diff --git "a/test.csv" "b/test.csv" new file mode 100644--- /dev/null +++ "b/test.csv" @@ -0,0 +1,2295 @@ +Text,labels +"CCJP Ikufuna DPP Ipereke Mwambo kwa ma Cadet Wolemba: Thokozani Chapola content/uploads/2019/09/CHIBWANA.jpg"" alt="""" width=""400"" height=""344"" />Wasayinira chikalatacho-Chibwana Bungwe la chilungamo ndi mtendere mu mpingo wa katolika la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) lapempha chipani cholamula cha DPP kuti chipereke mwambo kwa achinyamata ake ochitsatira kuti apewe kuyambitsa zipolowe mdziko muno. +Malinga ndi chikalata chomwwe bungweli latulutsa chomwe chasaindidwa ndi mkulu wa bungweli Boniface Chibwana, kuchita ziwonetsero ndi ufulu wa munthu wina aliyense choncho mlangizi wa boma pa za malamulo, chipani kapena apolisi alibe udindo woletsa anthu kuchita ziwonetsero. +Chikalatachi chadza patangodutsa tsiku limodzi pamene anthu ena otsatira chipani cha DPP anasokonzeza ziwonetsero zomwe a bungwe la HRDC amatsogolera mu mzinda wa Blantyre. +CCJP yapempha nthambi za chitetezo mdziko muno kuti zipereke chitetezo chokwanira kwa anthu amene akuchita ziwonetsero za bata ndipo apempha mtsogoleri wa dziko lino komanso komiti ya nyumba ya malamulo yokhudziwa ndi nkhaniyi kuti ichitepo kanthu ndi kuthetsa mavuto amene alipo mdziko muno pa nkhani za ndale. +Tikufuna a President achitepo kanthu pa nkhaniyi kuti zinthu ziyende bwino. Apolisi komanso asilikali ateteze anthu ochita ziwonetsero kaamba koti ndi ufulu wawo kutero ndipo palibe amene ali ndi mphamvu yoletsa ziwonetsero, anatero a Chibwana. +Komabe iwo alangiza anthu omwe akuchita ziwonetsero kuti achite izi mwa bata ndi mtendere posawononga chuma cha boma komanso katundu wa anthu osalakwa. +",11 +" Mundibwezere voti yanga, amalawi athafulira APM pazionetsero Amalawi athera Chichewa mtsogoleri wa dziko lino komanso nduna zake pa zionetsero zomwe zidachitika Lachisau. + Zionetserozo zidatsogoleredwa ndi amipingo, amabungwe komanso azipani amene amakakamiza boma kuti liyankhepo pa mavuto amene dziko lino likudutsamo. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mwa zina ndi kuuza mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti athothe nduna ya zachuma Goodall Gondwe komanso ya maboma angono Kondwani Nankhumwa pokhudzidwa ndi nkhani ya K4 biliyoni yomwe imagawidwa kwa aphungu 83 zisadasinthe kuti ziperekedwa kwa aphungu onse. + Amabungwewa akuda kukhosi ndi boma pankhani ya kuzimazima kwa magetsi chikhalirecho boma lidagula majeneleta kuti athane ndi kuzimazima kwa magetsiwo. + Patsikulo, mizinda ya Blantyre, Lilongwe, Zomba ndi Mzuzu komanso maboma monga Rumphi kudawirira pamene anthu adayenda kukapereka madandaulo awo kwa akuluakulu a boma. + Mwa zina, anthu adagwiritsa ntchito nyimbo popereka uthenga ku boma. Mwa nyimbo zina ndi monga: Tichotse nkhalamba ndi mtima umodzi. Bewubewula Peter, bewula Chaponda, bewula Goodall. Mukamva hi! Ho! agogo athawa, Mmanja mwako mlamu tachokamo, undibwezere mavoti anga mlamu mwazina. Ku Mzuzu, nyimbo idazunguza idali yolimbana ndi nduna zomwe zatopa ndi ukalamba mboma. + Mukutani mboma, pitani muzikacheza ndi adzukulu kumudzi, idatero. + Kupatula nyimbo, anthuwo adagwiritsiranso ntchito zikwangwani zomwe mudalembedwa mauthenga osiyanasiyana. + Mwa mauthengawo adali monga; Ngolongoliwa, Kyungu, Lukwa ndi Lundu si mafumu koma ogwira ntchito a chipani cha DPP. + Uthenga wina udalunga ku wailesi ya boma ya MBC. Sumbuleta ndi Phillip Business, MBC si nyumba ya abambo anu. + Uthenga wina umanena Gondwe: Adada Goodall taweya mwachekula, lutani kukaya mukachezgenge nawazukulu [bambo Goodall mwakula, pitani kumudzi mudzikacheza ndi zidzukulu]. + Zina zimafunsa nkhani ya K4 biliyoni. Kulubwalubwa ndi K4 biliyoni yathu? Mmodzi mwa akuluakulu amabungwe amene amatsogolera zionetserozi Gift Trapence wa bungwe la Centre for the Development of people (Cedep) adati zionetserozo zidachitika bwino. + Ganizo lathu lakwaniritsidwa, tapereza madandaulo athu ku boma ndipo tikuwapatsa masiku 30 kuti atiyankhe ndipo akalephera kupitanso ku msewu, adatero Trapence. +",11 +"Bungwe la Save the Children Lati Lidzipereka Poteteza Ana ku Coronavirus Bungwe la Save the Children lati lidzipereka pothandiza boma pa ntchito yoteteza ana ku mliri wa Coronavirus. +Mkulu wa bungweli mchigawo chakummwera a Thoko Bemu ndi omwe anena izi pamene bungweli limapereka zipangizo zosiyanasiyana zomwe zizithandizira ogwira ntchito pa chipatala cha Ntcheu polimbana ndi mliri wa COVID-19. +Iwo ati ana ndi omwe amakhudzidwa kwambiri panthawi yomwe kwadza ngozi zadzidzidzi. +Pakachitika ngozi zadzidzidzi ana ndi omwe amachitidwa nkhaza, kusowa chakudya komanso chithandizo nde ife tikugwira ntchito imeneyi ya Child Protection mothandizana ndi boma, anatero a Bemu. +Mwazina bungweli likuyembekezera kuthandiza maboma asanu ndi imodzi a kummwera kwa dziko lino. +",6 +" Mamonitala ena sakupezeka kolembetsa Mamonita a zipani zina sakupezeka mmalo olembetsera mavoti, Tamvani wafukula. + Mmalo 7 a mmidzi yomwe Tamvani adazungulira mkati mwa sabatayi, malo amodzi okha a Kasambwe kwa T/A Kabudula ndiko kudapezeka monitala wa chipani cha Peoples Party (PP) koma mmalo ena onse mmangopezeka a zipani za Malawi Congress (MCP) ndi Democratic Progressive (DPP) basi. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ansah: Tidauza zipani Nkhaniyi yakhumudwitsa bungwe loyanganira zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lomwe lati mchitidwe otere ndiwo umayambitsa kusakhutira ndi zotsatira za chisankho. + Mkulu wa MEC, Jane Ansah adati: Tidapempha zipani zonse kuti zitumize mamonitala mmalo olembetsera kuti aziona momwe zinthu zikuyendera nkupereka malipoti ku zipani zawo koma takhumudwa kuti zipani zina zilibe ma monitala, Watero mkulu wa MEC Jane Ansah. + Malingana ndi bungwe lowona za momwe ndondomeko ya zisankho ikuyendera la Malawi Electoral Support Network (Mesn), monitala ndi diso komanso khutu la chipani kapena bungwe lokhudzidwa pachisankho. + Mkulu wa bungwelo Steve Duwa adati monitala amayenera kukhala pamalo wolembetsera, kuvotera kapena kuwerengera zisankho ngati mboni ya chipani kapena bungwe lake ndipo amayenera kusayinira zotsatira pamapeto. + Nkofunika kwambiri kuti chipani chikhale ndi monitala pa kalembera, chisankho kapena kuwerenga zotsatira ndipo amayenera kusayinira pamapeto pake akakhutira kapena kukana ngati ali ndi umboni woti pena pake sipadayende bwino, adatero Duwa. + Zipani zina zomwe zimayembekezeka kukhala ndi mamonitala ake mmalo olembetsera ndi United Democratic Front (UDF), Alliance For Democracy (Aford) ndi United Transformation Movement (UTM). + Mneneri wa UTM, Joseph Chidanti Malunga adati msabatayi adaali kuthamanga zolembetsa gululo ngati chipani choncho sanatumize mamonitala. + Malamulo amalola chipani chomwe chidalembetsa ndipo nchodziwika kutenga nawo mbali, ife tidali tisadamalize mbali yolembetsayo koma mtsogolomu tizikhala nawo paliponse, adatero Malunga. + Mneneri wa UDF Ken Ndanga adati asankhabe mamonitala mtsogolomu. Iye adati zimavuta kuika mamonitala mpaka pamene chipani chawo chidachititsa msonkhano wake waukulu. + Malinga ndi wofalitsa nkhani za PP, Noah Chimpeni, chipanicho chili ndi chikhulupiriro kuti mamonitala a mabungwe omwe siaboma agwira ntchito yoyenera. +",11 +" ANATCHEZERA Wamkulu ndine Zikomo agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi chibwenzi koma timasiyana ndi chaka chimodzi, wamkulu ndineyo. Kodi tingathe kukwatirana? Iyeyu akufunitsitsa atandikwatira chifukwa amandikonda kwambiri ndipo inenso ndimamukoinda zedi. + CM Lilongwe Wokondeka CM, Zikomo pondilembera. Kusiyana zaka chisakhale chopinga kuti mukwatirane, bola chikondi ndi kulemekezana. Si chifukwa mkazi kukhala wamkulu pakubadwa bola chikondi. Chimene chimavuta nthawi zina ndi kudererana mbanja, kapena kusapatsana ulemu. Pali akazi ena amene salemekeza amuna awo ati poti iwowo ndiwo ndi aakulu pobadwa, koma pachikhalidwe chathu mkazi ayenera kulemekeza mwamuna wake ngakhale akhale wochepa msinthu ndi zaka zobadwa. Chimodzimodzi mwamuna akakhala wamkulu pobadwa naye ayenera kulemekeza banja lake, osatenga mkazi wake ngati mwana chifukwa choti ndi wa zaka zocheperako kuposa iye. Mbanja laulemu mudza mwamuka akuti awa ndi akazi anga ndipo mkazi naye amati awa ndi amuna anga osati uyu ndi mkazi wanga kapena uyu ndi mwamuna wanga pagulu. Tsono ngakhale wamkulu ndiwe pobadwa umulole mwamunayo kuti mukhale thupi limodzi ngatidi pali chikondi chenicheni pakati panu. + Akukana woyera Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 23 ndipo ndapeza mwamuna ndipo iye akuti akufuna ndimuberekere mwana koma akuti tisamange ukwati woyera. Komanso ndamva kuti anakaonetsa kale mkazi kwawo. Koma kunena zoona mwamunayu ndamukonda , nditani pamenepa? LL, Area 1, Lilongwe Wokondeka LL, Apa ndiye ukufuna ndikuuze chiyani, mwana wanga? Ukufunsa chinyezi mbafa, nanga ndinene kuti chiyani? Apa zikuonekeratu kuti mwamunayu alibe chidwi choti mukwatirane koma akuti akufuna mwana, mwana wachiyani? Ungomuberekera mwana basi, mwanayo azikachita naye chiyani ngati simukhala limodzi? Iwe mwana ulibe naye ntchito? Zachibwana basi! Ndiye ukuti umamukonda mwamunayu, chikondi chako chili pati poti iye wachita kunena yekha kuti sakufuna ukwati ndi iwe koma zogonana basi, ndipo wanena wekha kuti adakaonetsa kale mkazi wina kwawo, ndiwe iwe ukufunsa kuti utani pamenepa? Umusiye basi, upeza wina wofuna banja osati zamasanje zomwe akunena mwamunayo ayi. Kulera mwana si ntchito yapafupi, imafunika banja lachikondi ndi logwirizana. Ndiye ngati iyeyo za banja ali nazo kutali ndi iwe, chotayira ntchawi yako ndi iyeyo nchiyani? A Gama abwerere Ine ndine Mrs Jean Makolosi. Amuna anga adachoka chaka chatha kupita ku Mzuzu komwe ndamva kuti akwatira mkazi wina. Ndikufuna mwamuna wanga abwereko mwamnsanga popeza sitinayambane. Mwamuna wanga ndimamukonda, abwere mwezi uno usanathe chonde. Dzina lawo ndi a Paul makolosi Gama. +",12 +" Kuyezetsa magazi kwayenda bwino Mlembi wamkulu mu Unduna wa Zaumoyo wati sabata yolimbikitsa kuyezetsa magazi pofuna kudziwa ngati uli ndi kachilombo koyambitsa Edzi idali yapamwamba popeza anthu ochuluka adakayezetsa magazi. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkuluyu, Dr Charles Mwansambo wati ngakhale sabatayi yatha dzulo, anthu apitirize kuyezetsa kuti adziwe momwe mthupi mwawo mulili ndikukonza tsogolo lawo. + Iye adati mutu wa ntchitoyi chaka chino udali Kayezetseni lero kuti mukonze tsogolo lanu ndipo undunawo udachalira kufikira anthu 250 000. + Ntchitoyo idayamba pa 6 mwezi uno ndipo mwambo wokhazikitsa sabatayi udali mboma la Mangochi. + Mwansambo adati chaka chino maso adali mwapadera pa omwe ali pa ubwenzi komanso mbanja. + Aliyense akayezetse Iye adati wodziwa momwe mthupi mwake muliri amachita chisankho chabwino cha ubwenzi komanso ndondomeko monga ukwati. + Ngakhalebe tikutero, sikuti taika malire; aliyense, kaya ndi mwana wa zaka 13, akhoza kuyezetsa. Apa makolo tikuwapempha atithandize kuti ana azidziwa momwe mthupi mwawo muliri, adatero Mwansambo. + Ku Mulanje kwa Gulupu Chisinkha mdera la T/A Mabuka, ntchitoyi yayenda mophangirana. + Gulupu Chisinkha, yemwe timalankhula naye Lachiwiri akuyezetsa magazi, adati anthu a mmudzi mwake sadachite kukakamizidwa kuti akayezetse. + Adatumiza zipangizo zokwana 2 000 koma ndikunena pano zatsala zochepa koma anthu ndiye akubwerabe, adatero Chisinkha. + Iye adati mmudzi mwake adakhazikitsa lamulo lothana ndikusalana kotero aliyense amakhala womasuka kukaona momwe mthupi muliri. + Kusalana ndi mlandu ndipo wolakwa ndimamukokera kubwalo, adatero Chisinkha. + Koma ku madera ena, ntchitoyi idali yovutirapo. + Gulupu Njobvuyalema ya kwa T/A Ngabu mboma la Chikhwawa yati pofika Lachiwiri pa 7 achipatala adali asadafike. + Chonsecho ati nkuti achipatala atauza anthu kumeneko kuti ntchitoyo idzagwirika pa 6 ndi pa 7, zomwe sizidachitike. + Tadikirira, koma zosathandiza. Tidakonzekera chifukwa chipatala chili pamtunda wa pafupifupi makilomita 30. + Anthu adachoka kutali monga Kalogamudzi womaliza pakati pa Mozambique ndi Malawikoma angobwerera, adatero gulupuyu yemwe mudzi wake uli ndi anthu 3 000. + Ena zidavuta Mwansambo adati alankhula ndi mkulu wa chipatala cha Ngabu kuti amve chomwe chidachitika kuti anthu a kwa Njobvuyalema asalandire thandizo panthawi yake. + Mwansambo wati mwa zina ntchitoyi yayenda bwino popeza kusalana kwachepa. + Iye wati poyamba anthu ankaopa kukayezetsa poopa kuti anzawo adziwasala akapezeka ndi kachilombo koyambitsa Edzi, zomwe ati pano sinkhaninso chifukwa anthu asintha maganizidwe. + Ndidali ku Mangochi komwe anthu adamasuka kulankhula za momwe mthupi mwawo muliri; ichi nchitsimikizo kuti kusalana mdziko muno kwachepa, adatero Mwansambo. + Ntchito zokhudza matenda a Edzi posachedwapa zazunguliridwa ndi manongongo, ena mwa iwo nkumati boma lisintha mankhwala otalikitsa moyo a ARV. + Koma Mwansambo adati angoonjezera zingapo zothandiza kuthana ndi mavuto omwe ena amakumana nawo akayamba kumwa mankhwalawa mmbuyomu. + Iye adati munthu ukamwetsa ma ARV pamakhala mavuto monga kutupa mitsempha komanso ena amadandaula kuti akukula kumtunda. + Iye adati zophatikizira zatsopanozo zithana ndi zovuta monga izi. + Pankhani ya thumba lomwe kumachokera ndalama zothandizira ntchitoyi, Mwansambo adatsutsa malipoti oti thandizolo likutha. + Iye adati padali zina zomwe eni thumbalo adafunitsitsa kuti zifotokozedwe bwino ndipo zonse zidatheka. + Iye adati pano thumbali likuthandiziranso kulimbana ndi matenda a chifuwa chachikulu (TB) komanso malungo. + Mchaka cha 2008, sabata yoyezetsa magazi idachailira anthu 250 000 koma mneneri wa Unduna wa Zaumoyo, Henry Chimbali, adati chiwerengerochi sichidakwanitsidwe. + Kuchokeranso chaka ichi, ntchitoyi sidagwirike ndipo mmalo mwake boma ati limaunguza zofooka kuti zikonzedwe. + Posachedwapa, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Khumbo Kachali, adati anthu 50 000 mdziko muno amatenga kachirombo ka HIV pachaka. + Kachali adanena izi ku Namitete mboma la Lilongwe pamwambo wokumbukira omwe adatsikira kuli chete kaamba ka matenda a Edzi. + Uko mkulu wa bungwe la UNAIDS mdziko muno, Patrick Brenny adati dziko lino lachita bwino pankhani za kadyedwe koyenera, kuthandiza omwe ali ndi kachiromo ka HIV kudzipereza podalira pachuma, kuteteza ana kupatsiridwa kachirombo ka HIV pobadwa komanso kuthandiza omwe ali ndi kachiromboka kupeza mankhwala otalikitsa moyo a ARV. + Malinga ndi Chimbali, anthu pafupifupi 380 000 akulandira mankhwala otalikitsa moyo pomwe pafupifupi 1 miliyoni ndiwo akudwala matendawa. +",6 +" Chikondi chidayambira kutchalichi Mipingo ina ponyadira chipembedzo chawo imati kupemphera ndi kwabwino kwatidziwitsa awa, awo ndi awo. Kukumana kwa mtundu womwewu kudasintha moyo ndi tsogolo la Elisha Mtambo ndi Menala Msiska womwe lero ndi banja. + Elisha yemwe amachokera mdera kwa mfumu Mwenelupembe mboma la Chitipa akuti adakumana ndi Menala wochokera mdera la mfumu Kachulu mboma la Rumphi mchaka cha 2015 kutchalitchi ya CCAP ya Sinodi ya Livingstonia ku Area 24 mu mzinda Lilongwe. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Elisha ndi Menela paukwati wawo Iye adati kupatula kukumana koyamba kutchalitchi, amakhulupilira kuti Mulungu ndiye adawalumikizitsa chifukwa atangowonana mitima yawo idadumpha mwachilendo pambuyo pake, adalonjerana nkupatsana nambala za lamya pompo. + Ambiri amadziwa kuti sichophweka kukumana ndi msungwana kapena mnyamata koyamba nkulankhulana naye pomwepo mpaka kupatsana nambala za lamya koma ndimo zidakhalira ndiye sindichotsera kuti dzanja la Atate lidayendapo, adatero Elisha. + Naye Menala wati tsiku lomwe adakumana ndi Elisha kutchalitchi, adamva kugunda kwachilendo mumtima mwake koma pokhala msungwana adayesetsa kugwira thupi lake kuti asawonekere kuti adali kumva mwachilendo mthupi. + Munthu aliyense amazidziwa momwe amakhalira kapena kumvera nthawi zonse mthupi mwake koma patsikuli, ndithu ndidamva mwachilendo makamaka momwe mtima wanga umagundira, watero Menala. + Elisha wati kuchoka tsiku lokumanalo, awiriwa adakhala miyezi itatu akungocheza palamya kudikira tsiku lomwe onse adakhutira wina ndi mnzake. + Tsiku lomwe ndidamufunsira, adaseka nkundifunsa kuti ndidaganiza bwanji potenga nthawi yonseyo. Chilungamo chidali chakuti ndinkafufuza kaye za khalidwe lake, adatero Elisha. + Iye wati atapereka yankho lakelo, adadzidzimuka Menala naye atamuuza kuti adagwa mchikondi kalekale tsiku la kukumana kwawo koma sadafune kuonetsera ndipo pamiyezi itatu yomwe amangochezayo, nayenso amafufuza mbiri ya Elisha. + Ngakhale onse adali atamasukirana, Menala sadavomere kutomera kwa Elisha ndipo adamuuza kuti adzamuyankhabe akamaliza kulingalira za mawuwo. + Ndidavomera maganizo akewo koma eeeeh! adandiyika mundende ya malingaliro usiku ndi usana. + Adandilora pakutha pa mwezi wachiwiri, pemene ine ndinkati zanga zada, Elisha adafotokoza. + Chibwenzi chitayamba mu 2015, akuti awiriwa adagwirizana zoti adzamanga ukwati mchaka cha 2018 ndipo chibwenzicho chidayenda bwino kwa zaka zitatu zomwe amakonzekera ukwati wawo omwe adamanga pa 7 July 2018 patchalitchi yomwe adakumanirayo. +",13 +" Takonzeka kuvotaAmalawi Pamene kwangotsala masiku awiri kuti Amalawi 6.8 miliyoni aponye voti yosankha mtsogoleri wa dziko lino, Amalawi ena asonyeza chidwi kuti akonzeka kukavota Lachiwiri. + Tamvani idazungulira kuona momwe anthu akukonzekera ndipo ena aonetsa kuti Lachiwiri adzakhala pikitipikiti kukaponya voti. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Apapa ngakhale atasintha kuti votiyo ikhale lero, ndipita kukavota ndipo sindikulira wina kupanga kampeni paine chifukwa chisankho ndidapanga kale, adatero MacDonald Kalimba wa ku Mchinji. + Joel Ngoma wa ku Mzimba adati: Chomwe ndimadikira ine nchoti tidzavota liti ndiye poti tsiku likudziwika, ndikungondikira mmawa wa Lachiwiri basi kukavota. + Amayi nawo ati akonzeka kukaponya voti Lachiwiri kuti dziko la Malawi likhale ndi mtsogoleri wovomerezeka. + Tonse tikudziwa kuti zinthu zambiri zidaima chifukwa cha ndalezi ndiye mpofunika kuti Lachiwiri lifike msanga kuti mtsogoleri adziwike tiyambe kusuntha chitsogolo, adatero Shupekile Mlotha wa ku Karonga. + Pomwe Patuma Usumani wa ku Phalombe adati: Tidavota koma pazifukwa zina akuti tikavotenso ndiye likafika tsikulo tikavota kuti tikhazikike. Izi zokokanakokana sizitithandiza. + Nalo bungwe lophunzitsa anthu la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust lati lazungulira dziko lonse kuphunzitsa anthu zakavotedwe ndipo likukhulupilira kuti anthu akavota mwaunyinji. + Mneneri wabungwelo Grace Hara wati bungwelo lidamwaza mauthenga mnjira zosiyanasiyana kuti Amalawi ngakhale akumudzi kwambiri amve za chisankho cha mkujachi. + Ulendo uno, ndi bungwe lathu lokha lomwe lidali kalikiliki kuphunzitsa ndi kumema anthu zachisankhochi kupatula zipani zomwe zomamemanso anthu. Chokondweretsa nchoti anthu akuonetsa kuti alandira uthenga mokwanira, adarero Hara. + Kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu mdziko Vincent Kondowe wati chisankho ndi chimenecho koma chofunika ndi umunthu kuti zinthu zidzayende bwino. + Iye wati munthu aliyense akuyenera kuzindikira kuti ufulu wake wokaponya voti ndi ufulu wa anthu enanso choncho ndi bwino kuti aliyense Lachiwirilo akaponye voti yake akathana nazo nkumapita kwawo kukadikira zotsatira. + Amalawi apite mwaunyinji kukavota chifukwa voti yawo ndi tsogolo lawo ndi la ana awo koma aliyense adzatsogoze umunthu osati kudzikonda ayi. Timanena nthawi zonse kuti dzikoli ndi lathu ndipo olichengetera ndife tomwe, adatero Kondowe. + Kadaulo pandale George Phiri wati Amalawi adapanga kale chiganizo cha kavotedwe koma adati mpofunika kuti asankhe mtsogoleri yemwe wawauza mfundo zomveka pakampeni kuopa kudzagwira fuwa lamoto. + Munthu wofuna voti amayenera kupanga kampeni kuuza anthu zomwe wakonza. Kungovotera kuti ndakonda uyu, mawa podzafunsa zitukuko amadzati Nnalonjeza liti? Anthu basi kakasi, adatero Phiri. + Kwa atsogoleri omwe akudzaima nawo, Phiri wati potengera malamulo, kampeni ikuyenera kutsekedwa mawa Lamulungu 6 koloko mmawa ndiye akuyenera kuti atsindika mfundo zawo moyenera. + Iye wati voti ya Lachiwiri ndi mwayi wachiwiri kwa Amalawi kusankha mtsogoleri wakumtima kotero akuyembekeza kuti Amalawi akavota mwaunyinji. + Wampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Chifundo Kachale adauza atolankhani sabata yatha kuti bungwelo ndi lokonzeka kuyendetsa chisankhocho ngakhale palo mavuto ena. + Vuto lalikulu lomwe lolipo ndikupelewera kwa ndalama ndi K7.8 biliyoni pa bajeti yonse ya chisankho. + Potengera zipsinjo zomwe zidaoneka pa kampeni, mneneri wa polisi James Kadadzera wati apolisi adzaonetsetsa kuti aliyense wavota mwamtendere Lachiwirilo. + Takhala tikupereka chitetezo ku zipani zonse pa kampeni. Tipitirira mpaka anthu avote komanso tidzapitirira kuteteza anthuwo, adatero Kadadzera. + Chisankhochi chichitika chifukwa khoti lidapeza kuti chisankho cha mtsogoleri wa dziko cha 2019 sichidayende bwino potsatira dandaulo la Lazarus Chakwera wa MCP ndi Saulos Chilima wa UTM omwe akupita kuchisankhochi pa mgwirizano. + Pachisankhochi, apikisane ndi mgwirizano wa MCP ndi UTM komanso zipani zina zisanu nziwiri ndipo mgwirizanowo akuutcha Tonse Alliance ndipo mgwirizano wa DPP ndi UDF komanso Mbakuwaku Movement for Development (MMD). + Chakwera akuimilira Tonse Alliance, Peter Mutharika akuimira mgwirizano wa DPP ndi UDF pomwe Peter Kuwani akuimira MMD. +",11 +"Namitembo College Iyendera Achinyamata ku Chingale Wolemba: Glory Kondowe Achinyamata a mdera la Chingale awapempha kuti akhale ndi chidwi chophunzira ntchito zamanja. +A Yohane Rodine omwe ndi mkulu okopa achinyamata mu project ya Hope For The Youth ku sukulu ya tchito za manja ya Namitembo mboma la Zomba anena izi pa mwambo wa zamasewero a mpira omwe unachitikira pa bwalo la Namitembo mboma la Zomba. +Cholinga cha masewerowa chinali chofuna kuphunzitsa ndi kukopa achinyamata-a kuti alembetse ndi kukayamba kuphunzira ntchito zamanja ku sukuluyi. +Tikumemeza achinyamata omwe kulembetsa kwawaphonya kuti akhoza kuzayamba nawo pa 26 August. Maphunziro omwe tikupeleka ndiwosiyana siyana malinga ndi centre komwe achinyamata akuphunzilira monga ku centre ya kwa William Mobile Center kuli zomanga-manga komanso zawukalipentara ndipo centre ya kwa Lisanjara parish aphunzira umisili wazamagetsi, zomanga manga ndinso umisili wawukalipentara ndipo onse omwe aziphunzira centre yathu ya ku technical college tikuphunzitsa umisili wazomanga manga, ukalipentara komanso umisili wazowotchelera, anatero a Yohane. +Mwazina a Yohane ati ntchito yomemeza achinyamata yayenda bwino malinga ndintchito yomwe anawapatsa achinyamata ena kuti alembe ophunzira omwe akufuna kukayamba maphunziro awo ndipo iwo ati achinyamata ambiri alembetsa ndipo ayamba kuphunzira pa 26. +",14 +" Chihana abweretse umboni za chuma cha Bingu Dausi: Pasathe masiku asanu Chipani cha DPP chati Yeremiah Chihana, amene adavumbulutsa zoti mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika adali ndi chuma choposa K61 biliyoni abwere ndi umboni wa nkhaniyi pofika Lachitatu. + Polankhula kwa atolankhani mumzinda wa Lilongwe, mneneri wa chipanicho, Nicholas Dausi adati zomwe adavumbulutsa Chihana zilibe umboni, ndipo zideafalitsidwa pofuna kudetsa mbiri ya DPP pomwe chisankho cha 2014 chili pamphuno. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pasanathe masiku asanu, Chihana abwere ndi zikalata zochokera ku mabanki amene akuti Mutharika adali ndi ndalama, chifukwa palibe banki yakunja imene ingangolankhula ndi Chihana pakamwa. Komanso abwere ndi zikalata za katundu ndi malo amene akuti Mutharika adali nazo, adatero Dausi. + Malinga ndi Dausi, mtsogoleri wakale wa dziko linoyu adalibe buku limodzi ndi mngono wake Peter, yemwe adzaimire DPP pampando wa mtsogoleri wa dziko lino pa chisankho cha chaka cha mawa. + Potha masiku asanu, abwere ndi umboni wochokera kubanki imene ili kulikonse padziko lapansi, ngakhalenso ku Malawi kuno kusonyeza kuti Bingu ndi Peter adali ndi buku lina la kubanki limene adatsegulira limodzi, adatero Dausi, pamsonkhano umenenso padali akuluakulu ena a DPP. + Koma Chihana, yemwe ndi mwini wake wa kampani yofufuza za katundu ya YMW Property Investment, Lachinayi adati akukambirana kaye ndi womuimira pamilandu asanayankhe zimene adanena a DPP. + Ndimve kuti andiuza zotani, chifukwa mlanduwu ukadali kukhoti ndipo angouimika kaye dzulo (Lachitatu) kuti tidzaupitirize pa 7 August, adatero iye. + Malinga ndi zomwe Chihana adapereka kubwalo la milandu, pomwe amatenga mpando Bingu adali ndi K150 miliyoni koma pomwe amatisiya, nkuti ali ndi ndalama zoposa K61 biliyoni mmabanki a mmaiko osiyanasiyana, kuphatikizapo Zimbabwe, South Africa, United States of America komanso kuno kwathu. + Vumbulutsolo litangophulika, boma lidatseka mabuku a Mutharika, pomwe ana a Mutharika: Duwa Mutharika-Mubaira ndi Tapiwa Mutharika amasamutsa ndalama zina kuchoka kumabuku ena a malemu bambo awo, kuika mwawo. Mutharika adasankha anawo kuti adzayendetse chumacho iye atatsikira kuli chete. + Mmbuyomu, Peter Mutharika adati boma likungofuna kulanga chipani cha DPP pomwe chisankho cha magawo atatu chili pamphuno. + Akutiopa. Akufuna kutilanda galimoto ndi mafamu kuti tisakhale ndi ndalama za kampeni, adatero iye. +",7 +" Bingu adafa bwanji, pakhale kafukufuku A mabungwe omwe si a boma, mfumu ina yaikulu komanso anthu angapo otumikiridwa ati nkoyenera kuti Amalawi adziwe bwino lomwe za imfa ya mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika choncho boma lisagonjere malingaliro ojejemetsa kafukufuku pankhaniyo. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kuunikiraku kwadza pomwe boma ndi banja la Mutharika akhala akuponyerana Chichewa pa ganizo la kafukufuku pa imfayo. + Pomwe a boma komanso mtsogoleri wa dziko lino Mayi Joyce Banda akhala akutsindika kufunika kwa zofufuzazo, akubanja malemuyo akhala akuti nkosayenera kutero chifukwa ati chomwe chidapha wawo chidadziwika kale. + Koma msabatayi ndemanga zati Mutharika anali wotumikira dziko, osati banja lokha, kotero anthu ayenera amve mvemvemve dziwe zambiri pa imfa ya mtsogoleriyo. + Mutharika adamwalira ndi matenda a mtima adzidzidzi ku mayambiliro a Epulo ndipo adalowa mmanda pa 23 Epulo. + Mwa zina, chinsinsi chachikulu chidakuta nkhani ya matenda komanso imfayo. + Malipoti a maudindo angapo amatsutsana; ena kumati Mutharika adamwalirira ku chipatala cha Kamuzu Central, ena amati kunyumba ya boma ku Lilongwe ndipo enanso amati ku chipatala mdziko la South Africa. + Pamtanda wa Bingu Nazo zolembedwa pa mtanda wosonyeza tsiku lobadwa komanso la kumwalira kwa Mutharika zimasinthasintha; mtanda wina umati anamwalira pa 5 Epulo, wina pa 6 Epulo ndipo wina nkumati pa 7 Epulo. + Masiku awiri thupi la Mutharika lisadalowe mmanda, ofesi ya Pulezidenti ndi nduna zake idati malemuyo adamwalira pa 5 Epulo koma mtanda womaliza udasonyeza kuti iye adatisiya pa 6 Epulo. + Apa anthu akhala akuti tsopano nkoyenera kudziwa tsiku lenileni lomwe Mutharika adamwalira komanso tsatanetsatane wa nthawi, malo komanso zochitika zomwe zidazinga maola ake omaliza. + Pa 4 Juni 2012, mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda, adalumbiritsa gulu loti lifufuze chenicheni pa imfa ya Mutharika koma a banja la malemuyo, motsogozedwa ndi mchimwene wake, Peter, adati kafukufukuyo nkungotaya nthawi. + Mtsogoleri wa mgwirizano wa mabungwe omwe siaboma la Council for Non-Governmental Organisations (Congoma), Voice Mhone, wati amabungwe achitapo kanthu ngati a banja la Mutharika akane kafukufukuyo. + Ife tikudabwa kuti kodi a banja akukaniranji. Kufufuzako nkoyenera ndipo tikuwapempha alole zomwe boma likufuna. + Amalawi sakudziwabe mmene Mutharika adamwalirira, adatero Mhone. + Mkulu wa bungwe loona ufulu wa chibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda, wati Mutharika adasankhidwa ndi anthu kotero anthuwo adziwe za imfa yake. + Ndikukhulupirira abanjawo chilipo akubisa. [Boma likafufuza] timva zambiri monga tsiku lenileni lomwe adafera, komwe adamwalirira komanso momwe zidachitikira kuti amwalire. + Timvanso za chuma chake ndiye a banja asakane, adatero Banda. + Akumudzi sadziwa Mfumu Yaikulu Malemia ya mboma la Nsanje yati anthu akumudzi sadziwabe tsiku lomwe Mutharika adamwalirira komanso matenda omwe adapha mtsogoleriyo kotero boma lisagonjere. + Iye wati zimamveka kuti kuti kunyumba ya boma komwe Mutharika adagwera kunalibe galimoto za boma zothandiza pa zadzidzidzi monga matendawa. + Malemia watinso nyumba zoulutsira mawu zakunja zidalengeza kuti Bingu wamwalira pomwe kuno akuluakulu amakana, kotero zenizeni sizinadziwikebe. + Ngati a banja akudziwa abwere poyera, apo ayi kafukufuku achitike, adatero Malemia. + Charles Kabaghe wa mmudzi mwa Mkombanyama kwa T/A Mwaulambia mboma la Chitipa wati ngakhale kafukufukuyo akhale wolira ndalama, achitike. + Zikumveka kuti Bingu adamwalirira kunyumba ndipo adangopita ndi thupi ku South Africa pomwe aboma panthawiyo adakana; izi zikutisokoneza. + Nalo tsiku lomwalira silikudziwika. Boma lifufuze tidziwe mutu weniweni, adatero Kabaghe. + Aubrey Jeke wa mmudzi mwa Sambani kwa T/A Mlolo mboma la Nsanje wati kumeneko anthu akufuna kudziwa zambiri. + Iye wati kumeneko zokamba nzambiri ndipo mpofumika boma likumbe nkhaniyi mwatsatanetsatane. + Boma limvere a banja Koma T/A Mwakaboko wa mboma la Karonga wati boma limvere zomwe abanja akunena chifukwa ngati iwo sakufuna kuti kafukufukuyo achitike sibwino kukakamira. + Mutharika adaikidwa kumalo ake ku Thyolo, malo amenewo si aboma ndiye a banja ali ndi ulamuliro onena zomwe afuna, adatero Mwakaboko. + Pulezidenti Banda adasankha gulu la anthu asanu ndi atatu kuti lifufuze za imfa ya Mutharika. + Gululi likutsogoleredwa ndi woweruza milandu ku bwalo lalikulu Elton Singini. + Enawo ndi Dr. Charles Dzamalala, yemwe adali mkulu wa apolisi, Joseph Airon, Dr. Tionge Loga, Dr. Elizabeth Sibale, Fr. Joseph Mpinganjira, Brian Nyasulu, Esther Chioko ndi woimira anthu pamilandu, Jabber Alide. + Lachisanu pa 15 akuchokera ku Mangalande, Banda adauza atolankhani kuti kafukufuku akhalapo pa imfa ya Mutharika. + Mayi Banda adati Mutharika adali mtumiki wa dziko lino kotero anthu akuyenera kudziwa chomwe chidamukokera ku masano. + Izi zidaipira mchimwene wa malemuyo, Peter, yemwe adauza nyumba youlutsira mawu ya Voice of America kuti sakumvetsabe zomwe boma likufuna pa nkhaniyi. + Iye anati ngati boma likufuna kudziwa chilungamo likafunse dotolo yemwe adalipo pomwe Mutharika amatengeredwa kuchipatala. + Iye adati ngati a banja ali okhutira ndi lipoti la imfa ya Mutharika palibenso chifukwa choti boma litaye nthawi kufufuzabe. + Nzamkutu komanso zopanda ntchito. Pali atsogoleri ambiri omwe amwalira mmaiko osiyanasiyana, kodi ndi kangati padali kafukufuku wa boma? Kafukufukuyu ndi wa zii. Ine monga wamkulu kubanja ndikukhulupirira kuti ndizopanda ntchito komanso kungotaya nthawi. + Ngati banja lakhutira bwanji boma likufunitsitsabe kupeza chomwe chidapha mtsogoleriyo? Akufuna chiyani? adadabwa Mutharika. +",11 +"MOAM Yati Ogwiritsa Ntchito Mitengo ya Minibus Yosavomerezeka Anjatidwe Bungwe la eni minibus mdziko muno la Minibus Owners Association of Malawi lati madalaivala omwe akugwiritsabe ntchito mitengo yokwera yomwe ndi yosavomerezeka ndi bungweli akuyenera kuti anjatidwe kamba koti kumeneku ndikuba. +Okwera minibus akulipirabe modula Wapampando wa bungweli Felix Mbonekera ndi yemwe wanena izi poyankhapo pa nkhawa zomwe a Malawi ochuluka ali nazo ndi kukwera kwa mitengo yokwelera ma minibus ngakhale kutsika kwa mafuta a galimoto kwachitika kawiri konse motsatana mdziko muno. +Iwo ati bungwe lawo linakambirana zotsitsa mitengo yokwelera minibus pa 8 May ndipo ngati oyendetsa minibus-wa sanatsitsebe, ndiye kuti akuphwanya malamulo. +Kungoti pansewu pachuluka nyasi zambiri. Pali madalaivala ndi makondakitala ena osamva. Ife tinawauza kalekale kuti mitengo ikuyenera kutsika ndipo akuyenera kumata mitengoyo pa galasi kuti aliyense asanakwere azidziwa mtengo wake woyenera ndipo ngati pali ena omwe sakutero apolisi agwire ntchito yawo, anatero a Mbonekera. +Mmwezi wa March chaka chino, boma linakhazikitsa ndondomeko yochepetsa anthu okwera minibus pofuna kuchepetsa kufala kwa kachilombo ka Coronavirus ndipo kutsatira izi mtengo wokwelera minibus unakweranso ndipo pambuyo pake mtengo wa Mafuta unatsika kawiri konse zomwe zimapereka chiyembekezo kuti eni minibus atsitsanso mitengo yawo zinthu zomwe sizinachiyike mpaka padakalipano. +",17 +" Basi ayisempha Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tsiku limenelo sitidakhale pa Wenela. Palibe ojiya, osolola, osenza ndi oitanira amene adatsala pa Wenela. + Tidakwera galimoto la mkulu wina kulowera ku Lilongwe. Si kuti timapita kuja kulikulu la boma kumene masamu ogula mmera asokonekera. + Sindingakambe nkhani imeneyo chifukwa tonse tikudziwa kuti lingaliro la Dizilo Petulo Palibe, malinga ndi kufotokoza kwa Joloji Chiponda, lidali logula chimangacho ku Brazil. Zoona mpaka kuoda chimanga ku Brazil! Nkhani ya chimangayi kwa ine ndiyongotaya nthawi. Ngati Moya Pete adalamula asilikali ake kukwidzinga uja wogona ndi amayi oposa 100 bwanji akulephera kulamulanso amene akuganiziridwa kukazinga mmera wa tonse pano pa Wenela? Zosamveka konse kuti mzimayi woti akufuna kugula chimanga choti adye pakhomo pake, mmalo mopita yekha kumsikako kutuma wina kuti akamugulire kenako nkumadandaula kuti waberedwa! Abale anzanga, tingoyerekeza kuti mwalemba wantchito, ndiye mukumukaikira kuti anaba ndiwo. Kenako mukuuza akazi kapena amuna anu kuti afufuze momwe anabera ndiwozo, wantchito wanu akapita pachulu nkumakuwa kuti: Sindinabe ine! Sindinabe! Chomwe ndimadabwa pano pa Wenela nchakuti nchifukwa chiyani aliyense amafuna kutalika zala pankhani za chimanga? Tidamvapo kuti Adona Hilida adagulitsa matani ochuluka kupita nawo ku Kenya. Nanga za Thursday Jumbo uja naye adadyapo zake za chimanga. Za makuponi ndiye ndisachite kunena. + Nsataye nazo nthawi izo. + Chaka chino talowa Talowa ndi adani omwe Akufuna moyo wanga Kuti aononge Chauta thandizeni Iyi ndi nyimbo imene tinkamvera mugalimoto ya mkulu amene adatitenga. Tidafika kubwalo la mpira latsopano kumene zipolopolo ndi nyerere zimamenyana. Inu, munthu nkupha nyerere poyiwombera! Ndidangomva kuti ena adathyola mipando, kutenga makalilole ndi zina zotero! Komanso abambo ena ankalowa kuzimbudzi za akazi! Utatha mpira, sindikudziwa kuti udatha bwanji, Abiti Patuma adandikoka kuti timuthawe mkulu uja. + Tidakakwera basi imene sindikuyidziwa bwino. Mudali anyamata a Chimwemwe kwambiri. Iwo amangoti 5 kwa 1, 5 kwa 1. Onse atamuona Abiti Patuma adakuwira limodzi: Abiti Patuma! Yo-yo-yo! Wina adamukumbatira, wina kumupsopsona patsaya. + Osadanda, mwayiphula basi! Ndikuthangatani nonse mbasi momwe muno, adatero Abiti Patuma. + Koma abale! Kudalitu kulandirana! Basi imamveka ndithu kuti mashoko siali bwino komabe mmodzimmodzi adali kulandira chithandizo kuchokera kwa Abiti Patuma. + Adati tinyamuke, ulendo wobwerera pa Wenela. + Tili mnjira, yemwe amaoneka kuti ndi mkulu wa anyamatawo adati: Tikakafika ku Mwanza, tikadzera kwa Ayaya tikayamike chifukwa watithandiza kupeza basi. + Ulendo wa kwa Ayaya sunatheke chifukwa basi idatchona pa Manjawira. Poyamba tinkadya kanyenya kuti mwina iyenda. Kenako kudali kusaka mango, ngumbi ndi zina mpaka mdima udagwa. +",19 +" Ankadzapepesa maliro a mkazi wanga Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Imfa ya mkazi kapena mwamuna wako si mathero amoyo. Mulungu amakoza njira ina kuti akupepese bwinobwino ndipo uyiwale zakale. + Iyi ndiyo nkhani ya momwe Excello Zidana mkonzi wa pologalamu ya Ulimi Walero adakumanirana ndi Keterina Mtambo, mphunzitsi pa Kamalambo FP School kwa Jenda ku Mzimba. + Keterina poyamba adakwatiwa ndi mbusa yemwe adamwalira zaka 7 zapitazo. Nayenso Excello adataya mkazi wake zaka zitatu zapitazo. + Excello ndi Keterina lero ndi banja Awiriwatu adakumana mu November 2013, apa Excello amapita ku Karonga kukagwira ntchito. Monga mkazi wa mbusa, Keterina adali ataiwala za imfa ya mwamuna wake ndipo adayamba kutonthoza Excello paimfa ya mkazi wake. + Kupatula kutonthoza, Keterina adalimbikitsa Excello ndi mawu a Mulungu, osadziwa kuti mawa awiriwa atonthozana zenizeni pokhala mayi ndi bambo Zidana. + Kuchoka apo, awiriwa akuti adagawana manambala kuti azilimbikitsana komanso kuchezerana kufikira mu January 2015 pamene nkhani idasintha. Chikondi chidayamba kumera pamtima pa aliyense, kodi Mulungu akufuna titani? Mu March 2015, ndidaganiza zomuyendera, kukangozindikira kuti ali ndi chilichonse chomwe ndimafuna..nditadzamuyenderanso mu May 2015, ohndiye mtima wanga kuferatu chifukwanso patsikulo adandikonzera nkhomaliro. + Basitu Keterina adangoti zitero monga momwe mukufunira.zonse zidatheka kuti basi tizikapepesana tokha pakuti tonse tidakumana ndi mavuto, adatero Zidana. + Pamene amakumana nkuti aliyense ali ndi ana atatu, pano poti awiriwa ndi thupi limodzi ndiye kuti banjali lili ndi ana 6 omwe ati akumvana motheratu. + Chinkhoswe chidachitika mu July ndipo ukwati wachitika pa 1 November, 2015 ku Likuni mumzinda wa Lilongwe. + Keterina amachokera mmudzi mwa Namasasa kwa T/A Mwabulambya ku Chitipa. Excello ndi wa mmudzi mwa Mtherereka T/A Namkumba mboma la Mangochi. +",15 +" Anatchezera Ndazunguzika Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 18 ndipo ndinazunguzika mutu chaka chatha pomwe ndinapezeka ndi kachilombo ka HIVkoma sindinagonepo ndi munthu ngakhale ndinali nacho chibwenzi. Amayi anga ali ndi HIV koma abambo anga alibe. Banja la makolo anga lidatha ndili ndi chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri. Ine ndine woyamba kubadwa koma ana onse obadwa kwa amayi anga amabadwa ndi kachilombo. Amayi anga akuti adatenganso pathupi ine ndili ndi miyezi 9 koma abambo anga amakana kuti mwanayo adali wawo. Ndiye ine zinandizunguza mutu kuti kodi zidayenda bwanji. Abambo anga ndi amayi anga ondipeza amandinena kuti ndinatenga kachilomboka kwa chibwenzi chomwe ndinali nacho. Mankhwala ndinayamba kumwa sabata yomwe anandipeza ndi kachilomboka popeza chitetezo chinali chotsika kwambiri, koma sindinadwale, ndidangopita ndekhala kukayezetsa ndipo ndinalibe nkhawa iliyonse. Koma pano ndikusowa mtendere. Ndithandizeni, chonde, nditani? RM, Mzuzu Zikomo RM, Nkhani yako ndaimva bwino lomwe ndipo ndakunyadira chifukwa ndiwe mtsikana wolimba mtima. Si ambiri amene amalimba mtima kukayezetsa magazi ngakhale sakudwala kuti adziwe momwe chitetezi chilili mthupi mwawo, ambiri amaopera kutalitali-safuna kudziwa nkomwe ngali ali ndi kachilombo kapena ayi. Wanena kuti udapezeka nndi kachilombo ka HIV chaka chatha koma wanenetsa kuti sudagonanepo ndi munthu wina aliyense ndiye zidatheka bwanji kupezeka ndi kachilomboka? Iyidi ndi nkhani yozunguza chifukwa ngakhale pali njira zambiri zotengera kachilomboka, njira yodziwika kwambiri ndi yogonana ndi munthu amene ali nako mosadziteteza. Koma zimatheka ndithu kutenga kachilomboka mwatsoka ndithu ndipo imodzi mwa njira zotere ndi kutengera kachilomboka pobadwa kuchokera kwa mayi amene ali nako. Ndikhulupirira iweyo udatenga kachilomboka panthawi yobadwa chifukwa wanena kuti ana onse obadwa mwa mayi ako akumapezeka ndi kachilombo ka HIV. Chomwe ndingakulangize nchoti pitiriza kumwa mankhwala otalikitsa moyo ndipo udzisunge monga wadzisungira nthawi yonseyi ndipo udzakhala ndi moyo wautali, wosadwaladwala. Uziyesetsa kuti usamakhale ndi nkhawa chifukwa izi zikhoza kubweretsa mavuto ena pamoyo wako. Uzilandira uphungu woyenera kwa akatswiri odziwa za kachilombo ka HIV kuti ukhalebe ndi moyo wathanzi ndi wansangala, osati kudzimvera chisoni. Kupezeka ndi kachilombo sikutanthauza kuti ufa nthawi iliyonse, ayi, utha kukhala zakazaka mpaka kukalamba monga ine, bola kudzisamalira. + Amadikira ndimuimbire Anatchereza, Ndine mtsikana wa zaka 15 ndipo ndili ndi chibwenzi koma anapita ku Nkhotakota. Poyamba timaimbirana foni koma panopa adaleka, amadikira ine ndiimbe. Kodi pamenepa ndimudikire? Agogo, ndithandizeni. + TG Mtakataka Zikomo TG, Kunena zoona mwana iwe wafulumiza kukhala ndi chibwenzi. Za sukulu uli nazo pafupi iwe? Ndakaika. Iwe, mwana wa zaka 15, chibwenzi nchachiyani, mwanawe? Ayi ndithu, ukayamba zibwenzi pamsinkhu wakowo sizidzakuthera bwino kutsogolo ndipo udzanongoneza bondo. Mwana wamngono ngati iwe sayenera kukhala ndi zibwenzi koma kuika mtima pamaphunziro chifukwa sukulu ndi yofunika kwambiri. Sunandiuze kuti bwenzi lakolo lili ndi zaka zingati, koma ngati ndi munthu wamkulu ndikhulupirira wazindikira kuti si bwino kukhala pachibwenzi ndi mwana wamngono ngati iwe, nchifukwa chake sakulabadira zokuimbira. Ndiye ngati umamva, chonde musiye ndipo uike mtima pasukulu! Ukapanda kumva langizo langa, kaya zako izo! Usadzati sindinakuuze. +",12 +" MESN ikufuna kuwerengera kwapadera Mgwirizano wa mabungwe a zachisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn) lati likumenyerera mabungwe ena kuti lidzakhale ndi malo apadera owerengera mavoti pachisankho cha 2014. + Bungweli likufuna malo apaderawa kuti adzafanizire zotsatira za chisankho ndi zimene bungwe loona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidzapeze. Izi ndi zothandiza kuti pasakhale chinyengo chobera mavoti poonkhetsa. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Msabata ikuthayi, Mesn idali ndi msonkhano wofuna kumva maganizo a mabungwe amene adapatsidwa chilolezo ndi MEC poyendetsa nawo chisankho. + Wapampando wa bungweli Steven Duwa adati njirayi ndi yabwino ndipo ingathandize akadaulo amene alibe mbali kuunikira bwino momwe anthu aponyera voti komanso kuwerengera mavotiwo. + Iye adati bungwelo likukonza zodzatumiza akadaulo 84 oona momwe chisankho chikuyendera komanso akadaulo 800 okaonkhetsa mwapadera mavoti komanso anthu ena 1 500 owona chisankho kuti pasakhale chinyengo. + Tikufuna kugwira ntchitoyi limodzi ndi mabungwe ena kuti pakhale chilinganizo chapadera kuti chisankho chilongosoke, adatero Duwa. + Ngakhale MEC idavomereza Mesn kuti ikhoza kukhazikitsa chilinganizochi, bungwelo lidati sichidzakhala chanzeru kuti Mesn idzangoonkhetsa mavoti mmadera ochepa. Bungwelo lidati ntchitoyi iyenera kugwiridwa mmadera onse a dziko lino. + Zikuoneka kuti chisankho cha 2014, mpikisano ukhala waukulu, choncho chilinganizochi chikhoza kuthandiza kuthana ndi ziwawa. +",11 +"Anjatidwa Atapezeka ndi Bokosi la MEC Apolisi mboma la Chiradzulu amanga anthu awiri omwe apezeka ndi bokosi la bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la MEC komanso katundu wina. +Bokosi ngati ili lapezeka litabedwa Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sergeant Yohane Tasowana wati anyamatawa agwidwa pa roadblock ya City Boundary atanyamulanso ma computer omwe malinga ndi mneneriyu si a bungwe la MEC koma abedwa pamalo ena obena nyimbo kwa Chikapa mu mzinda wa Blantyre. +Padakalipano anyamatawa atumizidwa ku polisi ya Limbe kuti akafunsidwe mafunso ena ndi ena. +",7 +" Boma litemera ziweto 10 000 Pofuna kuthana ndi mliri wa matenda a zilonda za m mapazi ndi mmkamwa a ngombe omwe agwa mboma la Chikwawa, boma lakonza zopereka katemera ku ziweto zoposa 10 000 mchigwa cha Shire posachedwapa. + Mlembi wa unduna wa zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi, Erica Maganga, watsimikizira Uchikumbe kuti boma laitanitsa kale mankhwala a katemerayu kuchoka kudziko la Botswana. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pakalipano mankhwala ali mnjira ndipo akhala akufika tsiku lina lililonse kuti ntchito yopereka katemera iyambike, adatero Maganga Lolemba. + Iye adati boma lachita machawi poitanitsa katemerayu pofuna kuti matendawa asafalikire mmadera ena komanso pofuna kuteteza ntchito zina za ulimi monga ulimi wa mkaka. + Boma lidakhazikitsa chiletso cha malonda a nyama ndi kutulutsa kapena kulowetsa ziweto mboma la Chikwawa zitatsimikizika kuti mbomali mudagwa mliri wa matendawa omwe pachizungu amati Foot and Mouth Disease. + Unduna wa zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi udatsimikiza za mliriwu womwe akuti udasautsa pamalo ena osambitsirapo ngombe a Mthumba omwe ali mgawo loyanganira za ulimi la Mitole EPA. + Mchikalata chomwe Maganga adasayinira sabata yatha, undunawu udati chigodola cha ngombe ndi nthenda yovuta kwambiri ndipo imagwira ziweto monga ngombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba komanso nyama zakutchire monga njati. + Potsirapo ndemanga pamliriwu, wachiwiri kwa mkulu woyendetsa ntchito za zaumoyo wa ziweto ndi ulimi wa ziweto, Dr Patrick Chikungwa, adati nthendayi ndi yowopsa kwambiri ndipo ngati yalekereredwa imafala msanga. + Nthendayi imafala kudzera mumpweya, kukhudzana kapena kudya msipu womwe uli ndi tizilombo (virus) toyambitsa matendawa, adatero Chikungwa. Adaonjezera kunena kuti anthunso atha kufalitsa tizilombo ta nthendayi kudzera mzovala kapena nsapato, koma adati alimi asade nkhawa chifukwa boma likuchita zothekera kuti nthendayi isafalikire madera ena. + Iye adati zizindikiro za nthendayi ndi kuchucha malovu, matuza mkamwa komanso pakati pa zikanamba za miyendo zomwe zimapangitsa kuti ngombe izivutika poyenda. + Ngati mlimi aona zizindikirozi, chomwe ayenerea kuchita nkupatula ziweto zodwalazi kuti zisakhudzane ndi zimene sizinakhudziwe ndi nthendayi, Chikungwa adalangiza. +",4 +"PAC, Ansah Sakuwulura Zomwe Akambirana Wolemba: Thokozani Chapola oads/2019/10/pac-ansah-pic.jpg"" alt="""" width=""770"" height=""462"" />Bungwe la PAC ndi Jane Ansah kutoletsa chithunzi pambuyo pa mkumano wawo Bungwe la Public Affairs Committee (PAC) lati lakhutira ndi mkumano wake ndi wapampando oyendetsa chisankho mdziko muno DR. JANE ANSAH omwe anali nawo lolemba mu mzinda wa BLANTYRE. +Arch-Bishop THOMAS LUKE MSUSA yemwe akutsogolera bungweri pa zokambirana zobweretsa mtendere mdziko muno ndi yemwe wanena izi kwa atolankhani atatha kuchita zokambirana zao ndi mayi DR JANE ANSA zomwe zinachitika ku ma ofesi a bungwe la MEC mu mdzinda wa BLANTYRE. +Ambuye MSUSA ati padakali pano gawo loyamba la zokambilanazi layenda bwino ndipo alowa gawo lachiwiri lomwe akhalenso akukambirana ndi mtsogoleri wa dziko lino PROFESSOR PETER MUTHALIKA, LAZARUS CHAKWERA mtsogoleri wa chipani cha MCP, ndinso wa chipani cha UTM, SAULOS CHILIMA kuphatikizapo bungwe la HDRC ngati magulu okhuzidwa ndi mpungwempungwe wa ndale omwe uli mdziko muno. +Koma poyankhapo ngati ali okonzeka kutula udindo pansi potsatira zokambiranazi mayi DR. ANSAH kumbari yawo sangayankhepo kathu koma anati ndi okhutira ndi momwe zokambirana zawo ndi bungwe PAC zayendera. +",11 +" Aganyu okhala ndi ziphaso Mwa zina zidabweretsa mawu woti tawuni ya Limbe imalira ochenjera, ndi kuberedwa kwa katundu ndi munthu yemwe udamukhulupirira kuti akunyamulire, wa ganyu. Tsopano padepoti ya Fumbi pali dongosolo lowumbanso chikhulupiriro chomwe chidagumuka pakati pa aganyu ndi mabwana komanso madona. TEMWA MHONE adakumana ndi Kassimu Sitande, mkulu wa anyamatawa, ndipo adacheza motere: Sitande (Wachitatu kuchokera kumanja) ndi ena mwa aganyu Akutanthauza chani anyamatawa ponena kuti ndi ovomerezeka? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nkhani ndi ya chiphaso. Ichi ndi chilolezo chawo kuchita ganyu padepoti ya Fumbi ino. Komanso mabwana ndi madona asadere nkhawa kuti katundu wawo asowetsedwa. + Ganyu mpaka ziphaso? Tilipo anthu 34 ndiye umboni wogwirika umafunika osati kungoyankhula kuti ndi waganyu. Zongodziwana ndi zimene zatiyika mmavuto kwambiri zaka zapitazo. Kwina kulibe dongosololi, koma ntchito ndi unzika wa pano zimafuna chiphaso ndithu. + Fotokozani zifukwa zokhazikitsira ziphaso pakati panu? Anthu akhulupirire kuti si ife okuba. Uku ndi kukhwimitsa chitetezo cha mabwana ndi madona komanso waganyu. Tikufuna kubwezeretsa chikhulupiriro mwa anthu kuti ife [aganyu] ndi wothandiza mu Limbe muno kunyamula katundu wawo. Kumbukirani kuti vakabu yakhala ikutivuta ndi kulepheretsa kupeza ndalama zochuluka. Apolisi ankatimanga pamlanduwu womwe timayenera kulipa ndalama zambiri, koma anthu sakutinyamulitsanso katundu. Iyinso ndi njira yoti anthu azidziwa wanyamula katundu ndi cholinga choti akathawa apezeke mosavuta. Bwana atenge chiphaso ndipo amubwezere wa ganyu akafika komwe amapita ndi kumulipira. Tikubweretsa dongosolo. + Koma mkalabongo umakuchotsani ulemu Iyayi. Zimenezo ndi zakale zomwe zatsala ndi aganyu ena osati ife. Pofika popanga ziphaso ndife ana odziwa dongosolo. Loweruka 2 koloko masana timakhala ndi maphunziro mmene tingalemekezere mwini katundu. Ngakhale amwe mkalabongo, amadziwa kasitomala ndi ofuna ulemu kuti apeze yomwera mawa komanso chakudya cha kunyumba. Mabwana ndi madona akanyamulitsa katundu adziwe dzina la mnyamata. Izi zimapezeka pachiphasochi ndipo akachitidwa chipongwe akuyenera kubwera kuti athandizidwe. + Zidatani kuti mupange gululi? Kusiyanitsa akuba ndi aganyu. Lidalinso khumbo lomathandizana muzilinganizo zina komanso mavuto. Mukudziwa kuti maliro amafuna ndalama zambiri ndiye tidaganiza zomatengera wodwala kumudzi kwawo kuti zikavuta abale apepukidwe komanso kuzondana wina akadwala. Nthawi ya vakabu ija timasonkherana ndalama yokawombola mnzathu akamangidwa kupolisi. + Ndi chiyani chomuyenereza munthu kukhala waganyu? Chidwi chonyamula basi. Koma abwere kuofesi kuti amve malamulo ndipo akagwirizana nawo ndi mfulu pano. + Chifukwa chiyani anyamatawa akusiya ziphaso poweruka? Iyi ndi njira imodzi yoteteza chiphaso chifukwa angataye kapena kuwabera kumowa. Anthu akhonza kukaba kwina ndi kuchita chipongwe pochitaya [chiphaso] ndi kupachika mnyamata wathu. Ntchito timayamba 6 koloko mmawa yomwe timagawira ziphasozi ndipo kuweruka 5 koloko madzulo. Paja malo ano [mlatho pamtsinje wa Limbe] athu amachitidwanso chipongwe ndiye timaweruka [5 koloko] kuti zisatikhudze za chifwambazo. + Ofesi yanu imachitanso chiyani? Timagwira ntchito ndi mabungwe osiyanasiyana polimbikitsa anyamatawa kuyezetsa magazi komanso okwatira kumalera. Tili ndi dongosolo lopereka peshoni (K4 000) kwa waganyu yemwe adakula pa 15 mwezi uliwonse kuti asachite kusowa ya sopo. Ndalamazi ndi zomwe mamembala timapereka pa sabata. Pakadalipano, tikudikira yankho kupolisi ya Limbe pa pempho lathu logwira nawo ntchito pokhwimitsa chitetezo. + Mavuto omwe mumakumana nawo ndi ati? Kukanika kwa anthu kutipatsa ntchito chifukwa cha zikhomo adakumana nazo kale. Ena amatinyozanso kuiwala kuti tonse sitingakhale mabwana. Koma sitizitengera podziwa kuti Mulungu amatithokoza kaamba ka madongosolo obweretsa bata mu Limbe. +",10 +" Malawi ali mu mdima Zasokonekera! Malawi ali pamoto wosaneneka ndi kuzimazima kwa magetsi. Anthu akumudzi akugona kuchigayo kudikira magetsi pamene alimi a ngombe zamkaka akutaya mkaka. + Ndi Loweruka usiku cha mma 10 koloko pamene timafika pachigayo cha Muhiriri mdera la mfumu Kasisi mboma la Chikwawa. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Si zidaonekenso: Amayi kugona mchigayo podikira kugayisa chimanga Anthu 16, atatu mwa iwo abambo, ali pachigayopa kudikira magetsi. Anayi okha ndiwo ali maso pamene onse agona. + Matumba a chimanga komanso mapira andandana kuti magetsi akayaka agayise. Magetsiwatu akuti adazima Lachisanu mmawa. + Pafupi nane pali mayi wachikulire, ndi wothodwa. Sindikudziwa kuti ayaka nthawi yanji, koma ndabwera pano mmawa cha mma 7, adatero mayiyu, Ezelesi Stanton wa zaka 60. + Ngakhale atayaka, Stanton sangabwerere kumudzi chifukwa wayenda mtunda wa makilomita 8. + Awa ndiye ndi mavuto adzaoneni: Anthu akudikira magetsi ayake pa chigayo cha ku Chikwawa Kunyumba kulibe ufa, ndasiya ana ndi bambo. Kuti ndibwerere ndiye sitikadya chifukwa ufa udatheratu, adatero mayiyu. + Awa ndiwo mavuto amene akungana kumudzi pamene bungwe lopanga magetsi la Electricity Generation Company of Malawi (Egenco) likungopanga pafupifupi theka la magetsi amene dziko lino likufuna. + Izi zikupangitsa kuti anthu ena, monga aku Chikwawa, azitha masiku awiri osaona magetsi. + Eleni Kalavina wa mmudzi mwa Chikalumpha akuti mwezi wa November wokha wagona kuchigayo kanayi, kudikira magetsi kuti agayise. + Pamene timafike pa chigayopa, Kalavina adali mtulo. Iye adadzidzimuka pemene mwana wake wa miyezi 7 amalira. Iye adadzuka ndi kumuyamitsa. + Pachigayopatu pali ana oyamwa anayi amene agona kumimba kwa amayi awo. + Ambuye adzatitenge, dziko lino latopetsano, Kalavina adatero. Mwina nkukaona zina kumwambako. + Kodi Ambuye abwera liti? Tatopa abale. Iye adati kuzimazima kwa magetsi kukuzuza moyo wawo komanso mabanja awo. + Nthawi zina amunanga amandikaniza kuti ndisadzagone kuno poganizira kuti mwina ndikukayenda ndi amuna ena pamene si choncho, adatero. + Pamene nthawi imathamangira 12 koloko usiku, bambo wina adafika pamalopo mokuwa. Kodi kuli akazanga kumeneko? Bamboyu, Davie Kachiza wa zaka 49, amachokera mmudzi mwa Josamu mdera la mfumu Katunga-mtunda wa makilomita 7-kudzasaka mkazi wake. + Ndakhala ndikumudikira koma mpaka pano sakubwera. Ndanyamuka cha mma 9 koloko usiku kuti ndisake chigayo chomwe ali, adatero mkuluyu. + Kunyumba wasiya mwana wa zaka 14 ndi wina wa zaka 9. Koma pachigayopo padalibe mkazi wake ndipo adatsetserekera ku chigayo china komwe adakamupeza. + Kachiza adapempha atsogoleri kuti athetse mavuto amene akunga Malawi. Tivomereze zinthu sizili bwino mdziko muno. Malawi waipa, adatero Kachiza. + Nyakwawa Zakaliya idati anthuwa alibe kothawira chifukwa amayenera ayende mtunda wa makilomita 17 kuti akapeze chigayo cha dizilo. + Iye adati ali ndi mantha ndi anthu ake. Kugona kuchigayo komanso kumayenda ndi usiku kusaka magetsi, ndi zachisoni, anthuwa atha kuchitidwa chipongwe komanso kunyumba kwawo akumasiya ana pamene makolo ali kuchigayo, adatero Zakaliya. + Pamene timachoka pa chigayopo mmama wa Lamulungu nkuti magetsi asadayakebe ndipo akuti adayaka cha mma 5 madzulo a Lamulungu. + Mavutowa sadasiye malo, ku Ntcheu, Thyolo ndi Nkhata Bay, anthu akuti ayamba kumasinja pamanja pamene ena akuyenda mitunda yotalika kusaka chigayo cha dizilo. + Tayamba kusinja pamanja kuno, adatero mfumu Kabunduli ya mboma la Nkhata Bay. + Boma lisagawe pakati Escom. Izi ndi zomwe zikubweretsa mavutowa. Aleke Escom izipanga ndi kugulitsa yokha magetsi, idaonjeza choncho mfumuyo. + Samuel Mugwa, mlimi wa ngombe za mkaka wa kwa Goliati mboma la Thyolo, akuti akusowa kogulitsa mkaka chifukwa makampani ogula mkaka ayimika kaye chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi. +",2 +" Kudali ku Presbyterian Church of Malawi Kudali kuphwanya mafupa ku Dream Centre Assemblies of God mumzinda wa Blantyre Loweruka pa 2 May pamene Faith Mussa amamanga ukwati ndi bwenzi lake Brenda Chitika. + Brenda ndi kanjole ka mmudzi mwa Sikoya kwa T/A Chikumbu mboma la Mulanje ndipo ndi wachinayi kubadwa mbanja la ana asanu. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Faith, amene adatchuka kwambiri ndi nyimbo ya Desperate, akuti ubongo wake udasokonekera pamene adaona njoleyi Lamulungu mu 2009 pomwe mnyamatayu adapita kumpingo wa Brenda wa Presbyterian Church of Malawi (PCM) mumzinda wa Blantyre kukatsitsimuka. + Faith adatsitsimuka zenizeni chifukwa kusalalanso kwa njoleyi kudaziziritsa mtima wake. Tsikulo Mulungu adamupatsadi chosowa chake. + Ndili mtchalitchimo foni idaitana ndiye ndidapita panja kukayankha. Ndili panjapo kulankhula pafonipo, ndidaona namwaliyu chapakataliko akutonthoza mwana, adatero Faith. + Faith Mussa kuimbira namwali wake kanyimbo kachikondi Maso adali panamwali, khutu lidali pafoni. Iye samasunthika ndipo pena Brenda akuti amathawitsa diso lake kuti asaphane maso ndi mnyamatayu koma Faith samasunthika. + Izi zidatanthauza kanthu kena mumtima mwa Faith ndipo nkhani yonse idakambidwa patangotha mwezi. + Titaweruka, ine ndi mchimwene wanga tidaperekeza Brenda. Ndinene apa kuti mwana amatonthozayo sikuti adali wake. + Poyamba Brenda amacheza ndi mbale wanga ndiye pamenepa ndidadziwiratu kuti ndikuyenera kuchitapo kanthu, adatero Faith. + Pangonopangono awiriwa adakhazikitsa macheza ndipo Faith sadachedwetse koma kugwetsera mawu oti adzalumikize awiriwa kukhala banja. + Padatha nthawi kuli zii, za yankho tidakaika koma pa 28 August 2009 ndidangolandira foni kundiuza kuti wagwirizana ndi zomwe ndidamuuza, adatero Faith wachiwiri kubadwa mbanja la anyamata atatu. + Ndipo Brenda adati Faith ndi munthu wochezeka, wachikondi komanso woopa Mulungu. Chinsinsi chathu chidali kukonda Mulungu, nditaona kuti Faith ndi munthu wokondanso kupemphera, ndidadziwa kuti mwamuna koma ameneyu, adatero Brenda. Tags: Kudali ku Presbyterian Church of Malawiudali kuphwanya mafupa ku Dream Centre Assemblies of God mumzinda wa Blantyre Loweruka pa 2 May pamene Faith Mussa amamanga ukwati ndi bwenzi lake Brenda Chitika. +",13 +" Chisangalalo chafika, Samalani kuli mavuto Mawa laliwisiri ndi tsiku la Khirisimasi ndipo Lamulungu sabata ya mawa ndi tsiku lokumbukira kulowa chaka cha 2017. Iyi ndi nthawi imene ena amasangalala ngati kulibe mawa, koma akadaulo anenetsa kuti iyi ndi nthawi yokumbukiranso kuti kuli msilikali wamkulumwezi wa Januaryamene amasiya ambiri mmatumba muli mbeee! Ena amavulala kapena kufa kumene chifukwa chosangalala mosasamala. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Katswiri pa zachuma, Henry Kachaje, wati matumba amabooka mu January chifukwa cha kusakaza ndalama mosasamala nyengo ya zikondwereroyi. + Iye adati ndondomeko yabwino pakagwiritsidwe ntchito ka ndalama ingathandize kupeputsa ena mwa mavuto omwe amaoneka mu January monga ngongole zosakonzekera. + Anthu adali pakalikiliki kugula katundu msabatayi Iyi ndi nthawi yomwe timaona anthu akumwa, kudya ngakhalenso kuvala moposa mapezedwe awo. Mchitidwewu ndiwo umabala mavuto mwezi wa January, adatero Kachaje. + Iye adati kukonzekera kwa nzeru nkuonetsetsa kuti zinthu zofunikira kwambiri monga chakudya zagulidwa mokwanira nkusungidwa moyenera mapwando asadayambe. + Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe olimbikitsa maphunziro la Civil Society Coalition for Quality Education, Benedicto Kondowe, adati ana ena alephera kupita ku sukulu chifukwa choti makolo awo adaononga ndalama za fizi. + Kondowe adati pomwe makolo akukonza zisangalalo zosiyanasiyana, alingalirenso za ndalama za fizi ya ana awo kuti asadzagwire njakata nthawi yotsegulira sukulu ikadzafika. + Chowawa kwambiri pamoyo wa mwana nkuona anzake akupita kusukulu iye ali pakhomo kaamba kosowa fizi. Kuli bwino kuchepetsa chisangalalo koma nthawi ikafika, ana adzapite kusukulu, adatero Kondowe. + Mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Prince Kapondamgaga adati kusangalala nkofunika pamoyo wa munthu koma adachenjeza alimi kuti asaiwale kugula zipangizo zaulimi kaamba kokomedwa ndi zisangalalo. + Iye adati mlimi wanzeru amaonetsetsa kuti chilichonse chomwe angafune paulimi wake chilipo asadayambe kulingalira zina chifukwa iyi ndiyo njira yomwe iye angapindule nayo paulimi wake. + Aliyense amafuna kusangalala mmoyo mwake koma zinthu zimakoma zikamayenda ndi nthawi komanso kuthekera komwe kulipo. Osayamba maphwando ulibe zipangizo zaulimi ngati ndiwe mlimi, adatero Kapondamgaga. + Mkulu wa bungwe loyanganira za anthu ogula la Consumers association of Malawi (Cama) John Kapito adati anthu asaiwale za njala yomwe iliko chaka chino. + Iye adati nzopanda phindu kusangalala masiku ochepa koma kenako nkudzavutika masiku ambiri ndi njala zomwenso adati zingapangitse chitukuko kulowa pansi. + Tonse timadziwa kuti munthu amagwira bwino ntchito ndi mkhuto ndiye ndi njala ya chaka chinoyi, nkofunika kusamala kwambiri pa momwe tingakonzere zisangalalo zathu. Tiyeni tionetsetse kuti tasungako ndalama ndi chakudya mmakomomu, adatero Kapito. + Mchikalata chake mnyengoyi, bungwe loonetsetsa kuti malonda akuyenda mokomera aliyense mdziko muno la Competition and Fair Trading Commission (CFTC) lati nyengo ngati iyi amalonda ena amafuna kukokera ponyenga ogula. + Bungweli lati nyengoyi, anthu a mabizinesi amagwiritsa ntchito bodza potsatsa malonda awo ndi cholinga choti anthu akopeke ndipo kawirikawiri anthu sazindikira kuti apusitsidwa kaamba kakukomedwa. + Ambiri amanama kuti atsitsa mitengo. Mwachitsanzo, amatha kunena kuti katundu wafika pa K15 000 kuchoka pa K25, 000 chonsecho katunduyo sanagulitsidweko pa K25, 000, lidatero bungwelo. +",15 +" Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Gift Banda ndi mkazi wake Tisunge Mandala adakumana koyamba ali ku sukulu ya sekondale ya Chiradzulu komwe ankaphunzira. + Atatsiriza maphunziro awo aku sekondale, amakumanabe mnjira ndipo amacheza nkhani ziwiri zitatu. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tikakumana tinkangocheza mmene anthu amachezera, koma padafika poti tayamba kukumana mowirikiza ndipo chidwi ndi chikondi chidayamba kuchuluka mpaka ubwenzi udayamba, adatero Banda. + Iye adati adamufunsira Mandala atakopeka ndi kumvera kwake akamuitana kuti abwere azacheze. + Komanso nkhani zomwe tinkakambirana tikakumana ndi zomwe zidandikopa kwambiri mtima, adatero Banda. + Awiriwa adakhala pa chibwenzi zaka zitatu asadalowe mbanja. + Gift Banda ndi mkazi wake Tisunge Paubwenzi wawo adakumana ndi zokhoma zingapo monga kukaikiridwa ndi makolo awo omwe amaganiza kuti akungochita zachibwana ngakhale eni akewo amadziwa kuti chikondi chawo nchozama komanso chili ndi tsogolo lowala. + Iwo akulangiza achinyamata omwe akufuna kupanga chiganizo chopeza wachikondi kuti azidekha, kukhala ndi nthawi yabwino yomudziwa wachikondi wawo ndipo asathamangire zogonana asadapange dongosolo lonse lofunika. + Awiriwa akuti akakumana ndi mavuto mbanja mwawo amagwada pansi nkupemphera kuti Mulungu awathandize. + Ngati mwamuna ndimapereka mpata kwa mkazi ngati mbali imodzi ya banja kuti nayenso azitha kupereka maganizo ake pa momwe tingagonjetsera mavuto omwe takumana nawo, adatero bamboyo. + Banda amagwira ntchito youlutsa mawu ku wailesi ya Capital FM pamene Mandala ndi mphunzitsi pa sukulu ya pulaimale ya Bangwe CCAP. + Pakadali pano awiriwa akukhala ku Mthandizi ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre. + Banda amachokera mmudzi mwa Chauwa, Mfumu Ndakwera, mboma la Chikwawa pamene Mandala amachokera mmudzi mwa Kabambe, Mfumu Likoswe, mboma la Chiradzulu. +",15 +" JB wati mafumu alandira fetereza padera Mafumu angapo ati alibe vuto ndi chilinganizo chatsopano cha Pulezienti Mayi Joyce Banda choti atsogoleriwa asalandire makuponi a panyumba pawo popeza alandira fetereza wawo padera. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma katswiri pandale, yemwenso adachitapo kafukufuku pa ndondomeko ya zipangizo zaulimi zotsika mtengozi, Blessings Chinsinga, akuti sakukhulupirira kuti njirayi ingakhale yankho pamavuto omwe akhala akubuka chaka ndi chaka. + Polankhula Lolemba lathali ku Salima, Mayi Banda adati mafumu akhala akukhudzidwa ndi nkhani za ziphuphu pa makuponi kotero chaka chino angothandizira chabe, osati kukhala nawo mgulu lolandira. + Izi zikudza pomwe mafumuwa akhala akunjatidwa ndi nkhani zimenezi. Chitsanzo chaka chatha, apolisi ku Mangochi adamanga Nyakwawa Kalapwito ya kwa T/A Chimwala pozembetsa matumba 38 otsika mtengowa komanso makuponi 27. + Pothirira ndemanga pa ganizo la Banda, T/A Kalonga ya mboma la Karonga yati Banda wamva kulira kwa anthu kotero akukhulupirira kuti ganizoli lithandiza. + Ngati akunena izi kuchokera pansi pa mtima ndiye kuti zitithandiza, adatero Kalonga. + Naye T/A Mlumbe ya mboma la Zomba yati apa mfumu yadyera ionekera poyera. + Izi zikuwonetsa kuti Pulezidenti waganiza mofatsa; si zobisa, tamvapo kuti mafumu akukhudzidwa ndi nkhaniyi. Apa mafumu atilemekeza, idatero mfumuyi. + T/A Mlauli ya mboma la Neno yati ganizoli lilibwino, bola zichitike mwa chikonzero. + Koma Chinsinga akuti ili silingakhale yankho, ati chikonzerochi nchoponderezabe omwe sangakwanitse kugula thumba la fetereza. + Ndikuganiza choncho chifukwa ndondomeko imeneyi ndi ya anthu osauka omwe sangakwanitse kugula thumba la fetereza. Sindikudziwa ngati mafumuwa ali mgulu la anthu osaukitsitsa omwe sangakwanitse kugula. + Ena angaganize kuti ganizoli labwera pofuna kuhonga mafumuwa, akutero Chinsinga. + Iye adati kafukufuku yemwe wachita wapeza kuti mafumu akukhudzidwa ndi mchitidwe wa ziphuphu poyendetsa ndondomekoyi. + Mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, tidalephera kulankhula naye kuti afotokoze za ndondomeko yatsopanoyi. +",4 +" MBS iletsa mafuta a mtimachubu Amalawi amene akhala akukazingira mafuta a mmachubu tsopano ayenera kupeza njira ina chifukwa bungwe loyesa zopangidwa zosiyanasiyana mdziko muno la Malawi Bureau of Standards (MBS) laletsa mafutawa ndipo amene azigulitsa azengedwa mlandu. + Mkulu wa bungweli Davlin Chokazinga adati sikukhala zonyengerera pokwaniritsa izi, pofuna kuteteza miyoyo ya Amalawi. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Aliyense amene akugulitsa mafutawo adziwe kuti tithana naye. Talanda kale mavenda ena ku Mulanje, adatero iye. + Chokazinga adati mafutawo angabweretse matenda pamoyo wa munthu kotero nchifukwa adaganiza kuti asapezekenso mdziko muno. + Iye adati izi akuchita potsata malamulo awo kuti katundu ogulitsidwa mdziko muno ayenera kukhala wabwino wosapereka chiopsezo ku miyoyo ya anthu. + Ganizo la MBS ladzidzimutsa anthu amene amagulitsa mafutawa pamene adati boma kapena akuluakulu a bungweli awapatse chochita asadaletse kugulitsako. + Gift Majongoti yemwe akuti amagulitsa chigubu cha malita 20 patsiku pamsika wa Mbayani mumzinda wa Blantyre, wati apa boma lamutsekera mpita. + Ndili ndi ana ndi mkazi komanso kumudzi anthu amadalira ine ndiwatumizire thandizo monga feteleza ndi zina. Zonsezitu zikuchokera mgeni imeneyi. Kuletsa kwa boma ndi imfa yanga yomwe chifukwa palibe chomwe ndingachite kuti chindibweretsere ndalama. Ngati akufuna kuletsa ndiye atipezere zochita, adatero Majongoti. + Iye adati Pali anthu ambiri amene sangakwanitse kugula mafuta okwera mtengo. Taganizani anthu amabwera ndi K20 kuti tiwagulitse mafuta andalamayi ndipo timawayezera. Lero anthu amenewa mukawauze kuti akagule mafuta a K1 000 angakwanitse? adazingwa Majongoti. + Si ogulitsa okha, nawo ogula akuti MBS ikuwaika kumpeni chifukwa sangakwanitse kugula mafuta ena amene ndi otsika mtengo kuposa oyezawa. + Mmodzi mwa anthuwa, Clara Nyandula wa mmudzi mwa Maduwani, T/A Nkaya ku Balaka polankhula ndi Tamvani pafoni adati banja lake limadalira mafutawa ndipo sapezanso mtengo wina wogwira. + Pa mwezi ndimagwiritsira ntchito malita awiri amene timagula pa mtengo wa K600 pa lita. Akaletsa ndiye akutiganizira kumene? adafunsa motero Nyandula. + Iye adati boma liyenera kuwaganizira chifukwa akadya zokazingira, mafuta ake amakhala oyezetsawo. + Modester Chimpando wa kwa Manje kwa T/A Kapeni mboma la Blantyre adati izi zisachitike chifukwa apweteka anthu osauka. + Sindikukana, mafuta enawa ali ndi chiopsezo pamoyo wamunthu. Chofunika nchakuti ngati akufuna kuletsa ndiye aonetsetse kuti mafuta abwinowo akugulitsidwa motsika mtengo komanso pa mlingo wochepa kuti aliyense akwanitse kugula. + Ngati sizitero ndiye akhala ngati akukonza koma akuika miyoyo ya anthu ovutikitsitsa pamoto, adatero Chimpando. + Koma izi sizikusintha ganizo la Chokazinga pamene akuti anthu akuyenera kusankha moyo kapena imfa. + Ngati moyo ndi imfa chabwino chili moyo ndiye ife tipitirirabe ndi ganizo lathu kuti anthu akhale moyo, adatero Chokazinga. + Chokazinga akuti moyo ndi wodula kotero anthu avomereze. Kodi kutaya K20 ndikuti ukataye ma miliyoni kuchipatala chabwino nchiyani? Anthu adziwe kuti moyo wathu ndi wodula kuposa mafuta amene akugulawo. + Pachifukwa chilichonse ife sitikubwerera mmbuyo koma kugwira amene akugulitsa mafutawa chifukwa simafuta abwino kumbali ya ukhondo wa munthu, adatero Chokazinga. + Iye adati ntchitoyi sikuti ayamba lero koma kuti adangozimirira. Adaonjeza kuti bungwe lawo lalembera makampani ena amene akumapanga mafutawa kuti alekeretu. + Aliyense atha kupanga mafuta koma mafutawo akuyenera kuvomerezedwa ndi ife komanso mafutawo akhale ndi uthenga onse kuti akabweretsa mavuta kwa anthu, tione kolowera. Koma chomwe chikuchitika ndi mafutawa nchakuti palibe uthenga wa amene akupanga, munthu atamwalira ndi mafutawa tingasowe koloza. Kaamba ka izi nchifukwa tikuletsa, adatero Chokazinga. + Kumbali ya matenda amene mafutawa angabweretse, Chokazinga akuti sakuona matenda amene angabwere koma kuti, mafutawa si abwino pa moyo wa munthu. Ngati chinthu sichili bwino chingabweretse matenda osiyanasiyana mosatchula amodzi chifukwa chinthucho sichoyenera pamoyo wa munthu. + Iye wati mafuta angathe kugulitsidwira mmasacheti koma akhale wodinda bwino ndipo yemwe akupanga mafutawo akuyenera kuvomerezedwa ndi bungwe lawo. + Naye mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito adati MBS yachita bwino kuletsa mafutawa. + Takhala tikuwauza a MBS kuti aletse mafutawa, ngati ayamba kuletsa ndiye zili bwino. Ogula adziwe ndithu kuti mafutawa siabwino. Mafuta abwino ndi amene amapakilidwa bwino komanso pali zizindikiro za kampani yomwe ikupanga kuti zikativuta ifeyo monga ugula tikaone kodandaula. + Sitikusangalala kuti anthu akugula zinthu zonyasa ngati zimenezi. Amene akugulitsa alekeretu, kodi bizinesi ndiye kugulitsa zoipa? Izitu mapeto ake tidzalola a chamba kuti azigulitsanso chifukwa akuchita bizinesi, adatero Kapito. + Mafutawa amagwiritsidwa kwambiri ndi anthu akumudzi maka chifukwa cha kutchipa kwake. +",18 +" Madzi achita thope ku DPP Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Madzi sakudikha kuchipani cha DPP pamene mpungwepungwe wolimbirana amene adzatsogolere chipanichi ku chisankho cha 2019 wafika pa kamuthemuthe. + Atsogoleri ena a chipanichi anenetsa kuti kaya wina afune kaya asafune, amene atsogolere chipanichi ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika basi, osati wachiwiri wake Saulos Chilima monga ena akufunira. Ofuna Chilima akuti Mutharika, yemwe ali ndi zaka 79, wakalamba ndipo sangadzapambanitse chipanicho pachisankho cha chaka chamawa. + Ena akufuna Mutharika (Kumanja) pomwe ena kuti koma Chilima Mkokemkokewu ukudabwitsa kadaulo wandale ku Chancellor College, Ernest Thindwa amene akuti izi zimayenera zikachitike kumsonkhano waukulu. + Iye adati akuluakuluwa akuyenera kuchita manyazi chifukwa izi zimatuluka kumsonkhano waukulu osati zomwe zikuchitikazi. + Ngati chipanicho chili cha demokalase, ndiye sakuyenera kubwera kale ndi mtsogoleri wawo pokhapokha msonkhano waukulu utachitika. Amene akusankha APM akuyenera kuchita manyazi chifukwa izi zikusemphana ndi ndale za demokalase, adatero Thindwa. + Lachiwiri msabatayi, wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanicho mchigawo cha kummwera, George Chaponda adati Mutharika akadutsa kumsonkhano waukulu popanda wopikisana naye. + Naye mneneri wachipanicho Nicholas Dausi adati wina afune kaya asafune koma Mutharika ndiye atsogolere chipanichi mchisankho cha 2019. + Tichititsa msonkhano waukulu womwe ukasankhe mtsogoleri, koma wathu ndi Mutharika basi, adatero Dausi. Akupitiranji kumsonkhano waukulu pamene asankha kale mtsogoleri? zikudabwitsa Thindwa. + Mlembi wa chipanichinso Greselder Jeffrey adati kaya satana afune kaya asafune koma Mutharika mpaka 2024. + Wathu ndi APM amene timutengere kuchisankho cha 2019. Kaya ena afuna kaya ayi koma zichitika motero, adatero Jeffrey. + Mbali inayi, phungu wa chipanicho kummawa kwa boma la Mulanje, Bon Kalindo adati kaya wina afune kaya asafune, chipanichi chitsogozedwa ndi Chilima. + Iye adati zomwe akupanga akuluakulu ena a DPP kuli ngati kuwaonjezera mafuta kuti ganizo lawo lobweretsa Chilima litheke. + APM ayi, wakula. Kodi atitsogolere kuti? koma nchifukwa chiyani tikufuna kuti okalamba azititsogolera? Atitsogolere kuti? Tilipo gulu, tikukumana ndipo posakhalitsa tidziwitsa Amalawi zomwe takonza, adatero Kalindo. + Iye adati vuto lalikulu ndi anthu amene azinga Mutharika. Izi zikupherezera zomwe adanena mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Callista Mutharika, ayemwe adashosha mavu mkhomola pobwera poyera kunena kuti mlamu wake Peter akukakamizidwa kudzaimanso ndi zilombo zimene zamuzungulira. + APM ndi munthu wabwino koma wazunguliridwa ndi ngona. Ndipo ngati sasamala zimudya.komwe kuli Bingu [wa Mutharika] adziwe kuti anthu amene adasangalala pa imfa yawo azungulira mbale wake ndipo tsiku lililonse amukhzadzulirana, adatero iye. + Mkulu woyanganira achinyamata mchipanicho Louis Ngalande adati nkhaniyi kuti itheretu pafunika kuti DPP ichtitse msonkhano waukulu komwe akasankhe mtsogoleri. + Ngalande amene achinyamata ena mchipanicho amupempha kuti atule pansi udindo wake posankha Chilima wati sakubwerera mmbuyo mpaka ganizo lake litatheka. + Izi zikuchitika kutsatira moto womwe adayatsa Callista Mutharika, mkazi wa Bingu wofuna Chilima adzaime osati mlamu wake amene akuti wakalamba. +",11 +"Parishi ya Kausi Ichita Chaka cha Nkhoswe Yake Wolemba: Sylvester Kasitomu Akhristu a muparish ya kausi mu dayosizi ya mangochi awapempha kuti akhale achikondi monga nkhoswe zawo Anna ndi Joakimu woyera amaonetsa ali pansi pano. +Vicar general wa dayosiziyi bambo Frank Chingale ndi omwe anena izi pambuyo pa mwambo wamisa yokumbukura nkhoswe za parishiyi zomwe ndi Ana ndi Joakimu woyera. +Iwo ati Anna ndi Joackim woyera anali banja la chikondi ndi loopa mulungu kotero akhristu mu parishiyi nawonso akuyenera kuonetsa chikondi pakati pawo. +Monga nkhoswe za parishi yanu zinali zachikondi inunso muonetse chikondi pakati panu pokonda kuthandizana komanso kupephererana. +Mwapadera ndithokoze akhristu nonse amene mwatenga nawo gawo pamwambowu kuti uchitike ena mwaika ndalama ena mapemphero amene ndipempha mulungu odziwa kupereka awonjezere pomwe mwachotsa, anatero bambo Chingale. +Mwazina bambowa anati pamene akkhristu asonkhana pa miyambo ngati iyi zimasonyeza umodzi ndi ubale omwe ulipo pakati pawo. Mpingo wakatolika umakondwererea Anna ndi Joakimu woyera pa 26 july chaka chilichonse lomwe chaka linali lachisanu lapitali ndipo parishiyi yachita chakachi la mulungu pa 28 July 2019. +",13 +"Papa Walimbikitsa Chikondi, Kulemekezana Mbanja Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wati chikondi komanso kulemekezana ndi zofunika mbanja. +Papa Francisco walankhula izi lachisanu pa Misa yomwe anatsogolera ku likulu la Mpingo ku Vatican lomwe ndi tsiku loganizira ma banja pa dziko lonse. +15 May chaka chilichonse ndi tsiku loganizira ma banja pa dziko lonse, International Day of Families. +Mmawu ake pa Misa yomwe anatsogolera pa tsikuli mtchalichi lalingono la Casa Santa Marta, Papa Francisco watsindika kufunika kodzamitsa moyo wa chikondi chenicheni komanso kufunika kolemekezana pofuna kukometsa moyo wa banja. +Lero ndi tsiku lomwe dziko lonse la pansi likuganizira ma banja tiyeni tipempherere ma banja onse kuti akule mchikondi cha Ambuye komanso kuti kulemekezana ndi ufulu zikhazikike mma banja onse pa dziko la pansi, watero Papa Francisco pa Misayo. +Mchaka cha 1993 bungwe la United Nations lidakhazikitsa kuti tsiku la 15 May likhale tsiku loganizira ma banja onse pa dziko la pansi ndi cholinga chofuna kuti maiko ndi mabungwe azitha kuunika momwe ndondomeko zosiyana-siyana zoyendetsera maiko zikhudzira moyo wa banja. +",14 +" Amayi abisa katundu wa K16 000 mu panti Ukathyali wakasololedwe wachitika pamalo omwetsera mafuta a Puma pa Wenela pomwe apolisi adanjata mkulu wina wa ku Zambia pomuganizira kuti amathandizira amayi awiri omwe akuwaganizira kuti amatulutsa katundu mushopu pomubisa kumalo obisika. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Blantyre, Yona Thembachako, watsimikizira Msangulutso za kunjatidwa kwa John Bwanga, yemwe akuti padakalipano amutumiza kwawo chifukwa adalibe zikalata zokwanira zomuyenereza kukhala mdziko muno. + Malinga ndi Thembachako, ogwira ntchito mshopumo amadabwa ndi kusowa kwa katundu wina koma osadziwa yemwe akuba. Iye wati izi zidachititsa ogwira ntchitowo kuti ayangane ma vidiyo kamera mshopumo kuti aone chomwe chimachitika. + Thembachako wati ogwira ntchito pamalopo atayangana pakamera adaona amuna awiri akumatchingira mlonda yemwe ankalondera mushopumo pomwe amayi awiri akulowetsa katundu kumanyazi. + Wogwira ntchito wina mushopumo, yemwe sadafune kutchulidwa, wati tsiku loyamba amayiwo adatenga zitini ziwiri za mkaka wa ana zolemera magalamu 400 nkuulowetsa mmadiresi. + Kenaka akuti adaonanso mayi akutenga chigubu cha mafuta ophikira cholemera malita 5 nkuchipanira kumeneku. + Atatero adatuluka panja pomwe padali galimoto ndi diraiva wawo ndi kuuyatsa, adatero iye. + Iye adati adadabwa ndi momwe amayiwa amalowetsera katunduyo pakati pa miyendoyo. + Amangokweza diresi nkupanira katunduyo. Pomwe amalowetsa zitinizo mmphechepeche zimaoneka koma komwe kumalowa katunduyo ndiye sikumaoneka, adatero kufotokoza zomwe zimachitika pa 27 April. + Akuti katunduyo adali wa ndalama zokwana K15 955. + Atazindikira izi akuti adakhala mochenjera ndipo pa 5 May adabweranso. Patsikulo akuti adatenganso mowa wa Carlsberg Green ndi mpunga wolemera makilogalamu asanu. Sadadziwe kuti la 40 lakwana! Ogwira ntchito mushopumo akuti adali tcheru malinga ndi zomwe adaona pa vidiyopo kuti akaona anthu ofanana ndi amenewo achenjere nawo. + Patsiku logwidwali anthu ogwira mushopumo atamuwona Bwanga adatseka pakhomo ndi kumugwira ndipo adamutengera kupolisi ya Blantyre komwe apolisi adamusunga kuti amufufuze. + Thembachako wati Bwanga adavomereza kuti ndi iyeyo amene akuoneka pavidiyopo koma adati amayi enawo adangokumana nawo momwemo. + Bwanga akuti adatinso mayi mmodziyo ndi nzika ya ku Zambia. + Thembachako akuti Bwanga adakana mlandu woti amathandizira kapena kuba nawo katundu. + Titamufunsitsitsa mpomwe tidapeza kuti alibe ziphaso zokhalira mdziko muno ndiye a ku ofesi ya Immigration adamutumiza kwawo. + Ndi zoonadi kuti akadatithandiza kafukufuku wa amayiwo koma timawona kuti tikungomusunga woti adakana za nkhaniyo, adatero Thembachako, yemwe adati apolisi akufufuza ndi kusakasaka amayiwo ndi mwamuna yemwe akuwoneka pavidiyopo. +",15 +" MEC, MCP yakhutira ndi kalembera Zinthu zasintha. Anthu akulembetsa mwaunyinji mgawo lachiwiri la kalembera wa zisankho zomwe zidzachitike mdziko muno chaka cha mawa. + Mkulu wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah ndi mneneri wa Malawi Congress Party (MCP) Maurice Munthali adati ndi wokhutira ndi mmene anthu akulembetsera mgawoli. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ntchito ya kalembera Izi zikusiyana kwambiri ndi momwe kalembera adayendera mgawo loyamba momwe anthu amabwera mosisitika moti mabungwe ndi chipani chotsutsa boma cha MCP ati sadakhutire ndi momwe adayendera kalembera mgawolo ndipo apempha MEC kuti ibwererenso mmabomawo. + Mgawo loyamba MEC yachititsa kalembera mmaboma a Kasungu, Salima ndi Dedza pamene mgawo lachiwiri bungweli likulembetsa anthu ku Mchinji, Nkhotakota, Dowa ndi Ntchisi. + Ansah adati MEC ndi yokhutira ndi momwe anthu akubwerera moti mmalo ena anthu odzalembetsa akumafika 700. + Kungoyambira tsiku loyamba pa July 13 2018 anthu akubwera mwaunyinji kudzalembetsa moti mmalo ena chiwerengero cha anthu odzalembetsa chikumafika 700 patsiku, iye adatero. + Naye mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust, Ollen Mwalubunju, watsimikiza zoti zinthu zasintha kwambiri mgawo lachiwiri la kalembera wa zisankho. + Mwalubunju adati ngati zinthu si zisintha, 40 peresenti ya anthu ikhala atalembetsa pofika dzulo. + Zinthu zikapitirira chonchi, ndiye kuti zolinga za demokalase zomwe nkupereka mphamvu kwa anthu, zikwaniritsidwa, adatero Mwalubunju. + Ngakhale anthu akupita kukalembetsa mwaunyinji, ena akubwerera osalembetsa kaamba koti zipangizo za MEC zikumaonongeka, komanso malo ena akumatsegulidwa mochedwa. + Ngakhale zinthu zikuyenda bwino, koma nkhawa yathu ili pa makina a MEC omwe sakukhalira kuwonongeka, adatero Munthali. + Anthu omwe adapita kwa Tembwe ndi Chiwaula ku Mchinji tsiku lotsegulira gawo lachiwiri la kalembera wa zisankho, adabwerera kaamba koti makina a bungwe loyendetsa zisankho adali atawonongeka. + Mdera la mfumu Dambe mboma lomwelo makamaka kwa Chankhanga, Nthema, Gaandali ndi Kapiri kudali mizere italiitali ya anthu ofuna kulembetsa, koma zinthu zimayenda mwapangonopangono kaamba koti makina a MEC amangowonongeka. + Ansah adati bungwe lake latumiza akatswiri mmaboma onse okhudzidwa kuti azikakonza msanga makina awo akawonongeka. + Patsiku lotsegulira kalembera ku Dowa, anthu 210 ndiwo adalembetsa kwa Kainja, 48 kwa Pheleni, 176 kwa Mbido, 126 kwa Tsache, 64 kwa Msaderera ndipo pa sukulu ya pulayimale ya Mvera padalembetsa anthu 64. + James Gama, yemwe akuyanganira zisankho mbomalo, adati ntchito imayenda pangonopangono chifukwa amagwiritsa ntchito makina woyendera dzuwa womwe samagwira bwino ntchito chifukwa cha nyengo. + Pano tikugwiritsa ntchito ma generator ndipo zinthu zasintha moti tikukhulupirira kuti tikwanitsa chiwerengero chomwe tikuyembekezera, adatero Gama. + Nako ku Ntchisi ndi Nkhotakota vuto lidali kusagwira bwino ntchito kwa makina. + Malingana Summy Nganjo, yemwe akuyanganira kalembera ku Ntchisi, MEC ikuyembekezera kulembetsa anthu 163 352 ndipo anthu ambiri akubwera kudzalembetsa. + Nyakwawa Galeta ya ku Nkhotakota idati mmadera ena ogwira ntchito a MEC ndi achitetezo akumabwera mochedwa. + Mlembi wamkulu wa MCP, Eisenhower Mkaka, adati momwe zinthu zikhalira mgawo, zawonetsa poyenera kuti MEC idalephera ntchito mgawo loyamba. + Naye mneneri wa UDF, Ken Ndanga, adati MEC isapupulume kufalitsa malipoti abodza isadafufuze mokwanira chomwe chidachitika mgawo loyamba lakalembera. +",11 +"Boma la Zomba Lati Lakonzekera Kuchititsa Chisankho Bwanamkubwa wa boma la Zomba, Smart Gwedemula wati boma la Zomba lakonzeka kuchititsa chisankho cha President lachiwiri likudzali. +Gwedemula wauza Radio Maria kuti padakalipano a zipani za ndale awona kale kuchuluka kwa mapepala ovotera omwe afika mbomalo. +Iwo atsimikizira anthu onse a mboma la Zomba kuti zipangizo zovoterazi zifika mmadera onse mu nthawi yake ngakhale madera ena omwe ndi ovuta mayendedwe. +Ngati zomba district council tili okonzeka kuchititsa chisankho chimenechi ndipo tinaphuzitsidwa bwino ndipo tiyendetsa chisankho chimenechi mwandondomeko, anatero Gwedemula. +Iwo ati malo onse ovuta kufika, akafika cholinga choti onse okhala kumeneko apatsidwe mwayi wosankha mtsogoleri wa kumtima kwawo. +Pothilirapo ndemanga phungu wa dera la Zomba Changalume John Chikalimba yemwenso ndi mkulu wa zofufuza-fufuza mu chipani cha Peoples, wati pakali pano anthu madera onse a mboma la Zomba akonzeka kuti akaponye voti patsikuli. +",11 +" Obindikira mnyumba azengedwa mlandu Bwalo la milandu la majisitireti mumzinda wa Blantyre lakhazikitsa Lachitatu, 25 May, ngati tsiku lomwe lidzapereke chigamulo kwa banja lina lomwe lakhala likudzitsekera mnyumba kwa zaka zitatu ndi kulephera kupereka chisamaliro kwa ana awo anayi. + Govt to review Genset deal MBC clean up APM aide nabbed Mneneri wa nthambi ya zachilungamo, Mlenga Mvula watsimikizira Msangulutso za nkhaniyi. + Mvula adati nkhaniyi idalowa mkhoti pa 13 May ndipo banjali lidakana mlandu wolephera kupereka chithandizo kwa ana awo ndipo ilowanso mbwaloli Lachitatu likubwerali pa 25 May pamene oimira boma abweretse mboni. + Adakana kulakwa: Banda ndi mkazi wake akuyankha mlandu wosapereka chisamaliro kwa ana awo Sabata yatha, apolisi ya Manase mumzinda wa Blantyre adanjata Peterson Mtchini Banda, wa zaka 44, ndi mkazi wake Agnes, wa zaka 41, atatsinidwa khuku kuti banjali silimatuluka mnyumba kuyambira mchaka cha 2013. + Mneneri wa polisi ya Blantyre, Elizabeth Divala, wauza Msangulutso kuti banjali lidauza apolisiwo kuti adachita izi ngati njira imodzi yodzitetezera kwa anthu achipongwe. + Akuti tsiku lina bamboyo adafuna kuchitidwa chipongwe ndi anthu ndipo nkhaniyo ati adafotokozera apolisi koma sadaione mutu wake. Kuyambira panthawiyo, iye akuti adauza banja lake kuti asadzatulukenso mnyumbamo, adatero Divala. + Moti tsiku lomwe tidapita kunyumbako, tidagogoda koma sadatsegule, tidagwiritsira ntchito mphamvu pothyola chitseko ndipo tidawapeza makolowo komanso ana awo anayi akuoneka ofooka. Tidawatengera kupolisi kuti tidzawafunse. + Banjali akuti lidauza apolisiwo kuti akafuna ndiwo, kapena chakudya chilichonse, amaitana anthu amene ayandikana nawo ndi kuwapatsira ndalama kuti akawagulire zomwe akufunazo. + Nyumbayo ili kumpanda, ndiye chilichonse chili kumpandako monga chimbudzi komanso madzi. Ali ndi nyumba za lendi zomwe amatolera ndalama pakutha pa mwezi, ndalama amazipeza motero ndipo ati amadzawapatsira ndalamazo pazenera, adatero Divala. + Chidzitsekerereni mnyumbamo mu 2013, ana a banjali akuti adawaleketsa sukulu. Pano mwana woyamba ndi wa zaka 17, wina 14, wina 11 ndi wina wa zaka zinayi. + Divala wati makolowo adawatsegulira mlandu wolephera kupereka chithandizo kwa ana awo. +",13 +" Mpira uthera panjira wosewera atamwalira Anthu akugwedeza mitu yopanda nyanga ku Choma, mboma la Mzimba kaamba ka imfa ya mnyamata wa Fomu 3 pasukulu ya sekondale ya Choma yemwe adaombana ndi goloboyi poti agwire mpira ali paliwiro lamtondo wadooka lokagoletsa Lachisanu lapitalo. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Patsikulo, timu yomwe Isaac Phiri wa zaka 20 amasewera imapimana mphamvu ndi timu yachisodzera ya pa sukulupo. + Isaac amasewera ngati wogoletsa. + Malinga ndi mphunzitsi wamkulu pasukulupa, Mathews Phiri, yemwenso amaonerera masewerowa, izi zidachitika patangodutsa mphindi 30 mpira utayamba ndipo udathera pomwepo. + Phiri adati Isaac yemwe adali wogoletsa wodalilika, adanyamuka ndi mpira mwa liwiro zedi ndi cholinga chokagoletsa, ndipo atayandikira golo kuti aponyere muukonde naye goli adachoka pagolo ndi kuombana ndi mnyamatayo. + Iye adati, apa onse adagwa pansi ndipo Isaac adayamba kudzigwiragwira moonetsa kuti ali muululu woopsa. + Malinga ndi lipoti la chipatala, kuombana pachifuwa kwa awiriwo kudachititsa avulazane mkati komanso womwalirayo apweteke kapamba. + Tidathamangira konko, pamodzi ndi achipatala omwe adalinso pompo, tidayesa kumutsira madzi koma sizidathandize ndipo apa mpamene tidathamangira naye kuchipatala chomwe chilli pafupi ndi bwalo lamaseweroli komwe atamupima adatiuza kuti watisiya, Phiri adatero. + Iye adati masewerawo, omwe amakonzekera masewero akulu ndi timu ya sukulu ya pulaiveti ya Chiume adathera pomwepo ndipo aliyense sakumvetsa zomwe zidachitikazo. + Koma Levi Mwale yemwe ndi dokotala wa timu ya dziko lino adati ngozi zotere sizichitikachitika. + Mwale adati nthawi zambiri zikachitika zimakhala kuti wosewera mpira wameza lilime lomwe limatseka modutsa mpweya. + Iye adati vuto ndi loti masewera ambiri mdziko muno, amaseweredwa opanda akatswiri a za udotolo. + Anthu sadziwa kuti munthu akavulala akusewera mpira, amasamalidwa bwanji, Mwale adatero. + Iye adati ndi zachisoni kuti imfa zoterozi zimagwa chifukwa chosowa chidziwitso. + Tikufunika tiphunzitsidwe kasamalidwe ka ovulala mu mpira, kuyambira matimu a supa ligi, maligi aangono komanso a mmadera ndi msukulu, Mwale adatero. + Polankhulapo mneneri wa apolisi mchigawo cha kumpoto Maurice Chapola adati Issac yemwe amachokera mmudzi mwa Msafiri T/A Mtwalo mbomalo adamwalira kaamba kovulalira mkati. Iye adati adavumbulutsa izi ndi a chipatala cha Mzuzu. + Chapola adatsimikiza kuti Isaac adakomoka ataombana ndi goli ndipo achipatala cha Choma ndiwo adalengeza za imfa yake ndi kutumiza thupi lake ku chipatala cha Mzuzu kukafufuza chidadzetsa imfayi. +",16 +" Kamuleni ndi Polisi Palibe Tsikulo nkhani idavuta ndi ya anyamata ena aja adabutsa bwalo la milandu mtaunimu. Adaganiza bwanji anthuwa? Uku nkugenda kupolisi wamkulu fodya ali mthumba la kumbuyo. + Kukhala mavuto, anthu tsopano aziyenda kuchoka ku Chirimba, Ndirande ndi Chilomoni kupita kuja koonekera ku Chichiri. Yalakwa, adatero Abiti Patuma. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Apatu khoswe ali pamkhate koma ndani angaope kuswa mkhate lero? Ndani lero angaloze kuti uwo ndi mkhate? Kuuswa basi! Tisachedwe ndi anyamata olangika ndi zotsatira za mkalabongo. Nkhani idazunguza anthu pa Wenela ndi ya zochitika ku Polisi Palibe, gulu la masiye. + Ndikumva kuti nkhani ikuvuta ndi ya kulimbana pankhani ya Kamuleni Kaduwa komanso Udadili Issa omwe anenetsa kuti libolonje lalowa ku Polisi Palibe kuchokera ku Dizilo Petulo Palibe, adatero Gervazzio, wapamalopo. + Abodza amenewo. Kodi onsewo ndimayesa adali ndi zipani zawo lero akudzetsa mpungwepungwe kwa Adona Hilida. Kodi Kaduwa suja adazunguza Mpando Wamkulu ndi PDM yake? Nanga uyu Issa sankati tonse ndi Amaravi? adayankha Abiti Patuma. + Abale anzanga, musandifunse kuti ankatanthauza chiyani chifukwa sindikuuzani. Ndipo mukadziwa mukufuna mutani? Nthawi yomweyo, Gervazzio adaika nyimbo ya San B komanso Nepman, inde nyimbo imene adaimba uja mnyamata wa ku Chileka. + .Amatigoneka kukada Amatidzutsa kukacha Amatidyetsa tikamva njala Ili ndi pemphero limene lalowerera paliponse pamene kulira ndi njala kwafika pena. Kugona kumsika kuti ugule chimanga, kuotha dzuwa komweko mpaka nthawi ya nkhomaliro opanda chakudya. + Ndimakumbuka tsiku lina titamupanikiza Moya Pete kuti atifotokozere bwino za mmene abweretsere chakudya pano pa Wenela. Mmalo mwake adati: Amalawi tikutukwanana kwambiri pa Facebook. Tikuphana osati masewera kwambiri. + Koma ine ndikuona ngati kuimbanso nyimbo za Michael Jackson kapena Bob Marley nkutaya nthawi. Adaziimba bwino kale, adatero Gervazzio. + Palibe uyo adayankhira nkhani imeneyo chifukwatu maimbidwe ali mmagulu. + Tili pa Wenela chomwecho adatulukira Fula Kasamba. Tonse chimwemwe chidadzala tsaya. Koma abale, kuphwetsana madzi kotereku bwanji? Walakwanji munthu? Ndatulukamo motenthamo. Iwe Tade usandilankhule, sindikufunanso kupalamula. Zoona tsiku ngakhale limodzi osabwera kudzandiona? Ufiti wako udafika pamenepo? adafunsa Fula. +",7 +"Papa Wati Akhristu Akhale Okhulupirika Papa Francisko wati anthu akuyenera kukhala okhulupirika ndi odalira Mulungu nthawi zonse. +Papa Francisko Papa Francisco walankhula izi lachiwiri pa Misa yomwe anatsogolera ku likulu la mpingo ku Vatican. +Iye wati kawirikawiri pamene zinthu zikuyenda bwino anthu amayamba kuyiwala Mulungu ndi kumazidalira okha. +Pamenepa iye wati ndi kofunika kuti anthu azikhala okhulupirika kwa Mulungu ndi kuyika chikhulupiriro chawo mwa Mulungu monga Maria wa ku Magadala. +",13 +" HRDC ikufunabe zionetsero mzipata Gulu lomwe likutsogolera zionetsero zofuna kuchotsa wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) laimitsa zionetsero kuti lipeze njira yochotsera chiletso chotseka mabwalo a ndenge ndi zipata za dziko lino. + Bungwe loona za misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) adakamangala kuti zionetsero zisachitike kumalowo chifukwa zisokoneza ndalama zimene limatolera. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Bungwelo lidaimitsa zionetsero zomwe zimayenera kufika dzulo zionetserozo zitangochitika Lachitatu lokha pomwe zidakoka makamu a anthu mmaboma a Karonga, Mzuzu, Zomba, Lilongwe ndi Blantyre. + Wachiwiri kwa wapampando wa bugwelo Gift Trapence Lachinayi adati zionetsero sizipitirira Lachinayi ndi Lachisanu ngati momwe chikonzekero chidalili kuti akuluakulu a bungwelo akumane ndi owayimilira pa mlandu. + Taimitsa zionetsero pofuna kupeza njira yochotsera chiletso chokatseka mmabwalo a ndenge ndi zipata zotulukira mdziko lino. Khumbo ilili tikadali nalo chifukwa mwina ndi njira yokhayo yomwe angamvere pempho lathu, adatero Trapence. + Koma ngakhale HRDC idati zionetserozo ziime, anthu ena ku Mzuzu Lachinayi adapitabe pamsewu kukachita zionetsero zofuna kuti Ansah atule pansi udindo. + Katswiri pa ndale George Phiri adati akugwirizana ndi zomwe HRDC yapanga poimitsa zionetserozo kuti ligundane mitu mozama ndi owaimira pamilandu kuti apeze njira yomwe ingatsegule pakamwa pa akuluakulu a boma. + Anthu akapereka kalata ya madandaulo, amayembekezera kuti ayankhidwa ndi ofesi yomwe ayilembera kalatayo, ndiye ngati akungopereka kalata koma osayankhidwa, ndiye kuti pena pake pali vuto. Tsono alekeni afufuze pali vutopo, adatero Phiri. +",11 +"Papa Wadandaula ndi Kusowa kwa Chilungamo Mmayiko Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati kusowa kwa chilungamo ndikomwe kukuchititsa anthu ambiri adzikudzidwa ndi imfa pochokera ku mayiko awo ndi kupita ku maiko ena. +Papa pa umodzi mwa maulendo ake oyendera mayiko Papa Francisko walankhula izi lachinayi kulikulu la mpingo-wu ku Vatican pamene amalandira gulu la anthu othawa kwao lochokera pa chilumba cha Lesbos mdziko la Greece. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican. +Iye wati ndikusowa kwa chilungamo kumene kukukamiza anthu ambiri kuthawa mmaiko awo kupita maiko ena pofuna kukapeza bata ndi mtendere. +Pamenepa Papa Francisko watsimikizira anthu-wo kuti mpingo wa katolika upitiriza kupereka chisamaliro kwa anthu onse otha-wa kwawo. +",14 +"Anjatidwa Kamba Koba Mankhwala pa Chipatala cha Thyolo Apolisi ku Thyolo amanga amuna awiri powaganizira kuti anaba mankhwala a ndalama zokwana 500 thousand kwacha pa chipatala cha boma la Thyolo. +Awiriwa ndi a George Nankhuni ogwira ntchito ku chipinda chosungira ndi kugawira mankhwala ndipo wina ndi mlonda. +Mneneri wa apolisi ku Thyolo, Amosi Tiwone wati awiriwa amangidwa lachiwiri kutsatira kafukufuku yemwe anachitika pa chipatalacho. +Iye wati oganiziridwawa awatengera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe milandu ya kuba pa malo a ntchito komanso kupezeka ndi mankhwala opanda chilolezo. +",7 +" Mavuto osakata pa Wenela Tidakhala malo aja timakonda pa Wenela ndipo zidaonekeratu kuti zochita zikusowa. Kodi nkumachitanji pomwe zinthu zikukwera mtengo tsiku ndi tsiku ngati palibe womanga mabuleki? Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Musandiuze za Moya Pete chifukwa momwe ndidakuuzirani muja, palibe icho achita. Dziko lili pa auto pilot basi. + Nanga inu! Kusakaza nkhalango kwagundikaku mungati zinthu zikuyenda? Kodi nkhalango ndidaisiya kwathu kwa Kanduku lero ndingakaipeze pamene ootcha makala sakugona koma kusaka njira zothera mitengo kumeneko? Pamene nkhalango zikutha, Moya Pete akungoti asiya kugwirizana ndi awo ampalamatabwa, kuwaletsa kudula kesha ndi msetanyani? Nanga abale ake andale amene amatulutsa nkhuni, matabwa komanso mbande za mitengo akuwasiya bwanji? Aliyense akudziwa kuti Mowe Pati ali mgulumo. Mulinso uyu Mulibe wa galimoto zake. Nanga uja mbale wathu wosowa ya lendi mtauni Shati Choyamba wa ku Lower Shire! Onse akuwadziwa. + Nanganso bwanji osauza abale ake a Eisssshcom, inde anyamata oonetsetsa kuti kuzima kwa magetsi kukufalikira bwino, inde kampani yogulitsa mdima nawonso amakhapa mitengo ati akonze mapolo! Kodi mdima amagulitsa? Mukadzapeza munthu akugulitsa mdima, dziwani satana ali bwino. Inde, Dyabulosi akaona munthu wotere amavula chipewa nkugwada ndi kunena kuti: Dutsani amfumu. Inu ndi munthu wamkulu zedi, thambo la kumwamba ndi dziko lapansi zonse zilambira ufumu wanu. Kuguwa kwanu palibe angayerekeze kufikako. + Abale anzanga, nanga tsiku ndi tsiku, munthu wopuma, wa umunthu wake, angamasangalale kunena kuti lero ndizimitsa kuwala kuti akuba atambalale? Munthu wokhala ndi umoyo wauzimu nkumanyadira kuti timakanda tifera kumagetsi chifukwa cholephera ntchito? Zamanyazi. + Chilichonse sichikuyenda. + Nanga Adona Hilida ndiye ali kuti? Kuthawa pano pa Wenela mopanda mantha, mayi uyu ali ndi mafunso akuti ayankhe. + Nanga mwaiwala kuti iyeyo ndiye adanena kuti: Amene adaombera Yomphwi ndikuwadziwa. Ndipo awo adasolola makobidi nkundigawira ndi zawo. Wakudya nawo alibe mlandu. + Zoti ameneyu ndiye ankatsogolera tonse ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela? Kodi iyeyo ndi Abiti Patuma bola ndani? Ndipo pomwe ndikukuuzani nkhaniyi, mbale wake Oswin Pitapo akuyembekezera kulandira udotolo wake. Ndangomva kale kuti atatsindika kuti palibe katakwe ngati iye posolola, sukulu yaukachenjede kuja kwa Chikanda ku Zomba Lachisanu imayembekezera kumupatsa udotolo wovuta. Ati iye ndi Doctor of Philosophy in Colossal Tax Payer Pilferage of Extraordinary Proportions. Dotolo wamkulu. Chifwamba. Tsinzinantole wamkulu. Wamtali zala wamkulu kuposa onse. Nyapala. Wandende. Kaidi Nanga ndatukwana? A Ndirande iyi! Machinjiri iyo! Lilongwe kwerani ka Starlet aka mukafika! ndidakuwa. +",15 +" Aphangirana ufa Mwambo wa mapemphero Achisilamu otchedwa dawa udasokonekera kwa Chitulu kwa T/A Mwambo mboma la Zomba Loweruka pa 2 April pomwe khwimbi la anthu lidakhamukira kumeneko kukalimbirana ufa womwe amati agawe mwambowo ukatha. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kuderalo kudafika bungwe la Eid Charitable la mdziko la Qatar lomwe limachititsa mapemphero Achisilamu ndipo pakutha pa mapemphero amayenera kugawa ufa kwa Asilamu ndi anthu ena ovutika. + Asanayambe kugawa chakudyacho amayamba ndi mapemphero a dawa ndi kupereka mwayi kwa ofuna kulowa Chisilamu kuti atha kutero povomereza kuti Muhammad ndiye mneneri wa Mulungu womaliza. + Mapemphero akupita kumapeto, Asilamuwa adapempha anthu amene ankafuna kulowa Chisilamu kuti anene pemphero loti Ashihadu anla ilaha llah. Wa a shadu anna Muhammad u rrasulu llah (Ndikuikira umboni kuti pali Mulungu mmodzi yekha. Ndipo ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi mtumiki wake womaliza). + Khwimbi la anthu kudikira kuti alandire kangachepe Apa mpomwe gulu la anthu ambiri, ena mwa iwo Akhrisitu, adanena nawo pempheroli ndi kuvomereza kuti alowa Chisilamu, adatero Shehe Mustapha Saidi, yemwe amayanganira mzikiti wa Chitulu. + Mwambo wa dawa uli mkati, galimoto yomwe idanyamula ufawo idatulukira, zomwe zidayambitsa kuti khwimbi la anthu likhamukireko ndipo padali ali nmwana agwiritse pomwe amati ayambe kugawa ufawo. + Mwina poona kuti suwakwana onse, zidavuta kuti akhale pamzere ndipo ena adayamba kukwera okha pamwamba pa loleyo kukadzithandiza okha potenga matumba a ufa. Ena amatenga awiri ena atatu amene, olemera makilogalamu 25 limodzi. + Martin Umi, wa mmudzi mwa Chitulo, akuti iye ndi Mkhristu koma adalumbira nawo ponena pemphero la Chisilamulo kuti alandire nawo ufa. + Kunena zoona ndidavomereza kuti ndalowa Chisilamu koma ndimangofuna kuti ndilandire nawo ufawo chifukwa cha njala pakhomo panga. Komabe mwina mtsogolomu ndilowadi Chisilamu, nanga si anthu amene akutithandiza, adatero Umi. + Iye adati adakwanitsa kutenga matumba awiri, koma adavulala atapondedwa pamene amathawitsa ufawo. + Mfumu Chitulu idati kudera lake komanso madera ena kuli njala yadzaoneni chifukwa mvula idasiya kugwa mu January kupangitsa kuti chimanga chipserere. + Momwe njala yavutira kuno, nkovuta kuti wina angatsale pakhomo atamva kuti kwina kukubwera chakudya. Si zodabwitsa kuona kuti anthu adaphangirana ufawo, idatero mfumuyi, yomwe mmudzi mwake muli anthu 1 470, omwe ndi mabanja 240. + Shehe Saidi adati chipwirikiticho chidakhumudwitsa mamembala awo amene sadalandireko ufawo. + Zachisoni kuti mamembala athu ambiri sadalandire nawo ufawo, zomwe zachititsa kuti ena asiye kutumiza ana awo kumadrasa [sukulu ya ana ophunzira Chisilamu], adatero Saidi, yemwe adati akuyembezabe kuona ngati omwe amati alowa Chisilamu patsiku logawa ufalo abwere kumzikiti kudzapemphera. + Si bwino kunamizira kulowa mpingo kaamba koti ukufuna chithandizo cha kuthupi koma uzilowa mpingo kaamba kofuna kukapulumuka kumwamba, adaonjezera Shehe Saidi, pouza Msangulutso Lachisanu lapitali. + Lero Lachisanu olo mmodzi mwa omwe adati alowa Chisilamu patsikulo palibe amene wabwera kumapemphero. Amatero? Bungwe la Eid Charitable lidabweretsa ufa mdziko muno womwe udagawidwa mboma la Zomba, Machinga ndi Mangochi. + Mkulu wa gululi, Ali Muhammad Al-saaq, adati adauzidwa ndi bungwe la Zamzam Foundation la ku Malawi za mavuto amene Amalawi akukumana nawo kaamba ka njala. + Titamva za mavutowa, tidabwera ndi ufa kuti ovutika athandizike. Tipemphenso anthu ena kuti athandize dziko lino. Ifeyo tikabwerera tikasakanso thandizo lina ndipo tipitiriza kuthandiza dziko lino, adatero Al-saaq. +",15 +" Anatchezera ANATCHEREZA Akundikakamira Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi mkazi yemwe ndili naye mwana mmodzi. Vuto lake ndi limodzi: amakhalira kunyoza makolo ndi abale anga. Amati banja sakulifuna koma ndikati amange zake, amakakamira. Ndichitenji? H, Blantyre. + Zikomo H, Kodi banja lanu mudamangitsa kuti? Kodi mudangogwiriziza kwa ankhoswe? Ngati ndi choncho bwanji osakatula nkhawazo kumeneko? Ngati mudamangitsa kumpingo, mukhonzanso kupita uko akakuthandizeni. + Banjatu sakakamiza ndipo apapa zikuonetseratu kuti mkazi wanuyo ali ndi chibwana komanso musakaike, ameneyo ali ndi wina amene amamulimbitsa mtima. Nkutheka kuti winayonso ali pabanja ndipo amamunamiza kuti adzasiya mkazi wake ndi kutengana ndi wanuyo. + Izi si nkhambakamwa, ndipo mumufufuze bwino mayendedwe ake. Samalani naye mudzalirira kuutsi atakubweretserani kwayauotche. + Akuti ndidzamukwatire iyeyo basi Zikomo agogo, Bambo ndi mayi anga adasiyana ukwati ndipo adakwatirana ndi mkazi wina yemwe analinso ndi ana ena. Mmodzi mwa anawo ndi wamkazi ndipo ndamulera mpaka kusukulu ya ukachenjede kumene akuphunzira panopa. + Vuto langa nali, iyeyo akuti sakufuna adzamve zoti ndakwatira mkazi wina chifukwa amandikonda kwambiri. Iye adati adzamuikira chiphe mkazi amene ndingadzakwatire. + Iyeyo akuti ndi bunthu ndipo akuti sadzalola mwamuna aliyense kudzamuyamba koma ine ndekha. Iyeyotu amati palibe chibale pakati pa ine ndi iyeyo. Ndichitenji? TD, Lilongwe. + TD Monga ndanena, banja sakakamiza. Chikondi chili ngati fupa, ukakakamiza, mphika umasweka. Apatu mlongo wanuyo ayenera kuti palibe angakakamize wina kukonda mnzake, mapeto ake ndi ngozi. + Chomwe muyenera kumuuza nchakuti, si kuti munthu akakuchitira zabwino ndiye kuti nawenso udzikakamize kubwezera zabwino, kuphatikiza zimene zili zosadziwika bwino. Tamvapo za amayi ena amene apatsidwa mimba komanso matenda ndi abambo ena amene amawathokoza powapatsa ntchito. + Mumuuzitse kuti pamene mumamuthandiza, si kuti mumayembekezera kuti adzabwenza china chake. +",12 +"Bungwe la IPEQI Liphunzitsa Adindo a za Chitukuko Kumidzi Bungwe la Institute for Participatory Engagement and Quality Improvement (IPEQI) lati liphunzitsa adindo omwe amayanganira ntchito za chitukuko ku madera a kumidzi mboma la Zomba za momwe angalimbikitsire chitukuko mmadera awo. +Mlangizi wamkulu wa bungweli Dr. Zikani Kaunda ndi omwe anena izi lachiwiri mboma la Zomba pomwe bungwe lawo limakumana ndi alangizi a zachitukuko ku madera akumidzi komanso akuluakulu a khonsolo ya boma la Zomba. +Iwo ati ali ndi chikhulupiliro kuti pakutha pa maphunziro amenewa adindowa adziwa momwe ndalama zogwilira ntchito za chitukuko zikuyenera kuyendera. +Mmawu ake mkulu owona za chitukuko mmadera akumidzi mboma la Zomba mayi Flora Mvuta ati ali ndi chikhulupiliro kuti ntchito yophunzitsa adindowa ikatha, zinthu zisintha ndipo adindowa azitha kugwira ntchito yawo bwino ponena kuti chiwasankhire sanachitepo maphunziro ena aliwonse okhudza ntchito yawo. +",14 +" Ulimi wa tomato, kabichi ndi nyemba wakolera Alimi abebetsa ulimi wa tomato, kabitchi komanso nyemba mboma la Ntcheu pamene ulimi wa mmadimba wachiwiri wayambika. + Boma la Ntcheu, lomwe lachita malire ndi Dedza komanso Balaka, lili ndi anthu pafupifupi 700 000 tsopano malinga ndi chiwerengero cha anthu cha mu 2010. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ambiri mwa anthuwa ndi alimi ndipo ulimi wa nyemba, tomato, mbatata ya kachewere ndi kholowa, chimanga komanso kabitchi ndi mbewu zina ndizo amadalira kwambiri. + Madera monga Tsangano, Mphepozinayi, Mozambique border, Kampepuza, Nsipe, Mulangeni, Lizulu, ndi Kasinje ndiwo amene amatchuka kwambiri polima ndi kugulitsa mbewuzi. + Monga akunenera mlangizi wamkulu mbomali, Annily Msukwa, chaka chinonso ulimiwu wabonga ndipo pafupifupi khomo lililonse latangwanika. + Panopa alimi akugulitsa komanso kukonza minda yawo kuti abzalemo mbewu zina, adatero Msukwa polankhula ndi Uchikumbe Lachiwiri msabatayi. + Iye akuti ulimi wa kabitchi, tomato komanso nyemba panopa wafika pachimake. Tili otangwanika kulangiza alimi panopa kuti ayambiretu kugwiragwira kudimba pamene ntchito yogulitsa zokolola ili mkati. + Alimi ambiri ayamba kukumba zitsime chifukwa posakhalitsapa mitsinje imakhala yayamba kuphwa ndiye madzi amasowa. Ndiye ngati madzi aphwa, ulimi wamthirira umavuta nchifukwa chake ayambiratu kukumba zitsime, adatero Msukwa. + Kupatula kukumba zitsime, Msukwa akuti alimiwa akuwalangizanso kuti ayambiretu kupanga manyowa kuti zigwirane ndi mbewu zomwe akufuna alime. + Malinga ndi mlangiziyu, chaka chino ulimi wa tomato komanso kabitchi ndi nyemba wachita bwino kusiyanako ndi chaka chatha. + Panopa alimi akukolola mbewu zomwe adabzala kumapeto a mvula. Ndikulankhulamu alimiwa ayamba kale kulima zina za mthiriranso ndipo podzakolola zimenezi mvula idzakhalanso yayandikira. Kunotu kulibe nthawi yopuma, adatsindika. +",4 +"Papa Wasankha Mamembala Atsopano a Sukulu ya Ukachenjede ya Pontifica Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wasankha mamembala atsopano a sukulu ya ukachenjede ya Pontifical Academy of Social Sciences. +Malinga ndi malipoti a Vatican Radio, Papa lachisanu wasankha mamembala atatu a sukulu ya ukachenjede yomwe ili pansi pa ofesi ya Papa yotchedwa Pontifical Academy of Social Sciences. +Sukuluyi imawunikira pa maphunzitso a mpingo wa katolika pa magawo osiyana-siyana a moyo wa thupi wa anthu. +Papa Francisco wasankha Professor Pedro Morand Court kuchokera mdziko la Chile; Professor Mario Draghi kuchokera mdziko la Italy ndi Professor Kokunre Eghafona mayi wa ku Nigeria. +Mwazina Professor Morande Court ali ndi degree ya Sociology kuchokera ku sukulu ya ukachenjede ya Pontifical Catholic mdziko la Chile komanso doctorate ya Sociology kuchokera ku sukulu ya ukachenjede ya Friedrich-Alexander mdziko la Germany. +Pamene mwa zina Professor Mario Draghi ali ndi degree ya Economic Policy kuchokera ku sukulu ya ukachenjede ya Sapienza ku Rome. Professor Draghi analinso Executive Director wa World Bank. +Ndipo mayi Professor Kokunre Eghafona wagwirapo ntchito ndi bungwe la United Nations. +Sukulu ya Pontifical Academy of Social Sciences anaikhazikitsa ndi Papa Yohane Paulo Wachiwiri Woyera pa 1 January 1994 ndipo imaunikira maphunzitso a Mpingo wa Katolika otchedwa Social Teaching of the Catholic Church pa magawo a nkhani za chuma, chikhalidwe, za malamulo komanso ndale. +",3 +"Three Arrested In 7 Million Fake Land Deals Police in Lilongwe have arrested three men for fraudulently selling other peoples plots of land. +The suspects, who include a deposed Group Village Head, allegedly swindled three people out of K 7. 1 million in their latest fake land deals. +They are said to have been previously arrested on similar charges and they are on court bail. +The suspectsBlessings Chiipila, Manase Chipala and deposed Group Village Head Chapata, real name Frank Kachitsekoare said to have been selling fake lands to unsuspecting buyers. +The three used to pose as agent, land owner and group village head in their scam in Kaphiri, Six Miles, By-Pass and Kalumba areas. +The latest fraud, however, came to light when original landowners showed up to lay claim on the same portions of land. +The duped buyers reported to Chitsime Police Unit, leading to the arrest of the suspects on Thursday. They have since been charged with fraud other than false pretence contrary to Section 319 of the Penal code. +The Section says any person who by deceit or other fraudulent means obtains property from any person shall be guilty of an offence and shall be liable to imprisonment for seven years. The suspects will be taken to court soon to answer their relevant charge. +Chiipila, 43, is from Kalumba Village, Kachitseko, 39, comes from Chapata Village, and Chipala, 32, hails from Mlewa Village all under Traditional Authority Kalumba in Lilongwe. +Meanwhile, police are calling on any other people who may have fallen victims to the scam to report to the police. +",7 +" Kusowa kwa madzi kusokoneza zambiri ku Lilongwe Chidziwitso cha Lilongwe Water Board (LWB), bungwe lopopa ndi kugawa madzi mumzinda wa Lilongwe, choti madzi akhala akuvuta kufikira dzinja chatsimikiza kuti ntchito zambiri, makamaka za umoyo, zisokonekera mumzindawu, womwe ndi likulu la dziko la Malawi. + LWB idalengeza sabata ziwiri zapitazo kuti iyamba kugawa madzi mosinira potengera mlingo wa madzi womwe kampaniyi ili nawo mmadamu ake awiri a Kamuzu 1 ndi 2. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Bungweli lidati pomwe madera ena azilandira madzi mumzindawu, kwina kuzikhala kopanda madzi ndipo izi zipitirira mpakana mvula ya chaka chamawa idzabwere. + Kuvuta kwa mvula kwachititsa kuti madzi achepe modetsa nkhawa mmadamu awiri a Kamuzu 1 ndi 2 omwe timasungiramo madzi. Madzi omwe alipo panopa sangapose theka la madzi omwe timafuna kuti tikwaniritse ntchito yathu, chidatero chikalata cha bungweli. + Madamuwa alibe madzi okwanira kaamba koti mvula sidagwe bwino komanso mitengo yomwe imathandiza kusunga madzi idatha mmphepete mwa mtsinje wa Lilongwe. + Timadalira madzi ochokera mumtsinje wa Lilongwe womwe umatsira mmadamu athu. Mtsinjewu umachokera mnkhalango ya Dzalanyama koma poti mitengo idatha mnkhalangomu, mtsinjewu uli pambalambanda ndiye madzi sachedwa kuuma, chidatero chikalatachi. + Mneneri wa chipatala chachikulu mumzindawu cha Kamuzu Central Hospital (KCH), Mable Chinkhata adati ngakhale kuti madziwo sadayambe kuvuta pachipatalachi, ali ndi nkhawa kuti zidzatha bwanji madzi akadzayamba kuvuta chifukwa ntchito zambiri pachipatalachi zidzasokonekera Ntchito zaumoyo, makamaka pachipatala, zimafuna madzi kwambiri. Mwachitsanzo, makina omwe timachapira zipangizo zochitira opaleshoni ngakhaleso zochapira zogonera ndi zofunda kapena makatani zimasiya kugwira ntchito madzi akangosiya chifukwa zimayendera kompyuta, adatero Chinkhata. + Iye adati makinawa salola madzi ochita kuthiramo, koma opopa okha kudzera mmakina a kompyuta, ndiye madzi akangosiya makinawa nawo amasiya kugwira ntchito. + Chinkhata adati nkhani ina yomwe ingavute ndi yaukhondo potengera kuti pachipatalachi palibe zimbudzi zokwanira zokumba moti odwala ndi owadikirira omwe amadalira zimbudzi zamadzi. + Timasunga odwala pafupifupi 1 000 patsiku ndiye ena pomwepo amakhala ndi owadikirira awiri kapena atatu. Mukawerengera ndi anthu angati amenewo? Tsono onse azigwiritsa ntchito zimbudzi zamadzi, chonsecho madziwo palibe, sikubala mavuto ena kumeneku? adatero Chinkhata. + Vutoli ndi lomweso anthu okhala mumzindawu omwe amagwiritsa ntchito zimbudzi za madzi aona ndipo ali nalo mantha kuti likhoza kubutsa matenda osiyanasiyana nkusokoneza ntchito zambiri. + Tangoganizani pamalo poti pali zimbudzi zamadzi zokhazokha popanda chokumba anthu akamva mmimba azipita kuti madzi atasowa kwa masiku awiri? Mapeto ake anthu akhoza kumapita mtchire kapena kungodzithandiza mtoileti nkusiyamo choncho. Poterepa munthu mmodzi kungodwala matenda ammimba ndiye kuti komboni yonse, adatero Innocent Mzungu, wa ku Falls mumzindawu. + Derali ndi limodzi mwa madera omwe nyumba zambiri zili ndi zimbudzi zamadzi ndipo zidamangidwa moyandikana. + Nkhani ina yomwe vutoli likhudze ndi la ulimi poti bungwe la BWB laletsa anthu okhala kumtunda kwa mtsinje wa Lilongwe omwe umatsira madzi mmadamu awo kuchita ulimi wamthirira. + Apa zikukolana ndi ganizo la boma loti anthu achilimike paulimi wamthirira polingalira kuti kakololedwe ka chaka chino sikadayende bwino, koma mlembi wamkulu muunduna wa zamalimidwe, Erica Maganga, adati ayambe wakambirana ndi kampaniyi kaye. + Choyamba sitikudziwa kuti ndi anthu angati amagwiritsa ntchito madamuwa kapena mtsinje wa Lilongwe paulimi wamthirira. Ndikuyenera kuti ndikambirane ndi akuluakulu a kampaniyi kuti tione pomwe pali vuto ndi momwe tingapangire, adatero Maganga. + Phungu wa kunyumba ya malamulo yemwe nkhalango ya Dzalanyama ili mdera lake, Peter Dimba, adati vutoli ndilochita kuweta chifukwa mzaka 10 mpaka 15 zapitazo atsogoleri adalibe chidwi choteteza nkhalangoyi. + Iye adati mzakazi, mitengo yambiri idadulidwa makamaka ndi anthu owotcha makala ndi ogulitsa nkhuni ndipo pomwe akuluakulu amadzidzimuka, madzi adali atafika kale mkhosi. + Mpanopotu pomwe zikukhala ngati akuluakulu akukhuzumuka. Muone chitumizireni asirikali ankhondo mnkhalangoyi zinthu zikusintha. Tsono ankalekeranji kuganiza zimenezi kalelo? adatero Dimba. + Iye adati ali ndi chikhulupiriro kuti ndi chitetezo chomwe chilipochi, chiyembekezo chili pa mphukira za mitengo kuwonjezera pa mitengo yomwe ikubzalidwa chaka ndi chaka. + Izi zili chonchi mumzindawu, makampani opopa ndi kugawa madzi mmizinda ya Blantyre ndi Mzuzu ati iwo alibe nkhawa ina iliyonse chifukwa mitsinje ndi madamu omwe amapopamo muli madzi okwanira. + Pakalipano, mkulu wa bungwe la anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito malonda la Consumers Association of Malawi (CAMA) John Kapito adati ichi chikhale chitsegula mmaso kwa aliyense. + Iye adati mnyengo ino yakusintha kwa nyengo chilichonse chikhoza kuchitika ndiye mpofunika kuti mabungwe opopa ndi kugawa madzi akhale ndi malo ambiri komanso odalirika osungirako madzi kupewa mavuto ngati omwe agwa mumzinda wa Lilongwe. + Tizidziwa kuti madzi ndi moyo. Chilichonse chomwe munthu amapanga pamoyo wake chimalira madzi ndiye mpofunika kusamala kwambiri pankhani yokhudza madzi, osamachita zinthu modzidzimukira, adatero Kapito. +",2 +" Admarc isagulitse chimanga kunja Bungwe la Admarc lisatengeke ndi zakuti dziko lino likhoza kukolola chimanga chochuluka chaka chino nkugulitsa chimanga kunja padakalipano, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi la CisaNet Tamani Nkhono-Mvula watero. + Nkhono-Mvula adauza Tamvani pomwe Admarc ikulingalira zogulitsa chimanga chimene lidagula ku Zambia kumaiko a Kenya ndi Tanzania. Izi zadza pomwenso mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika atalamula asilikali kuti akhamukire kumalire a dziko lino ndi kugwira ofuna kugulitsa kunja chimanga mozemba. Lamulolo lidadza apolisi atagwira galimoto 17 zimene zimafuna kutulutsa chimanga mozemba. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zina mwa galimoto zimene zidagwidwa Iye wati mmera omwe uli mminda usapereke chiyembekezo chabodza kuti Admarc igulitse kunja chimanga. + Njala ikadalipo. Zonse zidzadziwika bwino kafukufuku womaliza wa zokolola akadzatulutsidwa. Posakhalitsapa timasaka chimanga Amalawi atasauka ndi njala, choncho kuchigulitsa panopa kunja ndi chibwana cha mchombo lende, adatero Nkhono-Mvula. + Iye adati chimanga sichingasowe msika ngakhale mdziko momwe muno, koma phuma silingathandize konse. + Pamene boma lakhwimitsa chitetezo kuti chimanga chisatuluke, pakuyeneranso kukhala chitetezo momwe chimanga chikugulitsidwira mdziko momwe muno. Pali vuto lalikulu pamene chimanga chochokera kumwera chikukagwidwa ku Karonga, adatero mkuluyo. + Iye adatinso mpofunika kuti boma kudzera ku unduna wa za malonda kapena malimidwe azipereka ziphaso zapadera kwa anthu ofuna kuchita malonda achimanga. + Ndipo polankhula pomwe amakhazikitsa ntchito ya magetsi mmidzi, Mutharika adati ngakhale maiko a Kenya ndi Tanzania ati akufuna kugula chimanga kuchoka ku Admarc, salola kuti izi zichitike. + Zidachitikapo mmbuyomu kuti pamene tili ndi chimanga chochuluka tidachigulitsa ku Kenya koma chaka chotsatira kudali njala yadzaoneni mpaka kumakagulanso ku Kenya komweko, adatero Mutharika, nkupemphanso Amalawi kuti asagulitse chimanga chawo kwa mavenda koma kudikira misika ya Admarc itsegulidwe. + Wapampando wa nthambi yoyanganira ntchito za Admarc James Masumbu adati mapulani ogulitsa chimanga ku Tanzania ndi Kenya alipo koma akudikira kuti alimi akolole kaye. + Panopa, pologalamu yonse yaima chifukwa tikufuna tiyambe takolola kuti tiwone chakudya chomwe alimi akolole kuti tidziwe pomwe chitetezo cha dziko chilili kumbali ya chakudya kenako tidzapanga ganizo lenileni, adatero Masumbu. + Iye adati kugulitsa chimangachi sikuzungulira mutu koma kuti bungweli lili ndi ngongole yofunika kubweza ndipo ndalama zobwezera ngongoleyi zikhoza kupezeka msanga pogulitsa chimangachi. + Polankhulapo pa ganizoli, wapampando wa komiti yoyanganira za malimidwe mnyumba ya malamulo Joseph ChintantiMalunga adati ganizo la Admarc lofuna kugulitsa chimangacho ndi labwino polingalira kuti akufunika kubweza ngongole zomwe adatenga zogulira chimangacho. + Wachiwiri kwa mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress Elsenhower Mkaka adati ngati mpata ogulitsa chimangacho ungapezeke, Admarc igulitse koma ndondomeko yake iyende moyera. + Ndi ganizo lofunikira koma ziyende mwachilungamo komanso zisakwirire nkhani ya kagulidwe ka chimanga ku Zambia yomwe ikadali ikuyenera kuoneka mapeto ake, adatero Mkaka. + Pali malipoti akuti chaka chino anthu pafupifupi 1 miliyoni akhala ndi njala mdziko la Tanzania pomwe dziko la Kenya lawona ngamba yomwe silidawonepo kutanthauza kuti njala ivuta mdzikolo. + Malingana ndi mgwirizano wa maiko a mu Common Market for East and Central Africa (Comesa) maiko amayenera kugwirana manja wina a kapezeka ndi vuto ngati la njala. + Masiku apitawo, apolisi adagwira galimoto zomwe zimafuna kutulutsa chimanga kupititsa ku Tanzania kudzera mmaboma a Karonga ndi Chitipa. + Mneneri wapolisi James Kadadzera adati galimotozo ndi chimanga chomwe akuzisunga kudikira upangili wa boma kuti chimangacho atani nacho ndipo eni galimotozo adzazengedwa mlandu ofuna kuzembetsa chimanga. +",10 +" Konvenshoni ya MCP yalephereka Chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chati msonkhano wake waukulu wa konvenshoni umene umayenera kukhalapo pakati pa lero ndi Lolemba wamwa madzi. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Wapampando wa msonkhanowo Joseph Njobvuyalema, Lachinayi adati msonkhanowo walephereka chifukwa chipanicho chalephera kupeza K35 miliyoni yochitira msonkhanowo komanso ana asukulu ku Natural Resources College komwe nthumwi 700 zimayenera kukagona sanatsekere. + Mmalo mwa K35 miliyoni tangopeza K20 miliyoni ndipo tikadati tichititse msonkhanowu, sukadakhala wapamwamba momwe timafunira. Komanso chifukwa ana asukulu ku NRC sanatsekere, nthumwi 500 zikadasowa kogona chifukwa kusukuluko kuli malo a anthu 200 okha basi, adatero iye. + Izi zidadza pomwe mtsogoleri wa chipanicho John Tembo adapereka zikalata zosonyeza kuti akufuna kupikisana nawo pampando wa mtsogoleri wa chipanichi ngakhale malamulo a chipanicho sakumulola kutero. + Kadaulo wa ndale Henry Chingaipe adati kuimanso kwa Tembo kudadzetsa mafunso omwe Tembo ndiye angayankhe. + Chingaipe adadabwa kuti Tembo adapereka zikalata zake chipanichi chitaonjezera tsiku limodzi loti anthu apereke zikalatazo. + Anthu amene akuoneka kuti alidi ndi khumbo lodzaimira chipanichi ndi kuchitsogolera adapereka mnthawi yoyenera, koma Tembo adakapereka chipanichi chitaonjezera tsiku limodzi. Bwanji sadali woyambirira kukapereka zikalatazo, adatero Chingaipe. + Msabatayi, Jodder Kanjere, Chris Daza, Felix Jumbe, Betson Majoni, Lazarous Chakwera, Lovemore Munlo ndi Eston Kakhome nawo adapereka zikalata zawo. + Malinga ndi mmodzi mwa akuluakulu amene akhala akulandira zikalatazo Potipher Chidaya adati Tembo adaonjezera tsiku limodzi lolandirira zikalatazo. + Chipanichi chidatulutsa ndondomeko ya zoyenereza munthu wopambana. Mwa zina, pali mfundo yakuti mtsogoleri wa chipanichi ayenera kukhala yemwe wakhala membala kwa zaka zisanu, akhale ophunzira ndiponso akhale wakuti sadalowepo chipani china. + Kakhome, yemwe adali mtsogoleri wa chipani cha Social Democratic Party (SDP) nthawi yomwe ndale za dziko lino zimasintha, adati iye ndiwokonzeka kutsogolera MCP. + Ndidagwirapo ntchito mu MCP. Ndikudziwa kuti ichi ndi manthu wa zipani mMalawi ndipo ndine wokonzeka kuchitsogolera komanso kuti tipambane pachisankho ndikubwezeretsa dziko lino mchimake, adatero Kakhome. + Ndipo Jumbe, yemwe adali mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) adati sikuti nkhani yaikulu ndi kugonjetsa Tembo, koma kutsogolera fuko. + Dziko lino limadalira ulimi, ndipo ine ndi chitsanzo pa momwe tingatukukire ndi ulimi, adatero Jumbe. + Chakwera, yemwe anali mkulu wa mpingo wa Assemblies of God adati sakuonapo cholakwika kuti Tembo akufuna kuima nawo. + Ndi ufulu wake. Sichoncho? adatero Chakwera, yemwe akutinso akufuna kubweretsa msintho muutsogoleri wa chipanicho. + Munlo, yemwe adatula udindo wake wa mkulu wa malamulo, adati iye wakhala ali membala wa MCP kuyambira kale. + Ndidangochoka mu 2000 pomwe ndimakagwira ntchito kubungwe la United Nations komwe samafuna andale. Komanso pomwe ndidali mkulu wa za malamulo, sindimayenera kukhala ndi chipani, adatero Munlo. + Malinga ndi Kanjere, yemwe adakhalapo nduna mu ulamuliro wa mtsogoleri woyamba wadziko lino Dr Hastings Kamuzu Banda, adzaonetsetsa kuti ulamuliro siukukhala paphewa la munthu mmodzi. + Nthawi yakwana kuti MCP ilamulire, osati kumangokhala mbali yotsutsa boma, adatero Kanjere. + Daza, yemwe ndi mlembi wamkulu wa MCP, ndiye wakhala nthawi yaitali akuneneratu kuti wakonzeka kutsogolera chipanichi nthawi ya Tembo pampandowu ikatha. +",11 +"Police Arrest Three Criminals, Recover Stolen Motor Vehicle Namwera Police Post in Mangochi is keeping in custody a 21-year-old man, Shafi Hassan and two others on allegations that they stole a Mazda Demio vehicle registration number MJ 2339 worthy K1.7 million. +According to Mangochi Police Deputy Spokesperson Amina Daudi, Hassan and the other two, Rashid James, 23, and Julius Saidi, 28, were apprehended on the wee hours of April 1, 2020. +Confirmed the incident Daudi The three went to the house of Yusuf Nelson on the night of January 23, 2020 dressed in camouflage attire and disguised themselves as police officers from Mangochi Police Station. +According to Daudi, the criminals lied that the said car was wanted because it was involved in a hit and run road accident in Monkey-Bay. +Eventually, they demanded keys of the vehicle and drove away with the victim and his son who were later dumped at Namwera. +Namwera police officers successfully apprehended the three during patrols and recovered the stolen motor vehicle. +Daudi says investigations are still underway to recover the camouflage attire and all suspects will appear before court to answer charges of theft of motor vehicle and personating a police officer. +The suspects come from Katuli Village in the area of Traditional Authority Katuli in Mangochi. +",7 +" Leo Mpulula: Alibe 2 koloko Akulu, ligi ikuyamba, inu ngati kochi wa Max Bullets mwakonzeka bwanji? Tapimana ndi matimu ambiri, zikuonetsa kuti anyamata agwira ntchito momwe ndikufunira. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mudasewera ndi Wanderers, masewero adali bwanji? Adali bwino, anyamata akuonetsa kulimba mtima, kusonyeza kuti ntchito igwirika. + Masewero atatha, mudawayankha atolankhani zamwano, vuto lidali chiyani? Mpulula: Ndazitaya Amwene, si mwano, koma atolankhani ena amadabwitsa. Adandifunsa kuti anyamata anga sadamenyere pagolo chifukwa chiyani. Ndiye ndidamufunsa kuti Wanderers idamenyera pagolo? Yekha adaona, ndiye amafuna chiyani? Amafuna timu ithe kapena? Nanga bwanji apapa mwandiyankha momwe masewero adathera? Inu kudalibe, komanso mtima wanga wakhala pansi ndipo ndapeza chomwe chidavuta, koma mudakandifunsa komweko ndiye mudakaona kuti ndi mwano koma chili chilungamo. + Mukafunsidwa momwe masewero mwawaonera, nthawi zonse mumabweza funso, pali vuto kodi? Akandifunse momwe ndawaonera? Iyeyo adali kuti? Ndipo ngati iyeyo adaonera, bwanji osakalemba zomwe waonazo? Ndimabweza chifukwa si funso ayi. Nchimodzimodzi kumafunsa kuti madziwa akupezeka bwanji kubafaku. Ine ndiye ndiziti chiyani? Akudziwa kuti timu sili bwino, ndiye akufunsa kuti ndaiona bwanji? Iyeyo adali kuti? Akufuna chiyani? Yankho ali nalo koma akufunsanso, ndiye akufuna chiyani, amwene? Amwene, koma ndamva kuti mwazitaya ku Max Bullets, zoona? Kwambiri kwake. Ndazisiya. Amwene, mwini wake wa Max Bullets, Max Kapanda, samva za munthu ndiye ndangoti khala nayo timu yakoyo, ndapita. + Nkhani yake? Ndinamuuza kuti apereke ma contract abwino kwa ma players koma iye amati player aliyense asayinire K100 000 kwa zaka zitatu, zoona zimenezo? K100 000 ndi chiyani kwa player wa mu Super League, si salale ya pamwezi imeneyo? Ndiye ma players amene ndimafuna anakana kusayinira K100 000 ndipo anapita ndiye inenso ngati kochi ndinangoti ngati ma players apita ndiye nditsala ndi nda? Nchifukwa chane nane ndachoka ku Max Bullets. Ubwino wake sindinasayine contract. +",16 +" Katsoka: Mutu wa alakatuli Ulakatuli ndi limodzi mwa maluso omwe akuphukira kumene mdziko muno. Zaka zambiri zapitazo, anthu samatenga ndakatulo ngati njira yofalitsira uthenga kapena kuphunzitsa monga momwe zikukhalira pano. Pazaka zochepa zokha, alakatuli mdziko muno atumphuka ndipo anthu ambiri ayamba kukonda ndakatulo. Alakatuliwa adakhazikitsa bungwe lawo lomwe mtsogoleri wake ndi Felix Njonjonjo Katsoka. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Katsoka: Ndidayamba mu 1994 Tandiuza dzina lako ndi komwe umachokera. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Felix Njonjonjo Katsoka. Ndimachokera mmudzi mwa Chingamba mboma la Ntcheu koma pano ndikukhala ku Nkhotakota. Ndidaphunzira za uphunzitsi koma ndimagwira ntchito ya zaumoyo kumbali ya zakudya zamagulu. + Utsogoleri wa alakatuli udaulowa liti? Ndidauyamba mchaka cha 2009. Malingana ndi malamulo athu, timayenera kukhala ndi zisankho zaka zisanu (5) zilizonse moti panopa tili kalikiriki kuthamangathamanga kuti tipeze ndalama zopangitsira nkhumano ina komwe tidzakhalenso ndi zisankho. + Kodi bungwe limeneli lidayamba liti? Bungweli lidayamba mchaka cha 1997 pomwe alakatuli adakumana kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium. Ena mwa akatakwe omwe adali kumeneko ndi monga Laurent Namarakha, malemu Aubrey Nazombe, Edward Chitseko ndi malemu George Chiingeni. Pa 4 September, 1998, bungweli lidalembetsedwa kunthambi ya kalembera wa mabungwe. + Cholinga chake nchiya? Cholinga cha bungweli ndi kufuna kutukula luso la ulakatuli mMalawi muno komanso kufuna kufalitsa mauthenga ndi kuphunzitsa anthu kudzera mndakatulo monga momwe amachitira azisudzo kapena oyimba. + Iweyo udayamba liti ndakatulo? Ndidayamba ulakatuli mchaka cha 1994 ndili pasukulu ya sekondale ya Likuni Boys. + Uli ndi masomphenya anji pa ndakatulo mmalawi muno? Masomphenya anga ndi akuti ndakatulo zidzafike pabizinesi ngati momwe maluso ena alili pano. Kuti izi zidzatheke mpofunika kupeza akatswiri oti adzatithandize moti boma ndi mabungwe atalowererapo zikhoza kutithandiza kwambiri. Njira ina ndi yakuti alakatuli onse azilembetsa ntchito zawo kubungwe la Cosoma kuti tizitha kukhala ndi chithunzithunzi chenicheni cha chiwerengero cha alakatuli omwe tili nawo. +",0 +" Idali nthawi ya nkhomaliro Wina mtolankhani wina namandwa wa zamalonda koma kokasungitsa ndalama ndiko adawonana nkutsimikiza kuti Chauta adawalenga kudzakhala limodzi. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Umu mudali mu 2012 pomwe Agnes Chinyama, yemwe kwawo ndi kwa Mchere, T/A Kapeni mboma la Blantyre, ankagwira ntchito kunthambi yofalitsa nkhani ya Malawi News Agency. + Andy ndi Agnes tsiku la ukwati wawo Apa, Andy Tango Ngalawa, yemwe amachokera kwa Kapenuka, T/A Kamenyagwaza ku Dedza, ankagwira ntchito ku Arkay Plastics ndipo awiriwa adakumana mbanki momwe amakatapa ndalama zokagulira nkhomaliro. + Agnes akuti adazindikira kuti Andy adali naye mawu potengera momwe amamuyanganira koma poti uku kudali kuwonana koyamba mate adauma mkamwa mpakana onse adatuluka mbankimo. + Dzanja la Chauta likalemba lalembadi moti tsiku lomwelo awiriwa adakumananso pamalo odyera a Steers mumzinda wa Blantyre ndipo uku nkomwe adayamba kulankhulana, ubwenzi wa macheza chabe nkuyamba. + Titakumana ku Steers adandipatsa moni ndipo tidacheza uku tikudya nkhomaliro yathu. Umu mudali mu April. Chinzake chimayenda kufikira mwezi wa June pomwe adandifunsira ndipo chibwenzi chenicheni chidayambika mwezi wa August, adatero Agnes. + Chibwenzichi chidatha zaka ziwiri ndipo pa 2 March 2014 adamanga unkhoswe womwe udakathera muukwati woyera pa 30 August chaka chomwecho. + Tidakadalitsira ukwati wathu kutchalitchi cha Bethsaida Pool International ndipo madyerero ake adali ku Chimaliro Gardens mumzinda wa Blantyre, adatero Agnes. + Iye akuti adamukonda Andy kaamba ka moyo wake wodzichepetsa, wachikondi, woopa Mulungu ndi wokhulupirira kupemphera. + Ndimakonda banja langa kwambiri moti nthawi zonse ndikakhala ndimapemphera kuti Mulungu atisunge ndipo banja lanthu lipitirire kukhala lopambana ndi loopa Chauta, adatero Agnes. + Naye Andy akuti atangomuona Agnes mbankimo mtima wake udagunda mwachilendo ndipo ngakhale amasiyana naye atamaliza zomwe amachita mmenemo ankamva ngati wataya mwala wa golide. + Ndidadzitenga wolephera kwambiri nditatuluka mbankimo moti nditakumana nayenso ku lunch ndidadziuza mumtima kuti chondigwera chindigwere, koma na apa pokha ndilankhula naye basi, adatero Andy. + Iye adati atamupatsa moni koyamba adaona kuti Agnes ndi munthu wosadzikweza ngati momwe amachitira asungwana ena kuyankha mothimbwidzika ndipo adadzilonjeza yekha kuti achilimika mpaka atengeretu namwaliyo. + Pano awiriwa ndi bambo ndi mayi ndipo Andy akupitiriza ntchito yake ku Arkay Plastics komwe akugwira ngati woyanganira zamalonda pomwe Agnes akugwirabe ngati mtolankhani ku Star Magazine ku South Africa. +",15 +" Akwiya ndi bungwe la MEC Mpungwepungwe umene ukuchitika kubungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) wakwiyitsa zipani zotsutsa komanso omenyera ufulu omwe apempha kuti zinthu zikonzedwe msanga kubungweli kuti ntchito yochititsa zisankho isaime chifukwa kutero nkuphwanya ufulu wa anthu wosankha atsogoleri awo. + Mneneri wa chipani cha Peoples Party (PP) Ken Msonda, komanso wa chipani cha UDF Ken Ndanga kudzanso mkulu womenyera ufulu wa anthu, Unandi Banda, apempha bungweli kuti likonze zinthu msanga kuti zipani zonse zikhale ndi chikhulupiriro pa bungweli. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Msonda: Sitikukondwa nazo zimezi Ndemanga za akuluakuluwa zikudza pamene kubungweli kwachitika zingapo monga kulephereka kwa zisankho zachibwereza mmadera asanu; kusokonekera kwa ndalama; kutumizidwa kutchuthi kwa akuluakulu ena a bungweli mokakamizidwa; komanso pamene bungweli likutha masiku opanda wapampando chimwalirireni mwadzidzidzi amene adali mtsogoleri Maxon Mbendera. + Msonda adati zomwe zikuchitika ku MEC zikuonetseratu kuti bungweli silikugwira ntchito mokomera zipani zotsutsa. + Kutumiza ogwira ntchito ena kutchuthi ndi nkhani yabwino, chifukwa tikufuna tidziwe momwe ndalama [zoposa K15 miliyoni] zidasowera. Koma vuto lathu ndi kuimitsa zisankho [zapaderazi] kuti zisachitike. + Ife sitikukondwa nazo, zikuonetseratu kuti bungweli likunjenjemera ndi boma. Ichi nchipongwe kuti zisankho zapadera zisachitike. Tadandaula nazo, adatero Msonda. + Iye adati kusachititsa zisankho zapaderazi ndi kuwaphwanyira ufulu anthu a maderawo chifukwa ntchito zachitukuko komanso zakumtima kwawo sizingapherezere kaamba kosowa wokatula nkhawa zawo ku Nyumba ya Malamulo kapena kukhonsolo. + Naye Ndanga adati chikuwadandaulitsa iwo si kuimitsidwa kokha kwa zisankho chachibwereza, koma kuti izi zingakhudze chisankho cha 2019. + Ntchito yochititsa chisankho simangochitika tsiku limodzi, ndi ndondomeko yomwe imachitika kwa nthawi yaitali. Nanga poti anthu ena kulibeko, ntchito igwirika bwanji? Izi tikudandaula nazo, adatero Ndanga. + Mogwirizana ndi akulu a zipani ziwirizi, Banda adati kutumizidwa kutchuthi kwa akuluakulu ena komanso kusowa kwa mtsogoleri wa bungweli ndi nkhani yaikulu komanso yodandaulitsa. + Mwachidule, izi zikutanthauza kuti tilibe bungwe loyendetsa zisankho. Bungweli limakhalapo ngati lili ndi mtsogoleri komanso ena omuthandizira. Ndiye bungwe lilipo? akudabwa Banda. + Koma mkulu wa nthambi yoona za chuma kubungweli, Linda Kunje, akuti anthu asadandaule chifukwa zonse zilongosoka. + Palibe chovuta ndipo zipani zisadandaule, adatero Kunje. + Malamulo a zisankho amati pasadutse miyezi itatu dera lisadachititse chisankho chopeza mtsogoleri chichokereni kapena chimwalirireni mtsogoleri amene adalipo. Kunje aadati akudziwa za izi komabe sangachitire mwina. + Inde taphwanya lamulo koma sitingachitire mwina chifukwa pali zifukwa zomveka zomwe zatilepheretsa kuchititsa zisankhozi, adatero Kunje. +",11 +"Epifania Imathandiza Ana Kuzama mu Chiphunzitso cha Mpingo-Bambo Thawani Arkdayosizi ya Blantyre yati chaka cha ana cha epifaniya ndi chofunika kwambiri chifukwa chimawapasa mwawi anawa kutsogolera zochita pa msembe ya ukaristiya choncho anawa amakula akuzindikila kuti nawo ndi wofunika mu mpingo. +Bambo Matias Thawani omwenso ndi mkulu woona utumiki wa ana pansi pa mabungwe utumiki wa apapa Portifical Mission Society PMS mu Arkidayosiziyi ndi omwe anena izi lamulungu pa 5 January 2020 ku Limbe cathedral pa mbuyo pa msembe ya ukaristiya komanso zochitikachitika zomwe ana aku chalitchili anakonza pa tsiku la epifaniya. +Bambo Thawani kujambulitsa ndi ena mwa ana patsikulo Bambo Thawani anati tsiku ili limapereka mangolomera kwa anawa kuti azikangalika ndi za mpingo pozindikira kuti nawonso ndi mbali imodzi ya mpingowu. +Mwazina bambowa anati tsiku ngati ili limathandiza kuzindikira mphatso zosiyanasiyana zomwe anawa ali nazo. +Pamene ana apasidwa mpata kutenga gawo pazochitika za mpingo, mphatso zawo zauzimu zimatumphuka komanso amazindikira mwachangu maitanidwe awo, anatero bambo Thawani. +Iwo anapitiliza kuthokoza ansembe onse mu arkidayosiziyi powapatsa mpata anawa patsiku lawoli. + Ndikuthokoza ansembe anzanga onse mu parishi zonse za mu arkidayosiziyi popereka mpata kwa anawa, anathokoza motero bambo Thawani. +Mau ake katikisiti Paul Muheko wa mparish ya Limbe anayamikira dongosolo la mpingo wakatolika pokhazikitsa tsiku la chaka cha ana ponena kuti limathandiza anawa kutumikirana okhaokha ku uzimu komanso ku thupi. +Dongosolo la mpingo wakatolika ndilapamwamba chifukwa linakonza kale kuti tsiku ngati lero nawo ana azitenga gawo pachipembezo, anatero a Muheko. +Naye mmodzi mwa ana omwe anatenga nawo gawo patsikuli Patricia Likomwa anati tsikuli lamupindulira makamaka momwe angatumikire ana azake. +Ndasangalala kwambiri moti sindinasangalalepo chonchi moyo wanga wonse chifukwa ndazindikira kuti nane ndikhoza kutimikira ku mpingo makamaka kwa ana amzanga, anatero Patricia. +Chaka cha Epifaniya chimachitika lamulungu loyambilira mchaka chilichonse pamene Yesu khristu anadzera anthu a mitundu yonse pomwenso mpingo wakatolika pa dziko lonse umachita chaka cha utumiki wa ana. Mutu wa chaka chino Ana amabatizidwa ndikutumidwa kuti alalikire mau a Mulungu. +",13 +" Asintha mlandu wa fisi Apolisi Lachinayi adasintha mlandu wa Eric Aniva, amene adamangidwa ataulula kwa mtolankhani wa BBC kuti amagona ndi ana achichepere komanso amayi amasiye potsata miyambo ya makolo. Mneneri wapolisi mdziko lino Nicholas Gondwa adati adasintha mlanduwo kuchoka pomuganizira kugona ndi ana, kufika ku mlandu woika moyo wa wina kukhala pachiopsezo cha imfa. + Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adalamula apolisi kugwira Aniva wa zaka 40 atauza atolankhaniwo kuti adagona ndi amayi ndi ana 104 mosadziteteza potsata mwambo wa kusasafumbiumene umachitika msungwana akatha msinkhundi wa kulowakufa, umene umachitika kwa mkazi wamasiye pofuna kukhazika pansi mzimu wa mwamuna wake. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Adamangidwa: Aniva Gondwa adati akumuzenga mlandu woika miyoyo ya ena pachiswe mosemphana ndi ndime 1 komanso 2 za gawo 5 ya malamulo oti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pantchito. Iye adati adasintha polingalira kuti ngakhale Aniva amadziwa kuti ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV, iye amagonabe ndi asungwana ndi amayiwo osawauza. + Atapezeka wolakwa akhoza kulipa K1 miliyoni kapena kukakhala kundende zaka zisanu akugwira ntchito ya kalavula gaga, adatero Gondwa. + Mneneriyo adaonjeza kuti padakalipano, Aniva waulula abambo ena amene amagwira ntchito yaufisi, pomwe amalandira K3 500 mpaka K5 000 akagona ndi mayi kapena msungwana. + Aniva, yemwe adakaonekera kukhoti la Nsanje Lachinayi, akusungidwa kundende ya mbomalo pomwe apolisi akufufuzabe za nkhaniyo. + Polankhula ndi BBC, Aniva akuti adati adayamba ntchitoyi mzaka za mma 1980 ndipo wakhala akugona ndi asungwana a zaka zoyambira 12 komanso amayi amasiye. Iye adauzanso atolankhaniwo kuti amayi ndi asungwana amayamikira ntchito yake. Mkazi wake naye adati amalola amuna ake kugwira ntchitoyo chifukwa amapeza ya mchere. + Koma atafunsa ena mwa amene adagona nawo ali achichepere, adati adavulala ndipo adangolola chifukwa miyambo yawo inkaneneratu kuti ngati salola mwambowo adzadzetsa mlili mmudzimo. +",7 +" Katundu wobwera ku Malawi ali pachiopsezo ku Mozambique Magulu a zachifwamba mdziko la Mozambique akuchitira mtopola galimoto zonyamula katundu wosiyanasiyana wobwera mdziko muno kuchokera kumaiko ena podutsa mdzikolo. + Pali malipoti oti mdzikomo muli nkhondo yapachiweniweni pakati pa asirikali a boma ndi zigawenga za chipani chotsutsa cha Renamo chomwe mtsogoleri wake ndi Afonso Dhlakama, koma boma la Mozambique lakhala likutsutsa malipotiwo ngakhale anthu ena zikwizikwi athawa mdzikomo kudzapeza mpumulo mdziko lino. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mtopolawu udayamba Lachitatu sabata yatha pomwe maguluwo adatentha galimoto ina yomwe idanyamula mafuta a petulo wandalama zokwana pafupifupi K28 378 800 yemwe amabwera mdziko muno. + Mtopolawu usadaiwalike, maguluwo adatenthanso galimoto zina zitatu Lachisanu masana ndipo ziwiri mwa galimotozo zidanyamulanso mafuta ndipo msabata imodzi yokha, galimoto zoyatsidwa zakwana zisanu. + Chiwembuchi chikuchitika kwambiri kwa galimoto zodutsa njira ya Tete ndi Beira ndipo maguluwo sakusankha kochokera kapena kopita galimotozo. + Malingana ndi mkulu wa bungwe la makampani oitanitsa mafuta mdziko muno, Enwell Kadango, ndalama zokwana pafupifupi K70 miliyoni zapita mmadzi kaamba ka ziwembuzi ndipo iye adati iyi ndi nkhani yoipa pamalonda. + Mwachidule, galimoto iliyonse yonyamula mafuta, imanyamula mafuta a ndalama zapakati pa K22 miliyoni ndi K23 miliyoni ndiye mukawerengera ndalama zomwe zamwazika nzambiri zedi, adatero Kadango polankhula ndi Tamvani. + Potsatira zokambirana pakati pa maiko a Malawi ndi Mozambique, dziko la Mozambique lidatumiza asirikali ake kuti azikaperekeza galimoto zotuluka ndi kulowa mdziko muno podzera mdzikolo. + Mneneri wa unduna woona za maubale a dziko lino ndi maiko ena, Rejoice Shumba, adatsimikiza nkhaniyi. +",17 +" Kulumana pa ofunika kulandira chakudya Kusankha ovutikitsitsa kuti alandire thandizo la chakudya kuchokera ku boma kwavuta mmidzi ina pamene anthu ndi mafumu ayamba kulumana. + Izitu zadza pamene boma kudzera mnthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma) yayamba kugawa chakudya kwa anthu amene sadakolole chakudya chokwanira chifukwa cha ntchemberezandonda ndi ngamba. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kugawa chimanga kuli mkati mmaboma ena Nthambi ya Dodma idapempha alangizi a zamalimidwe komanso ofesi ya DC mboma lililonse kuti itolere maina a anthu amene athiphwa ndi njala. + Pa ntchitoyo, Dodma idatolera mabanja oposa 400 000 malinga ndi amene akuyendetsa ntchitoyi ku Dodma, Paul Kalilombe. + Awatu ndi anthu oposa 2 miliyoni amene tikuyenera tiwapatse thandizo. Iyi ndi nambala yomwe tigwiritse ntchito dziko lonse, adatero Kalilombe. + Koma nambalayi yakhumudwitsa mafumu ena amene akuti mmadera awo asiya anthu ambiri amene akhudzidwa ndi njala. + Gulupu Cheghama wa mboma la Karonga kwa Paramount Kyungu adati mdera lake anthu a mwa nyakwawa 5 ndi amene akhudzidwa ndi njala ndipo ayenera thandizo madzi asadafike mkhosi. + Cheghama adati anthu pafupifupi 300 ndi amene akuphupha ndi njala mwa mfumu Ngingekemo, Mwangwabila, Kazguli, Kazguli 2 ndi Mwaphoka. + Chomwe tadabwa ife nchakuti ngakhale tidapereka mainawo kuti boma liwathandize, iwo avomereza anthu 75 okha kuti ndiwo alandire chakudya, adatero Cheghama. + Gulupu Mpochera ya kwa mfumu yaikulu Tsikulamowa mboma la Ntcheu yati idapereka maina a anthu 250 amene adakhudzidwa ndi njala mdera lake. + Poyamba akuti adadziwitsidwa kuti nambala ija ayidula ndipo anthu 115 ndi amene alandire thandize. + Sabata yatha adaitananso mafumu onse, titapita akatiuza kuti nambala ija ayidulanso ndipo anthu 45 okha ndi amene alandire thandizo, adatero Mpochera. + Anthu 250 tonse takambirana kuti chimanga chikabwera, tonse tikhala pansi ndipo tigawana. Kaya aliyense adzatenga chimanga chodzadza mbale yokha bolani akaphike kaphala ndi kumwa, adaonjeza. + Mfumuyo idati dera lake kapuchi ndi ngamba ndi zimene zidasokoneza moti palibe amene adapeza ngakhale thumba limodzi la chimanga. + Kunoko kuli moto, ineyo ndimakolola matumba oposa 10 koma chaka chino ndidapeza ndowa imodzi basi, adatero iye. + Koma Kalilombe akuti nthambi yawo ikuyangana anthu okhawo amene alibe pogwira ngakhale nkhuku yeniyeniyi alibe. + Zoti chiwerengero chabwera chochepa bwanji ife zimenezo sitikudziwa chifukwa tidadalira ena kuti afufuze amene akufunika thandizo ndipo nambalayo tidapatsidwa. + Komanso zoti chimangacho azigawana gulu ife sitikondwera chifukwa ndiye kuti akupha cholinga chathu kuti anthu asafe ndi njala. Anthu ena angovomereza basi kuti si onse amene angalandire thandizo, adatero Kalilombe. + Iye adati pa banja la anthu pafupifupi asanu likulandira thumba limodzi la chimanga lolemera ndi makilogalamu 50. + Lipoti la Malawi Vulnerability Assessment Committee (Mvac) lomwe lidatuluka mwezi watha lidati anthu 3.3 miliyoni atuwa ndi njala chaka chino chifukwa choti anthu sadakolole chakudya chokwanira. + Kodi anthu enawo athawira kuti? Kalilombe akuti akamaliza gawo ayambalo, akhala pansi kuti aunguze za anthu 3.3 miliyoni amene Mvac yafunthula. + Amene tikuwagaira pano sitidagwiritsire ntchito zomwe yatulutsa Mvac, koma tikamaliza gawoli ndiye kuti tikhala pansi kuti tigawirenso anthu 3.3 miliyoni amene Mvac yatulutsa, adatero Kalilombe Lachitatu pamene amagawa chimanga mmaboma a Dowa ndi Mchinji. + Pofotokoza mmene ndondomekoyo ikuyendera, Kalilombe adati ntchitoyo yayamba sabata yatha mmaboma a Phalombe ndi Chikwawa. + Iye adati ndondomekoyi yachedwerako chifukwa mndandanda wa oyenera kulandira umachedwa kuperekedwa ku nthambi yawo. + Malinga ndi Kalilombe, sabata ino amayenera kugawa mboma la Blantyre koma ofesi ya DC yachedwa kupereka mndandanda wa amene akuyenera kulandira. + Tikufunitsitsa kuti pofika pa 14 mwezi uno tikhale titamaliza. Sitikupereka kwa mafumu koma kwa amene adalembedwayo, adatero. +",2 +"Papa Alalika za Kulolerana Wolemba: Thokozani Chapola rancis-300x168.jpg"" alt="""" width=""418"" height=""234"" />Papa Francisko Papa Francisko wati kulolerana komanso kukhalirana bwino pakati pa anthu azikhulupiliro ndi mitundu yosiyana kumathandiza pa ntchito yomanga maziko a mtendere pakati pa mayiko pa dziko lonse. +Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco walankhula izi pomwe amapereka uthenga wa mafuno abwino kwa anthu a mdziko la Thailand pomwe wakonza ulendo wokawachezera kumapeto a mwezi uno. +Mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu wakonza zokacheza mdziko la Thailand, kuyambira pa 20 mpaka pa 23 November 2019, ndipo pali chokenzero chakuti akadzatha kucheza mdzikomo, adzamalizira ulendo-wu pokachezanso mdziko la Japan. +",14 +" Mafumu okwezedwa ndi JB ali padzuwa Zasolobana kumpando wa chifumu pamene mafumu ena atsopano amene adakwezedwa ndi mtsogoleri wakale Joyce Banda ayamba kuona mbonawona. + Tikunenamu, mafumu akuluakulu ena alembera boma kuti lichotse mafumuwa poti adakwezedwa ndi kulongedwa mosatsata ndondomeko yake. Izi zikuchitika pamene mafumu atsopanowa alowa mwezi wachinayi asakulandira mswahara. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ndalembera unduna wa maboma a angono kuti achotse mafumu amene adakweza mdera langa. Awa ndi magulupu ndi nyakwawa zomwe zilipo 76. Adawakweza pazifukwa za ndale, T/A Kabunduli ya mboma la Nkhata Bay yatemetsa nkhwangwa pamwala. + Koma mkulu woyanganira nkhani za mafumu mu unduna wa zamaboma a angono, Lawrence Makonokaya wati sadalandire kalata ya Kabunduli ndipo wati mfumuyi ikatumire kalatayo kwa DC wa boma lake kuti afikitse kuundunawu. + Izi zikudza kutsatira mkwezakweza womwe Banda adachita pa zaka ziwiri zomwe wakhala akulamula dziko lino ndi chipani chake cha PP. Pa zakazi, Banda adakweza mafumu 40 000. + Ku Nkhata Bay, Kabunduli akuti mafumuwa amakwezedwa mosatsata ndondomeko zomwe zidachititsa kuti adye khonde ndi magulupu ake 14 ndikulembera undunawu kuti uchotse mafumu atsopanowa. + Sikuti ndi mafumu onse, madera ena zidayenda bwino koma mafumu 76 ndi amene kulongwedwa kwawo kukudabwitsa, adatero Kabunduli. Amapatsa ufumu ena oti si mbadwa za boma lino. Ena ndi ogwira ntchito mboma monga olondera kunkhalango, alangizi a zaulimi komanso ena ndi atsogoleri a chipani. + Iye akuti magulupu komanso nyakwawa zakale akhala akumudandaulira za mafumu atsopanowo. + Mafumu akalewa akaitanitsa chitukuko amadabwa kuti anthu ena sakubwera, kuwafunsa umadzidzimuka kumva kuti adapatsidwa ufumu. Mavuto ndi ambiri, kodi inuyo angakulembereni munthu wina muofesi yanu osakudziwitsani? akudabwa Kabunduli yemwe akuti sadauzidwepo ndi boma pokweza mafumuwo. + Izi ndi ndale. Ndidalemba kalata mu April kudandaulira boma lapitali koma sadandiyankhe. Pano ndalembanso kalata kupempha boma latsopanoli kuti lichotse mafumuwa, adatsimikiza Kabunduli amene wati kalatayo idatumizidwa pa 27 June. + Mmadera ena monga Mwanza, Thyolo ndi Machinga, mavutowa akuti sadachulukire monga zilili ku Nkhata Bay. + Mafumu a mmabomawa akuti mavuto amene ayanga kumeneko ndi kusalandira mswahara maka kwa mafumu atsopanowa. + Senior Chief Nthache ya mboma la Mwanza yati kumeneko mafumu onse 50 amene adakwezedwa mdera lake akuyenda mayomayo ndipo mwezi uno ndi wachinayi. + Mafumu akale onse akulandira bwinobwino koma atsopanowa ndiye sakupeza kanthu, adatero Nthache. + Senior Chief Kawinga wa mboma la Machinga akuti kumenekonso kuli mdima maka ndi mafumu atsopanowa omwe alipo 93 mdera lake. + Koma Makonokaya akuti mafumu atsopanowa sadaikidwe pamndandanda woti ayambe kulandira ndalama chifukwa akudikirira ndondomeko ya zachuma ya 2014/15 yomwe sidaperekedwe kunyumba ya Malamulo. + Pakhala pali kukolana pakati pa mtsogoleri wa dziko ndi mafumu kaamba koti mphamvu zonse zili mmanja mwake zokweza ndi kuchotsa mfumu. + Kodi kugwebanaku kungathe bwanji? Kadaulo pandale ndi kuonetsetsa kuti mphamvu zikupita kwa anthu, Augustine Magolowondo, akuti mavutowa azichitikabe chifukwa mpaka pano sitidapezebe udindo weniweni wa mafumu pamene dziko lino likutsata ndale za demokalase. + Tili ndi lamulo lokhudza mafumu lomwe lidakhazikitsidwa mu 1967. Panthawi imene lamuloli limakhazikitsidwa, dziko lino nkuti lili pansi pa ulamuliro wa chipani chimodzi. Nchosadabwitsa kuti lamuloli limatenga mafumu ngati mbali imodzi ya boma kuiwala kuti boma limayendetsedwa ndi anthu a ndale, watero Magolowondo. + Iye wati mavutowa akula kwambiri lero chifukwa andale amagwiritsa ntchito mafumu ngati zida zopititsira patsogolo zofuna zawo. + Mafumu ena adyera amatengerapo mwayi wosatayana ndi andalewo kuti awaganizire. Tionetsetse udindo wa mafumu pokozanso malamulo athu ndipo mpungwepungwe wotere sudzakhalapo, akutero Magolowondo. +",8 +" Azula mitanda kumanda Bambo wina wa mmudzi mwa Mikayeli, kwa Mfumu Zulu, mboma la Mchinji walaula dziko atakazula mitanda pa mitumbira isanu chifukwa abale a malemu sadamalize kupereka ngongole ya mabokosi omwe adatenga kwa mkuluyo. + Mneneri wa apolisi mbomalo Kaitano Lubrino watsimikiza za nkhaniyo ndipo wati apolisiwa adamanga Robert Phiri wa zaka 21 pamlandu wopezeka kumanda ndi kusakaza zinthu. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lubrino adati malinga ndi banja limodzi lokhudzidwa la Alfonso Sankhani wa zaka 60 wa mmudzi omwewo, Phiri yemwe amagwira ntchito yokhoma mabokosi, adakongoza banjalo mabokosi awiri. + Banjalo lidaperekako ndalama pangono za mabokosiwo, ndipo adalonjeza kuti zinazo adzamalizabe, adatero Lubrino. + Iye adatinso koma pa 21 mwezi uno, Phiri adapita kumanda a mmudziwo komwe adakachotsa mitanda pamitumbira isanuyo kuphatikiza ya Sankhani ndi kupita nayo kwa mabanja ofedwawo. + Uku adawaonetsa mitandayo nkuwauza kuti amubwenzere ndalama zake zomwe zidatsalazo, adatero Lubrino. + Pakadalipano Phiri ali kupolisi ya Kamwendo podikira kukaonekera kubwalo la milandu. +",19 +" Kudali kosungitsa ndalama Ena ukamalowa mbanki amangoganiza kuti chaphindu chochoka mmenemo ndi kusunga kapena kutapa ndalama komatu ena akusimba lokoma chifukwa tikukamba pano ali pa banja lokoma. + Sadock Ngambi wa ku Chitipa yemwe amagwira ntchito yoonkhetsa chuma kubungwe la Unesco akuti amakaika ndalama za bungweli kubanki ndipo mwamwayi adakumana ndi Tumenye Mwenitete wa ku Karonga yemwenso amakasungitsa ndalama. + Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Awiriwa akuti adakhala pa mzere umodzi mbankimo ndipo amacheza ngati adadziwana kalekale apo kudali kukumana kwawo koyamba mwinatu chilankhulo chidagwilapo ntchito. + Mpaka imfa kudzawalekanitsa: Sadock ndi Tumenye Adandisangalatsa momwe adamasukira nane ndipo mumtima ndidangomva kuti tseketseke. Mmene amamwtulira, timanyazi pangono ndi sangala ndidaona ndekha kuti koma mkazi ndi uyu, adatero Sadock. + Iye adati panthawiyo mchaka cha 2010 sadathe mawu adangopempha nambala ya lamya ya mmanja yomwe adalandira naye nkupereka yake ndipo kuyambira apo udali ubale ochezerana pa lamya. + Ataona kuti bobobo amuzulitsira boonaona adalimba mtima nkupita kukaonekera kwawo kwa Tumenye ndipo monga mwa mwambo wa kwawo adapereka malowolo nthawi yomweyo kuti ena asowe khomo lolowera. + Nditapereka malobolo, padapita chaka china ndipo mchaka cha 2012 ndi pomwe tidamanga woyera ku Kawale CCAP ndipo madyerero ake adali kusukulu ya sekondale ya Chipasula, adtero Sadock. + Iye adati akaona mkazi wakeyo amakhala ngati waona makolo ndi abale ake chifukwa cha chikondi ndi chisamaliro chomwe amalandira. + Naye Tumenye sadafune kuotcha chofunda koma kuyamikira ndi kuthokoza kuti adapeza mwamuna wakukhosi kwake. + Ambiri alipo okwatira ndi kukwatiwa koma ineyo pandekha ndimadzitenga wodala. Mwinanso ena amadzitenga odala mmaanja awo ndiye kuti nawo adapeza wawo ngati mmene ndidapezera wanga, adatero Tumenye. + Tikunena pano awiriwa ndi bambo ndi mai aulemu wawo, opemphera komanso okondana ngati mkazi ndi mwamuna. +",15 +"Chaka cha Chibalalitso Chichitikira ku St. Pius Parish Wolemba: Sylvester Kasitomu maria.mw/wp-content/uploads/2019/09/st-pius.jpg"" alt="""" width=""533"" height=""399"" />Chaka cha chibalalitso chidzachitikira mu tchalitchi limeneli Arkidayosizi ya mpingo wakatolika ya Blantyre yalangiza parish ya St. Pius kuti iyambepo kukonzekera bwino miyambo ya chipembedzo yomwe imachitika pokonzera tsiku la chibalalitso cha mpingowu mu mwezi wa October. +Bambo Alfred Chaima omwe ndi mlembi wa zautumiki mu arkdayosiziyi alankhula izi pambuyo pa ulendo oyendera atsogoleri a parishiyi ndi cholinga chowakonzekeretsa chaka chapadera cha chibalalitsochi. +Iwo apereka pempholi kwa akhristu mu parishiyi kaamba koti Parish yawo ndi yomwe itsogolere mpingo wakatolika mdziko muno mwambo wa Chaka chachibalalitsowu. +Timafuna kuti tikumane ndi adindo komanso ansembe kuno ku st pius parish popeza iwo ndi amene ali pa tsogolo kono kumalawi kuyendetsa chaka chachibalalitso mwezi wa mawa extraordinary mission month, tikuyembekezera zabwino kuchokera ku parish imeneyi malinga ndi mmene apap Francisco akuphunzitsira, anatero bambo Chaima. +Mwazina bambo Chaima ati chakachi kuti chidzakhale chopambana akhristu a mparishiyi akuyenera kuzikonzekeretsa bwino maka ku miyambo yosiyanasiyana ya chipembedzo monga kuwerenga malembo, kucheza ndi ambuye yesu okhala mu sacrament la ukalisiya ngakhalenso kukonzekera kupereka molowa manja chopereka cha pa tsikuli. +",13 +" Amayi tizivulana tokhatokha? Pali zinthu zina zoti mnzako akachita owonawe umazizwa, kuchita kakasi kuti kodi winayo waganiza bwanji? Mwachitsanzo, pali zakudya zina zoti kumuona wina akutafuna, iwe umasowa mtendere. Chimodzimodzi mavalidwe; pali zovala zina zimadabwitsa kuti kodi mayiyu kapena bamboyu analimba mtima bwanji kutuluka mnyumba mwake akuoneka tere. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Nkutheka ichi nchifukwa chake amayi ena ku Lilongwe adadabwapo masiku apitawa ndi mmene mayi mnzawo adatulukira mnyumba mwake atavala mini. + Koma mmalo mongolekera podabwapo, amayiwa adatengera zinthu pamgongo nkumuvula mnzawoyo kuti akhale mbulanda ati nzomwe amafuna. + Kodi anzanga, mmene tachulukira mdziko muno, munthu nkumayembekeza kuti onse achite zofuna zako ndithu? Anthufe takulira kosiyana zomwe zimachititsa kuti kavalidwe kathu, kakonzedwe ka tsitsi ndi zokonda zina zilekane. + Kuonjezera apo, ntchito kapena bizinezi zomwe tikuchita nzosiyana zomwe zimachititsanso kuti maonekedwe athu asiyanenso. + Nthawi ndi nthawi tonsefe timaona ndithu zosatikondweretsa pa matupi a ena. Tsitsi lina ukaliwona umalakalaka utalimeta; magalasi ena wina akavala ngati ukamutaire; wina akakhwefula thalauza ngati ukamukwezere. + Koma izi sizingathandize chifukwa ubwino ndi kuipa timakudziwa mosiyana Pamene wina amakonda kuti miyendo yake ikhale poonekera, wina amati ine yangayi ndiyibise. + Wina akukonda zothina, wina amati koma zotaya. Pamene mnyamata wina akonda chiuno cha thalauza yake chikhale mchimake, wina amati chake chikhale mmusi. + Pozindikira kulekana kwa zofuna za anthu, padakhazikitsidwa ufulu wa kavalidwe kuti aliyense avale umo zingamukomere. Ubwino wake aliyense ali ndi lake thupi lake. + Ndipo malinga ndi malamulo, mphamvu zomwe munthu angakhale nazo pakavalidwe zimathera pathupi lake osati lawina. + Tsono khalidwe lofuna kuti anthu achite zofuna zathu kapena molingana ndi mmene ife tifunira ndilosathandiza komanso lolakwira lamulo. + Izi mwina ukhoza kuchita ndi mwana kapena mbale wako, koma osati munthu wadera ongokumana naye pamsewu. Zilibe kanthu kuti walaula bwanji winayo, mleke. Samala za thupi lako chifukwa ulibiretu mphamvu yokakamiza wina kuti avale mwakufuna kwako. +",1 +" Moto lawilawi mu TNM Super League Ligi ya TNM yafika pa lekaleka pamene matimu ena akutenga mapointi ndipo ena kutaya mwachibwana pamene ligiyi tsopano yalowa sabata ya chinambala 22. + Timu ya Big Bullets yomwe idali timu yokhayo yomwe isadaone kugonja mligiyi yakumana ndi chakuda sabata yatha pamene idapunthidwa ndi asilikali a Airborne Rangers ku Dwangwa komwe Bullets idagonja 2-1. + Chisale watuluka nkumangidwanso Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Kugonjaku kumadza timuyi itatibulidwa ndi Civo United mchikho cha Standard Bank 2-1. Kodi minyamayi ipitiriranso mawa pamene timuyi ikusinjana ndi asilikali a Moyale? Technical director wa Bullets, Billy Tewesa, adati sakuonanso akugonja mmanja mwa Moyale ndipo wati okonda Bullets abwere kudzaonera masewerawo ndipo adzasamba mkaka. + Banja lathu lidazolowera kudyera nyama, ndiye apapa nyama inasowa ndipo timadyera masamba. Koma mukamadyera masamba si zitanthauza kuti simudzadyanso nyama. + Pamene padavuta pakonzedwa, chilichonse tsopano chili mchimake ndipo okonda Maule abwere Lamulungu ndipo adzamwa mkaka, adatero Tewesa. + Mphekesera zamveka kuti timuyi ikufuna kutenga mphunzitsi wakale wa timuyi Kinnah Phiri amene wangobwera kumene kuchokera ku South Africa. + Izi zikudza malinga ndi kugonjaku ndipo lingaliro ndi lakuti timuyi iteteze ligiyi yomwe akuitsogolera ndi mapointi 41 pamasewero 18 ndipo Mafco ndiyo ikutsatira ndi mapointi 34 mmasewero 20. + Lero masewero alipolipo pamene Azam Tigers iswane ndi Be Forward Wanderers pa Kamuzu Stadium. Mumzinda wa Lilongwenso ndiye muli fumbi pamene Civo United ipumunthane ndi Silver Strikers pa Civo. Red Lions yaitana Moyale pa Zomba lero ndipo Blue Eagles yaitananso Kamuzu Barracks pa Nankhaka. +",16 +" ANATCHEZERA Akundikaikira Anatchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndine mtsikana wa zaka 17 ndipo ndili Fomu 4. Ndili ndi chibwenzi chomwe ndakhala nacho miyezi 6 ndipo timakondana kwambiri ngakhale anthu amayesetsa kuti tidane poimba foni ndi kutumiza mauthenga a pafoni zammanja (SMS) pamene sindili naye limodzi. Mnzangayu adayamba wanenapo zogonana kamodzi koma ndinakana ndiye kuyambira pamenepo amati ndiye kuti ndili ndi chibwenzi china chomwe ndimagonana nacho. Ngakhale zili choncho timakondanabe; sanasinthe chikondi chake pa ine ngakhale amalimbikira kunena kuti ndili wina mpaka timafika poyambana. Agogo, nditani kuti asiye kundiganizira zimenezi? Mwana wanga, Ndasangalala kwambiri chifukwa chondilembera kupempha nzeru kuti ndikuthandize kuti bwenzi lakolo lisiye kukukaikira za chibwenzi china. Choyamba ndikuthokoz kwambiri kuti bwenzi lakolo litakuuza zogonana iwe udakana kugonjera chilakolako cha thupi. Apo wadya 10 pa 10. Umenewo ndiye umunthu, mwana wanga. Atsikana ambiri amsinkhu wako agwa mmavuto aakulu chifukwa chovomereza kugonana ali pachibwenzi. Zimachitika ndi zambiri mukamagonana nthawi yoteero isanakwanekutenga mimba, kutenga matenda opatsirana kuphatikizapo Edzi, kulephera kupitirza sukulu ndi zina zotero. Zitakere ndiye kuti wadzionongera tsogolo lako. Ndiye iwe limbikira sukuluyo mpaka upite nayo patali; usalolere zogonanazo mpaka mutalowa mbanja. Ngati cholinga cha chibwenzi chanu nchoti mudzalowe mbanja, mwamuna wako adzakhala wosangalala kwambiri kuti iwe unali wodzisunga kufikira pomwe walowa mbanja. Ukadzangomuvulira ameneyo muli pachibwenzi sadzakhalanso nawe ndi chidwi, ndikuuze. Adzakhala kuti wathana nawe basi ndipo mathero ake adzakusiya. Ndithudi, mtima umenewo usausiye, mwanawe, ndipo kutsogolo udzasimba lokoma! Akuti Ndimusiye Anatchereza, Ndithandizeni. Ndili ndi chibwenzi chomwe chimafunitsitsa banja ndipo ndinavomera zochitenga. Koma poyamba mnzanga ndiye adandifunsirira ndiye pano mnzanga yemweyo akuti mkaziyo ngwachisawawa pomwe poyamba nditamufunsa adati ndi mkazi wabwino. Pano akuti ndimusiye ndipo ndikatenge tanga tonse kwa mkaziyo. Nditani pamenepa? ABWAM, Chiradzulu ABWAM, Chibwenzi sachita kufunsirirana. Inu vuto lanu ndi chiyani kuti mnzanu ndiye azichita kukupezerani mkazi wachibwenzi? Chimene chachitika apa ndi chinyengo basi. Mnzanuyo wakuyendani njomba ndipo sindikukaika kuti wayamba kudyerera maso pa mkaziyo. Naye akumufunanso nchifukwa chake akuti umusiye ndipo ukatenge katundu wako. Koma mwina nditafunsako, kodi inu ndi mkaziyo mudaonanapo nkuchezerana? Mwakhala pachibwenzi nthawi yaitali bwanji? Inu maganizo anu pa mpaziyo ndi otani? Mnzanuyo akamati mkaziyo ngwachisawawa, akutanthauza chiyani? Zili ndi inu kufufuza kuti mudziwe zoona zake za mkazi muli naye pachibwenziyu musanathamange zothetsa chibwenzi chanu chifukwa mwina payenda dumbo ndi kaduka pamenepa. Nthawi zambiri vuto lotuma mnzako kuti akufunire mkazi kapena mwamuna limakhala ngati limeneli. Mudziwa bwanji kuti pofunsirana kuseriko akukhuthulanso zakukhosi kwawo? Dziwani kuti fumbi ndiwe mwini. +",12 +"Flames Iyamba Zokonzekera Lolemba Mphunzitsi wamkulu wa timu yayikulu ya dziko lino ya Flames, Meke Mwase watulutsa ndandanda wa osewera omwe atumikile timuyi pomwe ikuyembekezeka kusewera masewero ake ndi timu ya Burkina Faso mu mpikisano wa maiko amuno mu Africa wa African Cup of Nations pa 26 March 2020 mdziko la Burkina Faso. +Watulutsa mndandanda wa osewera-Mwase Polakhula lero pa msonkhano wa atolakhani omwe unachitikira ku maofesi a bungwe loyendetsa mpira mdziko muno la FAM ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre, Mwase wati osewerawa akuyenera kuyamba zokonzekera zawo lolemba pa 2 March 2020, timuyi isanachite masewera ake opimana mphanvu ndi timu ya dziko la Zambia. +Ena mwa osewera omwe mphunzitsiyi wawayitana koyamba ndi monga Paul Ndovi wa timu ya MAFCO komaso Mphatso Magaleta yemwe amasewera timu ya Ntopwa ndipo chiwerengero chonse cha osewera akuno kumudzi omwe mphunzitsiyu wawayitana ku zokonzekerazi ndi okwana 31. +Mwazina Mwase wati alimbikitsa osewerawa kuti adzachite bwino pa masewero ake ndi timu ya Burkinafaso. +",16 +" APM akuzemba PAC Akatswiri a ndale Othirira ndemanga pa ndale mdziko muno ati zimene mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wachita posakumana ndi a bungwe la Public Affairs Committee (PAC) kuti amve zomwe msonkhano wawo udagwirizana pa za mmene zinthu zilili mdziko muno zikuonetsa kuti mtsogoleriyu akuzengereza dala kuti nkhaniyi izizire ndi kuiwalika. + Aphunzitsi awiri a kusukulu ya ukachenjende ya Chancellor College omwenso ndi anamatetule pa nkhani za ndale, Boniface Dulani ndi Joseph Chunga anena izi msabatayi pothirapo ndemanga pa kulephereka kwa mkhumano wa akuluakulu a bungweli ndi mtsogoleriyu. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akuti mpata sakuupeza: Mutharika Kawiri konse Mutharika wasintha nthawi yokumanirana ndi akuluakulu a PAC ponena kuti ndi wotanganidwa ndi ntchito zina. + Poyankha PAC imayembekezera kukumana ndi Mutharika pa 25 February koma zidakanika ndipo boma lidati mkhumanowu uchitika pa 29 March zomwenso zalephereka. + Mkulu wa bungweli la PAC Robert Phiri wati iwo adafika mumzinda wa Blantyre kuti akumane ndi Mutharika koma mwadzidzidzi adangomva kuti nkhumanoyo yalephereka. + Izi zachititsa kuti PAC ilephere kufotokozera Mutharika zomwe msonkhano wawo, womwe udachitika pa 17 February chaka chino, udagwirizana. + Koma akadaulowa akuganiza kuti Mutharika akungozemba chabe osati watanganidwa ndipo ati izi sizingachitire ubwino anthu amene akuyembekezera mayankho pa mfundo zomwe zikukhudza Amalawi. + Dulani adati zomwe akuchita Mutharika ndi kuzemba chabe ncholinga choti nkhani zomwe zidatuluka ku PAC zizizire ndi kuiwalika. + Akungozemba chabe. Inde, Pulezidenti amakhala wotangwanika, koma sindikukhulupirira kuti angalephere kupeza nthawi yokumana ndi a PAC. + Chomwe tingadziwe, dziko lino lili pamavuto aakulu kotero tikuyenera kupeza mayankho mwachangu ndipo izi ndi zomwe bungwe la PAC lidachita kumva maganizo kwa anthu osiyanasiyana, adatero Dulani. + Koma mneneri wa boma, Jappie Mhango, wati si zoona kuti Mutharika akuzemba, koma kuti mtsogoleriyu amakhala wotanganidwa ndi ntchito zambiri. + A Pulezidenti amayeneradi kukumana ndi a PAC koma sizidatheke chifukwa cha nkhumano zinazo zomwe akuyenera akakhalepo, koma si kuti akuthawa, ayi, adatero Mhango. + Mhango wati tsiku lomwe akumane ndi akuluakulu a PAC awadziwitsa akuluakuluwa koma izi zichitika Mutharika akakhala ndi mpata wotero. + Kadaulo wina pandale ku Chancellor College, Joseph Chunga, wati Mutharika ali ndi nthawi yambiri yomwe angakwanitse kukumana ndi PAC koma izi zikungoonetsa kuti sakufuna. + Ndikuganiza kuti mtsogoleriyu akungofuna kugula nthawi kuti akonze zomwe PAC idakambirana ncholinga choti pamene azikumana nawo akhale atakonza zinthu zina, adatero Chunga. + Chunga watinso Mutharika adauzidwa kale ndi akuluakulu a boma amene adali nawo pamsonkhanowo za zomwe adakambirana. + Si kuti sakudziwa zomwe zidakambidwa, zidali mmanyuzipepala komanso nduna zake zikuyenera kuti zidamufotokozera, komabe ngakhale izi zili chonchi, akuyenera kukumana ndi a PAC chifukwa ndi oima paokha, adaonjeza. + Msonkhano wa PAC mwa zina udagwirizana kuti Mutharika akonze zinthu pano. Izi ndi monga kusowa kwa chimanga. Zinanso zomwe adagwirizana nkuti boma lichotse zinthu zina zomwe likuchita pofuna kupeza mavoti monga kukweza mafumu ndi pologalamu yomangira anthu nyumba ya Cement and Malata Subsidy. +",6 +"Brother Dostie a Chipani cha Marist Amwalira Aku likulu la chipani cha Marist Brothers kuno ku Malawi, alengeza za imfa ya Brother Fernand Dostie. +Malingana ndi mkulu wa chipanichi Brother Francis Jumbe, Brother Dostie amwalira lamulungu pa 21 June 2020 ku chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe atadwala kwa nthawi yayitali nthenda ya Khansa. +Mwambo woyika mmanda thupi la malemu Brother Dostie uchitika lachitatu, pa 24 June 2020 ku Marist Secondary School (Mtendere Campus) mboma la Dedza. +Malinga ndi brother Jumbe, amaene adzatsogolere mwambowu ndi arkiepiskopi wa arkidayosizi ya Lilongwe, Ambuye Tarcizio Ziyaye ndipo ati palinso chiyembekezo chakuti Ambuye George Desmond Tambala a dayosizi ya Zomba komanso episkpi opuma wa arkidayosizi ya Lilongwe ambuye Remi Ste Marie akakhala nawonso pa mwambowo. +Iwo ati potsatira njira zopewera mliri wa Coronavirus, anthu ochepa okha ndi amene akapezeke ku mwambowu. +Brother Fernand Dostie amwalira ali ndi zaka 87 zakubadwa ndipo akhala akugwira ntchito kuno ku Malawi kuyambira chaka cha 1962. +Mzimu wa Brother Fernand Dostie uwuse mu mtendere wosatha. +",14 +" Zinthu zitatu mu nkhuku imodzi ya Mikolongwe Katswiri wa ulimi wa ziweto wa ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Timothy Gondwe wati kukhala ndi nkhuku ya Mikolongwe imodzi ndi chimodzimodzi kukhala ndi nkhuku zitatuyanyama, yachikuda ndi yamazira. + Nkhuku ya Mikolongwe imafika makilogalamu 4.5 Iye adati nkhuku ya Mikolongwe imakula kwambiri, imaikira mazira ambiri, komanso kukoma kwa mazira ndi nyama yake ndi chimodzimodzi nyama ndi mazira a nkhuku yachikuda. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nkhuku ya Mikolongwe imakula kwambiri moti tambala mpaka amafika makilogalamu 4.5 pamene thazi amatha kulemera makilogalamu 4 pa miyezi 4 kapena 6 yokha. + Pachaka nkhuku ya Mikolongwe imaikira mazira apakati pa 200 ndi 250, adatero Gondwe. + Kuonjezera apo, katswiriyu adati mlimi atha kukwatitsa anapiye ake ndi a nkhuku zachikuda kuti akhale nkhuku zolimba komanso zopirira ku matenda. + Gondwe adati ichi nchifukwa chake nkhukuzi zikhoza kuwetedwa kumudzi ndikumabweretsa phindu lochuluka. + Malingana ndi katswiriyu, nkhuku zokwatitsazi zimakula ndi kuikira mazira ambiri oposa azachikuda. + Mazira ake amaposa a nkhuku zachikuda ndi magawo a pakati pa 20 ndi 30 pa 100 aliwonse ndipo zimatha kuikira okwana 200 pachaka, iye adatero. + Gondwe adati izi zimathandiza mlimi kupeza nyama yochuluka ndi mazira ambiri choncho ndalama, komanso ndiwo sizisowa pakhomo. + Mlangizi wa ziweto wa ku Blantyre Agriculture Development Division (Bladd) John Pirate Kothowa adati ngakhale nkhukuzi zimakula, komanso kuiikira mazira ochuluka nzosiyana kwambiri ndi zachikuda mchikhalidwe chake. + Iye adati ichi nchifukwa chake zimatha kumayenda nkumadzitolera zokha chakudya. + Chifukwa choti zimatenga nthawi yotalikirapo kuti zikule, kuziweta ngati zachizungu pomazidyetsa chakudya chogula nkudzichepetsera phindu, adatero Kothowa. + Gondwe adati alimi akumidzi akhoza kuweta nkhukuzi ngati momwe amawetera zachikuda, koma zimafunika kumazipatsa chakudya choonjezera mmawa, masana ndi madzulo. + Iye adati chakudyachi ndi monga gaga wothira mchere pangono ndipo ngati pali zakudya zina za mgulu la nyemba, azisakanizako gawo limodzi mwa magawo atatu aliwonse. + Katswiriyu adafotokoza kuti mlimi aziika chakudyachi pafupi ndi khola kapena pamene nkhuku zimakonda kudutsapo zikamapita kukadya. + Pambali pa chakudya pazikhala madzi akumwa aukhondo kuti zizimwa momwe zafunira. + Mlimi azitsatira dongosolo lonse la katemera wa chitopa kuti zikhale zotetezeka, iye adatero. + Gondwe adafotokoza kuti khola lizikhala lotakasuka, louma, lolowa bwino mpweya ndipo ngati nkotheka la mmwamba chifukwa ndi lomwe nkhuku zoyendayenda zimakonda. + Katswiriyu adafotokoza kuti alimi amtauni omwe amatha kupeza mwayi oweta nkhuku zokwatitsa, akhoza kumazipatsa chakudya chopanga okha kapena chogula cha nkhuku za mazira, koma chizingokhala choonjezera chabe. + Iye adati izi zili choncho chifukwa nkhuku za Mikolongwe zimadana ndikutsekeredwa mkhola. + Lastseen Jonamusi ndi mmodzi mwa alimi a nkhuku za Mikolongwe mu mzinda wa Blantyre wayamikira ulimiwu kuti ndi wabwino. + Iye adati adayamba kuweta mu December chaka chatha koma padakali pano zakula kale. + Pano maso ali kunjira kudikirira tsiku lomwe ziyambe kuikira mazira kuti ndiyambe kudyerera, adabwekera motere mlimiyu. +",4 +" Akana nyau yogwiririra Senior Chief Lukwa, mmodzi mwa mafumu akuluakulu a Achewa mdziko muno, yemwenso amayankha pankhani za mafumu, wati munthu yemwe khothi mboma la Dedza lidamupeza wolakwa pamlandu wogwiririra si wagulewamkulu monga momwe iye adakonzera kuti zioneke. + Khothi la Dedza, lomwe wogamula wake adali First Grade Magistrate Enett Banda, lidapeza Lazaro Maxwell, wa Zaka 19, wolakwa pamlandu wogwiririra mtsikana wa zaka 14 atadzizimbaitsa ngati gulewamkulu kuti asadziwike ndipo lidagamula kuti akagwire ndende yakalavulagaga kwa zaka 8. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Achewa amalemekeza gulewamkulu chifukwa ndi gule wa mizimu Malingana ndi apolisi mbomali, Maxwell adavomera mlanduwo mbwalolo ndipo woimira boma pamlanduwo, Inspector Wedson Nyondo, adapempha bwalololo kuti lipereke chilango chokhwima kwa wopalamulayo kaamba koti woyimbidwa mlanduyo adanyozetsa chikhalidwe cha Achewa. + Mpofunika kulingalira kuti munthuyu wanyazitsa chikhalidwe cha Achewa chomwe eni ake amateteza kuyambira kalekale kotero, nkofunika kumpatsa chilango chokhwima kuti zotere zisamachitikechiteke, adatero Nyondo. + Poperekapo maganizo ake pankhaniyi, Senior Chief Lukwa adati munthu yemwe adachita izi si wagulewamkulu yemwe amadziwika kuti ndi gule wa mizimu, koma munthu wazifukwa za mtopola wofuna kunyazitsa Achewa. + Lukwa: Umenewo ndi mtopola Uwu ndiye timati mtopola. Mdziko muli khalidwe lolemekezana ndi kulemekezerana miyambo ndi zikhulupiriro zoyenera ndipo Mchewa weniweni sangachite zimenezi. Ameneyu ndi munthu wongofuna kuononga mbiri yabwino ya Achewa, adatero Lukwa. + Iye adati khothi lomwe lidagamula mlanduwo lidachita bwino kumulanga chotero kuti iye ndi ena anzeru zangati zakezo atengerepo phunziro lolemekeza mitundu ndi miyambo a anthu. + Malingana ndi umboni umene udaperekedwa mbwalo la milandulo, pa 8 mwezi womwe uno, Maxwell ndi mnzake wina yemwe sadatchulidwe adadziveka ngati gulewamkulu pomwe adakumana ndi msungwana wogwiririridwayo patchire lina lomwe limalekanitsa midzi ya Bowazulu ndi Kalipande. + Umboniwo udapitirira kenena kuti msungwanayo atangodutsana ndi gulewamkuluyo, Maxwell adayamba kumuthamangitsa ndipo atamugwira adamukokera patchire nkumugwiririra. + Poti wogwiririrayo adali mchigoba, msungwanayo adati munthu woyambirira kumuganizira adali Maxwell chifukwa adakhala akumuvutitsa kuti amamufuna chibwenzi koma amamukana ndipo nkhaniyi itafika kukhothi iye sadataye nthawi koma kuvomera mlanduwo. + Mlandu wogwiririra mwana wamngono umatsutsana ndi ndime 138 ya malamulo ogamulira milandu ndipo munthu akapezeka wolakwa, chilango chake chachikulu ndi zaka 14 akugwira ntchito yakalavula gaga kundende. + Maxwell amachokera mmudzi mwa Chatondeza pomwe msungwanayo amachokera mmudzi mwa Kalipande kwa T/A Chilikumwendo mboma la Dedza. +",7 +"Bishop Tambala Apempha Boma Liyike Ndalama Zokwanira Polimbana ndi Coronavirus Episikopi wa dayosizi ya mpingo wa katolika ya Zomba Ambuye George Desmond Tambala wapempha boma kuti liyike ndalama zokwanira zomwe zithandizire pa ntchito yolimbana ndi mliri wa Coronavirus. +Tambala: Unduna wa zaumoyo uchitepo kanthu Ambuye Tambala anena izi polankhula ndi Radio Mari Malawi. Malinga ndi Ambuye Tambala, boma likuyenera likonze ntchito zaumoyo mdziko muno kaamba koti padakali pano munthu akadwala sangathenso kupita naye kuchipatala cha kunja. +Unduna wa zaumoyo ukuyenera kupeza zipangizo zabwino ndi zokwanira zomwe zithandizire pa ntchito yolimbanirana ndi kuthana ndi matendawa mdziko muno, anatero Ambuye Tambala. +Pamenepa Ambuye Tambala alangiza anthu mdziko muno kuti apitilire kutsatira malangizo omwe a zaumoyo akupereka komanso malamulo omwe boma lakhazikitsa pofuna kupewa nthendayi. +",6 +"Miyoyo ya Akayidi ku Zomba ili pa Chiwopsezo Miyoyo ya akayidi ku ndende ya Zomba ili pa chipsezo kutsatira kuwonongeka kwa khoma komanso denga za ndendeyi. +Mneneri wa ndende za mdziko muno (Malawi Prison Service), Supretendent Chimwemwe Shawa watsimikiza za nkhaniyi polankhula ndi Radio Maria Malawi ndipo wati pali chikonzero chomwe nthambiyi komanso bungwe la European Union likuchita chofuna kusamutsa akayidi omwe ali ku ndendeyi kukawasiya ku ndende ya Chitedze mu mzinda wa Lilongwe. +Ndende ya Zomba Ndendeyi inamangidwa kalekale choncho pofuna kupewa ngozi tinawona kuti pakufunika kuti timangendende ina yomwe idzakhale mlowammalo wa ndende ino kuti ndende ya Zomba tizangoyiyiwala basi tisadzasungekonso akayidi. +Tinayamba kumanga ndende ya Chitedze koma chifukwa cha mavuto ena yachedwa kutha ndipo pano bungwe la EU lalowelerapo kuti ntchitoyi ithe msanga, anatero Supretendent Shawa. +Miyoyo yawo ili pa chiopsezo Iye wati ndende ya Chitedze ndi yomwe ilowe mmalo mwa ndende ya Zomba. +Supretendent Shawa wati kupatula kuwonongekaku, mu ndendeyi mulinso akayidi ochuluka kaamba koti inamangidwa kuti idzisunga akayidi 850 koma padakalipano muli akayidi oposa 3,000. +",6 +"Akakhala ku Ndende Zaka 7 Kamba ka Mmemo By Thokozani Chapola Bwalo lachiwiri la milandu ku Limbe mu mzinda wa Blantyre lalamula bambo wina wa zaka 22 Chikondi Lester kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavulagaga kwa zaka zisanu ndi ziwiri kamba komu peza olakwa pa mulandu wovulaza mzake kamba ka mmemo. +Malinga ndi wapolisi wotengera milandu ku khoti pa polisi ya Limbe, Ian Ntaba anauza bwalo la milandu kuti pa 8 June, gulu la anthuwa linkagwira ganyu pa nsika wa Machinjiri ndipo nthawi ya nkhomaliro itakwana adagwilizana kuti asonkhe koma Briton Mchetsera wa zaka 24 zakubadwa sanakwanitse kusonkha koma kuti analoledwa kuti adye nawo chakudyacho zomwe zinakwiyitsa a Lester ndipo anafika pokankha ndi kuvulaza mzawoyi pomugenda ndi duka. +Anthu akufuna kwa bwino ndi omwe anatengera bamboyu kuchipatala cha Queen Elizabeth komwe anakathandiza mkulu-yi. +Yemwe wapereka chigamulochi ndi Second Grade Magistrate George Chimombo. +",7 +" Tidagwirizira ukwati wa mnzathu Akuti wokaona nyanja adakaona ndi mvuu zomwe. Naye wokagwirizira ukwati wa mnzake, adakapezako banja. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izitu zikupherezera pa wolemba nkhani wa Times Group ku Mzuzu, Sam Kalimira, yemwe adakumana ndi bwenzi lake Chisomo Makupe pogwirizira ukwati wa mnzawo. + Awiriwa adavinira limodzi paukwatiwo. + Udali mwezi wa August, mchaka cha 2014, pomwe Kalimira adamuona koyamba Chisomo patchalitchi cha CCAP cha Mchengautuwa mumzinda wa Mzuzu. + Monga achitira atsikana ambiri, Chisomo adali pakagulu ka atsikana anzake. Chisomoyutu adali atachokera ku Lilongwe komwe amakhala kudzagwirizira ukwatiwu. + Ngakhale akuti adalibe maganizo omufunsira, koma pansi pamtima adayamikira ndithu kuti namwaliyu ndi mkazi wabwino. + Ndikulonjeza: Sam kuveka mphete Chisomo patsiku la chinkhoswe chawo Nditangomuona, mumtima mwanga ndidadziuza kuti namwaliyu ndi mkazi wabwino ngakhale ndidalibe ganizo loti ndingamufunsire ndipo tsiku lina nkudzaganiza zomanga naye banja, adatero Sam. + Mwina tingati, mtima wa mnyamayu sudasunthe kwenikweni chifukwa panthawiyo adali ali ndi bwenzi lina lomwe ankalifera. + Koma poti mtima wa mnzako ndi tsidya lina, ubwenziwu udatha ndipo Sam adakhala kwa miyezi yokwana 8 opanda bwenzi. + Apatu adali akulingalira zina ndi zina za moyo maka pankhani zachikondi. Monga mukudziwa kuti nkhani zachikondi ndi zovuta. + Ndidayambanso kulingalira zopeza mkazi womanga naye banja, ndipo mwachisomo cha Mulungu maganizo a Chisomo adandibwerera, adatero Kalimira. + Apa ndi pomwe mwana wammuna nzeru zidamuthera chifukwa adali atapanga ubale wa pachilongo ndi Chisomo. + Kalimira adalongosolera Msangulutso kuti awiriwa ankaitanana kuti achimwene ndi achemwali. + Komabe monga mphongo, Sam adachita zotheka kuthetsa zachilongozo ndi kumufunsira namwaliyo. + Tsoka ilo, adakanidwa. + Komabe nditayesayesa mwawi adandilola ndipo chibwenzi chidayamba mwezi wa August 2015, adalongosola motero Kalimira. + Awiriwa sadachedwetsenso koma kupangiratu mwambo wa chinkhonswe nkuyamba kukonzekera zomanga banja. +",1 +"Papa Wayamikira Bungwe Lowona Zapamadzi Kamba Kofalitsa Mthenga Wabwino Wolemba: Thokozani Chapola diomaria.mw/wp-content/uploads/2019/08/francis.jpg 308w"" sizes=""(max-width: 300px) 100vw, 300px"" />Papa Francisko Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse PAPA FRANCISCO lolemba wayamikira bungwe la INTERNATIONAL MARITIME ASSOCIATION kamba kodzipereka pofalitsa uthenga wabwino kwa anthu okhala mu nyanja zikuzikulu pa dziko lonse. +Papa walankhula izi kudzera mu uthenga wpakanena umene watumizira mamemba a bungweli omwe ali mkati kuchita msonkhano wawo wa nambala khumi ndi chimodzi (11) mdziko la TAIWAN. +Muuthenga-wo mtsogoleri wa mpingo wakatolika-yu PAPA FRANCISCO wafuniranso zabwino mamembala a bungwe-li ndikuwalimbikitsa kuti asatope koma kudzipereka pa ntchito zawo ndi cholinga choti anthu onse okhala ku madera a ku nyanjadzi azitha kupeza uthenga wabwino mosavuta. +Bungwe la INTERNATIONAL MARITIME ASSOCIATION analikhadzikitsa mchaka cha 1969 ndi cholinga choti lidzithandiza kufalitsa uthenga wabwino kwa anthu okhala mmadera a ku nyanja zikuluzikulu pa dziko lonse, moti mwa zina ku msonkhanowu awunikira momwe bungwe-li lagwilira ntchito zake mu zaka 50 zapitazi. +Msonkhano-wu wayamba lero pa 21 ndipo udzatha pa 25 OCTOBER 2019. +",13 +" Atenge ligi yaTNM ndani? Akatswiri pa zamasewero ndiye akamba, aphunzitsi nawo ndi ochemerera alosera zambiri koma kamuna adziwika lero nthawi ikamati 4:00 madzulo ano. + Zonse ndi lero pamene timu ya Big Bullets ndi Moyale Barracks akumane lero pa Kamuzu Stadium masewero amene angadziwitse katswiri wa ligi ya TNM ya chaka chino. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Bullets ili ndi mapointi 56 ndipo yatsala ndi masewero awiri, oyamba ndi a lero ndipo imalizitsa sabata ya mawa ndi Blantyre United yomwe yatuluka mu mligiyi. + Moyale ili ndi mapointi 53, nayonso yatsala ndi magemu awiri, yoyamba ndi ya lero ndipo imalizitsa ndi Blue Eagles yomwe ikuphupha kuti ithere panambala 3 mligiyi. + Ngati Moyale ipambane lero ndiye kuti ligiyi tidikirabe sabata yamawa kuti ithe pamene matimuwa akudzasewera masewero awo womaliza. + Kulepherana mphamvu kwa matimuwa lero kapena ngati Bullets ipambane zipereka chilimbikitso kuti Bullets yatenga ligiyi. + Izi zikusonyeza kuti Moyale ikuyenera kupambana masewero alero ngatidi yathemba zotenga ligiyi. Moyale ikapambana ndiye kuti nkhondo ikhala pa zigoli zochinya ndi zochinyitsa komanso mapointi atatu amene atsala mmasewero asabata ya mawa. + Bullets yachinya zigoli 41 ndipo yachinyitsa zigoli 18. Moyale yachinya zigoli 43 ndipo yachinyitsa zigoli 22. Izi zikutanthauza kuti Moyale ikachinya Bullets ndi chigoli chimodzi komanso kudzachinya Eagles ndi chigoli chimodzi ndiye kuti Bullets ikuyenera kudzachinya Blantyre United ndi zigoli zoposa ziwiri kuti itenge ligi. + Apa nchifukwa ligiyi ili ya masamu zomwe Nicholas Mhango wa Moyale komanso Elijah Kananji wa Bullets akunenetsa kuti ndi bwino kupambana kuti nkhondoyi ichepe. + Masewero andime yoyamba, Bullets idapambana ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi ndipo masewerowa adachitikira ku Mzuzu. Lero ndi Kamuzu Stadium yomwe inyamule ntchitoyi. +",16 +" Kusanthula ntchito ya fisi Miyambo ya makolo ndi yambiri ndipo ina akuti siyofunika kupitirira chifukwa ikuthandizira kufalitsa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi. Sabata yathayi, mafumu adali ndi msonkhano mumzinda wa Lilongwe wokambirana za miyambo. Umodzi mwa miyambo yomwe ikukanidwa ndi mwambo wa fisi omwe ambiri amausokoneza ndi mwambo wa kusasafumbi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu pa zamwambowu. Adacheza motere: Lukwa: Mafumu tikuthana ndi miyamboyi Gogo tandimasuleni eti mwambo wa fisi ndi mwambo wanji? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Pamwambowu munthu amalembedwa ganyu yobereka ana mnyumba ya munthu yemwe zikumukanika. Imakhala ganyu ngati kuti munthu wagula galimoto koma satha kuyendetsa ndiye amalemba munthu yemwe amatha kuyendetsa kuti azimuyendetsera nkumulipira. + Basi? Nanga Fisi uja amalowa mnyumba yoti mwini wake wamwalira kapena asungwana akuchoka kutsimba ndi uti? Choyamba ndikonze kuti amene uja si fisi. Umene uja ndi mwambo wa kuchotsafumbi. Fisi ndi pokhapokha ngati wina akulephera kubereka ana mnyumba ndiye pofuna kuti asachite manyazi mmudzi, amalemba fisi kuti amuberekere mwana kapena ana koma zimakhala zachinsinsi zongodziwa bambo, mayi ndi fisiyo basi. + Nanga kusasafumbi nkutani? Ndikufunatu ndimvetsetse. Kusasafumbi kuli pangapo. Nthawi zina mwamuna akamwalira, mnyumbamo mumabwera mwamuna wina kudzagona ndi mai osiyidwayo akuti kugoneka mzimu wa malemuyo. Nthawi zina mkazi akachotsa pakati kapena anamwali akamachoka kutsimba, amatenga mwamuna woti agonane nawo pokhulupirira kuti kutero ndiye kuti ayendetsa mwambo momwe uyenera kukhalira. + Malipiro ake amakhala chiyani? Zimatengera pangano la awiriwo, ena amatha kulipirana mbuzi kapena nkhuku mwinanso ndalama. Apa palibe dipo lenileni lokhazikika chifukwa nzachinsinsi moti ozidziwa amakhala okhawo okhudzidwa. + Nanga pambuyo pake fisi atatembenuka kuti akufuna ana ake zingathe bwa? Ichi nchibwana chachikulu chifukwa potengera momwe mwambowu umayendera, iye akagwira ntchito pathupi nkuoneka, akangolandira zake basi kwatha zammbuyo muno nza eni nyumbayo. Kuchita masewera, akuluakulu akhoza kugwirapo ntchito chifukwa woteroyo waphwanya mwambo wachinsinsi omwe adavomereza yekha. + Boma ndi mabungwe amati miyambo yotereyi ndi yoipa makamaka nkubwera kwa kachilombo koyambitsa matenda a Edzi, muti bwanji? Zimenezo nzoona zokhazokha moti mafumu kuyambira ku Chitipa mpaka ku Nsanje, Nkhotakota mpaka Mchinji tidagwirizana chimodzi kuti mmadera mwathu miyamboyi isamachitike. Tidachita izi dala chifukwa omwe amazunzika kwambiri ndi amai ndi asungwana chifukwa kumatheka bambo mmodzi kusasafumbi asungwana kapena amai angapo choncho matenda a Edzi sangathe ayi. + Nanga poti mwambo ndi mwambo, mungathe kuwaletseratu anthu? Mfumu siyilephera makamaka pomwe ikutsogolera anthu ake pachinthu chabwino. Monga ndanena kale, mafumu tidamanga fundo imodzi moti kumupeza wina akuchita khalidweli, timamulanga potengera malamulo omwe tidamanga komanso timaonetsetsa kuti onse okhudzidwawo akayesedwe kuchipatala ngati sadavulazane ndi matenda. +",1 +" Mandela alowa mmanda mawa Galimoto yonyamula thupi la Mandela kutuluka kuchipatala cha asirikali Thupi la mtsogoleri woyamba wachikuda wa dziko la South Africa, Nelson Mandela, likuyembekezeka kulowa mmanda mawa kumudzi kwawo ku Qunu mdzikolo. + Mandela, yemwe adali ndi zaka 95, adatisiya Lachinayi sabata yatha atadwala kwa nthawi ndipo maliro ake adakhudza anthu ambiri padziko lapansi. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pamwambo wokumbukira ntchito yaikulu imene Mandela adaigwira polimbana ndi tsankho, umene udachitika Lachiwiri mumzinda wa Johannesburg mdzikolo, padafika atsogoleri oposa 90 a maiko osiyanasiyana a dziko lapansi, kuphatikizapo mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda. Kuchikumbukirocho, chimene chidachitikira kubwalo la za masewero la FNB, kudafika anthu oposa 90 000. + Atsogoleri osiyanasiyana, kuphatikizapo Barack Obama wa dziko la United States, komanso mlembi wamkulu wa mgwirizano wa maiko la United Nations Ban Ki Moon ndi ena ambiri adatamanda Mandela chifukwa cha kulimba mtima kwake, kutsata chilungamo, kukhululuka ndi kulemekeza ena. + Mandela adatiphunzitsa mphamvu ya kuchita komanso maganizo. Inde, ubwino wolingalira mwakuya ndi mtsutso. Ubwino wounikira momwe amene timagwirizana nawo ngakhalenso amene sitigwirizana nawo akuchitira zinthu zawo. Adationetsa kuti palibe ndende yozinga malingaliro kuti ngakhale chipolopolo cha maliwongo sichingafafanize maganizo, adatero Obama. + Lero, asirikali akuyembekezeka kunyamula thupi la Mandela kupita ku Qunu kuchoka ku Pretoria kumene anthu a maiko osiyanasiyana akhala akuona nkhope komaliza kuyambira Lachitatu. + Mandela adabadwa mchaka cha 1918 ku banja lachifumu wa mtundu wa Thembu. Iye amadziwika ndi maina aulemu monga Madiba komanso Rolihlahla (kutanthauza kuti munthu wovuta). Omukonda enanso amamutchula kuti Tata (kutanthauza kuti Tate mChichewa). + Iye adali mchipani cha African National Congress (ANC) chimene chidalimbana kwambiri ndi tsankho mdzikolo. Iye adamangidwa mu ndipo adatulutsidwa mchaka cha 1990. + Ngakhale iye adazunzidwa zaka 27 kundende ya Robben Island, imene ili mkatikati mwa nyanja ya mchere ya Indian Ocean, iye sadabwezere choipa ndipo sadafune kuimanso pampando wa pulezidenti mu 1999, pamene Thabo Mbeki adalowa mmalo mwake. + Mandela adakwatirapo katatu. Mkazi wake woyamba adali Evelyn Mase mu 1944 ndipo kenako adatengana ndi Winnie Madikizera-Mandela mu 1958 ndipo ukwati wawo udatha mu 1996. Mchaka cha 1998, Mandela adakwatira Graa Machel, yemwe adali mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko la Mozambique, malemu Samora Machel. + Atachoka ku mwambo wokumbukira ntchito za Mandela, mtsogoleri wa dziko lino adalowera ku Kenya kukakhala nawo pamwambo wokumbukira ufulu wa dzikolo. Iye akuyembekezeka kukakhala nawo kumwambo woika mmanda Mandela mawa. + Malinga ndi mneneri wa ku nyumba ya boma Steve Nhlane, maulendowa akulipiridwa ndi anthu akufuna kwabwino. +",15 +" Mafumu akuopa Ebola Boma likuyeza anthu kubwalo la ndege, nanga oyenda pansi? Mantha a matenda a Ebola agwira anthu okhala mmalire a dziko lino, pamene anthu othawa mmaiko awo akulowabe mdziko muno ngakhale nthendayi ikupitirira kufala. + Izi zapangitsa mafumu a mmabomawa kupempha Unduna wa Zaumoyo kuti ukhwimitse chitetezo ponena kuti chiyambireni nthendayi undunawu sudafike mmadera awo kuwaphunzitsa za matendawa. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mwachitsanzo, msabatayi apolisi mboma la Karonga kwa Paramount Kyungu adagwira anthu 52 othawa mmaiko awo amene adalowa mdziko muno popanda zitupa. + Senior Chief Kalonga ya mbomalo ikuti anthu mbomalo ali ndi mantha chifukwa cha anthuwa. Kunoko sikuli bwino, pafupifupi tsiku lililonse kukulowa anthu mophwanya lamulo. Vuto lakenso akagwidwa akupatsidwa chilango chochepa zomwe sizikupereka mantha kwa anthuwa. Mantha athu ndiwoti kodi anthu amenewa ali bwinobwino? Ngati ali ndi matenda a Ebola satipatsira? wadandaula Kalonga amene wati kwinanso komwe kwachuluka mchitidwewu ndi ku Chitipa. + Iye adati ambiri olowa mdzikomo amachokera ku Tanzania koma ambiri mwa iwo amakhala ochokera maiko a DRC, Burundi, Rwanda, Ethiopia ngakhalenso Somalia. + Naye Senior Chief Nthache ya mboma la Mwanza ndi Kabunduli ya mboma la Nkhata Bay akuti mmaboma awo chitetezo sichili bwino zomwe ati zingalowetsa matendawa mosavuta mdziko muno. + Kungoyambira pachipata cha Chitipa, Karonga mpaka kutsidya kwa Nkhata Bay mpaka ku Likoma chitetezo mulibe. Mmene mabwato amayendera kuchokera pa Likoma, umangozindikira anthu alowa mdziko muno, adatero Kabunduli. + Tili pachiopsezo chachikulu chifukwa chiyambireni nthendayi unduna wa zaumoyo sudafike kuno. Sitikudziwa kuti munthu wa Ebola amaoneka bwanji ndipo tingaipewe bwanji. + Mfumuyi yati ikuchita mantha ndi phiri lina ku Tukombo moyandikana ndi nyanja komwe ati ndiko kumafikira anthu othawa kwawo pafupifupi tsiku lililonse. + Naye Nthache akuti boma la Mwanza limalandira anthu ambiri amene akutulukira mdziko la Mozambique koma anthuwa sakupimidwa ngati ali ndi matendawa. + Timalandira anthu ambiri kuchokera ku Zobue mdziko la Mozambique komanso anthu a ku Malawi kuno akumapita kumeneko mosaunikidwa kuti abwera bwanji. Zikutipatsa mantha. Vuto lake sitikudziwa za matendawa monga momwe tingawapewere komanso momwe tingatengere, adatero Ntchache. + Sabata yatha undunawu udayamba kukhwimitsa chitetezo mmabwalo a ndege kuti anthu amene akulowa mdziko muno azipimidwa. + Nanga undunawu ukuchitanji pothana ndi anthu amene akulowa mdziko muno mozemba? Mlembi mu undunawu, Chris Kangombe, akuti anthu asachite mantha chifukwa ayamba kalikiliki wofikira maboma onse. + Tayamba kudziwitsa anthu za matendawa kudzera mmawailesi komanso mnyuzipepala. Takhala tikufika mmaderawa kudziwitsa anthu za matendawa, adatero Kangombe. + Anthu akaona othawa kwawowa azikadziwitsa apolisi komanso kudziwitsa amene amaona za anthu otuluka ndi olowa mdziko muno kuti aliyense wolowa azipimidwa. + Koma anthu amene amapereka maganizo awo poimba foni pawailesi ya Matindi Lachiwiri amapempha undunawu kuti uchitepo kanthu. + Anthuwa amene ambiri amayimbira kuchokera mmaboma a Mulanje, Nsanje, Chikwawa, Blantyre, Phalombe, Mwanza, Neno ndi ena amati chiyambireni matendawa sadauzidwe kanthu ndi aundunawa. + Matenda a Ebola apha kale anthu oposa 1 200 makamaka maiko a kumwera kwa Africa a Nigeria, Liberia, Sierra Leone ndi Guinea. + Matendawa alibe mankhwala koma akatswiri ena akuyeserayesera kupeza mankhwala a matendawa. + Pofika kuchokera ku Zimbabwe Lachiwiri, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adati padakalipano palibe ndalama zapadera zimene zaikidwa kuti zithandindire kuthana ndi matendawa ngati atalowa mdziko muno. +",6 +" Nkhawa akafuna kudzathandiza Ngati satenga madzi kunyumba, amavutika akafuna kuchita chimbudzi chifukwa kumalo awo antchito kulibe madzi. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ichi ndi chibalo chomwe ogwira ntchito kunthambi yosunga katundu wa boma ku Blantyre, Central Government Stores, akuchita chifukwa bungwe la Blantyre Water Board (BWB) lidadula madzi mu March chaka chino. Apa nkuti madziwo atangotuluka mu January ndi February kuchokera pamene adadulidwa zaka zitatu zapitazo. + Mmodzi mwa ogwira ntchito paofesiyo yemwe adakana kutchulidwa dzina adati atopa kutenga madzi mmakomo mwawo kukagwiritsa ntchito kuchimbudzi. + Mabikiri a madzi akumachoka kunyumba Ena sakubwera kuntchito chifukwa cha vutoli ndipo tipita kutchuti nkudzabwera akayamba. Munthu ngati satenga madzi amadzipana kapena kukalipira ku Wenela. Palibe kuchitira mwina chifukwa zimbudzi ndi zamadzi, si zokumba, iye adatero. + Wogwira ntchito wina adati ukhondo ukulephereka ndipo miyoyo ili pachiopsezo kaamba koti madzi omwe amabweretsa anthu sakwanira. + Patsikulo, zidadziwikiratu kuti pamalowa nkhani yodzithandiza ku chimbudzi ndi yovuta. Pomwe mtolankhaniyu amatengeredwa kuchipinda chosungira mbendera, amayi ena amachenjezana zosamala madzi adabweretsa ponena kuti ndi wochepa ndipo udali uli 10 koloko mmawa. + Mtolankhaniyu atapempha malo okazithandizira adalowetsedwa mu chimbudzi cha amayi chomwe adati ndi cha ukhondo kaamba koti amabweretsa madzi tsiku lililonse. + [Monga kasitomala] Asakaone nyasi ku chimbudzi cha abambo chifukwa sasamalako. [Abambo] kufooka kutenga madzi kuzisokoneza chisamaliro cha amuna ogula katundu, adatero mayi wina. + Mchimbudzimu mudali bigiri ya madzi ndi mwaukhondo, koma ntchentche zikuwetedwa gawo la abambo komwe nyansi zikudzadza mtondo wa chimbudzi. + Mu zaka ziwirizo, anthuwa amagwiritsa ntchito zimbudzi za bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) komwe adawaletsa chifukwa amachulukitsa ndalama yolipirira madzi ku BWB pa mwezi. + Ngakhale adatiletsa, mmimba mukawira timakangocheza ku MEC komweko. Vutoli likusokoneza madongosolo achuma chathu chifukwa kupatula kudya tikufunika ndalama ya chimbudzi, adatero bambo wina. + Pothirira ndemanga pankhaniyi, mneneri wa BWB, Priscilla Mateyu adati vuto ofesiyi siyimalipira ndalama yogwiritsira ntchito madzi. + Iye adati sanganene ndalama zomwe CGS ikuyenera kupereka ngati njira yolemekeza ufulu wa kasitomalayu. + Naye mneneri ku nthambi ya chuma cha boma, Alfred Kutengule, adati zangovuta kagwiritsidwe ntchito ka ndalama ku CGS, koma amalandira ndalama ngakhale zolipirira madzi. +",15 +"Future Vision Yapereka Zipangizo Zopewera Coronavirus Mdera la Sinuzi Bungwe la Future Vision International lazindikiritsa anthu mdera la Sunuzi mmudzi mwa mfumu Taulo kwa mfumu yaikulu Ngwelero mboma la Zomba, njira zabwino zolimbikitsira ukhondo pofuna kupewa kutenga ndi kufalitsa kachirombo ka Coronavirus. +Mkulu wa bungweli mdziko muno a Newton Sindo yemwenso ndi wapampando wa mabungwe omwe si a boma ku Zomba walankhula izi mdelaro pomwe bungweli limapereka zipangizo zosambira mmanja, monga ndowa ndi sopo kwa anthu a kwa a mdela la mfumuyi mbomalo. +Iwo ati kachilombo ka Coronavirus ndi kopeweka, choncho ndi kofunika kumatsatira mfundo zomwe akuluakulu a zaumoyo akulimbikitsa pofuna kupewa kutenga kachilomboka. +Coronavirus ndi yotheka kuyipewa pokhapokha nmgati titsatira bwino ndondomeko zones zaukhondo. Tikukhulupilira kuti zipangizo zimenezi zilimbikitsa ukhondo mdera lino, anatero a Sindo. +Polankhulanso a Group Village Headman Taulo a mdelaro, ati adzipereka polimbikitsa mafumu anzawo za kapewedwe kamatendawa. +",6 +" K85 000 kapena chaka kundende atapha galu Ena amangopha agalu koma sapatsidwa chilango, koma khoti la Ulongwe Majisitireti ku Balaka lalamula kuti mfumu ina ilipe K85 000 apo ayi, ikakhale kundende chaka chimodzi kaamba kopha galu ndi kuwononga mmera mdimba la mkulu wina. + Malinga ndi mneneri wa polisi ya Balaka, Joseph Sauka, mfumuyi ndi Peter Kasanga koma dzina lake lenileni ndi Michael Mailosi, wa zaka 62. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Sauka adauza Tamvani msabatayi kuti nyakwawayi pa 19 March chaka chino idapezeka mdimba la Yona Nansambo ikuswa malambe. Poswapo akuti idawandanso chimanga cha mkuluyu. + Iye adati Nansambo atadzudzula mfumuyi kuti isiye zimene imachita mdimbamo, iyo idakula mtima ndipo idayamba kuthafulira mwini dimbali ndipo ndewu idabula pakati pa awiriwa. + Achibale 6 a mfumuwo akuti atamva kuti mfumuyi ikugogodana ndi munthu, adathamangira kudimbako komwe adakalowerera ndewuyo. + Bwalo la milandu lidamva kuti anthuwo sadalekere pomwepo koma adalonda mwini dimbayu kunyumba kwake komwe adakaswa galasi la galimoto komanso kupha galu, adatero Sauka. + Kubwaloko, anthuwa adakana za mlandu wopha chiweto malinga ndi gawo 343 la malamulo a dziko lino, komanso adakana mlandu wowononga galimoto malinga ndi gawo 344. Koma bwalo litabweretsa mboni, anthuwa adapezeka ndi mlandu. + Wapolisi woimira boma pamlanduwo, Sergeant Yohane Chaomba, adapempha bwalo kuti lithambitse mfumuyi ndi chilango chokhwima chifukwa monga mfumu sidaonetse chitsanzo chabwino. + Sauka adati mfumuyi idapempha bwalo kuti limumvere chisoni chifukwa ndi yokalamba komanso kuti mkazi wake akudwala. + Koma Third Grade Magistrate Peter Mkuzi adalamula mfumuyi kuti ilipe K60 000 powononga komanso K25 000 popha galu, apo ayi, akaseweze chaka kundende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga. + Mkuzi adalamulanso abale asanu a mfumuyi kuti alipe K25 000 aliyense, apo ayi, akaseweze kundende miyezi isanu ndi inayi (9). + Omangidwa akuchokera mmudzi mwa Peter Kasonga, kwa T/A Kalembo mbomalo. Pofika Lachinayi pa 11 June nkuti anthuwa asadapereke chindapusacho. +",7 +"Apha Gogo Pomuganizira Kuti ndi Mfiti Anthu okwiya mboma la Chitipa apha gogo wina pomuganizira kuti ndi mfiti. +Mneneri wa apolisi mbomalo Gladwell Simwaka watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati gogoyu ndi mai Philines Mulenga. +Malinga ndi a Simwaka, anthuwa akuti akukhulupilira kuti gogoyu anapha mdzukulu wake mdera la mfumu yaikulu Mwaulambya mbomalo. +Wadzudzula mchitidwewu-Dausi Mdzukulu wawo wa agogowa anamwalira ndiye agogowa sanakakhale nawo pa malirowo zomwe zinachititsa kuti anthuwo aganize kuti ndi omwe apha mdzukuluyo, anatero a Simwaka. +A Nicholus Dausi omwe ndi nduna yoona za chitetezo cha mdziko adzudzula mchitidwe wopha anthu okalamba powaganizira kuti ndi mfiti. +Aliyense ali ndi nthawi yake yokufa yomwe Mulungu anamulembera. Ndiye munthu akadwala ndi kufa sikuti azinamizira azigogo ayi. Amenewa tiwalemekeze chifukwa kupanda iwowa sibwenzi ife tili moyo, anatero a Dausi. +",14 +"CRON Idzudzula Katuni wa Malawi News Mgwirizano wa mabungwe omwe umawona za Ufulu wa Ana Mdziko muno wa Child Rights Organisations Network wadzudzula chithunzi chomwe chimadziwika ndi dzina loti Achalume (cartoon) chomwe chidatuluka mu News Paper ya Malawi News yapa 28 December Chaka chatha chifukwa chokamba zosemphana ndi ufulu wamwana wankazi pankhani yogonana. +Chithunzi chomwe chinadzudzulidwacho Mgwirizanowu muli mabungwe monga Save the Children, World Vision, Plan International Malawi komanso SOS Childrens Village Malawi ndipo anena izi kudzera mu Chikalata chomwe mabungwewa chomwe chati zomwe anajambula a HASWELL KUNYENJE pa Cartoon yawo yotchedwa Achalume zinali zokhumudwitsa pomwe analemba kuti Mamuna wina adagonana ndi Mtsikana wangono wadzaka 16 ndipo mtsikanayo anapereka matenda opatsilana pogonana kwa Bamboyo. +Iwo ati mwana yemwe sadafike zaka 18 ayenera kumalimbikitsidwa ku nkhani yamaphunziro osati nkhani zogonana. Mabungwewa ati malamulo adziko lino amaletsa kukamba nkhani zogonana ndi mwana yemwe sanakwanitse dzaka 18 zakubadwa ndipo kutero ndi mulandu waukulu. +Mai Edith Tsikidzani ndi Mmodzi mwa ogwira ntchito ku Bungwe la Save the Children ndipo iwo anati ndizomvetsa chisoni kuti mpaka pano mdziko muno anthu ena akugwiritsa ntchito mphanvu komanso kutchuka kwawo pofuna kuchitira ana zachipongwe komanso kulimbikitsa mchitidwewu komwe ndikupha tsogolo la anawa. +Ifeyo ndife okhudzika kaamba ka katoon imeneyi yomwe ikukolezera abambo ambiri kuti azichita zosayenera ndi wana aatsikana omwe sanakwane zaka 18 chomwe ndi chitonzo chzchikulu kwa anawa komanso amayi mdziko muno, anatero mayi Tsikidzani. +Mwazina mayi tsikidzani anati kuika katoon imeneyi ndikukolezera mchitidwewu kwa abambo omwe amakhala ndi maganizo ofuna kugona ndi ana mmalo moika uthenga oti utha kuthandiza komanso kuteteza anawa. +",14 +"Apolisi ku Dedza Achenjeza Angaliba Wolemba: Thokozani Chapola Apolisi mboma la dedza achenjeza angaliba onse mbomalo kuti apewe kuvinira chinamwali cha jando ana omwe makolo awo ndi a zipembedzo zina mokakamiza. +Malinga ndi kalata yomwe Radio Maria Malawi yawona yomwe polisi ya mbomali yalembera kwa ma shehe onse a mbomalo kudzera mwa mneneri wa wa bungwe lalikulu la chipembedzo cha chisilamu mdziko muno Sheikh Dinala Chabulika, chati kuchita izi ndi kotsutsana ndi malamulo a dziko lino komanso buku loyera la quaran komanso chiphunziti cha mtumiki muhammad wa chipembedzochi. +Apolisiwa apempha ma shehe-wa kuti aphunzitse bwino angaliba-wa chiphunzitso chenicheni cha chipembedzochi pa nkhaniyi zomwe ati sizosemphana ndi malamulo a dziko lino omwe amatsindika kuti aliyense ali ndi ufulu osankha chipembedzo cha ku mtima kwake komanso kukakamiza munthu kuchita zomwe asakufuna ndi zosaloredwa. +Iwo ati poganizira kuti mdulidwe ndi mbali imodzi ya chipembedzo cha chisilamu, sipoyenera kuti uzichitika mokakamiza.Izi zikudza pomwe chaka chatha angaliba awiri a mbomalo anakawonekera ku bwalo la milandu atavinira jando mokakamiza ana awiri a mlangizi wina wa zaumoyo mbomalo. +Apolisiwa achenjezanso kuti aliyense amene adzapezeke atalowa ku ndagala ya jando pongofuna kukawona zochitika kumeneko adzayimbidwa mlandu wopezeka ku malo osayenera ndipo adzalandira chilango. +",14 +"Poly Alumni Ithandiza Ophunzira Osowa kudzera mma SMS Wolemba: Precious Chipondeponde Sukulu ya ukachenjede ya Poletekiniki yayambitsa kulandira mauthenga a lamya ndicholinga chofuna kuthandiza ophunzira amene akuvutika kulipira sukulu komanso kupeza zowathandizira pamaphunziro awo. +Edna Nkono, amene ndiwosonkhanitsa chuma kugulu la Polytechnic Alumni Association (PAA), watinjira yolandira mauthenga pa lamya ithandiza kupeza ndalama zothandizira ophunzira amene sangakwanise kulipira sukulu mwaiwo okha komanso enaamene amasowa thandizo pazofunik ammaphunziro awo. +Sukuluyi ili ndi ophunzira oposa zana limodzi amene amasowa thandizoli. Ophunzirawa amaosowa malo ogona, chakudya, zipangizo zowathandizira pa maphunziro awo ndi zina zambiri. Ndizomvetsa chisoni kuti ena amatha kugona mkalasi kamba kosowa malo ogona. Anatero a Nkono Pofuna kupeza ophunzira osowa thandizoli tidzagwira ntchito limodz indi bungwe la ophunzila la Polytechnic Students Union. Izi zitithandiza kupeza ophunzira eni eni amene akusowa thandizoli. +Chiyambireni guluri mu chaka cha 2016, guluri lapeza ndalama zokwana 16 miliyoni ndipo pakadali pano guluri liri ndi ophunzira okwana oposa 80 amene amathandizidwa A Nkono apempha anthu ofuna kuthandiza kuti alowe nawo polemba uthenga pa lamya oti YAMBA mu Chichewa kapena START muchingerezi ndipo atumize ku 2025 ndipo adzilandira mauthenga tsiku ndi tsiku pa nkhani zokhudza sukuluyi. Utheng auliwonse udzadula ndalama zokwana K50. +",3 +" Pac ifuna mayankho pa za kukwera kwa mitengo Kukwera kwa zinthu mdziko muno kwaika Amalawi pamoto wa mavuto zomwe zachititsa kuti bungwe la Public Affairs Committee (PAC) likonze msonkhano wopeza mayankho a mavutowa. + Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Mkulu wa bungweli Robert Phiri watsimikizira Tamvani za msonkhanowu koma wati tsiku ndi malo amsonkhanowu adziwitsidwa posakhalitsapa. + Kukweza kwa mitengo ya madzi ndi K45 pa K100 iliyonse, mitengo ya magetsi ndi K39 pa K100, shuga ndi K10 pa K100 iliyonse komanso zina zakudya ndi kukwera kwa chiongola dzanja choperekedwa munthu akakongola ndalama kubanki ndi zinthu zomwe zapangitsa kuti moyo ukhale wopweteka. + Msonkhano wa PAC mu 2012 kudali chitetezo chokhwima zedi Izi ndi zomwe si zidakhazike chete bungwe la PAC pamene akonza nkhumano kusaka mayankho. + Bungwe la PAC likudziwa nyengo zowawitsa zomwe Amalawi akudutsamo. Chomwe tikufuna nchakuti Amalawi tikhale pamodzi kuti tipeze mayankho pa mavutowa, adatero Phiri. + Titamufunsa ngati msonkhanowo ungabale zipatso, Phiri adati iwo akukhulupirira kuti ukhala ndi chophula kusiyana nkuti aliyense azizilankhula payekha. + Padakalipano tikulumikizana ndi mabungwe komanso mbali zina momwe tingakonzere msonkhanowu komanso momwe tingapezere mayankho ku mavuto amene tikukumana nawowa, adatero Phiri. + Iye adaonjeza kuti: Zomwe mabungwe ndi anthu onse adzagwirizane ndi zomwe zidzachitidwe chifukwa ife kwathu ndi kupereka mwayi kuti anthu akambirane ndi kupeza mayankho. + Bungweli lidachititsanso msonkhano wotere mu March 2012 pamene kudali chitetezo chokhwima pamene ena amati msonkhanowo udali ndi cholinga chofuna kuthana ndi boma. + Msonkhanowu womwe mbali ya boma sidafikeko, udachitikira ku Limbe Cathedral mumzinda wa Blantyre. + Koma Phiri wati msonkhano ukudzawu umemeza mbali zonse kuphatikizapo a boma chifukwa bungwe lawo limapereka kumva kwa boma lililonse lomwe likulamula. + Koma mkulu wa bungwe loona ufulu wa ogula la Consumer Association of Malawi (Cama) John Kapito wati boma lakhumudwitsa Amalawi chifukwa cholephera kukonza zinthu. + Panopa zinthu zaipa ndipo zasokonekera, makuponi kulibe, chiongola dzanja chakwera ku mabanki zomwe zichititse kuti katundu akwere zomwe zizunze Amalawi. Zomwenso boma likuchita sizikuoneka ndipo tilibenso chiyembekezo ngati zinthu zibwerere mchimake, adatero Kapito. + Iye adati Amalawi akuyenera kumadya mosinira komanso amange malamba chifukwa komwe tikupitaku zinthu zinyanya kuwawa. +",11 +"MISA Malawi Idzudzula Kumangidwa kwa Atolankhani Bungwe lomenyera ufulu wa atolankhani mdziko muno la MISA-Malawi ladzudzula zomwe apolisi achita pomanga atolankhani atatu pabwalo la ndege la Kamuzu International mu mzinda wa Lilongwe, pamene anali mkati mogwira ntchito yawo. +Wasayina chikalatacho-Ndanga Bungwe-li lanena izi kudzera mu chikalata chomwe latulutsa pomwe limathilirapo ndemanga kutsatira kumangidwa kwa atolankhaniwa omwe anamangidwa pomwe nthumwi za bungwe la Europian Union (EU) zimafika mdziko muno kuti zidzapereke lipoti lokhudza momwe chisankho cha pa 21 May 2019 chinayendera. +Malingana ndi wapampando wa bungwe-li mdziko muno Teleza Ndanga, zomwe apolisi-wa anachita ndi zosayenera, kotero wati bungweli liyesetsa kuti likumane ndi apolisi ndi cholinga choti pakhale ubale wabwino pakati pa apolisi ndi atolankhani mdziko muno. +Atolankhani-wa ndi Steve Zimba ndi Francis Chamasowa omwe ndi a wailesi ya Zodiak, komanso Golden Matonga wa Nation Publications Limited ndipo anawatsekulira mulandu wochita zachisokonezo pa bwalo la ndege. +",14 +" ACB idayamba kale kufufuza Chaponda Nthambi yofufuza za ziphuphu ya Anti-corruption Bureau (ACB) yati idayamba kale kufufuza nkhani ya momwe bungwe la Admarc lidagulira chimanga mdziko la Zambia. + Mkulu wa ACB Lukas Kondowe adanena izi Lachitatu, patangotha masiku angapo kuchokera pomwe komiti imene lidasankhidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti lifufuze ngati nduna ya za malimidwe George Chaponda ikukhudzidwa pankhani yoti bungwe la Admarc lidasokoneza zina pogula chimangacho kupyolera mu kampani ya Kaloswe Courier and Commuter Services ya ku Zambia. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Afufuzidwe: Chaponda Mwa zina, gululo, limene limatsogoleledwa ndi Anastazia Msosa, lidapempha Mutharika kuti ACB ifufuze momwe nkhaniyi idayendera. Koma Kondowe adati adayamba kale izi. + Tidayamba kale ngakhale mtsogoleri wa dziko lino asadakhazikitsenso komiti yapadera. Choncho tingopitiriza basi, adatero Kondowe. + Polankhula ndi mtolankhani wathu, Kondowe adati adangomva pawailesi za kupsa kwa ofesi ya Chaponda Lachiwiri ndipo adati akudikira lipoti la momwe maofesi a Chaponda ndi akuluakulu ena adapsera. + Sitikudziwa ngati zomwe tikadafuna mkafukufuku wathu kumeneko, zaonongeka nawo ndi motowo, adatero Kondowe. + Motowo udaononga ofesi ya nduna Malinga ndi mkulu wa apolisi Lexten Kachama amene adafika pamalo a ngoziyo adati apolisi akufufuzabe chidayambitsa motowo cha mma 11 koloko mmawa. + Motowo udadzetsa mtsutso pakati pa Amalawi pamene ena ankati udabuka pofuna kusokoneza umboni pomwe ena ankati ndi ngozi chabe. + Polankhulapo, mmodzi wa a mabungwe omwe si a boma omwe adakatenga chiletso mwezi watha kuti ndunayi ayiimitse kaye pantchito mpaka kafukufukuyu atachitika Moses Mkandawire adati kuyaka kwa ofesiku kukufunika kufufuzidwanso mwapadera. + Mkandawire, yemwe ndi mkulu wa bungwe loona za kakhalidwe ka anthu ya Church and Society mu sinodi ya Livingstonia, adati pakadalipano ndi zovuta kuloza zala munthu kuti ndiye wayatsa motowo. + Sitingaloze zala munthu kuti ndiye wayatsa moto; koma chofunika ndi kafukufuku wina kuti ofesiyi idayaka bwanji panthawi ngati ino pomwe ili mkamwamkamwa mwa anthu? Bwanji siyidayake ofesi ya zofalitsa nkhani kapena ofesi ina? Kodi tingati izi zangochitika? adadabwa Mkandawire. + Iye adati chopweteka kwambiri nchoti failo ndi uthenga wambiri waboma waonongeka ndi motowo zomwe zingasokoneze ntchito za boma zomwe zimayenera kupitilizidwa ndi anthu osiyanasiyana. + Izitu nzopweteketsa ana athu chifukwa tawaonongera uthenga wofunika womwe akadadzaugwiritsa ntchito mtsogolo muno kaamba koti zinthu zathu zambiri sizili pa intaneti n gati maiko aanzathu, adatero Mkandawire. + Komabe Mkandawire adayamikira Mutharika pokhazikitsa komiti yapaderayo komanso adayamikira zotsatira za kafukufukuyo ati popeza adangotsimikizira zomwe mabungwe omwe siaboma akhala akunena kuti Chaponda ngofunika kufufuzidwa bwino. + Malinga ndi lipotili Chaponda akuyenera kufufuzidwa pa momwe adalowerererapo kuti kampani ya Transglobe ikhale nawo mgulu logulitsa boma chimanga. + Pali kukaikitsa pa njira yomwe kampani ya Transglobe idapezera chiphaso chotumizira chimanga kuchokera mdziko la Zambia kubweretsa kuno, choncho Chaponda akuyenera kufufuzidwa mbali yomwe adatengapo, idatero lipotilo. + Lipotili lidatinso bungwe la ku Zambia la Zambia Cooperative Federation lomwe adali pamgwirizano ndi bungwe Admarc loperekera chimanga chokwana matani 100 000, lidangoperekapo matani 4 000 okha. + Padakalipano komiti yapadera ku Nyumba ya Malamulo, Lachitatu limayembekezera kutulutsa zotsatira zake. + Poyankha mafunso a komitiyo sabata yatha, Chaponda adati nkhaniyo siyimamukhudza kwambiri chifukwa gawo lake lidali kukambirana ndi nduna ya malimidwe ku Zambia kuti boma la Malawi likufuna chimanga. Za ndondomeko yogulira chimangacho, iye adatero, idali mmanja mwa Admarc. + Dziko lathu lidali pamoto wa njala. Ngati nyumba ikupsa, mukhonza kuthyola zitseko ndi mawindo kuti mupulumutse mwana amene angafere momwemo. Ndondomeko zina sizinatsatidwe chifukwa tidali pampishupishu, Chaponda adatero. +",11 +" Kanthu nkhama: Alimi akuchita kuthirira fodya Kudula kwa mvula kutionetsa zachilendo mpaka alimi kuchita kuthirira mminda ya fodya kuti mwina angaphulepo kena kake. Alimi ochenjera akuyesetsa kupulumutsa mbewu zawo pothirira ngakhale kuti ntchitoyi ili yowawa ndi yotenga nthawi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Lingilirani Chikhwaya, mmodzi mwa alimi omwe akuchita kuthirira fodya kumunda kuti aphulepo kanthu mvula ikapanda kuchita chilungamo. + Ndikudziweni. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chikhwaya: Zikavute kumsika Ndine Lingilirani Chikhwaya, mlimi wochokera mdera la Nkhoma mboma la Lilongwe. + Mumalima chiyani? Ndimalima mbewu zosiyanasiyana malingana nkuti masiku ano ntchito ya ulimi njosapanganika. Ukhoza kudalira mbewu imodzi nkugwa nayo osakolola kanthu ndiye potengera upangiri wa alangizi, ndimangobzala mbewu zosiyanasiyana. + Ulimi wanu chaka chino ukuyenda bwanji? Bambo, kunena zoona zinthu zatembenuka. Tayamba kukhala ndi mantha tsopano kuti kodi chikutilonda nchiyani? Chaka chatha mvula sidalongosoke, anthu sitidakolole bwino ndiye pano pomwe timaona ngati mwina chaka chino tipeza polirira, zikuonekanso ngati mavuto ankira mtsogolo. + Ndiye mwangokhala basi nkumadikira chakudza? Ayi, tikuyesetsa njira iyi ndi iyo kuti mwina mbewu zina zipulumuke. Mminda ina tili kale bwinoko chifukwa tidatchingira koma mminda ina monga ya fodya tikuchita kuthirira ndithu ngati ndiwo zamasamba kudimba kuchitira kuti nanga tachoka kale kutali ndipo taononga ndalama, mphamvu ndi nthawi ndiye tikagwere mphwayi pano? Kuli bwino kungodzipereka basi. + Ndiye momwe umakhalira munda wa fodya muja ntchito yake imakhala bwanji? Tidazolowera. Nkale tidayamba ulimi wa fodya ndipo ululu wake tikuudziwa kale ndipo tidauzolowera. Umatheka kugwira ntchito yakalavulagaga chaka chonse nkukakhumudwira kokagulitsa ndiye kuli bwino ulimbe nazo zikamadzavuta kumsika ndi nkhani ina. + Ndiye zimakhala bwanji? Monga ngati ine, munda wanga uli pafupi ndi mtsinje omwe alimi a kuno timagwiritsa ntchito ya mthirira komanso tili ndi sikimu yomwe akatswiri adatiphunzitsa kakololedwe ka madzi ndipo mvula itangoyamba muja tidakololapo madzi. Madzi amenewo ndi omwe tikugwiritsa ntchito pano. Kumunsi kwa mtsinje womwe timadalirawo, tidayamba tautseka kuti madzi asamapite ambiri kupangira kuti mwina mvula ikhoza kutenga nthawi isadayambirenso. + Ndikufuna ndimve za mathiriridwewo potitu munda wa fodya simasewera. + Sitidzipanikiza kwambiri, ayi, timatengako gawo lina lero nkuthirira kenako mawa mbali ina, choncho. Nthawi zina tikakhala ndi nthawi timakathirira mbali ina mmawa madzulonso nkukathirira mbali ina kungofuna kuonetsetsa kuti pomwe mvula izidzabwereranso, fodya adzakhale ali bwino. + Koma muli ndi chiyembekezo chanji pa fodya wanu? Ngakhale nkhawa ilipo komabe ndikayerekeza ndi momwe zikuonekera mminda ya anthu ena, mwina fodya wanga akhoza kudzakhala nawo mgulu la fodya wochititsa kaso chifukwa ngakhale kuli dzuwa chonchi, ayi, masamba ake akuoneka kuti ali ndi mphamvu moti mvula itangoti lero yagwa yambiri, pakhoza kudzuka fodya. + Chaka chatha mvula idachita chimodzimodzi kugwa nyengo yochepa nkudula kenako nkudzagobwera moononga. Pemphero lanu nlotani? Ayi ndithu, pemphero langa nloti zinthu zisakhale choncho chaka chino, Mulungu akadatichitira chifundo. Chaka chatha tidaona zowawa kwambiri chifukwa mbewu zambiri zidakokoloka ndi madzi a mvula osefukira moti chaka chino kuli mavuto, makamaka pachakudya, ndiye timati mwina chaka chino tingaoneko chozizwitsa. +",4 +" Waganyu: Nzeru zayekha adaviyika Flames Akulu adati nzeru zayekha adaviyika nsima mmadzi. Lero tikuti nzeru zayekha adaviyika Flames mmadzi. Zidachitika ku Algeria sindizo, timu yathu aivupulanso. + Msabata imodzi Algeria yatipuntha 5-0. Izi zikusonyeza kuti pamasewero anayi amene Flames yasewera yachinyitsa zigoli 9. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Aganyu kudzanso akatswiri alankhulapo zoti Young Chimodzi achite koma zikuoneka kuti bwana Young sangamvenso zamunthu. Lero ndi izo tsopano, titani apa? Kodi nchifukwa chiyani Robin Ngalande mukumuseweretsa kumbali pamene tili ndi osewera amene angachite bwino kuposa iye? Robin amasewera kutsogolo nthawi zonse koma inu mwamusintha. + Anthu akuti tayesani osewera monga Fisher Kondowe amene mmbali amachita bwino. Chifukwa chiyani kuseweretsa Chiukepo Msowoya amene ku Mozambique sakusewera? Nanga mukusiiranji osewera ngati Deus Nkutu amene wachinya zigoli 15 muligi? Bwana Chimodzi mukutithetsatu mawu inu. Bwanji osamvera zomwe anthu akulankhula kuti zikanike zokha? Kumbukirani, chisankhidwireni kukhala mphunzitsi wa Flames tangopambana magemu atatu, Ethiopia, Benin ndi Chad ndipo talephera magemu 10. Kodi bwana Chimodzi zikuvuta pati? Pano mwayi wochita bwino wacheperatu chifukwa tikuyenera tikaphe Ethiopia kwawo komanso kupha Mali pamene ikubwera kumudzi kuno zomwe zikukaikitsa. Mali ikukonza zodzapha Flames podziwiratu kuti gemu yawo ndi Algeria zikawavuta. +",16 +"Papa Wati Moyo ndi Mphatso ya Mtengo Wapatali Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wati moyo ndi mphatso ya mtengo wa patali. +Papa Francisko Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa walankhula izi mu uthenga wake kwa ma episkopi a ku United Kingdom komanso Ireland pa tsiku lomwe akhristu a mpingowu amakondwerera mphatso ya mtengo wa patali ya moyo. +Mu uthengawo iye wati pozindikira kuti moyo ndi mphatso ya mtengo wapatali, anthu akuyenera kulemekeza ulemelero wa munthu aliyense. +Kusankha moyo ndiye mutu wa chikondwerero cha chaka chino. +",13 +" Kudali ku sitolo ya Peoples Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Khalidwe la Gift Simkonda lokonda kukagula katundu kusitolo ya Peoples kwa Magalasi ku Ndirande mumzinda wa Blantyre mchaka cha 2010 lidathera kwa mnyamatayu kuzulamo nthiti yake, Eunice Chingoni. + Panthawiyo nkuti Eunice akugwira ntchito ya pa till msitolomo pamene Gift adali akugwira ntchito ku sitolo za Dapp ngati wophunzitsa anthu za mmene angamachitile malonda ku Ndirandeko. + Malinga ndi Eunice, nthawi zonse akaona Gift akulowa musitoloyo, mtima wake umakankha mwazi mwaliwiro kulakalaka mnyamatayu atadzakhala wakumkeka wake koma poti ndi mkazi sakadalankhula kotero amayesetsa kumuchitira mkomya musitolo momwemo pomudindira komanso kumulongezera mnyamatayu katundu bwino mujumbo akagula katundu. + Banja la Simkonda tsiku la ukwati Zinkandiwawa Gift akapita podinditsira mitengo pamunthu wina chifukwa ndinkadziwa kuti sindimva mawu ake komanso sandiona, adatero Eunice. + Iye adati, chimene chinkamuzula moyo kwambiri mwa Gift ndi lilime lake la Chitumbuka, maonekedwe ake ofatsa komanso kuumbidwa bwino kwa mnyamatayu. + Naye Gift adati mtima wake udayamba kuthawathawa mmalo ngati netiweki ya lamya za mmanja atasiyanitsa umunthu umene nthandayi idali nayo pa makasitomala kufikira pamene naye adayamba kudyerera maso padonalo. + Gift adati kupatula kudzichepetsa komanso nsangala zimene zidakuta wakumkeka wakeyu, mnyamatayotu akutinso ankakopeka ndi dzino logamphuka limene lili mkamwa mwadonalo limene limaonekera akamamwetulira. + Nditayizindikira nyenyeziyi sindidachedwe koma kupatsana nayo nambala ya foni ndipo patadutsa masiku tidagwirizana kuti tikumane kuti ndikatule nkhawa zanga pa iye, adatero Gift. + Koma Gift akuti adakhumudwa ataponya khoka lake la chikondi mudziwe la chikondi la njoleyi pamene duwali lidatemetsa nkhwangwa pamwala kuti silikufuna kugwa mchikondi ndi iye. + Ndidakana dala ngakhale pansi pamtima ndinkadziwa kuti ndikumufuna. Ndinkafuna kuonetsetsa kuya kwa chikondi chake paine ndipo pakutha pa miyezi iwiri ndi pamene ndidampatsa makiyi a mtima wanga, adatero Eunice. + Nkhani ya awiriwa itafika mmakwawo kuti akufuna akwatirane idautsa mapiri pachigwa chifukwa akwawo kwa Eunice, mngoni, sankafuna akwatirane ndi mtumbuka ndipo akwawo kwa Gift sankafuna kuti mwana wao akwatirane ndi mngoni. + Awiriwa adati zidali zopweteka kwambiri ngati dzino lobooka kuzimvetsetsa kuti asakwatirane chifukwa cha kusiyana chilankhulo ndi mtundu. + Pafupifupi chaka chinadutsa anthu akwathu atatisiyanitsa koma sitidakhale chete tidayetsetsa kuwaunikira kuti chikondi adalenga ndi Mulungu ndipo Mulunguyo ali ndi mphamvu yolumikizanitsa anthu amitundu yosiyanasiyana ndikukhala thupi limodzi. Tidali okondwa anthu ambali zonse ziwiri atatimvetsetsa ndikutilola kuti titengane, adatero Gift. + Awiriwa adamangitsa woyera pa August 4 2013 ndipo ali ndi mwana mmodzi, Wongani, amene akwanitse chaka chimodzi chaka chino. Banjali likukhala ku Zomba kumene Eunice akugwira ntchito ku sitolo ya Peoples ya Matawale pamene Gift akugwira ku Dapp ya mumzinda wa Zomba. +",15 +" Adatengera Lucky Dube: Liwonde Chibwe Oimba akubadwirabadwira mdziko muno. Mmodzi mwa oimba omwe adza ndi mkokomo ndi MacDonald Liwonde Chibwe wa ku Mponela mboma la Dowa koma watambalala mumzinda wa Blantye. DYSON MTHAWANJI adacheza ndi katswiriyu motere: Wawa, tidziwane Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chibwe: Mulungu ndi wachikondi Ndine MacDonald Liwonde Chibwe, ndimachokera mmudzi mwa Chimbudzi, mfumu yandodo Mponela mboma la Dowa. Mbanja mwathu tidabadwa ana asanu ndi awiri ndipo ine ndi wachisanu. + Ndibenthulire chiyambi cha maimbidwe ako. + Chidwi changa pa maimbidwe chidabadwa pomwe ndidali wamngono. Kuyambira ndili wamngono ndakhala ndikukonda kumvera nyimbo zakunja komanso zamdziko mommuno. Lucky Dube wa ku South Africa ndi Lucius Banda wa kuno ku Malawi ndiwo adandipatsa chidwi kuti ndikhale ndi loto lodzakhala woimba. Mchaka cha 2013 ndidajambula chimbale changa cha nyimbo choyamba chotchedwa Lingakome. Nyimbo zambiri mchimbalechi zikuseweredwabe pawayilesi zambiri ndipo anthu akuzikonda. Zina mwa nyimbo zili mchimbalechi ndi Facebook, Kadende, Hello komanso Mama Africa kungotchulapo zochepa. Zambiri mwa nyimbozi zili mchamba cha reggae. Kapekedwe kanga ka nyimbo kamagwirizana ndi chamba chimenechi. + Oimba ena oyamba kumene sachedwa kufooka ndipo amazilala msanga. Iwe suchita chimodzimodzi? Kuimba kuli mmagazi anga kotero ine ndabwera kudzakhazikika pa maimbidwe. Anthu ambiri andilandira pa nkhani ya maimbidwe. Izi zikundipatsa mangolomera kuti ndikhazikika palusoli ndipo sindikubwerera mmbuyo. Pakalipano ndikujambula chimbale chachiwiri chomwe dzina lake ndi Tingathe. Chimbalechi chanyamula uthenga womwe ukugwedeza Amalawi kuti adzuke ndi kuyamba kukonda dziko lawo komanso kugwira ntchito molimbika kuti tithetse mavuto a zachuma omwe tikukumana nawo. Pakalipano ndajambula nyimbo zinayi zomwe zipezeke mchimbale chimenechi. Nyimbozi ndi Namondwe, Dona, Ndimtima komanso True Love. Nyimbo zinayizi zikuseweredwa kale pawayilesi, komanso zikuchita bwino mupologalamu ya MBC Top 20 pa MBC Radio 2. + Chifukwa chiyani nyimbo zako zambiri zanyamula uthenga wachikondi? Mulungu ndi wachikondi ndipo sitingalekanitse Iye ndi chikondi. Ngati pali chikondi pakati pa anthu awiri pamalopo pamakhala mtendere. Kotero ndidachiona chofunika kulalikira chikondi kudzera mnyimbo zanga. +",9 +" Chisamaliro choyenera cha ngombe za mkaka Ngakhale alimi ambiri a ngombe za mkaka amabwekera kuti akupeza phindu ku ulimiwu, Jacob Mwasinga, mlangizi wa ziweto ku Mzuzu Agricultural Development Division (Mzadd) akuti alimi akhonza kusimba lokoma atasamalira moyenera ziweto zawo. + Malinga ndi mlangiziyu, ngombe ya mkaka ya mtundu wa Friesian yosasakaniza (pure breed) yomwe alimi ambiri akuweta, ili ndi kuthekera kotulutsa mkaka okwana malita 50 patsiku ngati ikudyetsedwa zakudya zoyenera ndi zokwanira, ikupatsidwa madzi nthawi zonse, ikukamidwa moyenera komanso ngati siikubisiridwa mwana pamene mlimi akukama. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Alimi ena akukama mkaka wochepa Pamene izi zili chomwecho, alimi monga Taulo Chisoso ndi Chrissy Wyson a mgulu la alimi lotchedwa Namahoya, kwa T/A Chimaliro, mboma la Thyolo akuti akati apeza mkaka ochuluka, ndi okwana malitazi 15 okha pa ngombe imodzi ya mtunduwu. + Madzi amathandizira kwambiri kuti ngombe ya mkaka itulutse mkaka wochuluka chifukwa pafupifupi 90 peresenti ya mkaka ndi madzi ndipo ichi nchifukwa chake ngombe ya mkaka imatha kumwa madzi pafupifupi malita 200 patsiku. + Ichi nchifukwa chake mkhola la ngombezi mmayenera kukhala madzi nthawi zonse. Chachiwiri, zakudya zoonjezera ku udzu womwe ngombezi zimadya monga gaga kapena zakasakaniza zija zimadziwika ndi dzina loti dairy marsh pachizungu, zimathandizira kuti ngombezi zitulutse mkaka wochuluka, adatero Mwasinga. + Iye adati ngombe ya mkaka imayenera ikamidwe kawiri, masana ndi madzulo ndipo pokama, mlimi awonetsetse kuti wachotsa mkaka wonse chifukwa izi zimathandiza kuti ngombe ipangenso mkaka wina. + Kuonjezera apo, iye adati ngombe zina zimakhala ndi chizolowezi chobisa mkaka ngati mwana wake sanayamweko kapena ngati mwana wake siyikumuona pafupi nthawi yomwe ikukamidwa choncho mwana amayenera akhale patsogolo kuti izitha kumuona komanso amayenera ayamweko pangono kenako kumuchotsa ndi kuyamba kukama. + Pothirirapo ndemanga pa nkhani ya kadyetsedwe, Jonathan Tanganyika, mphunzitsi wa ziweto ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) adati mlimi akhonzanso kumaonjezera chakudya monga gaga kapena chakasakaniza kufikira ataona kuti ngombe yafika pamalekezero opanga mkaka ochuluka, singathenso kupitiriza ngakhale ataonjezera chakudya china. + Iye adafotokoza kuti mlimi amayenera kudyetsera ngombe za mkaka chakudya chopangidwa kuchokera ku mbewu kawiri patsiku, sayileji kamodzi kapena kawiri patsiku makamaka mlimi akamaliza kukama pomwe heyi akuyenera kumapezeka nthawi zonse kuti zizidya umo zafunira ndipo poopetsa kuti udzu wina ukhonza kumangoonongeka, ndi bwino kuti mlimi aziyika pangonopangono. + Kadyetsedwe komanso mlingo wa chakudya sukuyenera kusintha kwa chaka chonse chifukwa ukasintha, mkakanso umachepa. Chakudya cha ngombe za mkaka chotchipa ndi udzu koma nthawi zambiri umachuluka nthawi ya dzinja kotero mlimi amayenera kufutsa mu njira ya heyi komanso sayilegi kuti apitirize kudyetsera bwino ngombe zake kwa chaka chonse, iye adatero. + Tanganyika adaonjeza kuti popanga heyi, mlimi akuyenera kusakanizako udzu wa mgulu la nyemba monga gilisidiya, zotsalira popanga shuga zotchedwa molasezi komanso mchere kuti adzakhale wa michere yochuluka ndi wokoma. + Ngakhale izi zili chomwechi, Tanganyika adati mlimi akuyeneranso kudziwa kuti ngombe ya mkaka ikabereka kokwana kasanu, imayamba kutulutsa mkaka ochepa komanso khola ngati lili losasamalirika, matenda monga yotupitsa bere (mastitis) amene amachepetsanso mkaka. +",4 +"Papa Wati Mawu a Mulungu Amafalikira Ponseponse Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse, Papa Francisco wati mawu a Mulungu ali ndi mphavu yofalikira ponseponse. +Papa Francisko Papa walankhula izi lachitatu pa bwalo la Saint Peters Square ku likulu la mpingowu ku Vatican. +Polankhula kwa anthu omwe anasonkhana pa bwaloli Papa Francisco wati ngakhale mpingo wakhala ukukumana ndi mavuto osiyanasiyana kuyambira nthawi ya Apostoli maka pofalitsa Uthenga wa Yesu Khristu, komabe Mau a Mulungu akhala akufalikira ponseponse. +Pamenepa iye wati izi zikusonyeza mphamvu yodabwitsa yomwe Mau a Mulungu alinayo yotha kufikira pena paliponse. +Iye wati zimenezi zikusonyeza kuti palibe angamangire mpanda mawu a Mulungu. +",13 +" Kasakaniza pa Khrisimasi Pa 25 Disembala chaka chilichonse Akhristu padziko lapansi amakumbukira kubadwa kwa Yesu. + Tsikuli ndi mawa laliwisili. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mmalo ambiri mnyengoyi, chisangalalochi chimakathera mmaphwando a kunyumba komanso kuntchito, mpaka kulowa mchaka chatsopano. + Pofika tsiku la Khirisimasilo, chisangalalo chimakhala chitakuta miyoyo ya anthu ambiri. + Ena amakayambira kutchalitchi nkukamalizira kunyumba komwe pena fumbi limakhala liri koboo! magule ndi maphwando ali mkati. + Uku zifuyo zimakhala zikuphedwa kuti zikometsere zonse. + Zakumwa zimayenda ponseponse, wailesi zikusonkhezera dansi za mnanu pomwe ana amakonza maulendo kukayendera abale. + Koma pomwe ena akuti chaka chino ziyenda monga kale, ena akuti mavuto akula ndipo chisangalalochi chiwalambalala. + Makosa Fumani wa mmudzi mwa Mankhamba 2 kwa T/A Tomasi mboma la Thyolo wati kukhala kovuta kuti munthu wakumudzi alowerere manyado a Khirisimasi. + Chaka chatha zinthu zidali bwino ndipo tidakwanitsa kugula zoyenera pachisangalalo. + Chaka chino mavuto ayanga ponseponse ndipo chisangalalo chasowa, watero Funani. + Geoffrey Assam Banda wa mmudzi mwa Manjeza kwa T/A Kadewere mboma la Chiradzulu wati iye sadaonepo chaka chowawa ngati chino. + Iye wati zinthu zakwera mtengo kangapo konse chaka chino, zomwe wati zisokoneza chisangalalo. + Pambali pa mapemphero, iye wati chaka ndi chaka amasonkhana ndi anzake komanso banja lake nkudyera limodzi. + Izi akuti zimafuna pafupifupi K10 000. + Koma iye wati chaka chino izi kulibe chifukwa sizingatheke kuti atulutse ndalamayi. + Nyengoyi ambiri tayilowa tilibe mtendere wa mumtima, adatero Banda. + Njerina Mapuno wa mmudzi mwa Yoyola kwa T/A Masasa mboma la Ntcheu wati amayenera adye kankhwiru nkutsitsira ndi zakumwa zoziziritsa kukhosi. + Koma iye wati chaka chino sizitheka. + Kodi chisangalalo chingakhalepo pomwe nkhawa zili poti fetereza palibe? Pano koponi [ya fetereza wotsika mtengo] ili mmanja; sitidagule fetereza. + Kachimanga kafika pothira fetereza koma kogulako fetereza wasiya kubwera. Iyi si khirisimasi yabwino, adatero Mapuno. + T/A Nthache ya mboma la Mwanza yati khirisima iyi ikhala yovuta chifukwa zolira maganizo zachuluka. + Iye wati anthu ali manja mkhosi kaamba kosowa mvula ndi ndalama. + Zinthu zakwera mtengo kotero nkovuta kupeza ndalama yogulira chakudya chapadera cha pa khirisimasi. + Manja ali mkhosi pomwe tikumva kuti mmadera ena abzala kale. Apa palibe khirisimasi; nanga khirisimasi imakhala ya dzuwa? adadandaula Nthache. + Koma Mfumu Yaikulu Chikulamayembe ya mboma la Rumphi yati pali chiyembekezo kuti chisangalalo cha chaka chino chisiyana ndi zaka zina. + Mfumuyi yati chaka chino banja lake liri ndi ziweto zothandizira kukometsa chisangalalochi. + Iye wati chaka chatha sadasangalale bwino chifukwa adasowa chiweto chomwe akadapha koma chaka chino mmakola muli ngombe, mbuzi ndi nkhuku zomwe angasankhepo pokometsera chisangalalochi. + Koma mfumuyi yati kusowa kwa ndalama ndi mafuta agalimoto ndiko kungasokoneze chisangalalochi, maka kwa anthu ake. + T/A Kachindamoto ya mboma la Dedza yati chisangalalo cha chaka chino chili bwino ndipo padali chiyembekezo kuti Lachinayi pa 22 kukhale kusangalala ndi magulupu ake. + Tsiku la khirisimasili ndikhala ndili ku Zomba ndiye Lachinayili ndikhala ndikusangalala ndi magulupu adera langa. + Apa tidzakhala tikuvina magule achikhalidwe chathu komanso kuonetsa za miyambo ya mafumu. + Uku nkusangalala kuti tagwira ntchito yolemetsa chaka chikuthachi; uku nkuchalirira momwe tigwirire ntchito chaka tikuchilowachi. + Khilisimasi ya chaka chino ikhala yosiyana ndi ya chaka chatha chifukwa chaka chino takonzekera bwino ndipo zinthu zomwe tikufuna kudzachita zili kale mmalo, akutero mfumuyu. + Iye adati kusowa kwa ndalama ndikusowa kwa mafuta sizingasokoneze chisangalalochi chifukwa izi zimakhudza anthu akutauni osati iwo chifukwa kumudziko amakwera ngolo ngati afuna kuyenda. + Mneneri wa boma, Patricia Kaliati, wati khirisimasiyi ikhala yopambana chifukwa akadzachoka kopemphera adzakhala akusangalala ndi anthu osiyanasiyana, kumwa thobwa. + Iye wati khilisimasi ya chaka chino ndi chaka chatha sikusiyana chifukwa khirisimasi iliyonse imabweretsa chimwemwe kubanja lake kaamba koti adabadwanso pa 21 Desembala. + Khilisimasi imeneyi ingokhala yothokoza Mulungu potitumizira mwanayo [Yesu] kuti adzatifere kumachimo athu. + Tikuyenera kukhululukirana mangawa monga mwanayo adakhululukira ifenso ku machimo athu. + Pomwe tikusangalala tikuyenera kutenga ena angapo kuti tisangalale nawo, adatero Kaliati. +",2 +"Bungwe la CHRR Ladzudzula Zipolowe pa Ndale Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Center for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) lati ndi lokhumudwa ndi kukula kwa mchitidwe wa zipolowe pa ndale mdziko muno. +Kudzera mu chikalata chomwe bungwe-li latulutsa, mkulu wa bungweli a Micheal Kaiyatsa ati ndi zomvetsa chisoni kuti otsatira zipani akuchitirana ziwembu mu njira zosiyanasiyana ngakhale munthu aliyense ali ndi ufulu wa chibadwidwe. +Bungweli lalankhula izi potsatira zachiwembu zomwe otsatira zipani za UTM, DPP komanso MCP akumana nazo masiku apitawa. +Bungweli ndi lokhuzidwa ndi zamtopola zomwe zikuchitika mdziko muno ndipo lamulo likuyera kugwira ntchito, anatero a Kaiyatsa. +Iwo apempha atsogeleri a bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la MEC kuti awonjezere achitetezo mmalo olembetsera chizankho kuti nkhanzazi zichepe komanso apempha apolisi kuti agwire ntchito yawo moyenera. +",11 +"Bambo Amangidwa Kamba Kopezeka ndi Chamba Apolisi mboma la Chikwawa akusunga mchitokosi bambo wina pomuganizira kuti wapezeka ndi chamba popanda chilolezo. +Malinga ndi wachiwiri kwa mneneri wa apolisi mbomalo Sergeant Dickson Matemba, bamboyu ndi Blessings Dumpha wa zaka 32 yemwe anamangidwa pa msika wa Dyeratu potsatira chipikisheni chomwe apolisiwa amachita pa nthawiyo. +Ndi choletsedwa Mkuluyu akuti anamupeza ndi mabola 142 a chamba mchikwama chake chomwe anaberekera. +Woganiziridwawa amangidwa pa 8 May pa msika wa Dyeratu pomwe apolisi amachita patrol ndipo anawapeza ndi chamba mu chikwama chomwe ananyamura, anatero Sergeant Matemba. +Iye wati oganiziridwayu akuyembekezereka kukaonekera ku khothi komwe atakayankhe mlandu opezeka ndi mankhwala ozunguza bongo popanda chilolezo. +",7 +"Papa Wapempha Abambo Akhale Olimba pa Chikhristu Wolemba: Thokozani Chapola Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati abambo omwe amadzipereka pogwira ntchito zotumikira Mulungu akuyenera kukhala olimba pa chikhristu chawo. +Papa Francisko Papa Francisco walankhula izi pomwe amapereka uthenga wake kwa mamembala a bungwe lina mu mpingowu la Servants of Mary lomwe likuchita mkumano wake ku likulu la mpingowu ku Vatican. +Iye wati abambo omwe akutumikira mbungwe-li akuyenera kumadzipereka kamba koti ntchito zomwe amagwira ndi zopambana. +",13 +"Atsogoleri a HRDC Atuluka pa Belo Bwalo la milandu ku Lilongwe lero lapereka belo kwa akuluakulu a bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC). + Akuluakuluwa omwe ndi a Timothy Mtambo, Gift Trapence komanso Macdonald Sembereka omwe ananjatidwa lamulungu, awalamula kuti apereke ndalama zokwa 100 thousand kwacha aliyense, 2 million kwacha komanso kuti apereke zitupa zawo zoyendera. +Judge Violet Chipawo yemwe wapereka chigamulochi watinso akuluakuluwa akuyenera kumakawonekera ku bwalo la milandu ku Lilongwe lachisanu lililonse. +Ndine okondwa kuti anthu anga atuluka ndipo chomwe ndikudziwa ine ndi chakuti anthu sanayambe alakwapio mdziko muno. Iwo amangoganiziridwa ndipo kuganiziridwa ndi zosiyana ndi kupezeka olakwa, anatero a Mchizi. +Polankhulapo wapampando wa bungwe la HRDC, Timothy Mtambo wati kumangidwaku kwawapatsa mangolomera ndipo apitirizabe ntchito zawo. +Tasangalala luti tatuluka. Koma panopa ndiye kumene tinaliku kwatiwonjezera mphamvu sitibweleranso mbuyo ayi. Amene akufuna kulimbana ndi lamulo akumana nalo, anatero a Mtambo. +Mtambo wati tsopano akupezako bwino kutsatira malipoti omwe anamveka kuti iye anadwala pamene anali kundendeku. +",7 +" Olandira makuponi pano mu 2016 sadzalandiranso Boma lati kuyambira chaka chino, yemwe wapindula nawo mupologalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya Farm Input Subsidy Programme (Fisp) wadyapo gawo lake lotsiriza chifukwa chaka chamawa kunka mtsogolo Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu sadzapezekanso pamndandanda wa olandira makuponi. + Nduna ya zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi, Allan Chiyembekeza, ndiye adalengeza izi pamsonkhano wa atolankhani kulikulu la undunawu mu mzinda wa Lilongwe Lachiwiri lapitali. + Iye adati boma lachita izi poona kuti anthu omwe amapindula mupologalamuyi ndi omweomwewo koma saonetsa kusintha kulikonse, zomwe zidachititsa maiko ndi nthambi zomwe zimathandizirapo mpologalamuyi kugwa mphwayi. + Mwayi womaliza: Ogula feteleza ndi mbewu za sabuside chaka cha mawa adzadzigulira okha Pologalamuyi idayambitsidwa ndi cholinga chopatsa alimi poyambira kuti zikawayendera azidzidalira koma malipoti akusonyeza kuti anthu omweomwewo ndiwo amalandira makuponi chaka nchaka popanda kuonetsa kusintha kulikonse, adatero Chiyembekeza. + Iye adati poona izi, boma laganiza kuti lipereke mwayi umodziumodzi kwa anthu oyenera thandizoli ndipo yemwe zimukanike azidzionera yekha zochita mtsogolo chifukwa mwayi upita kwa anthu ena. + Pakalipano, tili ndi mndandanda wa alimi a chimanga okwana 4.2 miliyoni ndipo mwa amenewa, tasankhamo alimi 1.5 miliyoni omwe athandizike chaka chino koma asayembekezere kuti chaka chamawa adzapezekanso pamndandanda wa alimi olandira makuponi, adatero Chiyembekeza. + Koma wapampando wa komiti ya zaulimi mNyumba ya Malamulo, Felix Jumbe, sakugwirizana ndi ganizoli ponena kuti kumeneku kukhala kuweta umphawi wadzawoneni mdziko muno. + Potsirapo ndemanga pa zomwe Chiyembekeza adanena, Jumbe adati nzosatheka anthu ovutikitsitsa kusintha nkukhala odzidalira paokha chifukwa cha matumba awiri a feteleza ndi paketi imodzi ya mbewu chifukwa zosowa pamoyo ndi zambiri. + Zimenezi nkungofuna kunyeketsa Amalawi opsa kalewa. Zoona munthu angasinthe ndi matumba awiri a feteleza ndi paketi imodzi ya mbewu basi? Ngati akufuna apange ndondomeko yabwino adzapereke zipangizo zokwanira zoti mlimi akhozadi kuimirapo iwo akasiya kupereka thandizo, adatero Jumbe. + Iye adati mmaiko ena monga Zambia, alimi ena adakwanitsa kuima paokha chifukwa boma lidawapatsa zipangizo zokwanira-matumba 8 mlimi mmodzi-moti pano adaleka kudalira boma. + Jumbe adati njira yomwe boma la Malawi limatsata mupologalamu ya sabuside ndi yongopeputsa alimi osati kutukula ulimi monga momwe maiko otukuka adachitira kwawo. + Naye mfumu yaikulu Kabudula ya ku Lilongwe idadandaula ndi ndondomekoyi yatsopanoyi ponena kuti zikakhala choncho ndiye kuti anthu ambiri azivutika ndi njala komanso umphawi. + Alimi ambiri malo awo olima ndi ochepa kwambiri moti ngakhale akolole nkugulitsa zonse sangadzakwanitsebe kugula feteleza ndi mmene udakwerera mtengomu. Thumba limodzi la feteleza ndi K23 000 pomwe la chimanga ndi K5 000 kutanthauza kuti mlimi akuyenera kusunga matumba 5 a chimanga kuti adzagule thumba limodzi la feteleza. + Nanga poti alimi ambiri amafuna matumba a feteleza 4 kapena kuposa apo ndiye kuti agulitse matumba angati a chimanga kuti aime paokha? Mwinanso pakhomopo pali ana angapo akufunika fizi, zovala ndi kudya, adatero Kabudula. + Mwezi wathawu, akadaulo pankhani za kayendetsedwe ka chuma a Economics Association of Malawi (Ecama) adalangiza boma kuti pologalamu ya sabuside ikuyenera kutha kaamba koti imapsinja ndondomeko ya chuma (bajeti). + Ngakhale mmadera ambiri mvula yobzalira yagwa kale, katundu wa sabuside yemwe wafika kale mmisika yomwe idakhazikitsidwa kuti anthu azikagulira zipangizozi sakukwana theka la katundu yense yemwe akufunika mupologalamuyi. + Mu pologalamu ya chaka chino, boma lakonza feteleza wokwana matani 150 000 omwe yemwe agawidwe pakatimpakati wokulitsira ndi wobereketsera ndipo matani okwana 3 000 ndi a mbewu za mtundu wa nyemba, soya, khobwe, nandolo ndi mtedza. + China chomwe chasintha mu pologalmu ya chaka chino ndi mitengo yomwe alimi azigulira zipangizozi monga K3 500 thumba la fetereza, K1 500 mbewu yachimanga ndinso K500 mbewu za mtundu wa nyemba. + Mitengoyi ndiyokwererapo kuyerekeza ndi mitengo yammbuyomu ati pofuna kuchepetsa ndalama zomwe boma limaononga mupologalamuyi. + Nduna ya zachuma Goodall Gondwe adati boma limaononga ndalama zankhaninkhani mupologalamuyi motero lidaona kuti nkoyenera kuwonjezera ndalama yomwe alimi amaikapo mupologalamuyi. +",4 +"CCJP Ipempha Mafumu Agwiritse Ntchito Malamulo Akumudzi Bungwe la chilungamo ndi mtendere (CCJP) mu dayosizi ya Dedza lapempha mafumu a mboma la Ntcheu kuti adzigwiritsa ntchito malamulo omwe anakhazikitsa mmadera awo ndi cholinga chothandiza magulu a wanthu omwe akukumana nkhaza mmaderawo. +Mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli mu dayosiziyi a Horace Kasudze ndi omwe apereka pempholi pa mwambo wokumbukira amayi omwe bungwe la amayi la Champiti Women Action Group linakonza pogwirizana ndi amayi pa dziko lonse, mwambo womwe kuno ku malawi unachitika pa 5 March mboma la Machinga. +A Kasudze ati adandaula kaamba ka kuchuluka kwa milandu yogwililira ana komanso nkhaza za mbanja mbomalo. +Tinayamba kale kulimbikitsa kuti amayi azipezeka mmabwalo. Ngati amayi sakupeza chilungamo pa nkhani za nkhanza amatha kutaya moyo wawo msanga chifukwa cha kuchuluka kwa nkhanza, anatero a Kasudze. +Poyankhulapo mfumu yaikulu Champiti ya mbomalo inatsimikiza kuti pali kukondera poweruza milandu yokhuza nkhaza ngakhale anadandaula kuti nkhani zambiri za mtunduwu siziwafika. +Pena chilungamodi chimasowadi. Sitilora kuti mzimayi azunzidwe koma aphunzitsidwe moyenera. Nagti sakukhutitsidwa kwa magulupu akuyenera kubwera kudzasuma kwaine koma nthawi zambiri zimathera komweko, inatero mfumu yaikulu Champiti. +Iye wapempha mafumu aangono kuti asonyeze chilungamo pa milandu yonse yomwe imafika kuti aweruze. +",8 +" Mkokemkoke patsiku la chisankho Zipani zotsutsa boma zalembera bwalo la milandu la Supreme Court kuti lifotokoze bwino pa za yemwe akuyenera kusankha tsiku loti Amalawi adzasankhe mtsogoleri wa dziko lino. + Izi zikudza pomwe mpaka lero zikuoneka kuti tsiku lenileni silinakhazikike kuchokera pomwe bwalo la Constitutional Court lidalengeza kuti chisankhocho chichitikenso pasanathe masiku 150 kuchokera pa 3 February. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Msukwa: Tiadasankha June 23 Kuchokera apo, aphungu a Nyumba ya Malamulo adasankha kuti chisankhocho chichitike pa 19 May koma mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adakana kusainira biloyo. Apa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza kuti likukonza zoti chisankhocho chidzachitike pa 2 July, patangotsala tsiku limodzi kuti masiku 150 akwane. + Koma Lachinayi, komiti ya Nyumba ya Malamulo younikira za malamulo idakumana ndi wapampando wa MEC Jane Ansah komanso mlangizi wa boma pamilandu Kalekeni Kaphale adagwirizana kuti chisankhocho chidzakhaleko pa 23 June. + Potsatira izi, woimira zipani zotsutsa dzulo adakapempha bwalo la Supreme Court kuti litambasule bwino yemwe akuyenera kusankha tsiku lochititsa chisankhocho. + Woimira mtsogoleri wa UTM Party Khumbo Bonzoe Soko adati adakamangala kubwalolo lomwe lidavomerezana ndi bwalo la Constitutional Court kuti chisankho cha chaka chatha sichinayende bwino ndipo china chichitikenso. + Pounikira bwino chigamulo cha Supreme Court komanso poona za malamulo a chisankho, sizikumveka bwino ngati woyenera kusankha tsiku latsopano ndi a MEC kapena Nyumba ya Malamulo. + Polankhula atakambirana ndi Kaphale komanso Ansah, wapampando wa komitiyo Kezzie Msukwa adati adamvana kuti chisankho chikhalepo pa 23 June. + Tinawafunsa a MEC ndipo atitsimikizira kuti zokonzekera zili mmalo mwake moti chomwe chatsala nkusandutsa tsikuli lamulo basi, adatero Msukwa. + Malinga ndi Kaphale, ntchito yake patsikulo idali kuunikira mwina ndi mwina tsikulo lisanasankhidwe. + Ntchito yanga idali kungounikira basi osati kupanga tsiku ndiye ndaunikira mofunikiramo. Chofunika kwambiri chomwe ndawauza nkutsata zomwe malamulo a dziko lonse okhudza chisankho chovomerezeka amanena, adatero Kaphale. + Pankhani yoti makomishona ena ntchito ikutha pa 5 June 2020, Msukwa adati si ntchito ya komitiyo kukambirana poti Mutharika akudziwa kale zonsezo komanso akudziwa choyenera kuchita. + Ntchito yathu idali kupanga tsiku ndipo tapanga zinazo ndi udindo wa mtsogoleri wa dziko lino. Komanso ku MEC kuli likulu ndikukhulupirira kuti akudziwa chochita kuti chisankho chidzapitirire ngakhale ntchito ya makomishona itatha, adatero Msukwa. +",11 +" Adona Hilida afika pa Wenela Adafika pa Wenela tsikulo Abiti Patuma akuimba nyimbo yatsopano ya Lucius Banda. Inde ija waimba ndi Thocco Katimba: Mwandikumbuka. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Yahwe, wandimasula Wandimasula Yahwe wandimasula Wandipepesa Yahwe wandipepesa Nditi zikomo Yahwe wandimasula Ndinu patali. + Koma isanathe nyimboyo, wapamalo aja timakonda pa Wenela, Gervazzio, mnyamata wa ku Nkhotakota, adaika nyimbo ina ya mkulu wa kwa Sosola uja. + Kudali kuthyola dansi mkati mwa usiku. Musandifunse kuti nthawi idali bwanji chifukwa sindikuuzani. Ndipo mukadziwa mukufuna mutani? Idali nthawi yotaika basi. + Dansi ili mkati, mdima utafika pena, tidangoona kunja kukuwala ngati msana! Aliyense adanthunthumira. + Kutuluka panja, tidaona mzimayi ali palichero. Mzimayiyo adaponya nsalu imene idali paphewa pake pansi. Idali kufuka moto lawilawi ngati dziko la Malawi, dziko lamoto. + Tonse tidanthunthumira. + Posakhalitsa, ndegeyo idatera. Mayiyo adatsika. + Osandiopa, ndine wanuwanu Dona Hilida. Mumati sindigabwere kuno kumudzi? Ndabwera kudzaona mbale wanga Pitapo. Mudziwa adandigawirapo mawiribala 50 mmbuyomu, adayamba nkhani. + Mitima idakhalako pansi. Koma nanga munthu akafike pa Wenela pandege yausiku? Kodi kuchoka ku Zambia kufika pa Wenela kulibe basi? Izo zili apo, kudzera ku Zambia kuchokera ku Jubeki si kudzitalikitsa? Ayi ndithu, abale anzanga, tizionera limodzi. + Tsono bwanji mukubwera usiku chonchi? Nanganso bwanji mukubwera pamene mwana wanu Pitapo akufuna kuweruzidwa? adafunsa Abiti Patuma. + Mukumuzunziranji Pitapo? Simukuona akuzunzika? adafunsa Adona Hilida. + Taonani momwe abambo ovala nkhwaira, amene amayi awo adamwalira kaamba kosowa mankhwala akuzunzikira pomunyamula pamachira aja adanyamulira Listonia Susi ndi Chuma kalelo, adatero Abiti Patuma. + Koma, abale, inetu palibe chimene ndimatolapo pankhani zawozo. Kodi nanga ndidapondapo ku Nyumba ya Malamulo? Inetu Nyumba ya Chimfiti ku Zomba sindiyidziwa. Za Chingwes Hole, Emperors View ngakhalenso Mulunguzi Dam, inde koona nsomba za trout komanso mpandankhuku, ndimangomva mwa anthu. + Koma mayi, simungachititse msonkhano masana pa Nyambadwe pompa? Kuchoka pano pa Wenela simungathe mphindi 10, ndidatero. + Ndidaonjeza: Mukadzangoti mwafika pa Chimsewu, ndidzakuimbirani nyimbo ija ya Adona Hilida! Wa-wa-wa-wa. Komanso: Tulutsani wanuyo, timuone, ngati si dona, ife wathu ndi dona! Ngakhale ndikudziwa Moya Pete zikumulaka, nthawi yanga sinakwane. Mundiona ndibwera. Kugona kozizira ndakana. Inetu sangandipatse belo muja adachitira Kakali wathawa uja! adayankha Adona Hilida. + Koma, abale, kunjaku kuli zigawenga. Zoona kuthawa belo! Koma Kakali! Ndikumvatu kuti mnyamata ameneyu si pano. Sachita nawo za mowa, koma amagulira ena mkati mwa usiku. Mwina timaona afika pa Wenela ngati sanalowere ku Zobue kukaletsa nkhondo ya Renamo. +",15 +" NGAMBA IOPSEZANSO CHAKA CHINOUNDUNA Chaka chatha kudali kakasi pankhani ya ulimi mvula itadula pomwe mbewu zambiri, maka chimanga, zimamasula ndipo izi zidachititsa kuti alimi ambiri asakolole mokwanira moti pano ena njala idalowa kale. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Vutoli lidagwa kaamba ka mvula ya njomba, makamaka potsatira kusintha kwa nyengo, ndipo unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi wachenjeza kuti zomwe zidaoneka chaka chatha zingathe kuchitikanso chaka chino mmadera ena. + Mlimi kudandaula ndi kufota kwa mmera mmunda chaka chatha Undunawu wati potengera zomwe apeza a nthambi ya zanyengo, madera ena akhoza kulandira mvula yokwana pomwe ena ayi ndipo izi zikhoza kuchititsa kuti mvula idzadule msanga mmadera ena. + Polingalira kuti alimi ambiri amadalira ulimi wa mvula, undunawu wati alimi amalize msanga kukonza minda yawo kuti mvula ikangogwa adzabzale mbewu ndi mvula yoyambirira. + Pali chiyembekezo chakuti madera ena akhoza kulandira mvula yochepa, zomwe zingapangitse ngamba mkati mwa nyengo ya mvulayi komanso zikhoza kupangitsa kuti mvula isiye msanga, chidatero chikalata chomwe udatulutsa unduna wa malimidwe sabata yathayi. + Undunawu wati pofuna kuthana ndi vuto ngati lomwe lidaoneka chaka chatha mvula itadula mosayembekezera, alimi amalize kukonza minda yawo mwachangu. + Undunawu watinso alimi alingalire kubzala mbewu zocha msanga komanso atsatire njira ya kasakaniza ndi njira zamalimidwe zamakono zosunga nthaka, chinyontho ndi chonde monga kuphimbira nthaka. + Undunawu watinso pomwe ntchito zakumunda zikuyenda, alimi akangalikenso nkukolola madzi kuti ngati mvula ingadzadule mdera lawo, adzakhale ndi madzi okwanira a mthirira komanso omwetsa ziweto. + Polingalira za chakudya cha ziweto mtsogolo muno, undunawu wati alimi omwe ali ndi ziweto akumbukire kubzala nsenjere ndi mitundu ina ya udzu chinyezi chikakhathamira mnthaka kuti asadzavutike nyengo ya chilimwe. + Tikufuna alimi atsatire zimenezi kuti udindo wathu woonetsetsa kuti mdziko muno muli chakudya chokwanira ukwaniritsidwe. Chaka chatha alimi adadzidzimutsidwa chifukwa sadayembekezere zomwe zidachitika. + Si kuti tayamba izi chifukwa cha phunziro la chaka chatha, ayi. Tidayamba kalekale kulimbikitsa alimi kuti azikonzeka nthawi yabwino nkumadikira mvula kuti ikangogwa azithamangira kumunda kukabzala, adatero mlembi wamkulu muundunawu, Erica Maganga. +",18 +" Papsa tonola, kusolola kwaphweka ku Kapitolo Anthu ambiri agwidwa: Manjolo Kwagwa papsa tonola kulikulu la dziko lino (Capital Hill) ku Lilongwe komwe akuluakulu ena ogwira ntchito zowerengera chuma cha boma akuyendera zija amati mbuzi imadya pomwe aimangirira. + Sabata yokha ino akuluakulu awiri ogwira ntchito yowerengera ndalama za boma anjatidwa atapezeka ndi ndalama zokwana K10.8 million ndi ndalama zina zakunja zokwana $25,400 (pafupifupi K10 miliyoni) zomwe akuganiziridwa kuti adasolola mchikwama cha dziko. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Escom in free-for-all fuel scam Mneneri wa polisi mdziko muno Rhoda Manjolo wati anthu awiriwa ndi Martha Banda, wa zaka 35, yemwe amagwira ntchito yothandizira wowerengera chuma kunthambi yoyanganira chuma cha dziko lino yemwe adapezeka ndi ndalama zokwana K7.8 miliyoni mnyumba mwake Lachitatu lapitali. + Manjolo wati Banda adagwidwa patangotha tsiku limodzi wamkulu wowerengera chuma cha dziko lino Roosevelt Franklyn Ndovi atamangidwa kaamba kopezeka ndi ndalama zokwana K3 miliyoni mgalimoto mwake komanso $25,400 kunyumba kwake ku Area 25. + Tidakapanga chipikisheni kunyumba kwa Banda ku Area 49 ku Lilongwe ngati njira yofuna kufukula zomwe zimachitika mmaofesi owerengera chuma. Zonse zidayamba Lolemba titagwira mkulu wowerengera ndalama za dziko yemwe amafuna kutuluka ndi ndalama zokwana K3 miliyoni kuchoka kulikulu la dziko ndipo tidakapanga chipikisheni kunyumba kwake komwe tidakapeza ndalama zakunja zokwana $25,400, adatero Manjolo pouza Tamvani. + Iye adati kutengera ndi mmene kafukufuku wa polisi akuyendera, anthu ambiri ogwira ntchito kulikuluku amangidwa chifukwa pakuoneka kuti kusololaku kumayenda mmanja ambiri. + Panopa komiti ya Nyumba ya Malamulo yowona mmene ndalama za dziko zikuyendera la Public Accounts Committee (PAC) lalamula boma kuti liunike bwino mmene ndalama za boma zikuyendera kulikuluku. + Wachiwiri kwa wapampando wa komitiyi, Davieson Nyadani, wati komitiyi yaganiza zoti ofesi ya mkulu woyanganira za chuma ndi ofesi yomwe imayendetsa chuma cha boma ziunikidwe mwachifatse ndipo boma lilengeze zotsatira zake kuti anthu adziwe momwe ndalama zawo zikuyendera. + Mgwirizano wa mabungwe omwe si aboma wa Civil Society Organisations Grand Coalition wapereka masiku 30 kuboma kuti likonze chisokonezo chonse chomwe chafungatira kayendetsedwe ka boma. + Chisokonezochi chikukhudza katangale, kuba katundu wa boma komanso kuulula chuma chomwe akuluakulu a boma ali nacho. + Mchikalata chomwe mgwirizanowu walemba, mabungwewa akuti boma likalephera kukonza zolakwikazi pakhala zionetsero zosiyanasiyana kuphatikizapo kuletsa anthu kudula msonkho. + Zikuoneka kuti palowa chibwana, zikungokhala ngati palibe wotsogolera mmene zinthu zikuyenera kuyendera, chatero chikalatacho. + Mabungwe omwe alemba chikalatacho ndi Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP), Council for Non-Governmental Organisations in Malawi (Congoma), Civil Society Education Coalition (Csec) Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Centre for the Development of People (Cedep), Centre for Youth and Children Affairs (Ceyca). + Ena ndi Citizens for Justice (CFJ), Civic and Political Space (CPS), Church and Society-Livingstonia Synod, Malawi Health Equity Network (MHEN), Human Rights Consultative Committee (HRCC), NGO Gender Coordination Network (NGO GCN), The Governance Platform (GP), Malawi Economic Justice Network (Mejn), Public Affairs Committee (Pac) ndi Malawi Congress for Trade Unions (MCTU). + Mwezi wathawu apolisi adagwira mkulu wina, Patrick Sithole, wogwira ntchito yaukalaliki mboma, atamupeza ndi ndalama zokwana K120 miliyoni mgalimoto yake ya Toyota Fortuner, zomwe akumuganizira kuti adasolola mboma. Izi zidachitika mkulu woyanganira chuma mboma (budget director) Paul Mphwiyo, asadawomberedwe. + Tikumbamba pano Mphwiyo adakali kuchipatala cha Milpark ku South Africa komwe akulandandira chithandizo cha mankhwala atamuchotsa zipolopolo zinayi mmutu. +",2 +"Bungwe la AGRICOS Lati Ulimi wa Nthochi Ubwelera Mchimake Wolemba: Glory Kondowe Bungwe lothandiza alimi ndi luso lapadera la AGRICOS lachitatu, lati lili ndi chiyembekezo chakuti ulimi wa nthochi ubwereranso mchimake zaka zitatu zikubwerazi. +Mkulu oyendetsa bungweri a Justin Kaliwo anena izi mu mzinda wa Blantyre pa maphunziro a alimi a mbewuyi. +Chinthunzi chosonyeza imodzi mwa matenda a mbewu ya nthochi Pa tsikuli a Kaliwo anafotokodza zamene angatukulire ulimi wa nthochi ndi nyemba omwe bungweli ukulimbikitsa. +Iwo ati bungwe lawo lapeza misika yabwino kunja kwa dziko lino komwe nthochi ikufunika yochuluka ngakhale ulimiwu unalowa pansi kamba ka matenda omwe anagwira mbewuyi zaka zapitazi. +Bungwe la AGRICOS layika chidwi chothandiza alimi a mbewu ya nthochi komanso a mbewu za nyemba omwe ali ndi mwayi wa misika yabwino, anatero a Kaliwo. +A Kaliwo anati bungwe lawo likufuna kuthandiza alimi a nthochi kuti ulimuwu uyambenso kuyenda bwino ndipo anati athandiza alimi pothetsa matenda omwe anawononga mbewuyi zomwe zinachititsa kuti alimi ataye ndalama za nkhaninkhani. +Mwazina bungwe la AGRIGOS limathandiza alimi omwe ali mamembala ake pa luso la malimidwe a makono komanso momwe angapezere misika ya mbewu zawo. +",4 +"Mafumu Ayamba Kulandira Thandizo la Mankhwala Lapamwamba-Nduna Boma lati lili mkati mokonza dongosolo lakuti mafumu aakulu onse mdziko muno akhale pa ndondomeko yolandira thandizo la mankhwala mzipatala zapamwamba. +Nduna yowona za maboma aangono ndi chitukuko chakumidzi, Dr. Ben Phiri ndi omwe anena izi mboma la Mangochi pamene amakweza mafumu aakulu Chowe, Katuli ndi Makanjira kukhala Senior Chief, komanso kukweza magulupu ena anayi kukhala ma Sub T/A. +Pa mwambowu, ndunayi yalonganso a Cassim Linje Sinoya kukhala T/A Namabvi kutsatira imfa ya mfumu yomwe inalipo. +Dr. Phiri anati boma lapeza kuti mafumu ambiri amavutika pa nkhani za umoyo ndi zina ndipo walonjezanso kuti ma Paramount Chief onse akhala ndi chiphaso choyendera chapamwamba (Diplomatic Passport). +Polankhulapo Senior Chief Chowe inati kukwezedwaku kwawapatsa mangolomera kuti apitirize kugwira ntchito za chitukuko ndipo wapempha mafumu anzake kuti apewe kulpwetsa katangale pa ntchito yawo. +",11 +"Bambo Wafa Atawombedwa ndi Galimoto ku Kasungu Bambo wina wa zaka 30 zakubadwa wa mboma la Kasungu wafa atawombedwa ndi galimoto yomwe sikudziwika. +Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi mboma la Kasungu Sergeant Miracle Mkozi watsimikidza za ngoziyi poyankhula ndi Radio Maria Malawi. +Iye wati bambo ngoziyi yachitika pamudzi wa Chitete mbomalo ndipo zotsatira za kuchipatala zasonyeza kuti malemuyu, Masawu Ndawu wafa kaamba kovulala kwambiri mutu. +Kuno ku Kasungu mzibambo wa zaka 30 wafa ataombedwa ndi galimoto yomwe siikuziwika ndipo ngoziyi inachitika dzulo pa 25 May 2020 mmudzi wa Chitete pafupi ndi chikwangwani cha chitukuko cha mmatauni, anatero Mkozi. +Sergeant Mkozi wati muthuyu wafa kamba kovulala kwambiri mmutu ndipo apempha anthu oyendetsa galimoto kuti aziyima akachita Ngozi ponena kuti galimoto yomwe yachita izi siyinayime pa malopo. +",14 +"Makwaya a Amayi Akuyenera Kulimbikitsidwa Makwaya a Amayi mu arkidayosizi ya Blantyre awapempha kuti apitirize kudzipereka pofalitsa mthenga wabwino monga momwe makwaya a achinyamata amachitira. +Mkulu wowona luso la nyimbo mu kwaya ya amayi ya St. Marys ku Limbe Cathedral mu arkidayosiziyo a Steve Amidu alankhula izi pakutha pa maphunziro a tsiku limodzi omwe kwayayi inakonzera mamembala ake. +Iwo ati anakonza maphunzirowa ndi cholinga chofuna kulimbikitsa kwayayi kuti idzichita bwino potsogolera miyambo yosiyanasiyana ya chipembezo komanso kuti izichita bwino mu mipikisano yosiyanasiyana ya makwaya mdziko muno. +Makwaya a amayi akuyenera kulimbikitsidwa kuti mayimbidwe awo apite patsogolo kuti azichita bwino potsogolera mapemphero mtchalitchi komanso pa nthawiya festival, anatero a Amidu. +Mmawu ake wapampando wa kwayayi, mayi Ellena Abobolera anati kudzera pa maphunzirowa adzindikira kuti akuyenera kukhala olimbikira komanso achidwi ndi cholinga choti azichita bwino nthawi zonse. +",14 +"Apempha Akhristu Alimbike Popemphera Kolona Wolemba: Sylvester Kasitomu Bambo Edwin Lambulira omwe amatumikira mu dayosizi ya Mangochi loweruka lapitali alimbikitsa akhristu a mpingo wakatolika kuti azikonda kulimbika pa moyo wa mapemphero maka mumwezi uno wachibalalitso cha mpingo. +Bamboo lambulira amalankhula izi pambuyo pa mapemphero a kolona komanso nsembe ya ukalistiya yomwe inachitikira pa Goroto Ya Amayi Maria Amayi A Kolona ku kulikulu la wailesiyi ku Mangochi. +Iwo ati kuchita mapemphero pa goroto ya amayi Maria mu mwezi uno olemekeza amayi Maria wa kolona ndi chinthu cha mtengo wapatali. +Lero tachita misa pa goroto ya amai maria, ku wailesi ya amai maria mu mwezi wakolona zonsezi kulumikizana bwino ndipo zikungofuna kutithandiza kuti tidzindikire kuti nthawi zonse tikuyenera kupempha uneneri wa amai maria kuti atinenere kwa mulungu, anatero bambo Lambulira. +Mwazina iwo alimbikitsa akhristu kukonda mapemphero mu mwezi uno wachibalalitso cha mpingo kuti mpingo ufalikire ponseponse. +",13 +"Vicar General wati Maphunzitso a Mpingo Akuyenda bwino Wolemba: Glory Kondowe .mw/wp-content/uploads/2019/09/chilolo.jpg"" alt="""" width=""553"" height=""368"" />Bambo Chilolo: Maphunzitso akuyenda bwino kwambiri Vicar General wa dayosizi ya Zomba bambo Vincent Chilolo lachinayi lapitali ayamikira akhristu a mpingo wa katolika mu dayosizi ya Zomba kamba koonetsa chidwi pamaphunziro a mpingowu. +Bambo Chilolo ananena izi pofotokozera Radio Maria Website momwe ntchito ya zamaphunziro a akhristu mu mpingo-wu zikuyendera mu dayosizi-yo. +Bambo Chilolo ati ma sacrament amalimbikitsa moyo wachikhristu ndipo iwo amathandiza pokuza ubale wa akhristu ndi mulungu. +Maphunziro amenewa akuyenda bwinokwambiri. Chachikulu ndi chakuti Mulungu amafuna kuti ubale wathu ndi Iyeyo udzikula komanso ndi anzathu uziyenda bwino chifukwa iye amafuna kuti tizikhara naye pa ubwezi wabwino, anatero bamboo Chiwaya. +Bambo Chiwaya omwe padakalipano akutumikira ku Namitembo parishi ati ansembe akutenga nawo popereka maphunzitso kwa akhristu awo kuti athe kumvetsetsa bwino. +Iwo ati atenga gawo lalikulu pamaphunzitsowa mu dayosiziyi kuti maphunzirowa apitilire kuyenda bwino. +Iwo ati chiyambireni maphunzitsowa akhristu ambiri ali ndi chidwi kwambiri ndipo anthu ambiri adalitsa mabanja awo, kubatidza ana awo komaso kubwelera masacrament mosavuta. +",13 +" Mbusa amuganizira kugwirira wozelezeka Apolisi mboma la Neno akusunga mchitokosi mbusa wina wa zaka 52 yemwe amatchuka kutyi Pastor Joshua wa mpingo wa United of God pomuganizira kuti adagwirira mtsikana wodwala nthenda yakugwa wa zaka 16. + Mbusayo, yemwe dzina lake lenileni ndi Juwayo Antoniyo amachokera mmudzi mwa Siyali Traditional Authority(T/A) Chapananga mboma la Chikwawa. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi mneneri wa apolisi mboma la Neno Raphael Kaliati, Antoniyo adakumana ndi mtsikanayo Lachisanu pa May 5 akuchokera ku chigayo. + Mtsikanayo adaima panyumba ya mbusayo kupemphako madzi akumwa, ndipo mbusayo adamuuza kuti angolowa nkukamwera madziwo mnyumbamo. Apa adamutsatira mtsikanayu ndi kumugwiririra, adatero Kaliati. + Iye adati mtsikanayo adakamuneneza mbusayo kwa mayi ake omwe adakadandaula kupolisi. + Kalata yaku chipatala yatsimikiza kuti mtsikanayu adagwiriridwadi, adatero Kaliati. + Malinga ndi apolisiwa mbusayo aonekera kubwalo la milandu masiku akubwerawa. + Izi zakhumudwitsa mamembala a mpingowu. + Mkucheza kwathu ndi Traditional Authority Mlauli yemwenso ndi mmodzi mwa anthu omwe amapemphera mumpingowo, adati chokhumudwitsa nchoti mtsikanayu amagwa. + Mlauli adati mbusayo adayamba mpingowu mchaka cha 2014 ndipo anthuwa amamukhulupirira. + Mbusayotu amaonetsa ngati weniweni mzochitika zake. Nthawi zina amakafika mpaka ku Tete mdziko la Mozambique kukalalikira, choncho titamva kuti wagwidwa pokhudzidwa ndi nkhaniyo, tazunguzika, adatero Mlauli. + Iye adati Antoniyo wabwerera kuchoka ku Mozambique chaka chathachi. + Mlauli adaonjezera kuti mbusayu wasiya anthu opemphera pa mpingowo pa umasiye. + Ife pakutivutanso ndi poti iyeyu adayambitsa mipingo ku Mulanje komwe iliko iwiri, ku Ndirande mumzinda wa Blantyre, ku Zomba ndi ku Chikwawa, kodi nkhosa zake mmadera onsewa zitani, adadandaula motero Mlauli. + Mbusayu ali pa banja. +",15 +" Ngambi, Atusaye uncertain Flames midfield star Robert Ngambi and striker Atusaye Nyondo on Tuesday said they are most likely to miss Saturdays swim-or-sink 2015 Africa Cup of Nations preliminary round return leg against Benin. + The two players told The Nation in separate interviews from South Africa that, unless something develops up, they have already given up hope due to logistical hitches beyond their control. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Has returned to action: Ngambi The development comes as a setback for the Flames who need a full-strength squad for Saturdays showdown to overturn the tables having lost the first leg 1-0 away in Cotonou which both Ngambi and Nyondo also missed. + I had a meeting with the clubs [Platinum Stars] management over the issue, but what came out very clearly was that they do not want to release me and the reasons they are giving are my level of fitness having just recovered from injury and that the Benin match clashes with the clubs MTN8 match against Mamelodi Sundowns which will also be played on the same day, said Ngambi from Rustenburg in South Africa. + Ironically, Ngambis last appearance for the Flames was against Nigerias Super Eagles in a 2014 World Cup qualifier in September last year. Since then, he has missed a number of competitive and friendly matches due to injuries. + Nyondo also cast a doubt on his availability saying: I do not think my work permit will be ready anytime soon. I had assumed that it would be ready by this week, but from the look of things, I might even miss the early part of the season here. + It is very frustrating, but there is nothing I can do about the situation. Nevertheless, I am confident that the guys will do the job. + Nyondo cannot travel outside South Africa as his passport is with the department of Home Affairs for work permit renewal. + And with the increasing doubts on the availability of the duo, FAM has called up battle-scarred forward Esau Kanyenda, who according to chief executive officer Suzgo Nyirenda, is expected to fly in today. + However, Kanyenda said his release would be determined after meeting his club Polokwane Citys director Johnny Mogaladi yesterday. + Commenting on Ngambi, Nyirenda said they were waiting for Platinums final decision that was expected to be communicated later yesterday. + The problem is that apart from assessing his fitness, they [Platinum] also have a game on the very same day. So, it is indeed a tricky situation, but we havent given up yet. + As for Atusaye, it seems there is a change in the process of acquiring work permit in South Africa and it takes a bit longer. He is not the only player who has been affected. However, his club [Pretoria University] chairperson is scheduled to meet the PSL later today because they too fear they may miss the services of their key foreign players when the season starts, he said. + Apart from Kanyenda, defender Harry Nyirenda, midfielder Chimango Kayira and another striker Chiukepo Msowoya are also expected to arrive today. + Robin Ngalande arrived on Monday, DR Congo-based midfielder Joseph Kamwendo is expected on Thursday while Bloemfontein Celtic duo of Limbikani Mzava and Frank Gabadinho Mhango will be the last to join the team just over an hour before the match on Saturday. +",16 +"Mtolankhani Mdziko la Morocco Amangidwa Kaamba Kochita Zogonana Asanalowe Mbanja Wolemba: Thokozani Chapola 77"" src=""http://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/09/rassoin.jpg"" alt="""" width=""588"" height=""388"" /> Mlandu omwe mtolankhani wina wachizimayi wa mdziko la Morocco amayimbidwa pomuganizira kuti anachita zogonana asali pa banja komanso anachotsa pathupi, ayamba awuyimitsa kuti uzamvedwabe mtsogolomu kutsatira ziwonetsero zomwe anthu ena anachita panja pa bwalo la milandu. +Malipoti a wailei ya BBC ati kuchita zogonana usanalowe mbanja komanso kuchotsa pakati ndi milandu mdziko la Morocco. +Mtolankhaniyu Hajar Raissouni yemwe amagwira ntchito ku nyumba ina yosindikiza nkhani yomwe imadzudzula kwambiri boma la dzikolo akuukana mlanduwu ndipo nkhaniyi yadzetsa mpungwepungwe kwambiri mdzikolo pa nkhani yokhudza maufulu a wanthu. +Atolankhani komanso mabungwe omenyera ufulu wa anthu akukhulupilira kuti kumangidwa kwa mtolankhaniyu kwachitika pa zifukwa za ndale, ngakhale boma la dzikolo latsutsa izi. +Malinga ndi malamulo a mdziko la Morocco, anthu amene achita zogonana asanalowe mbanja amayenera kumangidwa kwa chaka chimodzi komanso mayi amene wapezeka kuti wataya mimba amayenera kumangidwa pakati pa theka la chaka mpaka zaka ziwiri. +Mlanduwu ati uzamvedwanso pa 16 September ndipo pa nthawiyi mtolankhaniyu akhala adakali mchitolokosi cha apolisi. +",7 +" Chaka cha anamwino ku Salima lero Kuli chaka lero ku Salima pamene anamwino mdziko lino akukondwerera tsiku lokumbukira ntchito yawo pa dziko lapansi. + Anamwino padziko lonse amapatula tsiku la 12 May chaka chili chonse ati popereka ulemu kwa katswiri wina wakale yemwe anayambitsa unamwino wa makono, Florence Nightingale yemwe anamwalira mchaka cha 1910 ali ndi zaka 90. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkulu wa bungwe la anamwinowa la National Organisation of Nurses and Midwives of Malawi (NONM), Dorothy Ngoma, anauza atolankhani kuti chikondwerero cha chaka chinochi chilunjika pa mutu womwe ukulimbikitsa zotengapo mbali polimbana ndi matenda ndi imfa. + Ngoma anatambasula kuti ngakhale dziko lino limadziwa zofooka zambiri pantchito za umoyo, magawo ochepa okha a anthu ndi amene amayesa kuchitapo kanthu. + Iye anati izi zikukweza chiwerengero cha odwala komanso omwalira kaamba ka matenda mdziko muno. + Mwachitsanzo, bungwe loona za umoyo pa dziko lonse la World Health Organization limalimbikitsa kuti namwino aliyense adziyanganira odwala osapyolera zana limodzi koma kuno kwathu namwino akumasamalira odwala oposa 3800 kaamba kuchepa kwa anamwinowa. Anatero Ngoma. + Pa mwambo wa ku Salimawu, anamwino onse akuyembekezeka kukagawana ntchito zosamalira odwala pa chipatala cha mbomalo komanso kusamalira mabwalo a sukulu ya sekondale ya Salima, ati pochitira umboni kuti ntchito za umoyo zingathe kupita patsogolo ngati manja angachuluke. + Kukakhalanso kupereka mphoto kwa ogwira ntchito za umoyo omwe achita bwino mchakachi ncholinga chowalimbikitsa komanso kukuza chidwi mwa anzawo. +",6 +" Sibwino kulekeza panjira kumwa ma ARV Mmodzi mwa anthu amene adapezeka ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ndipo akukangalika kuphunzitsa ena za matendawa Hannah Mandanda wati ntchito yolimbikitsa anthu amene akulandira ma ARV kuti asasiye kumwa mankhwalawa ndiyaikulu. + Polankhula pamaphunziro amene bungwe lothandiza anthu amene adawapeza ndi kachilombo la Dream ku Balaka, Mandanda adati kusiya kumwa mankhwala kwadzetsa imfa zomwe sizikadakhalapo. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Anthu ena amalandira mankhwala koma osamamwa. Uku nkulakwa. Masiku apitawa, tidali ku maliro a mayi wina amene ngakhale ankalandira mankhwala mwezi ndi mwezi, amangowabisa kuchipinda ndipo tidawapeza atatisiya, adatero Mandanda. + Mkulu woyanganira ntchito za Dream ku Blantyre, Jane Gondwe, adati vuto la odwala kuleka kumwa mankhwala likukulira kulira. + Ena amasiya chifukwa achipembedzo awauza kuti Mulungu wawachiritsa pomwe ena amanamizidwa ndi asinganga. Enanso amasiya chifukwa chitetezo cha mthupi mwawo chakwera koma ayi sichoncho. Mankhwalawa ndi akumwa moyo wonse, adatero Gondwe. + Iye adati ena amasiya kumwa ndipo akaona kuti matenda ayambanso kuvuta amayambiranso kumwa mankhwala. + Koma palibe chimene angaphule chifukwa kachilombo kamakhala kuti kakhwima ndi kupeza njira zina kuti mankhwalawo asagwire ntchito, adatero Gondwe. + Iye adati nchifukwa chake bungwe lawo limaphunzitsa anthu 65 woti azikaphunzitsa ena momwe angadzisamalire atawapeza ndi kachilombo ka HIV. +",6 +"DCT Ikuthana ndi Mchitidwe Woba Mankhwala Bungwe la Development Communication Trust (DCT) lati ndilokhutira ndi momwe ntchito zake za mu project ya Titeteze Umoyo Wabwino yomwe akuyitcha Influencing Citizen Participation Against Drug Pilferage, yayambira mboma la Mangochi. +Mmodzi mwa akulu-akulu a mbungwe-li mbomalo, mayi Zione Mayaya Mkanda ndi omwe anena izi pomwe bungwe-li limafotokozera adindo a zachitukuko pa za momwe ntchito za bungwe-li zakhala zikuyendera chiyambireni mwezi wa February chaka chino mbomalo. +Iwo ati ndi momwe bungwe-li lawonera, zikusonyeza kuti anthu a mdera la mfumu yayikulu Chilipa komwe akugwirako ntchito-yi tsopano ayamba kudziwa za udindo wotetedza miyoyo yawo pa nkhani za umoyo ndi zina zambiri. +Ntchitoyi yapereka mphamvu komanso liwu kwa anthu pa nkhani yokhudza mankhwala mzipatala ndipo akumatha kuwulura anthu omwe amagula komanso kugulitsa mankhwala mosavomerezeka, anatero a Mkanda. +Iwo ati padakalipano ntchitoyi yapita patsogolo kwambiri ndipo yathandiza kukweza umoyo wa anthu a mdera la Chilipa mboma la Mangochi. +",6 +"Mlatho uwu si uli ku Mwanza +Munthu atakutenga ku Blantyre usiku, kukumanga kumaso nkukakusiya pamlatho uwu, ukhoza kuyesa uli ku Mwanza utawerenga chikwangwani ichi. Nkhawa tsopano ikhoza kukhala kuti kubwerera ku Blantyre uyenera kulowera kuti? Komatu mtsinje uwu si uli ku mlatho uwu siuli ku Mwanza koma ku Nsanje! Mtsinjewu umakathira mumtsinje wa Shire. Kumayenda! +",11 +" Nganga yochotsetsa mimba ithawa ku Mchinji Kwa Brenda Tadi, singanga Nasikiti udali ulalo wochotsera pathupi kufuna kuzemba uchembere omwe tate wake sakudziwika koma mapeto ake watsikira kuli chete. + Singangayo atazindikira kuti mankhwalawo agwira ntchito molakwika adasamuka mwachinsinsi ndipo mpaka pano anthu a mmudzimo ndi apolisi sakudziwa komwe adalowera. + Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Wojambula watu akuona ngati zidali choncho patsikulo Msungwanayu yemwe adali ndi zaka 20 adazindikira kuti ali ndi pathupi pa miyezi itatu ali kale ndi mwana wina wa chaka chimodzio ndipo sadali pabanja. + Mneneri wa polisi ya pa Mchinji Moses Nyirenda adatsimikiza za imfa ya Tadi ndipo adati wachinansi wake, Chifundo White, adauza apolisiwo kuti Tadi adakwatiwapo koma banja lidatha ndipo amangokhala pankhomo pamakolo ake. + White adati pa 11 October, 2015 Tadi atazindikira za mimbayo adapita kwa singanga Nasikiti yemwe adamupatsa mankhwala azitsamba nkumuuza kuti akamwe kuti mimbayo ikachoke koma zinthu zidatembenuka. + Atamwa mankhwalawo, pa 12 [October 2015] adayamba kudandaula mmimba momwe amagudubuka namo nkumabuula ngati mwana. Titamufunsa adaulula kuti adakatenga mankhwala ochotsera mimba kwa singanga Nasikiti, adatero White. + Iye adati singangayo adali wodziwika kuderalo koma sadamvekeko mbiri yopereka mankhwala omwe zotsatira zake zidali zomvetsa chisoni ngati imfa ya mnasi wake, Tadi. + White adati Tadi adamwalira pa 13 October 2015 vuto la mmimbalo litafika posautsa kwambiri ndipo azitsamba ena atalephera kukonza zinthu. + Nyirenda adati za imfa ya msungwanayo zitamveka, anthu adali balalabalala kumusakasaka koma sadamupeze ndipo apolisi atafika kusakako kudapitirira komabe popanda chooneka. + Iye adati singangayo akadzapezeka adzazengedwa mlandu wopereka mankhwala oipa kwa munthu komanso kuchotsa pathupi zomwe zimatsutsana ndi malamulo a dziko lino. + Tadi amachokera mmudzi mwa Nkhumba T/A Mavwere mboma la Mchinji. + kuderalo koma sadamvekeko mbiri yopereka mankhwala omwe zotsatira zake zidali zomvetsa chisoni ngati imfa ya mnasi wake, Tadi. + White adati Tadi adamwalira pa 13 October 2015 vuto la mmimbalo litafika posautsa kwambiri ndipo azitsamba ena atalephera kukonza zinthu. + Nyirenda adati za imfa ya msungwanayo zitamveka, anthu adali balalabalala kumusakasaka koma sadamupeze ndipo apolisi atafika kusakako kudapitirira komabe popanda chooneka. + Iye adati singangayo akadzapezeka adzazengedwa mlandu wopereka mankhwala oipa kwa munthu komanso kuchotsa pathupi zomwe zimatsutsana ndi malamulo a dziko lino. + Tadi amachokera mmudzi mwa Nkhumba T/A Mavwere mboma la Mchinji. +",6 +" Gulewamkulu, agumula sitolo Gulewamkulu wina Lachwiri lapitalo akumukayikira kuti adagumula sitolo ina pamsika wa Nkhalambayasamba mboma la Mchinji ndipo akumukaikira kuti adasakaza katundu wa K3.5 miliyoni. + Mneneri wapolisiyo, Kaitano Lubrino, Lachisanu adati apolisi amanga anthu 16 amene akuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyo. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apolisi kuyendera sitolo idathyoledwayo Anthu onsewa tikuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi zophwanya sitoloyo komanso kuba katundu, adatero Lubrino. + Malinga ndi Lubrino, kuderalo kudamwalira mkulu wina wa bizinesi Rabson Wisalamu ndipo imfayo idadabwitsa anthu. + Malinga ndi mfumu Nani yomwenso ndi mbale wa malemuyo, imfayo anthu amaganiza kuti imfayo idali yamatsenga. + Adali mushopu yake akugulitsa katundu. Kenaka tidangomva kuti mthupi mukumuwawa, kupita naye kuchipatala cha St Gabriel, adangoti ndagona pano. Kwathu sadayambane ndi aliyense, tikupenekera kushopuko kuti alipo adayambana naye kuti mpaka amuchitire chipongwe, adatero Nano polankhula naye pafoni. + Patsiku logumula sitoloyo, maliro a Wisalamu adaikidwa, ndipo mwambo utatha, akuti kudavumbuluka gulewamkulu pamsikawo. + Guleyo akuti adalipo 20, ndipo atafika pagolosale ya Julaye, adagumula shopuyo ndi kuyamba kutenga katundu wina akumusakaza. + Kafukufuku wathu wapeza kuti pamene guleyo amafika nkuti Julaye ndi banja lake atathawa kale ndipo komwe ali sikukudziwika koma tikufufuzabe, adatero Lubrino. Izi zitachitika guleyo adabwerera atatuta katundu wa mshopumo. + Mphekesera zikumveka kuti guleyo amachokera ku dambwe la Nani chifukwa kumeneko ndi komwe kumachokera malemuwo. + Koma mfumu Nani yauza Msangulutso kuti ilo ndi bodza. Ine ndi anthu anga titachoka kumanda tidabwerera kunyumba kukapitiriza mwambo wa maliro. Dziwani kuti ife tidavomereza imfa ya munthu wathu ndipo palibe amene tikumuganizira, adatero amfumuwo. + Lubrino wati apolisi anjata gulupu Kabuthu amene dzina lonse ndi Tenthani Nsaima a zaka 46 komanso woyanganira msika wa Nkhalambayasamba, Daniel Joseph wa zaka 40 onse a kwa mfumu Mavwere mbomalo kuti akayankhe mafunso angapo za umbandawo. + Posakhalitsapa, gulewamkulu adagwidwa ku Chikwawa ataba mbuzi, komanso mumzinda wa Lilongwe guleyo wakhala akugenda galimoto zomwe sizimupatsa ndalama. + Mfumu ya mtundu wa Achewa, Kaomba akuti uyu si gulewamkulu koma zigandanga dzomwe zikufuna kuononga chikhalidwe chawo. + Awa akungotionongera mbiri. Gulewamkulu amasunga mwambo. Ichitu ndi chikhalidwe, adatero. + Apolisi ati akufufuzabe kuti anjate amene adachita chipongwecho. +",15 +"CWO Yagawira Ansembe Zipangizo Zozitetezera ku Coronavirus Mpingo wa katolika mu arkidayosizi ya Blantyre wayamikira bungwe la amayi achikatolika la Catholic Women Organisation (CWO) kamba kopereka thandizo la zipangizo zotetezera ansembe ku nthenda ya COVID-19. +Tamani: Awonetsa chitsanzo chabwino A Vicar General a mu arch-dayosiziyi bambo Boniface Tamani alankhula izi ku nyumba ya asembe opuma ya St. James ku Limbe Cathedral pomwe amayiwa amapereka thandizoli. +Bambo Tamani ati ndi okondwa kuti amayiwa athandiza ansembe awo, maka padakalipano pomwe chiwerengero cha anthu opezeka ndi nthenda-yi chikukwera mdziko muno. +Iwo ati izi zithandiza pa ntchito zopereka chitetezo chokwanira kwa ansembewa ku kachilomboka. +Amayiwa awonetsa chitsanzo chabwino. Ndipo ma mask amenewa atithandiza ife ansembe kuti tigwire ntchito yathu moyenera pamene tikukapereka ma sacrament ndi zina, anatero bambo Tamani. +Mayi Lucy Vokhiwa ndi wapampando wa bungwe la amayi achikatolika la Catholic Women Organisation mu arch-dayosiziyi yemwenso ndi wapampando wa bungweli mdziko muno ndipo anati, Tinagwiritsa ntchito luso lathu ife ngati amayi ndipo tinatolera nsalu za CWO ndi kuzisoka kuti zikhale ma mask ndipo ndi zomwe tazapereka panozi. +Pamenepa iwo alimbikitsa amayi achikatolika mmadayosizi onse mdziko muno kuti atengepo mbali pogwiritsa ntchito luso lawo mu njira zosiyanasiyana pofalitsa nthenga wa kapewedwe ka Coronavirus. +",6 +" Ngakhale panali zovuta, chisankho chayenda Bungwe lophunzitsa Amalawi zosiyanasiyana kuphatikizapo za demokalase la National Initiative for Civic Education (Nice) lati ngakhale chisankho cha chaka chino chinakumana ndi mikwingwirima, chidayenda bwino. + Povumbulutsa zimene bungwelo lidapeza pa momwe chisankhocho chidayendera ku hotela ya Victoria mumzinda wa Blantyre Lachinayi, mkulu wa bungweli Ollen Mwalubunju adati Amalawi ayenera kudekha podikira chisankho chimene chidachitika Lachiwiri. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ollen Mwalubunju Pofika Lachinayi, zotsatira za chisankhocho zidali zisadalengezedwe ndipo madera ena adali asanamalize kuvota. + Chisankhochi chakumana ndi mikwingwirima monga kusowa kwa zipangizo zina, zimene zidachititsa zipolowe mmadera ena. Koma zonse zili apo, chisankhocho chidayenda bwino, adatero Mwalubunju. + Malinga ndi Mwalubunju, Amalawi ayenera kudekha poyembekeza zotsatira za chisankhocho chifukwa kuchita phuma kukhoza kudzetsa mavuto. + Tiyamike a MEC chifukwa pamene pamakhota, iwo samachedwa kupakonza. Umu ndiye ziyenera kukhalira, adatero Mwalubunju. + Chisankho cha Lachiwiricho chidali cha chisanu kuchitika mdziko muno kuchokera pamene kudadza ndale za zipani zambiri. Pamene timalemba, nkuti wopambana asadadziwike. +",11 +" Adzikonzera mpumulo wa bata Ukayenda umaona agalu a michombo ndithu. Ku Rumphi aliko oyenda masanasana pamene bambo wina wa zaka 62 wakumbiratu manda owaka bwino kuyembekezera tsiku lomwe Namalenga adzati kwatha. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Sasintha Mnozga, yemwe ndi mbusa wa mpingo wa African Church adakonza mandawa ndi ndalama zoposa K200 000 mmudzi mwa Mnozga, mfumu yaikulu Chikulamayembe mbomalo. + Koma mafumu mderali ndi wodabwa ndi mchitidwewu, zomwe akuti ndi zotsutsana ndi chikhalidwe cha Atumbuka pakuti munthu saloledwa kukumbiratu manda ake. + Mandawo ndi amenewa: Pali tsiku lakubadwa koma palibe lakufa Mnozga, pocheza ndi Msangulutso Lachitatu, adati sakuonapo vuto lililonse mwakuti pano akusakasaka makobidi ena kuti aguliretu bokosi lomwe adzamuyikemo akamwalira. + Ndikufuna kukonzeratu zonse kuti abale anga asadzavutike kusakasaka makobidi okonzera manda anga ndikadzamwalira. Abale anga ambiri ndi ovutika moti sangadzakwanitse kugula ngakhale bokosi, adatero Mnozga yemwe ali ndi ana 10. + Iye adati china chomwe chidamuchititsa kuti akumbiretu manda ndi momwe anthu salemekezera maliro kumanda. + Anthu amangoponya dothi pamwamba pabokosi ngakhale litakhala la makobidi ochuluka bwanji. Izi sizimandisangalatsa konse. + Mandawa ndawakonza ndi miyala komanso matumba 11 a simenti. Izi zikutanthauza kuti bokosi langa silidzakhunzana ndi dothi monga mmene zimakhalira mmanda ena, adatero Mnozga. + Mnozga amachitanso bizinesi pa boma la Rumphi. Ali ndi chigayo komanso malo ogonapo alendo. Iye adali mfumu kumudzi kwawo koma adasiyira mwana wawo atayamba ubusa mchaka cha 2001. + Pamene adayamba kukumba mandawa mchaka cha 2013, abale awo adawakaniza koma iwo adakakamirabe. Poyamba ankakana koma nditawalongosolera chifukwa chomwe ndimachitira izi adavomera mosasangalala momwemo. + Koma kwa mafumu silidali vuto chifukwa adali anzanga paja nane ndidali mfumu, adatero Mnozga. + Mfumu yaikulu Chikulamayembe, yomwe idati idawaonapo mandawa, idakana kulankhulapo pankhaniyo. + Koma mfumu Kayiwale Chirambo ya mderali idati zomwe adachita Mnozga sizololedwa pa chikhalidwe chawo. + Pachikhalidwe chathu sitivomera munthu kukumbiratu manda ake. Koma vuto ndi lakuti masiku ano anthu ali ndi ufulu ochita zomwe akufuna. Pachifukwa ichi, mpovuta kuti timuletse, adatero a Chirambo. + Iye adati sakudziwa chomwe chidachititsa Mnozga kubwera ndi ganizo lotereli. + Ife sitikudziwa kuti kaya ndi misala, kaya ndi uKhristu kapena chuma. Tonse ndife odabwa, koma palibe chomwe tingachitepo chifukwa chakuti ndi ufulu wake kutero. + Koma kukanakhala kwakale tikadawaitanasa nkuwaletsa kuchita zimenezi. Atati akana tikadatha kuwalanga, adatero Chirambo. + Mnozga siwoyamba kudzikumbira manda mbomali. Pa Mzokoto padalinso a SS Ngoma yemwenso adazikumbira manda. Koma atamwalira abale awo adakhaniza zokawayika kwina ndi komwe adamanga mandawo. + Asanamwalire, mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika adakonzeratu nyumba yomaliza yomwe adagonamo iye ndi mkazi wake Ethel. Mandawo amatchedwa Mpumulo wa Bata. +",15 +" Mutharika asosola nthenga atsogoleri .asankha nduna, koma Chimunthu Banda aukana Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika sabata imene ikuthayi anali wotangwanika zedi chifukwa ndiye wasosola nthenga akuluakulu ena mboma ngakhalenso mchipani chake cha Democratic Progressive Party (DPP). + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chimunthu Banda (Kumanja) wakana unduna wa zamigodi Lachinayi, Mutharika adasankha nduna zatsopano 32 kuphatikizapo zochokera kuchipani cha United Democratic Front (UDF) chomwe ali nacho mumgwirizano komanso Henry Chimunthu Banda, yemwe adapikisanapo ndi Mutharika pofuna kuimira DPP mu 2014. Dzulo Chimunthu Banda adakana undunawo. + Koma Mutharika, polengeza ndunazo, sanatchule dzina la wachiwiri wake Saulos Chilima, yemwe bwalo la Constitutional Court lidati abwerere pampando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko. Gawo 79 la malamulo a dziko lino limaneneratu kuti wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino amayenera kukhala mgulu la nduna za boma. + Ndipo Mutharika adasankha Atupele Muluzi, Lilian Patel komanso Clement Chiwaya kuchokera kuchipani cha UDF pamndandanda wa ndunazo. + Zina mwa nduna zimene zabwerera ndi Everton Chimulirenji, Chipiliro Mpinganjira, Bright Msaka, Ben Phiri, Joseph Mwanamvekha, Ralph Jooma, Mary Navicha, Jappie Mhango, Nicholas Dausi, Symon Vuwa Kaunda, Salim Bagus ndi Mark Botomani. + Ena mwa amene angosankhidwa kumene ndi Kamlepo Kalua, Kenneth Ndovie, Grace Kwelepeta, Chimwemwe Chipungu, Grezelder Jeffrey komanso Mary Makungwa. + Pambali pa izi, Mutharika adasonyezanso mphamvu zake msabatayi pomwe adakana mabilo ofuna kusintha malamulo a zisankho komanso adakana kumva pempho la komiti yoona zolemba ntchito akuluakulu ena mboma la Public Appointments Committee (PAC) kuti iye achotse makomishona a bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC). + Iye adakananso kusayinira mabilo ofuna kusintha malamulo ena oyendetsera zisankho popeza adati akutsutsana ndi malamulo aakulu a dziko lino. + Pambali pochotsa nduna zake zonse sabata yatha, Mutharika msabatayi adachotsa mkulu wa asilikali Vincent Nundwe ndi wachiwiri wake Clement Namangale ndi kusankha Andrew Namathanga kukhala mkulu wa asilikali komanso Davis Mtachi kukhala wachiwiri wake. Iye adasinthanso mipando ya akuluakulu ena a asilikaliwo. + Kusinthako kudafikanso kuchipani chake cha Democratic Progressive Party (DPP) komwe Mutharika adachotsa magavanala a kumpoto (Ken Sanga) ndi pakati (Bintony Kuntsaira). Iye adasanha Christopher Mzomera Ngwira kukhala gavanala wa kumpoto komanso David Kambalame kukhala gavanala wa pakati. + Nako kupolisi mipando ya akuluakulu ena idasintha pomwe akuluakulu ena mzigawo adasamutsidwa mosiyanasiyana. + Malinga ndi kadaulo wa zandale ku Chancellor College Mustapha Hussein adati kusasainako kuonetsa kuti Mutharika akufuna anthu adziwe kuti ndiye ali pa chiongolero. + Akufuna kuonetsa kuti akulamula ndiye ngakhale pali chikonzero choti chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chichitikenso, adatero Hussein. + Lachiwiri, Mutharika kupyolera mwa mneneri wake Mgeme Kalilani adati sangachotse makomishona monga a PAC adapemphera chifukwa padali zokhota zina. + Ndidalandira lipoti la PAC ndipo ndaliwerenga koma lili ndi zofooka zambiri. Mwa zina, silikunena ngati makomishona adauzidwa za zofooka zawo asadakaonekere, ngati adapatsidwa mpata wolumikizana ndi maloya awo komanso likuoneka ngati adangotengera chigamulo cha khoti chomwe tidapanga apilo kukhoti lalikulu la Supreme, adatero Mutharika. + Iye adapitiriza kuti makomishona omwewo ndiwo adayendetsa chisankho cha aphungu ndi makhansala zomwe zidavomerezedwa ndiye zidatheka bwanji kuti asakhale akadaulo pachisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chokha. + Pa zifukwa izi, apulezidenti akuti sadavomere lipoti la PAC ndipo sachotsa komishona aliyense kuphatikizapo wapampando wake Jane Ansah mpaka chigamulo cha apilo, adatero Kalilani. + Bwalo lounikira malamulo aakulu kwambiri mdziko lino lidagamula pa 3 February 2020 kuti komitiyo iunike makomishona onse mmodzimmodzi ngati ali oyenera kuyendetsa bungwe la MEC ndipo lipereke zomwe lipeze kwa mtsogoleri wa dziko lino. + Chigamulocho chimatsatira samani ya mtsogoleri wa Malawi Congress Party (MCP) Lazaru Chakwera ndi wa UTM Party Saulos Chilima omwe adadandaula kuti bungwe la MEC ndi chipani cha DPP adasokoneza chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino cha pa 21 May 2020. +",11 +" Apezereni obwera chochita, asadzabwererenso ku Joni Pamene Amalawi ena othawa kuinga anthu a maiko ena kumene kwagundika ku South Africa ati ndi zokhoma zimene aziona sabwereranso ku Joniko, mafumu ena apempha boma kuti lipereke mwayi wa ntchito kwa Amalawi kuti izi zitheke. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Sabata zapitazi, anthu a ku South Africa akhala akuthotha anthu a maiko ena chifukwa ati akuwalanda ntchito, akazi komanso mwayi wochita bizinesi. Ziwawazo zachititsa akunja ena kulandidwa katundu, kuvulazidwa ndi kuphedwa kumene. + Potsatira chipwirikiticho, inkosi ya Makhosi Mmbelwa ya ku Mzimba ndi Senior Chief Chimwala ya mboma la Mangochi apempha boma kuti lipereke mpamba kwa anthuwa woyambira bisinesi kapena ntchito za manja. Mzimba ndi Mangochi ndi ena mwa maboma amene amatumiza Amalawi ambiri ku Joni. + Mafumuwo ati kuchepa kwa malipiro pa ntchito, kusowa kwa ntchito, kukwera mtengo kwa chiongola dzanja anthu akakongola ndalama ku banki, ndi zina mwa zifukwa zomwe adathawira mdziko muno ndi kukwawira ku South Africa komwe ndalama si nkhani. + Mfumu Chimwala yomwe ana ake atatu ali ku Joni yati boma lionetsetse kuti lapereka mwayi wa ntchito kuti achinyamatawa azigwira kusiyana ndi kukhamukira ku South Africa. + Achinyamata akhale ndi mwayi wambiri wopeza ntchito komanso maganyu. Boma likakonza izi, mavutowa akhala mbiri yakale. Sindikutanthauza kuti sadzapitanso koma chiwerengero chake chingachepe kusiyana ndi momwe zilili pano, idatero mfumuyo. + Naye Mmbelwa, yemwe ndi mfumu yaikulu ya Angoni a ku Mzimba, akuti anthuwa sanganeneretu kuti sadzabwerera mdzikolo. + Koditu anthuwa amapita kukasaka buledi, ndiye ngati tikufuna kuti asadzapitenso, ndi bwino pakhale malipiro okwera mmakampanimu komanso pakhale mwayi wa ntchito, adatero iye. + Mkulu wa bungwe la zachuma la Economic Association of Malawi (Ecama) Henry Kachaje akuti Amalawi sadzaleka kupita mmaiko otukuka kukasaka ndalama ngati Malawi sakonza nkhani za chuma. + Achinyamata sadzasiya kupita mmaiko ena otukuka kukasaka mwayi, pokhapokha Malawi atatukuka pachuma. Nkovuta kusunga wachinyamata mdziko muno popanda ntchito, adatero Kachaje. + Iye adati Malawi akuyenera kuchilimika kuti athe kupereka mwayi wa ntchito kwa achinyamata. Tikuyenera kuthandiza kwambiri maunduna amene angapereke mwayi wa ntchito wambiri monga unduna wa zokopa alendo. Tsoka lakenso palibe chikuchitika chofuna kutukula undunawu, adatero Kachaje. + Lolemba nduna ya zofalitsa nkhani Kondwani Nankhumwa, Amalawi awiri adaphedwa pa ziwawazo ndipo 3 200 akhudzidwa ndipo ali pamndandanda wobwerera kuno kumudzi. Anthuwa adayamba kufika mdziko muno Lolemba usiku ndipo akusungidwa ku Blantyre ndi Lilongwe poyembekeza kuti atumizidwe mmakwawo. + Anthu onse amene tidacheza nawo adakana kwa mtuu wa galu kuti sangabwererenso. Mmodzi mwa anthu obwererawa, Yusuf Amidu wa mboma la Mangochi, akuti amagwira ntchito yowotcherera zinthu kwa munthu wina mdzikolo. Amidu akuti amalandira K16 000 pa sabata, kusonyeza kuti pa mwezi amapeza K64 000. + Ntchito ngati iyi mdziko muno ili ndi malipiro osaposera K25 000 pa mwezi malinga ndi Amidu. Iye adati ndalamayo siyingathandize munthu amene ali pabanja. + Zingathandize boma litaunikira kuti izi zayanganidwa bwino. Zitatero, palibe ngakhale mmodzi pagululi angabwererenso ku South Africa. Kuli mavuto, timangopitira kuthawa zokhoma kuno, adatero Amidu amene watha zaka zitatu mdzikolo. + Zokhoma zimene Amalawi ena akumana nazo si ndizo. Mwachitsanzo, Alick Wyson wa mboma la Mangochi adaomberedwa pachifukwa. Iye akuti adachitidwa chipongwecho ndi anthu a mdzikolo pa 24 December chaka chatha. + Ngakhale Amalawi ambiri akumva za zipolowezo panopa, zidayamba kumapeto a chaka chatha pomwe nanenso ndidaona zokhoma, adatero iye. + Zione Khombeya amene ali ndi pathupi pa miyezi 7 akuti adathamangitsidwa mnyumba mwake madzulo pamene amati aziphika chakudya. + Gulu la anthu limene limasaka obwera akuti lidayamba kuthethetsa anthu amene si mbadwa za dzikolo ndipo iye limodzi ndi mwamuna wake adathawa ndi kukabisala. Adavulazidwa mwendo pothawapo. + Evelyn Thumba wa mboma la Thyolo adamuvulazanso mwendo pamene amathawa. Pamene amatsika pa Kamuzu Stadium, miyendo yake idali yotupa ndipo adafikira mmanja mwa achipatala. + Aka sikoyamba kuti zipolowe zotere zibuke ku South Africa. Mu June 2008, dziko la South Africa lidachitiranso mtopola alendo a mmaiko ena amene akukhala mdzikolo ndipo anthu 60 adaphedwa pamene anthu oposa 600 adavulazidwa. + Dziko la Malawi lidakatengako mzika zake zoposa 1 000 kaamba ka ziwawazo koma zipolowezo zitazizira, khamu la anthu lidabwereranso mdzikomo. + Koma Nankhumwa akuti padakali pano boma laponya maso ake populumutsa mzika zomwe zikuvutika ku South Africa ndipo zina zonse zibwera pambuyo. + Nankhumwa akuti boma lili ndi ndondomeko zambiri zomwe lakonza zofuna kuthandizira anthuwa. + Maso athu ali powapulumutsa kaye ndipo zina zonse zitsatira. Sikuti tangokhala, adatero iye. + Kutsatira chipwirikiticho, dziko la Malawi lidayamba kututa nzika zake kuyambira Lolemba pamene anthu 390 adatengedwa pa mabasi 6 amene adafikira pabwalo la Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre. +",10 +" Chitetezo chachepa, tithandizenianthu Anthu mdziko muno apempha boma kuti lichite changu pobwezeretsa chitetezo chomwe ati chalowa libolonje mmasiku apitawa. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zalankhulidwa mkati mwa sabatayi pomwe mmadera mwina anthu aphedwa ndi achiwembu komanso kuba kwakula. + Pempho la anthuli likudza pomwenso mkulu wa apolisi mdziko muno, Lot Dzonzi adaitanitsa akuluakulu apolisi mmadera osiyanasiyana sabata yathayi kuwafotokozera za kukhumudwa kwake kaamba ka kusokonekera kwa chitetezo mmadera ena mdziko muno. + Iye adati ngakhale adalibe mndandanda wa momwe zilili, komabe malipotimaka ku Lilongwe ndi ku Blantyreakukusonyeza kuti chitetezo chasokonekera. + Mwachitsanzo, ku Namatapa mu mzinda wa Blantyre, dalaivala wina adapezeka ataphedwa sabata ziwiri zathazi. Munthu wina adapezeka ataphedwa pamsika wa Bangwe ndipo wina adapezekanso atafa ku BCA mumzinda womwewu. Madera atatuwa ndi oyandikana. + Mneneri wapolisi ya Limbe, Chifundo Chibwezo adatsimikiza za kuphedwa kwa anthuwo. + Umbanda Ndipo msabatayi, mbanda zomwe sizikudziwika zidazunguza madera angapo mumzinda wa Mzuzu, pomwe zidaswa nyumba ya mwenye wina ndikuba K10 miliyoni ndi katundu wina. Mbavazo, zidakathyolanso nyumba ina ndikuba K500 000 ndi golide wa K400 000. + Nako ku Chilomoni, malinga ndi Gulupu Chibwana, anthu asanu akhapidwa ndi achiwembu mwezi wa Juni wokha, zomwe mfumuyo ikuti nzachilendo chifukwa deralo limadziwika kuti ndi la bata. + Chibwana wati Lamulungu lathali apolisi adakachititsa msonkhano wa momwe angathanirane ndi aupanduwo ndipo adakhazikitsa achitetezo a mmudzi. + Kukumabwera anyamata oposa 15 omwe akumakhapa anthu omwe akuchita bizinesi. Akafika msitolo akumakhapa mwini malowo ndipo anthu asanu agonekedwa kuchipatala cha Gulupu potsatira ziwembu zotere, adatero Chibwana. + Naye mneneri wa apolisi mdziko muno, Davie Chingwalu, watsimikiza zakusokonekera kwa chitetezo mmadera ena, koma wati anthu asade nkhawa chifukwa apolisi akhwimitsa chitetezo. + Iye adati apolisi agwira kale ena omwe akuganiziridwa milandu yosiyanasiyana. + Nzoonadi kuti madera ena asokonekera, mwachitsanzo, ku Lilongwe. Koma anthu asadandaule. + Pano tagwira anthu asanu omwe tikuwaganizira kuti adaba K24 miliyoni ku Crossroads mumzinda wa Lilongwe. + Takhazikitsanso ndondomeko mmadera zoti zitithandize kugwira omwe akuchita izi, adatero Chingwalu. + Iye adatsutsa mphekesera zoti apolisi aletsedwa kumayenda ndi mfuti. Ndipo iye adatinso sizoona kuti chitetezo chikulowa pansi chifukwa cha mawu a Dzonzi, yemwe adachotsa zoti apolisi akhoza kuombera ndi kupha mbanda. + Apolisi amaloledwa kugwiritsa ntchito mfuti mwa malamulo, koma pali ndondomeko zoyenera kutsata potero. Mawuwa adali kungotambasula kuti apolisi ayenera kukumbukira kulemekeza ufulu wachibadwidwe wa anthu, komanso kutsatira ndondomeko yogwirira ntchito yawo, adatero iye. + Chitetezo chofooka Chingwalu adati zaka zonsezi, chitetezo pena chimafooka, kaamba ka zinthu zina, koma apolisi nawo amabwera ndinjira zawo zotetezera anthu. + Nduna ya chitetezo Uladi Mussa adati ndi udindo wa Amalawi onse kuthandiza apolisi kuthana ndi umbava komanso umbanda mdziko muno. + Tonse tikhale alonda ndi kuneneza anthu amene tikuwakaikira umbanda, adatero iye. + Thambo Linyoka wa mmudzi mwa Matchereza kwa T/A Phambala mboma la Ntcheu wati madera ena oyandikana ndi kumeneko anthu akuthamangitsidwa ndi achipongwe. + Angapo adandaula kuti akuthamangitsidwa, koma sizidafike poopsetsetsa, adatero mkuluyo. + Laitoni Kufandiko wa ku Chilomoni wati anthu ochita geni kumeneko ali pachiopsezo chifukwa cha ambandawa. + Akumaponya mwala nkutchola chitseko; anthu oposa asanu akhapidwa ndi akubawa. Izi zangoyamba kumene. + Mkulu wina wogulitsa mayunitsi amukhapa ndikumulanda ndalama; kuno kwavuta koma tikukhulupirira kuti zinthu zisintha chifukwa cha polisi ya mmudzi yomwe yakhazikitsidwa, adatero wageniyu. + Bata T/A Mlumbe ya mboma la Zomba yati kumeneko adakhazikitsa polisi ya mmudzi ndiye zikumangomveka mwa apo ndi apo kuti kwina kwatcholedwa. + Mfumu yaikulu Kaomba ya mboma la Kasungu yati kumeneko kuli bwino ndipo palibe zosokonekera. + Kaomba wapemphabe apolisi alimbikitse chitetezo kuti pasapezeke wina wosokoneza. + Pano apolisi ku Mtandire mumzinda wa Lilongwe amanga tenti pafupi ndi pamalo pomwe mtsogoleri wadziko lino Joyce Banda adati amayi ndi atsikana oposa 70 akugwiriridwa pa mwezi. + T/A Njewa ya ku Lilongweko idayamikira apolisiwo ponena kuti anthu akhala akupempha polisiyo kwanzaka 20 kotero kukhazikitsidwa kwa polisiyo kukhwimitsa chitetezo mderalo. +",7 +"PMS Yapempha Makolo Asamalire Ana Awo Ofesi yowona za mabungwe a utumiki wa a Papa ya Pontifical Mission Societies (PMS) yapempha makolo mu mpingowu kuti athandize ana awo kutenga nawo mbali pa maphunziro a mpingowu kudzera pa Radio Maria Malawi. +Mkulu wa ku ofesiyi bambo Vincent Mwakhwawa anena izi pambuyo pa program ya ya anawa pa Radio Maria. +Iwo ati maphunzirowa anawakonza kuti anawa adzipitiriza kuphunzira za mu katikisimu wa katolika kudzera pa wailesi, poyanganiranso kuti anawa anasiya kukumana mmatchalitchi mwawo, kamba kofuna kuwateteza ku matenda a COVID-19, omwe akufala kamba kopatsirana kachilombo ka Coronavirus. +Tikulimbikitsa makolo ndi onse omwe amakhala ndi ana kuti adziwalimbikitsa ukhondo komanso apewe kuyendayenda, anatero makhwawa. +Iwo apempha anthu akufuna kwabwino kuti athandize program ya ana imeneyi yapawailesi komanso athokoza onse omwe akuthandiza padakali pano. +",14 +"COMSIP Ilumikizitsa Bank Nkhonde ndi Bank Zikuluzikulu By Sylvester Kasitomu Bungwe la Community Savings Improved Programe (COMSIP) lati lilumikizanitsa magulu akumudzi a Bank Nkhonde komanso village bank ndi mabank akuluakulu kuti azitha kusunga ndi kubwereka ndalama ku mabankiwa. +Mkulu wa bungwe la COMSIP mdziko muno Tenson Gondwe ayankhula izi ku khonsolo ya Zomba pomwe amafotokozera akuluakulu a Zomba District Excutive Committee (DEC) za ntchito yomwe bungweli likufuna kuyambitsa mbomali. A Gomwe ati kupatula kulimbikitsa ma bank nkhonde kuti azitha kubweleka ndalama kuchokera ku bank anatinso akhazikitsa magulu ena a bank nkhonde kuti apindule nawo mu pologalamu imeneyi. +Iwo anati ntchitoyi ayigwira mmadera a mafumu aakulu Mwambo, Mulumbe komanso Malemia. +Mmau ake mkulu owona za mapulani ndi chitukuko ku khonsolo ya Zomba a Water Chikuni anati pologalamu yomwe bungwe la COMSIP layambitsa lofuna kuti anthu akumudzi azitha kupindula ndi ma bank oti azitha kupeza ndalama ithandiza kukweza busines zawo. +Ife ngati a khonsolo tiri okondwa kwambiri chifukwa choti mapulani athu akukwaniritsidwa ndipo puloject imeneyi tayilandila kwambiri kaamba koti anthu ambiri amalephera kupititsa ma business awo patsogolo kaamba kosowa ngongole zokuzila ma businesi-wa, anatero a Chikuni. +iwo anapitilira kunena kuti izi ziri mu mapulani awo omwe boma la Zomba layika kuchokera chaka chino kufika chaka cha 2022 kuti akhazikitse magulu omwe alumikizidwe ndi ma banki akuluakulu mdziko muno. +",2 +"Bishop Tambala appeals for concerted efforts for unity by all pastoral agents. +By: Judith Sonkho Bishop of Zomba Diocese, Rt. Rev. George Desmond Tambala, has urged all groups discharging pastoral duties in the diocese, to be united in all areas for the benefit of the church. +Rt. Rev. Tambala was speaking at Zomba Cathedral during the feast of Presentation of the Lord and the commemoration of World Day of Consecrated Life. +Bishop Tambala said, among others, unity brings in effectiveness in all missions of the church. +Rt. Rev. George Desmond Tambala Bishop of Zomba Diocese There is strength in unity, it contributes in the effectiveness of all missions of the church by bringing together your resources, talents and gifts, the church benefits a lot. Bishop Tambala said. +Commenting on what the Bishop said, Fr. Harvey Chikumbu of the Capuchin, echoed that unity was brought by Jesus Christ himself during the time he was leaving his disciples, he advised them to be one, meaning unity, therefore, the church has to emulate it. +Unity was brought by Jesus Christ himself during the time he was leaving his disciples, he advised them to be one, meaning unity, therefore in the Catholic church we have different charisms that have to be shown in different areas. There are different orders in the church, some are working in hospital, schools and some are working hand in hand with the people in the field, therefore all these have different works in the church and at the end all these become one which is the body of Christ. Concluded Fr Chikumbu The eucharist celebration mass brought together all the pastoral agents in the diocese and celebrates their unity. +",14 +" Samalani ndi chitopa Kuchokera ku phindu la ulimi wothirira, Catherine Bamusi wa mboma la Blantyre adaganiza zogulako nkhuku zachikuda kuti zizimupatsa manyowa, ndiwo ngakhalenso ndalama akazingwa. + Iye adayamba ndi nkhuku 6 chaka chathachi ndipo pamene amalowa mchaka chino zidali zitachulukana kufika 50. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili mkati modyerera, nkhuku zanga zidagwidwa ndi chitopa ndipo padakalipano ndilibe ndi imodzi yomwe chifukwa zonse zidafa, adandaula motero Bamusi. + Pezani phindu lochuluka ku nkhuku zachikuda pozipatsa katemera Marcus Twayah wa mboma la Mulanje akuti chitopa chimamusautsa chaka chilichonse koma khama pa ulimiwu ndi lomwe limamuchititsa kuti zikafa, agule nkhuku zina ndi kuyambiranso kuweta. + Padakakhala kuti palibe chitopa, bwenzi ndikutakata kwambiri chifukwa ulimiwu ndi waphindu. + Ndimakwanitsa kuyambiranso chifukwa siulira zambiri ngati momwe umakhalira ulimi wa nkhuku za mazira ndi zanyama, adabwekera motero mlimiyu. + Malingana ndi mphunzitsi wa zaulimi wa ziweto ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Jonathan Tanganyika, matenda a chitopa ndi oopsa kwambiri. + Iye adati awa ndi matenda omwe amapha nkhuku zambiri zachikuda mdziko muno. + Matenda ena akagwira nkhuku amapha koma sangafanane ndi momwe chitopa chomwe ena amachitchula kuti chideru chimasakazira. + Matendawa amagwira nkhuku panthawi ndi kupha zambiri ndipo pamadutsa miyezi ingapo asadabwerenso, iye adafotokoza motero. + Malingana ndi mphunzitsiyo, matendawa amayamba ndi mavayilasi choncho chifukwa choti tizilombo tamtunduwu timavuta kupha, palibe mankhwala omwe amachiza chitopa chikagwa mkhola. + Iye adachenjeza alimi kuti asamanamizidwe kuti pali mankhwala a chitopa kapena zitsamba zochiza matendawa. + Alimi ayenera kuteteza nkhuku zawo ku matendawa pozipatsa katemera wa matendawa monga I-2 yemwe akupezeka msitolo za vetenale za mdziko muno. + Katemerayu ndi wotsika mtengo ndipo alimi akuyenera kumapatsira nkhuku zawo mmiyezi inayi iliyonse kuti zizitetezeka, adatero Tanganyika. + Mphunzisiyu adati mbotolo la katemerayu mumakhala madontho 200 omwe mlimi amayenera kupatsira ku nkhuku 200. + Iye adati mlimi amayenera kudonthetsera mdiso limodzi la nkhuku iliyonse. + Kadaulo wa ulimi wa ziweto mboma la Blantyre Edwin Nyondo adati katemera wina wotetezera ku chitopa ndi lasota. + Alimi amayenera kumwetsa nkhuku katemerayu miyezi itatu iliyonse komanso anapiye asanakwane sabata ziwiri, adafotokoza motero. + Tanganyika adati katemera ndi njira yokhayo yotetezera nkhuku zachikuda ku matendawa mdziko muno chifukwa nzosatheka kuziweta mnjira yoti zisamasakanikirane ndi nkhuku zina ngati momwe amachitira mmaiko ena. + Mphunzisiyu adati izi zili chomwechi chifukwa nkhuku zachikuda mdziko muno zimayendayenda kusakasaka zakudya. + Kuonjezera apo, iye adati nyengo ino ndiyamaukwati komanso zinamwali choncho nkosavuta kufalitsa matendawa. + Ichi nchifukwa china chomwe chimachititsa kuti mnyengo yotentha matendawa afalikire kwambiri. + Chinthu china chomwe chimachititsa izi nchoti mnyengo yotentha nkhuku zimayenda mtunda wautali kusakasaka zakudya chifukwa chimachepa ndipo potero zimakatengako matendawa, iye adatero. + Mphunzitsiyo adaonjeza kuti katemera wa chitopa sioopsa ndipo sasintha kaonekedwe ndi kakomedwe ka nyama ya nkhuku koma amangoiteteza basi. + Tanganyika adafotokoza kuti katemerayu sagwira ntchito ku nkhuku zomwe zagwidwa kale ndi matendawa choncho alimi akuyenera kutsatira ndondomeko. + Katemerayu amagwira ntchito kwa miyezi inayi ndipo ichi nchifukwa chake mlimi ayenera kupatsira mmiyezi inayi iliyonse, iye adatero. + Tanganyika adaonjeza kuti zizindikiro za matendawa zimaonekera mbali ya thupi yomwe agwira. + Mwachitsanzo, iye adati akagwira mu ubongo khuku imapinda khosi, imazungulira malo amodzi kapena kumangogwa. + Akagwira mapapo nkhuku imatsokomola, kuyetsemula ndi kutulutsa mamina. + Akagwira mmatumbo nkhuku imatsegula mmimba, adafotokoza motero. +",4 +" Kusamala ndi antchito olera ana Ana ambiri masiku ano akuleredwa ndi antchito mmakomomu popeza makolo awo amakhala otangwanika kusaka makobidi kuntchito kapena mabizinezi. + Ndipo alipo ena antchito odziwa kulera mwana mwachikondi oona nkumadabwa kuti zoterezi zikutheka bwanji, koma si onse antchito omwe amaika mtima posamala mwana wa bwana. Ena ngankhanza; ena achibwana; ena amgwazo ndipo kupanda kupenyetsetsa bwino akhonza kubweretsa mavuto pamoyo wa ana komanso banja. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Nthawi zina chifukwa cha kutangwanika makolo amalephera kuonetsetsa kuti ana awo akuleredwa bwanji pakhomo. Makolo ena amangotayirira chilichonse nkusiya mmanja mwa anthu omwe kwawo kumakhala kungothandizira kaleredwe ka ana. + Antchito enanso chidwi chawo sichikhala kwenikweni posamalira mwana, koma pa ndalama zomwe amalandira mwezi ukatha. + Poterepa pamafunika kupenyetsetsa. + Tamvapo za antchito ena omwe mwana akawavuta ndi kulira amatha kungomuyamwitsa, mmalo momupatsa mkaka wambotolo. + Mmakomo momwe miswachi imangounjikidwa kubafa, antchito ena wawo mswachi ukatalikira amangotolapo wa mwana nkutsukira mkamwa mwawo. + Kaya ndi chibwana kaya ndi umbuli, masiku ano a matenda opatsirana ngati Edzi, nkwapafupi kuti mchitidwe ngati uwu ukhale chiopsezo kumoyo wa ana. + Antchito ena aulesi amangomusiya mwana muthewera loonongeka nkungomusintha kapena kumusambitsa kumadzulo make akayandikira kubwera chonsecho tsiku lonseli mwana wakhalira kupsa muthewera losalongosoka. + Ana ena oliralira akukhalira kutsinidwa kapena kumenyedwa kumene ndi anthu othandizirawa, enanso omwe amakhalira kumudyera zakudya mwana, makolo nkumangodabwa kuti sikelo ya mwana sikulongosoka. + Zilipo zambiri zomwe anthuwa amatha kuchita ndi ana omwe pokhala achichepere sangawiringule chilichonse. + Ngakhale pakhomo pali wothandizira, kumachitako chidwi kuti zinthu akuyendetsa bwanji. + Nanga anawo akuwasamalira bwanji chifukwa tsiku lina nkudzalirira kuutsi. +",15 +" Adzikhweza pamkangano wa madzi osamba ku Nkhatabay Chisoni chakuta banja lina ku Bula, T/A Mbwana, mboma la Nkhata Bay pomwe mnyamata wa Sitandade 8 wadzimangirira atayambana ndi mlongo wake. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Malinga ndi mfumu Dumbulira ya derali, Chrispin Mwale adayambana ndi mlongo wake pankhani ya madzi osamba. + Mfumuyi idati chifukwa cha ichi mnyamatayo adadzimbuka ndi kupita kutchire. + Abambo ake adamutsatira kutchire konko koma adadzawathawanso nkubwererako. Adafikira kuchipinda chake chogona, idatero mfumuyo. + Malinga ndi mfumuyo, mayi a mnyamatayo adadabwa pomwe adatuma mwana wina kukatenga chinangwa choti aphike ndipo mwanayo adapeza mbale wakeyo atadzimangirira ndi chitenje. + Koma pambalipa adasiya kalata yomwe adalembera mphunzitsi wamkulu wa pasukulu ya pulaimale ya Munthelele yowatsanzika kuti sapitiriza sukulu chifukwa moyo wake watha, Dumbulira adatero. + Iye adati kudzikhweza kukukula mderalo koma samayembekezera kuti mwanayo angalimbe mtima motere chifukwa adali wanzeru komanso wolimbikira pa maphunziro. + Naye mneneri wa polisi mboma la Nkhata Bay Ignatius Esau adatsimikiza za imfayo. + Ndi zoona kuti mwana wa zaka 15 wadzikhweza ku Bula ndipo nawo achipatala atsimikiza kuti adadzipha kaamba kodzimangirira, adatero Esau. +",15 +"Oyendetsa Truck Akuchita Sitiraka Wolemba: Thokozani Chapola ploads/2019/10/trucks.jpg"" alt="""" width=""573"" height=""421"" />Oyendetsa galimoto ngati izi akufuna azilipidwa 500 000 kwacha Oyendetsa ma galimoto za mtundu wa TRUCK lero ayamba kunyanyala ntchito ati kaamba kakuchepa kwa malipiro a ntchito yawo. +Malinga ndi mtolankhani wathu amene anayankhula ndi mmodzi wa madalaivala-wa, kunyanyala ntchitoku kukuchitika mmadera onse olowera ndi kutulukira mdziko lino monga ku KARONGA, MCHINJI ndi MWANZA komanso ku BLANTYRE ndi ku KANENGO mu mzinda wa LILONGWE. +Mmodzi mwa atsogoleri a madalaivalawa Masautso Chagomerana wati amalandira ndalama zochepa poyerekeza ndi ndalama zomwe madalaivala anzawo ammaiko ena mchigawo cha SADC amalandira. +Tinapempha mabwana athu kuti atiwonjezere ndalama ndi zina zokhudza ntchito koma sizinasinthe. Tinalemba makalata ku unduna koma mpaka pano palibe yankho limene tikulandira, anatero a Chagomerana. +Iwo ati akufunitsitsa kuti madalaivalawa adzilandira ndalama kuyambira 400, 000 kwacha mpaka 500, 000 kwacha kaamba koti padakali pano ena mwa iwo amalandira ndalama ysapyola 50,000 kwacha. +Madalaivalawa ati achita sitirakayi kufikira boma lizalowelerepo pa nkhaniyi. +",14 +" Mashado a PP ndiwo agawe chimanga cha boma Banda (pakati) kulandira chimanga kwa nthumwi ya ku United Arab Emirates Anthu amene satsatira chipani cha PP ali pachiopsezo chosumbudzuka ndi njala pamene boma lauza mashado a PP kuti ayambe kugawa chimangachi kwa anthu ovutika mmadera awo. + Mneneri wa Pulezidenti Joyce Banda Steven Nhlane wati nkovuta kuti mashado a zipani zina zimene zakhala zikulalatira ndi kuipitsa mbiri ya Pulezidenti atumidwenso kugawa nawo chimangachi. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Aphungu komanso omwe akufuna kudzaimira PP ndi imodzi mwa njira zomwe zikugwiritsidwa ntchito pogawa chimangachi komanso pali mafumu amene akugawa chimangachi mosayanganira ndale, adatero Nhlane. + Lachinayi sabata yatha pamsonkhano wa atolankhani ku Sanjika mumzinda wa Blantyre komanso Lamulungu pamwambo wokumbukira kuti patha chaka chimodzi chimwalirireni Inkosi ya makhosi Mmbelwa IV ku Edingeni mboma la Mzimba, Banda adauza mashado a PP kuti apite ku Farmers World ku Lilongwe kukatenga chimangachi kuti azikagawira anthu amene alibe chakudya mmadera mwawo. + Chimanga chomwe chikugawidwachi ndi chomwe dziko lino lidalandira kuchokera ku United Arab Emirates (UAE) kudzera mbungwe la Khalifa Bin Zayed Al Nahyan Foundation kuti chithandize mabanja pafupifupi 7 500 amene akusowa chakudya. + Dzikoli lidapereka matani 13 500 kudziko la Malawi Banda atadandaulira dzikoli kuti Amalawi ali pamoto. + Abdulrahim Jali yemwe amaimira dziko la United Arab Emirates polankhula pamene ankapereka chimangachi a 17 February adati: Cholinga chathu ndi kuthandiza ovutika ndipo pamene Pulezidenti Banda adapempha thandizo, tidaganiza zobwera ndi [chimangachi] kwa ovutika. + Koma Nhlane akuti chimangachi chidaperekedwa kwa Banda, kotero ali ndi ufulu wosankha momwe chingagawidwire. + Kupatula aponso, PP ili ndi mashado mzigawo zonse 193 amene angafikire anthu onse amene akufunika thandizoli. + Mashado MP a zipani zina si odalirika kwa mtsogoleri wa dziko lino, kotero si oyenera kugawa nawo chimangachi. A Pulezidenti sangagwiritse ntchito amene tsiku lililonse amakhalira kuwanyoza kuti agwire nawo ntchitoyi, adatero mneneriyu. + Izi zadabwitsa katswiri pa zandale, Prof Chijere Chirwa amene akuphunzitsa kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College ku Zomba, yemwe akuti zaboma siziyenera kukhudzana ndi chipani. + Ngati chimangacho chimaperekedwa kuti chithandize anthu ovutika ku Malawi, ndiye njira yabwino kudali kukachisiya ku Admarc kapena mwa ma DC osati mwanja mwa chipani. Koma ngati sichinabwere mnjira ya chipani ndiye chaperekedwa bwanji kuchipani? akudabwa Chirwa, potsindika kuti chipani si boma. + Chirwa akuti magawidwe a chimanga otere kukuonetseratu kuti palowa ndale, makamaka pamene zisankho za pulezidenti, aphungu ndi makhansala zayandikira, osati kuthandiza ovutika. + Posakhalitsapa bungwe la Malawi Vulnerability Assessment Committee lidatulutsa lipoti kuti anthu oposa 1.5 miliyoni ndiwo akuthatha ndi njala mdziko muno. + Amene akuyanganira kagawidwe ka chimangachi, Macward Themba, yemwenso ndi mkulu wa Mudzi Transformation Trust (MTT), wati akugwirita ntchito aphungu a PP ndi mashado a chipani kuti kagawidwe kasavute. + Koma aneneri a chipani cha UDF ndi DPP ati izi ndi zodandaulitsa ndipo anenetsa kuti zipani zawo zichitapo kanthu. + Izi ndi ndale zoipa, ndale sitipangira pamoyo wa munthu. Anthu akuvutika ndi njala ndiye mukumupatsa wachipani kuti ndiye azigawa chimanga kwa ovutika chifukwa chiyani? Tiwauza anthu kuti asanyengeke ndi chimangacho. Komabe tilembera bungwe loyanganira za zisankho la Malawi Electoral Commission kuti lione ndale zomwe boma layamba, adatero mneneri wa DPP, Nicholas Dausi. + Naye Ken Ndanga wa UDF akuti izi ndi ndale zoipa chifukwa mashado a chipani chawo sadapatsidwe ntchitoyi. + Mashado athu palibe amene wapatsidwa chimanga kuti azigawa. Komabe adziwe kuti anthu atopa ndipo akufuna kusintha, adatero Ndanga. + Azigawa mosankha, anthu a zipani zathu sangapatsidwe chimangachi, ndi kuononga zinthu zothandizira anthu kumeneku. Ndale zotere sitikuzifuna. + Koma mneneri wachipani cha MCP Jessie Kabwira samayankha foni yake ya mmanja pamene timati tilankhule naye Lachitatu msabatayi. + Mashado ena a maboma a Thyolo, Ntchisi ndi Lilongwe atsimikiza kuti atenga kale matumba a chimanga amene ayamba kugawa pamene ena akuti akhala akukatenga chimangachi msabatayi. + Raja Khan, yemwe ndi shado wa PP kummwera kwa boma la Thyolo, akuti akhala akutatenga chimangachi msabatayi. + Kampeni ikuyenda bwino ndipo chimanga ndikatenga msabatayi kuti ndigawire anthu anga, adatero Khan pouza Tamvani. + Naye Banda ali kalikiriki kugawa chimanga mdziko lonse, zomwe ena anena kale kuti ndi ndale chabe. + Koma mneneri wa Pulezidentiyu watsutsa izi ponena kuti kugawa chakudya kwa anthu ovutika si ndale. + Pomapereka chimanga kwa mabanja amene akuvutika ndi njala Pulezidenti akupulumutsa miyoyo ya anthu ndipo atsogoleri ena a zipani zina atha kutero ndipo akupemphedwa kuthandiza Pulezidenti wa dziko lino patchitoyi, adatero Nhlane. +",11 +"Bambo Agwililira Mwana Wake Weniweni Mkuthawa Apolisi mboma la Ntcheu akusakasaka mkulu wina yemwe akumuganizira kuti wagwililira mwana wake weniweni. +Chigalu: Mchitidwe umenewu ukuchulukira Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub Inspector Hestings Chigalu wati bamboyu George Gwalidi yemwe padakalipano wathawa ndipo sakudziwka komwe ali, anagwililira mwana wake wa zaka 16 lachiwiri, pa nthawi yomwe mkazi wake anachokapo. +Mayiyo atamva za nkhaniyo akuti anamuuza msungwanayo kuti asaulure powopa kuwaika bambo akewo pa mavuto, koma msungwanayu anakauza agogo ake omwe anakanena za nkhaniyi ku polisi. +Chigalu wati mchitidwewu wachulukira kwambiri mbomalo ndipo wati zimenezi zayamba kuwululika kwambiri kaamba ka ntchito yomwe apolisiwa akugwira pomemeza anthu kuti azikanena ku polisi nkhani zoipa zomwe zikuchitika mmadera mwawo. +Pamenepa Chigalu walangiza anthu kuti apitirize kunena nkhanza zilizonse zomwe zikuchitika mmadera mwawo kuti malamulo agwire ntchito pa iwo kudzera mu kuzengedwa mlandu ku bwalo. +",14 +" Samalani ndi sikelo za chinyengoMBS Nthawi yokolola yakwana, pomwe alimi amataya zokolola zawo kwa mavenda akuba amene amamanga sikelo pofuna kuliza alimi. + Koma bungwe loona zoyezayeza za malonda la Malawi Bureau of Standards (MBS) lati a malonda akuyenera aonetsetse kuti sikelo zawo zayezedwa ndipo zili pamlingo wabwino. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wachiwiri kwa mkulu wa bungweli Willy Muyila wati bungwe lake ndi lokhalo lomwe lingapime sikelo zisanayambe kugwira ntchito. + Tili ndi zida zoyenera kupima zoyezera zomwe amalonda akugwiritsa ntchito. Zida zathu zimapimidwa ndi maiko akunja kotero ndife wothekera kuyeza zida za amalonda onse mdziko muno, adatero Muyila. + Tikukambatu masikero oyeza zamadzi, mpweya, katundu wolemera bwanji komanso zipangizo zakuchipatala. Izi ndi zomwe timazipima kuti zisanayambe kugwira ntchito zikhale zili pamlingo wabwino, adatero Muyila. + Iye adati amalonda amene amaphika kapena kupanga katundu wosiyanasiyana ayenera aonetsetse kuti zipangizo zawo zapimidwa ndi bungweli. + Izitu zimalankhulidwa pamene bungweli lidaitana amalonda kumsonkhano wa zopimapima womwe umachitikira mumzinda wa Blantyre Lachiwiri msabatayi. + Muyila adati posakhalitsa bungwe lake likhala likuyenda mmidzi kuti akapime masikero amene mavenda akugwiritsa ntchito. + Ndipo tsiku lomwe tikupita sitinena kuopa kuwachenjeza mavendawo. Tiyenda paliponse kupima masikero, adatero. + Mkulu woona za kapangidwe ka katundu pa kampani ya Candlex Ltd, Aaron Nkhoma yemwe adalinawo pa mkumanowo adati zokambiranazo zidali zothandiza. + Ndi bwino kuti sikelo ikhale pamlingo wake chifukwa tidziwa zoyenera kuika popanga katundu wathu monga sopo. Komanso kuti tidziwe kukula kwa sopo amene tikufuna kupanga, adatero Nkhoma. +",7 +" Akufuna T/A Chekucheku achoke Anthu okwiya Lolemba ndi Lachiwiri msabatayi adasonkhana paofesi ya DC wa boma la Neno komwe amapempha bwanamkubwayo kuti achotse T/A Chekucheku avulidwe ufumu wandodowu ati chifukwa wanyanya ziphuphu. + Mmodzi mwa anthuwa, Steve Donda, wa mmudzi mwa Donda kwa T/A Chekucheku, akuti mfumuyi ikulanda minda ya anthu, ikumadyetsera ngombe zake mminda mwa anthu komanso ikulonga mafumu posatsata ndondomeko ya ufumu wa Chingoni. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma mfumuyi yati zomwe akunena nzabodza ndipo iye satula pansi ufumu. + Kusiya ufumu ndiye kuti ndamwalira, apo ayi sizitheka, idatero mfumuyi. + Iyo idaonjeza: Ndikukonza zowatengera anthuwa kukhoti. Pali milandu yambiri. + Donda adati sasiya kupempha boma kuti lichotse mfumuyi. Panopa tayamba kusonkhana kwa DC, sitikubwerera mmbuyo mpaka mfumuyi itachotsedwa, adatero iye. + DC wa bomalo, Memory Kaleso Monpeiro, watsimikiza kuti ofesi yake yalandira madandaulowa ndipo wati Lolemba kudavuta moti sadagwire ntchito. + Adatchinga ofesi yathu moti sitidagwire ntchito.Lero [Lachiwiri] bolani, angofika anthu oposera 100 pomwe dzulo [Lachiwiri] kudafika anthu oposa 200, adatero Monpeiro. + Iye adati watumiza madandaulo a anthuwo ku ofesi ya pulezidenti poti ndiye ali ndi mphamvu zonse. +",11 +" ANATCHEZERA Nditenge uti? Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Munthune ndili ndi zibwenzi ziwiri. Zonsezi zidayamba chaka chimodzi panopa zatha zaka zitatu ndipo onsewa ndimawakonda chimodzimodzi inenso onsewa amandikondanso. Ndiye panopa ndapanga chiganizo chokhala ndi mmodzi. Ndipanga bwanji pamenapa? Ine Zochenana A Zochenana, Akamati ichi chakoma ichi chakoma pusi anagwa chagada kapena kuti mapanga awiri avumbwitsa mumati akutanthauzanji? Ndi zimenezitu. Mwagwiratu njakata pamenepa chifukwa chosakhutitsidwa ndi bwenzi limodzi. Mwina mumayendera ija amati have many but choose one. Mphotho yosakhulupirika ndi imeneyo, achimwene. Ndanena kuti ndinu wosakhulupirika chifukwa kwa zaka zitatu mwakhala mukuyendetsa zibwenzi zanu pozinamiza kuti ndiwe wekha pamene mulinso ndi wina amene mukumuuzanso kuti ndiwe wekha. Nanga tinganene kuti zibwenzizo zikudziwana ngati? Ndakaika kuti zikudziwana. Koma ndikuthokozeni kuti tsopano mwapanga chilinganizo choti mukhale ndi chibwenzi chimodzi. Izi ndiye zotamandika chifukwa mwaonetsa kukula. Kaya mukufuna kukwatira tsopano-ngati simunakwatire kale? Ndiye zikafika apa pamakhala matatalazi kusankha chifukwa mukuti onse mumawakonda chimodzimodzi. Koma mukunena zoona? Zingatheke zimenezo kukonda anthu awiri chimodzimodzi? Zimalephera olo ana ako obala wekha umatha kusiyanitsa chikondi ngakhale mwina suonetsera. Ndiye apa tangolimbani mtima, musankhe amene ali ndi makhalidwe oyenera kulowa naye mbanja. Penapake ayenera kusiyana ndithu. Palibe amene angakusankhireni, koma inu nokha, a Zochenana. Ndili ndi chikhulupiriro kuti simunapulupudze zoti mwina muli ndi ana ndi zibwenzizo. Apo ndiye zingakuvuteni kusankha koma ngati mudadzigwira sipangakhale vuto lenileni kusiyapo mmodzi. Zimachitika koma si mmene zimayenera kukhalira, abale. + Ndili pasukulu Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 17 ndipo ndili pasukulu. Ndili ndi chibwenzi koma mnzangayo akuonetsa kuti sakukondwera nane ndiye ndimafuna kuti mundithandize maganizo kuti ndiziwerengerabe kapena ayi? Chonde ndithandizeni. + Iwe mtsikana, Ukufuna ndikuthandize motani poti wanena kale kuti mnzakoyo akunetsa kuti sakukondwera nawe? Chomwe ndingakulangize nchoti zisiye za chibwenzizo ndipo ulimbikire sukulu. Sukulutu ndi yofunika kwambiri ndipo uike patsogolo, zina zonse pambuyo. Udakali mwana wamngono tsono zoyamba zibwenzi nzachiyani? Sukulu ndi zibwenzi siziyenderana. Ngati ufuna kuti sukulu ikuyendere usamataye nthawi nkuganiza za zibwenzi chifukwa mmalo moti uzimva zimene aphunzitsi akuphunzitsa uzingoganiza za bwenzi lakolo, osamva olo chimodzi, mapeto ake 0 pa 10! Atsikana ambiri sukulu imawakanika chifukwa cha nzeru ngati zakozo-kuika mtima pa zibwenzi. Kaya, zakozo! Usankhepo chimodzi ngati ufuna zako zikuyendere. Mwina bwenzi lakolo sakukondwera nawe chifukwa uli pasukulu ndiye akufuna usiye sukulu kuti uike mtima wako wonse pa iye. Koma ine ndikadakhala iweyo ndikadasankha sukulu, chibwenzi pambuyo. + Sakundipatsa ulemu Ndine mwamuna wapabanja mkazi ndi wachiwiri koma sandipatsa ulemu chifukwa makolo ake ndi ochita bwino. Ndili naye mwana mmodzi. Kodi nditani kuti azindipatsa ulemu monga kale? Achimwene, Ulemu sachita kupempha! Umanena chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga. Lero ndi lero basi mkazi wanu wayamba mwano, osakupatsani ulemu poti makolo ake ndi ochita bwino? Chilipochilipo chimene chimamupangitsa mkazi wanu kuti asakupatseni ulemu, osati chifukwa makolo ake ndi olemera. Mwina adayamba akuuzani kuti sangakupatseni ulemu chifukwa makolo ake ndi olemera? Ayi ndithu, munene chifukwa china, osati chimenecho. Mwanena nokha kuti poyamba ankakupatsani ulemu wonse, koma pano wasiya kutero, mukutanthauza kuti poyambapo makolo ake sadali ochita bwino? Koma simukunena bwinobwino ulemu umene mumafuna kuti mkazi wanu azikupatsani-azikugwadirani kapena aziti wee bambo! mukamamuitana? Ulemu wake uti? Nkhanitu mukapanda kuilongosola inuyo bwinobwino kumakhalanso kovuta kuti munthu akuthandizeni zenizeni chifukwa simunaitambasule. Nditengerepo mwawi wopempha ena amene ali ndi mavuto ndipo akufuna kuti ndiwathandize kuti aziyala nkhani yawo bwinobwino, momveka kuti ndithe kumvetsa gwero la vuto lawo ndipo ndikatero nditha kupereka malangizo malinga ndi nkhani yawo mmene ilili. OFUNA MABANJA Ndine wa zaka 37 ndikufuna mkazi wa zaka kuyambira pa 40 mpaka 45. Wosangalatsidwa aimbe pa 0888 512 430 Ndili ndi zaka 27 ndipo ndikufuna mkazi woti ndipange naye chibwenzi ncholinga choti tidzakwatirane mtsogolomu. Akhale wa zaka za pakati pa 18-23, koma akhale wa ku Lilongwe. + Ndine mnyamata wa zaka 30 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 30 ndi 33 kuti ndipalane naye chibwenzi. Wotsimikiza aimbe pa 0888 904 690 kapena pa 0998 707 410. +",12 +" Fodya wakunja wayamba kulowa Pomwe dziko la Malawi lalima fodya wochepa ndi makilogalamu 27 miliyoni pamlingo omwe ogula fodyayu adaitanitsa, mavenda ena amachawi ayamba kulowetsa fodya kuchoka mmaiko oyandikana ndi dziko lino. + Fodyayu akumalowetsedwa pogwiritsa ntchito njira zozemba chifukwa mchitidwewu ngosemphana ndi malamulo a dziko lino. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wogwirizira udindo wa mkulu wa bungwe loyendetsa ulimi wa fodya mdziko muno la Tobacco Control Commission (TCC) David Luka adati bungwe lake likudziwa za mchitidwewu ndipo lidatumiza maofesala ake kumalo onse omwe izi zikuchitika. + Maofesala athu ali ku Nkhamenya, mboma la Kasungu komwe kumalowera fodya kuchokera mdziko la Zambia ndipo ena ali ku Mchinji komanso ku Namwera mboma la Mangochi komwe fodya wake amakhala ochokera ku Mozambique, adatero Luka. + Iye adati bungwe lake ndi lokhumudwa ndi mchitidwewu omwe uli vuto lalikulu pa ulimi wa fodya mdziko muno. + Ntchito yoyesetsa kuti fodya asalowe kapena kutuluka mdziko muno siyapafupi, ndipo sikwapafupi kuchitapo kanthu adatero Luka. + Iye adaonjezeranso kuti nkhanizi kwambiri ndi zokhudza dziko ndi dziko linzake. + Alimi a fodya ena mboma la Mchinji adatsimikiza za kulowa kwa Fodya mdziko muno. + Mmodzi mwa alimiwa, Lazarus Chitedze, yemwe wakhala akulima fodya kwa zaka pafupifupi 20 adati fodyayu akulowa pangono chabe kuchokera mdziko la Zambia kusiyana ndi momwe zimakhalira zaka zonse. + Akulowetsa fodya ndi mavenda angonoangono omwe amagwiritsa ntchito njinga, mwina chifukwa chakuti mmaliremu muli asilikali omwe akulondera chimanga kuti chisatuluke, adatero Chitedze. + Iye adati chaka ndi chaka fodya amalowa kuchokera ku Zambiako kapena kutuluka kuchoka mdziko muno. + Zimatengera komwe msika uli bwino chaka chimenecho.Ngati ku Zambia zili bwino, mavenda amazembetsa fodya kupita naye komweko, adatero Chitedze. + Iye adati zikatere zimawakomera alimiwa chifukwa mavendawa amawagula mokwera mtengo kusiyana ndi ku msika wa fodya. + Malinga ndi Chitedze, chiopsezo chimakhalapo fodya akamalowa kuchokera mdzikolo chifukwa zikhonza kuchulutsa fodya pamsika kuposera mlingo omwe ogula akufuna. + Polankhulapo mlimi wina yemwe sadafune kutchulidwa dzina lake adati fodyayu akulowa pangono chifukwa ku Zambiako ayamba kumene kusankha fodya. + Akangoti wafika pachimake kumeneko, timuona akulowa wochuluka zedi, adatero mlimiyo. + Mwezi wathawu, woyanganira dera la kummawa mboma la Zambia Chanda Kasolo adauza ena mwa atolankhani a dzikolo kuti asilikali omwe ali mmalire a dziko lino ndi dzikolo akutetezanso kuzembetsa fodya. + Dziko la Zambia lidalengeza chaka chathachi kuti likweza mlingo wa fodya yemwe amalima kuchoka pa ma kilogalamu 23 miliyoni kufika pa 30 miliyoni chaka chino. + Ndipo chaka chathachi mtsogoleri wa bungwe la alimi la Eastern Fodya Association of Zambia (Efaz) Franklyn Mwale adadandaulira bungwe loyendetsa ulimi wa fodya mdzikolo kuti msika wawo amautsekula mochedwa poyerekeza ndi wa dziko lino. + Koma limodzi mwa mabungwe a alimi la Tobacco Association of Malawi (Tama) lidati silidalandire lipoti lililonse lokhudza kulowa kwa fodya kuchokera mdziko la Zambia. +",2 +"Boma la Zomba Likuchita Bwino pa Zaumoyo Wolemba: Thokozani Chapola Mkulu wa zaumoyo mboma la Zomba,Dr. Raphael Piringuwati boma la Zomba likuchita bwino pa ntchito za uchembere wabwino. +Dr. Piringu amalankhula izi kwa mtolankhani wathu amene amafuna kudziwa momwe ntchito za umoyo zikuyendera mbomali padakalipano. +Iwo ati chaka chino mayi mmodzi yekha ndi amene wafera ku chipatala chachingono komanso amayi atatu ndi omwe afera ku chipatala chachikulu cha bomalo pa nthawi yobereka zomwe zikusonyeza kuti ntchitoyi ikuyenda bwino kusiyana ndi momwe zinalili chaka chatha ndi zaka zina zapitazo. +Zaka za mbuyomu ntchito ya uchembere wabwino imavuta pomwe amapezeka kuti amayi ambiri akufera ku zipatala zazingono pa nthawi yobereka koma pano zinthu zasintha kwambiri ndipo tikuchita bwino, anatero Dr. Piringu. +Iwo ati nayo ntchito yoyeza amayi khansa ya khomo la chiberekero yapitanso patsogolo mbomalo. +Mwazina, Dr. Piringu ati ntchito zonse za umoyo zikuyenda bwino mbomalo ngakhale pali zovuta zina zomwe ndi zochepa chabe. +",6 +"Kwaya ya St. Benadeta Chibavi Ikuyembekezeka Kukhazikitsa Chimbale Chatsopano Wolemba: Glory Kondowe Kwaya ya Benadeta oyera ku Chibavi mu diocese ya Mzuzu, yati zonse zokhazikitsa chimbale chawo cha nyimbo zomvera chatsopano chotchedwa Mwana Wa Maria zili mchimake. +A Ezekiel Nyirenda yemwe ndi mlangizi wa kwayayi alankhura izi pamene Radio Maria Malawi imafuna kudziwa zambiri za zakukhazikitsidwa kwa chimbalechi. +A Nyirenda anati kukhazikitsa kwa chimbalechi komwe kukachitikire ku St. Francis Kanengo akomzekera kwambiri ndipo anati chimbalechi akachikhazikitsira ku Lilongwe chifukwa, Kuli abwenzi ambiri ndipo tikuwona mansomphenya kuti abweziwa akatithandiza kwambiri. Abwenzi amenewa atithandiza munjira zambiri monga kulemba makalata okopera anthu za chimbalechi. +Iwo ati cholinga chenicheni cha chimbalechi ndi kufalitsa uthenga wa Mulungu kudzera mu nyimbo momwe mumakhalaso ulaliki wawukulu, ndinso kupeza ndalama zogwilira ntchito zachifundo monga kuthandiza ana ovutika, amasiye ndi okalamba. +",9 +" Phindu lochuluka mu ngombe za nyama Ngakhale ulimi wa ngombe za nyama umafuna mpamba wochuluka komanso phindu lake limabwera mochedwa, akadaulo a zaulimi wa ziweto akuti ndi ulimi wolemeretsa kwambiri kusiyana ndi wa ziweto zazingono mlimi akautenga bwino. + Akadaulowa akuti mlimi amadya nazo bwino ngombe za nyama akamazikwatitsa ndi zachizungu ndi kuzinenepetsa asadazigulitse. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Malingana ndi mkulu woyanganira ulimi wa ziweto mboma la Kasungu Jacob Mwasinga, ngombe ya Malawi zebu kuikwatitsa ndi ya chizungu monga ya chi Brahman kapena Bosimala, ana obadwawo akamafika chaka chimodzi amakhala akula ndipo afika poti mlimi akhoza kupha pamene osakwatitsa amatenga zaka ziwiri. + Ngombe za Brahman zimakhala ndi nyama yochuluka Mlimi akazitsekera mkhola ngombezi kwa miyezi itatu ndi kumazidyetsera momwemo zakudya monga mapesi, zotsalira za mtedza osaiwala madeya, kuzipatsa mankhwala opha nyongolosi ndikuzitetezera ku nkhupakupa zimanenepa kwambiri choncho phindu lake limapambana. + Mlimi akakwatitsa ngombe zake ndi zachizungu komanso kuzinenepetsa asadagulitse amakhala ngati wachepetsa nthawi yokolola komanso amadzichulukitsira zokolola ku ulimiwu choncho amapindula koposa, iye adatero. + Mkulu woona za ulimi wa ziweto ku Shire Valley Agricultural Development Division (Shivadd) Dickson Mangadzuwa adafotokoza kuti kuzera mundondomeko yonenepetsa ngombe, mlimi amatha kuchulukitsa kulemera kwa ngombe yake ndi theka kupita mmwamba pakutha pa miyezi itatu. + Ndaonapo alimi akuonjezera makilogalamu 0.7 pa kilogalamu iliyonse ya ngombe yake kuzera mu ndondomekoyi choncho akagulitsa amapha nayo makwacha ochuluka chifukwa ngombe imagulitsidwa malingana ndi kulemera kwake, adatero iye. + Iye adati kugula ngombe zazikulu kale ndi kumangozinenepetsa ndi kopindulitsa kwambiri chifukwa mlimi amangozinenepetsa kwa miyezi itatu yokha ndi kugulitsa choncho amapanga ndalama pafupipafupi ngati akuweta nyama zingonozingono. + Mangadzuwa adafotokoza kuti iyi ndi njira yokhayo yothandiza alimi a ngombe za nyama kuti aziutenga ulimiwu ngati bizinesi. + Medison Semba wa mboma la Blantyre ndi mmodzi mwa alimi amene amachita ulimi wonenepetsa ngombe za nyama ndikumagulitsa ndipo akuti ndi ulimi wopindulitsa. + Kale ndimangoweta ndi kumagulitsa koma phindu lake silimakhala logwirika kufikira pamene ndidayamba bizinesi yomagula kwa alimi anzanga ndi kumazinenepetsa ndi kumagulitsa. + Nthawi zambiri sindizinenepetsa kwa miyezi itatu chifukwa miyezi iwiri yokha zimakhala zafikapo poti ndikhoza kugulitsa. Ndikapyola miyezi iwiri anthu ogula amadadaula kuti nyama yachuluka mafuta chifukwa ndimapha ndi kumagulitsa ndekha, iye adatero. + Malingana ndi mlimiyu, amadyetsera ngombe imodzi chakudya chokwana makilogalamu 8 patsiku. + Iye adafotokoza kuti chakudyachi chimakhala chakasakaniza monga madeya a chimanga ndi mpunga, udzu ndi mamolase. + Udzu ndi umene umakhala wochuluka kwambiri pa zakudya zonsezi chifukwa ndi chakudya chodalirika kwambiri cha ngombe, iye adatero. + Ngakhale izi zili chomwechi, mphunzitsi wa zaulimi wa ziweto ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Jonathan Tanganyika adati ulimi wa ngombe za nyama mdziko muno ukukumana ndi mavuto monga kusowa kwa malo komanso zipangizo zodyetsera. + Kuonjezera apo, iye adati matenda komanso misika yosowa ndondomeko yoyenera ndi ena mwa mavuto amene akulowetsa pansi ulimiwu mdziko muno. +",4 +" Chisankho cha Mulhako chilephereka Adanyanyala: Katunga Kudali kuthafulirana Chilomwe kusukulu ya pulaimale ya Nyambadwe pulaimale Lolemba masiku apitawa pamene gulu la Mulhako wa Alhomwe ku Ndirande limachititsa chisankho. + Chisankhocho chimachitika patadutsa zaka zitatu chisadachitike ndipo amasankha maudindo a mkulu wa gululi ku Ndirandeko komanso wachiwiri wake, mlembi ndi msungichuma. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Escom in free-for-all fuel scam Anthu amene adatsina khutuTamvaniati chidasokoneza zonse ndi mkulu wina amene amafuna apikisane nawo koma adabwera ndi achipani amene amafuna amuvotere. + Patsikuli padali anthu atatu amene amafuna apikisane pampando wa mkulu wa gululi koma chisankho chisadayambe padachitika mpungwepungwe. + Vuto ndiloti mmodzi mwa amene amapikisana nawo pa mpandowu ndi wachipani cha DPP moti anabwera ndi omutsatira achipaniwo. Izitu si zachipani koma zachikhalidwe cha Alhomwe, adatero wotitsina khutuyu. + Amene adawatenga kuchipaniwo si a mtundu wathu zomwe zidakwiyitsa anthu. + Awiri mwa amene amafuna kupikisana nawo pampando wa wamkulu wa gululi adafumukapo kuti sapikisa nanawonso. + Mmodzi mwa amene adanyanyala kuti sachita nawo chisankhocho ndi Dolesi Katunga amene wakhala mkulu wa gululi kwa zaka zitatu. + Iye watsimikiziraTamvanikuti kudali mpungwepungwewo. Chisankho chalephereka, sindikudziwanso kuti zitha bwanji chifukwa chichokereni sindinabwererenso, adatero Katunga. + Ndidachokapo chifukwa cha mpungwepungwe omwe udabuka, ndidakonzeka kuchita nawo chisankhocho koma chidandikhumudwitsa ndi zokangana zomwe zidabukazo. Sikuti ndikukakamira mpando, adatero iye. +",11 +" TCC imema alimi a fodya kulembetsa Bungwe loyanganira za malonda a fodya mdziko muno la Tobacco Control Commission (TCC) lati alimi a fodya omwe sadalembetse nkulipira zitupa zawo alembetseretu kuti akhale nawo mkaundula wa alimi a fodya. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chikalata chomwe bungweli latulutsa chati pofika mwezi wa June chaka chatha, alimi 29 861 ndiwo adali atalembetsa nkulipira zitupa zawo. + Alimi ayenera kulembetsa mkaundula nthawi isanathe Kutsika kwa chiwerengerochi kwapangitsa kuti bungwe la TCC liwonjezere nthawi yomwe alimi angakalembetsere ndi kulipira zitupa zawo zogulitsira fodya chaka chino mpaka pa 29 January 2016. + Malingana ndi chiwerengero cha alimi omwe alembetsa ndi kulipira ziphaso zawo, taganiza zoonjezera nthawi yolembetsera ndi kulipira kuti alimi omwe sadatero akhale ndi mpata. Alimi onse omwe sadalembetse kapena kulipira ziphaso zawo apangiretu nyengo yoonjezerayi, chatero chikalatacho. + Mkulu woyanganira za ubale wa wa bungweli ndi makampani kapena nthambi zina Mark Ndipita adati vutoli ladza kaamba ka zovuta zingapo monga zokhudza malonda a fodya. + Tikuganiza kuti mwina alimi ena akadali otangwanidwa ndi nkhani zokhudza malonda a chaka chatha komanso zochitika zina zosiyanasiyana monga mudziwa mmene nkhani ya fodya imakhalira, adatero Ndipita. + Iye adati ngakhale zinthu zili choncho, si kuti malonda a fodya a chaka chino asokonekera poti alimi a fodya amayendera mlingo wa fodya omwe amapereka a TCC ndipo umaonetsedwa pa chitupa. + Mkulu wa TCC Albert Changaya, adauza nyuzipepala ya The Nation kuti ogula fodya akunja atsitsa mlingo wa fodya yemwe agule chaka chino kuchoka pa makilogalamu 192.6 miliyoni chaka chatha kufika pa 177 miliyoni. + Changaya sadafotokoze chomwe chapangitsa kuti mlingowu utsike komanso ngati izi zikutanthauza kuti atsitsa mlingo a fodya pa zitupa za alimi pokakhomera. + Fodya ndi mbewu yomwe dziko la Malawi limadalira kwambiri pachuma chake koma pakatipa malonda a fodya akhala akukumana ndi zokhoma makamaka kuchokera ku bungwe la zaumoyo padziko lonse la World Health Organization (WHO) lomwe limachenjeza za mchitidwe wosuta fodya. + Pa malonda a 2015, dziko la Malawi lidapeza ndalama zokwana K189 biliyoni kuchoka pa K205 biliyoni mmalonda a mchaka cha 2014. +",4 +" Covid-19 yakolera Chiwerengero cha Amalawi amene apezeka ndi kachirombo ka coronavirus chatumphuka msabata ikuthayi kuchoka pa 101 kufika pa 203. + Izi zachitika pamene komiti yoona za matenda a Covid-19 Lachinayi idalengeza kuti adapeza anthu 102 amene adachokera ku Zimbabwe ndi South Africa adapezeka ndi matendawa. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ena mwa omwe adafika ku Kamuzu Stadium Amalawi 441 amene adafika mdziko muno kuchoka mdziko la South Africa, msabatayi adathawa kumalo amene amawasunga ku Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre. Ndipo dzikoli limyembekeza kulandiranso anthu ena pafupifupi 300 kuchokera ku South Africa dzulo. + Msonkhano wapadera wa komiti ya Covid-19 omwe udali ku Bingu International Convention Centre mumzinda wa Lilongwe Lachinayi, udakambirana mwakuya nkhani zina ndi zina za matendawa koma adagwirizana kuti kuthawa kwa anthu ku Kamuzu Stadium kudachitika kaamba ka kunyozera. + Chiwerengero chambiri cha anthu omwe adapezeka ndi coronavirus mdziko muno mwezi umodzi wapitawu amakhala anthu omwe adangofika kumene kuchoka mmayiko okhudzidwa kwambiri ngati Tanzania ndi South Africa. + Koma unduna wa zaumoyo wati kubwera kwa abalewa kusabweretse nkhawa iliyonse chifukwa boma lapanga kale zoyenera kuti anthuwo apimidwe nkutsimikizika kuti ali bwino asadabwerere mnyumba zawo. + Mneneri waundunawu Joshua Malango wati ngakhale boma likupanga zotheka kuti kubwera kwa anthuwo kusasokoneze nkhondo yolimbana ndi coronavirus, anthu nawo ali ndi udindo waukulu. + Takhala tikunena kuti asilikali amphamvu pa nkhondoyi ndi anthu eni ake. Anthu akuyenera kutsatira zomwe amauzidwa kupanga kuti apewe matendawo basi, adatero Malango. + Mmodzi mwa anthu obwererawo amene sanafune kutchulidwa wadandaula kuti boma silikuonetsa chidwi pa anthuwo chifukwa likuwasunga pamtetete kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium ku Blantyre. + Chifikireni tikungokhala kuno akuti tidikire zotsatira za zomwe adatiyeza ngati tabwera nkachilomboko kapena ayi koma tikukhala pamtetete, adatero odandaulayo. + Apo nkuti anthuwo asanathawe. + Polankhula kwa atolankhani Lachinayi, wapampando wa komiti yapadera ya Covid-19 Dr John Phuka adati kuthawa kwa anthuwo, komwe kudachitika anthu enanso atathawa malo osungirako anthu kwa Kameza mumzinda wa Blantyre, ndi phunziro. + Takhazikitsa komiti yapadera imene iziunikira momwe anthu ofika kuchoka kunja tikuwalandirira ndi cholinga choti mavuto awa asaonekenso. Ndipepese kwa onse ochoka kunja amene akuoneka kuti anatopa ndi ulendo wochoka ku Joni komanso zochitika, adatero Phuka. + Koma Malango wati boma lakonza kale malo omwe anthuwo akasungidweko ndipo likhala likulengeza za malo oterowo komanso kusamutsa anthuwo kupita nawo mmalowo. + Boma likamapanga zinthu limakhala litakonza kale mapulani. Zonsezo zili kale mmapulani aboma, adatero Malango. + Woyendetsa ntchito za zaumoyo Dr Charles Mwansambo adati bwalo la Kamuzu Stadium lidasankhidwa ngati pofikira chabe potsata mpata woti anthuwo asathinane malo amodzi mpaka atatengedwera kumalo okhazikika. + Dziko la Malawi lidazemba mbindikiro wa mnyumba wa masiku 21 kuyambira pa 18 April 2020 mpaka pa 9 May 2020 gulu la zaufulu wa anthu la HRDC litakatenga chiletso polingalira kuti anthu ambiri adalibe chakudya cha panthawi yonse ya mbindikirowo. + Mmaiko ena omwe mbindikirowo udatheka, boma limathandiza anthu ake ndi chakudya komanso ndalama zogulira zinthu zogwiritsa ntchito pa mbindikirowo. +",6 +"Chikalimba Walonjeza Kugwira Ntchito ndi Tonse Alliance Phungu wa dera la Zomba Changalume, John Chikalimba wati agwira ntchito ndi mgwirizano wa zipani za ndale wa TONSE ponena kuti ndi omwe uli ndi kuthekera kotukula dera lake. +Chikalimba: Mgwirizano wa Tonse ndi wa phindu Chikalimba wauza Radio Maria Malawi kuti akufuna mdera lake mumangidwe chipatala komanso nsewu zomwe wati boma la chipani cha DPP lakanika kuchita mu ulamuliro wake. +Iye wati chipatala cha Namadidi chomwe chili mdera lake chili mu nyumba yobwereka yomwe amalipira 150-thousand-kwacha pa mwezi zomwe anati sizoyenera kuti zizichitika. +Ndi zomvetsa chisoni kuti padakali pano mudera lino tili ndi chipatala chimodzi cha Namadidi chomwe chili mu nyumba ya weni ndipo tikulipira ndalama zomwe zikutionongera ndalama choncho ndawona kuti mgwirizano wa TONSE uli ndi phindu lake maka pa mfundo zokomera anthu zomwe akulonjeza, anatero a Chikalimba. +Mwazina iye watinso mu dera lake mukufunika kumangidwa misewu ya tala komanso sukulu ya secondary yogonera komweko kuti ophunzira omwe asankhidwira ku sukulu za sekondale asamayende mtunda wautali kupita ku sukulu. +",11 +"Pafupi mpomwe wafika? +Mkulu ali pachithunzipa mosapeneka anapanidwa ndipo apa akudzithandiza. Eetu, munthu zikakuthina upanga bwanji? Koma chodabwitsa nchoti nyumba ikuoneka kutsogolo kwakeko ndi nyumba yaikulu (chimbudzi) yomwe idamangidwa ndi cholinga choti anthu ngati, mnzathuyu, azikadzithandiziramo akapanikizika, koma ayi ndithu, akuti pafupi mpomwe wafika. Mizinda ndi matauni athu ukhondo ukusowekera chifukwa cha mchitidwe ngati umenewu. Payenera kukhala malamulo, ngati mmene zilili kumaiko ena, kuti anthu otere azimangidwa akapezeka kuti akumadzithandizira paliponse. +",15 +" Kusanthula chaka cha ulamuliro wa JB Pamene dziko lino mawa pa 7 April likhale likusangalala kuti mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda watha chaka akulamulira, ena ayamikira ulamuliro wake pomwe ena akuti palibe chimene wachita cholozeka ndipo akuti nkungoononga nthawi ndi chuma polonza zisangalalo patsikuli. + Ndemangazi zikuchokera kwa anthu osiyanasiyana monga mkulu wa bungwe loona ufulu wa atolankhani la Media Institute of Southern Africa (MISA-Malawi) Anthony Kasunda; mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito; kadaulo pa zachuma Nelson Mkandawire; mafumu ndi anthu ena. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mwa zina, anthuwa akuti ngakhale zina ndi zina zayenda bwino muulamuliro wa Banda, mwina ndi mwina mwakhota kotero boma likuyenera kukonzamo. + Zina zomwe akuzidandaula ndi kukwera mitengo kwa zinthu, umphawi ndi kusowa kwa chimanga mmisika ya Admarc. + Kapito wati sakuona choti boma la mayi Banda lingamakumbukira kapena kusangalalira kuti patha chaka akulamula chifukwa moyo wa Amalawi uli pamoto. + Kusangalalira chani? Kusangalala kuti atha chaka akulamula? Bola pasakhale zisangalalo chifukwa sindikuona kanthu koti munthu ungasangalalire. Mwina atamasangalala kuti tsiku limeneli adakwanitsa kukhala mtsogoleri wa dziko, watero Kapito. + Iye wati umphawi wakula, maka kumidzi, ndipo kutenga boma kwa Banda kudali kungosonkhezera mavuto ena. + Sitinganene kuti boma lapita lija ndilo limakonza zinthu chifukwa mavuto adaliponso, koma ndalama zimapezeka, koma pano ndiye mavuto osasimbika, akutero Kapito poonjezera. + Kasunda wati ndi kudya mfulumira kunena kuti zinthu zili bwino mdziko muno chifukwa mwina mukuyenera kukonzedwa. + Zinthu zidaipiratu muulamuliro wapita wa Bingu wa Mutharika; idali nthawi ya mdima maka paufulu wa atolankhani. Monga momwe andale achitira, zikuonetsa kuti zomwe Pulezidenti Banda adalonjeza atangotenga dziko lino zidali njerengo chabe. + Adanena kuti MBC idzakhala yotumikira aliyense. Zomwe zikuchitika pano ndi kutumikira boma komanso chipani chake cha Peoples Party (PP), adatero Kasunda. + Iye adatinso msonkhano wa atolankhani kukumakhala otsatira chipani omwe akumadzuma atolankhani akamafunsa mafunso. + Izi ndizo tidadandaula muulamuliro wa Mutharika ndipo mayi Banda adatifunsa momwe akufunira msonkhanowu uzichitikira. Tidapereka maganizo athu kuti pamsonkhanowu pasamakhale otsatira chipani koma zikuoneka kuti izi zidalowa mmakutu osamva, adatero. + Koma Kasunda adathokoza bomali pochotsa msonkho panyuzipepala komanso kuonetsa chidwi chochotsa Gawo 46 la malamulo a dziko lino. + Gawoli limapereka mphamvu kwa nduna kutseka nyuzipepala kapena wailesi ngati awona kuti zalakwitsa. Lamuloli komanso kukweza msonkhowo zidadza muulamuliro wa Mutharika ndipo ena amaona ngati zikufinya ufulu wa atolankhani. + Koma Mkandawire wati zinthu zasintha mwaubwino ndipo dziko likuyenera kuyamika utsogoleri wa Banda. + Iye adati muulamuliro wa Mutharika mafuta ndi ndalama zakunja zinkasowa koma pano iyi ndi mbiri yakale. + Vuto ndi lakuti Amalawi sitiyamika, akutero Mkandawire. Kuti zinthu zibwerere mchimake zimatenga nthawi ndipo njira yomwe boma latenga ithandiza kuti tifike pomwe tikufuna. Inde pali mwina moti mukonzedwe, monga kasamalidwe ka chuma. + Koma T/A Mwakaboko wa mboma la Karonga wati zinthu zingapo zasintha koma zenizenizo sizidaoneke chifukwa Banda akungopitiriza zomwe Mutharika adayamba. + Ziwawa zakula mdziko muno zomwe zikuchititsa kuti ena aziphwanya ufulu wawo [wochita zionetsero] ndi kumaononga katundu wa anthu. Izi zikuyenera zichepe ndipo boma lichitepo kanthu, akutero Mwakaboko. + Koma Charles Kabaghe, wochokera mmudzi mwa Mukombanyama kwa T/A Mwaulambia mboma la Chitipa, wati zinthu zankitsa muulamuliro wa Banda. + Iye wati ngakhale zinthu zikupezeka ndi zokwera mtengo kwambiri ndipo munthu wakumudzi, ngakhale mtauni momwe, sangakwanitse kugula. + Thumba la fetereza tikugula mokwera zedi. Ngakhale anthu akuti zinthu zomwe zimasowa zayamba kupezeka koma tikulephera kugula. Boma lichitepo kanthu kuti mitengo ya zinthu itsike, apo ayi, tili pamoto ndipo tifa kumene, adatero Kabaghe. + Koma Banda adati zinthu mdziko muno zasintha mokomera Amalawi monga kupezeka kwa mafuta agalimoto ndi ndalama zakunja komanso ufulu wa atolankhani. + Msabatayi kudali manongonongo akumveka kuti boma likufuna kukonza zisangalalo kuti latha chaka zomwe kadaulo pazandale, Joseph Chunga, ndi ena adati ndi zosayenera. + Zisangalalozi zibwera pomwe Amalawi akulira ndi kukwera mitengo ya zinthu komwe kwadza ndi kugwa kwa ndalama ya kwacha. + Mutharika adamwalira pa 5 April 2012 ndipo Banda, yemwe adali wachiwiri kwa Mutharika pomwe amatisiya, adalowa mmalo mwake pa 7 April ndipo adasankha Khumbo Kachali kukhala wachiwiri wake. +",11 +"Beam Trust Ikufuna Kuchotsa Chitozo Kwa Mabanja Osabereka Wolemba: Glory Kondowe Bungwe la Beautify Malawi Trust lati anthu mdziko muno akuyenera kuleka kuchitira nkhanza anthu omwe akulephera kupeza mphatso ya mwana, ati ponena kuti zimene zimangopezeka kuti zikuchitika pakati pawo. +Mmodzi mwa akulu-akulu a bungwe-li mayi Emma Mabvunde ndi omwe anena izi kwa azibambo ndi azimayi omwe anasonkhana pa bwalo la mfumu yayikulu Bwananyambi mboma la Mangochi, komwe mwazina amawafotokozera zaudindo umene ali nawo ponetsetsa kuti sakutengapo gawo lotonza anthu omwe akukomana ndi mavuto a ku sabereka mdelaro ndikulimbikitsa anthu omwe ali ndi vutoli kuti azifulumira kukaonana ndi madototolo. +Poyankhulapo a Mabvunde ati nkhaniyi yatuluka chifukwa chamayi wafuko lino Getrude Mutharika chinawakomela kuti nkhaniyi ituluke chifukwa amayi ambiri amanyozeka ndi abale, amzawo komaso amuna awo zomwe zimawapangitsa kuti asa atuluke ndikugwira nawo ntchito za mdziko kuopa kutozedwa ndi anthu chifukwa chosalidwa pankhani yachitukuko. +Malinga ndi mayi Mabvunde, amayiwa amakumanaso ndi nkhaza zosiyanasiyana monga kutha kwa banja, kumenyedwa, kusalidwa pa nkhani ya chitukuko. +Mayi Mabvunde anati, Chifukwa amatozedwa zomwe mbuyomu zimawapangitsa kuti akanena kwandani nde kubwera kwa bungweri tikuona kuti anthuwa ayamba kumasuka kumabwera poyera ndikufotokoza mavuto awo zomwe mbuyomu zimapangitsa kubwedzeretsa chitukuko mbuyo Malawi muno ndetiyeni tizindikire kuwalimbikitsa ngati dzika zathu zomwe kuti tigwirane manja pankhani yachitukuko mdziko muno. +",14 +"Papa ndi Wokhudzidwa ndi Kutenthedwa kwa Nkhalango ya Amazon Wolemba: Sylvester Kasitomu Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati ndiwokhudzidwa ndi moto womwe ukupitiliza kusakaza mitengo ndi zinthu zina zachilengedwe mu nkhalango yayikulu ya Amazon yomwe ili mdziko la Brazil. +Papa Francisko Papa Francisco walankhula izi lero pa mapemphero a masana a ku likulu la mpingo-wu ku Vatican. Iye walankhula izi potsatira kukhudzidwa kwake ndi kubukanso kwa moto mu nkhalangoyi. +Iye wati nkhalango ya Amazon ndi nkhalango yofunika kwambiri chifukwa imapereke mpheya wabwino umene umathandiza kuti anthu aziugwilitsa ntchito ndi kupitilira kuhala ndi moyo. +Posachedwapa akatswiri ena a zofufuza fufuza anatulutsa lipoti lomwe kwambiri limasonyeza kuti ngozi za moto zaonjeza kwambiri kuchitika mu nkhalango yofunika-yi. +Kotero mtsogoleri wa dziko la Brazil naye anati adzipereke pa ntchito yotetedza nkhalangoyi. +Padakalipano anthu a mdziko akuti ayamba kuchita zionetsero zokwiya ndi kulekekera kwa boma la dzikolo pa ntchito yotetedza mkhalango-yi. +",18 +" Achotsa mavenda popanda ziwawa ku Lilongwe Kunali njinga yapulula machaka ku Lilongwe Lachisanu lapitalo pomwe anthu mazanamazana amabwerera mmakwawo opanda kanthu mmanja atalephera kukolola posalima akuluakulu awochita malonda munzindawu atatsogolera ntchito yochotsa ogulitsa malonda mphepete mwa misewu. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mazanamazana a achinyamata ochokera mmadera osiyanasiyana adakhamukira munzindawu okonzeka kuti ngati ntchitoyo ikanathera mziwawa ngati zimachitikira mmbuyomu, ndiye kuti apindula pothyola sitolo za anzawo ndikutolamo katundu. + Mmbuyomu, ntchito ngati yomweyi imayendetsedwa ndi apolisi okhaokha, imatha tsiku latunthu mwinanso kulowelera linalo kaamba kakuti achinyamata ambiri amapezerapo danga lakuba msitolo koma ulendo uno ntchitoyi idatenga maola atatu okha ndipo kunalibe chiwawa chodetsa nkhawa. + Mneneri wapolisi wa chigawo cha pakati John Namalenga adati ntchitoyi idayenda bwino chifukwa akuluakulu aochita malondawo adali patsogolo pantchitoyi ndipo ochita malondawo amaopa kuti angadzawapange chikuwawe ngati aonekere akudzetsa chisokonezo. + Ntchitoyi inayenda bwino chifukwa cha njira yomwe tinagwiritsa ntchito potsogoza atsogoleli aochita malondawo. Njirayi ndiyothandiza kwambiri chifukwa akanakhala apolisi okhaokha, anthu akanazitengera pamgongo ndiye sizikanayenda bwino. Tikuthokoza atsogoleriwo polola kugwira nafe ntchitoyi, adatero Namalenga. + Tsikulo, apolisi anali atayalana kale mu mzindawu ndipo adali atayambapo kale kuletsa ena mwaochita malonda omwe anali atayamba kale kuyala malonda awowo koma pamaoneka kusanvana. + Posakhalitsa, galimoto za polisi ziwiri zidatulukila zitadzala ndi a komiti yoyanganira mavenda munzindawu atavala mabibo a polisi ndipo adayamba kusamutsa anzawowo omwe sadavute. + Mmodzi mwa ochita malonda mumzindawu Ibrahim Yotamu adati mavendawo sakadalimbana ndiakuluakulu awowo chifukwa ndiamene angawapatse mwayi opeza malo ochitirapo malonda mumsika wobvomelezeka waboma ngati zinthu zingavutiletu. + Awa ndiye timati eni malo mumsikamu ndiye kuchita nawo masewera, ukhoza kudziotcha zala chifukwa kuti tipeze malo mumsikamu timadzera mwa iwowa ndiye kuti uoneke dolo pano, ukhoza kulirira kuutsi, adatero Yotamu. +",2 +"Anthu 14 Afa Mdziko la DRC Wolemba: Glory Kondowe Anthu pafupifupi 14 afa lachitatu potsatira kugumuka kwa nthaka kudera lina komwe anthu akukumba miyala ya mtengo wapatali ya gold mdziko la Democratic Republic of Congo DRC. +Ngoziyi yachitika mu tawuni ina yotchedwa Kampene ndipo malinga ndi wailesi ya BBC anthu ena atatu agonekedwa pa chipatala china atavulala modetsa nkhawa. +Malinga ndi malipoti zikusonyeza kuti ngozi za mtunduwu zikuchitika kwambiri mdzikolo kaamba kakusowa chitetezo komanso zipangizo zokwanirazamakono. +Pakadali pano boma la dzikolo lapereka uthenga opepesa ku banja omwe akhudzidwa ndi ngoziyi. +",14 +"YCW Ichilimike Polimbikitsa Akhristu za Baibulo-Sichinga Mamembala a bungwe la achinyamata mu mpingo wakatolika la Young Christian Workers (YCW) mu dayosizi ya Mangochi awapempha akuti akhale patsogolo pokonda kuwerenga baibulo kuti akhale mboni zenizeni zauthenga wabwino mu chaka chino cha baibulo. +Bambo mlangizi wa achinyamata mu dayosizi-yi bambo Christopher Sichinga ndi omwe anena izi lamulungu ku parish ya mpingowu ya Kausi komwe kumachitikira msonkhano wa atsogoleri a bungwe-li mma section onse opezeka mu dayosizi-yi. +Iwo ati mpingo kuyembekezera kuti membala a bungweli ndi omwenso akhale patsogolo polimbikitsa ena zaubwino wokonda kuwerenga mau a Mulungu. +Mpingo ukuyembekezera kuti iwowa akhala patsogolo kumemeza ena kuti akonde kuwerenga baibulo, kuhala nalo kumanso kukhala chomwe baibulo likunena, anatero bamboo Sichinga. +Polankhulanso wachiwiri kwa President wa bungwe la YCW mu dayosizi ya Mangochi, Peter Mukhori anati bungwe la YCW mu dayosizi ya Mangochi liyesetsa pa ntchito zokweza mpingo-wu mchakachi. +Anthu ambiri amati sitimakonda zauzimu koma ife tikutsutsa zimenezo. Chaka chino tikufuna tiwaonetse anthu kuti zauzimo ziliko ku YCW ndipo posachedwapa tikhala ndi retreat yomwe ikachitikire ku phiri la Unangu komwe ndi malo oyera mu dayosizi mwathu muno, anatero a Mukhori. +Iwo ati chakchimenechi awonetsetsanso kuti athandiza parishi imene ikusowa thandizo lapadera. +",13 +"Bungwe la Umodzi Community Lathandiza Zipatala za Mboma la Dedza Bungwe la Umodzi Community mboma la Dedza lapereka katundu osiyanasiyana othandizira pa ntchito yolimbana ndi matenda a COVID-19 mzipatala zosiyanasiyana mbomalo. +Mkulu wa bungweli a Philimon Kavala ati bungwe lawo linagula katunduyu ndi ndalama zosachepera 3 Milion Kwacha ndi cholinga chothandizira boma polimbana ndi muliri-wu. +Iwo ati bungwe lawo limagwira ntchito ndi anthu omwe anapezeka ndi kachirombo ka HIV omwe akuona kuti ali pa chiopsezo chachikulu kamba kakufika kwa ku matenda-wa. +Bungwe la Umodzi Community Development tikupanga project yomwe ikubweretsa anthu onse omwe anapezeka ndi kachilombo ka HIV. Titaona kuti anthu omwe amalandira mankhwala a ma ARV chitetezo chimakhala chotsika taganiza zothandiza ndi zipangizo zoyezera matenda a COVID-19, anatero a Kavala. +Iwo ati athandiza ndi katundu okwanira 3 million pomwe anagula ma thermometer, ma rechargerble batteries komanso ndowa. +",6 +"Sukulu za Katolika 7 Zitsekulidwa; Mkangano wa Hijab Watha Pali chiyembekezo chakuti sukulu zisanu ndi ziwiri za mpingo wa katolika zomwe zinatsekedwa chifukwa cha kusamvana pa nkhani ma hijab omwe ophunzira achisilamu amafuna kuti adziloredwa kuvala kumutu msukulu ati zitha kutsekulidwa pamene sukulu zina zidzatsekulidwe, nthenda ya COVID-19 ikadzatha. + Mkulu oyanganira maphunziro msukuluzi mu dayosizi ya Mangochi a Felix Masamba ati izi zili chomwechi potsatira zokambirana zomwe anali nazo ndi atsogoleri osiyanasiyana a zamaphunziro msukuluzi. +Iwo anenanso izi pamene amakumana ndi magulu ena monga aphunzitsi, mafumu ndi magulu oyendetsa sukuluzi pa sukulu ya sekondale yoyendera ya St. Marys mboma la Machinga. +Tikugwirizana bwino kwambiri ndi mafumu ndipo ife ndi okondwa ndi zimenezi. Tagwirizana kuti tikatsekulira sukuluzi sipapezekanso ophunzira ovala hijab ndipo mafumu alonjeza kuti ayitanitsa msonkhano kuwafotokozera makolo ndipo sukulu ikazayamba mwana aliyense azabwera ndi kholo lake kuzasayinira kuti samavala hijab, a natero a Masamba. +Ndipo mmawu ake Senior Group Village Headman Chileka yati anthu a mderalo agwirizana zakuti sukuluzi zikatsekulidwa pasapezeke ophunzira wovalanso chovala chotchedwa hijab ponena kuti akuyenera kutsatira malamulo a sukulu osati a chipembedzo. +",3 +" Agwira onyoza mtsogoleri wa dziko lino Amayi awiri ati apolisi adawamanga sabata ikuthayi powaganizira kuti adanyoza mtsogoleri wadziko lino, Joyce Banda ndi chipani chake cha Peoples Party (PP) ati atakana kulandira chovala chamakaka achipanichi kuti avinire mtsogoleriyu. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Amayiwa ati adakananso kulowa mgulu la amayi anzawo omwe amavinira mtsogoleriyu pomwe adakayendera dera lawo. + Oganiziridwawa, Eliza Kusheni wazaka 26 ndi Dorothy Ngonga wazaka 24 adatulutsidwa pabelo la bwalo lamilandu la Mwanza Magistrate Lolemba atakhala masiku asanu mchitokolosi cha apolisi. + Wapolisi wamkulu ku Mwanza, Ellobiam Banda, adatsimikizira zakunjatidwa kwa awiriwo koma iye adati amayiwo sadamangidwe pochitira mtudzu mtsogoleri wadziko lino monga akunenera. + Iye adati kumangidwa kwa awiriwo kudadza malinga ndi kusagwirizana pakati pa iwo ndi amayi amderalo. + Amayi awiriwa agamulidwa pogwiritsa ntchito mawu onyoza. + Zikuganiziridwa kuti amayi awiriwa adanyoza mayi wina, Martha Mazinzi potsatira nsanje yomwe idakula, adatero wapolisiyu. + Iye adati atangonjata amayiwo Lachinayi, oganiziradwawo adatulutsidwa pabelo Lolemba chifukwa apolisiwo adali otangwanidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino pomwe amakayendera kumeneko. + Zotolera za apolisi zikutsutsana ndi zimene oganiziridwawo komanso mkhalakale wachipani cha DPP, Bright Kachingwe kumeneko akunena. + Ngonga wati iye ndi mayi mnzakeyo adazizwa ndikumangidwa kwawo chifukwa patsikulo sadachitire mtudzu aliyense. + Patsikulo timachokera kundende ya Mwanza pomwe tidakumana ndi amayi 6, mmodzi mwa iwo adavala chovala cha makaka achipani cha PP, ndipo ndidathirira ndemanga kuti chovalacho chidali chabwino, adatero mayiyo. + Ngonga adati atazindikira kuti zinthu zidayamba kutentha, iye ndi mnzake adachoka pamalopo pomwe adabisala mgolosale yomwe awiriwo amagwira ntchito. + Iye adati apolisi adabwera pamalopo kudzawanjata popanda zifukwa zokwanira. + Awiriwo adatulutsidwa pabelo posapereka chikole chilichonse. Bwalo lidalamula kuti awiriwo adzikawonekera kupolisi Lolemba lililonse. + Kachingwe adati chipani ndichokhudzidwa ndi kunjatindwa kwa awiriwo. +",11 +" Ati boma lisabweze ndalama ku FDH Anthu ena otsata mmene zinthu zikuyendera mdziko muno aopseza kuti akonza zionetsero ngati boma limvere zonena za banki ya FDH kuti libwezeko K1.1 biliyoni mwa ndalama K9.5 biliyoni zomwe adagulitsira banki ya Malawi Savings Bank (MSB). + Sabata yatha zidadziwika kuti banki ya FDH yalembera boma kuti libweze ndalamazi ponena kuti padali zingapo zomwe sadaunikire bwino panthawi yogulitsanayo. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Koma boma lakana kale kuti silibweza ndalamazo, zomwenso zasangalatsa othirira ndemanga kuti ndalamazi zisaperekedwe. + Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa ogula la Consumers Association of Malawi (CAMA) John Kapito wati boma lichite zomwe likulankhula. + Zimatere kuti lero akutiuza kuti sabweza ndalamazo pamene kuseri apanga kale, tazionapo zotere zikuchitika. Pogulitsa bankiyi ife timati sagulitsa atatitsimikizira kuti satero koma mapeto ake tidamva kuti agulitsa. + Lero boma litha kutilimbitsa mtima kuti sabweza ndalamazo koma mawa mumva kuti abweza kale. Ife tikupempha kuti chonde boma lisatero, adatero Kapito. + Iye adati boma liganizire kuti zinthu sizili bwino mdziko muno kumbali ya chuma ndipo ndi kulakwa kuti ndalama zipite mnjira zotere. + Panopa tili pantchito yopeza ma triliyoni a bajeti ya dziko lino. Ndiye ngati tingapereke ndalamazi anthu akhala pamavuto chifukwa iyi ndi misonkho yathu, adaonjeza Kapito. + Mu July 2015, boma lidagulitsa MSB ngakhale Amalawi ambiri adachenjeza kuti lisagulitse bankiyi. Koma mathero ake, boma lidagulitsabe bankiyi pamtengo wa K9.5 biliyoni. + Winanso womenyera ufulu wachibadwidwe, Martha Kwataine, wati zomwe zikuchitikazi ndi kubera Amalawi ndipo boma lisayerekeze. + Banki idagulitsidwa pamtengo wotsika ndi kale, lero akuti tibwezenso ndalama zina, zoona? Ichitu nchibwana ndipo Amalawi tisalole zimenezi. Ngati boma libweze ndalamazi kumbali ife osadziwa, ndiye timema Amalawi kuti tichite zionetsero chifukwa uku nkutitengera pamgongo, adatero Kwataine. +",2 +"Papa Watsiriza Ulendo Wocheza Mmaiko a mu Africa Wolemba: Thokozani Chapola ria.mw/wp-content/uploads/2019/09/pp.jpg"" alt="""" width=""525"" height=""297"" />Papa pa ulendo wake wa mu Africa Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko watsiriza ulendo wake wocheza mdziko la Mauritius. +Ali mdzikolo, Papa wachita zokambirana ndi atsogoleri a ndale, ma episkopi komanso magulu ena a mumpingo. +Iye wayamikira ubale wabwino omwe ulipo mdzikomo pakati pa zipembedzo ndi mitundu ya anthu. +Dziko la Mauritius lili chi chiwerengero cha anthu okwana 1.3 million ndipo 52 percent ndi achipembedzo cha Hindu, 30 percent ndi akhristu a mpingo wa katolika ndipo 18 percent ndi achipembedzo cha chisilamu. +Papa wakhala ali pa ulendo kwa sabata yathunthu, woyendera mayiko ena a mu Africa komwe wayendera mayiko a Mozambique ndi Madagascar asanafike mdziko la Mauritius. +Mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu lero akubwelera ku likulu la mpingo wa katolika ku Vatican mdziko la Italy komwe amakhala. +",13 +" Tinkaimba limodzi kwaya Mdalitso suoneka pakudza munthu umangozindikira walandira mphatso koma osadziwa kuti yachoka kuti malingana ndi ntchito zomwe ukuchita monga momwe a mvula zakale adanenera kuti ntchito iliyonse ili ndi mphotho yake. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kudzipereka komwe adachita Joseph Kaluwa ndi Victoria Mdala Kaluwa mchaka cha 2014 posankha kutumikira Mulungu mnjira ya kwaya patchalitchi ya mpingo wa chikatolika wa Don Bosco ku Lilongwe kudawalunjikitsira kumoyo wina wopambana. + Awiriwa akuti amaimba kwaya limodzi ndipo kenako adagwa mchikondi atakhutitsidwa kuti iwo adalengedwa kuti adzakhale limodzi ngakhale kuti adabadwira ndi kukulira mbali ziwiri zosiyana za dziko lino la Malawi. + Joseph ndi Victoria tsiku la ukwati wawo Ndinkasangalala tikamaimba ndipo ndikamamva mawu ake a nthetemya. China chomwe chidanditenga mtima nchakuti amakonda kupemphera ndi kutumikira kutchalitchi, adatero Joseph. + Iye adati adayesetsa kuti awiriwa akhale pachinzake cha mchimwene ndi mlongo kwa miyezi yokwana 6 ndipo ataona kuti ena akhoza kungobwera nkuphumitsa adaganiza zomasuka ndipo mwa mphamvu ya Mulungu yomwe idawakumanitsa zinthu zidatheka. + Joseph adaonjeza kuti panthawiyo nkuti atangomaliza maphunziro ake a zowerengera ndalama koma asadayambe ntchito ndipo Victoria adali akadali pasukulu koma iwo sadawerenge izi pozindikira kuti Mulungu adzawatsogolera. + Tidalimba mtima ndipo tidasangalala kuti makolo ndi abale athu adatithandiza kwambiri mpaka tidapanga chinkhoswe ngakhale kuti chidali cha mnyumba koma pambuyo pake tidamanga ukwati woyera omwe tidakadalitsira ku Tchalitchi ya Don Bosco pa 29 September 2015, adatero Joseph. + Victoria adati sadalabadire zoti panthawiyo Joseph samagwira ntchito iliyonse chifukwa iyeyo adakonda munthu osati chuma ndipo adali wokondwa kwambiri makolo ake atavomereza chibwenzicho. + Iye adati ali ndi loto limodzi lokhala pa banja la ulemu ndi lowopa Mulungu monga momwe zilili pano.n Pemphero langa ndilakuti zipitirire monga momwe zilili pano. Ndili pabanja lokoma kwambiri ndipo ndimakonda mwamuna wanga kwambiri ndi ana anga atatu, adatero Victoria. + Joseph amachokera ku Nthalire mboma la Chitipa ndipo pano akugwira ntchito ku nthambi yolondoloza za momwe ndalama zikuyendera ya Financial Intelligence Unit ndipo Victoria amachokera kwa T/A Kwataine ku Ntcheu ndipo akugwira ntchito ku nthambi ya za nkhalango mboma. +",15 +" Boma likutengera a Malawi kumtoso Pamene nkhani ya malamulo oyendetsera zisankho ili mkamwamkamwa, mkulu womenyera ufulu wa anthu, John Kapito, wati nkhani za magetsi, madzi ndi kulowa pansi kwa chuma ndi zofunika kuti ziunikidwe mozama ndi Nyumba ya Malamulo yomwe yayamba dzuloyi. + Kapito amathirirapo ndemanga pankhani yomwe yamanga nthenje yoti aphungu a nyumbayo sakambirana malamulo azisankho kaamba koti nduna sizidathe kuwaunika. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kayendetsedwe ka chisankho sikasintha aphungu akapanda kukambirana malamulo atsopano Izi zakwiyitsa mabungwe omenyera ufulu wa anthu a Centre for the Development of People (Cedep) ndi Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) omwe adapempha aphungu kuti anyanyale nkhumano wa nyumbayo mpaka boma litaika pamndandanda wa zokambirana malamulo atsopano oyendetsera zisankho. + Koma Kapito akuti ngakhale nkhaniyo ili yofunikira kwambiri, mavuto a magetsi, madzi ndi kulowa pansi kwa chuma ndi zinthu zofunika kuthana nazo mwachangu. + Anthu ambiri akupanga phokoso kwambiri ndi malamulo oyendetsera zitsankho. Nzoona malamulowo ndi ofunika, koma pali nkhani zina zofunika kwambiri zomwe anthu sakuzitchula. Tiyeni tiunike vuto la magetsi, madzi ndi chuma omwe akhudza miyoyo ya Amalawi ambiri, adatero Kapito. + Iye adati kulimbikira kuti nyumbayo ikambirane malamulo azisankho nkusiya mavutowa nchimodzimodzi bambo kumasunga ndalama zogulira galimoto pamene ana ake akusowa chakudya, zovala, komanso athamangitsidwa fizi ku sukulu. + Padakali pano komiti yoona zokambirana za nyumbayo yatsimikiza kuti pali malamulo 6 omwe aphungu akambirane, koma Kapito wati sakuonapo lamulo lomwe lingathandize Amalawi mwachangu potengera ndi mavuto omwe akukumana nawo. + Ndaunika malamulo onse omwe ali pamndandanda woti nyumbayo ikambirane, koma palibe lamulo lomwe lithane ndi vuto la magetsi, madzi, komanso kukweza chuma cha dziko lino. + Koma Billy Mayaya, yemwe ndi wodziwika kwambiri pankhani yomenyera ufulu wa anthu, wati boma likutengera Amalawi kumtoso posaika malamulo a zisankho pamndandanda wa zokambirana. + Nzomvetsa chisoni kuti andale amafuna anthu panthawi yovota, koma kuti apange zofuna zawo amayangana kumbali, adatero mkuluyu. + Mayaya adati malamulo a zisankho ndi ndime yoyamba yoonesetsa kuti Amalawi akulamulidwa ndi anthu omwe akuwafuna. + Imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zili mu lamulolo nkuonetsetsa kuti boma lililonse mukhale dera lomwe amayi okhaokha azipikitsana pampando wa phungu. + Anthu ena omwe akhala akumenyera ufulu wa amayi akuti boma likulakwa kaamba kosatengera malamulowo ku Nyumba ya Malamulo. + Mmodzi mwa amayi omwe amamenyera ufulu wa amayi, Emmie Chanika, adati vuto la Amalawi nkuyanganira vuto mpaka likule ngati momwe mwana amayanganira chilonda mpaka chikule nkufika potukusira. + Amalawi, zitsanzo tili nazo za maiko omwe adapatsa amayi mpata ndipo lero akuchita bwino. Nanga ife tidzapereka liti mpata kwa amayi? adafunsa Chanika. + Iye adati anthu ambiri sachitapo kanthu pankhani zaphindu monga zotukula miyoyo ya amayi, koma nkhani zopanda pake. + Mabungwe a Cedep ndi CHRR adapempha aphungu kuti anyanyale nkhumano ya Nyumba ya Malamulo mpaka boma litabweretsa nyumbayo malamulo a zisankho. + Mkulu wa Cedep, Gift Trapence, ndi wa CHRR, Timothy Mtambo, adapempha boma kuti lichite zofuna za anthu potengera malamulowo ku nyumbayo. + Bungwe la Public Affairs Committee (PAC), lomwe posachedwapa limachititsa misonkhano yokambirana za malamulowo, lati silidayembekezere kuti boma lingawadyetse njomba yotere. + Mwa zina, malamulowo akuti mtsogoleri yemwe wachita bwino pa zisankho azilumbilitsidwa pakatha masiku 30 kuchokera patsiku loulutsa zitsakho, komanso kuti azipeza mavoto oposa theka la anthu omwe adaponya mavotiwo. Malamulowo akufunanso kuti mboma lililonse mukhale dera lomwe amayi okhaokha azipikitsana pampando wa phungu. + Malamulowo akufuna kuti bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lizipatsidwa ndalama zokwanira kuti ntchito zake ziziyenda bwino. +",11 +" Akhazikitsa tindege tothandiza zaumoyo Pali chiyembekezo chakuti mavuto omwe amakumana nawo ogwira ntchito mzipatala za kumidzi ndi anthu okhala mmaderawo achepa ndi makina a tindege otchedwa drone mChingerezi polumikizitsa maderawa ndi zipatala zikuluzikulu. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Unduna wa Zaumoyo, nthambi yoyendetsa za maulendo a pa ndenge ndi bungwe loyanganira za umoyo wa ana la Unicef atsimikiza za ndondomekoyi yomwe ati yayamba kale kugwira ntchito mmadera ena. + Kamodzi mwa tindegeto Mneneri wa bungwe la Unicef Doreen Matonga wati ogwira ntchito mzipatala za kumidzi amakumana ndi mavuto adzaoneni popereka ndi kulandira thandizo la zaumoyo komanso pakakhala ngozi zodza mwadzidzidzi Madera ena amavuta kufikako. + Iye adati mavuto odziwika kwambiri ndi nkhani ya mayendedwe pokatenga mankhwala kuchipatala chachikulu kapena pokayezetsa magazi ndi makhololo komanso polandira zotsatira za zoyesazo. + Tidapeza kuti pali zipatala zina zomwe ogwira ntchito amayenera kupalasa njinga mtunda pafupifupi makilomita 70 kuti akatenge mankhwala kuchipatala chapaboma ndi kubwereranso mtunda onga omwewo. + Kuwonjezera apo, pakakhala zofunika kuyeza monga malungo kapena makhololo, pamatenga nthawi kuti zikafike ku chipatala chomwe amayeza komanso kuti zotsatira zake zifike pomwe wodwalayo akungodikilira, adatero Matonga. + Iye wati apa azikgwiritsa ntchito tindegeto, timenenso tizithandiza kujambula zithunzi za Madera amene kwagwa ngozi komanso kupititsa patsogolo ntchito za Internet. + Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe wati ndondomekoyi idayamba mmwezi wa February mmadera ochepa ndipo idakhazikitsidwa mwezi watha kuti iwunikidwe ngati ndiyothandizadi. + Ikangogwira, mavuto ambiri atha chifukwa nzoonadi kuti anthu a mmadera a kumidzi amakumana ndi mavuto kuti alandire thandizo moyenera, adatero Chikumbe. + Woyanganira za maulendo a ndenge ku unduna wa za mtengatenga Hastings Jailosi wati ndondomeko yonse yaunikidwa kale bwinobwino ndipo sipazikhala kusokonezana pakati pa tindengeti ndi ndenge zikuluzikulu zonyamula anthu ndi katundu. + Iye wati tindegeti tikhala mmasayizi osiyanasiyana ndipo tizinyamula katundu wa milingo yosiyanasiyana. + Tina tikhoza kunyamula katundu wolemera makilogalamu 25 ndipo tina ntocheperako, adatero Jailosi. +",6 +" Chotsani chiletso chogulitsa chimanga kunjaMCCCI Bungwe loona za malonda ndi mafakitale la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) lapempha boma kuti lichotse chiletso chogulitsa chimanga kunja. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pulezidenti wa bungwelo Karl Chokotho adapereka pempholi Lachinayi potsegulira chionetsero cha malonda ku Gateway Mall mumzinda wa Lilongwe. + Iye adati chiletsochi chikupsinja kwambiri alimi angonoangono chifukwa omwe akukakamizidwa kugulitsa chimanga chawo mdziko mommuno pa mitengo yotsika poyerekeza ndi mitengo yomwe maiko ena akugulira. + Chokotho: Alimi akadapha makwacha Pa Tanzania pomwepa, chimanga chikugulidwa pamtengo okwera mwina kuposa katatu mtengo wa boma la Malawi ndiye alimi akadaloledwa kuti azigulitsa chimanga chawo mmisika ngati imeneyi, akadapha makwacha, adatero Chokotho. + Iye adati akudziwa kuti dziko la Malawi likuyenera kugula ndi kusunga chimanga kupangira zogwa chaka cha mawa zomwe sizikudziwika koma adati vuto lomwe lilipo ndi loti bungwe la Admarc lomwe limagulako bwino silikugulanso chimangachi. + Boma litakhazikitsa mitengo, alimi adali ndi chiyembekezo kuti mwina apindula pogulitsa ku Admarc koma nzosabisa kuti Admarc siyikugula chimanga moti alimi akungobwerera nacho mapeto ake mavenda akupezerapo danga, adatero Chokotho. + Nduna ya za ntchito, achinyamata, masewero ndi kuphunzitsa anthu ntchito, Francis Kasaila, yemwe adali mlendo wolemekezeka pa mwambowo, adati mpofunika kuzama ndi kukambirana bwinobwino chiletsochi chisadachotsedwe. + Ndunayo idati alimi ambiri angonoangono amadalira pologalamu ya boma ya sabuside paulimi pomwe omwe amagulitsa chimanga kunja ndi mavenda zomwe zikutanthauza kuti kuchotsa chiletsochi ndiye kuti mavenda ndiwo apindule pa sabuside ya boma. + Vuto lalikulu ndi loti omwe amagulitsa chimanga kunja ndi mavenda omwe amagula kwa alimi pamitengo yolira ndiye zikutanthauza kuti olo titachotsa chiletsochi, alimiwo sathandizika ayi agulidwabe pa mtengo olirawo ndipo mavenda ndiwo apindule, adatero Kasaila. +",2 +" Pepani Ngonamo, Chirwa Kudali ntchito ku FAM pamene amafuna kochi wa timu ya fuko ya Flames. Eddie Ngonamo, Nsanzurwimo Ramadhan, Ernest Mtawali ndi Gilbert Chirwa ndiwo adalembera ndipo a FAM atenga Mtawali ndi Ramadhan ngati kochi ndi wachiwiri wake. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Aganyu alankhula zambiri pa kutengedwa kwa akamunawa, komanso kuikapo maganizo awo potaidwa kwa Ngonamo ndi Chirwa. + Lero tikubweretsa zomwe aganyu akhala akulankhula pa za ganizo la FAM. Pamene ena akuti ganizo la FAM lilibwino, ena akuti zalakwika. + Amwene pamenepaja pakufunika Ngonamo. Mukudziwa kuti dala aja ali ndi Preparatory Certificate for A licence, akuphunzitsanso zamasewero ku Karibu Academy. A FAM adakonza kale zimenezo. + Mukudziwanso kuti dala aja adachita maphunziro limodzi ndi Jos Mourinho, komanso akhala akuphunzitsa mmaiko akunja. Basi dala aja asalemberenso ntchito imeneyi, chifukwa zikuoneka kuti samawafuna. Koma kuwasiya a Chirwa aja ndiye sadalakwe mukudziwanso kuti adaithawa Bullets, wina adatero. + Mkulu winanso adaperekapo maganizo ake. Zili bwino apapa, Ngonamo adalephera atapatsidwa mwayi ku Flames mu 2013. Flames idapambana gemu imodzi tikusewera ndi Namibia kwawo koma patsikulonso iyeyo panalibe. Namibia itabwera kuno tidalephera kuichinya. Amuchita bwino. + Komanso ndidamuona Ngonamo akukhazikitsa malamulo okhwima ukafuna kujambula Flames ku training, iye amati tizimupempha chifukwa bwana ndiyeyo. Inuyo mudazionapo kutiko zimenezi? Ngati mukuti akuphunzitsa ku Karibu ndiye kuti amaphunzitsa ana, ndiye mukufuna ayambe kuphunzitsa Flames mpakana? Imeneyo ndiyo ntchito ya pa Malawi. +",16 +" Tidakumana Bwanji: Padali pagalaja ku Area 25 Garage ndi malo okonzera galimoto, koma ukachita mphumi malowa uthanso kudya nawo bwino monga momwe Mike Tembo adachitira. + Iyetu adasodzerapo msoti womwe akumanga nawo banja pa 7 May pa Sana Multi-Purpose Hall mumzinda wa Lilongwe. + Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mike Tembo amagwira ntchito ku Leyland Motors koma amadziwika kwambiri chifukwa cha udindo womwe adali nawo kutimu ya Silver Strikers komwe ankagwira ngati mlembi. Njole yomwe mkuluyu watola ndi Annie Nkhandwe yomwe ikugwira ntchito ku JTI. + Annie ndi Mike patsiku la send-off Mike akuti mudali mu December 2013 pamene Mulungu adayamba kulumikizitsa awiriwa. Iye akuti adapita kugalaja ya ku Area 25 komwe amakakonzetsa galimoto. Amadikira kuti mpaka aikonze. + Akutitu mpaka cha mma 6 koloko madzulo ali pomwepo, anthu atayamba kuweruka ndipo apa naye Annie ataweruka amadutsira mbali yomwe kudali Mike. Apa nkuti awiriwa asakudziwana. + Koma likalemba lalemba basi, Mike adanunkhiza mafungo ndipo adamulonda mtsikanayo ngakhale samamudziwa. Moni ndi amene adali woyamba ndipo adasiyana atangofunsana maina. + Mosachedwa galimotoyo akuti adamaliza kukonza koma Annie nkuti atanyamuka kale. + Sindidachedwe, koma kukailiza kuyamba kumulonda mpaka ndidamuona akulowa pageti yakwawo. Ndidamukuwira, iyeamvekere, you were following me? Apo ndidalankhula molimba mtima ndimvekere, ndimafuna ndidzaone pamene my future wife akukhala ndipo adaseka, ine ulendo, adamusereula motero. + Kuchoka apa, awiriwa akuti amakumanabe, koma Mike akuti adapanga kaulendo kokaonera mpira wa Zambia pa Taytaz mmbali mwa msewu wa Mchinji osadziwa kuti mkuluyu alindi zina zoti achite kupatula mpirawo. + Chichewa chidagwa, namwali adayesera kuzemba koma Mike sadasinthe mawu. Njoleyi akuti idangomuuza kuti ukhale kaye serious. Mike adaonetsa izi ndipo ubwenzi udayamba. + Awiriwa apanga kale send-off sabata yatha pamene akukonzekera ukwati. + Mike amachokera mmudzi mwa Kamuthuleni Tembo kwa Inkosi Mtwalo mboma la Mzimba pomwe Annie ndi wa mmudzi mwa Kamunthambani Nkhandwe kwa Mtwalo komweko ndipo onse akuchokera kumabanja achifumu. +",15 +" Luso la mpira ndilo lidandidolola Sabata zitatu zapitazo Sindi Simtowe adamanga ukwati ndi Ardron Msowoya, mnyamata yemwe akugwira ntchito ku Inde Bank. Kwa iwo amene amadikirira pa Sindi, pepani, mtima wa njoleyi wasankha wokha. + Kodi Sindi, katswiri womwetsa zigoli mtimu ya Malawi Queens, adakumana bwanji ndi wachikondi wake? Ardron akuti lidali tsiku lomwe adasiya ntchito yake ya mbanki ulendo ku BYC kukaonera njoleyi ikudoda osati masewero. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Sindi ndi Ardron tsopano ndi thupi limodzi Iye akuti wakhala akuwerenga munyuzipela za luso la Sindi kotero adaganiza zoti akadzionere yekha momwe namwaliyu amachitira. + Iye adatchera mafainolo a chikho cha OG Issa pamene timu ya Sindi, Tigresses, inkakwapulana ndi Diamonds. Ndiyetu ati udalipolipo. + Ardron atangofika pabwalopo, akuti adafunsa anthu kuti amulozere Sindi. Atandilozera kuti Sindi ndi uyo, ndidamuitana ndi kumupatsa moni. Sindidathe nthawi chifukwa amayenera alowe mbwalo koma akadandipatsa nthawi yaitali, ndimafuna ndipemphe nambala yake pomwepo. + Masewero atayamba, Ardron adasangalala ndi ntchito za Sindi. Akuti amati akadumpha, kuthamanga, kuchinya zigoli, mtima wa Ardron udakanika kudzigwira ndipo adakalephera kugona. + Pakutha pa sabata zitatu adali atapeza kale nambala ya Sindi ndipo mu May 2014 macheza sadachedwe, koma apo akuti amangocheza ngati munthu ndi mnzake. + Mu August 2014 ubwenzi udayamba. Koma kuti nditulutse Chichewa zidavuta, zimaonetsa kuti aliyense amafuna mnzake koma woyambitsa amasowa, adatero Ardron. + Mu June ndidamulembera uthenga wapafoni, koma sadayankhe, ndiye ndidamulemberanso wina kuti darling why are you not responding? chiyambi cha ubwenzi wathu chidatero, adatero mnyamatayu, amene wachita kulowola Sindi. + Ukwati udali pa 6 August ku Red Cross Church of Christ mumzinda wa Blantyre. +",16 +"Amayi a CWO Asamala Chipatala Cha Mzuzu, Lilongwe Wolemba: Sylvester Kasitomu Amayi achikatolika ochokera mu Arch-Dayosizi ya Lilongwe ndi Mzuzu Loweruka awayamika kamba kotengapo gawo pa ntchito zolimbikitsa za ukhondo mmadera omwe akukhala. +Wapampando wa bungwe la amayi achikatolika mdziko muno Catholic Women Organisation (CWO) mayi Lucy Vokhiwa anena izi pothilirapo ndemanga pambuyo pa tchito yomwe amayi a mma dayosizi-wa achita maka pokasamalira mzinda wa Lilongwe komanso chipatala cha Mzuzu komwe kunali koipa kaamba ka zinyalala. +Iwo ati zomwe amayiwa achita zikusonyezadi kuti ali ndi chidwi komanso kudzipereka pa ntchito zokonza komanso kusamalira zachilengedwe zomwe mpingo ngakhalenso dziko zimaphunzitsa kwa anthu. +Amayi a ku Mzuzu anakayamba ndikupereka zinthu kuchipatala cha mzuzu pamene akulilongwe anapita mumsika wa mumzindawu zimene zikuonetsa kuti chilengedwe tikuchipanga control, anatero mayi Vokhiwa. +",14 +" Okhudzidwa ndi ngozi ya madzi alandira mbewu Nduna ya zaulimi Dr Allan Chiyembekeza yapempha alimi amene adakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi kuti abzale mbatata ndi chinangwa chinyezi chisadatheretu mnthaka kuti adzapeze chomwera madzi. + Ndunayo idanena izi masiku apitawa pomwe undunawo umakhazikitsa ndondomeko yopereka mbewuzi kwa alimi amene adakhudzidwa ndi ngoziyo mu January chaka chino. Mwambowo udachitikira mboma la Mulanje. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Maboma onse 15 amene adakhudzidwa ndi ngoziyi ndiwo alandire mbewuyi kuti abzale pamene mvula ikugwabe mmaboma ena. + Ngakhale ndi nkhani yabwino komabe alimi ena akuti izi ndi zosakwanira ndipo boma lisalekere pomwepa. + Olive Chamveka wa mmudzi mwa Mtiza kwa Senor Chief Mabuka mboma la Mulanje adali ndi munda wa maekala awiri koma mundawu udakokoloka. Iye adati mizere 7 yokha ndiyo idapulumuka. + Ndimalima chimanga mmunda umenewu ndipo ndimapha matumba 45. Chaka chino ngakhale thumba la makilogalamu 50 silingakwane. Mavuto awa achimwene, adatero iye. + Chamveka adalandira mbewu ya chinangwa yokwanira kubzala theka la ekala. Ngakhale ena angasangalale ndi mbewuyi, Chamveka sadakondwe. + Mvulatu idasiya kuno, kusonyeza kuti ndidalira chinyontho chomwe chidakalipo zomwe ndi zokaikitsa ngati tingaphule kanthu. Musadabwe kuti sindikusangalala kwambiri. + Boma litipatse chimanga chifukwa tifatu ndi njala. Kupatula zomwe atipatsa lerozi komabe boma lisalekere pomwepa, adatero Chamveka movomerezana ndi Edina Mutakha wa mmudzi mwa Misomali mbomalo amenenso adalandira mbewu ya chinangwa. + Koma Chiyembekeza polankhula atangokhazikitsa ndondomekoyi, adati pali zambiri zomwe boma likuchita kuti likwanitse kuthana ndi mavuto amene anthuwa akukumana nawo. + Iye adati boma lakonza mapologalamu osiyanasiyana kuti afikire alimiwa. + Iyi ndi ndondomeko yoyamba, posakhalitsapa pabwera ndondomeko ya mthirira yomwenso ithandize anthuwa. Izi zichitika pamene alimiwa akudikirira mvula kuti abzale mbewu zina, adatero Chiyembekeza. +",5 +" Gule alipo pa 17 October Zipani za UDF ndi PP zaimika manja kuti sizidzapikisana nawo pamipando ya phungu pachisankho cha chibwereza chimene chikhalepo pa 17 October chifukwa maso awo ali pachisankho chapatatu mu 2019. + Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza zochititsa chisankho cha chibwereza mmalo asanu ndi amodzi (6). Malo atatu akupikisana ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo pamene enawo ndi makhansala. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chisankho cha chibwereza chidalikonso mmbuyomu Chipani cha PP chikupikisana nawo pampando wa khansala wokha pamene UDF malo awiri a khansala ndipo onse sakupikisana nawo pampando wa phungu. + Mneneri wa UDF Ken Ndanga akuti ndondomeko ya chipani chawo ndi kupikisana malo amene akudziwa kuti achita bwino. + Komabe sikuti tangokhala, tili ndi zochitika mmaderawo, adatero Ndanga amene wati kusapikisana kwawo si tanthauzo lothandiza chipani cha DPP. + Ndipo mneneri wa chipani cha PP, Nowa Chimpeni adati maso awo lili pomanga chipani chomwe chidzalowenso mboma mu 2019. + Iyi ndiye ndondomeko yathu. Musandifunse kuti ndi ndondomeko zanji, adatero Chimpeni amene adatsindika kuti PP siyikutha. + Koma katsiwri wa ndale Mustapha Hussein wati zipanizo zikadaganiza mozama chifukwa chisankho chilichonse ndi mwayi wopima mphamvu za chipani. + Ndanga: Chipani sichikutha Zipanizo zati maso awo ali pachisankho cha patatu chomwe chichitike mu 2019. Mmalo mwake, chipani cholamula cha DPP ndi MCP ndiwo sakumwetsana madzi. + Koma Hussein wati PP ndi UDF akuyenera aganize kawiri chifukwa chisankho chilichonse nchofunika popima mphamvu za chipani. + Kukonzekera 2019 kumayenera kyamba pano, ndipo njira yabwino ndi kuchita nawo chisankho chachibwereza chomwe chimaonetsa mphamvu zachipani, adatero Hussein. + Poyankhapo pa maganizo a Hussein, Ndanga akuti chisankhochi sichisonyezo zomwe zidzachitike pachisankho cha 2019. + Chimpeni: Tikukonzekera 2019 Taonapo chipani chikupambana chisankho chachibwereza, koma kubwera chisankho chenicheni kugonja, adatero. + Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza zochititsa chisankho chachibwereza mmalo asanu ndi amodzi (6). Malo atatu akupikisana ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo pamene ena ndi makhansala. + Chipani cha PP chikupikisana nawo pampando wa khansala wokha pamene UDF malo awiri a khansala ndipo onse sakupikisana nawo pampando wa phungu. + MEC idakhazikitsa nthawi ya kampeni pa 13 September ndipo kampeniyi idzatsekedwa pa 15 October kuti pa 17 chisankho chidzachitike. + Bungweli lavomereza anthu 19 kuti apikisane nawo, amuna 15 ndi amayi anayi. Chisankho cha aphungu chichitika kumpoto chakummawa kwa boma la Lilongwe. Kumeneko apikisane ndi Ellen Shaban Kadango woyima payekha, Christopher Joseph Manja woyima payekha, Ulemu Msungama wa MCP ndi Ruben Ngwenya wa DPP. + Aphungu apikisananso kumpoto kwa Lilongwe Msozi komwe apikisane Bruno Daka wa DPP ndi Sosten Gwengwe wa MCP, yemwe adali wotsatira Joyce Banda wa PP pachisankho cha patatu mu 2014. + Ku Nsanje Lalanje apikisane ndi Gladys Ganda wa DPP, Laurence Mark Sitolo wa MCP, ndi Winnie Wakudyanaye woima payekha. + Chisankho cha makhansala chichitika ku Mtsiliza wodi komwe Brighton Golombe Edward wa UDF, Julio Benedicto Jumbe wa DPP ndi Kinwel Frank Zikaola wa MCP apikisane. Kummawa kwa Mayani wodi komwe Nicholas Fackson Josiya wa DPP, Everister Ndaziona Kusina wa UDF, Benson William Lameck wa MCP sakumwetsana madzi. + Nako ku Ndirande Makata wodi chilipo cha makhansala komwe Ishmael Chilambo wa UDF, Thom Lita wa DPP, Thom Harry Litchowa wa MCP, Mathews Joseph Shaba wa PP akupikisana. + Mneneri wa MEC, Sangwani Mwafulirwa wamema anthu ndi zipani kuti zisunge bata pa nthawiyi ndipo aliyense wodzetsa chisokoneza adzalangidwa. +",11 +"Episcope apempha Ansembe kukonzekera bwino chaka chachibalalitso Wolemba: Sylvester Kasitomu p://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/09/msusa.jpg"" alt="""" width=""375"" height=""319"" />Wapempha ansembe akonzekere chibalalitso cha mpingp-Msusa Arkiepiskopi wa arkidayosizi ya Blantyre Thomas Luke Msusa wapempha ansembe mu arkidayosiziyi kuti azikonda kulimbikitsa anthu za moyo wawo wa chikhristu ndi kuonetsetsa kuti akulandira masacrament omwe amayenera kuti alandire mu mpingowu. +Episcope yu wapereka uthenga-wu lachiwiri ku Nantipwiri Pastoral Centre kwa Bvumbwe mboma la Thyolo pa msonkhano wa tsiku limodzi wa ansembe otumikira mu ArchDayosizi-yo. +Iwo anati ndiokodwa ndi mene ansembe akufalitsira uthenga okhudza chaka cha chibalalitso wa chaka chino. +Ife ngati ansembe tikuyenera kukhala patsogolo kuphunzitsa komanso kuwapatsa akhristu athu zomwe akusowa kuti afalitse uthenga wabwino mmadera omwe akufuna kuti apite, anatero ambuye Msusa. +Ansembe pafupifupi 65 otumikira mu Arch-Dayosizi-yi ndi omwe achita nawo msonkhanowo, komwe mwa zina akumbutsana za mwezi wa wapadera wa chibalalitso Extra-ordinary Missionary Month. +",13 +"Papa Wati Akhristu Akhale Opilira pa Mavuto Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wati kukhala odekha popilira zovuta za moyo uno ndiye moyo weniweni wa chikhristu. +Malinga ndi malipoti a Vatican Radio Papa Francisco walankhula izi lamulungu ku likulu la mpingowu ku Vatican. +Iye wati akhristu akuyenera kukhala odekha monga mmene Mulungu achitira popereka mpata kwa anthu ake kuti alape ndi kutembenuka mtima. +Papa Francisco wati Yesu Khristu amawululira akhristu kuti Mulungu ndi wodekha chinthu chomwe iye wati ndi chosangalatsa komanso chobweretsa chiyembekezo. +Papayu walankhula izi pothilira ndemanga pa Uthenga Wabwino womwe unawerengedwa laMulungu la 16 mu nyengo ya pa chaka womwe ndi fanizo la mbewu zabwino ndi nansongole. +Iye wati mu fanizoli antchito anafunsa mbuye wao kuti awalole azule nansongole yemwe anali kukula limodzi ndi mbewu mmunda koma mwini munda anati ayi ndi bwino azisiye zonse zikulire limodzi poopa kuti angazule ndi mbewu zabwino zomwe ndipo kuti nthawi yokolola ndi yomwe idzasiyanitse nansongoleyu ndi mbewu zabwino. +Papa Francisco wati Mulungu yemwe ndi mwini munda amabzyala mbewu zabwino zokhazokha koma kuti satana amapeza mpata maka mu nthawi ya mavuto osiyana-siyana a moyo uno posokoneza anthu omwe mu fanizoli ndi mbewu. +Iye wati pali anthu ena a phuma ofuna kuthana ndi tchimo komanso onse ochimwa. +Pamenepa iye wati akhristu akuyenera kukhala odekha monga mmene Mulungu achitira popereka mpata kwa anthu ake kuti alape ndi kutembenuka mtima. +Papa Francisco wati kukhala odekha popirira zovuta za moyo uno ndiye moyo weniweni wa chikhristu. +",14 +" Kodi malubino tilowere kuti? Kodi tilowere kuti? Mndani amene adzatiteteze ngati boma likulephera kubweretsa yankho? Awa ndi mafunso amene Ian Simbota alinawo. Simbota ndi munthu wa chialubino. Iye ndi mtolankhani ku wailesi ya MBC. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ulendo wotsiriza wa Phiri Mafunso a Simbota akudza kutsatira kuphedwa kwa Yasin Kwenda Phiri, 54, wa mboma la Nkhata Bay. Phiri adaphedwa Lolemba msabatayi ndipo adamuchotsa manja. Imfa ya Phiri, ndiye kuti nkhani zokhudza malubino yafika pa 162 kuchokera mu 2014. Anthu 23 adaphedwa ndipo 10 adasowetsedwa. Komatu kuyambira 2014, palibe munthu amene walandira chilango chifukwa chokhudzidwa ndi nkhani zokhudza malubino. Kodi vuto nchiyani? Simbota akudabwa: Kukhotiko kwapita nkhani zokhudza [United Transformation Movement] UTM, mpaka milandu yawo yatha ife milandu yathu ikukakamirabe kukhotiko. Vuto nchiyani? Kodi akufuna tikakhale kuti? Tilowere kuti? Poyamba amati vuto ndi ndalama, nanga ndalama za ntchito zina zikupeza bwanji? Kukhoti kudapita milandu 44 koma palibe umene udatha. Pena amati vuto ndi akafukufuku palibe, kodi titani? Boma la DPP lidalowa mu 2014 ndipo icho ndi chaka chimene nkhanizi zidayamba mpaka lero pamene tikupita kuchisankho yankho silidabwere. Zaka zisanu ndi zambiri, bwezi boma litapeza yankho pa nkhani yokhudza kuphedwa kwa alubino, adatero Simbota. Koma mkulu wa apolisi mdziko muno Rodney Jose adati polisi yakhazikitsa kafukufuku kuti anjate amene adapha Phiri. Mabungwe kuphatikizanso chipani cha UTM alankhulapo pakuphedwa kwa Phiri ndipo adzudzula khalidwelo. UTM idati kuphedwa kwa Phiri ndi chisonyezo cha kulephera kwa boma la DPP poteteza anthu achialubino. Kuphedwa kwa anthu achialubino kwanyanya ndipo zikuoneka kuti boma lalephera kuthana ndi nkhanizi, ifeyo a UTM tidzaonetsetsa kuti tathana nazo, idatero kalata yosayinidwa ndi mneneri wachipanicho Joseph Chidanti Malunga. Mabungwe amene adzudzulapo pakuphedwa kwa Phiri ndi monga Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Centre for the Development of People (Cedep), Human Rights Defenders Coalition (HRDC) ndi Association of Persons with Albinism in Malawi (Apam). Mtsogoleri wa Apam, Overstone Kondowe adati kuphedwa kwa Phiri ndi chitsimikizo kuti boma la DPP lalephera. Taonapo maiko amene tayandikana nawo adathana nazo kale, koma ifeyo tikulepherabe, adatero Kondowe. +",7 +" Nyumba ya Malamulo yakhutira ndi MEC Komiti yolondoloza malonjezo a boma ku Nyumba ya Malamulo yati ndiyokhutira ndi lipoti la bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC). + Bungwe la MEC lidawonekera pamaso pa komitiyo Lachiwiri msabatayi kukapereka lipoti la momwe zokonzekera za chisankho chapatatu zikuyendera. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Alfandika: Tili ndi masiku 7 ofufuza atsogoleri Polankhula ndi Tamvani, wapampando wa komitiyo Yaumi Aufi Mpaweni adati lipoti la MEC likusonyeza kuti ntchito yokonzekera chisankho ikuyenda bwino ndipo komiti yonse idagwirizana ndi zomwe idawona ndi kumva kuchoka ku MEC. + Tidayitana bungwe la MEC kuti lidzatipatse lipoti. Zomwe adatiuza zikusonyeza kuti ntchito ikuyenda bwino ndipo mamembala onse akomiti adakhutira ndi lipotiro. Ngati kungawoneke zovuta, tiwona mtsogolomu, adatero Mpaweni. + Iye adati komitiyo ndiyokonzeka kuthandizira pomwe bungwe la MEC lingakumane ndi zovuta za mtundu uliwonse pofuna kuti chisankho cha chaka chino chidzayende mokomera zipani ndi anthu onse. + Mulipoti lake, mkulu woyanganira zisankho ku bungwe la MEC, Sam Alfandika adafotokoza momwe ntchito za kalembera, kuunika maina, kupeleka zikalata za ofuna kudzapikisana nawo pamipando ya mtsogoleri wa dziko ndi wachiwiri wake komanso aphungu ndi makhansala zidayendera. + Iye adalongosolanso zovuta zomwe akuyembekezera ndi ndondomeko zomwe bungwelo lakonza zofuna kudzathana ndi zovutazo zitadzawoneka. + Monga mukudziwa, anthu adalembetsa 6 859 570 pogwiritsa ntchito njira yamakono yomwe idatithandiza kuchepetsa chinyengo. Padali chiseso chochotsa maina opezeka kangapo mkaundula ndipo maina 13 244 adachotsedwa, adatero Alfandika. + Iye adati pozindikira kuti kunja kuli akathyali malinga ndi makono, bungwelo lidapeza akadaulo a nkhani za zida zamakono omwe azithandizira kuwonetsetsa kuti palibe yemwe walowerera chinsinsi cha bungwelo. + Alfandika adauzaso komitiyo kuti amene akufuna kupikisana nawo adapeleka kalata zowonetsa zolinga zodzapikisana nawo ndipo adati ntchitoyo idayenda bwino. + Tidalandira zikalata zonse koma tikuziunikabe moti pakutha kwa masiku 7, tikhala tikutulutsa maina omalizira omwe tawavomereza kudzapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko lino. Pamene ntchito younguza aphungu a Nyumba ya Malamulo idzatenga masiku 14. Ndipo makhansala itenga masiku 21, adatero Alfandika. +",11 +"Boma Lipempha Atolankhani Athetse Nkhani za Bodza 9/botomani.jpg"" alt="""" width=""325"" height=""368"" />Botomani: Timakhala okhumudwa ndi zolembedwa zina Boma lapempha atolankhani kuti ayike chidwi pa nkhani za zofufuzafufuza pofuna kuthana ndi kufala kwa nkhani zabodza. +Nduna ya zofalitsa nkhani ndi njira zamakono a Mark Botomani apereka pempholi potsekera msonkhano waukulu wapachaka wa bungwe la atolankhani a chigawo cha kumwera kwa dziko lino la Blantyre Press Club omwe unachitikira mboma la Mangochi. +Msonkhanowu unachitika pa mutu woti Kuthana Ndi Kufala Kwa Nkhani Zabodza ndipo atolankhani-wa anachitanso chisankho pofuna kusankha atsogoleri atsopano omwe ayendetse bungweli kwa zaka zitatu zikubwerazi. +Iwo ati atolankhaniwa akuyenera kugwiritsa ntchito ukadaulo wawo omwe anaphunzira polemba nkhani zomwe ndi zoona zokhazokha. +Ife ku bomaku, timakhala okhumudwa ndi zina zomwe zimalembedwa. Ndikukhulupilira kuti msonkhano umenewu uthandiza kusintha zimenezi, anatero a Botomani. +A Botomani ati nyumba zofalitsa nkhani zikuyenera kutengera phunziro pa nyumba zina zomwe zimapititsidwa ku bwalo la milandu kaamba kolemba nkhani za bodza. +",10 +" Lambani wadza ndi Knock Out Dzina la Limbani Banda, yemwe masiku ano amadzitcha kuti Lambanie Dube si lachilendo kwa otsata zoimba ku Malawi. Iye adatchuka zedi mmbuyomu ndi nyimbo yake ya Chisoni Nkumatenda ngakhalenso Kulira kwa Kholo. KONDWANI KAMIYALA adacheza naye kuti amve za chimbale chake chatsopano. Adacheza motere: Banda: Tithane ndi kupondelezana Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chimbalechi chaphulidwa liti? Chimbale chatsopanochi, chotchedwa Knock Out chidatulutsidwa pa 22 October chaka chomwe chino. Ichi ndi chimbale changa cha nambala 11. + Knock out, ndiye kuti chiyani? MChingerezi, ndikhoza kumalizitsa kuti Knock out oppression, inde kuthana ndi kuponderezana. Tikuyenera kuthana ndi nsanje ndi nkhanza komanso zoipa zonse. + Choyenera kuchita nchiyani? Maganizo athu ayenera kusintha basi. Sitingatukuke ngati tikupita kusukulu ndi cholinga chodzalembedwa ntchito basi. Tiyenera kupita kusukulu ndi maganizo akuti tidzalembe ena ntchito patsogolo. Dziko likusintha ili. Kalelo munthu akakhala ndi galimoto zimakhala ngati ndiwolemera koma onani lero aliyense akudziwa kuti galimo nchinthu choti chimafunika pamoyo wa munthu kukhala nacho. + Kodi mchimbalechi muli nyimbo zingati ndipo zina mwa nyimbozo ndi ziti? Muli nyimbo 13 ndipo zina mwa nyimbozo ndi Stuck on You, Living in the Jungle, Tikufuna Yesuyo komanso ndaimbanso nyimbo ya Chisoni Nkumatenda mwa njira ina. + Udajambula kuti? Nyimbo zina zidajambulidwa ku Greener Arts Studios msewu wa Chileka ndi Tiya Chalamwendo komanso ku Ralph Records ku Namiyango. Izitu ndi nyimbo za chamba cha reggae momwe onditsata amadziwira. + Mawu kwa Amalawi ndi wotani? Amalawi achilandira chimbalechi ndipo akusangalala nacho. Langa ndi pempho kuti apitirize kutigwira dzanja. Kungoyamikira kokha si kokwanira, akuyeneranso kumatigula zimbalezi. +",16 +" Mudalinji mchakachi? Ma alubino aona zakuda Mpotopola ku Joni, Amalawi 3 200 athothedwa Anthu 106 afa ndi madzi osefukira Tili mchaka china, 2015 wapita ndipo talowa 2016. Lero tikhale tikuunguza zina mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zidamera nthenje mchaka changothachi. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Maalubino aona mbonaona Kwa nthawi yoyamba, dziko lino lidaona zomwe zakhala zikungomveka mmaiko ena. Mchaka cha 2015 taona maalubino akusakidwa ngati nyama. Kuwapha, kuwachotsa ziwalo, komanso kuwagulitsa kumene pokhulupirira kuti ziwalo zawo zingabweretse chuma. + Mchitidwewu udatenga malo ku Machinga, Balaka, Dedza komanso Mangochi. Nkhaniyi yakhala ikudandaulitsa bungwe lomenyera ufulu wa anthuwa la Association of People with Albinism in Malawi (Apam) malinga ndi mkulu wa bungweli, Boniface Massah. + Massah adati zonsezi zakhala zikuchitika chifukwa cha zilango zomwe mabwalo akhala akupereka kwa yemwe wapezeka wolakwa. Mwachitsanzo, mboma la Dedza amayi ena adalamulidwa kukaseweza kundende zaka ziwiri atapezeka olakwa pankhani yofuna kusowetsa alubino, nkhani yomwe idadandaulitsa bungweli. + Mwezi wa March, anthu achialubino pamodzi ndi mabungwe adachita zionetsero mumzinda wa Blantyre pofuna kuonetsa mkwiyo wawo ndi zomwe zakhala zikuchitika. + Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, adalonjeza kuti athana ndi onse amene apezeke olakwa komabe ngakhale adalankhula motere, anthuwa akhalabe akukhala mobisala mdziko lawo lomwe. + Madzi osefukira, anthu 106 afa pangozi za madzi Pa 19 January chaka changothachi, ngozi idachitika mmaboma 15 mdziko muno pamene madzi a mvula yosakata adasefukira ndipo maboma a Nsanje, Mulanje ndi Chikwawa ndiwo adakhudzidwa kwambiri, komanso maboma ena monga Rumphi ndi Karonga kumpoto. + Ngoziyi idachitika chifukwa cha mvula yomwe idagwa yochuluka mdziko muno kwa sabata ziwiri osalekeza. + Anthu 145 000 adakhudzidwa mmaboma 6 ena adasamutsidwa mmalo mwawo ndi kukasungidwa mmisasa. + Anthu 106 adafa pangoziyi ndipo dera lokula ndi mahekitala 64 000 lidakokoloka. Kutsatira ngoziyi, matenda a kolera adabuka ndipo anthu 423 adakhudzidwa ndi matendawa omwe adapaha anthu 6. + Mutharika adalengeza kuti dziko lino ndi malo angozi ndipo kotero mabungwe ndi maiko akunja akuyenera kupulumutsa dzikoli kumavutowo. Mawuwa adachititsa kuti mabungwe akunja koma ena a mdziko la Malawi momwemuno ayambe kupereka thandizo losiyanasiyana kwa anthu amene adakhudzidwa. + Mtopola ku Joni, Amalawi athothedwa Nkhani inanso yomwe idakula mchakachi ndi zipolowe zomwe zidabuka mdziko la South Africa kuchitira alendo amaiko ena amene akugwira ntchito mdzikomo. + Maiko adayamba kusamutsa nzika zake mdzikolo chimodzimodzinso dziko la Malawi mu April lidasamutsanso nzika zake 3 200 zomwe zidakhudzidwa ndi mtopolawo. + Mtopolawo udali wachiwiri dziko la South Africa likuchitira alendo amene akudzafuna maganyu mdzikomo. Mu June 2008, dziko la South Africa lidachitiranso mtopola alendo a mmaiko ena amene akukhala mdzikolo ndipo anthu 60 adaphedwa pamene anthu oposa 600 adavulazidwa. + Lero pamene mwachita bata mdzikomo, Amalawi ambiri akhamukiranso mdzikomo kukafuna maganyu. + Ziwawazo zidayamba pamene mfumu ya Mazulu Gooodwill Zwelethini idakolezera moto ponena kuti nzika za mmaiko ena zibwerere kwawo ati chifukwa zikuwaphangira ntchito. + Ngakhale utsi sufuka popanda moto, Zwelethini adakana izi ponena kuti atolankhani ndiwo sadamumvetse. + Maiko komanso mabungwe mu Africa adadzudzula zomwe zochitika mdzikolo. + Dziko la Nigeria nalo lidayamba kusala nzika za dziko la South Africa. Ku Zimbabwe, mawailesi a mdzikolo adayamba asiya kuimba nyimbo za mdziko la South Africa, pamene ku Mozambique, nzika zina za mdziko la South Africa zidachitidwa chipongwe. + Ku Malawi kuno anthu adachita zionetsero pamene adakapereka chikalata cha madandaulo awo kwa kazembe wa dziko la South Africa. Kuphatikiza apo, Amalawi adachitanso zionetsero zina zokakamiza kuti anthu asamagule katundu msitolo za mdziko la South Africa zimene zili mdziko muno monga Shoprite, Game ndi Pep. + Boma lichotsa mafumu amtauni Nkhani ina yomwe idazunguza mchakachi mpaka lero ndi ya ganizo la boma lofuna kuchotsa mafumu mmizinda, mtauni komanso mmamanisipalite. + Unduna wa maboma angono ndiwo udatulutsa chkalata chomwe chidadzetsa kusagwirizana pamene mafumuwo adaopseza boma kuti achita zomwe angathe pofuna kuteteza ufumu wawo. + chikalatacho mwa zina, chidati mafumuwo sazilandiranso mswahara chifukwa tsopano ndi anthu wamba. Gawo 3 (5) la malamulo okhudza ufumu (Chiefs Act) ndi lomwe lidaomba mkota paganizo la bomalo. + Mafumu a mizinda ya Lilongwe, Mzuzu, Zomba ndi Blantyre komanso manisipalite za Luchenza ndi Kasungu, ndiwo adakhudzidwa ndi chikalatacho. + Nkhaniyi itafika pampondachimera, boma lidabweza moto ndipo mafumuwa akugwirabe ntchito yawo monga kale. + Boma liletsa masacheti Mchaka chimenechi dziko la Malawi lidabwera ndi ganizo loletsa mowa wa mmasacheti. + Msonkhano wa nduna za boma udavomereza zoletsa mowawu ndipo kwangotsala kuti pakhale lamulo lokakamiza aliyense kusiya kugulitsa mowawu. +",11 +" Miyoyo ya Amalawi ili pachiopsezo Mkulu wa bungwe loona za umoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) Martha Kwataine wati nzomvetsa chisoni kuti dziko la Malawi lasemphanitsa zoyenera kuika patsogolo. Iye wati izi zaika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kwataine adanena izi kaamba ka ganizo la boma losiya kulemba ntchito madokotala 51 omwe amaliza maphunziro awo kusukulu ya ukachenjede ya College of Medicine ati popeza bomalo silikulembanso anthu ntchito. + Koma unduna wa zaumoyo wati wasintha maganizo ake ndipo tsopano ulemba ntchito madokotalawa ngakhale kumene kuchokere ndalama zowalipira sikukudziwika. + Polankhulana ndi Tamvani mkati mwa sabatayi, Kwataine adati nzachisoni kuti boma lafika pokanika kulemba ntchito adotolo panthawi yomwe dziko lino likulira chifukwa chakuchepa kwa madotolo mzipatala. + Iye adati nzodabwitsa kuti boma lomwe lakhala likudandaula kuti madokotala akuthawa mdziko muno kutsatira ntchino zonona kunja, pano likukana kuwalemba ntchito. + Nanga akatithawa, kapena anthu akasiya kupita kusukulu ya udotolo, titani? adadabwa Kwataine. + Iye adati nzachisoni kuti ganizo la boma posalemba ntchito madotokotalawa kuika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo chifukwa madokotala alipo kale ochepa. + Ndikulankhula pano zinthu sizili bwino mzipatala zambiri momwe anthu akumwalira ndi matenda ochizika kaamba kakuchepa kwa madotolo, Kwataine adatero. + Ndipo msabatayi madokotala onse mdziko muno adaopseza kuti anyanyala ntchito ngati boma sililemba ntchito anzawowo pakutha pa sabata ziwiri. + Koma pozindikira kuti zinthu sizikhala bwino madokotalawo akanyanyala ntchito, unduna wa zaumoyo ndi a kuunduna wa zachuma adakhala pansi nkugwirizana kuti madokotalawo alembedwe ntchito zisanafike poipa. + Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe adatsimikiza za nkhaniyi Lachinayi polankhula ndi mtolankhani wa The Nation, koma adati undunawo sukudziwa kuti ndalama zolipira madokotala atsopanowo zichokera kuti. + Naye mneneri wa unduna wa zachuma Nations Msowoya adati ngakhale adagwirizana zoti madokotalawo ndi anamwino alembedwe ntchito, sakudziwa kuti malipiro awo azitenga kuti. + Malinga ndi kalata yomwe adatulutsa a bungwe la Medical Doctors Union of Malawi mogwirizana ndi bungwe la Society of Medical Doctors, kulemba ntchito adotolowa kuthandiza kuchepetsa kuperewera kwawo mzipatala. + Kalatayo idati boma la Malawi liganizire za umoyo wa anthu mdziko muno womwe ukufunika kuikidwa patsogolo ndipo zina zonse zibwere pambuyo.n Mkulu wa bungwe loona za umoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) Martha Kwataine wati nzomvetsa chisoni kuti dziko la Malawi lasemphanitsa zoyenera kuika patsogolo. Iye wati izi zaika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo. + Kwataine adanena izi kaamba ka ganizo la boma losiya kulemba ntchito madokotala 51 omwe amaliza maphunziro awo kusukulu ya ukachenjede ya College of Medicine ati popeza bomalo silikulembanso anthu ntchito. + Koma unduna wa zaumoyo wati wasintha maganizo ake ndipo tsopano ulemba ntchito madokotalawa ngakhale kumene kuchokere ndalama zowalipira sikukudziwika. + Polankhulana ndi Tamvani mkati mwa sabatayi, Kwataine adati nzachisoni kuti boma lafika pokanika kulemba ntchito adotolo panthawi yomwe dziko lino likulira chifukwa chakuchepa kwa madotolo mzipatala. + Iye adati nzodabwitsa kuti boma lomwe lakhala likudandaula kuti madokotala akuthawa mdziko muno kutsatira ntchino zonona kunja, pano likukana kuwalemba ntchito. + Nanga akatithawa, kapena anthu akasiya kupita kusukulu ya udotolo, titani? adadabwa Kwataine. + Iye adati nzachisoni kuti ganizo la boma posalemba ntchito madotokotalawa kuika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo chifukwa madokotala alipo kale ochepa. + Ndikulankhula pano zinthu sizili bwino mzipatala zambiri momwe anthu akumwalira ndi matenda ochizika kaamba kakuchepa kwa madotolo, Kwataine adatero. + Ndipo msabatayi madokotala onse mdziko muno adaopseza kuti anyanyala ntchito ngati boma sililemba ntchito anzawowo pakutha pa sabata ziwiri. + Koma pozindikira kuti zinthu sizikhala bwino madokotalawo akanyanyala ntchito, unduna wa zaumoyo ndi a kuunduna wa zachuma adakhala pansi nkugwirizana kuti madokotalawo alembedwe ntchito zisanafike poipa. + Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe adatsimikiza za nkhaniyi Lachinayi polankhula ndi mtolankhani wa The Nation, koma adati undunawo sukudziwa kuti ndalama zolipira madokotala atsopanowo zichokera kuti. + Naye mneneri wa unduna wa zachuma Nations Msowoya adati ngakhale adagwirizana zoti madokotalawo ndi anamwino alembedwe ntchito, sakudziwa kuti malipiro awo azitenga kuti. + Malinga ndi kalata yomwe adatulutsa a bungwe la Medical Doctors Union of Malawi mogwirizana ndi bungwe la Society of Medical Doctors, kulemba ntchito adotolowa kuthandiza kuchepetsa kuperewera kwawo mzipatala. +",10 +"Papa Apempha Akhristu Aziwerenga Baibulo ndi Cholinga Wolemba: Thokozani Chapola Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransisco lolemba walimbikitsa akhristu kuti pomwe akuwerenga mau a Mulungu adzikhala ndi cholinga. +Papa walankhula izi popitiriza kutsindika pa mfundo zomwe walemba mu chikalata chake cholimbikitsa anthu kuwerenga baibulu pafupipafupi. +Iye wati nthawi zambiri anthu amawerenga baibulo pamene asowa chochita zomwe wati sizoyenera kutero ndipo anati akhristu akuyenera kudzikonzekeretsa bwino pomwe akufuna kuwerenga mau ochokera mu buku loyera. +Pamenepa papa anapitiriza kupereka chitsanzo cha ophunzira ake a Yesu, omwe nthawi zambiri akafuna kuwerenga buku loyera amayamba aziyeretsa iwo eni. +Mwa zina Papa analimbikitsa akhristu omwe anasonkhana pa bwalo la St. Peters Square kukhala zida zamphamvu zolalika uthenga wa Ambuye ponseponse. +",13 +" Amalawi akulira, chitetezo chachepa Akuluakulu a mabungwe omwe siaboma ati kuchepa kwa malipiro a apolisi ndi chimodzi mwa zomwe zalowetsa pansi chitetezo mdziko muno popeza apolisiwo amatangwanika kusokerera malipiro ochepawo. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Undule Mwakasungula wa bungwe loona ufulu wachibadwidwe la Malawi Human Rights Consultative Committee (MHRCC) kudzasno Billy Banda wa Malawi Watch amaunikira kubooka kwa chitetezo komwe kwasiya anthu akulira ndi umbava komanso umbanda. + Mkulu wa apolisi mdziko muno, Lot Dzonzi wati sangakjane kapena kuvomera ngati malipiro ali vuto, koma wati apolisi akukumana ndi mavuto ambiri ndipo adziwitsa kale boma za izi. + Iye adati pano nkoyenera kuti apolisi aike maso pantchito ndipo kukambirana za malipiro kutsatire izo. + Munthu ngati akulemba ntchito umayenera kulimbikira ndipo zinazo kaya ndi zamalipo mumakambirana, adatero Dzonzi. + Kwa kanthawi tsopano, zipani zotsutsa, mabungwe, kudzanso anthu mmadera osiyanasiyana akhala akudandaula za kamphepo ka umbanda ndi umbava komwe kaomba mwamphamvu mdziko muno. + Mbalizi zakhala zikudzudzula boma kuti kuchotsa mfundo yothira mpholopolo ndikupheratu (Shot to kill) ndiko kwadzetsa mavutowa, ponena kuti izi bwezi zitangolankhulidwa pakati pa apolisiwo osati kulengeza. + Apolisi ena omwe sadafune kutchulidwa mayina awo avomereza kuti kuchepa kwa malipiro ndi nkhani yotentha yomwe imawagobola mafupa. + Mmodzi mwa iwo adati K20 000 yomwe ena amalandira pa mwezi nchitonzo chabe. + Zinthu zakwera. Nzoona wapolisi adzifera kandalama kameneka? adatero wapolisi wina mumzinda wa Blantyre. + Wapolisi wina wa nthambi ya kafukufuku mboma la Ntcheu adati malipiro a apolisi saphula kanthu. + Munthu angalimbikire bwanji ntchito apa? Tisamanamizane, adakatiganizira pamalipiro pokhapo, adatero wapolisiyo. + Mdziko muno chitetezo chasokonekera ndipo kumva kuti wina waphedwa kapena kuberedwa katundu sinkhani yachilendo. + Lolemba pa 30 Julaye alonda awiri adaphedwa pamalo ena omwetsera mafuta galimoto ku Machinga. + Malinga ndi Dzonzi anthuwo adasinjidwa mitu ndi osadziwika omwe nkutheka amafuna kubooleza malo olimba osungira ndalama pamalopo. + Nako ku Chirimba sabata zitatu zapitazi mkulu wina adapezeka atafa atakhapidwa ndi zikwanje. + Sabata ziwiri zangothazi bambo winanso yemwe amagulitsa nkhuku kwa Kachere mumzindawu adapezeka atafa, atapachikidwa mumtengo. + Lolemba mumzinda wa Lilongwe mbava zidathyola nyumba ina ndikuba ndalama zoposera K2 miliyoni. + Nayo Tamvani Lachisanu pa 20 Julaye idadziwonera anthu atatu atakhapidwa ndi mbava kuchipatala cha gulupu mumzinda wa Blantyre. + Mmodzi mwa anthuwo adali wapolisi wina yemwe adakhapidwa mmutu komanso paphewa ndi achiwembu omwe adakimana nawo kwa Kamba mumzindawu. + Iye adauza achipatalawo kuti adakhapidwa cha mma 7 koloko madzulo atangoweruka kuntchito. + Aapa amabungwewa ati ngati boma silikonza malipiro a apolisiwa, umbanda ndi umbava siutha ndipo osautsika akhala Amalawi. + Mwakasungula adati kugwa kwa ndalama ya kwacha kudakweza mitengo ya katundu wambiri ndipo ogwira ntchito ambiri mmakampani ngakhale mboma adakwezeredwa malipiro pomwe apolisi mpaka pano akulandirabe malipiro akalewo. + Nkhani ya malipiro a apolisi siyobisa, sizili bwino, ngakhale nyumba zawo mutaziona nzomvetsa chisoni. Boma likonze za umoyo wawo kaye, adatero Mwakasungula. + Banda wati anthu ngakhalenso aphungu anyumba ya Malamulo akuyenera kuchita mbali yawo pofuna kukhazikitsa chitetezo mmadera mwawo, osangolekera apolisi. + Iye adati Pulezidenti Joyce Banda akuyenera kupeza njira zobwezeretsa chitetezo mdziko muno. + Chitetezo siapolisi okha, zikufunika tigwirane manja. Ngakhale omwe amathandiza dziko lino amafuna chitetezo chisaguge. + Pakufunikanso kuti pakhale njira yabwino yokwezera maudindo apolisi olimbikira. Zimenezi zija zimachititsa apolisi kulimbikira ntchito. Wapolisi asakhale malo amodzi nthawi yaitali chifukwa izi zimabweretsa ziphuphu, adatero Billy Banda. + T/A wina ku Mwanza yemwe sadafune kutchulidwa adati zinthu sizili bwino kumeneko ndipo nkhani zoberana ziweto komanso kukhapana sizachilendo. + Iyo idati ndibwino mkulu wa apolisiyu atule pansi udindo chifukwa chitengereni udindowu nkhani yomwe yakula ndikusokonekera kwa chitetezo. + Mkulu wa apolisi akadangotula pansi udindo. , idatero mfumuyo. + Koma Dzonzi pazotula pansi udindo wake adati, Izo ndi momwe akuganizira iwo koma kwa ife ndikugwira ntchito. + Limbani Kaombe wa mmudzi mwa Kachepa kwa T/A Likoswe mboma la Chiradzulu wati apolisi akuyenera kumayenda ndi mfuti paliponse kuti azitha kuthira mpholopolo akuba. +",7 +" Flames inyamuka mawa Timu ya Flames ikunyamuka mawa mdziko muno ulendo ku Tanzania kukaswana ndi timuyi masewero amene alipo Lachitatu pa 7 October. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iyi ndi ndime yachipulula mumpikisano wa Fifa 2018 World Cup ndipo masewero achibwereza ali Loweruka likudzali pa Kamuzu Stadium. + Malinga ndi mlembi wa Fam Sugzo Nyirenda, osewera akumana cha mma 6:00 madzulo ano kuchoka kosewerera makalabu awo. + Timu ikanyamukira ku Lilongwe nthawi ikamati 7:30 mmawa. Masewerowa akachitikira pabwalo la Benjamin Mkapa ndipo adzayamba 3:00 masana nthawi ya ku Malawi kuno. + Mtawali adatenga osewera monga Simplex Nthala, Bighton Munthali, Stanley Sanudi, John Lanjesi, Yamikani Fodya, Miracle Gabeya, Pilirani Zonda, Limbikani Mzava, Isaac Kaliati, Chimango Kaira, Robert Ngambi, Micium Mhone, John CJ Banda, Levison Maganizo, Gerald Phiri Jnr, Dalitso Sailesi, Manase Chiyese, Robin Ngalande, Chawanangwa Kaonga ndi Frank Gabadinho Mhango. +",16 +" Nkhondo ilipo mu afcon Atusaye (kumanja) kuthambitsana ndi mnyamata wa Ethiopia Kuphedwa kwa Ethiopia Lachitatu pa Kamuzu Stadium ndi Malawi komanso kuphedwa kwa Mali tsiku lomwelo ndi Algeria zikusonyeza kuti mgulu B momwe muli matimu anayiwa mukhala ntchito yosayamba. + Tikukambamu timu iliyonse yasewera mipira iwiri, umodzi pakhomo ndi umodzi koyenda koma Algeria ndiyo yachita chamuna chifukwa yapambana onse. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Mali ndi Malawi ndiwo akusetekera pakamwa ngakhale sanadye mokwanira kutsatira kutolera mapointi atatu pamasewero awiri. + Mali idapha Malawi pakwawo 2-0 nkukagonja mmanja mwa Algeria 1-0 koyenda. Malawi idakwapula Ethiopia 3-2 nkugonja kwa Mali pamene Algeria yathambitsa Ethiopia 2-1 komanso Mali. + Mgululi ikutsogola ndi Algeria kutsatirana ndi Mali ngakhale ili ndi mapointi atatu chimodzimodzi Malawi koma iyo yachinyitsa chigoli chimodzi pamene Malawi yachinyitsa zigoli 4. Kumbuyo kuli Ethiopia yomwe sidatole pointi ngakhale imodzi. + Mumpikisano wa Afcon matimu awiri mgulu lililonse amene achita bwino ndiwo amapitirira kukapikisana nawo. Apa zikusonyeza kuti masewero onse akatha woyamba ndi wachiwiri adzapita ku Morocco chaka chikubwerachi. + Mpikisanowu ukatha, timu imodzi yomwe yathera pa nambala 3 koma yasewera bwino kuposa matimu onse amene sadachite bwino idzasankhidwa kuti ipite nawo ku Morocco. + Nkhondo mgulu B ikuoneka ikhala pakati pa Mali ndi Malawi kuti apitirire Algeria yomwe yathobola kale ngakhale Ethiopianso ili ndi mwayi wochita bwino. + Malawi pa 11 October ikulandira Algeria, timu yomwe adayigonjetsa 3-1 mu 2010. Masewerowa ali pa Kamuzu Stadium ndipo Lachitatu lake pa 15 Malawi idzatsatira Algeria mdziko lawo kukaphana. Timu ya Algeria idakhalapo katswiri wa mpikisanowu mu 1990 itaphwasula Nigeria. + Kuti Malawi ichite bwino ikuyenera ithethetse Algeria pamene ikubwera pa Kamuzu Stadium komanso kudzapha Mali imene idzafike pa Kamuzu Stadium pa 15 November komanso iyesetse kutidzimula pakati pa Ethiopia kapena Algeria kwawo kapena pakavuta kukangolepherana nawo. + Padakalipano, timu iliyonse mgululi ili ndi mwayi wopita ku Morocco ngati ingasamale ndi magemu akudzawa. + Masewero a Malawi ndi Ethiopia, adachinya zigoli za Malawi adali Atusaye Nyondo ziwiri ndi Frank Banda, pamene Ethiopia adayichinyira adali Getaneh Kebede ndi Yusuf Saleh. +",16 +" Masitalaka: Bwanji APM sakulankhulapo? Zafika pa mwana wakana phala. Akuluakulu a mabungwe komanso zipani apempha mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti alankhulepo pa kunyanyala ntchito kwa ogwira mboma komwe kwafika pa lekaleka mdziko muno. + Izi zikudza patatha mwezi mabwalo a milandu ali otseka, nazo sukulu za College of Medicine ndi Chancellor College (Chanco) zidatsekedwa kaamba ka sitalaka. Pothira mchere pabala ndiye ndi abungwe lothana ndi katangale la ACB lomwe maofesi ake atsekedwa Lachiwiri lapitali, komanso ogwira ntchito kuchipatala cha Kamuzu Central Hospital amenenso ayamba kunyanyala pofunitsitsa kuti boma liwakwezere malipiro awo. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ngakhale pali chipwirikitichi, Mutharika sakulankhulapo kuti tsogolo likhala lotani ndipo mmalo mwake yemwe akulankhulapo ndi nduna ya zachuma Godall Gondwe amene akukanitsitsa kuti palibe kuonjezera malipiro ponena kuti dziko lino lili pamoto malinga ndi momwe chuma chikuyendera. + Mkulu wa bungwe la Institute for Policy Interaction (IPI) Rafik Hajat akuti boma lisatenge nkhani yonyanyala ntchitoyi mwachibwana. + Boma lionetse chidwi chifukwa ngati silisamala zingabweretse mavuto adzaoneni, adatero Hajat polankhula ndi Tamvani Lachiwiri. + Mneneri wa chipani cha PP Ken Msonda akuti chipani chawo chakhumudwa kuti mpaka lero Mutharika sadalankhulepo kanthu, zomwe wati nzodabwitsa. + Mwina poti adanena [nthawi ya kampeni] kuti adzapitiriza pamene akulu awo adalekera ndiye mwina kupitiriza kwake nkumeneku pamene tayamba kuona masitalaka osalekeza monga zidalili nthawiwo, adatero Msonda. + Mneneriyu adati Mutharika akuyenera auze Amalawi zomwe zichitike pamene kunyanyala ntchito kuli mkati. + Nay Billy Banda wa bungwe la Malawi Watch akuti Mutharika akuyenera kuyankhulapo pamene aliyense ali kakasi kusowa chochita. + Mtsogoleri sayenera kulankhula wamba, nchifukwa chake pali mneneri wake kapena nduna yokhudzidwa kuti azilankhula, koma pomene zafikapa mtsogoleriyu ayenera kulankhulapo ndithu kuti Amalawi ayembekezere zotani ndi mmene zinthu zilili, adatero Banda. + Mkuluyu adati sakukhutira ndi momwe boma likuchitira pankhaniyi kotero akupenekera kuti kulankhula kwa Mutharika kungabweretse chiyembekezo kwa Amalawi. + Sizikudziwika ngati sitalaka ya ogwira ntchito kumakhoti ingathe msanga, koma pamene tikudikira kuti kumabwaloko kulongosoke, ndi izi tikumvanso kuti ena ogwira ntchito mboma ayambanso kunyanyala. Koma sitikumva kuti boma lakambirana ndi anthuwa kuti kunyanyalaku kuthe. + Apatu ife sitikukhutira, timayembekeza kuti mwina boma lilankhulana ndi anthuwa kapena kukambirana ndi bungwe limene limamenyera ufulu wawo kuti mwina kulowerera kwawo mavutowa akhoza kutha, adaonjeza Banda. + Koma malinga ndi mkulu wa zamalamulo kuboma Kalekeni Kaphale, bungwe la maloya la Malawi Law Society (MLS) lidakumana ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pomwe zidaoneka kuti sitalakayo ikhoza kutha posachedwa. + Boma la DPP lakhala likunena kuti mavutowa akudza kaamba ka kubedwa kwa ndalama mboma komwe kudaonekera muulamuliro wa PP. Koma Msonda akuti iyi si nkhani. + Ngati ndalama palibe, nanga ndalama zomwe amadzikwezera okha zija adazitenga kuti? Nanga amati azitenga kuti popeza ndalama mbomamo akuti mulibe? adatero Msonda. + Sabata ziwiri zapitazo zidadziwika kuti mtsogoleri wa dziko lino pamodzi ndi wachiwiri wake adzikwezera malipiro ndi K8 pa K10 iliyonse komanso nduna zake ndi sipikala wa Nyumba ya Malamulo kudzanso mtsogoleri wotsutsa. Koma Mutharika ndi wachiwiri wake Saulos Chilima adakana kuti ayambe kulandira malipirowo padakalipano kaamba ka mavuti a zachuma. + Naye mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga akuti sangayankhule zambiri chifukwa sadatsatire momwe boma lakhala likuchitira pankhani yokhudza kunyanyalaku. + Komabe Ndanga wati kukambirana kukufunika kuti sitalakazi zitheretu mdziko muno. + Koma mneneri wa Mutharika, Fredrick Ndala, komanso mneneri wa boma Kondwani Nankhumwa sadayankhe mafoni awo pamene Tamvani imati imve mbali yawo. + Nayenso mkulu wa bungwe loona za ufulu wa ogwira ntchitowa la Civil Servants Trade Union (CSTU), Servace Sakala, adakana kutsirapo ndemanga ponena kuti tilankhule ndi aboma pankhaniyi. +",11 +" Lundu, Kaomba apita ku mwambo wa Kulamba? Mafumu kukapereka zowonga kwa Kalonga Gawa Undi chaka chatha Mafumu aakulu a Achewa muno mMalawi Paramount Chief Lundu ndi Senior Chief Kaomba, akana kunena ngati apite kumwambo wa Kulamba omwe ufike pachimake lero kulikulu la mfumu yaikulu ya Achewa mmaiko a Malawi Mozambique ndi Zambia. + Mafumu awiriwa adasiya kupita kumwambowo, umene mafumu a Achewa mmaiko atatuwa amapereka ulemu kwa mfumu yawo yaikulu Kalonga Gawa Undi ndi kufotokoza momwe zinthu zikuyendera mmadera awo. Iwo adasiya kupita kumwambowo pamene Lundu, yemwe ndi mfumu yaikulu ya Amanganja ndi Achewa, amanena kuti Gawa Undi alibe ulamuliro paiye. + Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Lundu adati anthu ena akulowererapo pa nkhaniyi. + Sindikuyankhani kalikonse chifukwa ndikudziwa pali anthu ena omwe amakutumani kuti muzifunsa za nkhani imeneyi, adatero Gawa Undi nkudula foni. + Kaomba adati iye sanganenepo kanthu, chifukwa Lundu ndiye ali ndi mphamvu zonena chochita chifukwa iye ali pansi pake muchikhalidwe cha Achewa. + Yankhulani ndi a Paramount Chief Lundu ndi amene angakuuzeni chifukwa ine ndimatsatira zomwe iwo anena monga wamkulu kwa ine. Zomwe anganene ndipanga zomwezo, adatero Kaomba. + Koma wapampando wa Chewa Heritage Foundation (Chefo), Professor George Kanyama Phiri, wati ali ndi chiyembekezo choti mafumuwo apita kumwambowo. + Iye adati akuluakulu a gululi limodzi ndi mafumu akhala akukambirana ndi Kaomba ndi Lundu nkhani yokhudza kusemphana kwawoko ndipo zokambiranazo zimayenda bwino. + Phiri wati Kaomba ndi Lundu adali nawo ku zochitikachitika zofuna kupeza ndalama zomwe adakonza a Chefo pa 14 August 2013 zomwe akuti zidapereka chikhulupiliro chakuti mafumu awiriwa adzapita nawo kumwambo wa Kulamba. Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda adali mlendo wolemekezeka ku mwambowo. + Tidali nawo ku zochitika zomwe tidapanga kuti tipeze ndalama pokonzekera mwambowu ndiye ndikhulupilira kuti amenewa tidzakhala nawonso kumwambowu. Takhala tikukumana nawo kukambirana za nkhaniyi ndipo pamaoneka kuti zinthu zimayenda, Phiri adauza Tamvani Lachiwiri. + Iye wati kusamvanako kudangoona kuchitika chifukwa Gawa Undi ndi Lundu mpachibale choncho samayenera kulimbana. + Gawa Undi ndi mkulu wake weniweni wa Paramount Chief Lundu kotero padalibe vuto lililonse kumuveka udindo wa Kalonga, adatero Phiri. + Mwambo wa Kulamba umachitika Loweruka lomaliza la mwezi wa August chaka chilichonse ndipo pambali pa zolankhulalankhula, komanso mafumu kulamba pomwe amakapereka zokolola kwa Kalonga Gawa Undi ndipo kumakhala zakudya, zovala komanso magule osiyanasiyana a Achewa monga njedza, gulewamkulu, chisamba ndi ena otero. + Phiri wati chaka chino Achewa akonza magule osiyanasiyana kuphatikizapo nyau ya ndege ya mtundu wa Helicopter yomwe idzanyamule nyau zina za mitundumitundu kupita nazo kubwalo la mwambowo. + Yemwe adali wapampando wa Chefo Justin Malewezi, chaka chatha adauza Tamvani kumwambowo kuti dziko la Malawi lili ndi mafumu 136 a Chichewa, pomwe ku Mozambique kuli mafumu 42 pomwe ku Zambia aliko 36. + Malewezi panthawiyo adati kumwambowo kudafika Achewa 1.5 miliyoni. +",8 +"Ambuye Stima Apempha Akatolika Apewe Kuchita Nawo Ziwawa Pa Ndale Episkopi wa mpingo wa katolika mu dayosizi ya Mangochi, ambuye Montfort Stima wapempha akhristu a mpingowu kuti apewe kupezeka mmagulu omwe akulimbikitsa zipolowe zokhudza ndale mdziko muno. +Stima: Mkatolika asapezeke mmagulu ochita ziwawa Ambuye Stima anena izi pakutha pa mwambo wa misa ya chaka cha Utatu Woyera yomwe anatsogolera lamulungu, ku tchalitchi la St. John, yomwe ndi nthambi ya Kausi Parish mu dayosiziyo. +Iwo ati mkhristu aliyense wa mpingo wa katolika akuyenera kudziwa kuti iye ndi chifanizo cha Mulungu ndipo mwa iye muli Mulungu Atate Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera, kotero sakuyenera kumapezeka mmagulu ochita chisokonezo koma kulimbika pa ntchito yothandiza kudzetsa bata ndi mtendere. +Mkatolika sakuyenera kumapezeka nawo mmagulu opanga ziwawa chifukwa amakhulupilira Mulungu ndipo amayenera kuonetsa mtima wachikondi, wolezerana komanso wofunira ena zabwino, anatero ambuye Stima. +Ambuye Stima apemphanso akhristu kuti akhale odzetsa umodzi pa malo paliponse pomwe amapezeka. +",11 +"Phungu Akufuna Anthu a Dera Lake Akhale ndi Luso la Malonda Phungu wa kunyumba ya malamulo mdera La Blantyre Malabada, Ishumael Rafik Mkumba wati akufuna kuti anthu a mdera lake akhale ndi luso lochita malonda ngati njira imodzi yosungira ndalama. +Mkumba: Anthu akhale ndi luso losunga ndalama Phunguyi yemwenso ndi wachiwiri kwa nduna ya za maphunziro ndi luso la sayansi, wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre. +Iye wati potsatira kumusankha kukhala wachiwiri kwa nduna mboma la mgwirizano wa zipani za DPP ndi UDF akufuna kukwanilitsa nsanamira ya zipanizi pa nkhani za chitukuko. +Ifeyo a UDF ndi DDP timakhulupirira anthu kuti atukuke ndipo pamene timapanga mgwirizano uja sizinavute chifukwa zokhumba zathu zinali zofana, anatero Mkumba. +Iwo ati ngati dziko lisakuyenda bwino vuto si president koma vuto ndi MP chifukwa president amatuma MP kukawatumikira anthu ndipo ati awaphunzitsa anthu kuti azisunga ndalama moyenera. +",14 +" Tambala wameza chimanga Kusadabuzika kwa chipani cha DPP pa chisankho chapadera kukutanthauza kuti Amalawi atopa ndi ulamuliro wa chipanicho, akadaulo a ndale ena atero. + Malinga ndi zotsatira za bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), pachisankho chapadera chimene chidachitika Lachiwiri mmadera a phungu atatu ndi makhansalanso atatu, chipani cha MCP chidasesa mipando yonse ya phungu ndi iwiri ya khansala pomwe chipani cholamula cha DPP chidapeza mpanda wa khansala umodzi. + Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Otsatira MCP kusangalala mumzinda wa Blantyre Akadaulo pankhani za ndale, Henry Chingaipe ndi Mustapha Hussein paokhapaokha adati kusakwaniritsa malonjezo amene DPP idapanga pachisankho cha 2014, ndizo zapangitsa kuti anthu ade nacho kukhosi. + Hussein adati izi zikutanthauza kuti anthu sakukhutira ndi chipani cholamula cha DPP chimene wati sichikukwaniritsa malonjezo ake a pachisankho cha 2014. + Amalawi sakukhutira ndi momwe [DPP] ikuyendetsera zinthu. Ngati chipanicho sichisintha, adzaona zakuda mu 2019, adatero Hussein. + Zotsatira za chisankhochi zikudza pamene gulu lofufuza momwe ndale ndi zina zikuyendera mu Africa la Afro-barometer litatulutsa kafukufuku wawo amene amasonyeza kuti ngati chisankho chitachitika lero, Amalawi angavotere MCP pamene amati ataya chikhulupiriro mwa DPP. + Kafukufukuyu atatuluka, chipani cha DPP chidatsutsa ndipo chidati anthu sangayiwale ntchito zabwino zomwe akuchitira Amalawi. + Hussein wati zotsatira za chisankhochi zikuphera mphongo pa kafukufukuyo. Vuto chipani cha DPP chimakonda kutsutsa. Koma akuyenera kusinkhasinkha pa zomwe zachitikazi, adaonjeza. + Naye Chingaipe akuti chisankhochi ndi uthenga kuti anthu atopa ndi ntchito za DPP. Iye adati chisankhochi chili ngati mpeni wa nsengwa wothwa konsekonse. + Mu 2014, DPP idalonjeza zambiri monga kuthana ndi mavuto a kuzimazima kwa magetsi, kusowa kwa madzi, ziphuphu komanso nkhani za umoyo. Mpaka lero palibe chachitika. + Lero Amalawi apereka uthenga womveka ku boma kuti ngati sasamala, aika chikhulupiriro chawo pa chipani cha MCP, adatero Chingaipe. + Koma mneneri wa boma Nicholas Dausi adati avomereza kuti agonja. Ayi tivomere, tagonja ndewu koma nkhondo sitidagonje, adatero Dausi. + Iye adati abwerera kwa Amalawi kuti amve pakhota nyani mchira kuti mpaka ziwavute choncho. + Wachiwiri kwa mlembi wa MCP Eisenhower Mkaka wati ichi ndi chizindikiro kuti chipanichi chidaberedwa mavoti mu chisankho cha 2014. + Mwaona nokha zotsatira, tanthauzo kuti mu 2014 adatibera mavoti. Tili ndi chiyembekezo kuti mu 2019 chipani chathu chidzapambana, adatero Mkaka. + Polengeza Mkulu wa bungwe loyendetsa chisankho la MEC, Jane Ansah Lachitatu adalengetsa zotsatira za chisankho chapadera chomwe chidachitika mmadera atatu. + Chipani cha MCP chidapeza mipando ya kumpoto kwa Lilongwe Msozi, komwe adapambana ndi Sosten Gwengwe; kumwera cha kummawa kwa mzinda wa Lilongwe kumene adatola chikwama ndi Ulemu Msungama pomwe Lawrence Sitolo adatenga mpando wa ku Nsanje Lalanje. + Ndipo chipanicho chidazomolanso mipando ya khansala wa kuwodi ya Mtsiriza ku Lilongwe komwe adapambana ndi Kingwell Zikaola komanso kuwodi ya Ndirande Makata kumene adapambana ndi Thom Litchowa. + Wopambana yekhayo wa DPP adali Nicholas Josiya yemwe adatenga wodi ya kumpoto kwa Mayani ku Dedza. +",11