawo womwe umayembekezereka kuchitika pa April 19, wayimitsidwa kaye kuti athane ndi za milanduyi. Tili otangwanika ndi kumangidwa kwa akuluakulu a chipani, tikathana ndi izi tinena za tsogolo la msonkhano wa chipani chathu, adatero Chaponda ponena kuti kumangidwako nkwandale chifukwa pali mavuto ambiri mdziko muno omwe boma likuyenera kukonza kusiyana ndi milanduyo. Koma Dzonzi akuti DPP ingakhalebe moyo ngakhale mizati ya chipanicho yatoledwa. Ngati gamulo la khoti lingawaipire ndiye kukhale kugwedezeka kuchipanichi. Chipani chilipobe chifukwa DPP ili ndi anthu ambiri. Koma polingalira kuti awa adali akuluakulu komanso kuti mwezi ukudzawu akuyembekezera kuchititsa msonkhano waukulu, izi zikhudza chipanichi. Ndikutero chifukwa anthu atoledwawo amakambidwa kuti akukapikisana nawo kumsonkhanowo komanso ali ndi maudindo akuluakulu. Ngati atsogoleriwa angalandire chilango chowasunga kundende ndiye kuti zidzakhala zovuta kwa chipanichi kuti chigulitse atsogoleri atsopano, adatero Dzonzi. Iye adati kumangidwanso kwa Msaka ndi Gondwe kukhudza boma. Gondwe wangolowa kumene paundunawo kutsatira kuchoka kwa Atupele Muluzi. Iye adatinso Gondwe amadziwa momwe zina zingayendere ndiye kungomumanga pena pasokonekera. Gondwe wakhalanso mboma kwa nthawi ndipo amadziwa momwe za chuma zingayendere, apa zina zivuta, adatero Dzonzi. Iye adatinso uwu ungakhalenso mwayi ku DPP ngati mlanduwo ungawakomere chifukwa kudzakhala kuti atsogoleri ake ali ndi unyinji wa anthu owatsatira, zomwe sizidzawavuta kuchita bwino mmasankho akudzawa. Dzonzi adatinso kumangidwa kwa akuluakuluwa si zifukwa za ndale. Zimavuta nkuti aliyense wandale akamangidwa anthu timathamangira kuti ndi zifukwa za ndale zomwe apa ine sindikuziona, adatero Dzonzi. Naye Chunga adagwirizana ndi Dzonzi pazina ndipo adati zonse zili mmanja mwa abwalo kuti yemwe zikamuyendere ndani. Pomwe tinkalemba nkhaniyi nkuti zisadadziwike tsiku lomwe boma litengere oganiziridwawa kubwalo kuti liyambe kuzenga milanduyo.
11
Dziko la Malawi Silimayenera Kuchita Chikondwelero Cha Zaka 55 Mvula By Richard Makombe Mmodzi wa akatswiri pa nkhani za ndale mdziko muno wati sanagwirizane ndi ganizo la boma lochita chikondwelero chokumbukira kuti dziko lino lakwanitsa zaka 55 lili pa ufulu wodzilamulira pomwe boma likusowa ndalama zogwiritsira ntchito poyendetsera zina mwa ntchito zake. Mvula: Ndalama za chikondwelero akanatha kugwiritsa ntchito zina zofunikira kwambiri Katswiriyu a Humphreys Mvula wauza Radio Maria Malawi pomwe dziko lino loweruka limachita chikondwelero kuti lakwanitsa zaka 55 za ufulu odzilamulira. A Mvula ati ndi momwe zinthu zilili padakali pano boma limayenera kuganiza mozama potenga ndalama za chikondwelerochi ndikugwiritsa ntchito kugula mankhwala mzipatala komanso mavuto ena omwe achuluka mdziko muo. Dziko lino likukumana ndi mavuto a zachuma padakali pano komanso mpungwepungwe pa nkhani za ndale choncho kunali koyenera kukonza kaye mavuto amenewa,osati kuononga ndalama kuchita chikondwelero pomwe atsogoleri ena a ndale sakukondwa ndi momwe zinthu zikuyendera mdziko muno, anatero a Mvula. A Mvula apempha mtsogoleri wa dziko lino kuti apeze njira ndikukambirana ndi atsogoleri otsutsa kuti athetse mpungwepungwe omwe ukuchitika mdziko muno pa nkhani za ndale. Padakali Pano bungwe la Human Rights Defenders Coalition lakhala likukonza ziwonetsero zosagwirizana ndi momwe zisankho zinayendera pa 21 May chaka chino komanso mwa zina likufuna kuti wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission Justice Dr. Jane Ansah atule pansi udindo wake. Pa ziwonetserozi zomwe zakhala zikuchitika mmizinda ikuluikulu yonse ya dziko lino, anthu ena akhala akuononga katundu wa anthu ena ochita malonda kuphatikizapo akuluakulu a ndale ena. Dziko la Malawi linalandira ufulu odzilamulira pa 6 July mchaka cha 1964 ndipo chaka chilichonse dziko la Malawi limachita chikondwelerochi.
11
YAS Yati Boma Lifufuze Ndalama Zomwe Zawonongedwa ku ESCOM Mabungwe a National Anti-Corruption Alliance kudzanso la Youth And Society (YAS) apempha mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Muntharika kuti achotse a Thom Mpinganjira pa udindo wa wapampando wa bungwe la ESCOM. Boma lifufuze bwino za nkhaniyi-Kajoloweka Mabungwewa anena izi pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Mzuzu. Ndipo polankhulapo mmodzi mwa akulu-akulu ku bungwe la YAS a Charles Kajoloweka Mhango, afotokozera atolankhaniwa zina mwa mfundo zikuluzikulu zomwe zikupezeka mu lipoti lomwe boma lidatulutsa mu mchaka cha 2019, lomwe mwazina linafotokoza bwino momwe bungweli likugwilira ntchito zake. A Mhango ati ndizomvetsa chisoni kuti kufikira pano ngakhale lipotili likusonyeza kuti ndalama pafupifupi 8 Billion Kwacha zidasakazidwa ku bungweli , koma palibe aliyense yemwe wamangidwa, zomwe ati ndi zinthu zokolezera mchitidwe woononga chuma cha boma. Tithokoze boma kaamba ka kafukufuku wawo ku bungwe la escom zomwe zatiululira mmene ndalama zakhala zikuonongedwera ku bungweli chomwe tikufuna ndi choti athom mpinganjira asakhalenso pa udondo wa wapampando wa bungweli kaamba koti ali ndi mulandu ndipo afufuzidwenso, anatero a Mhango. Mwazina iwo apempha President wa dziko lino kuti achotse a Mpinganjira pa udindowu pofuna kuti bungweli liziyendetsedwa ndi anthu omwe ali okhulupirika maka kuti ntchito za bungweli ziyambe kuyendanso bwino.
2
Ana achoke mmindaNduna Mvula yagwa Madera ambiri moti anthu ali kalikiriki mminda kuthira manyowa, kubzala ndi kuwokera koma nkhawa yaikulu yagona pamchitidwe wogwiritsa ana achichepere ntchito za kumunda pofuna kuzemba mtengo wa anthu aganyu. Chaka chino, boma laneneratu kuti silidzasekerera munthu aliyense wopezeka akugwiritsa ana achichepere ntchito mmunda. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi nduna ya zamalimidwe Dr Allan Chiyembekeza pankhaniyi. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu A nduna, tamva mukuchenjeza za mchitidwe wogwiritsa ana achichepere ntchito mmunda, kodi mungatambasulepo bwino pamenepa? Eya, pamenepa tikutanthauza kuti pali anthu ena omwe amaganiza molakwika, mmalo moti azilimbikitsa ana kupita kusukulu, iwo amalemba ana ochepa msinkhu kwambiri ntchito mminda makamaka pano pomwe fodya wagundika. Mayi ndi mwana wake wachichepere kuchita ganyu mmunda wa fodya. Ana sayenera kugwira ntchito zoposa msinkhu wawo Kodi kumeneku nkulakwa? Kulakwa kwambiri moti ngakhale malamulo a dziko lino zimenezi salola, mwana amayenera kuti azipatsidwa nthawi yokwanira bwino yolimbikira maphunziro. Mwana yemwe amakhalira kugwira ntchito zoposa msinkhu wake monga zakumundazo, amakhala wotopa paliponse ndiye sangalimbikire maphunziro. Ndimayesa kumeneku nkuphunzitsa mwana ntchito? Ayi kumeneku nkuzunza mwana osati kumuphunzitsa ntchito, ayi. Munthu aliyense amakhala ndi nthawi komanso msinkhu womwe angagwire ntchito zamtundu wina wake osangoti basi tiyeni watopa azikapumira komweko, ayi, nkulakwa kwakukulu kumeneku. Chiyembekeza: Ana azipita kusukulu, osati kumunda Kodi vuto limeneli ndi lalikulu bwanji? Vutoli ndi lalikulu ndithu komabe poti tidayamba kale kudziwitsa anthu za nkhanza zopita kwa ana makamaka pankhani yowagwiritsa ntchito yoposa msinkhu wawo, anthu ena adamvetsetsa ndipo adasintha koma alipo ena omwe amakhulupirira kuti mwana safuna malipiro ambiri akagwira ntchito ndiye amaona ngati chidule kugwiritsa mwana ntchito kusiyana ndi munthu wamkulu. Koma zimakhala bwanji anawo sachita kukafunsira ntchitoyo okha? Tikudziwa za nkhani ya umphawi mmene ilili. Ana ambiri akhozadi kukafunsira ntchito okha kuti apezeko mwina chakudya komanso ndalama zodzithandizira kumavuto osiyanasiyana. Ambiri amakhala oti mwina alibe makolo kapenanso iwo ndiwo akuyanganira ana anzawo ndiye palibe chomwe angachite, pogwira alibe. Ambiri mwa ana omwe amakumana ndi nkhanza zamtundu umenewu ali mgulu limeneli. Nanga munthu utakhala ndi ndalama zolipira aganyu mwana uja nkukupeza kuti akufuna ganyu kuti athandizike ungatani? Apa mpamene pamabwerera mtima wa umunthu. Ngati munthu wamkulu uli ndi udindo wongothandiza mwanayo ngati uli ndi thandizo kapena kumuunikira kuti aike maganizo pasukulu osati maganyu. Ambiri mwa anawa amachokera mmadera momwe ifeyo timakhala ndipo mbiri yawo timayitsata tsono chotiletsa nchiyani kungowathandiza? Nanga poti anthu ena amagwiritsa ntchito ana awo omwe. Anthu oterewa sangadziteteze kuti ndi ufulu wawo poti mwanayo ndi wawo? Malamulo a dziko lino amaneneratu poyera kuti mwana aliyense apite kusukulu osati azikagwira ntchito mmunda, ayi. Palibe munthu yemwe ali ndi mphamvu zilizonse zosintha malamulo amenewa. Ngati lamulo likuti ichi ayi ndi ayi basi. Ndiye mukungodziwitsa anthu palibe zilango zake? Lamulo lililonse labwino limakhala ndi zilango zomwe olakwa angalandire ataliphwanya. Tikadzapeza munthu wolemba kapena kugwiritsa ana ntchito, tidzamutengera kubwalo la milandu komwe akagamulidwe potsatira zomwe malamulo akunena ndipo sitidzalola kuti anthu oterewa apatside ufulu wosalandira chilango.
3
KWAVUTA KUMSIKA WA NKHOTAKOTA Kunjatidwa kwa mkulu wina mboma la Nkhotakota kwavumbulutsa nkhani yosalana mumsika wa mbomali. Woyendetsa ntchito za polisi ya mbomali, Station Officer Mwiza Nyoni, watsimikiza za kunjatidwa kwa Shaban Nyambalo Mphepo, wa zaka 37, yemwe akuti adamutsekera pomuganizira kuti adabutsa malo omwe bambo wina, Joseph Kambwembwe, wa zaka 56, amagulitsirapo mbewa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Katundu woletsedwa mumsika wa Nkhotakota: Malo ena saloledwa kugulitsa mbewa ngati zili mumpanizi Akuti akumuganizira kuti adachita izi pofuna kukakamiza Kambwembwe kuti achoke pamalopo chifukwa amagulitsa malonda osaloledwa mumsikamo. Tamutsegulira mlandu wotentha malo mwadala zomwe zimatsutsana ndi ndime 337 ya malamulo a dziko lino. Malingana ndi zomwe tapezako, akuti mumsikawu adakhazikitsa lamulo loti onse ogulitsa nyama ya nkhumba ndi mbewa akhale ndi mbali yawo kunja kwa msika. Tikufufuza kuti adalamula izi ndi ndani koma akuti malo omwe anthuwo adapatsidwa ndi ochepa moti ena, ngati Kambwembwe, sadasamuke mumsikamo, zomwe zidapangitsa Nyambaloyo kukatentha malowo, adatero Nyoni. Koma Kambwembwe adauza Msangulutso Lachinayi lapitali palamya kuti iye wakhala akugulitsa mbewa pamalopo kwa zaka zambiri ndipo palibe chachilendo chomwe chidachitikapo mumsikamo kaamba ka malonda akewo. Iye adati akuona ngati nkhaniyi si yokakamira malo koma zifukwa zina zomwe iye sadazitchule ndipo adati zivute zitani, chomwe akufuna ndi katundu wake yemwe adaonongeka pachiwembucho. Chilungamo chimafunika paliponse kuti mtendere ukhalepo. Asandipusitse kuti nkhani ndi yokakamira pamalo ochitira malonda, ayi, chilipo chomwe chili kumtima kwawo koma sakuchinena. Zogawana mbali zidalephereka kalekale chifukwa akhonsolo adalephera kutipezera mbali enafe ndiye tizingokhala? Chomwe ine ndikufuna ndi katundu wanga yemwe adaonongedwa, basi, adatero Kambwembwe. Bwanamkubwa wa bomali, Felix Mkandawire, adati palibe munthu yemwe ali ndi mphamvu zothamangitsa mnzake mumsika chifukwa uli mmanja mwa khonsolo. Iye adatsimikiza kuti ofesi yawo idakamba nkhaniyi pofuna kukhazikitsa bata pakati pa anthu a mitundu ndi zipembedzo zosiyanasiyana ndipo adapereka nkhaniyo mmanja mwa apolisi kuti nawo aunike mbali yomwe ikuwakhudza. Mkandawire adavomera kuti khonsolo idalephera kupeza malo osamutsirako anthu ogulitsa nyama ya nkhumba ndi mbewa monga momwe amalonda ena amafunira ndipo adati sangaletse munthu kuchita bizinesi yomwe imamubweretsera ndalama. Anthu amayenera kugwira ntchito kapena kuchita bizinesi kuti adzizithandiza, ndiye ife sitingaletse munthu kuchita bizinesi. Ndipo chomwe chidatidabwitsa nchakuti anthuwa akuti sakuwafuna koma amadula matikiti a mumsika, adatero Mkandawire. Iye adadzudzula gulu lomwe lidachita zachiwembulo kuti lidalakwitsa potengera mphamvu mmanja mmalo mokadandaula kukonsolo, ngati eni a msika, kuti aone chochita. Bwanamkubwayu adati Kambwembwe adati katundu yemwe adamuonongera ndi wandalama zokwana K15, 000 ndipo munthu wina wakufuna kwabwino adapereka ndalamazo kukhonsolo kuti imupatse ayambirenso bizinesi yakeyo. Ndalamazo timupatsa lero (Lachinayi) komanso dzulo tidatuma anthu kukafufuza ngati malo apadera angapezeke ndipo atiuza kuti apeza malo omwe tikaikeko ogulitsa nyama ya nkhumba ndi mbewa kuti mwina ziwawa zithe, adatero Mkandawire.
15
Kulira kwanyanya mzipatala Kubangula ndi kulira mokweza kukumveka mzipatala za mdziko muno pomwe boma lachepetsa ndalama zopita kuntchito za chipatala potsatira mavuto a zachuma amene dziko lino likukumana nawo. Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe wavomereza za vutoli ndipo adati undunawo udalandira ndalama zochepa kuchokera ku nthambi ya za chuma. Chisale watuluka nkumangidwanso Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Odwala akuona masautso mzipatala Tikuyesetsa kuti tipeze ndalama zoonjezera ndipo pakadalipano tikuyankhula ndi mabungwe omwe angatithandize, adatero Chikumbe. Iye adati akuyembekezera kuti ayankhidwa mwezi uno kapena miyezi iwiri ikubwerayi. Zipatala zachepetsa ntchito zambiri makamaka mayendedwe a maambulansi komanso chakudya chikumaperekedwa kamodzi kapena kawiri patsiku mmalo mwa katatu. Dokotala pa chipatala cha Karonga Charles Sungani adauza Tamvani kuti achepetsa chakudya cha odwala kuchokera pa kudya katatu kufikira pa kawiri patsiku. Ambulansi nazo mafuta zilibe ndipo pakadali pano maambulansi akumangogwiritsidwa ntchito kunyamula amayi oyembekezera omwe ali ndi mavuto, adatero Sungani. Iye adati pofika sabata ya mawa mafuta amene ali nawo akhala atatha. Mmaboma a Mzimba ndi Nkhata Bay odwala akumadya chakudya kamodzi patsiku ndipo ambulasi zambiri zikungokhala kaamba ka kusowa kwa mafuta kuti galimotozo ziziyenda. Dokotala wamkulu mboma la Nkhata Bay Albert Mkandawire adadandaula kuti ndalama yomwe adalandira ndi yochepa kwambiri kuti ithandizire zipatala zonse mbomalo. Talandira K4.8 miliyoni yomwe ikuyenera kupita ku zipatala zoposa 20. Ndalama imeneyi ndi yochepa kwambiri kuti itithandize pantchito za pachipatala, adatero Mkandawire. Ngakhale zinthu zili choncho mmaboma ena, monga la Dedza, sadalimve kuwawa kwambiri vutoli chifukwa aphungu a Nyumba ya Malamulo awo adagwirana manja ndi kuthandizapo. Mneneri wa chipatala cha Dedza, Arnold Mndalira, adati achipatala adawauza aphunguwo za kuchepa kwa ndalama zomwe zidabwera kuchoka kuboma. Mndalira adati apa aphunguwo adasonkherana limodzilimodzi ndi kuonjezera ndalama pachipatalapo. Adapereka K2.4 miliyoni yomwe theka lidapita ku chakudya ndipo theka lina lidapita ku mafuta a galimoto, iye adatero.
6
Wopha Wame akasewenza moyo wake wonse Bwalo la milandu lalikulu mboma la Salima Lachitatu lidagamula Limbani Maliro, mnyamata yemwe adapha Mlaliki Shadreck Wame kukasewenza moyo wake wonse. Bwalolo lomwe lidalowa nthawi itangodutsa 6 koloko ya madzulo lidapereka chigamulochi mnthawi yosakwana ola limodzi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Adachita chobaya: Wame Apa nkuti Maliro ali zyoli pomwe makutu a anthu a nkhaninkhani omwe adafika kubwaloli kukamvera mlanduwu adali tcheru. Bwaloli lidadzadza moti ena mwa anthuwo adaima panja kutsatira zochitikazo kudzera mmazenera. Naye woweruza Esmie Chombo sadachedwe ndi zambiri koma kungolunjika mpaka kupereka chigamulocho chomwe chidaliza mayi ake a Maliro. Ndipo khope yake ili chigwere, Maliro yemwe adalibe omuimira pamlandu adapempha Chombo kuti amumvere chisoni chifukwa ndi wachichepere, ali ndi banja komanso amathandiza abale. Koma popereka chigamulo chake, Chombo adati Maliro akuyenera kusewenza moyo wake wonse chifukwa mlandu womwe adapalamula ngwaukulu wosayenera munthu wachichepere. Iye adatinso naye Wame adali ndi abale omwe amawathandiza moti ana ambiri omwe amawalipirira fizi pano apita msukulu zosakhala bwino chifukwa akulephera kukwanitsa kupeza fizi. Malinga ndi mneneri wa polisi mboma la Salima, Gift Chitowe, Maliro adauza bwalo la milandulo kuti adapha Wame poganizira kuti amasunga ndalama zambiri mnyumba mwake. Atadya mutu poona katundu yemwe Wame amabweretsa pakhomopo, Maliro adaganiza zomupha kuti amubere bwino. Patsiku lomwe adamuphalo Maliro adagwidwa ndi matumba a chimanga omwe adanyamula pa wilibala usiku. Koma mwatsoka adawathawa anthuwa pomwe ankagogoda pa nyumba ya a Wame kuti afufuze ngati adampatsadi chimangachi, adalongosola Chitowe. Iye adati Maliro adapepesa pa zomwe adachita ndipo amaoneka wokhudzika mnthawi yonse ya mlanduwu. Wame adaphedwa mwezi wa October, chaka cha 2016 ndipo Maliro dagwidwa patadutsa mwezi, mboma la Thyolo. Lolemba lapitali iyeyu adavomera kuti adaphadi Wame.
7
Mtsutso pa masiku a chisankho Mtsutso wabuka pa za masiku a chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chomwe chikuyembezeka kuchitika pa May 19 chaka chino. Pamene ena akuti masiku ndi okwanira, ena akutsutsa kaamba koti chisankho chimalira zambiri. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Jane Ansah: Mtsogoleri wa MEC Chisankhochi chikuyenera kuchitika pa May 19 2020 potsatira chigamulo cha khothi choti chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chichitikenso mmasiku 150 kuchokera pa February 3 2020 litapeza kuti chisankho cha pa May 21 2019 sichidaye bwino. Katswiri wa ndale George Phiri wati masikuwa ndiwokwana kuchititsa chisankho. Kupanda kupanga chisankho mmasikuwa ndiye kunyozera chigamulo cha khoti. Chofunika nkusankha akuluakulu oyendetsa zisankho mmasiku 10 akudzawa pambuyo pake kuchititsa kalembera mmasiku 30 kwinako nkosavuta chifukwa zambiri anthu akuzidziwa kale, adatero Phiri. Koma mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Justice Network (Mesn) Steve Duwa adati masiku 78 ndiosakwanira. Bungwe loyendetsa zisankho likuyenera kukhala ndi akuluakulu atsopano, komanso pali ndondomeko zina zomwe ziyenera kutsatidwa, watero Duwa. Komiti ya ku Nyumba ya Malamulo yoona zosankha anthu mmaudindo ena a mboma ya Public Appointments Committee (PAC) idapempha mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti achotse ntchito akuluakulu a Malawi Electoral Commission (MEC) omwe adayendetsa zisankho za pa May 21 2019 kaamba koti adasokoneza zinthu. MEC idapepha khoti kuti lionjezere masiku ochititsa zisankho, koma lidakana.
11
Kudali kumapemphero Mawu a Mulungu amati: Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za mkachisi amadya za mkachisi Mawu a Mulunguwa adakwaniritsidwa pomwe Rose Cross adakumana koyamba nkudyererana maso ndi Ephod Mahorya kumapemphero. Panthawiyo Rose ankapembedza kumpingo wa Living Word ndipo Ephod adali wa mpingo wa Church of Nazarene. Ngakhale ankapemphera kumipingo yosiyana, awiriwa ankakumana kumapemphero mkati mwa sabata. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tsopano ndi thupi limodzi: Rose ndi Ephod patsiku la ukwati wawo Rose ndi woyamba kubadwa mbanja la ana atatu ndipo akugwira ntchito ku unduna wa zofalitsa nkhani komwe ndi mtolankhani wa Malawi News Agency (Mana), pomwe Ephod ndi wachitatu kubadwa mbanja la ana asanu ndi awiri ndipo amagwira ntchito ngati msungichuma kubungwe la Compassionate Stewards. Rose adati iwo atakumana adayamba kucheza ngati munthu ndi mnzake koma kumapeto kwa chaka cha 2013 ndi pomwe Ephod adamumasulira Rose za chikondi chomwe chinkasefukira mumtima mwake iye ndipo Rose naye adaulula za mumtima mwake. Uku kudali kuyamba kwa chikondi chawo. Awiriwa adamanga ukwati woyera mumzinda wa Mzuzu pa 4 July chaka chino ndipo mwambo womanga banjalo udachitikira ku Church of Nazarene kenaka madyerero adachitikira ku Victory Temple komwe anthu adachita perekaniperekani wamphamvu nkudyerera ndi kumwerera mwachimwemwe. Ephod amachokera mmudzi mwa Mumbo, mfumu yaikulu Jenala mboma la Phalombe, pomwe Rose ndi wa mmudzi mwa Yohane Jere, Inkosi Mtwalo, mboma la Mzimba. Ndimamukonda Ephod, makamaka chifukwa cha mtima wake wokonda Mulungu, komanso ndi munthu wachikondi kwambiri ndipo satopa kuthandiza anthu ovutika, adatero Rose monyadira. Ephod naye sadabise mawu. Adati amamukonda Rose kaamba ka khalidwe lake labwino ndi mtima wake wansangala komanso wachikondi.
13
Kwaya ya St. Paul Ithandiza Odwala, Ovutika Kwaya ya achinyamamata ya St. Paul kuchokera ku St. Pius Parish ku Soche mu archdiocese ya Blantyre, lolemba yathandiza ena mwa akhristu a mu parishiyi ndi zinthu zisiyanasiyana zomwe amasowa pa moyo wawo. A Lucky Simwaka omwe ndi wapampando wa kwayayi ati iwo ngati achinyamata anawona kuti ndi kofunikira kuthandiza anthu omwe akusowekera zinthu zomwe zingathandize moyo wawao kuti upite patsogolo, ndi kangache komwe ali nako. Ife ngati kwaya ya achinyamata komanso pamene tinabatidzidwa ndi kutumidwa titamva kuti ena mwa akhristu amzanthu akusoweka zinthu zomwe zingathe kupititsa moyo wawo patsogolo, gulu lathu linagwirizana zothandiza anthuwa pogula zithu monga ma teyala anjinga komanso mankhwala a shuga zomwe tapereka kwa akhristu, anatero a Simwaka. Mwazina a Simwaka anayamikira mamembala a kwayayi kaamba kowonetsa chidwi pothandiza anthu ena. Mmodzi mwa athu omwe alandira nawo thaandizoli a Brian Mhango ayamikira zomwe gululi lawachitira. Ine ndikungothokoza kwayayi pazomwe yachita. Yapangitsa kuti mayendedwe anga akhale osavuta makamaka pondigulira zipangizo za njinga. Poyamba ndimavutika kuti ndiyende maka zipangizo za njinga yanga zinali zoonongeka tsono kubwera kwa thandizo limeneli kwachepetsa nkhawa yanga, anatero a Mhango. Kwaya ya St. Pauls ndi kwaya ya achinyamata yomwe ili pansi pa kwaya ya St. Pius ku St. Pius Parish mu arch diocese ya Blantyre ndipo mwa zinthu zina zomwe kwayayi inagula ndi kukathandiza nawo akhristu zinali monga mateyala komanso chubu cha njinga yakapalatsa, mankhwala komanso ufa.
14
Bullets iphana ndi Wanderers lero Ambiri adakamba kuti mwina masewero a lero pakati pa Bullets ndi Wanderers mu TNM Super League alephereka ponena kuti osewera akukatumikira Flames, koma izo ndi nkhani yakale chifukwa lero ntchito ilipo pa Kamuzu Stadium. Kochi wa Flames Ernest Mtawali Lachinayi adawalola osewera kuti akatumikire matimu awo. Osewerawo adangololedwa kuti asewere masewero alero ndipo abwerere ku Flames madzulo alero. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Bullets idachinya Wanderers mndime yoyamba 2-1 ndipo Wanderers idabweza chipongwe mu Carlsberg Cup pamene idapambana 2-1. Lero kamuna ndani? Mphunzitsi wa Wanderers Elijah Kananji akuti timu yake yakonzeka ngakhale palibe osewera monga Jabulani Linje ndi Rafiq Mussa chifukwa chovulala. Pamene Mabvuto Lungu wa Bullets akuti nawonso akonzeka komabe timu yawo isowa ntchito za Chiukepo Msowoya, Owen Chaima ndi Vincent Gona chifukwa chovulala pamene Sankhani Mkandawire wabwerera.
16
Chitetezo chaphwasuka Chitetezo chaphwasuka. Anthu akuberedwa, kumenyedwa ndi kuchitidwa zachipongwe zambiri. Akaitanitsa apolisi akuti akumatenga nthawi kuti abwera ndipo nthawi zina sabwera. Izi zikukhumudwitsa anthu ndi mafumu. Koma wachiwiri kwa mneneri wa polisi mdziko muno, Thomeck Nyaude, watsutsa nkhaniyi. Iye wati apolisi akalandira uthenga sanyozera, koma amathamangira komwe kwavutako. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kawinga kulankhula ndi mtolankhani wathu akutuluka ku chipatala cha Mwaiwathu T/A Nyambi ya mboma la Machinga yati chidodo cha apolisi ndicho chikuchititsa kuti anthu azilanga okha akagwira munthu yemwe akumuganizira kuti ndi wamtopola. Nyambi amathirira ndemanga pa nkhani yoti anthu okwiya adazunza atolankhani a BBC ku Karonga powaganizira kuti ndi anamapopa. Anthu adamenya atolankhaniwo, kuwalanda zipangizo zawo ndi kuswa galimoto yawo. Izi zidachitika kwa maola oposa 7, koma apolisi sadatulukire. Nako ku Machinga akuba adathira machaka mfumu Kawinga nkuibera ndalama zoposa K1 miliyoni, koma akuti apolisi sadalanditse mfumuyo ngakhale adadziwitsidwa. Koma Nyaude watsutsa ndipo wati anthu ambiri sadziwitsa apolisi zikawathina. Ndife anthu sitigwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga. Timadalira kuuzidwa ndipo ngati sadatiuze ndiye tigwira ntchito bwanji? Iye wati nkhani ya atolankhani a BBC idakhota chifukwa atolankhaniwo sadawadziwitse kuti akutsikira mmidzi ya Karonga. Adangopita kuderako osatidziwitsa. Amangoganiza kuti zinthu zili bwino, ndiye masiku ake si anowa. Atolankhaniwo, Dariud Gregory Barzagan, Ahmed Hussein Divela ndi Prince Anus Asamoah adathambitsidwa ndi anthu olusa a mdera la Malema pamene amalemba nkhani zokhudzana ndi matsenga. Iwo adatsogozedwa ndi mtolankhani wa mdziko muno Henry Mhango komabe izi sizidasinthe kanthu pamene anthu ammudziwo adaloza zala atolankhaniwo kuti ndi anamapopa. Nkhani zomwe amalembazonso zidali zosavuta kuti anthu alumikize ndi nkhani zopopa magazi. Amayenera atidziwitse kuti tikhale tikuponyako maso, adatero Nyaude. Pa nkhani ya kuvulazidwa kwa mfumu Kawinga yomwe idalephera kuthandizidwa ndi apolisi, Nyaude wati palibe amene amayembekezera kuti izi zichitika. Palibe amayembekezera kuti izi zichitika, kudalinso kovuta kuti tidziwe kuti tikalanditse mfumu yathu. Tidakauzidwa, tidakathandiza, tiyeni tidalirane, adatero Nyaude. Koma mkulu wa bungwe loona za ufulu wachibadwidwe wa anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Timothy Mtambo, wati vuto ndi apolisi komanso boma amene akulephera kuteteza anthu. Takhalapo ndi nkhani zopopa magazi komanso kupha anthu achialubino zomwe anthu samakhutira ndi momwe apolisi amagwirira ntchito. Nchifukwa chake anthu akumalanga okha zotere zikachitika, adatero Mtambo. Iye adati mavutowa akudza chifukwa apolisi akulephera kugwira bwino ntchito ndi anthu kuti azithandizira kubweretsa chitetezo. Tili ndi nkhani zambiri zomwe mutu wake sudziwika ndipo chomwe timamva ndi kuti akufufuza. Izitu ndi zomwe anthu alibenso chikhulupiriro ndi polisi yathu, adatero. Padakali pano, mfumu Kawinga yatulutsidwa mchipatala cha Mwaiwathu ku Blantyre komwe yakhalako sabata zitatu. Mfumuyi idaomberedwa pamwendo kawiri, kukhapidwa ndi chikwanje paphewa, pamkono komanso kumenyedwa ndi chitsulo pamwendo. Polankhula ndi Tamvani sabata yatha, Kawinga adati akubawo adaomberanso mlonda wake komanso kuvulaza mwana wake. Izi zimachitika atandibera K1 miliyoni komanso 200 euros. Adaphwanyira galimoto ziwiri, adatero.
7
Lamulo lochotsa mimba ladengula Akufuna ogwiriridwa, opatsana pathupi pachibale ndi ana achichepere aziloledwa kuchotsa pathupi Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lamulo lokhudza kuvomereza kuti amayi akhoza kumachotsa mimba movomerezeka latsala pangono kupita ku Nyumba ya Malamulo kuti aphungu akalikambirane, Msangulutso watsinidwa khutu. Mlangizi wa mmene ntchitoyi ikuyenera kuyendera kubungwe lomwe likulimbikitsa kuti boma livomereze kuchotsa mimba popanda mlandu la Coalition on Prevention of Unsafe Abortions (Copua), Luke Tembo, wati kukonza lamuloli kudatha kale ndipo kwatsala kuti aphungu akalikambirane. Tidasiya nkhaniyi mmanja mwa nthambi ya zamalamulo (Law Commission) kuti aunike lamulo lomwe lidalipo kale ndipo tikunena pano lamulo lina lidatha kale kukonzedwa ndipo likungodikira kupita ku Nyumba ya Malamulo, adatero Tembo. Wothandizira ntchito zounika malamulo kuthambi ya zamalamulo, Mtamandeni Liabunya, Lachisanu adatsimikiza kuti nthambiyi idamalizadi kukonza lamulo latsopanoli ndipo kwatsala kuti liyende mundondomeko zina lisadasindikizidwe. Zonse zoyenerera zidachitika kale ndipo tidamaliza, pano tikungoyembekezera kuti tikatule kuunduna woona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi komanso chisamaliro cha ana kuti ndondomeko izipitirira mpaka ku Nyumba ya Malamulo, adatero Liabunya. Nduna yoona kuti pasamakhalae kusiyana pakati pa amuna ndi amayi komanso chisamaliro cha ana, Patricia Kaliati, adati unduna wake sukudziwapo kanthu pa za lamulo latsopanoli. Kaliati: Sitingalole zimenezo Iye adati ali ndi njala yoona lamulolo kuti aone ngati zomwe zilimo zikugwirizana ndi zolinga za boma pa za tsogolo ndi moyo wa amayi ndi asungwana. Nkhaniyitu okhudzidwa kwambiri ndi amayi ndi asungwana ndiye ife ngati unduna wa boma, sitingalole chilichonse chomwe chikusemphana ndi mfundo za boma zotukulira amayi ndi atsikana. Atipatse tilione lamulolo ndipo tiliunike, adatero Kaliati. Bungwe la Copua likulimbikitsa zobweretsa lamulo latsopanoli pofuna kuchepetsa imfa za amayi ndi asungwana komanso ana chifukwa cha njira zochotsera mimba zamseri poopa kuti kuchipatala sakaloledwa komanso angaimbidwe mlandu wofuna kupha. Tembo adati lamulo lakale limangolola munthu kuchotsa pathupi pokhapokha ngati pali umboni wakuti moyo wa mayiyo kapena mwana uli pachiopsezo. Koma lamulo latsopanoli laonjezerapo zifukwa zina zochotsera mimba. Lamulo latsopanoli lawonjezera zifukwa zina zomwe munthu angathe kuchotsera mimba, monga mimba yobwera kaamba kogwiriridwa; mimba yopatsana pachibale; mimba zopatsana ana [osakhwima pamchombo]; komanso amisala aziloledwa kuchotsa mimba, adatero Tembo. Kaliati adati unduna wake sugwirizana ndi ganizo lovomereza kuchotsa mimba kaamba kakuti uku nkuphwanya ufulu wa mwana wosabadwayo. Iye adati akudziwa zoti magulu ena akulimbikitsa zokhazikitsa lamulo lovomereza kuchotsa pakati, koma boma lidanena kale poyera kuti kuteroko nkusokeretsa mtundu wa Amalawi, makamaka asungwana. Kodi kuuza anthu uti akhoza kumachotsa mimba mmene afunira ndiye kuti tikumanga dziko lanji? Zimenezi zikhoza kuchititsa kuti anthu, makamaka asungwana, atayirire podziwa kuti akatenga mimba akachotsa, adatero Kaliati. Iye adati boma limangovomereza lamulo lomwe lilipo pakalipano lomwe lidayamba kuonetsa mphamvu mchaka cha 2010. Lamuloli limalola munthu yemwe moyo wake uli pachiwopsezo kuchotsa pathupi. Wapampando wa komiti ya aphungu achizimayi mNyumba ya Malamulo, Jessie Kabwila adati komitiyi iyambe yaona lamulo lomwe lapangidwalo ndi mfundo zake. Tione kaye mfundo zomwe zili mulamulolo nkukambirana chifukwa mukomiti mumakhala anthu amaganizo osiyanasiyana. Ena amakhulupirira kuti kuchotsa mimba nkupha pomwe ena amazitengera paufulu wa anthu ndiye mpofunika titagwirizana chimodzi ngati komiti, adatero Kabwira. Iye adati kupatula kusemphana maganizoku, nkhani yochotsa mimba njofunika kuyiona bwino chifukwa amayi ambiri akutaya miyoyo yawo tsiku ndi tsiku kaamba kochotsa mimba. Mneneri wa polisi mdziko muno Rhoda Manjolo adati imfa zokhudzana nkuchotsa mimba zikuchuluka akatengera mmabuku a kupolisi. Iye adati malingana ndi kafukufuku wa polisi, ambiri mwa amayi ndi asungwana omwe amachotsa mimba amachita izi kaamba ka mantha kapena kukhumudwitsidwa ndi omwe adawapatsa mimbazo.
7
Papa Wayamikira Ansembe, Madotolo Potumikira Anthu Modzipereka Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wayamikira ansembe ndi madotolo chifukwa chotumikira anthu modzipereka. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican Papa walankhula izi lamulungu ku likulu la mpingo ku Vatican, tsiku lomwe mpingo umachita chaka cha Yesu Khristu Mbusa Wabwino. Papa Francisko Iye wayamikira ansembewa komanso madotolo chifukwa chokhala abusa abwino potumikira anthu modziyiwala iwo eni. Mmawu ake kumayambiriro a Misa yomwe anatsogolera mtchalichi lalingono la Casa Santa Marta kulikulu la Mpingo ku Vatican, Papa Francisco wathokoza ansembe ndi madotolo chifukwa chotumikira anthu modziyiwala mpaka kuika miyoyo yao yomwe pa chiswe mu nyengo iyi yomwe dziko lapansi lili pa mliri wa Coronavirus. Iye wati potumikira anthu mwa toto moyo ansembe komanso madotolowa aonetsa kuti naonso ndi abusa abwino polola kuika miyoyo yao pa chiswe chifukwa chofuna kuthandiza anthu. Papa Francisco wati ansembe oposa 100 komanso madotolo pafupi 154 mdziko la Italy lokha amwalira akutumikira anthu pa nthawi ya mliri wa Coronavirus kusonyeza poyera kuti ndi Abusa Abwino. Iye wati Yesu Khristu ndiye Mbusa wabwino amene adalola kusenza machimo a anthu onse mpaka kutaya moyo wake pa mtanda pofuna kupulumutsa anthu. Iye wati abusa onse akuyenera kutengera chitsanzo cha Yesu Khristu. Papa Francisco sadabise mau ponena kuti achulukirenji abusa a chinyengo masiku ano amene cholinga chao mwa zina ndi ndalama komanso kufuna ma udindo. Koma iye wati chosangalatsa nchakuti akhristu amadziwa kusiyanitsa pakati pa abusa enieni ndi abusa a chinyengowa. Iye wati mbusa akuyenera kumamvetsera komanso kudziwa nkhosa zake. Ndipo mu uthenga wake wa chaka chino pa za chiitanidwe, Papa Francisco wati Mpingo ukuyenera kupitiriza kulimbikitsa anthu kuti avomere chiitanidwe ku magawo osiyana-siyana a moyo wa chikhristu. Mu uthengawo iye watinso moyo uliwonse wa chiitanidwe usowa kulimba mtima, kupirira komanso kulimbika mmapemphero popeza zovuta nzambiri poyankha kuitana kwa Mulungu.
13
Obera malova akuchuluka Akapsala obera achimata amapepala awo powalonjeza ntchito zomwe chikhalirecho palibepo akuchulukirabe mmizinda ngakhale kuti apolisi ndi unduna wa zantchito akulimbana ndi mchitidwewu. Kumapeto a mwezi wathawu, pa 29 August, apolisi mboma la Mchinji adagwira Yohane Chimkumbi, wa zaka 32, wa mmudzi mwa Ndeleya kwa T/A Mamvere pomuganizira kuti adadya ndalama zokwana K87 000 atanamiza achinyamata 6 kuti awalemba ntchito mbungwe lake, koma adati aliyense ayambe wapereka K10 000. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi mbomali, Rome Chauluka, adati mkuluyu akuti adauza achinyamatawo kuti pali bungwe lotchedwa Young Advocacy lomwe likufuna anthu oti liwatumize mmadera osiyanasiyana kukagwira ntchito. Munthuyu adangobwera nkuyamba kuuza achinyamata kuti pali mwayi wa ntchito ndiye mwina ndi ulovawu aliyense akusakasaka mwayi wa ntchito kotero kuti atawauza kuti apereke K10 000 aliyense adangoona ngati mwayi wapezeka, adatero Chauluka. Akuti amati akamufunsa amanena masitetimenti osiyanasiyana monga oti akungodikira mabwana ake kuti amumasule kulemba achinyamatawo koma ataona kuti payamba kutentha, iye adathawa kuderalo, adatero Chauluka. Sabata zingapo zapitazo, Tamvani idasokolotsa nkhani ya akamberembere ena omwe amanka mmizinda kukhoma zikalata zoti akufuna achinyamata omwe akusowa ntchito koma atafufuza adapeza kuti nkhani yake idali yomweyi yofuna kuwabera. Wapampando wa bungwe loyendetsa mabungwe a achinyamata la National Youth Council of Malawi (NYCOM), Aubrey Chibwana adati vutoli lingathe achinyamata atakhala ndi mtima wongogwira ntchito modzipereka ngakhale asadamalize maphunziro awo ndi cholinga choti asadzavutike kupeza ntchito mtsogolo.
2
Ulangizi wa pafoni uthandiza alimi Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndizachidziwikile kuti dziko la Malawi limadalira ulimi pa chuma chake ndipo ambiri mwa alimi mdziko muno ndi alimi a minda ingonoingono omwe amadalira alangizi kuti awafikire ndi njira komanso luso la makono pa ulimi. Nawonso akatswiri a za ulimi omwe akukangalika kuchita kafukufuku pofuna kupeza njira komanso luso la makono paulimi amadaliranso alangizi kuti afikire alimi ndi luso ndi njira za makonozi. Koma ngakhale izi zili choncho, ntchito za ulangizi zikukumana ndi mavuto ochuluka monga mlili wa Edzi, kuchepa kwa zipangizo zogwiritsa ntchito, ufulu pankhani za misika komanso ufulu wa demokalase kungotchulapo ochepa. Kupatula zonsezi, onse okhuzidwa ndi ntchito za ulangizi akhala akutsatira njira za ulangizi zodalira kuti mlimi ndi mlangizi akumane maso ndi maso. Pofuna kuchepetsa ena mwa mavutowa polingaliranso kuti chiwerengero cha alangizi chikuchepa, unduna wamalimidwe kudzera ku nthambi ya ulangizi mogwirizana ndi mabungwe omwe siaboma, adakonza msonkhano wokambirana zolimbikitsa ulangizi pogwiritsa ntchito luso lamakono pogwiritsa ntchito malo oimbira foni kapena kuunguza zinthu pa Internet. Msonkhanowu udachitikira ku Malawi Institute of Management mumzinda wa Lilongwe ndipo udabweretsa pamodzi akatswiri kuchokera ku unduna wa zamalimidwe, sukulu za ukachenjede za Luanar komanso NRC ndi makampani komanso mabungwe a Self-Help Africa, TNM, Airtel, Farm Radio Trust, Technobrain, atolankhani, alimi komanso ena ambiri. Zolinga za msonkhanowu zidali zitatu. Cholinga choyamba chidali kukhazikitsa masomphenya a kayendetsedwe ka malo olandira ndi kupereka mauthenga a ulangizi (call centre). Chachiwiri chidali kugawana nzeru pakayendetsedwe ka malowa. Chomaliza chidali kupangana momwe dongosolo la malowa liyendere kuno ku Malawi. Akatswiri osiyanasiyana adapereka maganizo awo pakayendetsedwe ka malo amenewa. Call centre ndi malo omwe alimi amene ali ndi foni za mmanja amatha kuimba kapena kutumiza mauthenga kufuna kupeza ulangizi ndipo akatero amalandira mayankho malingana ndi zomwe adafunsa. Yemwe adatsogolera kupereka maganizo ake adali mkulu wa kampani ya foni za mmanja ya Airtel. Atatha mkulu wa Airtel, padabwera anthu asanu ndi awiri omwe adaperekanso maganizo awo motsatizana. Anthu adaloledwa kufunsa mafunso ndi kupereka ndemanga pa zomwe akuluakuluwa adalankhula. Pamapeto pa zokambirana, anthu onse adagwirizana kuti njira yogwiritsa ntchito malowa yingathandize kwambiri kupereka ulangizi kwa alimi makamaka pano pomwe chiwerengero cha alimi chikuchuluka kuyerekeza ndi alangizi. Pali chiyembekezo choti malowa athandiza kutukula nchito za ulimi popereka ulangizi woyenera panthawi yake. Ndipo poyankhula pa mwambowu, mmodzi mwa akuluakulu mu unduna wa za malimidwe yemwenso adali mlendo wolemekezeka pa mwambowu Dr Wilfred Lipita adati iye akukhulupilira kuti umphawi ukupita mtsogolo pakati pa alimi kaamba kosowa uthenga wokwanira ndipo podzindikira kufunikira kogwiritsa ntchito njira zamakono pa ulangizi, unduna wake wakhazikitsa komiti yapadera yoonetsetsa kuti luso lamakono likugwiritsidwa ntchito bwino pa ulangizi yotchedwa the National Agricultural Content Committee for ICT. Ngati unduna, tikudzindikira kufunikira kogwiritsa ntchito luso lamakono pa ulangizi kotero takhazikitsa komiti yapadera yoonetsetsa kuti pasakhale chisawawa pogwiritsa ntchito luso lamakono pa ulangizi,adatero Lipita. Ngati muli ndi mafunso kapena ndemanga pa nkhaniyi, lemberani kalata kapena kuimba lamya kwa: Head Extension Department P. O. Box 219 Lilongwe 01 277 260.
4
Si zonyengerera mu 2016Mkulu wa polisi Anthu ali kalikiriki kukonza mapulani a chaka chatsopano cha 2016 koma ngati mapulani ake akukhudza umbanda ndi ziphuphu, dziko lake si lino, waneneratu mkulu wa Polisi mdziko muno, Lexten Kachama. Kachama adalankhula izi pa 31 December 2015 pomwe apolisi amakondwerera chaka chatsopano kulikulu la polisi ku Area 30 mumzinda wa Lilongwe. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lexten Kachama Chaka cha 2016 chikhala chaka cha chitsanzo pankhani yolimbana ndi mchitidwe wa uchifwamba, umbanda ndi ziphuphu. Tithana ndi zigawenga zonse komanso onse omwe akufuna kulemera kudzera mziphuphu, adatero Kachama. Iye adati mchaka cha 2015, apolisi adayesetsa kulimbana ndi mchitidwe wa uchigawenga ndi umbanda koma ngozi za pamsewu zidakwera ndi 18 pangozi 100 zilizonse kuyerekeza ndi mchaka cha 2014. Kachama adati chimodzi mwa zifukwa zomwe zidachititsa izi ndi ziphuphu zomwe apolisi ena apamsewu amalandira kuchokera kwa eni galimoto zosayenera kuyenda pamsewu. Nkhani ya ziphuphu ndi imodzi mwa nkhani zomwe apolisi amatchuka nazo makamaka pamsewu. Komabe ndinene pano kuti si apolisi onse omwe amachita izi koma apolisi ochepa chabe adyera, adatero Kachama. Iye adati chaka chino akhwimitsa chilango chomwe apolisi opezeka ndi mlandu wa ziphuphu amalandira ndipo adachenjezanso anthu omwe amakopa dala apolisi ndi ndalama kapena zinthu zina kuti awatsekere milandu yawo. Malinga ndi kafukufuku wathu, wapolisi wongolembedwa kumene ntchito, maka amene ali ndi satifiketi ya fomu 4, amalandira ndalama zosaposera K50 000 asanaduleko msonkho. Ndi mmene mitengo ya zinthu ilili panopa, nkosatheka kuti munthu akwaniritse zofunika pamoyo wake wa tsiku ndi tsiku ndi malipiro achepa ngati awa poganizira chakudya, nyumba ya lendi, fizi ya ana asukulu, zovala ndi zina zotero zofunika pamoyo wa munthu. Mwina ichi nkukhala chimodzi mwa zifukwa zomwe mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu watenga malo pakati pa apolisi. Kachama adalonjeza kuti apolisi ayesetsa kugwira ntchito yokomera anthu koma adati kuti izi zitheke, anthu akuyenera kutengapo gawo makamaka potenga apolisi ngati abwenzi awo powatsina khutu akawona zodabwitsa mmadera momwe akukhala. Pothirapo ndemanga, mkulu wa bungwe loona za maufulu a anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Timothy Mtambo, adati uthenga wa mkulu wa polisiyu wafika panthawi yoyenera pomwe malingaliro a zauchifwamba za mu 2015 akadali mmitima. Iye adati mchaka changothachi, uchifwamba udakula mpaka apolisi kumaphedwa ndi zigawenga zomwe zimadetsa anthu nkhawa pazachitetezo cha moyo ndi katundu wawo. Chitetezo ndiye gwero la chitukuko cha mtundu uliwonse. Mabizinesi, zipembedzo, ufulu wa anthu ngakhaleso zomangamanga zimayenda bwino pakakhala chitetezo chokwanira chifukwa anthu amapanga zinthu mtima uli mmalo, adatero Mtambo. Iye adati pulani ya apolisiyi singatheke pokhapokha boma litaikapo mtima powapatsa zipangizo zokwanira zogwirira ntchito yawo komanso kuwaganizira pankhani ya umoyo ndi makhalidwe awo. Mwa zina, Mtambo adati apolisi amasowa chilimbikitso kaamba kakuti malipiro omwe amalandira ndi ogwetsa mphwayi, zomwe zimawafoola nkhongono; nyumba zomwe amakhalamo nzosaoneka bwino; komanso amagwira ntchito popanda zodzitetezera. Nthawi zina apolisi amalephera kupita kukagwira ntchito yawo kaamba kosowa mayendedwe chifukwa cha nkhani za mafuta komanso galimoto. Apolisi amapezeka kuti akugwira ntchito mmalo a zipolowe koma alibe zodzitetezera, choncho sangagwire ntchito momwe akadagwirira chifukwa nawo ndi anthu, amafuna kudziteteza, adatero Mtambo.
7
Nseula, Banda smile at Nampak Golf Charles Nseula and Carol Banda on Saturday contributed to the lineage of Nampak Golf Tournament champions and became the first titleholders since the company rebranded from Packaging Industries Limited (PIM) last year. The two proved good enough to take home glory in the men and ladies categories respectively during the 17th edition of the contest at Mulanje Golf Club, which was patronised by 60 golfers. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi With 41 individual stable-ford points, Nseula counted out the clubs golf captain Ajay Singh to the second slot as Sophie Kaira settled for the third place with 40 points. This is my special day; I played very well and I was consistent with my swing. I had a string of pars on the front nine. I was not surprised when I emerged victorious. Hard work has paid for me today, said Nseula, who has added a fourth trophy this year alone. On the flipside, Banda, who collected 40 points, three points ahead of her runner-up Beatrice Mangwana, attributed her success to some great shots on the fairway. I had a shaky start but some fantastic shots on the back-nine made up for that. Double strokes on some last holes gave me the much needed points for success, she said. John Gift Mwakhwawa did it in the mens category. Burdon Mbera took the nearest to the pin accolade while Harry Mukaka and Chris Kapanga claimed the best front-nine and back-nine awards with 22 points and 20 points in that order. Nampak marketing manager Nyakhoko Nsona said the main purpose of the golf competition was to promote the game and thank customers, including those working in the tea industry, for the business they give us.
16
Wosamutsa Dzina la Chilima Afa pa Ngozi ya Pansewu By Thokozani Chapola Munthu mmodzi wafa galimoto yomwe anakwera itawomba truck pa Linthipe 1 mboma la Dedza. Ngozi yomwe yapha mnyamatayo Mneneri wa apolisi mboma la Dedza, Cassim Manda watsimikiza za ngoziyi polankhula ndi Radio Maria Malawi ndipo wati amene wafayu ndi Sailas Kampango wa zaka 26 zakubadwa. Iye wati galimotoli lomwe nambala yake ndi RU 6494 limayendetsedwa ndi a Kalipo Mhango imachokera ku Lilongwe kulowera ku dedza ndipo itafika pa Linthipe 1 inawomba kumbuyo kwa truck yomwe inali itangoyima yomwe nambala yake ndi CK 4754 ndipo ngolo yake ndi CK 3075. Kutsatira izi a Sailasi Kampango anafera pa malo pomwepo kaamba koti anavulala kwambiri mmutu. Malipoti ena akusonyeza kuti omwalirayu ndi amene amamuganizira kuti anasamutsa dzina la a Saulosi Chilima kuchoka ku Lilongwe kupita ku Chizumulu Island pa chisankho chomwe changothachi. Sailas Kampango amachokera mmudzi mwa Kasinje mfumu yaikulu Ganya mboma la Ntcheu.
11
Paramount Chief Ngolongoliwa Amwalira, Ayikidwa Lachitatu Wolemba: Thokozani Chapola oads/2019/07/IMG-20190728-WA0129.jpg 600w" sizes="(max-width: 290px) 100vw, 290px" />Mfumu yaikulu ya Alhomwe-Ngolongoliwa Mfumu yaikulu ya mtundu wa alhomwe, Paramount Chief Ngolongoliwa yamwalira. Wofalitsa nkhani ku unduna woona za maboma aangono ndi chitukuko cha madera akumudzi Mulhabase Mughogho watsimikiza za nkhaniyi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Iye wati mfumuyi yamwalira lamulungu pa 28 July 2019 ku chipatala cha Mwayiwathu mu mzinda wa Blantyre atadwala kwa nthawi yaitali. Mwambo woyika mmanda thjupi la malemu Ngolongoliwauchitika lachitatu pa 31 July 2019 ku likulu la ufumuwu ku Mtundawosema mboma la Thyolo kuyambira nthawi ya 12 koloko masana. Thupi la malemu Paramount Chief Ngolongoliwa lili mu bokosi Padakali pano mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika walamula kuti mwambowu udzakhale mwambo wa boma ndi udzalandire ulemu wa asilikali a nkhondo a dziko lino. Malinga ndi a Mughogho, mtsogoleri wa dziko linoyu akakhala nawo pa mwambowu.
14
Bungwe la SRWB Latseka Ofesi Zake Chifukwa cha Coronavirus Bungwe lomwe limagawa madzi mchigawo chakummwera la Southern Region Water Board (SRWB) latseka ofesi zake kuyambira lero mpaka pa 4 August kamba ka mliri wa Coronavirus. Zatsekedwa-imodzi mwa ofesi za SRWB Wofalitsa nkhani za bungweli a Rita Makwangwala watsimikidza za nkhaniyi ndipo wati zimenezi zikutanthauza kuti akhala sabata ziwiri asakugwira ntchito. Kudzera mu chikalata chomwe bungweli latulutsa, ganizoli ladza kaamba koti mmodzi mwa ogwira ntchito ku bungweli wapezeka ndi kachilombo ka Coronavirus ndipo imeneyi ndi njira yopewera kufala kwa kachilomboka pakati pa ogwira ntchito ena. Chikalatachi chatinso anthu onse ofuna kugula madzi adzigwiritsa ntchito njira yogulira madzi kudzera pa lamya ya mmanja yomwe ndi Airtel Money kapena Tnm Mpamba kapenanso kudzera ku Bank.
6
Kayira challenges Masamba, bout on March 29 Mzuzu-based professional boxer Laston Kayira has challenged Lilongwe-based veteran Wilson Masamba in an eight-round non-title bout scheduled for Obrigado Leisure Park on March 29. This will be the first Mzuzu City fight this year. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Osgood Kayuni Kayira is claimimg that he has all the qualities to silence Masamba. We have, therefore, decided to give him an opportunity to prove his worth, Phillip Ngwira of Ken One and Nyamaz Boxing Promotions told The Nation on Monday. According to Ngwira, the fight has attracted supporting bouts involving Mwayi Kamanga, Amos Kayira, Patrick Kayira, Secret Chirwa, Israel Banda and Clifford Yahaya. This will be Kayiras fourth professional fight. In previous bouts, he defeated Alex Chimbalanga in a knockout, lost to Malani Kayuni on points and drew against Aubrey Masamba. Kayira, 24, is currently being trained by Gabriel Mkondowe. I am happy that sponsors have finally come to our rescue. I want to prove that my elevation to the professional [level] was not a fluke, said Kayira. On his part, Masamba said he is prepared for the fight and warned that Kayira is too young to fight him. The two will fight under lightweight category.
16
Wofuna kuba alubino amusinthira mlandu Mkulu yemwe akuimbidwa mlandu wofuna kuba alubino ndi cholinga chomupha zidamuthina Lachiwiri lapitali kubwalo la milandu la majisitireti ku Mzuzu pomwe boma lamusinthira mlandu. Tsopano Phillip Ngulube, wa zaka 21, akuyankha mlandu wofuna kupha munthu, womwe ndi waukulu kuposa wozembetsa munthu ndi cholinga chofuna kumupha. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Wa kulimandi: Ngulube (kumanzere) pambuyo pokaonekera kukhotiWa kulimandi: Ngulube (kumanzere) pambuyo pokaonekera kukhoti Ngati Ngulube angapezeke wolakwa pamlandu watsopanowu akhoza kukakhala kundende moyo wake wonse. Ngakhale Ngulube adavomera mlandu woyambawu pa September 15 pomwe adakaonekera kubwaloli koyamba, mlandu watsopanowu waukana. Ndikukana kuti ndinkafuna kumupha mtsikanayu. Zoona zake ndi zoti ndinkamufuna banja basi, iye adauza bwaloli. Yankholi lidadzi-dzimutsa majisitireti Gladys Gondwe chifukwa woganiziridwayu ankangoyenera kunena ngati akuuvomera kapena kuukana mlanduwu. Komabe woweruzayu adalemba kuti waukana poti woimira boma pamlanduwu ayenera kupereka umboni mwatsatanetsatane kuti cholinga cha woyankha mlanduwu chidali kupha chibwezi chakecho. Wapolisi woimira boma pamlanduwu, Christopher Katani, adalonjeza kuti abweretsa mboni zisanu ndi ziwiri pamene bwaloli lidzakumanenso pa September 30. Zina mwa mbonizi ndi Mswahili yemwe akuti adatsatsidwa malonda a mwalubinoyo kuphatikizapo mtsikana mwini wakeyo. Malinga ndi mneneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, oimira boma pamlanduwu aganiza zosintha poyesayesa kuti ozunza maalubino azilandira zilango zokhwima pofuna kuthetsa mchitidwewu. Bwalo la milanduli lidamva kuti Ngulube, yemwe amagwira ntchito ya uphunzitsi modzipereka pasukulu ya pulaimale ya Mongo, adafunsira mbeta mtsikana wachialubino, wa zaka 17, ndi cholinga chofuna kumuba kuti akamugulitse pamtengo wa K6 miliyoni. Kupha ndi kugulitsa anthu achialubino, makamaka ana, wayamba kukula mdziko muno pamene boma la Tanzania laletsa usinganga mdzikomo womwe akuti wapangitsa kuti maalubino ambiri aphedwe ndi anthu ofuna zizimba. Ku Tanzania ndi maiko ena a kuvuma kwa Africa ena amakhulupirira kuti ziwalo za munthu wachialubino ndi zizimba zopangira mankhwala ochulukitsira chuma ndi mwayi.
7
Apha mwana atasemphena za ndalama Apolisi mboma la Mangochi amanga ndi kutsekera mchitokosi mayi wa zaka 28 chifukwa chomuganizira kuti wapha mwana wake wa zaka ziwiri atasemphana ndi mwamuna wake pa nkhani za ndalama. Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi mboma la Mangochi Amina Tepani Daudi wati boma likuganizira mayiyo, Tamara Chirambo, kuti adapha mwana wake, Thomas Harawa Junior, ndipo onse ochokera mmudzi mwa Mwakhwawa mdera la mfumu yaikulu Wasambo mboma la Karonga. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Daudi: Adakangana za ndalama Malingana ndi Daudi nkhaniyo idachitika usiku wa pa 12 June chaka chino mmudzi mwa Ngombe mdera la mfumu yaikuru Namabvi ku Mangochi. Mayiyo ndi mkazi wachiwiri kwa msodzi wa nsomba, Thomas Harawa wa zaka 46 ndipo akhala akukhala limodzi pa doko la Ngombe. Patsikulo, banjalo lidakangana pankhani za ndalama ndipo zotsatira zake ndewu idabuka pakati pa awiriwa zomwe zidapangitsa kuti mwamunayu athawire kunyumba kwa mchimwene wake kukafuna malo obisala pa msika wa Makawa mbomalo, adatero Daudi. Iye adati mbandakucha wa tsikulo, mwamunayo adalandira lamya kumudziwitsa kuti mwana wake wamwamuna wamwalira ndipo apolisi adathamangira kumaloko atadziwa izo. Zotsatira za kuchipatala chachikulu cha Mangochi zidaonetsa kuti mwanayu adamwalira chifukwa chopotokoledwa khosi. Mayiyo akaonekera kubwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu wokupha. Pakadali pano apolisi mbomalo apempha anthu kuti apewe kutengera malamulo mmanja mwawo akasemphana pankhani za mbanja koma azikauza ankhoswe a mabanja awo kapena kupita kuma ofesi apolisi yoona za chinsinsi (Victim Support Unit) kukakambilana modekha.
7
Nkhawa ikulirakulira pankhani ya zaumoyo Mabungwe omwe si aboma ati mavuto a mgonagona omwe akuoneka pa nkhani za umoyo mdziko muno ndi umboni wakuti chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) sichikukwaniritsa zomwe chidalonjeza pomwe chinkachita misonkhano yokopa anthu kuti achivotere pachisankho cha chaka chatha. Kuperewera kwa ogwira ntchito zaumoyo, kusowa kwa mankhwala, kusowa kwa chakudya ndi ganizo la boma lochepetsa chakudya chomwe limapereka kwa odwala mzipatala ndi ena mwa mavuto omwe mabungwewa ati akula padakalipano. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Anamwino kukapereka madandaulo awo ku Nyumba ya Malamulo Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu pa nkhani za umoyo, Charles Nyirenda, wati zomwe boma likupanga pochita zinthu modzidzimukira ndi msampha waukulu pa miyoyo ya anthu. Nyirenda ndi mmodzi mwa oimira mabungwe amene athirapo ndemanga pa zomwe zikuchitika mdziko muno, makamaka pankhani ya za umoyo wa anthu womwe uli pachiswe chifukwa cha mikwingwirima yomwe unduna wa za umoyo akukumana nayo. Iye adati mmene zinthu zikuyendera pankhani za umoyo, tsogolo lenileni silikuwoneka ndipo kukadakhala bwino boma likadangopanga mfundo imodzi nkuikhazikitsa osati kuvinavina. Poyamba nkhani imene idavuta ndi yakuti anthu azilipira mzipatala yomwe idatsutsidwa mpaka kuzilala. Pano akuti anthu odwala azidya kamodzi patsiku komanso mankhwala mzipatala sakupezeka. Anthu akumawauza kuti akagule okha, tsono apa zikusiyana pati nkulipira kuchipatala? adatero Nyirenda. Iye adati chidali chanzeru kuyamba kulipiritsako bola anthu ovutika, koma odwala azidya chakudya chokwanira kuti mankhwala azigwira ntchito mthupi. Mmodzi mwa omenyera maufulu a anthu mdziko muno, Gift Trapence, adati boma likuyenera kuyankhapo pa nkhawa zomwe anthu, kudzera kumabungwe, akupereka mdziko muno chifukwa lidawalonjeza kukonza mavuto amene akukumana nawowo. Apa ndi nkhani yoti boma lichitepo kanthu msanga chifukwa lidalonjeza lokha anthu asadalisankhe ndiye zisakhale ngati anthu akupempha ayi koma akungokumbutsa zomwe adalonjezededwa, adatero Trapence. Mavutowatu akudza patangotha pafupifupi chaka ndi miyezi 6 kuchoka pomwe chipani cha DPP chidayamba kulamula chitapambana pachisankho cha mwezi wa May, 2014. Chisankho chisadachitike, chipanicho chidalonjeza kuti chidzatukula nkhani zaumoyo poonetsetsa kuti chiwerengero cha anthu ogwira ntchito zaumoyo ndi chokwanira, mankhwala akupezeka mzipatala, kutukula moyo wa anthu ogwira ntchito zachipatala ndi kuchepetsa imfa zokhudza uchembere. Malonjezowo ali choncho, boma lidaplephera kulemba ntchito madotolo 51 amene adamaliza maphunziro awo kusukulu ya ukachenjede ya College of Medicine, chonsecho ngakhale bungwe la zaumoyo padziko lino la World Health Organisation (WHO) limati madotolo 23 alionse ayenera kuthandiza anthu 10 000, ku Malawi, madotolo awiri amathandiza odwala 100 000. Ndipo posachedwa, Amalawi zikwizikwi mboma la Rumphi adayenda ulendo wokapereka madandaulo kwa DC wa mbomalo pokhudzidwa kuti odwala akulandira chakudya kamodzi patsiku pomwe akumwa mankhwala ofunika chakudya chokwanira. Ulendo wokapereka zodandaula za chakudya udakonzedwa ndi mgwirizano wa mabungwe omwe si aboma mbomalo ndipo wapampando wa mgwirizanowo, Eunice Banda, adati zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kuti boma likulephera kukwaniritsa lonjezo. Kutengera zomwe adalonjeza a Pulezidenti kuti sadzalola munthu aliyense kumwalira ndi njala, tikuona kuti zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kulephera kukwaniritsa lonjezolo, adatero Banda. Iye adati si zoona kuti munthu yemwe akulandira mankhwala aziperewera chakudya mthupi mwake chifukwa mankhwala amagwira bwino ntchito ndi chakudya. Komanso poona kuti sizikuwayendera pantchito yawo, anamwino ena adakaperekanso chikalata chawo ku Nyumba ya Malamulo pozizwa ndi ganizo la boma lakuti anamwino ena amene adalembedwa kale ntchito akayesedwenso. Mchikalata chawo, anamwinowo adadandaula za momwe ntchito za umoyo zalowera pansi mdziko muno ndi momwe umoyo wa Amalawi wakhudzidwira, zomwe adati gwero lake ndi kusalingalira nkhani za umoyo pakati pa atsogoleri. Mchikalatachi, adatinso ndi okhudzidwa kuti boma likulephera kulemba madotolo ndi anamwino omwe adamaliza maphunziro awo chonsecho ogwira ntchito zachipatala ndi ochepa, zomwe zimachititsa kuti ntchito yawo iziwawa. Koma nduna ya zachuma ndi chitukuko, Goodall Gondwe, ati pali mpumulo kumbali nkhani ya chiwerengero cha madotolo ndi anamwino chifukwa maiko omwe amathandiza dziko lino avomereza kuti boma likhoza kugwiritsa ntchito ndalama zina zomwe zidali za ntchito yolimbana ndi malungo, chifuwa chachikulu ndi matenda a Edzi polemba ntchito madotolo ndi anamwino omwe lidalephera kuwalemba.
6
Atatu Apezeka ndi Coronavirus Mdziko Muno Anthu atatu a mu mzinda wa Lilongwe apezeka ndi kachilombo ka Coronavirus mdziko muno. Walengeza za nkhaniyi-Mutharika Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika watsimikiza za nkhaniyi mu uthenga wake omwe walankhula ku mtundu wa aMalawi kudzera pa wailesi ya boma ya MBC. Iye wati oyamba kupezeka ndi nthendayi ndi mzimayi wina wa zaka 61 yemwe anapita mdziko la India ndipo atabwera mdziko muno anapatulidwa kwa masiku 14, ndipo ndi pomwe anawonetsa zizindikiro za nthendayi ndipo atamuyeza amupeza ndi nthendayi. Mutharika wati awiri enawo ndi wachibale wa mayiyo komanso wantchito wake. Atatuwa ndi anthu oyamba kupezeka ndi nthendayi mdziko muno.
14
Lonjezo la jb Lasanduka loto Bambo ake adamwalira, chiyembekezo chidali pa bambo womupeza, nawonso adamukhumudwitsa pomugwiririra nkumupatsa pathupi ndipo bwalo la milandu lidamugamula kuti akaseweze kundende zaka 13. Moyo wakhala wowawitsa; loto lodzakhala wapolisi lidasanduka la chumba. Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Koma pa 18 March 2013, chiyembekezo cha Zione (tangomupatsa dzinali) chidatukusira pamene yemwe adali mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda adamulonjeza kudzamulipirira maphunziro ake mpaka kuyunivesite. Malinga ndi mphunzitsi wa Zione, Dziwa Nazombe-Mbewe, Banda adalonjeza Zione patsiku lomwe amayendera ku One-Stop-Centre kuchipatala cha Queen Elizabeth Central mumzinda wa Blantyre. Patsikulo ogwira ntchito ku One Stop Centre adandiimbira kuti apulezidenti akhala akuyendera malowo ndiye akufuna Zione akalankhule zomwe zidamuchitikira. Ndidapita naye ndipo apulezidenti adafika mchipinda chathu momwe adacheza ndi Zione yemwe panthawiyo adali ndi zaka 13. Atamufunsa za sukulu, iye adati akufuna apitirize. Apa mpamene apulezidenti adati amulipirira sukulu yake, adatero Nazombe-Mbewe. Tsogolo sakuliona: Zione (kumanzere) ndi aphunzitsi ake Mayi Nazombe-Mbewe Iye adati Banda adauza mayi Lingalireni Mihowa amene adali nawo panthawiyo kuti ndiwo azilumikizana nawo pankhani ya thandizolo. Chimwemwe chidadza ngati mmawa kwa Zione, zoti adachitidwa chipongwe ndi bambo ake, zidaiwalika. Tsopano loto lodzakhala wapolisi lidayamba kuoneka tsogolo lake. Ndidali ndi chimwemwe. Titangotuluka, ndidaimbira foni malume anga ku Balaka komanso kudziwitsa anzanga akusukulu zomwe apulezidenti adandilonjeza, ndidasangalala kwambiri, adatero Zione. Chidatsala nkuti Zione, yemwe panthawiyo adali Sitandede 8, akhoze mayeso. Ndidakalimbikira kusukulu ndipo ndidakhozadi, adatero. Apa mpamene mphunzitsiyu adakambirana ndi Mihowa kuti Zione akalowe Fomu 1 kusekondale. Ndidapita kuofesi kwawo ndipo tidakambirana poti panthawiyo nkuti Zione adali asadabereke, adati tidikire abereke kaye kuti abwerere kusukulu, adatero Nazombe-Mbewe. Pa 9 January 2014, mwana adabadwa ndipo ati adagwirizana kuti pakatha miyezi 7 Zione akayambe sukulu. Mu July mwana adamuleketsa kuyamwa kuti abwerere kusukulu. Nazombe-Mbewe adayesera kutsatizira nkhaniyo koma sinaoneke mutu wake. Ndidapita kuofesi kwawo ndipo adati andiimbira. Poona kuti sakuimba, ndidapitanso ndipo adandiuza kuti ndisiye nambala aimba, koma sadaimbe. Ndidadzapitanso pamene adati ndilembe nkhani ya Zione ndipo aitsatizira koma sizidatero mpaka lero pamene ndatopa, adatero Nazombe-Mbewe. Ngakhale mphunzitsiyu adalembera ofesi ya Mihowa kalata zokumbutsa za lonjezolo, komabe palibe chidachitika mpaka lero. Msangulutso utaimbira foni Mihowa, iye adati tilankhule ndi Levi Mwase amene amayendetsa nkhaniyo. Koma Mwase adati sindine mneneri wa Joyce Banda, imbirani mneneri wake Tusekere Mwanyongo. Mwanyongo adati nzovuta kuti anene chifukwa chenicheni chomwe lonjezolo silidatheke koma wati mwina padalibe kulumikizana kwabwino. Mayi Joyce Banda akhala akuthandiza ndipo mpaka lero akuthandizabe ana ambiri asukulu. Nkutheka kuti padalibe kulumikizana kwabwino ndi mtsikanayo, adatero. Koma mthandizi wa Banda, Andekuche Chanthunya, akuti ndondomeko zoyenera sizidatsatidwe nchifukwa mtsikanayu sadathandizidwe. Samayenera apite kwa Mihowa koma abwere kwa ine kapena kwa Levi [Mwase]. Ngati akufuna kuthandizidwa akuyenera atsatire ndondomeko, adatero. Njovu zikamamenyana udzu ndiwo umavutika. Kuponyerana Chichewaku sikukuthandizabe Zione amene pano akusungidwa ndi banja lina ku Chirimba mumzinda wa Blantyre. Banja lomwe likusunga Zione silingakwanitsenso kumutumiza kusukulu. Bambo wa pabanjapo, Evance Milanzie wati moyo wa Zione wafika pomvetsa chisoni. Ndi mwana wanzeru, zangovuta kuti lonjezolo silidatheke, adatero Milanzie. Aka si koyamba kuti mtsogoleri wa dziko alonjeze mwana koma osakwanitsa lonjezolo. Mu 2004, mtsogoleri wakale Bingu wa Mutharika adalonjezanso Marietta Mhango wa mmudzi mwa Mawelera kwa Paramount Kyungu mboma la Karonga kuti adzamulipirira sukulu. Mutharika adalonjeza Marietta pamsonkhano kuti adzamulipirira atanena bwino ndakatulo, koma ngakhale adatsindika za thandizolo, izi sizidatheke ndipo lero Marietta akutuwa. Kodi izi zimatero chifukwa chiyani? Mphunzitsi wa zandale kusukulu ya Chancellor Collage Joseph Chunga akuti mtima wofuna awaone ndi omwe umachititsa. Amafuna kuti mwina aoneke kuti ali ndi mtima wabwino, cholinga akalonjeza apateko mavoti chifukwa cha mtima womwe aonetsa, koma nzachisoni, adatero Chunga. Pamene izi zili chonchi, Zione ndi wokhumudwa ndipo zasokoneza moyo wake. Katswiri kumbali ya kaganizidwe ka munthu, Chiwoza Bandawe akuti Zione kukhala wachichepere, izi zingakhudze moyo wake.
11
ACB Yalonjeza Kuteteza Oyitsina Khutu Bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu mdziko muno la Anti-Corruption Bureau (ACB) lati laika ndondomeko zabwino zotetezera ufulu wa anthu omwe amapereka mauthenga okhudza za katangale ku bungweli. Mmodzi mwa akuluakulu ku ofesi ya zophunzitsa anthu ku bungweli a Edward Kamvabingu ndi omwe anena izi lachiwiri pa msonkhano wa akuluakulu a mabungwe osiyanasiyana kumanso atolankhani mu mzinda wa Mzuzu. Iwo ati ndondomeko yachiwiri yomwe inakhazikitsidwa mu chaka cha 2019 ya National Ant-Corruption Strategy, ikubweretsa pamodzi magulu osiyanasisyana pogwira ntchito ndi bungwe la ACB pofuna kuthetsa mchitidwe wa ziphuphu komanso katangale mdziko muno. Mmawu ake mkulu wa bungwe la Youth and Society (YAS) komanso la National Anti-Corruption Alliance, Charles Kajoloweka Mhango wati nkhani yothana ndi katangale mdziko imagwirizana ndi utsogoleri wabwino.
7
Anatchezera Za chikondi ndi chibwenzi Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kodi chibwenzi ndi chikondi ndi zosiyana bwanji? Mwina funso limeneli likhoza kuoneka ngati lopanda nzeru koma kwa ine ndi lofunika kwambiri. Funso lina ndi loti kodi ngati mwamuna amakonda kulonjeza chibwenzi kapena wachikondi kuti adzakwatirana chonsecho mkazi samamulonjeza mwamuna wake, ndiye pamenepa mwamuna angathe kupitiriza chibwenzi kapena angomusiya? LF, Area 12, Lilongwe Wokondeka LF, Munthu utha kukhala ndi abwenzi ambirimbiri koma wachikondi mmodzi. Nthawi zambiri anthu satha kusiyanitsa pakati pa chikondi ndi chibwenzi. Chikondi ndi chozama kuposa chibwenzi; chikondi chimachoka pansi pa mtima ndipo nthawi zambiri anthu awiri akakondana maka pakati pa mwamuna ndi mkazi amagwirizana mzambiri moti nchifukwa chake mapeto ake amalolerana ndi kulumbira kuti adzakhala limodzi mpaka moyo wawo wonse mbanja, pamene chibwenzi mumatha kugwirizana pa zina koma kusiyana mzambiri zochitika. Nchifukwa chake munthu utha kukhala ndi abwenzi ambiri ngakhale uli pabanja, monga ndanena kale, koma amene umatherana naye nkhazi zakukhosi ndi zakumphasa ndi mmodzi yekha, wachikondi wako. Funso lako lachiwiri yankho ndi loti pachikhalidwe chathu mwamuna ndiye amafunsira mkazi ndipo ndi iyeyo amene amauza mkazi za cholinga chake pachibwenzi chawocho. Akazi ambiri amakhala ndi manyazi kunena kuti alola chibwenzi chonsecho mkati mwa mtima wawo alola kale. Ndiye munthu wamwamuna uyenera kumvetsa ndi kufatsa; osapupuluma chifukwa ukhoza kutsekereza mafulufute kuuna poganiza kuti mkazi sakunena chilichonse. Pamene pali chikondi sipasowa, zochitika zimasonyeza zokha kuti apa pali chikondi ngakhale wina asanene. Amandikonda koma ine ayi Ndili ndi mwamuna amene akufuna akaonekere kwathu koma sindimamukonda kwambiri ngakhale kuti iyeyo amandikonda kwambiri. Ndiye akuti andikwatira zaka zinayi zikubwerazo. Pano ndakumana ndi wina koma akuti andikwatira zaka ziwiri zikubwera kutsogolo. Ndiye nditani, agogo? LC, Area 49, Lilongwe Zikomo LC, Mwana wanga, chimene ukufuna sindikuchidziwa. Iwe ukufuna kukwatiwa ndi mwamuna wotani? Wokukonda kapena amene akufuna ukwati pompanopompano ngakhale sakukonda? Vuto ndi chiyani ndi mwamuna amene ukuti amakukonda ndipo akufuna kudzamanga nawe banja zaka zinayi zikubwerazi? Nchifukwa chiyani udamulola poyamba ngati sumamukonda? Ndiye pano ukuti wapeza mwamuna wina amene akuti akukwatira zaka ziwiri zikubwerazi, makamaka ukufuna kuti ndikhuthandize chiyani pankhani imeneyi? Zonse zili ndi iwe mwini, koma chomwe ndingakulangize ndi choti si amuna onse amene amakhala ndi chikondi chenicheni. Wina atha kunena kuti tikwatirane lero ndi lero, koma mumtima mwake mulibe chikondi, pomwe wina anena kuti tikhale pachibwenzi zaka zinayi kenako tidzakwatirane pazifukwa zina ndi zina. Pa Chichewa pali mawu oti lero ndi lero linadetsa mnthengu, komanso ukasauka sunga khosi mkanda woyera udzavala. Enanso amati kuona maso a nkhono nkudekha. Mawu onsewa akutiphunzitsa kuchita zinthu mofatsa kuti tione ubwino patsogolo, osati kuchita zinthu mwakhamanikhani. Tsono monga ndanena kale, zili ndi iwe mwini chifukwa ukudziwa chomwe ukufuna. Koma ndikanakhala ndili ine, ndikanamupatsa mpata mwamuna woti waonetsa chikondi chenicheni kwa ine ngakhale anene kuti atenga nthawi kuti andikwatire. Chikondi chenicheni sichimaona nthawitu paja.
12
Ukhansala uli ndi malireNice Bungwe lophunzitsa anthu zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (Nice) lalangiza makhansala mumzinda wa Zomba kuti azikhala ndi malire pogwira ntchito zawo. Mkulu woyendetsa ntchito za bungwelo ku Zomba, Albertina Nsongolo, ndiye adalankhula izi pamsonkhano wa mafumu, makhansala komanso mabungwe a chitukuko cha mmadera mumzindawo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chimene chidatsitsa dzaye kuti bungwelo lisonkhanitse atsogoleriwa ndi khalidwe la makhansala ena amene akumalumpha mafumu akafuna kuchita chitukuko mmadera mwawo. Nsongolo adati chitukuko chingapite patsogolo kapena kubwerera mmbuyo bwanji, mfumu ikuyenera kutsinidwa khutu chifukwa ili ngati nsanamira ya dera kulikonse. Kuipa kwa kumalumpha mafumu pankhani za chitukuko ndi koti chitukukocho chimakhala chopanda maziko chifukwa makhansala akachoka pampando munthu wopitiriza chitukukocho amasowa, adatero Nsongolo. Nsongolo adaonjezera kuti makhansala alekenso kudumpha atsogoleri a makomiti a chitukuko cha kumadera chifukwa atsogoleri amenewa ndi amene amakhala ndi chidziwitso cha chitukuko chimene chikuyenera kubwera kumadera. Kufunsa ndi bwino chifukwa chuma chambiri cha boma chimaonongeka anthu akamakana kugwiritsa ntchito zinthu monga mijigo, milatho ndi zina zambiri zimene khansala wabweretsa kudera asadafunse kaye anthu a kuderalo kuti akufuna chiyani, adatero iye. Gulupu Mtiya wa mumzindawu adayamikira bungweli chifukwa cha mkhumanowu. Iye adati chimkulirano chimene chidalipo pakati pa makhansala ndi mafumu chachedwetsa kubwera kwa zitukuko zosiyana-siyana mumzindawu. Nthawi yambiri yatayika polimbana kuti wamkulu ndani, koma msonkhanowu watitsegula mmaso kuti mtsogoleri aliyense ali ndi malire ake ogwirira ntchito, adatero gulupuyo. Pothirirapo ndemanga, Davie Maunde, amene akugwirizira mpando wa meya wa mzinda wa Zomba, adalimbikitsa makhansala kuti azidzichepetsa pamaso pa mafumuwa pozindikira kuti akuluakulu ndi mdambo mozimira moto.
8
Mayi Mutharika ndi mlatho wa amayi Anthu osiyanayana ayamikira mtsogolerio wa dziko lino Peter Mutharika poganiza zokwatira atangopambana pachisankho cha pa 20 May ati chifukwa mayi wa fuko amathandiza mtsogoleri pogwira ntchito yotukula dziko. Amayi ena omwe tidayankhulana nawo kumpingo wa St Michaels and All Angels Lamulungu, komwe ukwati wa awiriwua udamangidwa mumzinda wa Blantyre, adati kubwera kwa Mayi Gertrude Mutharika kwatsegula khomo lina loti amayi aziperekerako madadandaulo awo komanso kupempha zinthu zina zachitukuko. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mayi Mutharika Phungu wogonja pampando wa uphungu kudera la kumadzulo kwa mzinda wa Blantyre, Bertha Masiku, adati ali ndi chikhulupiriro kuti Mayi Mutharika athandiza dziko lino makamaka polimbikitsa ntchito za amayi ndipo adalangiza anzawo onse ogonja kuti aganizire zothandiza boma posayanganira chipani chawo. Tiyamikire a Pulezidenti komanso mayi a kunyumba kwawo pogwirizana kuti athandizane potukula dziko. Pachikhalidwe chathu, timadziwa kuti pempho lodzera mwa amayi limadutsa kwa abambo. Amayi tili ndi chiyembekezo kuti mtsogoleri wa dziko lino apereka chilichonse kudzera mwa mayi wa fukoyu pothandiza ntchito zotukula miyoyo ya amayi, adatero Masiku. Woyangamira ntchito za uchembere wabwino mdziko muno, Dorothy Ngoma, naye adayamikira mtsogoleri wa dziko lino ndipo adati izi zithandiza pantchito za amayi. Iye adati popanda mayi kunyumba yachifumu chidwi pankhani za umoyo wa amayi zidakakhala zochepa popeza ntchito zambiri zachitukuko mdziko muno zimadalira chidwi kuchokera kwa atsogoleri. Pokhala mayi wa fuko, tili ndi chikhulupiriro kuti azitiyankhulira pankhani zosiyanasiyana zokhudza amayi, makamakanso pomwe dziko likutaya miyoyo yambiri chifikwa cha kusowa kwa zipangizo zothandizira amayi oyembekezera ndi zina, adatero Ngoma. Iye adati dziko lino likutaya amayi pakati pa 3 000 ndi 4 000 pazifukwa za uchembere komanso matenda ena monga HIV ndi Edzi, khansa ndi TB. Phungu wogonja ku Mulanje Pasani Peter Nowa adati nzonyaditsa kuti mayi wa fuko ndi mayi woti adakhalapo mNyumba ya Malamulo ndipo akudziwa mavuto amene aphungu ngakhalenso makhansala amakumana nawo akamapempha zinthu zina. Iye adati mbiri ya mayiyu ikuonetsa kuti ndi wolimbikira ndipo pali chiyembekezo chachikulu kuti athamangathamanga ndi kugwira ntchito ndi athu onse pokweza dziko lino.
11
Apolisi aphunzira kagwiridwe ka ntchito yawo Polisi ya Nkhotakota yakhala yoyamba kuphunzitsidwa za momwe angagwirire ntchito yawo panthawi ya zipolowe komanso zionetsero. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Maphunzirowa akudza poyanganira chisankho cha pulezidenti, makhansala ndi aphungu a ku Nyumba ya Malamulo cha chaka chamawa. Panthawiyi pamakhala zingapo zotsamwitsa mwina anthu kunyanduka posagwirizana ndi zotsatira zomwe zatuluka kapena kusamvetsetsa ndi momwe zina zachitikira. Apolisi ndiwo amakhala kalikiliki kukhazikitsa bata kuti pasakhale zipolowe koma zonse zithere mokomera mbali zonse motsatira chilungamo. Malinga ndi mneneri wa polisiyo, Kaitano Lubrino, ganizolo lidabwera ndi mkulu wa apolisi mdziko muno Loti Dzonzi. Cholinga nchakuti apolisi onse mdziko muno aphunzitsidwe za momwe angachitire panthawi ya ziwawa pomwe anthu akufuna kuchita zionetsero. Polisi yathu yakhala ya mwayi kuti ndiyo yayamba kuphunzitsidwa za maphunzirowa. Maphunzirowa adachitika Lachinayi pa June 4, adatero Lubrino. Apolisi 40 adachita nawo maphunzirowo omwe mwazina amaphunzira za momwe angagwiritsire zida zawo ndi nthawi yake yomwe angagwiritsire zidazo.
7
Tipulumutseni ku ukwati wa ana Amati ana ndi tsogolo la mawa. Koma zikuchitika ku Neno zikukaikitsa ngati adzakhaledi atsogoleri mawa. Kumeneko ukwati wa ana akuti wafika pa lekaleka ndipo ngati boma ndi mabungwe sachitapo kanthu, zinthu zifika poipitsitsa. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lachinayi sabata yatha bungwe la Save the Children lidaitanitsa Nyumba ya Malamulo ya ana komwe anawa adatula nkhawa zawo kwa atsogoleri. Nyumbayo idakumana masiku awiriLachinayi mpaka Lachisanu. Momwe zimachitikira sizimasiyana ndi momwe imakhalira Nyumba ya Malamulo ya dziko lino chifukwa mudali sipikala komanso aphungu. Zonsezi zimachitika ndi ana amboma la Neno amene amachokera msukulu zosiyanasiyana za mbomalo. Malinga ndi mlangizi wa ana ku bungweli, Thandizolathu Kadzamira, anawa adachita kusankhana kuti apeze owayimira pa sukulu yawo. Amasankha phungu wawo amene akawalankhulire mnyumbayi ikamakumana. Adasankhanso sipikala wawo. Awatu ndi masukulu ambiri a mboma lino, adatero Kadzamira. Mnyumbayi, anawa adalankhula Chingerezi ndi Chichewa osachita mantha ngakhale holo ya Neno idakhoma ndi anthu ofuna kudzaonera nkhumanoyo. Nkhani zidamanga nthenje mnyumbayi zidali zodandaulira boma komanso mabungwe kuti awapulumutse ku maukwati a ana omwe akolera mbomalo. Anawa adapemphanso kuti boma liwamangire sukulu zabwino ndi kuikamo zipangizo zoyenera. Sipikala wa nyumbayo, Trifonia Kaduya, wa zaka 14 ndipo akukalowa folomu 2 pa sekondale ya Chiwale, adati akuluakulu asiye kuimba nyimbo ndipo ayambe kuchita. Timalankhula koma palibe chimachitika. Nkhumano ino tikufuna akuluakulu athu ayambe kuchita, adatero. Mwana wa zaka 14 umupeza wakwatiwa kale. Kodi apa palinso lonjezo loti mawa tidzakhala atsogoleri? adadabwa sipikalayu. Wotsogolera komiti yokhudza ana ku Nyumba ya Malamulo, Richard Chimwendo Banda, adalonjeza sipikala Kaduya kuti nkhawa zawo ziyankhidwa. Alankhula mopanda mantha. Izi ndi zomwe tikufuna kuti zithandizire chidwi chathu chofuna kuthandiza ana. Amve kwa ine kuti tichitapo kanthu, adatero Banda. Iye adati Nyumba ya Malamulo ya dziko lino ikamakumana adzatenga ena mwa anawa kuti akalankhule kunyumbayi cholinga aphungu akadzimvere mavuto amene anawa akukumana nawo.
1
MCP siidakhutire ndi kalembera Chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chati ngakhale ndime yachiwiri ya kalembera wa zisankho yayenda bwino poyerekeza ndi yoyamba, MEC iganizire zobwereranso mmaboma omwe yadutsamo kale kaamba koti anthu ambiri sadalembetse. Koma mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), Jane Ansah, wati ndi wokhutira ndi mmene kalembera wayendera mgawo lachiwiri. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ansah: Zinthu zayenda bwino Kalembera wa mgawoli amachitikira mmaboma a Dowa, Ntchisi, Mchinji ndi Nkhotakota. Malingana ndi lipoti lomwe MEC yatulutsa, mwa anthu 1 048 080 omwe limayembekezera kulembetsa, anthu 875 138 ndiwo alembetsa. Chiwerengerochi chikutanthauza kuti mwa anthu 100 aliwonse omwe amayenera kulembetsa, 83 ndiwo alembetsa zomwe zachititsa mlembi wa MCP, Maurice Munthali, kupempha MEC kuti ibwererenso mmabomawo. Pali chosekerera apa? Tiyenera kuyandikira kwenikweni ku chiwerengero cha anthu omwe tidayenera kuwalembetsa, koma zomwe zachitika apa zikusonyeza poyera kuti anthu ambiri sadalembetse. Choncho MEC iyenera kubwereranso mmabomawo, adatero Munthali. Mlembiyu adati mu ufulu wa demokalase ngakhale kusiya munthu mmodzi zimakhala zodandaulitsa. Mkulu wa bungwe la Human Rights Defenders, Timothy Mtambo, akugwirizana ndi MCP kuti kalemberayo adzachitikenso kaamba koti munthu aliyense ali ndi ufulu wovota. Mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust, Ollen Mwalubunju, adati zinthu mgawo lachiwiri zasintha kwambiri poyerekeza ndi loyamba. Pali kusintha kwakukulu chifukwa mgawo loyamba timanena za anthu 73 pa anthu 100 aliwonse, koma pano tikunena za anthu 83 pa anthu 100 aliwonse. Izi zikutanthauza kuti zinthu zikusintha, adatero Mwalubunju. Pazaganizo lobwereranso mmaboma momwe kalemberayu wachitika kale, Mwalubunju adati mpofunika kudikira kaye kuti MEC iwone mmene zinthu zitayendere mmaboma ena. Malingana ndi kalata ya MEC yomwe yasayinidwa ndi woyanganira zisankho, Sam Alfandika, mwa anthu onse omwe alembetsa mgawo lachiwiriri, 462 925 ndi amayi ndipo 411 706 ndi abambo. Ansah adati zinthu zasintha kwambiri mgawoli poyerekeza ndi mmene zidaliri mgawo loyamba mmaboma a Kasungu, Dedza ndi Salima. Mavuto a akulu omwe takumana nawo ndi kuwonongeka kwa zipangizo zogwirira ntchito, kusowa kwa dizilo wa ma generator athu, komanso zipangizo zoyendera mphamvu ya dzuwa sizimagwira bwino ntchito moyenera potengera ndi mmene nyengo ilili. Mavutowa tawapezera njira zake moti kukubwera konseku, anthu ayembekezere kalembera wabwino, iye adatero. Ansah adati MEC siidapange chiganizo pa nkhani yobwereranso mmaboma momwe yadutsamo kale.
11
One-man demo pa Wenela tsikulo pa wenela padaterera. zidaliko. nkhani idavuta ndi ija tidaiyamba sabata yatha. Inde, iyi nkhani yophana chisawawa, makamaka kwa abale athu achialubino. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izi zikumvekazi zidandikumbutsa zomwe ndidamvapo mmbuyomu kuti Manyasa kalelo ankaponyera kuphompho odwala khate, kuja ku Zomba. Mitembo yawo inkapezeka mumtsinje wa Namitambo. Koma nanga lero zoona kuphanaku zatani? Abiti Patuma adali pafoni ndipo amangodzuma. Uku tidali tikuonera kanema. Zoona pa CNN, BBC, Al Jazeera ndi ena onse akunja akufalitsa za nkhanza tikuchitirana tokhatokhazi! Kodi izi ndiye azungu abweranso kuno kwathu kudzatisiyira enafe ma dollars, ma rands ndi zina zotero? adafunsa. Zonsezi ndi Moya Pete ndi anzake. Izitu sizikadafika apa akadalimbana nazo koyambirira komwe kuja. Nkhani zikangokhudza United Nations komanso Amnesty International umangodziwiratu! Mwaiwala adathana ndi gogo uja ndani? adatero Gervazzio. Zoona, ndikumbuka masiku amenewo ndili kwathu kwa Kanduku, tinkamva kuti bungwe la Amnesty International lidalimbikitsa kuti zinthu kuno zisinthe makamakanso chifukwa cha kumangidwa kwa andale ena popanda chifukwa komanso kuphedwa kumene. Mwaiwalanso muja UN idavutira nthawi ya Mfumu Mose? Zoti munthu ngwamakani kuiwaliratu, adatero Abiti Patuma. Chomwe ndikudabwa ine nchakuti dziko lino lidaliko kuyambira kale koma izi zachuluka chomwechi nthawi ya Moya Pete, bwanji? ndidafunsa. Palibe adandiyankha. Adangoti duuu! Posakhalitsa adatulukira mkulu wina ali chibadwire. Iyetu adanyamula chikwangwani cholemba kuti Osapha! Tonse tidayangana kumbali. Abiti Patuma adathawira kukauntala, adatenga chikwama chake pomwe amasungitsapo nkusololamo chovala chamkati chofiira. Chonde, atate, amamangatu izi zoyenda bunobunozi. Amene samangidwa ngwamisala basi. Tavalani basi, tilibetu ndalama zogulira nthochi kuti tizikakuonani akakunjatani, adatero Abiti Patuma. Kaya mkulu uyu ndidamuonapo kuti kaya? Koma nkhope yake ndi yosasowa. Ndipo tangoganizani kuyenda malipsata mukuchitako, Paparazzi akatola zithunzi nkuika munyuzi, mwana wanu nkuona, ulemu wanu ukhalaponso? adatero Gervazzio. Nkhope yakeyo si yosowa, koma kaya ndidamuona kuti mkulu ameneyu? Kodi ndi uja adali ndi bwenzi lonenepa zedi ankalimbirana ndi mnyamata wa magitala uja? Tonse takwiya, koma chonde ife zomationetsa filimu zolaula masanasana takana. Akapanda kukutenga apolisi tiitanitsa a Censorship Board, adatero Abiti Patuma. Mwamaliza? Ndakwiyatu kwambiri. Ndine legistrator, ntchito yanga ndi yopanga malamulo. Apapatu aphungu komanso boma timayenera kubweretsa Group Areas Act chifukwa nkhaniyi ikuposa nkhani ya njala, adatero mkulu uja, thovu likukha. Dekhani, achimwene. Anzanu enatu adayamba ndi matukutuku chomwechi koma adakathera kuti atapezeka kuti satifiketi ya 8 adalibe? adafunsa Abiti Patuma. Kaya mkulu ameneyu ndidamuonapo kuti? Koma atavala bulauzi ndi phwanyamchenga zingamukhale bwanji! Kaya mundipha, kaya mundidya, ine ndivula basi, adafuna kuchotsa kabudula wamkati adapatsidwa ndi Abiti Patuma uja.
11
Akhristu a St. Francis Chidzanja Parish Athandiza Radio Maria Akhristu a mpingo wakatolika ku Parish ya St. Francis of Assis Chidzanja mu dayosizi ya Mangochi awayamikira kamba kothandiza Radio Maria Malawi molowa manja. A Director a wailesi-yi, bambo Joseph Kimu amayankhula izi pa mbuyo pa mwambo wa nsembe ya ukaristia omwe unachitikira ku parish-yi omwe cholinga chake ndikuthandiza wailesi-yi. Iwo anati potengera ndi momwe akhristu-wa achitira pothandiza wailesi-yi, zasonyezeratu kuti nawo amadziwa kufunika kothandiza wailesi-yi. Bambo Kimu anati ndi okondwa kuti bambo mfumu komanso akhristu a parish yi anavomera kuti Radio Maria ikachite misa yopempha thandizo ngakhale kuti parishiyi ikukumana ndi mavuto osiyanasiyana pa nkhani ya chuma. Ndalama yomwe mwapereka simunataye ndipo ndikudziwa kuti mwapereka ndi ndi chikhulupiliro komanso chifukwa chokonda wayilesi ya Radio Maria anatero Bambo Kimu. Pa mwambowu akhristuwa anathandiza wailesiyi ndi ndalama zokwana 1 hundred and 18 thousand kwacha.
13
Apha mkazi wake kaamba ka nsanje Akuluakulu amati pali nsanje pali chikondi, koma zina zinyanya. Nsanje zina zimaonjeza ndipo zimasanduka chiopsezo pa miyoyo ya anthu ena. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Monga zakhalira mboma la Dedza komwe bambo wina wapha mkazi wake pomukhapakhapa chifukwa cha nsanje. Ndipo chisoni chakuta mudzi wa Lumwira kwa Mfumu Kasumbu, mbomali chifukwa cha imfa ya Sipeniya David wa zaka 35. Malinga ndi mneneri wapolisi mbomalo Cassim Manda, Kasumbu adaphedwa usiku wa Lamulungu, kucha kwa Lolemba. Manda adati iwo ngati apolisi, omwe adaona thupi la David, akuchita kukanika kulongosola momwe Simthawika Sibombe wa zaka 40 adamukhapira mkazi wakeyo. Manda adati Sibombe yemwe amachokera mmudzi mwa Chiphuka kwa Mfumu Kasumbu komweko, adakwatirana ndi David zaka 7 zapitazo. Koma banjali silimamvana chifukwa Sibombe amamuchitira mkazi wakeyo nsanje yodabwitsa, adalongosola Manda. Iye adati zonse zidayamba Lamulunguli, nthawi ili cha mma 4 koloko masana pomwe David adali paulendo wopita kokazonda mchemwali wake yemwe adagonekedwa pachipatala cha Kanyama chomwe chili mderalo. Apa mwamuna wakeyu yemwe adambisalira David pa manda ena omwe ali mderalo, adavumbuluka ndikufikira kumukhapa mkaziyu manja onse komanso mmutu. David adafera pomwepo pomwe Sibombe adathawa atangochita izi, adalongosola motero Manda. Iye adati Sibombe sadapezekebe mpaka pano ngakhale apolisi amutsekulira mlandu wopha munthu mosemphana ndi gawo 209 la malamulo a dziko lino. Awiriwo ali ndi ana awiri.Chiwerengero cha anthu ophana chakhala chikukwera mboma la Dedza chifukwa mchaka cha 2018, anthu 20 ndiwo adaphedwa pomwe anthu 31 adaphedwa chaka chatha.
7
Khansala wa DPP Ali Mchitolokosi pa Mlandu Wa Kuba Khansala wa dera la Bangwe Mthandizi mu mzinda wa Blantyre, Isaac Jomo Osman ali mchitolokosi cha apolisi pomuganizira kuti akhuzidwa ndi mchitidwe owononga katundu komanso kuba. Akuyankha mlandu wakuba-Osman Malinga ndi ofalitsa nkhani za polisi ya Limbe, Inspector Patrick Mussa, khansalayu yemwe ndi wa chipani cha DPP ndipo amadziwikanso ndi dzina loti Mtopwa 1 wamangidwa lolemba mu tawuni ya Limbe. Inspector Mussa wati pa 25 May 2019, phungu wa kunyumba ya malamulo mdera la Bangwe, Orphan Shawa anali kunyumba kwake ku Mpingwe kukondwelera kupambana kwake pa chisankhocho ngati phungu woyima payekha. Chikondwelerochi chili mkati, Osman ndi anzake ena akuti anafika ku nyumbayi atanyamula zikwanje ndi kuyamba kuswa magalasi a galimoto zitatu komanso kuba lamya zammanja zisanu zomwe ndi za ndalama zokwana 1 million and 35 thousand kwacha. Isaac Jomo Osman amachokera mmudzi mwa Mtalimanja mdera la mfumu yaikulu Mponda mboma la Mangochi.
7
Atuma anthu kupha Apolisi mboma la Chitipa atsekera mchitokosi bambo wina pomuganizira kuti adatuma achiwembu kupha mkazi wake wakale. Facksoni Simbeye adatuma Filisoni Mbendera wa zaka 38 ndi bambo wina yemwe akungodziwika kuti Mshani kupha Lyness Mtawa, awiriwa atasemphana maganizo pankhani zina zambanja. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi mneneri wapolisi mchigawo cha kumpoto, Maurice Chapola, izi sizidamukomere Simbeye ndipo adakonza chiwembuchi pa 6 mwezi uno. Maiyu adapezeka ataphedwa mmunda wa chimanga, koma atakhapidwa kwambiri mmutu, adatero Chapola. Chapola adati anthu a mmudzi mwa Fyson Nyondo, T/A Mwabulambia mbomalo adatsatira mapazi kuchokera pomwe maiyu adaphedwera. Mneneriyu adati apa mapaziwa adalunjika mnyumba mwa Mbendera, yemwe ataona khamu la anthuli adalikumba liwiro la mtondo wadooka. Komabe adamugwira pomwe adaulula kuti Simbeye ndiye adawatuma kupha maiyu. Apatu anthu sadaugwire mtima koma adamtibula mpaka kumupha, adatero Chapola. Ndipo mmodzi mwa anthu omwe amachokera mudzi umodzi ndi Mtawa koma adakana kutipatsa dzina lake adatsimikizira Msangulutso kuti Simbeye ndiye adakonza chiwembuchi kaamba ka ndalama za banki mkhonde. Bamboyo adati ngakhale Simbeye adavomera atagwidwa ndi anthu a mmudzimo kuti ndiye adakonza upowo Banja lawo lidatha mwezi wa Novembala atakhala zaka zoposa zisanu, koma nkhani idagona pa K200 000 ya banki nkhonde yomwe mayiyo adatenga, adatero bamboyu.
15
Ntchito yomanga njanji iima Ntchito yomanga njanji yochoka ku Kachaso kupita ku Nkaya ayiimitsa mpaka kampani ya Mota-Engel ndi ogwira ntchito kukampaniyo atamvana chimodzi. Ogwira ntchitowo akunyanyala pofuna kukakamiza mabwana awo kuti awakwezere malipiro komanso kuti nzika 300 za ku Thailand zipakire. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kunyanyalaku kudayambira Lolemba pa 24 June ndipo Lachiwiri Nduna ya za Ntchito Eunice Makangala idatsetserekera kumeneko kukalankhula ndi ogwira ntchitowa kuti abwerere kuntchito koma izi sizidaphule kanthu chifukwa pofika Lachitatu mmawa nkuti ogwira ntchitowa asadabwerere kuntchito. Mmodzi mwa ogwira ntchito kumeneko ndipo akuchita nawo sitalakayo koma sadafune kutchulidwa dzina adauza Tamvani Lachitatu kuti iwo sagwira ntchito mpaka dandaulo lawo litamveka. Ndikukamba pano anzathu akubwera kuchokera ku Mwanza kudzatithandiza sitalakayi, sitibwerera kuntchito mpaka titaona malipiro athu akukwera komanso anthu omwe achoka mdziko la Thailand akubwerera kwawo, adatero mkuluyo. Padakhota nyani mchira mpakuti kampaniyi sabata zitatu zapita akuti inathotha gulu la ogwira ntchito kumeneko omwe ndi a mdziko muno ndi kulemba ena ochokera ku Thailand. Anthuwa akuti ndi pafupifupi 300 koma chenicheni chomwe amabwerera mdziko muno sichioneka chifukwa ena sadziwa ntchito ndipo amachita kuphunzitsidwa ndi Amalawi. Chodabwitsa nchakuti malipiro a akunjawo adali okwera kuposa a Amalawi omwe amatha ntchito. Ntchito yake yomwe akugwira ndi kuyendetsa mathirakitala ndi a mabewula zomwe Amalawi timatha, ena mwa alendowo sakuthanso kugwira ntchito ndipo tikuwaphunzitsa ndife. Tikudabwa kuti izi zikuchitika bwanji? Nanga nchifukwa chiyani akulandira ndalama zoposa ife omwe tikutha ntchito? adadabwa mkuluyo. Malinga ndi iye, Amalawi akulandira ndalama yosaposa K30 000 pomwe akamuna akunjawa akumatula makwacha owaposa iwo. Koma Makangala adati walankhula ndi akuluakulu a kampaniyi kuti mamulumuzana a mdziko la Thailand omwe alibe ukadaulo wa ntchito apakire ndipo azipita. Lolemba, mkulu wa kampaniyi Jose Denis da Silva wati akuluakulu a kampaniyi akukambiranabe ndi ogwira ntchitowa ndipo iye adapereka chiyembekezo kuti kusamvanaku kutha popanda zovuta. Mota-Engel ndi kampani yomwe yalemba kampani ya ku Brazil yotchedwa Vale kuti imange njanjiyi yomwe ikuchokera ku Moatize ku Tete mpaka ku Nacala Port mdziko la Mozambique kudutsira mdziko la Malawi. Malinga ndi yemwe amatitsina khuku pankhaniyi, pofika Lachinayi akuti mbali ziwirizi zinalepherabe kugwirizana ndipo zomwe auzana nkuti zokambirana zidzachitike Lachiwiri sabata ikudzayi. Izi zikusonyeza kuti sitigwira ntchito mpaka Lachiwiri lomwe tidzagwirizane mfundo zenizeni tisanabwerere ku ntchito. Pazokambiranazo akutinso kubwera akuluakulu ena a kampaniyi ochokera mmayiko ena komanso mbali ya boma. Sitikusinthika pa mfundo zathu kuti akuluakulu a dziko la Thailand azipita ndipo timva kuti pomwe tikumane Lachiwiriro atiuza zotani, adatero mkuluyo. Pomwe timalemba nkhaniyi nkuti yankho pa kunyanyalako lisanadziwike. Kampani ya Mota idalemba Amalawi oposa 3 000 omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana kumeneko.
17
Papa Wati Anthu ali ndi Njala ya Mtendere Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati dziko lapansi lili pa njala ya mtendere chifukwa anthu alibe mtendere wa mtima. Papa Francisko walankhula izi lachinayi pa misa kulikulu la mpingo ku Vatican. Papa Francisko wati dziko lapansi lingakhale pa mtendere weniweni pokhapokha ngati poyamba munthu aliyense paekhapaekha ali ndi mtendere mu mtima. Papa Francisko Iye wati nzosatheka kumakamba za mtendere pa dziko la pansi ngati anthu eni akewo alibe mtendere mu mtima mwao. Pamenepa iye wati mtendere wa mu mtima umabwera ngati anthu azika mizu ya moyo wao mwa mulungu. Aliyense wodzitchula kuti ndi mkhristu koma chonsecho ali kalikiliki kubweretsa chisokonezo pa banja lake, mmudzi mwake, ku ntchito kwake ndi malo ena onse omwe apezeka ngwabodza ndipo sayeneranso kudzitchula kuti ndi mkhristu, watero Papa Francisko. Iye wati mtendere ungabwere pa dziko ngati anthu agonjera Mulungu ndipo ngati azika mizu ya moyo wao mwa Mulungu. Papa Francisko wati ndi Mulungu yekha amene angabweretse mtendere pa dziko lapansi kudzera mwa Mzimu Woyera kuti Mzimu Woyerayo akhazikike mu mtima mwa munthu aliyense. Iye wati kuzika mizu mwa Mulungu zitanthauza kukondana wina ndi mzake. Ichi Papa Francisko wati ndiye chinsinsi chobweretsera mtendere pa dziko. Papa Francisko wafotokoza kuti kukondana wina ndi mzake zitanthauza kukamba zabwino za ena osati kukhalira miseche. Pamenepa iye wati aliyense akuyenera kumadzifunsa ngati kudzera mzokamba zake akuthandiza kubweretsa mtendere pa dziko kapena ayi. Papa Francisko wati satana amakondwa pamene anthu akumenyana kapena kukangana popeza cholinga chake chimakhala chakwaniritsidwa. Pomaliza Papa Francisko wati mtendere ndi mphatso ya Mzimu Woyera.
14
President Mutharika Wavomereza Ansah Kuti Atule Pansi Udindo Mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika wavomereza mayi Dr. Jane Ansah SC kuti atule pansi udindo wawo ngati wapampando wa bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC). Wazisiya-Ansah Lachinayi usiku, Dr. Ansah anafotokoza kuti walembera kalata akuluakulu omwe adamuika pa udindowu, za ganizo loti akufuna kuyima pa udindowu osati chifukwa chokakamizidwa, koma kuti ati amalemekeza malamulo. Ndipo polankhula ndi Radio Maria Malawi mneneri wa mtsogoleri wa dziko lino Mgeme Kalirani wati povomera ganizo la mayiyu, President Mutharika wati Dr. Ansah anali munthu okonda dziko lake. Ndizoona kuti President Professor Arthur Peter Mutharika wavomereza khumbo la mayi Dr. Ansah SC chotula pansi undindo ngati chairperson wa bungwe la MEC. Mmawu awo a President ati mayi Ansah anali munthu wokonda dziko lawo komanso anagwira ntchito yotamandika ku bungweli ndipo awafunira zabwino pa ntchito zina zomwe azigwira pamene achoka pa udindowu, anatero Kalirani. Chidwi cha anthu chili pa iye-Mutharika Pamenepa Kalirani wati president-yu achita machawi posankhanso munthu wina woti alowe mmalo mwa Dr. Ansah pokonzekera chisankho chomwe chikudzachi. Sipatenga nthawi yaitali. Ntchito imeneyi a President ayithamangitsa kuti ichitike mwachangu potengera ndi chisankho chomwe chikubwerachi, anatero a Kalirani. Mwazina Kalirani wati mtsogoleri wa dziko lino ali ndi mphamvu yolembanso ntchito makomishonala a bungwe la MEC omwe alipo pa dakalipano pamene contract yawo ifike kumapeto pa 5 June.
11
Teketeke popereka zikalata Mzinda wa Blantyre mudali teketeke msabatayi pomwe bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalandira zikalata za omwe akufuna kudzaimira nawo pachisankho cha pa 2 July. Ngakhale anthu amene adaloledwa mchipinda choperekera zikalatazo ku Sunbird Mount Soche adatsata ndondomeko zopewera matenda a Covid-19, chipwilikiti chidali panja pomwe anthu samakhala motalikana. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chakwera adzaima limodzi ndi Chilima Mwa anthu 9 omwe amayenera kupereka zikalata zawo, atatu okha ndiwo adavomerezedwa kutero. Lazarus Chakwera motsatana ndi Saulos Chilima adzaimira mgwirizano wa Tonse Alliance momwe muli zipani 9. Peter Kuwani adzaimira Mbakuwaku Movement for Development motsatana ndi Archibald Kalowongoma pomwe Peter Mutharika motsatana ndi Atupele Muluzi adzaimira mgwirizano wa zipani zaDPP ndi UDF. Smart Swira, Phunziro Mvula, Chikomeni Chirwa, Shaibu Mustafa, Khwechani Nkhoma ndi Levelend Kaliya adakanika kukhala nawo pamndandandawo kaamba ka zolinga zina, monga kulephera kukwanitsa zofunika. Mutharika ndi Muluzi atapereka zikalata zawookhawo Atamaliza kupereka zikalata zake, Chakwera adati nthawi yosintha zinthu tsopano yakwana ndipo adadzudzula kwambiri MEC posayendetsa bwino chisankho cha pa 21 May chaka chatha, chimene bwalo lamilandu lidagamula pa 3 February chaka chino kuti nchosavomerezeka. Kuwani, yemwe adasonyeza mkwiyo chifukwa chisankho cha 2019 sichidabale zipatso, adayamikira womutsatirayo posafooka. Ndipo mmawu ake, Mutharikaadati ngakhale akudziwa kuti adapambana chisankhocho, ali ndi chikhulupiriro chonse kuti iye apambana pachisankho chikudzachi chifukwa akuimalimodzi ndi Muluzi yemwe akudziwa bwino za chitukuko. Polankhula ndi opereka zikalatazo payekhapayekha, wapampando wa MEC Jane Ansah adati pochita kampeni, atsogoleriwo ayenera kubwera ndi njira zatsopano zochitira kampeni. Malinga ndi matenda a Covid-19, boma lidati anthu asakhale oposa 100 malo amodzi, zimene zingakhudze kampeni yomwe idayamba pa 2 May. Padakalipano, akadaulo a za ndale ena aikapo mlomo pa momwe chisankhochi chikuyendera. Ndipo kadaulo wina, Humphreys Mvula adachenjeza kuti ngakhale mwayi wa misonkhano uli wovuta malingana ndi nkhani ya Covid-19, zipanizi zisabwekere pa momwe zidachitira pa chisankho cha 2019 koma kuti apeze njira zodzigulitsira kwa anthu. Taona mtima wodzichepetsa kwambiri mwa atsogoleri a ndale chifukwa zomwe anthu ambiri amakayika kuti zingatheke, zatheka ndiye kwatsala nkuchilimika kukopa anthu kuti zidzayende bwino pachisankho, adatero Mvula. Oyendetsa ntchitoza mgwirizano wa mabungwe okhudzana ndi zisankho wa Malawi Electoral Support Network (Mesn) Andrew Kachasu adati zateremu zakhala bwino chifukwa zasonyeza kuti zokonzekera chisankho zikuyenda koma iye adati zipani zipewe mtopola. Zikamatere ndiye kuti zikuyenda bwino tsono chomwe ndingapemphe nchoti popanga kampeni, zipani ziyike mtima pogulitsa mfundo zawo osati kunena za ena kapena kulankhula monyodola ena ayi, adatero Kachasu. Kadaulo pa za malamulo Nandini Patel adatanthauzira mgwirizano ngati ubale omwe zipani ziwiri kapena koposa apo zimapanga ncholinga choonjezera mwayi wawo wopeza mavoti ochuluka pachisankho. Pachisankho chomwe bwalo lidatembenuza, chipani cha Mutharika yemwe adaimira DPP adapeza mavoti 1 940 709 kuimilira anthu 38 pa 100 aliwonse; Chakwera wa MCP adapeza 1 781 740 kuimilira anthu 35 pa 100 aliwonse; Chilima wa UTM Party adapeza mavoti 1 107 369 kuimira anthu 20 pa 100; pomwe Muluzi wa UDFadapeza 235, 164 kuyimira anthu 4 pa 100.Otolera: STEVEN PEMBAMOYO ndi WISDOM CHIROMBO idaphwanya malamulo a dziko pakayendetsedwe ka chisankhocho.
11
Mwambo wa maliro wasintha ku CoM Sukulu ya zaudotolo ya College of Medicine (COM) yasintha momwe mwambo wa maliro panyumba ya chisoni ya pasukuluyo mumzinda wa Blantyre uzichitikira kuyambira pa November 1 2015. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tsopano, galimoto imodzi yokha ndiyo iziloledwa kufika kumalowa yomwe izikhala ndi anthu osaposera 10. Panja pampanda wa sukuluyu pamene galimoto zimaima, tsopano sipakuloledwanso kuti paime galimoto. Woyendetsa sukuluyu Margaret Longwe adatsimikizira Msangulutso Lachinayi msabatayi ndipo adati anthu asaope ndi kusinthaku. Kotenga maliro kuzikhala anthu osaposa 10 Nayo mitengo yosamalira mtembo yasintha. Kuumitsa thupi (embalming) tsopano ndi K50 000 kuchoka pa K10 000, kusunga usiku umodzi ndi K10 000 kuchoka pa K1 000 pamene kusambitsa ndi kuveka ndi K15 000 kuchoka pa K10 000. China chomwe chasintha nkuti kumaloku sikuzikhalanso mwambo oona nkhope kapena mwambo wa mapemphero ndipo mmalo mwake izi zizikachitika kunyumba kapena kumpingo. Koma Longwe akuti zonsezi zachitika kufuna kusamala malowa. Palibe chodandaulitsa apa, dziwani kuti iyi ndi sukulu. Kukachitika maliro, kumabwera anthu ambiri mpaka kumachitira mapemphero zomwe si zabwino polingalira kuti apa ndi pasukulu. Panjapanso pamakhala galimoto zambiri moti ndi mwayi bwezi tikukamba kuti pachitika ngozi koma sizidachitikepo. Ndiye zonsezi tachita kuti tithandizane ndi anthu omwe amagwiritsira malo ano, adatero Longwe. Iye adati anthu akapita ndi thupi kumaloko, azifunsidwa kaye ngati akwanitse kutsatira malamulo atsopanaowo ndipo akakana, thupilo lizibwezedwa. Atafunsidwa kuti alankhulepo pa za kukwera mtengo, Longwe adati iyi si nkhani yoti tikambirane. Sitikulengeza mitengo mnyuzi, ndipo simudamvepo tikulengeza. Aliyense amadzamva komwe kuno akabwera za mitengo. Palibe nkhani pamenepa koma kungowadziwitsa anthu kuti iiyamba ndondomeko zatsopanozi pa 1 November, adatero iye. Wophwanya lamuliro, akuti adzalipa K50 000.
15
Mabungwe Akufuna Prophet Manyozo Anjatidwenso Wolemba: Thokozani Chapola Mgwirizano wa mabungwe omwe si a boma a mboma la Mangochi apempha kuti chilungamo chiwoneke pa nkhani yogwililira yokhudza Prophet Samson Manyozo ndi msungwana wina wachichepere. Wapampando wa mabungwewa Aggrey Mfune anati Prophet Manyozo anatulutsidwa pa belo ya khothi kaamba koti msungwanayu pamodzi ndi mayi ake anasowa mderali ndipo poganizira kuti awiriwa tsopano abweleranso, pakufunika kuti nkhaniyi ibwelerenso ku bwalo la milandu. Iwo ati zomwe anachita mneneriyu ndi zochititsa manyazi potengera udindo wake mdziko muno ndipo ati mkuyenera kuti lamulo ligwire ntchito mosayangana nkhope. Prophet Manyozo ndi muntu wa uemu wake koma zomwe anachita zija zikupereka chithunzithunzi choyipa kwa anthu. Ife timagwira ntchito ndi amipingo koma izizi sitingasekelere. Zomwe zinamuchitikira mwana uja sazayiwala mmoyo wake onse ndipo tikufuna kuti chilungamo chiwoneke pa nkhnaiyi, anatero a Mfune. A Mfune ati padakalipano mabungwewa akayitula kale nkhaniyi mmanja mwa apolisi ndipo apolisiwo alonjeza kuti alondoloza za nkhaniyi. Iwo ati mabungwewa apitiriza kumenyenera maufulu a wanthu kuphatikizapo ana achichepere ndipo wapempha boma kuti lizenge mlandu mayi wa mwanayu ngati sawonetsa chidwi choperekera umboni pa nkhaniyi. Kuthawa kwa mayiyu ndi mwana wake kukudabwitsa kwambiri komanso ndi komwe kunachititsa kuti Manyozo atuluke pa belo. Ngati mayiyo akukana kupereka umboni boma limatenga udindo wozenga mlandu mayiyo wobisa chilungamo. Izi ndi zomwe tikufuna ife kuti zichitike, chilungamo chiwoneke, anatero a Mfune. Prophet Manyozo anapalamula mlanduwu mmwezi wa June pomwe anagwililira msungwana wachichepere yemwe padakalipano akuphunzira pa sukulu ya pulaimale ya St. Augustine 3 mboma la Mangochi. Padakalipano mneneri wa apolisi mboma la Mangochi, Inspector Roderick Maida wakana kuthirapo mlomo ponena kuti nkhaniyi idakali ku bwalo la milandu.
7
Pulezidenti asamale ndi atidye nawo Mafumu, mphunzitsi wandale kusukulu ya ukachenjede ku Chancellor College kudzanso Amalawi ena ati mchitidwe wa andale ena posintha zipani kuti alowe chipani cholamulachonsecho maliro a mtsogoleri wakale ali mnyumbaungosonyeza kuti ndi anthu a dyera. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Akuluakuluwa ati ichi ndi chisonyezo kuti aphungu kapena nduna zina sizifuna kutukula Amalawi koma kusakaza zomwe zimayenera kuti zitukule anthu akumudzi. Akuluakuluwa ati kotero pomwe chipani cha Peoples (PP) chikulandira aphungu osomphoka kwina chisamale maka a chipani chakale cholamula cha DPP akhale tcheru ndi amadyowo. Ndemangazi zikudza kutsatira imfa yadzidzi ya mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bingu wa Mutharika yemwe adamwalira Lachinayi pa 5 mwezi uno atadwala matenda a mtima. Zitadziwika kuti a Bingu atisiya, yemwe adali wachiwiri wawo, Joyce Banda, adalumbiritsidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino potsatira malamulo a dziko la Malawi. Msamuko Koma Banda asadalumbiritsidwe nkomwe, aphungu komanso nduna zina zidaneneratu kuti izo zilowa chipani cha PP, ati potsatira zomwe anthu awo awauza. Nduna komanso aphungu ena akuti akhala akufika komwe kukukhala Banda kapena kuwailesi ya MBC kukalengeza kuti zalowa chipani cha Banda. Mwa ena, monga nduna ya zantchito, Lucious Kanyumba ndi wachiwiri kwa pulezidenti wa chipani cha DPP, Yunus Mussa adanenetsa kuti iwo tsono alowa chipani cha Banda ati anthu omwe adawasankha ndiwo anena. Apa ounikira ati ili ndi dyera chifukwa pachikhalidwe simuyenera kukamba nkhani zina pomwe maliro adakali mnyumba. Iwo achenjezanso kuti Banda akuyenera kusamala ndi atidyenawo chifukwa atha kudzathawanso ngati chipanichi sichikulamula. T/A Kapeni ya mboma la Blantyre yati pofika Lachitatu idali isadalumikizane ndi phungu wake kumeneko. Koma iyo adati pamiyambo ya makolo sikololedwa kumakamba nkhani zina maliro ali mnyumba. Pakhomo pakagwa azimu timadikira kuti tiike thupiro ndiye timakhala omasuka kukamba zina zokonza kapena kungounikira kumene. Tikamamva kuti zimenezi zayamba kale kuchitika zikutimvetsa chisoni; sibwino nthawi ino kukamba zoterezi. Ichi sichingakhale chitukuko chikunenedwacho, akuyenera kudikira mpaka titaika maliro, idatero mfumuyi. Aphungu adyera T/A Kachindamoto ya mboma la Dedza yati aphungu akumangonama kuti akutsata zomwe anthu omwe adawaika pampando anena. Ife phungu wathu kuno sadabwere kudzatifunsa maganizo ake ndipo sitingalolenso kuti tiyambe kukamba zimenezi maliro ali mnyumba. Umu simmene pachikalidwe chathu zikhalira. Tidikire kuti tikaike wokondedwa wathu bwinobwino monga a Pulezidenti anenera, adatero Kachindamoto. Senior Chief Malemia ya mboma la Nsanje yati phungu wawo yemwenso ndi wachiwiri kwa nduna ya zamigodi, Vera Chelewani adaitanitsa mafumuwo ndikuwafunsa chomwe iye ngati phungu wawo ayenera kuchita. Malemia wati zomwe adauza ndunayi nkuti igwire ntchito ndi boma chifukwa boma ndilo limaitanitsa chitukuko kumidzi monga kumanga mijigo ndi milatho komanso sukulu. Kaya akalowa chipani kaya ayi ife chomwe tikufuna nkuti agwire ntchito ndi boma kuti chitukuko chitifike. Ife mafumu tilibe chipani; chomwe tichita nkuthandiza boma lolamula kuti ligwire bwino ntchito yake. Zambiri sizili bwino mdziko muno monga kusowa kwa ndalama zakunja komanso mafuta, idatero mfumuyi. Iyo idati sidakambe zambiri ndi phunguyo ponena kuti sikulondola kukamba zambiri chikhalirecho maliro ali mnyumba. Sadatifunse Mlimi wa mtedza ndi chimanga, Nellie Banda wa mmudzi mwa Champiti kwa T/A Champiti mboma la Ntcheu wati phungu wawo kumeneko yemwe ndi wachiwiri kwa sipikala wa nyumba ya Malamulo, Jones Chingola, sadawafunsepo za ganizo losintha mawanga. Kuno tili ndi mavuto a kusowa sukulu, milatho koma phunguyu palibe chomwe wachita ndiye akamati akufuna chitukuko akutanthauza chani? Martin Susuwere wa mmudzi mwa Godeni kwa T/A Mpama mboma la Chiradzulu wati phungu wawo kumeneko yemwenso ndi nduna ya maboma angono, Henry Mussa sadafikenso kuti amve maganizo awo. Abwere adzatifunse maganizo athu, adatero dilaivalayu. Apa Chunga watsendera kuti aphungu kapena nduna zobulika ku zipani zawo lero zilibe mtima wofuna kutukula dziko kapena kuthandiza omwe adazisankha. Iye wati nduna zina zakhala zikuchita chimodzimodzi kuchokera kuchipani cha MCP, UDF ndi DPP ndipo pano zikufunanso zichite chimodzimodzi pomwe zikufuna zilowe ku PP. Banda asakomedwe Chunga wati ngakhale aliyense ali ndi ufulu wolowa chipani chomwe wafuna, komabe Banda asakomedwe ndi anthu oterewa ndipo sikoyeneranso kuwapatsa maundindo. Kastswiriyu adatsendera zonse ndi kuyamikira kusintha komwe Banda adachita pamaunduna ena. Lachiwiri msabatayi, Banda adasintha unduna wofalitsa nkhani omwe udapita kwa Moses Kunkuyu yemwe adalowa mmalo mwa Patricia Kaliati. Iye adasinthanso mkulu wa nyumba yowulutsira mawu ya boma ya MBC pomwe adachotsa Bright Malopa nkuika Benson Tembo komanso kuchotsa yemwe adali mkulu wa apolisi, Peter Mukhito ndikuika Loti Dzonzi. Iye adasinthanso mlembi wamkulu muunduna womwe umayendetsa chuma cha boma, Joseph Mwanamvekha nkuikapo Radson Mwadiwa yemwe adalinso paudindowu mu 2009. Banda wachenjeza kuti onse omwe akufuna kulowa chipanichi asapite pawailesi koma akumane ndi mlembi wachipanichi.
11
Azula chamba, achiyatsa ku KK Nkhani zoti apolisi alanda kapena azula chamba ndi zina zokhudza mbewu yozunguzayi sizikukata mboma la Nkhotakota. Lachiwiri sabata ino apolisi mbomalo, mogwirizana ndi asirikali oyanganira nkhalango ndi malo osungirako nyama zakutchire adazula chamba mmunda wamaekala atatu. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zachitika apolisi pa 12 September ataotchanso matani 4.5 a chamba amene adalanda kwa njonda zina. Aka nka chi 48 nkhani za mtunduwu kuchitika mbomalo chiyambireni January chaka chino, apolisi atero. Mneneri wa polisi mbomalo, Williams Kaponda, adati munda womwe adazula chambachi uli pakati pa midzi ya Senior Chief Mwadzama ndi T/A Mwansambo. Tidapeza chamba chochuluka mmundawu ndipo tidachizula ndi kuchiyatsa. Kufikira lero [Lachiwiri] palibe amene wanjatidwa pa nkhaniyi, koma apolisi tikufufuza kuti tipeze mwini mundawu, adatero Kaponda. Izi sikuti timapanga tokha, tidali ndi mboni zina monga akuluakulu a bwalo la milandu, khonsolo ya Nkhotakota, achipembedzo, atolankhani, a ku Parks and Wildlife Game Reserve ndi ena. Malinga ndi Kaponda, minda ina ya chamba yapezeka mmidzi ya Mwalawamphasa ndi Kanjedza mboma lomweli. Monga mwa mwambi woti moto umapita kumene kwatsala tchire, mmeneri wa polisiyu akuti mindayi nayonso aibutsa posachedwapa. Nkhanizi zikudza pamene pali mtsutso ngati kuli koyenera kuti dziko lino livomereze chamba kuti anthu azilima komanso kugulitsa. Mdziko muno chamba ncholetseddwa kkaamba koti chimazunguza ubongo. Boma la Nkhotakota limatchuka kwambiri ndi nkhani za chamba, chomwe anthu amalima mobisa mminda ya chinangwa, nzimbe ndi chimanga.
15
WLPS Ilimbikitsa Amayi Kukhala Mmaudindo a Zamasewero Bungwe lolimbikitsa amayi kutenga nawo mbali pa nkhani za masewero la Women Leadership Program in Sports lakonza mwambo wa masewero osiyanasiyana pakati pa masukulu a Primary a Chitawira komanso Mulambala ngati njira imodzi yolimbikitsira amayi ndi atsikana kutenga nawo mbali pamasewero osiyanasiyana mdziko muno. Mlembi wa ku bungwe loyendetsa masewero a tennis mdziko muno Regina Dembo wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Iye wati bungweli linakhazikitsidwa kuti lipereke mwawi kwa amayi ndi atsikana kuti azikhala maudindo oyendetsa ntchito za mmasewerowa. Bungweli likugwira ntchito zake matghandizidwa ndi ma bungwe Malawi National Council of Aports komanso Afican Union of Sports Council.
16
Aopa chinyengo pa mayeso a JCE Bungwe lokhudzidwa ndi kayendetsedwe ka maphunziro mdziko muno lati akhumudwa ndi zomwe lidachita bungwe la loyanganira mayeso la Maneb polola ophunzira ena kulemba mayeso a Junior Certificate of Education (JCE) a chaka chino popanda zitupa za umboni (ID). Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi nkhani za maphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC), Benedicto Kondowe, wati izi zikhoza kuchititsa kuti mayesowa alowe chinyengo. Polankhula ndi Tamvani Lachinayi lapitali, Kondowe adati ophunzira ambiri adalowa mpakana sabata yachiwiri ya mayesowo, amene adayamba pa 26 May, alibe ma ID ndipo zimadabwitsa kuti oyanganira mayeso amazindikira bwanji ophunzirawo ngati alidi olondola. Zimenezi, mphunzitsi kapena munthu wina aliyense akhoza kulembera wina mayeso oyanganira osadziwa chifukwa ntchito ya ID nkuthandiza oyanganira mayesowo kuzindikira ngati wolemba mayesoyo alidi iyeyo, adatero Kondowe. Mkuluyu adati izi zikusemphana kwambiri ndi malamulo oyendetsera mayeso omwe amaletsa wophunzira yemwe alibe nambala kapena ID kulemba nawo mayesowo. Mneneri wa bungwe loyendetsa mayeso la Maneb, Simeon Maganga, adatsimikiza kuti mayeso a JC adayambadi ophunzira ena alibe zitupa, koma adati mmene limafika tsiku lachinayi akulemba mayesowo ma ID onse adali atapita msukulu zoyenera. Maganga adati ophunzira pafupifupi 170 000 ndiwo adalemba nawo mayesowa koma adaonjeza kuti nkovuta kunena kuchuluka kwa ophunzira amene adalibe ma ID. Mmene mayeso amayamba tidali titapereka zitupa msukulu za Kumpoto ndi Kumwera koma tidakhalira ndi sukulu zina mchigawo cha Kumwera chifukwa zipangizo zopangira zitupazo zidali zosakwanira. Tidayesetsabe moti patatha masiku anayi chiyambireni mayeso tidali titatumiza zitupa zotsalirazo ndipo pano ophunzira onse ali ndi zitupa zawo, adatero Maganga. Koma Kondowe, yemwe alinso mkomiti yoona kuti mayeso akuyenda bwino komanso kuti palibe zachinyengo, adatsutsa zomwe adanena Magangazo ndipo adati mkati mwa sabata yomwe ino akuyendera mayeso adapeza ophunzira ena akulemba opanda zitupa zikunenedwazo. Tidapeza ophunzira ena msukulu zina mchigawo cha Pakati ndi ku Shire Highlands akulemba popanda zitupa ndiye zitupazo akapereka liti? adadabwa Kondowe. Potsutsapo za nkhawa ya chinyengo, Maganga adati a bungwe la Maneb mothandizana ndi oyanganira mayeso komanso akuluakulu a pasukulu amathandizana kuzindikira ophunzira omwe amalowa mchipinda cha mayeso, koma Kondowe adati pagulu lonselo amadziwa anawo bwino ndi akuluakulu a pasukulu moti atafuna kuchita chinyengo akhoza kupusitsa anzawowo. Takhala tikumva kuti akuluakulu a pasukulu amangidwa kapena kulipitsidwa chifukwa amachita chinyengo pamayeso ndiye angalephere bwanji kupusitsa anzawowo kuti zawo ziyende poti mphunzitsi aliyense amafuna mbiri yake izikoma ana akamakhoza mayeso? adatero Kondowe. Iye adati bungwe la Maneb likadavomereza kulakwitsa nkusintha kachitidwe ka zinthu kuti mavuto otere asamachitike kawirikawiri. Kondowe adati pologalamu yokonzekera mayeso a Maneb imasonyezeratu nthawi yomwe ophunzira oyembekezera kulemba mayeso akuyenera kupereka ndalama ya zitupa ndipo akatero bungweri limayenera kupanga zitupazo mayeso asadafike. Unduna wa zamaphunziro wasamba mmanja pankhaniyi ponena kuti nkhani ya mayeso si ya unduna koma bungwe la Maneb ndipo unduna ntchito yake nkuonetsetsa kuti silabasi ikuyenda bwino. Nkhani ikadakhala yakuti ana sadamalize silabasi ikadakhala yathu chifukwa ndiyo mbali timayanganira koma nkhani ya mayeso ndi ziphaso mufunse a bungwe la Maneb, adatero mneneri wa undunawu Manfred Ndovi. Komabe adati sikolondola kulola munthu yemwe alibe ID kulemba mayeso koma ngati unduna akambirana ndi a Maneb kuti zoterezi zisadzachitikenso. Kondowe adati musukulu 12 zomwe komiti idayendera mchigawo cha Pakati 6 mudapezeka ophunzira omwe amalemba mayeso popanda ziphaso ndipo pulezidenti wa eni sukulu zomwe si zaboma Joseph Patel adapereka lipoti lakuti msukulu 150 ophunzira adayamba kulemba mayeso opanda ziphaso. Ophunzira amaliza kulemba mayesowo dzulo pa 5 June.
3
Gulupa Mologeni Wapempha Akhristu Akonde Kuthandiza Radio Maria Mmodzi mwa agulupa a Parish ya Ntcheu mu Dayosizi ya Dedza a Molisiyo Felix Mologeni apempha akhristu ampingo wa katolika kuti atenge udindo othandiza Radio Maria ndi zomwe ali nazo kuti uthenga wamulungu upite patsogolo. Mgulupa Mologeni amalankhula izi lamulungu lapitali ku tchalitchi la Machira mu parishi-yi pomwe akhristu akutchalitchili amajambulitsa maprograme osiyana-siyana ku wailesi-yi. Iwo ati wailesi-yi imasowa zambiri ndipo akhristu ndi udindo wawo kuithandiza ndi ndalama kapena kujambulitsa maprogramme osiyanasiyana ku wailesi-yi ngati njira imodzi yotenga nawo gawo patchito yofalitsa uthenga wabwino, yomwenso ndi ntchito ya wailesi-yi. Ndi udindo wathu kuyithandiza Radio Maria njira ndipo njira ina yomwe tingaithandizire ndi mapologalamu chifukwa uthenga wathu umveka pa dziko lonse lapansi, anatero a Mologeni. Iwo ati ayamikira akhritsu akwa Machira Kamba kotenga nawo gawo popanga nawo mapologalamu omwe amamveka pa Radio Maria. Polankhulapo mkhala pampando wa tchalitchi cha Machira a Luka Fabiano anati ndi okondwa chifukwa achita mwayi ojambulitsa mapologalamu omwe wayilesiyi imaulutsa. Kudzera mu pologalamu ngati imeneyi timaphunzira zinthu zosiyanasiyana zomwe akhritsu osiyanasiyana akuchita, anatero a Fabiano.
13
Chipwirikiti pa Malawi Zomwe zikuchitika mdziko la Malawi zaimitsa mitu ya anthu kuphatikizapo akadaulo pa nkhani zosiyanasiyana. Msabata yomwe ikuthayi, zionetsero zomwe zidaima kwa masiku 14 zidayambiranso Lachitatu ndipo tsiku lomwelo, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika yemwe akuyenera kumva nkhawa za Amalawi ochita zionetserozo adanyamuka ulendo wa ku msonkhano waukulu wa mgwirizano wa maiko ku America. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ena mwa ochita zionetsero kusonyeza mkwiyo wawo Kuchokera pomwe zionetserozo zidayamba zotsatira za chisankho cha pa 21 May chitangochitika, Mutharika wakhala akutuma wachiwiri wake Everton Chimulirenji kukamuyimilira mmisonkhano yosiyanasiyana kunja kwa dziko lino. Mutharika adangotuluka sabata yatha kukakhala nawo kumaliro a mtsogoleri wakale wa dziko la Zimbabwe Robert Mugabe. Malinga ndi kadaulo pandale Makhumbo Munthali, ulendowu ukungotsimikiza kuti Mutharika sakukhudzidwa ngati mtsogoleri ndi zomwe zikuchitika mdziko lake. Ena mwa ochita zionetsero kusonyeza mkwiyo wawo Anyamuka bwanji momwe zinthu zililimu? Amayenera kukhalapo nkuona kuti chichitike nchiyani nkuonetsa utsogoleri wake. Apapa zikungoonekeratu kuti za anthu ake sizikumukhudza, adatero Munthali. Kadaulo pa ndale George Phiri wati zonse zomwe zikuchitika mdziko muno ndi nthabwala zokhazokha ndipo Amalawi apatsidwa mafunso omwe sakupeza mayankho ake konse. Kunena zoona, Mutharika samayenera kunyamuka ulendo wake akadatuma nthumwi ngati momwe wakhala akupangira mmbuyomo. Apa, ngakhale wapita, sikuti ndiye kuti mavutowa atha ayi, akamabwera adzawapezanso, adatero. Izi zili apo, bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), kupyolera mwa mkulu woyendetsa zisankho Sam Alufandika, lidalengeza kuti lichititsa chisankho chapadera kumwera mboma la Lilongwe November 5, 2019 ngakhale kuli zionetsero zoti mkulu wa bungwelo achoke. Chisankho sichidachitike mderalo pa 21 May chifukwa mmodzi mwa opikisana nawo, Agnes Penemulungu adamwalira chisankhocho chili pafupi kuchitika. Bungwe la MEC lidzakumana ndi onse okhudzidwa ndi chisankhochi pa 3 October 3 kuti lidzafotokoze ndondomeko yachisankhochi, adatero Alufandika mkalata yake. Koma akuluakulu a Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party ati sizingalole kuti bungwe la MEC liyendetsenso chisankho china mlandu omwe akukana zotsatira ukadali kukhoti. Zipanizo zidatengera kukhoti MEC ndi Mutharika powaganizira kuti adazondotsa zotsatira za chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino pomwe MEC idalengeza kuti Mutharika ndiye adapambana. Mlembi wamkulu wa MCP Eissenhower Mkaka adati chipanicho chilibe chikhulupiliro mwa bungwelo chifukwa ungwiro wake ukuyesedwa mbwalo la milandu. MEC siyikuyenera kuyendetsa chosankho chilichonse pokhapokha bwalo la milandu litapeza kuti ndi langwiro ndipo lidayendetsa bwino chisankho chapitacho, adatero Mkaka. Mneneri wa UTM Party Joseph Chidanti Malunga adati chisankho chapaderacho chayikidwa nthawi yolakwika. Ayi, ndi nthawi yakeyi sizidakhale bwino. A MEC amayenera kudikira asadapangitse chisankho china. Nthawi ndi zochitika sizikugwirizana, adatero Malunga. Munthali adadzudzula ganizo la MEC lochititsa chisankho chapadera pomwe Amalawi amachita zionetsero zotsutsana nalo. Apa zawonetseratu kuti kwa iwo, palibe kuthekera koti nkukambirana ndi Amalawi chifukwa asonyeza kuderera konse ndipo atenga Amalawi ngati opanda ntchito, watero Munthali. Koma poyankhapo, mneneri wa chipani cha DPP Nicholas Dausi adati MEC ikulondola pa zomwe ikupanga chifukwa ikutsatira malamulo. MEC ikuyenera kugwira ntchito yake potsatira gawo 76 ya malamulo imayipatsira mphamvu. Osasokoneza ntchito za MEC chifukwa cha mangawa, adatero Dausi.
11
Mutharika achenjeza akamberembere Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wasonyeza kuti amatsatira ukamberembere omwe umachitika mkatikati mwa malonda a fodya ndipo wachenjeza ogulitsa ndi ogula kuti sakufuna nyansizi chaka chino. Mutharika adapereka chenjezoli potsegulira msika wa fodya wa chaka chino ku ku Kanengo mumzinda wa Lilongwe Lachitatu lapitali. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Iye sadasiye mbali podzudzula ndi kuchenjeza onse okhudzidwa mmalondawa ponena kuti ogula ali ndi chisimo chosintha mawanga mkatikati mwa malonda pomwe ogulitsa adawadzudzula kuti amachulutsa ukamberembere poika zitsotso mmabelo awo. Inu makampani ogula fodya ndikuchenjezeni pano. Tsiku loyamba, mumagula fodya pamitengo yomwe idakhazikitsidwa koma kenako nkusintha mawanga mkatikati mwa msika. Zimenezi sitikuzifuna chaka chino, adatero Mutharika. Iye adati mchitidwe wotere umayambitsa mikangano pakati pa ogula fodya ndi alimi mpaka msika kumasokonezeka chifukwa cha kusamvana. Mutharika adatembenukiranso kwa alimi nkuwadzudzula kuti achepetse ukamberembere woika zitsotso mmabelo ndi cholinga chopusitsa makampani ogula fodya kuti mabelo awo azilemera pomwe muli fodya wochepa kapena woipa. Inuso alimi ndikuchenjezeni pakhalidwe loika zinthu zosayenera mmabelo a fodya. Khalidwe limene lija ndilo limapangitsa kuti makampani azibweza fodya wambiri pamapeto pake mumakhala ngatimudagwira ntchito yopanda malipiro, adatero Mutharika. Iye adati ali ndi chiyembekezo kuti malonda a fodya ayenda bwino chaka chino poyerekeza ndi zaka za mmbuyo pomwe kumakhala kusamvana kwakukulu pakati pa alimi andi makampani ogula fodya, makamaka pankhani ya mitengo ndi maonekedwe a fodya. Fodya wa chaka chino ayamba kumugula pamtengo wa $0.80 (pafupifupi K552) pa kilogalamu pomwe kusiyana ndi chaka chatha pomwe adayamba ndi $2.32 (pafupifupi K1, 044 pa kilogalamu potengera mphamvu ya kwacha panthawiyo). Izi zili chonchi, bungwe la Tobacco Control Commission (TCC) lati ndi lokhudzidwa ndi kuchuluka kwa fodya yemwe akubwezedwa potengera tsiku lotsegulira msikali pomwe mabelo 30 pa mabelo 100 alionse amabwezedwa. Mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira-Banda adati nzodabwitsa kuti kwacha yayamba kukwera mphamvu pomwe alimi akugulitsa fodya pomwe adagula zipangizo mokwera kwacha itagwa.
11
Okwiya aimitsa kumanga njanje Madzi achita katondo ku Nkaya mboma la Balaka komwe anthu okwiya aletsa kampani ya Mota Engil yomwe ikumanga njanje kumeneko kuti isiye kuthira dothi mminda mwawo komanso galimoto zawo zisadutsenso mmindamo. Anthuwa ati sasintha ganizo lawo pokhapokha akuluakulu a kampani ya sitima zapamtunda mdziko muno omwe akumangitsa njanjeyi ya Central East African Railways (Cear) awapepese. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kuyambira Lolemba mpaka Lachitatu msabatayi, ogwira ntchito pakampu ya Nkaya adangogwira mchiuno kudikira kuti akuluakulu awo akambirane ndi kugwirizana ndi anthuwo asanayambe kupitiriza kugwira ntchitoyo. Gulupu Nkaya adatsimikizira Tamvani Lachiwiri kuti anthu ake akwiya ndi zomwe anjanje akuchita pomatayira dothi mminda yawo popanda kukambirana kulikonse. Panopa anthuwo akufuna amvetsetse kuchokera kwa omanga njanjewa pazomwe zikuchitikazo, adabwera kunyumba kwanga kudzandifotokozera koma nanenso ndalephera kumvana nawo ndipo ndawauza anjanjewo kuti aime kaye ntchito yawo mpaka titakambirana, adatero Nkaya. Lachiwiri masana akuluakulu a Cear adakhamukira kumaloko kuti akakambirane ndi mfumuyo koma ngakhale Nkaya adatsimikizira anthuwo kuti ntchito iyambiranso, izi sizidachitike. Malinga ndi mneneri wa Cear, Chisomo Mwamadi, mgwirizanowo udali woti pofika 2 koloko masana a Lachiwiri ntchitoyo ikhala itayambiranso. Koma polowa kwa dzuwa Lachiwiri, ntchitoyo nkuti isadayambe, malinga ndi Nkaya. Ndayesera kukamba ndi anthu anga onse amidzi ya Nsoma, Mbiya ndi Nkaya kuti awalole anthu agwire ntchito yawo, koma ndalephera. Anthu akukana ndipo akuti pokhapokha a Cear awapepese [ndi kena kake osati pakamwa pokha] mpamene awalole kuti apitirize kugwira ntchito. Poyamba tidakambirana ndi akuluakulu a Cear ndipo tidagwirizana kuti tiwalole apitirize kugwira ntchito titagwirizana kuti tsiku lina abwera anthu ena kuchokera ku Cear kuti adzakambirane ndi anthuwo. Mpaka lero palibe chogwirika tachiona nchifukwa chake anthuwa akukana kuti ntchito isagwiridwenso pokhapokha anthu amene adawatchulawo atabwera, idatero mfumuyi. Koma mkulu wa Cear, Hendry Chimwaza, adati nayenso ndi wodabwa kuti mfumuyi ikulephera kulamula anthu ake kuti amvere zomwe adagwirizanazo. Njanje si yathu, njanje ndi ya anthu ndipo mfumuyi ndi mboni kuti kubwera kwa chitukuko cha njanje kwabweretsa ntchito zambiri zotukula anthu ake monga kulembedwa ntchito ndi malonda kungotchulapo zochepa. Za malo otaya dothi komanso modutsa makina athu tidakambirana koma tikudabwa lero kumva nkhaniyi. Mfumu kulephera kukambirana ndi anthu ake? Komabe tisathe mawu, tikambirana nawo ndipo ntchito ipitirira. Tikulankhula pano nkhaniyi taikamba kale ndipo kwatsala nkuona ntchitoyi ikugwiridwa, adatero Chimwaza Lachitatu. Atafunsidwa ngati nkhaniyi akuidziwa akuluakulu a boma, Chimwaza adati idakali kaye mmanja mwawo ndipo ngati pena patavuta adziwitsa akuluakuluwa. Kupatula kuthira dothi mminda, china chomwe anthuwa akudandaula ndi galimoto zikuluzikulu ndi makina awo zomwe zimadutsa mmindamo. Mmodzi mwa anthuwo, amene adakana kutchulidwa dzina, adati mgwirizano wawo ndi anjanje udali woti alandira ndalama kuti galimotozo zizidutsa mminda mwawo komanso kuti azitayira dothi mdera lawo. Poyamba amati angothira dothi mmalo amene minda yakokoloka ndipo dothilo athira ndipo akupitirizabe kuthira moti sitingalimenso nchifukwa chake tawaletsa, adatero. Ntchito yomanga Nkaya siteshoni idayamba chaka chatha mu November ndipo gawo loyamba latha June chaka chino. Chimwaza adati gawo loyamba lidali kumanga njanje zina ziwiri kuphatikizapo yakale yomwe idalipoyo, kukwanitsa zitatu. Kumanga kwa njanjezi kuthandiza kuti sitima zitatu zizitha kupatukirana pa Nkaya popanda vuto lililonse komanso azitha kuchulutsa ndi kuchepetsa mabogi, zomwe sizimachitika poyamba.
17
Alandira makuponi abodza kuchoka ku boma Mitu ya alimi ena ku Mpemba kwa T/A Somba ku Blantyre yabalalika pomwe auzidwa kuti makuponi omwe alandira ndi achinyengo. Iwo adalandira makuponiwo Lachiwiri pa 27 Novembala ndipo atapita kogula mbewu Lachitatu adauzidwa kuti makuponiwo ndi achinyengo.
4
Anthu oposa 20 afa pa ngozi ya Galimoto ku Ntcheu Anthu 20 afa ndipo ena 31 avulala galimoto yayikulu yonyamula katundu itawagunda pa msika wa Kampepuza mboma la Ntcheu. Wofalitsa nkhani za apolisi mbomali Sub-Inspector Hastings Chigalu wati galimotoyi nambala yake ndi 1152 ndipo imachokera ku Lilongwe kupita ku Balaka ndipo itafika pa msikapa dalaivala wa galimoto-yi analephera kuyiongolera bwino ndipo inaphonya msewu ndi kukagunda anthu-wo. Pali chiyembekezo choti chiwerengero cha anthu omwe afa chitha kukwera kaamba koti anthu ena agonekedwa ku chipatala cha boma la Balaka komanso ku Kamuzu Central Hospital. Padakalipano boma lati lichita chilichonse chotheka kuthandiza anthu omwe avulalawa komanso liyendetsa mwambo wonse wa maliro a anthu omwe afa pa ngoziyi.
14
Mkangano wa mafumu sukuzirala Ntchito za chitukuko zagwedera mboma la Neno, Nsanje komanso Salima kaamba ka mpungwepungwe wa mafumu womwe sukutha. Ku Neno boma lidathotha mfumu Chekucheku mu 2014. Mpaka lero boma silidabwezeretse mfumuyi zomwe zapangitsa kuti ofesi ya DC ndi khansala asowe wogwira naye ntchito za chitukuko. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chekucheku amene akudikira boma limubwezeretse DC wa boma la Neno, khalansala komanso phungu wa Nyumba ya Malamulo kumeneko akuti mdera la Chekucheku chitukuko chikuvuta chifukwa palibe mfumu yeniyeni yomwe angagwire nayo ntchito. Nako ku Nsanje, boma lidaimitsa mfumu Chimombo ndipo lidapatsa mphamvu Harrison Chimombo kuti abagwirizira. Mpaka lero boma silidapezebe wolowa mmalo mwake zomwe zapangitsa kuti anthu agawanike. Mfumu Bibi Kuluunda ya ku Salima yomwe idaimitsidwa paudindo ndi boma akuti maso ake ali ku boma kuti amubwezeretse ufumu wake chifukwa iye ndiye woyenera ufumuwo. Boma lidaika mbale wa mfumuyi kuti agwirizire ufumuwu kufikira mpungwepungwe utazirala. Mafumuwa ndiwo amathandizira kuti chitukuko cha paboma lawo chiyende bwino pogwira ntchito ndi makhansala, ofesi ya chitukuko pa boma, komanso ofesi ya DC. Koma mneneri wa ku unduna wa za maboma angono Muhlabase Mughogho akuti bata lidzabwerera pokhapokha eni banja atadya khonde ndi kutulutsa munthu woyenerera amene angagwire ntchito ndi boma. Tili ndi gawo lothandizira komabe mphamvu zili mmanja mwa abanja kuti atipatse mfumu, adatero Mughogho. Mughogho akuti boma silivomereza mfumu yogwirizira. Dziwani kuti boma siligwira ntchito ndi mfumu yogwirizira. Izi zikutanthauza kuti ku Salima, Nsanje ndi Neno kulibe mafumu omwe boma lingagwire nawo ntchito. Naye DC wa ku Neno Ali Phiri adapempha abanja kuti atulutse munthu amene angalowe mmalo mwa mfumu Chekucheku amene adachotsedwa, koma mwadzidzidzi kudaperekedwa maina asanu. Sizikadatheka kuti onse angakhale mfumu nthawi imodzi. Zidakanika. Ndiye ndivomereze kuti mpaka pano tilibe mfumu Chekucheku, adatero Phiri. Phiri adati akugwira ntchito ndi makomiti azachitukuko akumudzi chifukwa chosowa mfumu zomwe adati nzovuta. Komabe chitukuko chikutheka ngakhale zina zikufunika amfumu. Khansala wa dera la Chikonde kwa mfumu Chekucheku, MacPherson Dzimadzi adati ntchito yomanga midadada pa sukulu ya Kalioni ndi Chiwamba ikukanika chifukwa chosowa kwa mfumu Chekucheku. Pali ntchito yotuta mchenga, njerwa komanso kwale yomwe ikukanika. Ndidauza mafumu angonoangono kuti atsogolere anthu awo koma zikukanika chifukwa palibe wamkulu amene angawalankhule. Nthawi zina ndikumaweruza milandu ya mafumuwa akayambana nthawi zina ndikumawatengera kwa DC, adatero Dzimadzi. Ndivomere mavuto alipo chifukwa chosowekera kwa mfumu Chekucheku, adaomba mkota Dzimadzi. Malinga ndi ndime 23:03 gawo II gawo la malamulo okhudza mafumu, boma lidaimitsa mfumu Chekucheku yemwe dzina lake ndi Francis Magombo kuti asagwirenso ntchito za ufumuwu mboma la Neno kuyambira pa 15 May 2014. Lachiwiri msabatayi, Chekucheku adauza Tamvani kuti akudikirabe boma limuvomere kuti ayambirenso kugwira ntchito. Ufumu umene uja ndi wanga ndipo ndikungodikira mtsogoleri wa dziko lino kuti andibwezeretse pa mpandopo, adatero. Ku Nsanje mamembala ena abanja la mfumu Chimombo adalembera DC wa bomalo, komanso unduna wa maboma angono kuti asabwezeretse Chimombo amene adachotsedwa mu December 2012. Mfumu yochotsedwayo, Stanford Tukula, idachotsedwa pamene imaganiziridwa milandu yosowetsa katundu. Ku Salima boma lidaimitsa mfumu Kuluunda, Khadija Habib Saidi, mu May chaka chatha chifukwa chomuganizira ziphuphu. Mpaka lero boma silinabwezeretse mfumuyi ndipo mbale wake wa mfumuyi ndiye akugwirizira ufumuwo. Pocheza ndi Tamvani Lachiwiri, mfumuyi idati ndikudikirira aboma kuti andibwezeretse pampando. Koma katswiri pa zandale Henry Chingaipe mmbuyomu adauza Tamvani kuti dziko lino silidafike pomagwira ntchito yake popanda mafumu. Pakufunika Chiefs Act [Malamulo okhudza mafumu] atakonzedwanso kuti tidziwe ntchito za mafumu komanso za mtsogoleri wa dziko pa nkhani zokhudza mafumu, adatero. Sitidafikepo pomagwira ntchito popanda mafumuwa, ndiwofunikabe koma pokhapokha titadziwa ntchito zawo pamene tili [mu ulamuliro wa zipani zambiri]. Mkulu woyendetsa nkhani zachitukuko ku Neno, Henry Chitema, akuti kusowekera kwa mfumu Chekucheku kwasokoneza nkhani zachitukuko. Chitema akuti mfumuyi imayenera kutsogolera anthu ake ndi mafumu ake kuti agwire ntchito za chitukuko. Ena tikawauza kuti tigwire ntchito akumatiuza kuti iwo ndi abanja lachifumu kotero sangagwire ntchito, adatero. Boma la Neno lili ndi mafumu anayi panopa tatsala ndi ma T/A atatu. Tilibe amene angayimire anthu a kwa Chekucheku. Izi zatikhudza.
8
Nam yapindulanji pa Tigresses? Bungwe la Malawi National Council of Sports tsopano layeretsa timu ya Tigresses kuti Nam ndiyo yolakwa pankhani yoti timuyi ichotsedwe mchikho cha Presidential Initiative for Sports chifukwa idaseweretsa wotupa mchombo. Tithokoze kuti chilungamo chadziwika ndipo timuyi ipikisanabe mchikho cha apulezidenti. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Tilangizeko Nam kuti sibwino kuchita zinthu mwa nkhwidzi, zigamulo zinazi tiyeni tizilowa mmalamulo chifukwa zikusokoneza. Taonani chikho cha apulezidenti chidayima pamene timati tikupseda. Onaninso kuti osewera a timuyi asiyidwa ku Australia. Ndalama zawonongeka komanso mwasokoneza timu ya dziko lino. Nam sibwino kumaonetsa poyera matimu amene mumakwera. Kukhala ndi timu yapamtima sikoletsedwa koma zimafunika kuti matimu onse azithandizidwa mofanana. Zotere musadzachitenso, aka kakhale komaliza. Pajatu timuyi ili panambala yoyamba mu Africa muno ndiye sitikufuna ichoke pamenepo. Mwaphunzirapo kanthu chonde sinthani kusanade. Tifunire zabwino zonse timu ya dziko lino yomwe ili mdziko la Australia kukapikisana ndi matimu ena anayi. Mary Waya ndi Griffin Saenda gwirani ntchito ndi osewera 12 mwatengawo ndipo ife tikuyembekezera zabwino. Aganyu msabatayi timakambirana za mphunzitsi wabwino mdziko muno. Zikuonetsa kuti aphunzitsi odziwa ntchito alipo amene mwina utawapatsa mwayi atha kunyamula Flames. Aganyu ambiri akukambabe za mphunzitsi wakale Kinnah Phiri kuti ndiye wabwino. Ena akukamba za Elijah Kananji wa Blantyre United. Pamene Fam ikusakasaka mphunzitsi wa Flames, chonde tawunguzani mdziko muno.
16
DPP ikhumudwitsa ku KK Mafumu ena ku Nkhotakota ndi okwiya ndi chipani cha DPP chimene akuchidzudzula pogwiritsa ntchito galimoto ya chipatala pa ntchito zachipani. Lachisanu pa 15, chipanicho chidatenga galimoto ya chipatala cha Nkhotakota kukasiya otsatira chipani ku Lilongwe komwe amakatsanzikana ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pa ulendo wake wopita ku msonkhano wa United Nations General Assembly (Unga) mdziko la United States of America. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Galimoto limene lidanyamula a chipani kupita ku Lilongwelo Izitu zimachitika pamene anthu pachipatalapo amasowekera thandizo la mayendedwe malinga ndi phungu wa Nyumba ya Malamulo ku Nkhotakoka, Peter Mazizi. T/A wina amene adapempha kuti tisamutchule, adati mafumu ena akhala akupempha kuti mchitidwewu uthe komabe izi sizikuphula kanthu. Si koyamba kuti a DPP agwiritsire ntchito galimoto ya pachipatalapa. Timalankhula koma palibe yankho, idatero mfumuyi. Anthu amene akufuna thandizo la galimotoyo amadikira kaye kuti ithandize achipani. Koma mlembi wa chipanicho, Greselder Jeffery wati izi ndi ndale chabe ndipo si zoona kuti adagwiritsira ntchito galimoto ya chipatala. Mmmh! abale, komatu ndalezi ndiye zafika penapake, adatero potsutsa nkhaniyi. Si zoona kuti tidagwiritsira ntchito galimoto ya chipatala. Kodi anthu asamavale makaka a chipani chathu akakwera galimoto ya boma? Mwina anthuwo amapita ku maliro, chifukwa masiku ano anthu akumavala makaka achipani chathu ngakhale pa ukwati, adatero Jeffery yemwenso ndi phungu kumpoto kwa boma la Nkhotakota. Titafunsa mneneri wa chipatala cha Nkhotakota ngatidi zidali zoona kuti galimoto yawo idanyamula anthu a chipani, mneneriyu, Samson Mfuyeni adavomera koma adati galimotoyo si ya boma. Ogwira ntchito pachipatalachi ndiwo adagula galimotoyo. Adaonjeza: Ndi galimoto ya chipatala osati boma. Timaigwiritsira ntchito zinthu zambiri. Ndi zoona achipani cha DPP adabwereka poperekeza apulezidenti, adatero. Malinga ndi Mfuyeni, palibe cholakwika kubwereketsa galimotoyo chifukwa si ya boma. Koma kafukufuku wathu wapeza kuti galimotoyo, MG 697AJ ndi ya unduna wa zaumoyo ndipo ikugwira ntchito pachipatala cha Nkhotakota. Malinga ndi mkulu wina ku Plant and Vehicle Hire Organisationnthambi yomwe ili pansi pa unduna wa zamayendedwe, galimotoyi yomwe ndi lole, ili mmanja mwa boma ku unduna wa zaumoyo. Khalidwe la DPP lakwiyitsa phungu Mazizi wa deralo amene wati aka si koyamba kuti chipanichi chitenge galimotoyo. Iye wati wakwiya kwambiri chifukwa patsiku lomwe galimotoyo imatumikira chipani, pachipatalapo padali maliro anayi amene amafunika anyamulidwe. Anamfedwa adandidandaulira, ndipo ndidasiya zomwe ndimachita kukawathandiza pamene galimoto yathu imatumikira chipani, adatero. Nkhaniyi ikudza pamene a mabungwe omwe si aboma akukakamiza chipanichi kuti chibweze K13 miliyoni yomwe chidalandira ku nthambi zaboma pa mwambo womwe chipanichi chidachititsa pa 29 July ngati njira imodzi yopezera ndalama. Kadaulo pandale Mustafa Hussein wati zomwe chapanga chipani cha DPP pogwiritsira ntchito galimoto ya chipatala ponyamula masapota ake pokaperekeza pulezidenti Peter Mutharika ndi kulakwira Amalawi ndipo zotere zitheretu. Amalawi sangavomere kuti ndalama zawo zizigwiritsidwa ntchito chonchi. Ndi kulakwa posatengere chipani chomwe chikupanga izi, adatero Hussein.
11
A Escom adziwe kuti takwiyaKapito Si zachilendonso, nyimbo yomwe aliyense akuimba ndi kuzimazima kwa magetsi. Mmalo mopereka magetsi tsiku lililonse monga anenera, ayamba kupereka mdima tsiku lonse. Izi sizikukhumudwitsa anthu okha, nawo amabungwe akwiya nazo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kapito: Osasekerera zimenezi Monga akunenera mkulu wa bungwe loona ufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito, Escom isimba tsoka posakhalitsa. Escom imva nkhwangwa ili mmutu. Zafika pokwana ndipo tatopa ndi kulira. Uwu ndi mtopola ndipo zithera pa wina, watero Kapito. Kapito wati vuto ndi Amalawi chifukwa safuna kugwirizana zinthu zikafika povuta monga zilili pano. Tigwirane manja, tiyeni tionetse mkwiyo wathu ndipo awa a Escom adziwenso kuti takwiya. Si bwino kusekerera zotere, talankhula ndipo tatopa. Panopa tiyeni tichitepo kanthu, adatero Kapito. Naye mkulu woona mabungwe a mabizinesi angonoangono lotchedwa Small and Medium Enterprises Association (SMEA), James Chiutsi, akuti chuma cha dziko lino chikutsika chifukwa makampani ambiri sakugwira ntchito. Chiutsi wati Escom ikuyenera kupeza njira zina zothandizira anthu kusiyana nkumawanamiza nthawi zonse. Anzathu amapanga magetsi kuchokera kudzuwa komanso kumphepo. Ife tikudalira magetsi opukusidwa ndi mphamvu ya madzi, kodi nanga madziwo akadzaphwera ndiye kuti tidzakhalanso ndi magetsi? adadabwa Chiutsi. Panopa zinthu zaipa, makampani alowa pansi ndi pafupifupi theka. Ena atseka makampani awo chifukwa sangakwanitse kugwiritsira ntchito injini za magetsi (generator). A mabutchala nyama ikuonongeka, ometa ena asiya. Kodi dziko lingatukuke bwanji? Komanso muyembekezere kuti munthu yemweyo akuyenera kupereka ndalama ya lendi. Kodi aipeza kuti, adatero Chiutsi. Mkuluyu ndi Kapito apempha boma kuti lichitepo kanthu pa nkhaniyi kuti Amalawi aone kusintha pa nkhani ya kuthimathima kwa magetsi.
10
Mphekesera zizunza anthu ku Mangochi Zina ukamva, kamba anga mwala ndithu. Anthu a mboma la Mangochi sabata yapitayi adadzuka pakati pausiku, ena mbandakucha, nkuyamba kukupa phala pokhulupirira mphekesera zoti khanda longobadwa kumene laopseza kuti yemwe sachita zimenezo awona zakuda. Mfumu Makanjira ndi bwana mkubwa wa bomalo, Moses Mphepo, atsimikiza za nkhaniyo, koma ati sakukhulupira zoti mphepo yamkuntho yomwe yaononga nyumba, mizikiti ndi katundu mbomalo ikugwirizana ndi mphekeserazo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Makanjira: Anthu amwa phala Mfumu Makanjira ikuti munthu wina adaitchaila lamya usiku yofotokoza kuti khanda longobadwa kumene la mdziko la Mozambique lalosera kuti mboma la Mangochi mugwa mavuto aakulu ngati anthu sakupa ndi kudya phala. Nditatsiriza kulankhula pa lamyayo, ndinatuluka panja koma ndinadabwa kuona anthu ali pikitipikiti kukupa phala, ena akumwa. Anthu ena anafika kunyumba kwanga kukafunsa nzeru. Tsiku lotsatira chimphepo chachikulu chidaononga nyumba, mizikiti ndi katundu wambiri moti anthu ena akuti zikugwirizana ndi mawu akhanda lija, adatero Makanjira. Mphekeserazo zikuti khandalo, lomwe lidabadwira mdera Kumwembe mdziko la Mozambique, lidamwalira litangotsiriza kupereka uthengawo. Mussa Malekano ndi mmodzi mwa anthu omwe adakupa ndi kumwa phalalo. Ndinalandira foni yondichenjeza kuti ndiona zakuda ndikapanda kukupa ndi kudya phala ndi banja langa lonse. Mneneri wapolisi wa mbomalo, Rodrick Maida, adati ofesi yawo siigwiritsa ntchito zikhulupiriro pogwira ntchito, koma malamulo a dziko. Chimphepo adati mphepo yomwe yawononga katundu ndi mizikiti mbomalo siikugwirizana ndi mphekesera za khandalo. Ndalandira malipoti woti mphepo yaononga katundu, koma sindikukhulupirira kuti zikukhudzana ndi mphekesera za khandalo, adatero bwanamkubwalo.
15
HRDC Yati Sigonja Wolemba: Sylvester Kasitomu 4w" sizes="(max-width: 560px) 100vw, 560px" />Anatsogolera ziwonetserozi mu mzinda wa Lilongwe-Mtambo Bungwe lomwe likutsogolera ziwonetsero za bata zofuna kukakamiza wapampando wa Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Dr. Jane Ansah kuti atule pansi udindo wake posakhutira ndi momwe adayendetsera chisankho cha pa 21 May lati silisiya kuchita ziwonetsero kufikira zofuna zawo zitakwaniritsidwa. Poyankhulapo lachitatu mu mzinda wa Zomba, wapampando wa Bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) mchigawo chaku mmawa cha dziko lino a Madalitso Thoko Banda ati cholinga cha ziwonetserochi ndikufuna kuti DR. JANE ANSAH komanso ma Commissioner a bungwe la MEC atule pansi ma udindo awo. A BANDA adzudzulanso anthu ena omwe akumatumiza mauthenga oopseza anthu omwe akuchita zionetserowa kudzera pa ma phone awo ponena kuti awapha akapitilidza kutsogolera kuchita ziwonetserodzi kuti asiye mchitidwe otero chifukwa kuchita ziwonetsero ndi ufulu wa wina aliyense. Anthu ena ali ndi nkhalidwe loipa amene akumaopseza anthu omwe akuchita zionetserozi, ife ngakhale mutiopseze sitisiya kuchita mademostations mpaka chokhumba chathu chitachitika, anatero Banda. Malinga ndi malipoti zionetserozi ziptilira kuchitika lachinayi mpaka lachisanu mmizinda yonse ikulu ikulu mdziko muno.
11
Ntchentchefly zivuta ku Lilongwe Tsiku limenelo tidakhala pa Wenela ndipo Abiti Patuma adati tipite ku Lilongwe kumenetu ndalama zabooka malinga ndi ungano wa aphungu komanso malonda a fodya. Adati nditsagane nawo kumeneko. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tidaimatu pa Roundabout pa Kameza kuimitsa galimoto iyi ndi iyo. Nthawiyo nkuti Abiti Patuma atapita kukagula madzi koma atangobwera, galimoto zitatu zidatiimira. Anti, mukupita kwa Chingeni? Tiyeni, adatero mkulu mmodzi. Ayi ndithu, adayankha Abiti Patuma. Inetu wa ku Mwanza, mukupita kumeneko? Kwerani ulere anthu atatu, mzimayiyo akhale kutsogolo, adateronso mkulu wina wa galimoto yake yopuma. Abiti Patuma adapukusa mutu. Ndidagwira mchiuno, kuthodwa. Posakhalitsa padatulukira galimoto ina yofiira. Sindinaonepo galimoto yopuma ngati imeneyo. Tikukakhazikitsa galimotoyi ku Lilongwe. Ya madzi iyi. Mtidzi osanena. Tiyeni, adatero amene amayendetsayo. Ndani akadakana mayesero okwera galimotoyo? Abiti Patuma adakwera kutsogolo. Nkhani imodziimodzi zidali kuphulika. Ndikuchokera ku Nansadi ku Thyolo. Ndaona kuti kukumangidwa nyumba zina. Mudzi uja basi ukhala tauni, Blantyre kulenga, adatero mkuluyo, tikudutsa pa Zalewa. Apolisi adali mbweee! Koma palibe adaimika galimotoyo. Mwati ku Thyolo kukumangidwa nyumba zina? adafunsa Abiti Patuma. Sindinatero. Malo angopezeka kuti pamangidwenso manor ina. Mulimba? adafunsa mkuluyo. Abale anzanga, musandifunse kuti amatanthauzanji chifukwa sindikuyankhani. Nanga kwathu kwa Kanduku ziliko izi za ma manor? Mpumulo wa Noma nawo ulipo kale. Kodi simukudziwa iyi ndi penshoni? Ndani safuna zabwino kuukalamba? adafunsa mkulu uja. Adandipindanso. Tsono titafika ku Lilongwe, mkulu uja adati tizungulire. Ndisaname, tidazungulira monse adayenda anyamata aja asadaomberane kalelo. Mukuwadziwa. Aja adazungulira Lilongwe yonse akusakana, mikangano ya ziboliboli kufuna kusinthitsa ndalama kuzungulira malo onse omwera mpaka kukaomberana pachipata kulimbirana ndalama zobooka za Adona Hilida. Koma Adona Hilida ali kuti? Kodi nsalu ija ankapachikira paphewa akupachikabe? Nanga Richie, bambo wa kwawo akupita nawo konse ayenda muja ankachitira kalelo? Tidafika ku Nyumba ya Malamulo. Tidapeza anthu akupha tulo. Inde, adali atalumidwa ndi kashembe, ntchentchefly ija yotchedwa tsetse imene imayambitsa trypanosomiasis, nthenda yogonetsa. Tsono mkulu akupha tulo apayu, uyu Joliji, mwati akudzatenga fupa la Moya Pete? Nanga tulo take timeneti adzatithandiza? adanongona Abiti Patuma. Mwamuiwala kodi? Pajatu ankati aletsa zotsitsa mpweya pagulu, ndidatero. Tsono momwe mukumuonera iyeyo, akuchita emit ma gas ochuluka bwanji to bring environmental degradation or is it climate change? adafunsa Abiti Patuma. Adandipinda. Sindimagona ine. Ndimaphethira ine. Ine wanuwanu, amene ndidzatenge mpando wa Moya Pete sindimagona ine. Ndimaphethira ine. Mwana wanga ndi msangalatsi. mwamuiwala Izeki? Mwana wanga ankafuna kukhala ngati Izeki. Koma ineyo ndikufuna kudzakhala Moya Pete, musandiipitsire mbiri ndi za tulo, adalira munthu wamkulu. Abiti Patuma adamupatsa sand paper. Ati chibwano kaya chatani kaya.
4
Afisi Apha Mayi Woledzera ndi Mowa ku Ntcheu Afisi olusa apha ndi kuchotsa ziwalo za mayi wina wa kwa Doviko, mmudzi mwa Layiti mfumu yaikulu Mpando mboma la Ntcheu. Mmodzi mwa anthu a mderali a Elizara Cornelius Chiwaula auza Radio Maria Malawi kuti izi zachitika kucha kwa tsiku lamulungu pa 19 July 2020. Iwo ati mayiyu Elenita Zemberani analedzera kwambiri atamwa mowa zomwe zinamuchititsa kuti agone pansewu pomwe afisiwa anamupeza. Ndi zowonadi kuti a Elenita Zemberani apezekadi atagwidwa ndi fisi komanso atadyedwa ziwalo zina ndi zina pamene amachokera ku mowa. Zimenezi zachitika cha mma 3 koloko mbandakucha wa lero, anatero a Chiwaula. Padakalipano apolisi mbomalo ati akufufuzabe za nkhaniyi.
14
Mtunda ulipo pa zokambirana Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bakili Muluzi sali kutali kwenikweni ndi khumbo lake lofuna kukumana ndi atsogoleri a Human Right Defenders Coalition (HRDC) pa nkhani ya zionetsero koma atsogoleriwo ampatsa mtunda woti akwere izi zisadatheke. Mwa zina, Muluzi akuyenera kukambirana ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika, wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah, bungwe la Public Affairs Committee (PAC) ndi atsogoleri a zipani zina za ndale kuti adzakhale nawo pa zokambiranazo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akufuna mkumano: Muluzi Muluzi adalembera kalata atsogoleri a HRDC pa 19 August 2019 kuwapempha kuti akumane nkukambirana pa chikonzero cha HRDC chofuna kupanga chionetsero mzipata za dziko ndi mabwalo a ndenge kuyambira pa 26 mpaka 30 August. Msabata ikuthayi, iye adapempha kuti mkumanowo utakhalapo dzulo kapena lero lino zingathandize chifukwa zionetserozo zomwe zikuyembekezeka kuyamba Lolemba zikhala zisadachitike. Pofunira zabwino dziko lathu, ndikupempheni kuti bwanji tikumanenso nkukambirana nkhani ya zionetseroyi. Ndikuona ngati njira yabwino yothanirana ndi mavuto omwe ali mdziko lathuli nkukhala pansi, adatero Muluzi mkalatayo. Ndipo poyankha kudzeranso mkalata, bungwe la HRDC lati Muluzi adalephera kukwaniritsa pangano lake ndi bungwelo utatha mkumano woyamba omwe udachitika pa 23 July 2019. Choyamba mudatilonjeza kuti mukumana ndi Mutharika komanso Ansah ndipo mutiuza zomwe mukambirane naye pasadathe sabata imodzi koma mpaka pano sitidamve kanthu ndiye kukukhulupirirani kuvuta, yatero kalata ya HRDC. Kalatayo yapitiliza kuti mkumanowo kuti utheke, Ansah atule pansi udindo yekha kapena Mutharika yemwe adamusankha amuchotsepo ndipo izi zifalitsidwe kudzera mnyumba zofalitsa nkhani kuti anthu mdziko lonse adziwe. Malingana ndi momwe yalembedwera kalata ya HRDC, zikutanthauza kuti Muluzi akapanda kukwaniritsa zinthuzi, mkumano ndi HRDC walephereka. Koma katswiri pa ndale George Phiri wati iyi si ntchito yamasewera kwa Muluzi ndipo wati nzokaikitsa kuti akwanitsa kubweretsa mbali zonsezi pamodzi. HRDC yanena za nzeru chifukwa zokambirana zimayenera kukhala olimbanawo pomwepo, mkhalapakati pomwepo komanso ena okhudzidwa ndi wothandizira mkhalapakatiyo pomwepo koma sindikuona izi zikutheka, adatero Phiri. Kadaulo winanso yemwe amaphunzitsa za ndale ku Chancellor College, Mustafa Hussein, wagwirizana ndi milingo yomwe HRDC yapereka kwa Muluzi polingalira kuti adalephera kale poyamba. Poyamba HRDC idali ndi chiyembekezo choti Muluzi auza Amalawi zomwe adakambirana ndi Mutharika koma adasankha kusunga chinsinsi. Muluzi abweretse pamodzi Mutharika, Ansah ndi HRDC, adatero Hussein. n Nkhani yokwenza mtengo wa chimanga nd iyabwino, koma yadza nthawi yolakwika alimi ambiri atagulitsa kale chimanga chawo kwa mavenda. Awa ndi maganizo a alimi osiyanasiyana omwe adacheza ndi Tamvani patatha sabata imodzi unduna wa malimidwe utalengeza kuti mtengo omwe bungwe la Admarc lizigulira chimanga wasintha. Nduna ya zamalimidwe Kondwani Nankhumwa adalengeza Lachisanu kuti kuyambira sabata yatha, mtengo wa chimanga wakwera kuchoka pa K150 pa kilogalamu kufika pa K180 pa kilogalamu Admarc ikakagulira chimanga kumudzi ndipo K200 pa kilogalamu mlimi akapititsa yekha chimanga ku msika wa Admarc. Koma pocheza ndi Tamvani, alimi ena ati ngakhale nkhaniyo ili yabwino, palibe chomwe alimi angonoangono apindulepo chifukwa adagulitsa kale chimanga kwa mavenda pa mitengo yotsikirapo yomwe panthawiyo inkaoneka yabwino. Mmodzi mwa alimiwo, William Guza wa ku Waliranji mboma la Mchinji ndipo awa ndi madandaulo amene amakhalapo chaka chilichonse. Chaka ndi chaka timadandaula nkhani yomweyi kuti Admarc imachedwa kuyamba kugula chimanga ndipo ikamabwera mbwalo, mavenda amakhala atagula kale chimanga mmidzimu motola mapeto ake mavendawo ndiwo amakapindula pokagulitsa chimanga chomwecho ku Admarc, adatero iye. Moses Kawodzera mlimi wa ku Chisi mboma la Zomba naye wati Admarc ikadayamba kugula chimanga pa mtengo watsopanowu nthawi yabwino, iye akadapeza phindu lokwana kawiri lomwe adapeza chifukwa chogulitsa kwa mavenda. Panthawiyo, mavenda adayamba kugula chimanga pa mitengo ya pakati pa K70 ndi K100 pa kilogalamu pomwe boma lidali lisadayambe kugula chimanga, adatero Kawodzera. Izi zikutanthauza kuti alimi omwe adagulitsa chimanga chawo moyambirira, adaluza ndalama zokwana K100 kapena K120 pa kilogalamu iliyonse yomwe adagulitsa kwa venda. Apa ndiye kuti mlimi yemwe adagulitsa matumba 20 a makilogalamu 50 lililonse pa mtengo wa K80 pa kilogalamu, adagulitsa makilogalamu okwana 1 000 nkupeza K80000 koma akadagulitsa chimangacho ku Admarc panopo pa K200 pa kilogalamu akadapeza K200 000. Katswiri pa za malimidwe Tamani Nkhono Mvula adati iyi ndi nkhani yomvetsa chisoni chifukwa venda ndiye amapeza phindu lomwe mlimiyo akadapeza ndipo mlimiyo amangokhala pamodzimodzi osasuntha. Ichi nchifukwa chomwe ndimanenera kuti Admarc imayenera kukhala ndi ndalama ukamafika mwezi wa March kuti alimi akangoyamba kukolola, izitsegula misika yake. Izi zikhoza kuthandiza kuti mavenda atsatire mitengo ya boma pofuna kulimbirana chimanga ndi Admarc, adatero Mvula. Maganizo a Mvula akugwirizana ndi lipoti ya bungwe la Civil Society Agriculture Network (Cisanet) lomwe lidati ndale za msika wachimanga zimapweteka alimi angonoangono nkumatukula mavenda. Mavenda amabwera nkudzagula chimanga chifukwa Admarc ikuchedwa koma alimi akufuna ndalama msanga. Admarc ikamayamba kugula chimanga pa mtengo ikwera, chimanga chimakhala ndi mavenda omwe amapindula. Nkhanza siyithera pomwepa, njala ikayamba, alimi omwe aja amadzagula chimanga ku Admarc mokwera chifukwa Admarc idagula kwa mavenda mokwera ndiye nayo ikufuna ipezepo phindu pangono pokha, likutero lipoti la Cisanet. Izi zikugwirizana kwatunthu ndi momwe zakhalira chaka chino chifukwa alimi adagulitsa chimanga pa mtengo wa K80 pa kilogalamu kwa venda yemwe akukagulitsa pa mtengo wa K200 pa kilogalamu ku Admarc ndipo mlimi yemweyo adzayenera kugula chimangacho ku Admarc pa mtengo osachepera K200 pa kilogalamu. Pano mtengo wachimanga wayamba kale kukwera mosalingalira za mavuto a zachuma moti mmadera ambiri thumba la makilogalamu 50 lili pa K12 000 koma mmadera ena monga ku Chikwawa lafika pa K14 400 pomwe ku Machinga ena akugulitsa pa K18, 000. Mkulu wa bungwe la Cisanet Pamela Kuwali wati boma lachita bwino kukwenza mtengo wa chimanga koma lionetsetse kuti pali chilungamo pa kagulidwe kake kuti alimi angonoangono apindule nawo.
15
Bungwe la St. Vincent Lathandiza Odwala ku Queens Bungwe la zachifundo mu mpingo wa katolika la Society of Saint Vincent De Paul lapempha akhrisitu akatolika mdziko muno kuti athandize anzawo osowa mu nyengo ino ya Lenti. Mkulu wa bungweli a Charles Kimu anena izi mu mzinda wa Blantyre pamene bungweli limapeleka katundu osiyanasiyana pa chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth. Iwo apempha magulu osiyanasiyana mu mpingowu kuti azikumbukira Anthu omwe ali mmavuto komanso matenda powathandiza ndi zomwe ali nazo ngati njira imodzi yoonetsa ntchito za chifundo zomwe zimalimbikitsidwa mu nyengo ino ya lent. Bungwe lathu ndi lazachifundo nde tinachiona cha nzeru kuti tibwere kuno kuchipatala kuti tizagawabne ndi anzathu zochepa zomwe tiri nazo munye ngo ino ya lent yomwe timalimbikitsiidwa kuchita izi, anatero a Kimu. Naye mkulu wachinyamata ku bungweli a Vincent Ndawu analimbikitsa achinyamata omwe akulipilidwa sukulu ndi bungweli kuti azitengerapo chitsanzo pakayendetsedwe ka bungweli kuti nawo azakhale atsogoleri abwino abungweli pano ndi mtsogolo.
14
Chilima Wati Akuluakulu a Nthambi Zomwe Zachedwa Kupereka Malipoti Alandire Chilango Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Saulos Chilima wati akuluakulu a nthambi za boma zomwe zakanika kupereka malipoti a ntchito zawo kufikira pa 17 July chaka chino, akuyenera apatsidwe chilango. Chilima yemwenso ndi nduna yowona za chitukuko cha dziko komanso kagwiridwe ntchito ka nthambi za boma, pa 7 ndi pa 9 July anakumana ndi akuluakulu a nthambi za boma mchigawo chapakati komanso chakumwera komwe anawauza kuti pasanafike pa 17 July, akhale atapereka malipoti a momwe agwilira ntchito zawo. Walamula kuti akuluakulu a nthambi alandire chilango Kudzera mu kalata yomwe mneneri wa wachiwiri kwa mtsogoleriyu Pilirani Phiri walemba, mwa nthambi 66 zomwe zimayenera kupereka malipoti awo, 56 ndi zomwe zinapereka malipotiwo mu nthawi yake pomwe 9 zapereka mochedwa ndipo nthambi imodzi yomwe ndi ya Malawi Institute of Management (MIM) siyinaperekebe. Polankhula ndi Radio Maria Malawi wofalitsa nkhani ku nthambi ya kagwiridwe ntchito ka nthambi za boma a Mccarthy Mwalwimba ati wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu ndi wokhumudwa ndi khalidwe lomwe akuluakulu a nthambi khumi-zi awonetsa ndipo walamula kuti akuluakuluwa alandire chilango. Kalatayi ndi yoona yachokeradi ku ofesi ya Vice President ndipo padakali pano nthambi zomwe zalephera kupereka malipotiwa zapemphedwa kudzudzulidwa ndi akuluakulu kuchokera ku nthambi zimenezi, anatero Mwalwimba. Iwo ati padakali pano chilangochi sichinaziwike ndipo zitengera kuti mkulu oyenganira mabungweyu awadzuzula motani.
11
2019 ikudetsa nkhawa Chikhulupiliro chapita. Amalawi 28 mwa 100 aliwonse akuti akuona chisankho chopanda mtendere ndi chilungamo chaka cha mawa. Izi zadziwika potsatira kafukufuku wa nthambi yofufuza za maganizo a anthu pankhani zosiyanasiyana ya Institute of Public Opinion and Research (Ipor). Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kafukufukuyo yemwe adayendetsa ndi akadaulo pa kayendetsedwe ka boma ndi ndale wasonyeza kuti Amalawi ali ndi nkhawa kaamba ka zina mwa zomwe zikuchitika mdziko muno pokonzekera chisankhochi. Anthu omwe ataya chikhulupilirowa akuti nkhani za zipolowe, mphekesera zodzabera chisankho, malingaliro okondera ku bungwe la MEC ndi kusayenda bwino kwa zisankho za mmbuyomu ndizo zifukwa, latero lipoti la kafukufukuyu. Koma pomwe chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) chadzudzula kutsogoza maganizo otere, zipani zotsutsa zati maganizo a anthuwo ali ndi tanthauzo. Zisankho za mmayiko a mu Africa zimasokonekera chifukwa cha mchitidwe wotsogoza kutaya chikhulupiliro mmalo momasakasaka njira zokonzera zinthu, adatelo mneneri wa DPP Nicholas Dausi. Iye adati chofunika nchoti anthu angokhulupilira kuti chisankho chidzayenda bwino basi kuti pasadzakhale kukokanakokana pa zotsatira zachisankhocho. Mneneri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) Maurice Munthali adati nkhawa yachisankho chopanda chilungamo ndi mtendere zidabwera Nyumba ya Malamulo itangokana kusintha malamulo oyendetsera chisankho. Kusintha malamulo kuja lidali ganizo la nthambi zosiyanasiyana zomwe zidali zitaona kufooka kwa malamulo oyendetsera chisankho ndiye nkhaniyi itangokanidwa, anthu adataya chikhulupiliro pompaja, adatelo Munthali. Iye adati zipani zandale nazo zikuonjeza kunyogodolana pamisonkhano ndi kuchulutsa mawu odzetsa mkwiyo ndi kuyambitsa ziwawa. Tikapanda kusintha khalidwe lonyoza ndi kulankhula zodzetsa mkwiyo ndi kuyambitsa phokoso pa misonkhano yathu, tiyembekezere ulendo owawa wa ku chisankho, adatelo Munthali. Mneneri wa United Transformation Movement (UTM) Joseph Chidanti Malunga adati akugwirizana kwa thunthu ndi anthu omwe akuwona mdimawa potengera zomwe zikuchitika mdziko muno. Taona kangapo konse pakuchitika zofuna kulepheretsa anthu kubwela ku misonkhano yathu, apa akulimbana nafe kuti tisalembetse chipani komanso mukumbuka kuti adatiwotchera galimoto ku msonkhano wa ku Mangochi. Zonsezi anthu amaona, adatero Malunga. Kafukufukuyo, yemwe adachitika mmiyezi ya August ndi September 2018, akusonyeza kuti DPP yomwe ili ndi oyitsatira ambiri kumwera ili ndi danga lalikulu lodzapambana chisankho. Lipotilo lasonyezaso kuti MCP ikubwela pachiwiri ndipo mphamvu zake zadzadzana pa chigawo cha pakati kutsatidwa ndi UTM yomwe mphamvu zawoneka ku mpoto. MCP kudzera mwa mneneli wake Munthali yatsutsa zoti iyo ili ndi mphamvu mchigawo chapakati chokha ponena kuti chipanichi chidazika mizu mzigawo zina za dziko lino. Sitikudelera omwe adapanga kafukufukuyu koma patokha tikuwona kuti talanda malo mzigawo zina. Chitsanzo ndi zotsatira za chisankho chachibwereza cha 2017, adatero Munthali. Chipani cha MCP chatchulidwa kuti ndicho anthu ambiri ali nacho chikhulupiliro choti chitha kudzakonza zinthu zomwe zidaonongeka pa kayendetsedwe ka dziko. Iye adati DPP ndi yolimbikitsidwa ndi zotsatira za kafukufukuyo ndipo yati ilimbikira kukonza zofowoka zomwe kafukufukuyo wayipeza nazo. Zipani ziwirizi zagwirizana maganizo kuti UTM yangogweramo mbwalo kaamba koti kafukufukuyo adachitika nthawi yomwe gululi limakhazikitsidwa kumene ndiye lidali nchikoka. Malunga adati UTM nchiwopsezo chachikulu ku zipani za DPP ndi MCP ndipo adati zotsatira za kafukufukuyo zatsimikiza mphamvu ndi kuwopsa kwa UTM.
2